/1 Koma Mulungu atsimikiza kwa ife cikondi cace ca mwini yekha m'menemo, kuti
pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.
Koma pasanafike phwando la Paskha, Yesu, podziwa kuti nthawi yace idadza
yakucoka kuturuka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ace
a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira cimariziro.
Ndi kwa Yesu Kristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi
mkulu wa mafumu a dziko lapansi; Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula ku
macimo athu ndi mwazi wace.
Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi cikondi
cosatha; cifukwa cace ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace
wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo
wosatha.

/2 Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndi inu nthawi yaikuru yotere, ndipo
sunandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe
bwanji, Mutionetsere Atate?.
Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine?.