The New Testament of our Lord and Saviour Jesus Christ

Mateyo 1

1 Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu. 2 Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake; 3 Ndipo Yuda anabala Faresi ndi Zara mwa Tamara; ndi Faresi anabala Ezironi; ndi Ezironi anabala Aramu; 4 Ndi Aramu anabala Aminadabu ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala Salimoni; 5 Ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabe; ndi Boazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jese; 6 Ndi Jese anabala Davide mfumuyo; ndipo Davide mfumuyo anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya; 7 Ndi Solomoni anabala Rehabiyamu; ndi Rehabiyamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa; 8 Ndi Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya; 9 Ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya; 10 Ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya; 11 Ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi ya kutengedwa kumka ku Babulo: 12 Ndipo pambuyo pake pa kutengedwa ku Babulo, Yekoniya anabala Salatiyeli; ndi Salatiyeli anabala Zerubabele; 13 Ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro; 14 Ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi; 15 Ndi Eliyudi adabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo; 16 Ndi Yakobo anabala Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene Yesu wotchedwa Khristu adabadwa mwa iye. 17 Motero mibado yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inayi; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kumka ku Babulo mibado khumi ndi inayi, ndi kuyambira pa kutengedwa kumka ku Babulo kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inayi. 18 Tsopano kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kudali kotere: Amayi wake Mariya adapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asadakomane iwowo, adapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. 19 Koma Yosefe, mwamuna wake, adali wolungama,ndiponso sadafuna kunyanzitsa iye, nalingirira mumtima kumleka iye m’seri. 20 Koma posinkhasinkha iye zinthu izi, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera kwa iye m’kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chiri cha Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wa mwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iye adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo. 22 Tsopano zonsezi zidakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa m’neneri, ndi kuti, 23 Onani namwali adzayima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutchadzina lake Emmanuel; ndilo losandulika, Mulungu ali nafe. 24 Ndipo Yosefe adawuka kutulo take, nachita monga adamuwuza m’ngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake; 25 Ndipo sadamdziwa iye kufikira adabala mwana wake woyamba wamwamuna; namutcha dzina lake Yesu.

Mateyo 2

1 Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m’masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum’mawa anafika ku Yerusalemu, 2 Nanena, Ali kuti amene adabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tidawona nyenyezi yake kum’mawa, ndipo tidabwera kudzamlambira Iye. 3 Pamene Herode mfumuyo adamva ichi adavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye. 4 Ndipo pamene adasonkhanitsa ansembe akulu onse ndi alembi a anthu, adafunsira iwo, adzabadwira kuti Khristuyo? 5 Ndipo adamuwuza iye, M’Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kudalembedwa kotere ndi m’neneri kuti, 6 Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wam’ng’onong’ono mwa akulu a Yudeya; pakuti wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisrayeli. 7 Pomwepo Herode adawayitana Anzeruwo m’seri, nafunsitsa iwo nthawi yake idawoneka nyenyeziyo. 8 Ndipo adawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mawu, kuti inenso ndidzadze kumlambira Iye. 9 Ndipo iwo, m’mene adamva mfumu, adamuka; ndipo onani, nyenyezi ija adayiwona kum’mawa, idawatsogolera iwokufikira idadza niyima pamwamba pomwe padali kamwanako. 10 Pamene adayiwona nyenyeziyo, adakondwera ndi kukondwa kwakukulu. 11 Ndipo pamene adafika ku nyumba adawona kamwanako ndi Mariya amake, ndipo adagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chawo, nampatsa Iye mphatso zawo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure. 12 Ndipo iwo, pochenjezedwa ndi Mulungu m’kulota kuti asabwerere kwa Herode, adachoka kupita ku dziko lawo panjira yina. 13 Ndipo pamene iwo adachoka, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera kwa Yosefe m’kulota, nati Tawuka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuwuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukawononga iko. 14 Ndipo iye adanyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Aigupto. 15 Ndipo adakhalabe kumeneko kufikira adamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa m’neneri kuti, ndidayitana Mwana wanga atuLuka mu Aigupto. 16 Pamenepo Herode, powona kuti adampusitsa Anzeruwo, adapsa mtima ndithu natumiza ena kukawononga tiana ta m’Betelehemu ndi ta m’milaga yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating’ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye adafunsitsa kwa Anzeruwo. 17 Pomwepo chidachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya m’neneri, kuti, 18 Mawu adamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo. 19 Koma pamene Herode adamwalira, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera m’kulota kwa Yosefe mu Aigupto. 20 Nanena, Tawuka, nutenge kamwana ndi amake nupite kudziko la Israyeli; chifukwa adafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako. 21 Ndipo iye adawuka natenga kamwana ndi amake, nalowa m’dziko la Israyeli. 22 Koma pamene iye adamva kuti Arikelao adali mfumu ya Yudeya m’malo mwa atate wake Herode, adachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene adachenjezedwa ndi Mulungu m’kulota, adapita nalowa ku mdera lina la Galileya: 23 Ndipo adadza nakhazikika mumzinda wotchedwa Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.

Mateyo 3

1 Ndipo m’masiku aja adadza Yohane m’batizi, nalalikira m’chipululu cha Yudeya, 2 Nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira. 3 Pakuti uyu ndiye adanenayo Yesaya m’neneri, kuti, Mawu a wofuwula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. 4 Ndipo Yohane yekhayo adali nacho chobvala chake cha ubweya wangamila, ndi lamba la chikopa m’chiwuno mwake; ndi chakudya chake chidali dzombe ndi uchi wa kuthengo. 5 Pamenepo padamtulukira iye aku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordano; 6 Ndipo adabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordano, ali kuwulula machimo awo. 7 Koma pamene iye adawona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki alimkudza ku ubatizo wake, adati kwa iwo, wobadwa a njoka inu, ndani adakulangizani kuthawa m’kwiyo ulimkudza? 8 Wonetsani inu zipatso zoyenera kutembenuka mtima: 9 Ndipo musamayese kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuwukitsira Abrahamu ana. 10 Ndipo tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chifukwa chake mtengo uli wonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto. 11 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wondiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. 12 Chowuluzira chake chiri m’dzanja lake ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m’nkhokwe koma mankhusu adzatenthedwa ndi moto wosazimitsika. 13 Pamenepo Yesu adachokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. 14 Koma Yohane adamkaniza, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? 15 Koma Yesu adayankha nati kwa iye, Balola tsopano; pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo adamlola Iye. 16 Ndipo Yesu, pamene adabatizidwa, pomwepo adatuluka m’madzi ndipo onani, miyamba idatsegukira Iye, ndipo adapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda, ndi kuwala kudatera pa Iye: 17 Ndipo onani, mawu akuchokera ku miyamba akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.”

Mateyo 4

1 Pamenepo Yesu adatsogozedwa ndi Mzimu kupita ku chipululu kukayesedwa ndi m’diyerekezi. 2 Ndipo pamene Iye adatha kusala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, pambuyo pake adamva njala. 3 Ndipo woyesayo adafika nati kwa Iye,Ngati muli Mwana wa Mulungu, lamulirani kuti miyala iyi ikhale mkate. 4 Koma Iye adayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse wotuluka m’kamwa mwa Mulungu. 5 Pamenepo m’diyerekezi adapita naye ku mzinda woyera; namuyika Iye pamwamba pa songa la denga la kachisi. 6 Ndipo adati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi; pakuti kwalembedwa kuti, Adzawuza angelo ake za inu, ndipo pamanja awo adzakunyamulani inu, mungagunde phazi lanu pa mwala. 7 Yesu adanena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako. 8 Pomwepo mdiyerekezi adapita naye ku phiri lalitali, namuwonetsa mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo; 9 Ndipo adati kwa Iye, Zinthu zonsezi ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndikundipembedza ine. 10 Pomwepo Yesu adanena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzampembedza ndipo Iye yekha yekha udzimtumikira. 11 Pomwepo m’diyerekezi adamsiya Iye, ndipo onani, angelo adadza, namtumikira Iye. 12 Tsopano pamene Yesu adamva kuti Yohane adaponyedwa mundende adapita ku kulowa mGalileya; 13 Ndipo adachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m’Kapenawo wa pambali pa nyanja m’malire a Zebuloni ndi Nafitali: 14 Kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi Yesaya m’neneri kuti, 15 Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano, Galileya wa amitundu; 16 Anthu wokhala mumdima adawona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo wokhala m’malo a m’thunzi wa imfa, kuwala kudawatulukira iwo. 17 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kulalikira, ndikuti, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wakumwamba wayandikira. 18 Ndipo Yesu poyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, adawona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya m’bale wake, adalikuponya khoka m’nyanja popeza adali asodzi a nsomba. 19 Ndipo Iye adati kwa iwo, Nditsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu. 20 Ndipo iwo adasiya pomwepo makoka awo namtsata Iye. 21 Ndipo popitilira Iye adawona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake, mu ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wawo, adalikusoka makoka awo; ndipo adawayitana iwo. 22 Ndipo adasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wawo; namtsata Iye. 23 Ndipo Yesu adayendayenda mu Galileya monse, adalikuphunzitsa mu masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, nachiritsa kudwala konse ndi nthenda zonse mwa anthu. 24 Ndipo mbiri yake inabuka ku Suriya konse; ndipo adatengera kwa Iye onse wodwala, wogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundu mitundu, ndi wogwidwa ndi mizimu yoyipa, ndi akhungu ndi amanjenje; ndipo Iye adawachiritsa. 25 Ndipo idamtsata mipingo mipingo ya anthu wochokera ku Galileya ndi ku Dekapole ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordano.

Mateyo 5

1 Ndipo powona makamu, adakwera m’phiri; ndipo m’mene Iye adakhala pansi adadza kwa Iye ophunzira ake; 2 Ndipo adatsegula pakamwa pake, nawaphunzitsa iwo; nati; 3 Odala ali wosauka mu mzimu; chifukwa uli wawo Ufumu wa kumwamba. 4 Odala ali achisoni: chifukwa adzatonthozedwa. 5 Odala ali wofatsa chifukwa adzalandira dziko lapansi. 6 Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta. 7 Odala ali akuchita chifundo; chifukwa adzalandira chifundo. 8 Odala ali woyera mtima; chifukwa adzawona Mulungu. 9 Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu. 10 Odala iwo akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo; chifukwa uli wawo Ufumu wa kumwamba. 11 Odala muli inu m’mene anthu adzanyanzitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoyipa ziri zonse chifukwa cha Ine. 12 Sekererani, sangalalani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu m’Mwamba; pakuti potero adazunza aneneri adakhalawo musadabadwe inu. 13 Inu ndinu m’chere wa dziko lapansi; koma m’cherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu. 14 Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. 15 Palibe munthu ayatsa nyali nayibvundikira m’mbiya, koma amayiyika iyo pa choyikapo chake; ndipo imawunikira onse ali m’nyumbamo. 16 Chomwecho muwalitse inu kuwunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa kumwamba. 17 Musaganize kuti ndidadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri; sindinadza kupasula koma kukwaniritsa. 18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang’ono kamodzi kapena kasonga kake kamodzi sikadzachoka kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse. 19 Chifukwa chake yense womasula limodzi la malamulo amenewa ang’onong’ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng’onong’ono mu Ufumu wa kumwamba; koma yense wochita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wa mkulu mu Ufumu wa kumwamba. 20 Pakuti ndinena ndi inu, Ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa kumwamba. 21 Mudamva kuti kudanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu: 22 Koma Ine ndinena kwa inu, Kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu; koma amene adzati, chitsilu iwe; adzakhala wopalamula gehena wamoto. 23 Chifukwa chake ngati wabweretsa mphatso yako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe; 24 Usiye pomwepo mphatso yako, patsogolo pa guwa, nupite, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndi pamenepo idza nupereke mphatso yako. 25 Fulumira kuyanjana ndi mdani wako, pamene uli naye panjira; kuti kapena mdani wako angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe m’nyumba yandende. 26 Indetu ndinena ndi iwe, Sudzatulukamo konse, koma utalipira kakobiri komaliza ndiko. 27 Mudamva kuti kudanenedwa, Usachite chigololo: 28 Koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense woyang’ana mkazi momkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake. 29 Ndipo ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti n’kwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chiwonongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu gehena. 30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chiwonongeke, losamuka thupi lako lonse mu gehena. 31 Kudanenedwanso, yense wochotsa mkazi wake ampatse iye kalata wa chilekaniro: 32 Koma Ine ndinena kwa inu, Kuti yense wochotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chiwerewere, am’chititsa chigololo; ndipo amene adzakwatira wochotsedwayo achita chigololo. 33 Ndiponso, mudamva kuti kudanenedwa kwa iwo akale, Usadzilumbirire wekha, koma udzachita malumbiro ako kwa Ambuye. 34 Koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu: 35 Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa liri lopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yayikulu. 36 Kapena usalumbire ku mutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbuu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. 37 Koma manenedwe anu akhale, inde, inde; Iyayi, iyayi; ndipo chowonjezedwa pa izo chichokera kwa woyipayo. 38 Mudamva kuti kudanenedwa, Diso kulipa diso, ndi Dzino kulipa dzino; 39 Koma ndinena kwa inu, Musakanize choyipa; koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umtembenuzire iye linanso. 40 Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako. 41 Ndipo amene akukakamiza kumperekeza ulendo wamtunda umodzi, upite naye mitunda iwiri. 42 Amene wakupempha umpatse, ndipo iye wofuna kukukongola usampotolokere. 43 Mudamva kuti kudanenedwa, Udzikondana ndi m’nansi wako, ndikudana ndi mdani wako. 44 Koma Ine ndinena kwa inu, kondanani nawo adani anu, ndi kudalitsa iwo akutemberera inu, chitirani zabwino iwo akuda inu, ndikupempherera iwo amene amakunyozetsani ndi kunzunza inu; 45 Kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa kumwamba; chifukwa Iye amakwezera, dzuwa lake pa woyipa ndi abwino nabvumbitsira mvula pa wolungama ndi pa wosalungama. 46 Chifukwa ngati muwakonda iwo akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? 47 Ndipo ngati muyankhula abale anu wokhawokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu amisonkho sachita chomwecho? 48 Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.

Mateyo 6

1 Yang’anirani musachite zachifundo zanu pamaso pa anthu kuti muwonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa kumwamba. 2 Chifukwa chake pamene pali ponse upatsa mphatso za chifundo, usamawomba lipenga patsogolo pako, monga amachita wonyenga mmasunagoge,ndi m’makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo. 3 Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja: 4 Kotero kuti mphatso zako za chifundo zikhale za mseri; ndipo Atate wako mwiniyekha wokuwona mseri adzakupatsa iwe mowonekera. 5 Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga wonyengawo; chifukwa iwo akonda kuyimilira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti awonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo. 6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere kwa Atate wako ali mseri, ndipo Atate wako wakuwona mseri adzakupatsa iwe mowonekera. 7 Ndipo popemphera musabwereze bwereze chabe iyayi, monga amachita achikunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kuyankhula yankhula kwawo. 8 Chifukwa chake inu musafanane nawo; pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musadayambe kupempha Iye. 9 Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate Wathu Wakumwamba, dzina lanu Liyeretsedwe. 10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano. 11 Mutipatse ife lero mkate wathu wa tsiku ndi tsiku. 12 Ndipo mutikhululukire ife mangawa athu, monga ifenso tiwakhululukira amangawa athu. 13 Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse ife kwa woyipayo. 14 Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa kumwamba. 15 Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu. 16 Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope ya chisoni, ngati wonyengawo; pakuti ayipitsa nkhope zawo, kuti awonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya.Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo. 17 Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako; 18 Kuti usawonekere kwa anthu kuti ulimkusala kudya, koma kwa Atate wako ali mseri, ndipo Atate wako wokuwona mseri adzakubwezera iwe mowonekera. 19 Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zichiwononga; ndi pamene mbala zibowola ndi kuba: 20 Koma mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala sizibowola ndi kuba; 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, komweko udzakhala mtima wakonso. 22 Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa kwatunthu. 23 Koma ngati diso lako liri loyipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa kwatunthu. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu! 24 Palibe munthu angathe kutumikira ambuye awiri; pakuti pena adzamuda m’modziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa m’modzi, nadzanyoza 25 Chifukwa chake ndinena kwa inu, musadere nkhawa za moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu; chimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa chakudya ndi thupi liposa chobvala? 26 Tawonani mbalame za kumwamba sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa kumwamba azidyetsa. Nanga inu simuziposa kodi? 27 Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi? 28 Ndipo muderanji nkhawa ndi chobvala? Taganizirani za maluwa a kuthengo, makulidwe awo; sagwira ntchito, kapena sapota: 29 Ndipo ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sadabvala monga limodzi la amenewa. 30 Ngati Mulungu abveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga inu sadzakubvekani mopambana ndithu, inu wokhulupirira pang’ono? 31 Chifukwa chake musadele nkhawa, ndi kuti, tidzadya chiyani? Kapena tidzamwa chiyani? Kapena tidzabvala chiyani? 32 (Pakuti anthu amitundu:) azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. 33 Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu. 34 Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo

Mateyo 7

1 Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. 2 Pakuti ndikuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, mudzayesedwa nawo inunso. 3 Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma mtengo uli m’diso la iwe mwini suwuganizira? 4 Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo wona, mtengowo uli m’diso lako. 5 Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m’diso lako mtengowo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa chitsotso m’diso la m’bale wako. 6 Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingapondereze ndi mapazi awo, ndi potembenuka zingang’ambe inu. 7 Pemphani ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; 8 Pakuti yense wopempha alandira; ndi wofunafunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa. 9 Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala? 10 Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? 11 Chomwecho ngati inu, muli woyipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wakumwamba sadzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? wokha. Zikwanire tsiku zobvuta zake 12 Chifukwa chake zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. 13 Lowani pachipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yopita nayo kuchiwonongeko ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. 14 Pakuti chipata chimene chiri chopapatiza, nichepetsa njirayo yopita nayo kumoyo, ndipo wochipeza chimenecho ali wowerengeka. 15 Chenjerani ndi aneneri wonyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m’kati mwawo ali mimbulu yolusa. 16 Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? 17 Chomwecho mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphutsi upatsa chipatso choyipa. 18 Mtengo wabwino sungathe kupatsa chipatso choyipa, kapena mtengo wamphutsi kupatsa chipatso chokoma. 19 Mtengo uli wonse wosapatsa chipatso chokoma, awudula, nawutaya kumoto. 20 Chomwecho ndi zipatso zawo mudzawazindikira iwo. 21 Siyense wonena kwa Ine, Ambuye, Ambuyeadzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wochitayo chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba. 22 Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye,Ambuye,Kodi sitidanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoyipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? 23 Ndipo pamenepo ndidzawawuza iwo, poyera, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu wochita kusaweruzika. 24 Chifukwa chimenechi yense amene akamva mawu anga amenewa, ndi kuwachita ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera amene adamanga nyumba yake pathanthwe. 25 Ndipo idagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zidawomba mphepo, zidagunda pa nyumbayo; koma siyidagwa; chifukwa idakhazikika pathanthwepo. 26 Ndipo yense akamva mawu anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe adamanga nyumba yake pamchenga; 27 Ndipo idagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zidawomba mphepo, zidagunda panyumbayo; ndipo idagwa; ndi kugwa kwake kudali kwakukulu. 28 Ndipo kudali kuti, pamene Yesu adatha mau amenewa, makamu wa anthu adazizwa ndi chiphunzitso chake: 29 Pakuti adawaphunzitsa monga mwini ulamuliro, wosanga alembi awo.

Mateyo 8

1 Ndipo pamene adatsika paphiripo, idamtsata mipingo yambiri ya anthu. 2 Ndipo onani, wakhate adadza namlambira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza. 3 Ndipo Yesu adatambasula dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake lidachoka 4 Ndipo Yesu adanena naye, Iwe, usawuze munthu; koma pita, udziwonetsere wekha kwa wansembe, nupereke mphatso imene adayilamulira Mose, ikhale mboni kwa iwo. 5 Ndipo m’mene Iye adalowa mu Kapenawo anadza kwa Iye Kenturiyo, nampempha Iye, 6 Ndipo adati, Ambuye, wantchito wanga ali gone m’nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa kowopsa. 7 Ndipo Yesu adanena naye, Ndidzafika Ine, ndikumchiritsa iye. 8 Koma Kenturiyoyo adabvomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa denga langa ayi; koma mungonena mawu, ndipo adzachiritsidwa wantchito wanga. 9 Pakuti inenso ndiri munthu womvera ulamuliro, ndiri nawo asilikali akundimvera ine; ndipo ndikanena kwa uyu, pita, napita; ndi kwa wina, idza, nadza; ndi kwa wantchito wanga, chita ichi, nachita. 10 Pamene Iye adamva ichi, Yesu adazizwa, nati kwa iwo womutsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israyeli, sindidapeza chikhulupiriro chotere. 11 Ndipo ndinena ndi inu, Kuti ambiri a kum’mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu ufumu wa Kumwamba. 12 Koma anawo a ufumu adzatayidwa ku mdima wa kunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 13 Ndipo Yesu adati kwa Kenturiyoyo, Pita; kukhale kwa iwe monga udakhulupirira, ndipo kuchitike kwa iwe. Ndipo adachiritsidwa wantchitoyo nthawi yomweyo. 14 Ndipo pamene Yesu adafika kunyumba ya Petro, adawona mayi wamkazi wake wa Petro ali gone, alikudwala malungo. 15 Ndipo adamkhudza dzanja lake, ndipo malungo adamleka iye; ndipo adawuka, nawatumikira iwo. 16 Ndipo pakudza madzulo, anabwera nawo kwa Iye anthu ambiri wogwidwa ndi mizimu yoyipa; ndipo adatulutsa mizimuyo ndi mawu ake, nachiritsa wodwala onse; 17 Kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya m’neneri, kuti Iye yekha adatenga zofowoka zathu, nanyamula nthenda zathu. 18 Tsopano Yesu, powona makamu ambiri wa anthu womuzungulira Iye, adalamulira wophunzira amuke ku tsidya lina. 19 Ndipo adadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kuli konse mupitako. 20 Ndipo Yesu adanena kwa iye, Nkhandwe ziri ndi mayenje awo, ndi mbalame za mumlenga lenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe pogoneka mutu wake. 21 Ndipo wina wa wophunzira wake adati kwa Iye, Ambuye mundilole ine ndiyambe ndapita kuyika maliro wa atate wanga. 22 Koma Yesu adanena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa ayike akufa awo. 23 Ndipo pamene Iye adalowa mchombo wophunzira ake adamtsata Iye. 24 Ndipo wonani, padawuka namondwe wa mkulu panyanja, kotero kuti chombo chidafundidwa ndi mafunde; koma Iye adali m’tulo. 25 Ndipo wophunzira ake adadza, namudzutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tiri kuwonongeka. 26 Ndipo adanena Iye kwa iwo,Muli amantha bwanji, wokhulupirira pang’ono inu? Pomwepo Iye adadzuka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo padagwa bata lalikulu. 27 Ndipo adazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye? 28 Ndipo pamene adafika Iye kutsidya lina, ku dziko la Agadara, adakomana naye awiri wogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, awukali ndithu, kotero kuti samkatha kupitapo munthu panjira imeneyo. 29 Ndipo onani, adafuwula nati, tiri nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siyidafike? 30 Ndipo padali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zirimkudya. 31 Ndipo mizimu yoyipayo idampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m’gulu la nkhumbazo. 32 Ndipo adati kwa iyo, Pitani. Ndipo pamene idatuluka, idapita, kukalowa mu nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse lidathamangira kunsi kuphompho m’nyanjamo, ndipo zidafa m’madzi. 33 Ndipo woziweta adathawa, napita kumzinda, nanena zonse, ndi zomwe zidamugwera waziwanda uja. 34 Ndipo onani, mzinda wonse udatuluka kukakumana naye Yesu, ndipo m’mene adamuwona Iye, adampempha Iye kuti achoke m’malire awo

Mateyo 9

1 Ndipo Iye adalowa mchombo, nawoloka, nafika ku mzinda wa kwawo. 2 Ndipo onani, adabwera naye kwa Iye munthu wodwala manjenje, wogona patchika; ndipo Yesu pakuwona chikhulupiriro chawo, adati kwa wodwala manjenjeyo, mwana; Kondwera machimo ako akhululukidwa. 3 Ndipo onani, ena mwa alembi adanena mwa iwo wokha, Munthu uyu achitira Mulungu mwano. 4 Ndipo Yesu pozindikira maganizo awo, adati, Chifukwa chiyani muli m’kuganizira zoyipa m’mitima yanu? 5 Pakuti chapafupi n’chiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka nuyende? 6 Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo adanena kwa wodwala manjenjeyo,) Tanyamuka, nutenge tchika lako, nupite ku nyumba kwako. 7 Ndipo adanyamuka nachoka napita kunyumba kwake. 8 Koma pamene makamu a anthu adachiwona, adazizwa, nalemekeza Mulungu, wopatsa anthu mphamvu yotere. 9 Ndipo Yesu podutsa kuchokera kumeneko, adawona munthu, dzina lake Mateyu, atakhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye adadzuka namtsata. 10 Ndipo padali pamene Yesu adali mkukhala pa chakudya m’nyumba, onani amisonkho ndi wochimwa ambiri adadza nakhala pansi pamodzi ndi Iye ndi wophunzira ake, 11 Ndipo pamene Afarisi adawona ichi, adanena kwa wophunzira ake, Chifukwa chiyani Mphunzitsi wanu alimkudya pamodzi ndi amisonkho ndi wochimwa? 12 Ndipo m’mene Yesu adamva ichi, adati, kwa iwo, Olimba safuna sing’anga ayi, koma wodwala. 13 Koma pitani muphunzire kuti n’chiyani ichi, ndifuna chifundo, si nsembe ayi; pakuti sindinadza kudzayitana wolungama, koma wochimwa kukulapa. 14 Pomwepo adadza kwa Iye wophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa chiyani ife ndi Afarisi tisala kudya kawiri kawiri, koma wophunzira anu sasala? 15 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Nanga ana a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nawo? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya. 16 Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu ya tsopano pa chobvala chakale pakuti chigamba chake chizomoka ku chobvalacho, ndipo kuzomoka kwake kukhala kwakukulu. 17 Palibe munthu athira vinyo watsopano m’mabotolo akale; atatero mabotolo akhoza kusweka, ndipo vinyo akhoza kutayika, ndipo mabotolo angawonongeke; koma amathira vinyo watsopano m’mabotolo atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika. 18 M’mene Iye adali kuyankhula nawo zinthu zimenezo, onani, adadza munthu wina wolamulira, nampembedza, Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mubwere muyike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo. 19 Ndipo Yesu adanyamuka namtsata iye, nateronso wophunzira ake womwe. 20 Ndipo onani, mkazi adali ndi nthenda yokha mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, nadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chobvala chake; 21 Pakuti adalikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chobvala chake chokha ndidzachira. 22 Koma Yesu potembenuka ndi kuwona iye adati,Kondwera, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo adachira kuyambira nthawi yomweyo. 23 Ndipo pamene Yesu amalowa m’nyumba yake ya wolamulirayo, ndi powona woyimba zitoliro ndi khamu la anthu wobuma, 24 Iye adanena kwa iwo, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m’tulo. Ndipo adamseka Iye pwepwete. 25 Koma pamene anthuwo adatulutsidwa, Iye adalowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadawuka. 26 Ndipo mbiri yake imene inabuka m’dera lonse limenelo. 27 Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, adamtsata iye anthu awiri akhungu; wofuwula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, Mwana wa Davide. 28 Ndipo m’mene Iye adalowa m’nyumbamo, akhunguwo adadza kwa Iye; ndipo Yesu adati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Adanena kwa Iye, Inde Ambuye. 29 Pomwepo iye adakhudza maso awo, nati chichitidwe kwa inu monga chikhulupiliro chanu. 30 Ndipo maso awo adaphenyuka. Ndipo Yesu adawawuzitsa iwo, nanena, Yang’anani, asadziwe munthu aliyense. 31 Koma iwo atatulukamo, anabukitsa mbiri yake m’dziko lonselo. 32 Ndipo pamene iwo adalimkutuluka, onani, adabwera naye kwa Iye munthu wosayankhula, wogwidwa ndi chiwanda. 33 Ndipo m’mene chidatulitsidwa chiwandacho, wosayankhulayo adayankhula, ndipo makamu adazizwa, nanena, Kale lonse sichidawoneke chomwecho mwa Israyeli. 34 Koma Afarisi adati, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda. 35 Ndipo Yesu adayenda yenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, naphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda ili yonse ndi zofowoka zonse. 36 Koma Iye, powona makamuwo, adagwidwa ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza adali wokambululudwa ndi womwazikana, akunga nkhosa zopanda m’busa. 37 Pomwepo Iye adanena kwa wophunzira ake, Zokolola zichulukadi, koma antchito ali wochepa. 38 Chifukwa chake pempherani mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.

Mateyo 10

1 Ndipo pamene Iye adadziyitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, adapatsa iwomphamvu pa mizimu yoyipa, yakuyitulutsa, ndikuchiza nthenda ili yonse ndi zodwala zonse. 2 Tsopano mayina wa atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa:- woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andreya m’bale wake; Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake; 3 Filipo, ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Lebayo amene dzina la atake ake ndi Tadeyo; 4 Simoni mkanani, ndi Yudasi Isikariyote amenenso adampereka Iye. 5 Awa, khumi ndi awiriwa, Yesu adawatumiza, ndikuwalamulira ndi kuti, Musapite ku njira ya kwa amitundu, ndi kumzinda uliwonse wa Asamariya musamalowamo: 6 Koma makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli; 7 Ndipo pamene muli kupita lalikani kuti, Ufumu wa kumwamba wayandikira. 8 Chiritsani wodwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda; mudalandira kwaulere, patsani kwaulere. 9 Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m’zikwama zanu, 10 Kapena thumba la kamba la panjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake. 11 Ndipo mu mzinda uli wonse, kapena mudzi mukalowamo, mumfunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo. 12 Ndipo polowa m’nyumba muwayankhule. 13 Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siyili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mutuluka m’nyumbayo, kapena mumzindamo, sasani fumbi m’mapazi anu. 15 Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wawo wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mzinda umenewo. 16 Tawonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani inu wochenjera monga njoka,ndi owona mtima monga nkhunda. 17 Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo; 18 Ndipo adzakutengerani kwa a kazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa amitundu. 19 Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa kuti mudzayankhula bwanji kapena mudzanena chiyani; pakuti chimene mudzachiyankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo. 20 Pakuti woyankhula sindinu, koma Mzimu wa Atate wanu woyankhula mwa inu. 21 Ndipo mbale adzapereka mbale wake ku imfa, ndi atate mwana wake; ndipo ana adzawukira akuwabala, nadzawafetsa iwo. 22 Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wopilira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa. 23 Koma pamene angakuzunzeni inu mumzinda uwu, thawirani inu mwina; indetu ndinena kwa inu, simudzayitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza. 24 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena mtumiki saposa mbuye wake. 25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi mtumiki monga mbuye wake. Ngati adamutcha, mkulu wanyumba Belezebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake? 26 Chifukwa chake musawopa iwo; pakuti palibe kanthu kanabvundikiridwa kamene sikadzawululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika 27 Chimene ndikuwuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m’khutu, muchilalikire pa madenga a nyumba. 28 Ndipo musamawopa iwo amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuwupha; koma makamaka muwope Iye, wokhoza kuwuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena. 29 Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siyigwa pansi popanda Atate wanu; 30 Komatu inu, tsitsi lonse la m’mutu mwanu liwerengedwa. 31 Chifukwa chake musamawopa; inu mupambana mpheta zambiri. 32 Chifukwa chake yense amene adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzam’bvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. 33 Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. 34 Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga. 35 Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake wamkazi.. 36 Ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake. 37 Iye wokonda atate kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine. 38 Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine. 39 Iye amene apeza moyo wake, adzawutaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzawupeza. 40 Iye wolandira inu, andilandira Ine, ndi wondilandira Ine, amlandira Iye amene adanditumiza Ine. 41 Iye wolandira m’neneri, pa dzina la m’neneri, adzalandira mphotho ya m’neneri; ndipo iye wolandira munthu wolungama, mudzina la munthu wolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama. 42 Ndipo aliyense amene adzamwetsa m’modzi wa ang’ono awa chikho chokha cha madzi wozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.

Mateyo 11

1 Ndipo zitapita izi, pamene Yesu adatha kuwalamulira wophunzira ake khumi ndi awiri, Iye adachoka kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m’mizinda yawo. 2 Tsopano pamene Yohane pakumva m’nyumba yandende ntchito za Khristu, iye adatuma wophunzira ake awiri, 3 Ndipo anati kwa Iye, Inu ndinu wakudzayo kodi, kapena tiyembekezere wina? 4 Ndipo Yesu adayankha, nanena nao, Pitani mubwezere mawu kwa Yohane azimene mulikumva ndi kuziwona: 5 Akhungu akulandira kuwona kwawo, ndi wopunduka miyendo akuyenda, akhate akukonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino. 6 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine. 7 Ndipo m’mene iwo adalimkupita, Yesu adayamba kunena ndi makamu zokhudzana ndi Yohane. Mudatuluka kumka kuchipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? 8 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Munthu wobvala zofewa kodi? Onani, wobvala zofewa ali m’nyumba za mafumu. 9 Koma mudatuluka Kukawona chiyani m’neneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu,koma woposa m’neneri. 10 Uyu ndiye amene kudalembedwa za Iye, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu. 11 Indetu ndinena kwa inu, sadawuke wobadwa mwa mkazi munthu wa mkulu woposa Yohane M’batizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye. 12 Ndipo kuyambira masiku a Yohane M’batizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wakumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu. 13 Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chidanenera kufikira pa Yohane. 14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza. 15 Amene ali ndi makutu akumva, amve. 16 Koma ndidzafanizira ndi chiyani wobadwa awa a makono? Ali wofanana ndi ana wokhala m’mabwalo a malonda amene ali kuyitana anzawo, 17 Ndi kuti, Tidakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simudabvine; tidakubumirani maliro, ndipo inu simudalire. 18 Pakuti Yohane adadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, ali ndi chiwanda. 19 Mwana wa munthu adadza wakudya, ndi kumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyayidya ndi wakumwayimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi wochimwa! Ndipo nzeru yilungamitsidwa kwa ana ake. 20 Pomwepo Iye adayamba kutonza mizindayo, m’mene zidachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa iwo sadalape konse. 21 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsayida! Chifukwa ngati ntchito zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Turo ndi mu Sidoni, atalapa kale kale m’ziguduli ndi m’phulusa. 22 Koma ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wawo wa Turo ndi Sidoni udzachepa ndi wanu. 23 Ndipo iwe, Kapernawo, udzakwezedwa kodi kufikira kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira kugehena! Chifukwa ngati ntchito za mphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uwo ukadakhala kufikira lero. 24 Koma ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa koposa wako. 25 Nyengo imeneyo Yesu adayankha nati, Ndikuyamikani Inu Atate mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti mudabisira izi kwa anzeru ndi kwaw odziwitsa, ndipo mudaziwululira izi kwa makanda. 26 Indetu, Atate: chifukwa chotero chidakhala chokondweretsa pamaso panu. 27 Zinthu zonse zidaperedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana koma Atate yekha; ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha ndi iye amene Mwana afuna kumuwulullira. 28 Idzani kuno kwa Ine nonsenu wolema ndi wothodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. 29 Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30 Pakuti goli langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka

Mateyo 12

1 Nyengo imeneyo Yesu adapita tsiku la sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipowophunzira ake adali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya. 2 Koma Afarisi pakuwona, adati kwa Iye, Tapenyani, wophunzira anu achita chosaloleka tsiku la sabata. 3 Koma Iye adati kwa iwo, Kodi simudawerenge chimene adachita Davide, pamene adali ndi njala, ndi iwo amene adali naye? 4 Kuti adalowa m’nyumba ya Mulungu, nadya mikate yowonetsa, imene idali yosaloleka kudya iye kapena amene adali naye, koma ansembe okhaokha. 5 Kapena simudawerenga kodi m’chilamulo, kuti tsiku la sabata ansembe m’kachisi amayipitsa tsiku la sabata, nakhala opanda tchimo? 6 Koma ndinena kwa inu, kuti woposa kachisiyo ali pompano. 7 Koma mukadadziwa n’chiyani ichi, ndifuna chifundo si nsembe ayi; simukadaweruza wolakwa iwo wosachimwa. 8 Pakuti Mwana wa munthu ali Mbuye mwini wa tsiku la Sabata. 9 Ndipo Iye adachokera pamenepo nalowa m’sunagoge mwawo; 10 Ndipo onani, mudali munthu wadzanja lopuwala. Ndipo adamfunsitsa Iye, ndi kuti, N’kuloleka kodi kuchiritsa tsiku la sabata? Kuti ampalamulitse mlandu. 11 Ndipo Iye adati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m’dzenje tsiku la sabata, kodi sadzayigwira ndikuyitulutsa. 12 Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa n’kotani? Chifukwa cha ichi n’kololeka kuchita zabwino tsiku la sabata. 13 Pomwepo adanena Iye kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako, ndipo iye adalitambasula, ndipo lidabwezedwa lamoyo longa limzake. 14 Pamenepo Afarisi adatuluka, nakhala upo womchitira Iye momwe angamuonongere. 15 Koma pamene Yesu adadziwa, adawachokera kumeneko; ndipo adamtsata Iye makamu akulu; ndipo Iye adawachiritsa iwo onse. 16 Ndipo adawalamulira ndi kuti asamuwulule Iye; 17 Kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi Yesaya m’neneri uja kuti; 18 Tawona mtumiki wanga, amene ndidamsankha, wokondedwa wanga amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzayika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa amitundu. 19 Sadzalimbana, sadzafuwula, ngakhale m’modzi sadzamva mawu ake m’makwalala; 20 Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzayizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse. 21 Ndipo amitundu adzakhulupirira dzina lake. 22 Pomwepo adabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosayankhula; ndipo Iye adamchiritsa, kotero kuti wosanyankhulayo adayankhula, napenya. 23 Ndipo anthu onse adazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi? 24 Koma Afarisi pakumva adati; Munthu uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebule,mkulu waziwanda. 25 Ndipo Yesu adadziwa maganizo awo, nati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mzinda uli wonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala; 26 Ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye wagawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake? 27 Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebule, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala woweruza anu. 28 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu wafika pa inu. 29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m’banja la munthu wolimba, ndi kuwononga akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzawononga za m’banja lake. 30 Iye wosakhala ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza. 31 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse za mwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. 32 Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoyipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu Woyera zoyipa sadzakhululukidwa m`dziko lino kapena m`dziko liri mkudzalo. 33 Ukakoma mtengo chipatso chake chomwe chikoma; ukayipa mtengo, chipatso chake chomwe chiyipa; pakuti ndi chipatso chake, mtengo udziwika. 34 Wobadwa inu a njoka mungathe bwanji kuyankhula zabwino, inu wokhala woyipa? Pakuti m’kamwa mungoyankhula mwa kusefukira kwake kwa mtima. 35 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma cha mtima wake wabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoyipa m’chuma chake choyipa. 36 Koma ndinena kwa inu, Kuti mawu onse wopanda pake, amene anthu adzayankhula, adzawawerenga mlandu wake tsiku lakuweruza. 37 Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mawu ako, ndipo ndi mawu ako omwe udzatsutsidwa. 38 Pomwepo mwa alembi ndi Afarisi ena adayankha nati, Mphunzitsi, tifuna kuwona chizindikiro chochokera kwa Inu. 39 Koma Iye adayankha nati kwa iwo, Wobadwa woyipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona m’neneri. 40 Pakuti monga Yona adali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu usana ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usana ndi usiku. 41 Anthu aku Nineve adzawuka pa mlandu pamodzi ndi wobadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo adalapa ndi kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wamkulu woposa Yona ali pano. 42 Mfumukazi ya kumwera idzawuka pa mlandu pamodzi ndi wobadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye adachokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wamkulu woposa Solomo ali pano. 43 Pamene mzimu wonyansa, utuluka mwa munthu, umayenda nupitilira malo wopanda madzi kufunafuna mpumulo, koma osawupeza. 44 Pomwepo unena, ndidzabwerera kumka kunyumba kwanga, konkuja ndidatulukako; ndipo pakufikako uyipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa. 45 Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina imzake isanu ndi iwiri yoyipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthuyo akhala woyipa woposa woyamba. Kotero kudzakhalanso kwa wobadwa woyipa amakono. 46 Pamene Iye adali chiyankhulire ndi anthu, onani, amake ndi abale ake adayima panja, nafuna kuyankhula naye. 47 Pamenepo m’modzi adati kwa Iye, Onani, amayi wanu ndi abale anu ayima pa bwalo, akufuna kuyankhula nanu. 48 Koma Iye adayankha, nati kwa iye wonenayo, Amayi wanga ndani? Ndi abale anga ndi ayani? 49 Ndipo adatambalitsa dzanja lake pa wophunzira ake, nati, Penyani amayi wanga ndi abale anga! 50 Pakuti ali yense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye m’bale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.

Mateyo 13

1 Tsiku lomwelo Yesu adatuluka m’nyumbamo, nakhala pansi m’mbali mwa nyanja. 2 Ndipo makamu ambiri wa anthu adasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye adalowa m`chombo, nakhala pansi, ndipo khamu lonse lidayima pamtunda. 3 Ndipo Iye adayankhula zinthu zambiri kwa iwo m’mafanizo, nanena, Onani, wofesa adatuluka kukafesa. 4 Ndipo m’kufesa kwake mbewu zina zidagwa m’mbali mwa njira ndipo zinadza mbalame, nizitolatola izo. 5 Zina zinagwa pa miyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zidamera koma zidalibe dothi la kuya: 6 Ndipo m’mene dzuwa lidakwera zidafota ndipo zidapserera; popeza zidalibe mizu yozama. 7 Ndipo zina zidagwera paminga, ndipo mingayo idayanga, nizitsamwitsa izo; 8 Koma zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu. 9 Iye amene ali ndi makutu akumva, amve. 10 Ndipo wophunzirawo adadza, nati kwa Iye, chifukwa chiyani muyankhula ndi iwo m’mafanizo? 11 Iye adayankha nati kwa iwo, chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa kumwamba, koma sikudapatsidwa kwa iwo. 12 Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndipo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye. 13 Chifukwa chake ndiyankhula kwa iwo m’mafanizo; Chifukwa kuti akuwona koma wosaonetsetsa, ndi akumva koma wosamvetsetsa, kapena samadziwitsitsa. 14 Ndipo mwa iwo mwadzaza uneneri wa Yesaya, amene adati, pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzawona konse; 15 Chifukwa udalemera mtima wa anthu awa, ndipo m’makutu mwawo adamva mogontha, ndipo maso awo adatsinzina; kuti asawone konse ndi maso awo, asamve ndi makutu awo, asazindikire ndi mtima wawo, asatembenuke ndipo ndisawachiritse iwo. 16 Koma maso anu ali wodala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. 17 Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu wolungama adalakalaka kupenya zimene muziwona, koma sadaziwona; ndi kumva zimene muzimva, koma sadazimva. 18 Ndipo tsono mverani inu fanizo la wofesa. 19 Munthu aliyense wakumva mawu a Ufumu, osawadziwitsayi, woyipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m’mbali mwa njira. 20 Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mawu, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera; 21 Ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaying’ono; ndipo pakudza msautso kapena mazunzo chifukwa cha mawu, iye akhumudwa pomwepo. 22 Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mawu; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mawu,ndipo akhala wopanda chipatso. 23 Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mawu nawadziwitsa; amene abaladi chipatso, nafikitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu. 24 Fanizo lina Iye adawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu amene adafesa mbewu zabwino m’munda mwake; 25 Koma pamene anthu adalimkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati patirigu, nachokapo. 26 Koma pamene m’mela udakula nubala chipatso, pomwepo adawonekeranso namsongole. 27 Ndipo atumiki ake a mwini nyumbayo adadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simudafesa mbewu zabwino m’munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? 28 Ndipo iye adanena kwaiwo, munthu m’dani wanga wachichita ichi. Ndipo atumiki adati kwa iye, kodi mufuna tsopano kuti tipite, tikansonkhanitse uyo pamodzi? 29 Koma iye adati, ayi, kuti kapena m’mene musonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. 30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m’nyengo yakututa ndidzawuza wotutawo, muyambe kusonkhanitsa namsongole, mum’mange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m’nkhokwe yanga. 31 Fanizo lina Iye adawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi kambewu kampiru, kamene adakatenga munthu, nakafesa pa munda pake; 32 Kamene kakhaladi kakang’ono koposa mbewu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mumlengalenga zimadza, nizibindikira munthambi zake. 33 Fanizo lina adanena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chotupitsa mkate, chimene mkazi adachitenga, nachibisa m’miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse udatupa. 34 Zinthu zonsezi Yesu adaziyankhula m’mafanizo kwa makamu; ndipo kopanda fanizo sadayankhula kanthu kwa iwo. 35 Kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi m’neneri, kuti Ndidzatsegula pakamwa panga m`mafanizo kuwulula zinthu zobisika zimene chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi. 36 Pomwepo Yesu adabalalitsa makamuwo, Iye nalowa m’nyumba; ndimo wophunzira ake adadza kwa Iye, nanena, mutitanthawuzire fanizo lija la namsongole wa m’munda. 37 Iye adawayankha nati kwa iwo, Wofesa mbewu yabwino ndiye Mwana wa munthu; 38 Munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbewu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woyipayo; 39 Mdani amene adafesa uyu, ndiye m’dierekezi; ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi wotutawo ndiwo angelo. 40 Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, motero mudzakhala m’chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. 41 Mwana wa munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi iwo wochita kusayeruzika, 42 Ndipo adzawataya iwo m’ng’anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 43 Pomwepo wolungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu akumva amve. 44 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m’munda; chimene munthu adachipeza, nachibisa; ndipo m’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse adali nazo, nagula munda umenewu. 45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wofuna ngale zabwino; 46 Amene adayipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, adapita, nagulitsa zonse adali nazo nayigula imeneyo. 47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m’nyanja, limene lidasonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse. 48 Limene podzaza adalibvuwulira pa mtunda; ndipo m’mene adakhala pansi, adasonkhanitsa zabwino mu zotengera, koma zoyipa adazitaya kuthengo. 49 Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; angelo adzatuluka, nadzawasankhula woyipa pakati pa abwino. 50 Nadzawataya iwo m’ng’anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukuta mano. 51 Yesu adati kwa iwo, mwamvetsetsa zonsezi kodi? Iwo adati kwa Iye, Inde Ambuye. 52 Pamenepo Iye adati kwa iwo, chifukwa chake mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m’chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano. 53 Ndipo panali, pamene Yesu adatha mafanizo awa, adachoka kumeneko. 54 Ndipo pamene adafika kudziko la kwawo, adaphunzitsa iwo m’masunagoge mwawo, kotero kuti adazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi ntchito zamphamvu izi? 55 Kodi uyu si mwana wa m’misiri wamatabwa? Kodi dzina lake la amake si Mariya? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda 56 Ndipo alongo ake Sali ndi ife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti? 57 Ndipo iwo adakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu adati kwa iwo, M’neneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwawo ndiko, ndi kubanja kwake. 58 Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, sadachita kumeneko ntchito zamphamvu zambiri.

Mateyo 14

1 Nthawi imeneyo Herode mfumu adamva mbiri ya Yesu. 2 Ndipo adati kwa atumiki ake, Uyu Yohane M`batizi; adawuka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi ntchito zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye. 3 Pakuti Herode adamgwira Yohane, nam’manga, namuyika m’nyumba yandende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo. 4 Pakuti Yohane adanena kwa iye, sikuloledwa kwa iwe kukhala naye. 5 Ndipo pofuna kumupha iye, adawopa khamu la anthu, popeza adamuyesa iye m’neneri. 6 Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya adabvina pakati pawo, namkondweretsa Herode. 7 Pomwepo iye adamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chiri chonse akapempha. 8 Ndipo iye atampangira amake, adati, Ndipatseni ine kuno m’mbale mutu wa Yohane M’batizi. 9 Ndipo Mfumuyo idamva chisoni koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo adali naye pachakudya, adalamulira kuti upatsidwe kwa iye; 10 Ndipo adawatumiza kukadula mutu wa Yohane m’nyumba yandende. 11 Ndipo adawutenga mutu wake m’mbalemo, napatsa buthulo; ndipo iye adamuka nawo kwa amake. 12 Ndipo wophunzira ake adadza, natenga thupi, naliyika m`manda; ndipo adadza nawuza Yesu. 13 Ndipo Yesu pakumva, adachokera kumeneko m’chombo, kupita ku malo a chipululu pa yekha; ndipo anthu, pamene adamva, adamtsata Iye poyenda pamtunda kuchokera m’mizinda. 14 Ndipo Yesu adatuluka, nawona khamu lalikulu, ndipo adagwidwa ndi chifundo ndipo anachiritsa wodwala awo. 15 Ndipo pamene panali madzulo, wophunzira ake adafika kwa Iye, nanena, Malo ano ngachipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kawuzeni khamulo lidzipita ku midzi likadzigulire lokha kamba. 16 Koma Yesu adati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa chopitira, apatseni ndinu adye. 17 Ndipo iwo adanena kwa Iye, Ife tiribe kanthu pano koma mikate isanu ndi nsomba ziwiri. 18 Ndipo Iye adati, Mudze nazo kuno kwa Ine. 19 Ndipo Iye adalamulira khamulo kuti likhale pansi pa udzu; ndipo Iye adatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m’mene adayang’ana Kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa wophunzira ake ndi wophunzira kwa khamulo. 20 Ndipo adadya onse, nakhuta; ndipo adatola makombo wotsala, mitanga khumi ndi iwiri yodzala. 21 Ndipo adadyawo adali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana. 22 Ndipo pomwepo Iye adafulumiza wophunzira alowe m’chombo, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lina, kufikira Iye atawuza makamu apite. 23 Ndipo pamene Iye adawawuza makamuwo kuti achoke, adakwera m’phiri pa yekha kukapemphera: ndipo pamene padali madzulo, Iye adakhala kumeneko yekha. 24 Koma chombo tsopano chidafika pakati pa nyanja, chozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo idadza mokomana nacho. 25 Ndipo pa ulonda wa chinayi wa usiku, Yesu adadza kwa iwo, akuyenda pamwamba pa nyanja. 26 Ndipo m’mene wophunzirawo adamuwona Iye, alikuyenda panyanja, adanthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo adafuwula ndi mantha. 27 Koma pomwepo Yesu adayankhula nawo, nati, Kondwerani; Ndine; musaope. 28 Ndipo Petro adamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiwuze ndidze kwa inu pamadzi. 29 Ndipo Iye adati, Idza. Ndipo pamene Petro adatsika m’chombo, nayenda pamwamba pamadzi, kupita kwa Yesu. 30 Koma m’mene iye adawona mphepo yamkuntho, adawopa; ndipo adayamba kumira, nafuwula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine! 31 Ndipo pomwepo Yesu adatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, iwe wokhulupirira pang’ono, wakayikiranji mtima? 32 Ndipo pamene iwo adalowa m’chombomo, mphepo idaleka. 33 Pamenepo iwo amene adali m’chombomo adampembedza Iye, nanena, Zowonadi, ndinu Mwana wa Mulungu. 34 Ndipo pamene iwo adawoloka, adafika kumtunda, ku Genesarete. 35 Ndipo m’mene amuna a pamenepo adamzindikira Iye, adatumiza ku dziko lonse lozungulira, nadza nawo kwa Iye onse wokhala ndi nthenda. 36 Ndipo adampempha Iye, kuti angokhudza kokha mphonje yachobvala chake; ndipo onse amene adamkhudza adachiritsidwa.

Mateyo 15

1 Pomwepo adadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, wochokera ku Yerusalemu, nati, 2 Kodi chifukwa chiyani wophunzira anu akulumpha miyambo ya akulu? Pakuti sasamba manja awo pakudya mkate? 3 Koma Iye adayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu? 4 Pakuti Mulungu adalamulira kuti, lemekeza atate wako ndi amako; ndipo wotemberera atate wake ndi amake, afe ndithu. 5 Koma inu munena, aliyense wonena kwa atate wake kapena amake, Mphatso iyi ndi ya Mulungu ndipo simungathe kulandira thandizo kuchokera kwa ine; 6 Ndipo nakhala wosalemekeza atate wake kapena amake adzakhala wopanda m`mlandu. Inu mupeputsa malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. 7 Wonyenga inu! Yesaya adanenera bwino za inu, ndi kuti, 8 Anthu awa ayandikira chifupi ndi Ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo ulikutali ndi Ine. 9 Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa ziphunzitso, malangizo wa anthu. 10 Ndipo Iye adayitana khamulo, nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse; 11 Sichimene chilowa m’kamwa mwake chiyipitsa munthu; koma chimene chituluka m’kamwa mwake, ndicho chiyipitsa munthu. 12 Pomwepo adadza wophunzira ake, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi adakhumudwa pakumva chonenacho? 13 Koma Iye adayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa kumwamba sadawubzala, udzazulidwa. 14 Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwera m’mbuna. 15 Pamenepo Petro adayankha nati kwa Iye, mutifotokozere ife fanizoli. 16 Ndipo Yesu adati, Kodi inunso muli wosazindikira? 17 Kodi simudziwa kuti zonse zolowa m’kamwa zipita m’mimba, ndipo zitayidwa kuthengo? 18 Koma zotuluka m’kamwa zichokera mumtima; ndizo ziyipitsa munthu. 19 Pakuti mumtima muchokera maganizo woyipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama ndi zamwano. 20 Izi ndizo ziyipitsa munthu,koma kudya osasamba manja sikuyipitsa munthu ayi. 21 Pamenepo Yesu adatulukapo napatukira ku mbali za Turo ndi Sidoni. 22 Ndipo, Onani, mkazi wa ku Kenani adatuluka m’malire, nafuwulira kwa Iye, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye Mwana wa Davide; mwana wanga wa mkazi wabvutitsidwa kowopsa ndi chiwanda. 23 Koma Iye sadamyankha ngakhale mawu amodzi. Ndipo wophunzira ake adadza, nampempha Iye, nati, Mumuwuze apite; pakuti afuwula pambuyo pathu. 24 Koma Iye adayankha nati, Sindidatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israyeli. 25 Pamenepo iye adadza, nampembedza Iye nanena, Ambuye, ndithangateni ine. 26 Koma Iye adayankha nati, Sichabwino kutenga chakudya cha ana, ndi kuponyera agalu. 27 Ndipo iye adati, Zowona, Ambuye, pakutinso agalu amadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye wawo. 28 Pomwepo Yesu adayankha nati kwa iye, mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake adachira nthawi yomweyo. 29 Ndipo Yesu adachoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m’phiri, nakhala pansi pamenepo. 30 Ndipo makamu ambiri adadza kwa Iye, ali nawo wopunduka miyendo, akhungu, osayankhula, wopunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake; ndipo Iye adawachiritsa; 31 Kotero kuti khamulo lidazizwa pamene adawona osayankhula nayankhula, wopunduka ziwalo nachira, ndi wopunduka miyendo nayenda, ndi a khungu napenya ndipo iwo adalemekeza Mulungu wa Israyeli; 32 Pamenepo Yesu adayitana wophunzira ake kwa Iye, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamuli la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya ndipo sindifuna kuwawuza iwo apite osadya, kuti angakomoke panjira. 33 Ndipo wophunizira ake adanena kwa Iye, tiyiwona kuti mikate yotere m’chipululu yokhutitsa unyinji wotere wa anthu? 34 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo adati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang’ono. 35 Ndipo Iye adalamulira khamulo kuti likhale pansi; 36 Ndipo adatenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika, nanyema, napatsa kwa wophunizira ake, ndi wophunzira ake kwa makamuwo, 37 Ndipo onsewo adadya, nakhuta; ndipo adatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzadza. 38 Ndipo amene adadyawo adali amuna zikwi zinayi kuwaleka akazi ndi ana. 39 Ndipo adawawuza makamuwo kuti apite,ndipo adalowa m’chombo, nafika m’malire a Magadala.

Mateyo 16

1 Afarisi ndi Asaduki adabweranso, namuyesa, namfunsa Iye kuti awawonetse chizindikiro cha Kumwamba. 2 Iye adayankha, nati kwa iwo, Pamene pakhala madzulo munena, kudzakhala ngwe; popeza thambo liri lacheza. 3 Ndipo m’mawa, Lero n’kwamphepo: popeza thambo liri la cheza chodera.Wonyenga inu mudziwa kuzindikira za nkhope yake ya thambo; koma simuzindikira zizindikiro za nyengo yino. 4 Wobadwa woyipa ndi a chigololo wofunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona m`neneri. Ndipo Iye adawasiya, nachokapo. 5 Ndipo pamene wophunzira adafika tsidya linalo, adayiwala kutenga mikate. 6 Pamenepo Yesu adati kwa iwo, chenjerani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki. 7 Ndipo iwo adafunsana wina ndi mnzake, nati, Kodi ndi chifukwa kuti sitidatenge mikate? 8 Koma Yesu, m’mene adadziwa, adati, Ha, inu wokhulupirira pan’gono, mufunsana chifukwa chiyani wina ndi mzake, chifukwa kuti simudatenge mikate? 9 Kodi simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya zikwi zisanu, ndi mitanga ingati mudayitola? 10 Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya zikwi zinayi, ndi madengu angati mudatola? 11 Bwanji nanga simukudziwa kuti sindidanena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki. 12 Pomwepo adadziwitsa kuti sadawawuza kupewa chotupitsa cha mkate, koma chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki. 13 Pamene Yesu, adadza kudziko la ku Kayisareya wa Filipi, adafunsa wophunzira ake, kuti, anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani? 14 Ndipo iwo adati, Ena ati, ndinu Yohane M’batizi; koma ena Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena m’modzi wa aneneri. 15 Iye adanena kwa iwo, koma inu mukuti ndine yani? 16 Ndipo Simoni Petro adayankha nati, Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu wamoyo. 17 Ndipo Yesu adayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Ba-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizidakuwululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba. 18 Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanhtwe ili ndidzamanga mpingo wanga; ndipo zipata za gahena sizidzawungonjetsa uwo. 19 Ndipo ndidzakupatsa iwe mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene chili chonse uchimanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba; ndipo chimene chilichonse uchimasula pa dziko lapansi chidzakhala chomasulidwa Kumwamba. 20 Pamenepo adalamulira wophunzira ake kuti asawuze munthu kuti Iye ndiye Yesu Khristu. 21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kuwalangiza wophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu ndi, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa; ndi tsiku lachitatu kuwuka kwa akufa. 22 Ndipo Petro adamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Chikhale kutali ndi Inu, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ayi. 23 Koma Iye adapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chokhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu koma za anthu. 24 Pomwepo Yesu adati kwa wophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine. 25 Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya; ndipo iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. 26 Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake/ kapena munthu adzaperekanji chosinthana ndi moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera mphoto kwa munthu aliyense monga mwa ntchito zake. 28 Indetu ndinena kwa inu, Kuti alipo ena a iwo ayima pano amene sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzawona Mwana wa munthu akudza mu Ufumu wake.

Mateyo 17

1 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane m’bale wake, napita nawo pa wokha pa phiri lalitali. 2 Ndipo Iye adasandulika pamaso pawo; ndipo nkhope yake idawala monga dzuwa, ndi chobvala chake chidakhala choyera mbu monga kuwala. 3 Ndipo onani, Mose ndi Eliya adawonekera kwa iwo, alimkuyankhula ndi Iye. 4 Pamenepo Petro adayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola kuti timange pano mahema atatu; imodzi ya Inu, ndi yina ya Mose, ndi yina ya Eliya. 5 Akali chiyankhulire, onani, mtambo wowala udawaphimba iwo; ndipo onani, mawu ali kutuluka mumtambo akunena, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa mwa Iyeyu ndisangalitsidwa, mverani Iye. 6 Ndipo pamene wophunzira adamva, adagwa nkhope zawo pansi, nawopa kwakukulu. 7 Ndipo Yesu adadza, nawakhudza iwo nati, Ukani, musamawopa. 8 Ndipo pamene adakweza maso awo, sadawona munthu, koma Yesu yekha. 9 Ndipo pamene adali kutsika pa phiri, Yesu adawalamulira iwo kuti, Musakawuze munthu masomphenyawo, kufikira Mwana wa Munthu atadzawuka kwa akufa. 10 Ndipo wophunzira ake adamfunsa Iye, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza? 11 Ndipo Yesu adayankha, nati kwa iwo, Eliya zowonadi ayenera ayambe kudza, nadzabwezeretsa zinthu zonse. 12 Koma ndinena kwa inu, Kuti Eliya adadza kale, ndipo iwo sadamdziwa iye, koma adamchitira zonse zimene zidalembedwa. 13 Pomwepo wophunzira adazindikira kuti adayankhula nawo za Yohane M’batizi. 14 Ndipo pamene iwo adadza ku khamulo, kudafika kwa Iye munthu, nam’gwadira Iye, nati, 15 Ambuye, chitirani wana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, akuzunzika koyipa; pakuti amagwa kawiri kawiri pamoto, ndi kawiri kawiri m’madzi. 16 Ndipo ndidadza naye kwa wophunzira anu, koma iwo sadathe kumchiritsa. 17 Ndipo Yesu adayankha nati, Ha, wobadwa wosakhulupilira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? M`bweretseni kwa Ine. 18 Ndipo Yesu adamdzudzula woyipayo: ndipo adatuluka mwa iye; ndipo mwanayo adachiritsidwa kuyambira nthawi yomweyo. 19 Pamenepo wophunzira adadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, chifukwa chiyani ife sitidakhoza kumtulutsa iye? 20 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, chifukwa chakusakhulupirira kwanu: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, senderapo upite kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakhala kosatheka ndi inu. 21 Mtundu uwu sutuluka wamba koma pokhapokha umatuluka ndi pemphero ndi kusala kudya. 22 Ndipo m’mene adali kukhalabe m’Galileya, Yesu adanena nawo, Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja a anthu; 23 Ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzawukitsidwanso tsiku lachitatu. Ndipo iwo adali ndi chisoni chachikulu. 24 Ndipo pamene adafika ku Kapenawo amene aja wolandira ndalama za msonkho adadza kwa Petro ndipo adati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka msonkho? 25 Iye adabvomeza Inde, apereka. Ndipo pamene iye amalowa m’nyumba, Yesu adatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana awo kodi, kapena kwa alendo. 26 Petro adati kwa iye, kwa alendo. Yesu adanena kwa iye, Ndiye kuti anawo ali a ufulu. 27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuyitole nsomba yoyamba kuyiwedza; ndipo ukayikanula pakamwa pake udzapezamo ndalama; tatenga imeneyi; nuwapatse iyo pa iwe ndi ine.

Mateyo 18

1 Nthawi yomweyo wophunzira adadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wamkulukulu mu Ufumu wa Kumwamba? 2 Ndipo Yesu adayitana kamwana kakang`ono nakayimika pakati pawo. 3 Ndipo adati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka mtima, nimukhala ngati tianato, simudzalowa konse mu ufumu wa Kumwamba. 4 Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wamkulukulu mu Ufumu wa Kumwamba. 5 Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; 6 Koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi katiana iti, takukhulupilira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yayikulu yamwala ikolowekedwe m’khosi mwake, namizidwe pakuya panyanja. 7 Tsoka liri ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka liri ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye! 8 Chomwecho ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; n’kwabwino kuti ulowe moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m’moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri. 9 Ndipo ngati diso likukhumudwitsa, ulikolowore, nulitaye; n’kwabwino kuti ulowe m’moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa m’gehena wa moto, uli ndi maso awiri. 10 Yang`anirani kuti musanyoza m’modzi wa ang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo awo apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba. 11 Pakuti Mwana wa Munthu adadza kudzapulumutsa chotayikacho. 12 Mukuganiza motani? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi,ndipo isokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, napita kumapiri, kukafunafuna yosokerayo? 13 Ndipo ngati ayipeza, indetu ndinena kwa inu, akondwera koposa chifukwa cha nkhosayo ndi makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi zosasokera. 14 Chomwecho sichiri chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti m’modzi wa ang’ono awa atayike. 15 Chomwecho ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numuwuze panokha iwe ndi iye, ngati akumvera iwe, wam’bweza mbale wako. 16 Koma ngati sakumvera iwe, wonjeza kutenga ndi iwe wina m’modzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. 17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uwuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga munthu wakunja ndi wamsonkho. 18 Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba; ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba. 19 Ndiponso ndinena kwa inu, Kuti ngati awiri a inu abvomerezana pansi pano chinthu chiri chonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. 20 Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndiri komweko pakati pawo. 21 Pamenepo Petro anadza kwa Iye nati, Ambuye, m`bale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi? 22 Yesu adanena kwa iye, sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri. 23 Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi, mfumu ina amene adafuna kuwerengera nawo atumiki ake. 24 Ndipo pamene adayamba kuwerengera, adadza kwa iye ndi wina wa mangawa a ndalama za matalente zikwi khumi. 25 Koma popeza iye adasowa kanthu kom’bwezera, mbuye wake adalamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse adali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo. 26 Mtumikiyo choncho adagwa pansi, nampembedza, nati,Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzakubwezerani inu. 27 Pamenepo mbuye wa mtumikiyo adagwidwa ndi chisoni mumtima, nam’masula iye, namkhululukira ngongoleyo. 28 Koma mtumiki uyu, potuluka adapeza wina wa atumiki amzake yemwe adamkongola iye malupiya zana, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Ndibwezere zija udandikongola. 29 Ndipo mtumiki mzakeyu adagwa pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekezera ine, ndipo ndidzakubwezera iwe yonse. 30 Ndipo iye sadafuna; koma adapita, namponya iye m’nyumba yandende, kufikira atam’bwezera ngongole. 31 Choncho pamene mtumiki amzake adawona zochitidwazo, adagwidwa ndi chisoni chachikulu, nadza, nafotokozera mbuye wawo zonse zimene zidachitidwa. 32 pomwepo mbuye wake adamuyitana iye, nanena naye, kapolo iwe woyipa ndidakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja udandipempha ine; 33 Kodi iwenso sukadamchitira mtumiki mzako chisoni, monga inenso ndidakuchitira iwe chisoni? 34 Ndipo mbuye wake adakwiya, nampereka kwa azunzi kufikira akabwezere iye mangawa onse. 35 Chomwecho Atate wanga wa Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense m’bale wake ndi mitima yanu.

Mateyo 19

1 Ndipo panali pamene Yesu adatha mawu amenewa, adachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano. 2 Ndipo makamu akulu adamtsata Iye; ndipo Iye adawachiritsa kumeneko. 3 Ndipo Afarisi adadzanso kwa Iye, namuyesa Iye, nanena kwa Iye, Kodi n’kololedwa kuti munthu achotse mkazi wake pachifukwa chiri chonse? 4 Ndipo Iye adayankha, nati kwa iwo, Kodi simudawerenga kuti Iye amene adapanga iwo pachiyambi, adawapanga iwo mwamuna ndi mkazi. 5 Ndipo adati, pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi? 6 Kotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu adachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. 7 Iwo adanena kwa Iye, Nanga n’chifukwa chiyani Mose adalamulira kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumchotsa? 8 Iye adanena kwa iwo, chifukwa cha kuwuma mtima kwanu, Mose adakulolezani kumchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikudakhala chomwecho. 9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chiwerewere, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndi iye amene akwatira wochotsedwayo achita chigololo. 10 Wophunzira ake adanena kwa Iye, ndipo ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira. 11 Koma Iye adati kwa iwo, Anthu onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. 12 Pakuti pali osabala, amene anabadwa wotero m’mimba ya amawo: ndipo pali osabala ena adawafula anthu; ndipo pali osabala ena amene adadzifula wokha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire. 13 Pamenepo anadza nato tiana tating`ono kwa Iye, kuti Iye ayike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma wophunzirawo adawadzudzula. 14 koma Yesu adati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine; chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere. 15 Ndipo Iye adayika manja ake pa ito, nachokapo. 16 Ndipo onani, m’modzi anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, wabwino, chabwino n’chiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha? 17 Ndipo Iye adati kwa iye, unditcha bwanji kuti ndine wabwino? Kulibe wabwino, koma m’modzi, ndiye Mulungu: koma ngati ufuna kulowa m’moyo, sunga malamulo. 18 Iye adanena kwa iye Wotani? Yesu adati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama. 19 Lemekeza atate wako ndi amako, ndipo, Udzikonda mzako monga udzikonda iwe mwini. 20 M’nyamata wachichepereyo adanena kwa Iye, Zonsezi ndidazisunga kuyambira ndiri mwana, ndisowanso chiyani? 21 Yesu adanena kwa iye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate. 22 Koma pamene m’nyamatayo adamva chonenacho, adapita ali wachisoni; pakuti adali nacho chuma chambiri. 23 Pamenepo Yesu adati kwa wophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti wa chuma adzalowa mobvutika mu Ufumu wa Kumwamba. 24 Ndiponso ndinena kwa inu, N’kwapafupi kuti ngamila ipyole pa diso la singano, koposa munthu wa chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba. 25 Pamene wophunzira ake adamva ichi, adazizwa kwambiri, nanena, Ngati n’kutero angapulumuke ndani? 26 Koma Yesu adawayang’ana iwo, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu. 27 Pomwepo adayankha Petro, nati kwa Iye, Onani, ife tidasiya zonse ndi kutsata inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani? 28 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Kuti inu amene mudanditsata Ine, n’kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli. 29 Ndipo ali yense amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena mkazi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa mazanamazana, nadzalowa moyo wosatha. 30 Koma ambiri woyamba adzakhala akumapeto, ndi akumapeto adzakhala woyamba.

Mateyo 20

1 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene adatuluka mamawa kukalembera antchito m’munda wake wampesa. 2 Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa khobiri limodzi patsiku, ndipo iye adawatumiza iwo kumunda wake. 3 Ndipo iye adatuluka kubwalo pa ola la chitatu, nawona ena atangoyima pa malo wochitira malonda. 4 Ndipo adati kwa iwo, Pitani inunso kumunda wa mpesa, ndipo ndidzakupatsani chimene chiri choyenera. Ndipo iwo adapita. 5 Ndiponso adatuluka pa ola la chisanu ndi limodzi ndinso la chisanu ndi chinayi nachita chimodzi modzi. 6 Ndipo pa ora la khumi ndi limodzi adatuluka, napeza ena atangoyima chabe, ndipo adati kwa iwo, Chifukwa chiyani mwangoyima pano chabe tsiku lonse? 7 Iwo adanena kwa iye, chifukwa palibe munthu adatilemba. Iye adati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa; ndipo ndidzakupatsani chimene chiri choyenera. 8 Ndipo pakufika madzulo, mwini munda adati kwa kapitawo wake, Kayitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwawo, uyambe kwa womarizira kufikira kwa woyamba. 9 Ndipo pamene adafika kwa iwo wolembedwawo pa ora la khumi ndi limodzi munthu aliyense adalandira khobiri. 10 Koma pamene woyamba adadza, adalingalira kuti adzalandira zambiri, ndipo iwonso adalandira onse khobiri. 11 Ndipo m’mene iwo adalandira, anadandawula motsutsana ndi mwini nyumba wa bwinoyo. 12 Nati, Omalizira awa adagwira ntchito kwa ola limodzi, ndipo mudawalinganiza ndi ife amene tidapilira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake kwa tsiku. 13 Koma iye adayankha m’modzi wa iwo, ndipo adati; Mzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sudapangana ndi ine pa khobiri limodzi? 14 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. 15 Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako layipa kodi chifukwa ine ndiri wabwino? 16 Chomwecho omalizira adzakhala woyamba, ndipo woyamba womalizira pakuti woyitanidwa ndi ambiri koma wosankhidwa ndi wowerengeka. 17 Ndipo pamene Yesu adalikukwera ku Yerusalemu, adatenga wophunzira khumi ndi awiri aja napita nawo pa wokha, ndipo panjira adati kwa iwo, 18 Onani tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi, ndipo iwo adzamutsutsa kuti ayenera imfa. 19 Ndipo adzampereka kwa anthu amitundu kuti am’nyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika Iye; ndipo Iye adzawukitsidwa tsiku lachitatu. 20 Pomwepo adadza kwa Iye amake a ana a Zebedayo ndi ana ake omwe, nampembedza ndi kumpempha kanthu kena. 21 Ndipo Iye adati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye adanena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu la manja, ndi wina kulamanzere, mu Ufumu wanu. 22 Koma Yesu adayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Ndikubatizidwa ubatizo umene ndibatizidwa nawo? Iwo adanena kwa Iye, Ife tikhoza. 23 Iye adanena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi,ndikubatizidwa ubatizo ndi batizidwa nawo, koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kudzapatsidwa kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga 24 Ndipo m’mene khumiwo adamva, adapsa mtima ndi abale awiriwo. 25 Koma Yesu adawayitana, nati kwa iwo, Mudziwa kuti mafumu amitundu amachita ufumu pa iwo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. 26 Koma sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma aliyense amene akufuna kukhala wamkulu, mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; 27 Ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; 28 Monga Mwana wa Munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo kwa anthu ambiri. 29 Ndipo pamene iwo analikutuluka mu Yeriko, khamu lalikulu lidamtsata Iye. 30 Ndipo onani, amuna akhungu awiri adakhala m’mphepete mwa njira; m’mene iwo adamva kuti Yesu adalikupitilirapo, adafuwula nati, Mutichitire ife chifundo Ambuye, Inu Mwana wa Davide. 31 Ndipo khamulo lidawadzudzula iwo, kuti atonthole; koma adakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide. 32 Ndipo Yesu adayima, nawayitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitire chiyani? 33 Iwo adanena kwa Iye Ambuye, kuti maso athu aphenyuke. 34 Ndipo Yesu adagwidwa chifundo ndi iwo, ndipo adakhudza maso awo; ndipo pomwepo adapenyanso, namtsata Iye.

Mateyo 21

1 Ndipo pamene iwo adayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, ku phiri la Azitona, pamenepo Yesu adatumiza wophunzira awiri; 2 Nanena kwa iwo, Mukani ku mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nawo kwa Ine. 3 Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye afuna iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza. 4 Ndipo ichi chidatero, kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi m’neneri kuti, 5 Tawuzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Tawona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu. 6 Ndipo wophunzirawo adapita, nachita monga Yesu adawalamulira iwo; 7 Ndipo anabwera ndi bulu ndi mwana wake, nayika pa iwo zobvala zawo, nakhazika Iye pamenepo. 8 Ndipo chikhamu chachikulucho chidayala zobvala zawo panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo naziyala m’njiramo. 9 Ndipo makamuwo akumtsogolera ndi akumtsatira, adafuwula, kuti, Hossana kwa Mwana wa Davide! Wodalitsika ndiye wakudza m’dzina la Ambuye! Hossana Wam`mwamba mwamba! 10 Ndipo m’mene adalowa mu Yerusalemu muzinda wonse udasokonezeka, nanena, Ndani uyu? 11 Ndipo makamu adati, Uyu ndi m’neneri Yesu wa ku Nazarete wa Galileya. 12 Ndipo Yesu adalowa ku kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse wogulitsa ndi kugula malonda, nagudubuza magome a wosintha ndalama, ndi mipando ya wogulitsa nkhunda. 13 Ndipo adati kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga idzatchedw nyumba yopemphereramo; koma inu mwayipanga kukhala phanga la mbava. 14 Ndipo adadza kwa Iye kukachisiko akhungu ndi wopunduka miyendo, ndipo adachiritsidwa iwo. 15 Ndipo pamene ansembe akulu ndi alembi, m’mene adawona zozizwitsa zomwe Iye adazichita, ndi ana alimkufuwula ku kachisiko kuti, Hossana kwa Mwana wa Davide; adapsa mtima kwambiri. 16 Ndipo adati kwa Iye, Mulikumva kodi chimene ali kunena awa? Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Inde, simudawerenga kodi, Mkamwa mwa makanda ndi woyamwa mudafotokozera zolemekeza? 17 Ndipo Iye adawasiya natuluka mu mzinda napita ku Betaniya, nagona kumeneko. 18 Ndipo mamawa m’mene Iye adali kupitanso kumzinda, adamva njala. 19 Ndipo pamene adawona mkuyu umodzi panjira, adafika pamenepo, napeza popanda kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso ku nthawi zonse. 20 Ndipo pamene wophunzira adawona ichi adazizwa, nati, Mkuyu udafota bwanji msanga? 21 Yesu adayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiliro, osakayika kayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja, chidzachitidwa. 22 Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m’kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira. 23 Ndipo pamene Iye adalowa m’kachisi, ansembe akulu ndi akulu a anthu adadza kwa Iye ali kuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani adakupatsani ulamuliro wotere? 24 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani chinthu chimodzi, amene ngati mundiwuza Inenso ndikuwuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi: 25 Ubatizo wa Yohane, udachokera kuti, kumwamba kapena kwa anthu? Koma iwo adafunsana wina ndimzake, kuti, Tikati uchokera Kumwamba, Iye adzati kwa ife, mudalekeranji kukhulupirira iye? 26 Koma tikati, kwa anthu, tiwopa anthu ; pakuti onse amuyesa Yohane m’neneri. 27 Ndipo adamuyankha Yesu, nati, sitinganene ife. Iyenso adanena nawo, Inenso sindikuwuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi. 28 Koma mukuganiza bwanji inu? Munthu wina adali nawo ana amuna awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito ku munda wanga wampesa. 29 Iye adayankha nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake adalapa napita. 30 Ndipo adadza kwa wachiwiriyo, natero momwemo.ndipo Iye adabvomera, nati, ndipita mbuye; koma sadapite. 31 Ndani wa awiriwo adachita chifuniro cha atate wawo? Iwo adanena kwa Iye, Woyambayo. Yesu adanena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi a chiwerewere adzatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Mulungu. 32 Popeza Yohane adadza kwainu m’njira ya chilungamo, ndipo simudakhulupirira iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere adakhulupirira iye; ndipo inu, m’mene mudachiwona, simudalapa pambuyo pake, kuti mukhulupirire iye. 33 Mverani fanizo lina; Padali munthu, mwini banja, amene adalima munda wamphesa, nawuzunguliza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, nawubwereketsa kwa wolima munda, napita ku dziko lakutali. 34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso idayandikira, adatumiza atumiki ake kwa wolima munda aja, kukalandira zipatso zake. 35 Ndipo wolimawo adatenga atumikiwo, nampanda m’modzi, wina namupha, wina namponya miyala. 36 Adatumizanso atumiki ena, wochuluka kuposa woyambawo; ndipo adawachitira iwo momwemo. 37 Koma potsiriza pake adatumiza kwa iwo mwana wake wa mwamuna, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu. 38 Koma pamene wolimawo adawona mwana wa mwamunayo, adanena wina ndi mzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake. 39 Ndipo adamgwira iye, namponya kunja kwa munda, namupha. 40 Tsono atabwera mwini munda, adzachitira wolimawo chiyani? 41 Iwo adanena kwa Iye, Adzawononga moyipa anthu woyipawo, nadzapereka mundawo kwa wolima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake. 42 Yesu adati kwa iwo, Kodi simudawerenga konse m’malembo, Mwala umene adawukana womanga nyumba womwewo udakhala mutu wa pangodya; Awa ndiwo machitidwe a Ambuye ndipo ali wozizwitsa m’maso mwathu? 43 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake. 44 Ndipo aliyense wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma kwa iye amene udzamgwera, udzampera iye monga ufa. 45 Ndipo pamene akulu ansembe ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, adazindikira kuti adali kunena za iwo. 46 Ndipo pamene adafuna kumgwira Iye, adawopa khamu, chifukwa adamuyesa Iye m’neneri.

Mateyo 22

1 Ndipo Yesu adayankha, nayankhulanso kwa iwo m’mafanizo, nati, 2 Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi mfumu ndi mfumu ina imene mwana wake wamwamuna phwando la ukwati. 3 Natumiza atumiki ake kukayitana iwo woyitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sadafuna kudza. 4 Pomwepo adatumizanso atumiki ena, nanena, Uzani woyitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng’ombe zanga, ndi zonenepa ndidazipha ndipo zinthu zonse zapsa:bwerani ku ukwati. 5 Koma iwo adanyalanyaza, nachoka, wina ku munda wake, wina ku malonda ake: 6 Ndipo wotsala adagwira atumiki ake, nawachitira chipongwe, nawapha. Mat 22:7 Koma pamene mfumu idamva idakwiya; idatuma asilikali ake napululutsa ambanda aja; nitentha mzinda wawo. 8 Pomwepo idanena kwa atumiki ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma iwo woyitanidwawo sadali woyenera. 9 Chifukwa chake, Pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeza, muyitaneni ku ukwatiwu. 10 Ndipo atumikiwo adapita kunjira, nasonkhanitsa onse amene adawapeza, ngakhale woyipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo udadzala ndi alendo wokhala pachakudya 11 Ndipo pamene mfumuyo idabwera kudzawona woyitanidwawo, adapenya momwemo munthu wosabvala chobvala cha ukwati; 12 Ndipo adanena kwa iye, Mzanga udalowa bwanji muno wosakhala nacho chobvala cha ukwati? Ndipo iye adalibe mawu. 13 Pomwepo mfumu idati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumtenge ndi kumponya ku mdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 14 Pakuti woyitanidwa ndiwo ambiri, koma wosankhidwa ndiwo wowerengeka. 15 Pomwepo Afarisi adapita, nakhala upo wakumkolera Iye m’kuyankhula kwake. 16 Ndipo adatumiza kwa Iye wophunzira awo, pamodzi ndi Aherode nanena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli wowona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu mowona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang’anira pa nkhope ya anthu. 17 Chifukwa chake mutiwuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kayisara, kapena iyayi? 18 Koma Yesu adadziwa kuyipa kwawo, nati, Mundiyeseranji Ine, wonyenga inu? 19 Tandiwonetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo adadza nalo kwa Iye khobiri. 20 Ndipo Iye adati kwa iwo, N’chayani chithunzithunzi ichi, ndikulemba kwake? 21 Nanena iwo kwa Iye, Cha Kaisara. Pomwepo Iye adati kwa iwo, chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. 22 Ndipo pamene iwo adamva mawu awa, adazizwa, namsiya Iye, nachokapo. 23 Tsiku lomwelo adadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; namfunsa Iye, 24 Nanena, Mphunzitsi, Mose adati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, m`bale wake adzakwatira mkazi wake, nadzamuwukitsira m’bale wake mbewu. 25 Tsono padali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba adakwatira, namwalira wopanda mbewu, nasiyira m’bale wake mkazi wake; 26 Chimodzimodzi wachiwiri, ndi wachitatu kufikira wachisanu ndi chiwiri. 27 Ndipo pomalizira adamwaliranso mkaziyo. 28 Chifukwa chake m’kuwuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wayani wa asanu ndi awiriwo? Pakuti onse adakhala naye. 29 Koma Yesu adayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu. 30 Pakuti mkuwuka kwa akufa sakwatira kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Mulungu akumwamba. 31 Koma za kuwuka kwa akufa, simudawerenga kodi chomwe chidanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti, 32 Ine Ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Mulungu Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo. 33 Ndipo pamene khamu lidamva, lidazizwa ndi chiphunzitso chake. 34 Koma pamene Afarisi adamva kuti Iye adatontholetsa Asaduki, adasokhana pamodzi. 35 Ndipo m’modzi wa iwo, mphunzitsi wa chilamulo, adamfunsa Iye funso ndi kumuyesa Iye, nati, 36 Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo 37 Ndipo Yesu adati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. 38 Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. 39 Ndipo lachiwiri lofanana nalo ndi ili, Uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. 40 Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri. 41 Ndipo pamene Afarisi adasonkhana pamodzi, Yesu adawafunsa iwo, 42 Nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo adanena kwa Iye Mwana wa Davide. 43 Iye adati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena, 44 Ambuye adanena kwa Ambuye wanga, Khala pa dzanja la manja langa, kufikira Ine ndidzayika adani ako pansi pamapazi ako. 45 Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? 46 Ndipo padalibe m`modzi adatha kumuyankha mawu. Ndipo sadalimbika mtima munthu aliyense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.

Mateyo 23

1 Pamenepo Yesu adayankhula kwa makamu ndi wophunzira ake. 2 Nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose: 3 Chifukwa chake zinthu ziri zonse zimene iwo akawuza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zawo;pakuti iwo amayankhula, koma samachita. 4 Pakuti amanga akatundu wolemera ndi wosawutsa ponyamula, nawasenzetsa pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo. 5 Koma amachita ntchito zawo zonse kuti awonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chithando chake cha njilisi zawo, nakulitsa mphonje. 6 Nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m’masunagoge, 7 Ndi kuyankhulidwa m’misika, ndi kutchulidwa ndi anthu, Rabi, Rabi. 8 Koma inu musamatchedwa Rabi, pakuti Mphunzitsi wanu ali modzi ndiye Khristu, ndipo inu muli abale. 9 Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo m’modzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. 10 Ndipo musatchulidwa Ambuye, pakuti alipo m’modzi Ambuye wanu, ndiye Khristu. 11 Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. 12 Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa. 13 Koma tsoka inu, Alembi, ndi Afarisi wonyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pawo; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa kuti asalowemo. 14 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mukwawira m’nyumba za amayi amasiye, ndipo mupemphera pemphero lalitali; chifukwa chake mudzalandira chilango chachikulu. 15 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mupitapita ku nyanja ndi kumtunda kuyesa munthu m’modzi m’tembenuki; ndipo m’mene akhala wotere,mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri. 16 Tsoka pa inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golidi wa kachisi, wamangawa. 17 Inu wopusa, ndi akhungu; pakuti choposa n’chiti, golidi kodi, kapena kachisi amene ayeretsa golidiyo? 18 Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mphatso za pamwamba pake wachimwa. 19 Inu wopusa ndi akhungu, pakuti choposa n’chiti, mphatso kodi, kapena guwa lansembe limene liyeretsa mphatsoyo? 20 Chifukwa chake wolumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake. 21 Ndipo wolumbira kutchula kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wokhala momwemo. 22 Ndipo wolumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wokhala pomwepo. 23 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi tsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro: koma zijazo mudayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. 24 Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma ngamila mumeza. 25 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. 26 Mfarisi iwe wa khungu, yambakutsuka m’kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera. 27 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mufanana ndi manda wopaka njereza, amene awonekera wokoma kunja kwake, koma adzala m’katimo ndi mafupa wa anthu akufa ndi zonyansa zonse. 28 Chomwecho inunso muwonekera wolungama pa maso pa anthu, koma m’kati muli wodzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika. 29 Tsoka pa inu Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda wa aneneri, ndipo mukonza manda a anthu wolungama, 30 Ndikuti, ife tikadakhala m’masiku a makolo wathu, sitikadakhala woyanjana nawo pa mwazi wa aneneri. 31 Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene adapha aneneri. 32 Dzazani inu muyeso wa makolo anu. 33 Njoka inu, wobadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa gehena? 34 Chifukwa cha ichi, Onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, ndikuwapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m’masunagoge mwanu, ndi kuwazunza kuchokera ku mzinda umodzi kufikira ku mzinda wina. 35 Kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wolungama wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira mwazi wa Zakariya mwana wa Barakiya, amene mudamupha pakati pa kachisi ndi guwa la nsembe. 36 Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono. 37 Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo wotumidwa kwa iwe! Ine ndidafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simudafuna ayi! 38 Onani nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja. 39 Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandiwonanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wodala Iye amene akudza m’dzina la Ambuye

Mateyo 24

1 Ndipo Yesu adatuluka nachoka ku kachisi; ndipo wophunzira ake adadza kwa Iye kudzamuwonetsa mamangidwe a kachisiyo. 2 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Simuwona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa umzake, umene sudzagwetsedwa pansi. 3 Ndipo pamene Iye adalikukhala pansi pa phiri la Azitona, wophunzira adadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiwuze ife zija zidzawoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano? 4 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Chenjerani, kuti asasokeretse inu munthu. 5 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri. 6 Ndipo inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi ziwoneke; koma chitsiriziro sichinafike. 7 Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu udzawukirana ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi miriri ndi zibvomerezi m’malo akuti akuti. 8 Zonsezi ndicho chiyambi cha zowawa. 9 Pamenepo adzakuperekani kuzosautsa nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa. 10 Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mzake, nadzadana wina ndi mzake. 11 Ndipo aneneri wonama ambiri adzawuka, nadzasokeretsa anthu ambiri. 12 Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala. 13 Koma iye wakupirirabe kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. 14 Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro. 15 Pamene mudzawona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli m’neneri, chitayima m’malo woyera (iye amene awerenga azindikire.) 16 Pomwepo iwo ali mu Yudeya athawire kumapiri: 17 Iye ali pamwamba pa denga asatsike kukanyamula za m’nyumba mwake; 18 Ndi iye ali m’munda asabwere kutenga chofunda chake. 19 Koma tsoka ali nalo iwo wokhala ndi mwana, ndi woyamwitsa ana m’masiku amenewo! 20 Koma pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzakhale pa nyengo yozizira, kapena pa tsiku la Sabata. 21 Pakuti pomwepo padzakhala masautso akulu, monga sipadakhale wotero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. 22 Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense; koma chifukwa cha wosankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa. 23 Pomwepo ngati munthu anena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musakhulupirire; 24 Chifukwa Akhristu wonama adzawuka, ndi aneneri wonama nadzawonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa; kotero kuti akanyenge, ngati n’kotheka, wosankhidwa womwe. 25 Onani ndakuwuziranitu pasadafike. 26 Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, iye ali m’chipululu; musamukeko. Onani, ali m’zipinda; musakhulupirire. 27 Pakuti monga mphezi idzera kum’mawa, niwonekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. 28 Pakuti kumene kuli konse uli mtembo, miphamba imasonkhana komko. 29 Koma pomwepo, atapita masautso a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzawonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: 30 Ndipo pomwepo padzawoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzalira, nidzapenya Mwana wa munthu alimkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero wa ukulu. 31 Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake ku mphepo zinayi, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena. 32 Tsopano phunzirani fanizo la mtengo wa mkuyu; Pamene nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja likuyandikira; 33 Chomwechonso inu, pamene mudzawona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo. 34 Indetu ndinena kwa inu, m`bado uwu sudzachoka, kufikira zinthu zonsezi zidzakwaniritsidwa. 35 Thambo ndi dziko la pansi zidzachoka, koma mawu anga sadzachoka ayi. 36 Koma za tsiku ilo ndi nthawi yake sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, koma Atate yekha. 37 Ndipo monga kudali masiku a Nowa, koteronso kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. 38 Pakuti monga m’masiku aja, chisadafike chigumula, anthu adali mkudya ndi kumwa, adalikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa adalowa m’chingalawa, 39 Ndipo iwo sadadziwe kanthu, kufikira pamene chigumula chidadza, chidapululutsa iwo onse, koteronso kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. 40 Pomwepo adzakhala awiri m’munda; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: 41 Akazi awiri adzakhala akupera pamphero; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa 42 Chenjerani, pakuti simudziwa nthawi yake yakufika Ambuye wanu. 43 Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibowoledwe. 44 Chifukwa chake khalani inunso wokonzekeratu; chifukwa munthawi imene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza. 45 Ndani kodi ali mtumiki wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adamkhazika woyang’anira banja lake, pakuwapatsa zakudya pa nthawi yake? 46 Wodala mtumiki amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye ali kuchita chotero. 47 Indetu, ndinena kwa inu, Adzamkhazika iye womulamulira zinthu zake zonse. 48 Koma mtumiki woyipa akanena mu mtima mwake, Mbuye wanga wachedwa: 49 Nadzayamba kupanda mtumiki amzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi woledzera; 50 Mbuye wa mtumikiyo adzafika tsiku losamuyembekezera Iye, ndi nthawi yosadziwa iye. 51 Nadzamdula, nadzayika pokhala pake ndi anthu wonyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mateyo 25

1 Pomwepo Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi anamwali khumi, amene adatenga nyali zawo, natuluka kukakomana ndi mkwati. 2 Ndipo asanu a iwo adali wopusa, ndi asanu adali wochenjera. 3 pakuti wopusawo, m’mene adatenga nyali zawo sadadzitengeranso mafuta. 4 Koma anzeruwo adatenga mafuta msupa zawo, pamodzi ndi nyali zawo. 5 Ndipo pamene mkwati adachedwa, onsewo adawodzera, nagona tulo. 6 Koma pakati pa usiku padali kufuwula, Onani mkwati ali mkudza! Tulukani kukakomana naye. 7 Pomwepo adauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zawo. 8 Ndipo wopusa adati kwa wochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu ziri kuzima. 9 Koma wochenjera adayankha nati, Iyayi kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa wogulitsa malonda, mukadzigulire nokha. 10 Ndipo pamene iwo adalikumuka kukagula, mkwati adafika; ndipo wokonzekawo adalowa naye pamodzi mu ukwati; ndipo adatseka pakhomo. 11 Koma pambuyo pake adadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. 12 Koma Iye adayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani inu. 13 Chifukwa chake, dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake yakudza Mwana wamunthu. 14 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu wakumka ulendo, kudziko lakutali amene adayitana atumiki ake, napereka kwa iwo chuma chake. 15 Ndipo m’modzi adampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye. 16 Pomwepo uyo amene adalandira ndalama zisanu, adapita nagula nazo malonda, napindulapo ndalama zina zisanu. 17 Chimodzimodzi uyo waziwirizo, adapindulapo zina ziwiri. 18 Koma uyo amene adalandira imodziyo adamuka, nakumba pansi, nayibisa ndalama ya mbuye wake. 19 Ndipo itapita nthawi yayikulu, anabwera mbuye wa atumiki awo, nawerengera nawo pamodzi. 20 Ndipo uyo adalandira ndalama za matalente zisanu adadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena,Mbuye mudandipatsa ndalama za matalente zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina. 21 Ndipo mbuye wake adati kwa iye, chabwino, mtumiki iwe wabwino ndi wokhulupirika popeza iwe udakhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe wolamulira pa zinthu zazikulu; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wanga. 22 Ndipo wa ndalama ziwiriyo anadzanso, nati, mbuye, mudandipatsa ine ndalama ziwiri; onani, ndapindulapo ndalama zina ziwiri. 23 Ndipo mbuye wake adati kwa iye, chabwino, mtumiki iwe wabwino ndi wokhulupirika; udali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe wolamulira pa zinthu zazikulu; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wanga. 24 Ndipo uyonso amene adalandira ndalama imodzi, adadza, nati, mbuye, ndidakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simudafesa, ndi kusonkhanitsa kumene simudafese: 25 Ndidawopa ine, ndidapita, ndidabisa pansi ndalama yanu: Onani, siyi yanu. 26 Koma mbuye wake adayankha, nati kwa iye, mtumiki iwe woyipa ndi waulesi, udadziwa kuti ndimatuta kumene sindidafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindidawaza: 27 Chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa wokongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. 28 Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muyipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. 29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene ali nacho. 30 Ndikuponya mtumiki wopanda pake ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 31 Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake , ndi angelo woyera onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake: 32 Ndipo adzasonkhanitsidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi: 33 Nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake la manja, koma mbuzi kulamanzere. 34 Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu wodalitsika wa Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: 35 Pakuti ndidali ndi njala, ndipo mudandipatsa Ine kudya; ndidali ndi ludzu, ndipo mudandimwetsa Ine; ndidali mlendo, ndipo mudandichereza Ine. 36 Wamaliseche Ine, ndipo mudandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndidali m’nyumba yandende ndipo munadza kwa Ine. 37 Pomwepo wolungama adzayankha Iye kuti, Ambuye tidakuwonani Inu liti wanjala, ndikukudyetsani? Kapena wa ludzu ndikukumwetsani? 38 Ndipo tidawona Inu liti mlendo, ndikukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukubvekani? 39 Ndipo tidakuwonani Inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tidadza kwa Inu? 40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, chifukwa mudachitira ichi m’modzi wa abale anga, ngakhale ang’ono ngono awa, mudandichitira ichi Ine. 41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo akudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine wotembereredwa inu, ku moto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake. 42 Pakuti ndidali wa njala, ndipo simudandipatsa Ine kudya: ndidali ndi ludzu ndipo simudandimwetsa Ine: 43 Ndidali mlendo, ndipo simudandilandira Ine; wamaliseche ndipo simudandibveka Ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simudadza kundiwona Ine. 44 Pomwepo iwonso adzayankha Iye kuti, Ambuye tidakuwonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena wodwala kapena m’nyumba ya ndende, ndipo ife sitidakutumikirani Inu? 45 Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa mudalibe kuchitira ichi m’modzi wa ang’onong’ono awa, mudalibe kundichitira ichi Ine. 46 Ndipo amenewa adzachoka kumka ku chilango chosatha; koma wolungama ku moyo wosatha.

Mateyo 26

1 Ndipo padali pamene Yesu adatha mawu onse amenewa, adati kwa wophunzira ake, 2 Mudziwa kuti akapita masiku awiri, ndi phwando la paskha, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kukapachikidwa. 3 Pomwepo adasonkhana ansembe akulu ndi alembi ndi akulu a anthu, ku bwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa. 4 Nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi mochenjera, namuphe Iye. 5 Koma adanena iwo, Osati pa tsiku la phwando, kuti pasakhale chipolowe pakati pa anthu. 6 Ndipo pamene Yesu adali mu Betaniya, m’nyumba ya Simoni wakhate, 7 Anadza kwa Iye mkazi, adali nayo msupa ya alabastero ndi mafuta wonunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m’mene Iye adalikukhala pachakudya. 8 Koma m’mene wophunzira ake adawona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuwononga kumeneku? 9 Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kupatsa anthu aumphawi. 10 Koma Yesu podziwa, adati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino. 11 Pakuti nthawi zonse muli nawo aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse. 12 Pakuti mkaziyo, m’mene adathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuyikidwa kwanga m`manda. 13 Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m’dziko lonse lapansi ichi chimene mkaziyo adachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake. 14 Pomwepo m’modzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudase Isikariyote, adamuka kwa ansembe akulu, 15 Nati kwa iwo, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo adamuwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu. 16 Ndipo kuyambira pamenepo iye adafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye. 17 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, wophunzira anadza kwa Yesu nati kwa Iye, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye? 18 Ndipo Iye adati, Mukani kumzinda kwa munthu wakuti, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena, nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi wophunzira anga. 19 Ndipo wophunzira adachita monga Yesu adawauza, nakonza Paskha. 20 Ndipo pakufika madzulo, Iye adalikukhala pachakudya pamodzi ndi wophunzira khumi ndi awiri. 21 Ndipo m’mene adalimkudya Iye adati, Indetu ndinena kwa inu, m’modzi wa inu adzandipereka Ine. 22 Ndipo iwo adagwidwa ndi chisoni chachikulu, nayamba kunena kwa Iye m’modzi m’modzi, Kodi ndine Ambuye? 23 Ndipo Iye adayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lake m’mbale, yemweyu adzandipereka Ine. 24 Mwana wa munthu achokatu, monga kudalembedwa za Iye: koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa. 25 Ndipo Yudase, wompereka Iye adayankha nati, Ambuye, kodi ndine? Iye adanena kwa iye, Iwe watero. 26 Ndipo pamene iwo adalimkudya, Yesu adatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m’mene adapatsa kwa wophunzira, adati, Tengani, idyani; Ili ndi thupi langa. 27 Ndipo pamene adatenga chikho, adayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse. 28 Pakuti uwu ndiwo mwazi wanga wa chipangano chatsopano, wokhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuchotsa machimo. 29 Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi cha mpesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu mu Ufumu wa Atate wanga. 30 Ndipo pamene adayimba nyimbo, adatuluka kumka ku phiri la Azitona. 31 Pomwepo Yesu adanena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno: pakuti kwalembedwa, ndidzakantha m`busa, ndipo zidzabalalika nkhosa zagulu. 32 Ndipo nditawukitsidwanso ndidzatsogolera inu ku Galileya. 33 Koma Petro adanena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse. 34 Yesu adati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asadalire, udzandikana Ine katatu. 35 Petro adanena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafe pamodzi ndi inu, sindidzakukanani Inu ayi. Adateronso wophunzira onse. 36 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo wotchedwa Getsemane, nanena kwa wophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere. 37 Ndipo adatenga Petro ndi ana awiri a Zebedeyo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi kulemedwa kwambiri ndi chisoni . 38 Pamenepo adanena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho ku imfa: khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine. 39 Ndipo adamuka patsogolo pang’ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate anga, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine: koma si monga ndifuna Ine, koma monga mufuna inu. 40 Ndipo adadza kwa wophunzira, nawapeza iwo ali m’tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Kodi Simukhoza kuchezera ndi Ine ora limodzi? 41 Khalani maso ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa: mzimu ndithu ali wakufuna, koma thupi liri lolefuka. 42 Adamukanso kachiwiri, napemphera, nanena, Atate wanga, ngati chikho ichi sichingandipitirire ine chabwino, ndimwera ichi, kufuna kwanu kuchitidwe. 43 Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali mtulo, pakuti maso awo adalemera ndi tulo. 44 Ndipo iye adawasiya nachokanso, napemphera kachitatu, nateronso mawu womwewo. 45 Pomwepo anadza kwa wophunzira ake, nanena kwa iwo, Gonani tsopano, mupumule; onani, nthawi yayandikira, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m’manja a wochimwa. 46 Ukani, timuke; tawonani, iye wakundipereka wayandikira. 47 Ndipo Iye ali chiyankhulire, onani, Yudase m’modzi wa khumi ndi awiriwo, anadza ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu, ndi malupanga ndi zibonga, kuchokera kwa ansembe akulu ndi akulu a anthu. 48 Koma wompereka Iye adawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsopsona ndiyeyo, mumgwire Iye. 49 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuwoneni, Rabi; ndipo adampsopsona Iye. 50 Ndipo Yesu adati kwa iye, Mzanga wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namtenga Iye. 51 Ndipo onani, m’modzi wa iwo adali pamodzi ndi Yesu, adatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha mtumiki wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake. 52 Pomwepo Yesu adanena kwa iye, Tabwezera lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga. 53 Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera tsopano kwa Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino magulu a angelo woposa khumi ndi awiri? 54 Koma pakutero malembo adzakwaniritsidwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho? 55 Nthawi yomweyo Yesu adati kwa makamuwo, Kodi mudatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi zibonga, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m’kachisi kuphunzitsa, ndipo simudandigwira. 56 Koma izi zonse zidachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniritsidwe. Pomwepo wophunzira onse adamsiya Iye, nathawa. 57 Ndipo iwo akugwira Yesu adamka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe. 58 Koma Petro adamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi atumiki kuti awone chimaliziro. 59 Ndipo ansembe akulu ndi akulu a milandu onse adafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye; 60 Koma sadaupeza zingakhale mboni zonama zambiri zidadza, koma sadawupeze umboni koma pamapeto pake zidadza mboni ziwiri zonama. 61 Ndipo adati, Munthu uyu adanena kuti, Ndikhoza kupasula kachisi wa Mulungu, ndi kum’manganso masiku atatu. 62 Ndipo mkulu wa ansembe adayimilira, nati kwa Iye, Sukuyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe? 63 Koma Yesu adangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe adanena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wa moyo, kuti utiwuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu wa moyo 64 Yesu adati kwa iye, Mwatero ndinu: koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzawona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja la manja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya Kumwamba 65 Pomwepo mkulu wa ansembe adang’amba zobvala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo. 66 Muganiza bwanji? Iwo adayankha nati, Ali wochimwa woyenera kumupha. 67 Pomwepo iwo adamlabvulira malobvu pankhope pake, nam’bwanyula Iye; ndipo ena adampanda ndi manja awo, 68 Nati, Utilote ife, Khristu iwe, wakumenya iwe ndani? 69 Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo buthu linadza kwa iye, linena, Iwenso udali ndi Yesu wa ku Galileya. 70 Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, kuti, Chimene unena sindichidziwa. 71 Ndipo pamene iye adatuluka kumka kuchipata, mkazi wina adamuwona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyunso adali ndi Yesu wa ku Nazarete. 72 Ndipo adakananso ndi chilumbiro, kuti Sindidziwa munthuyo. 73 Ndipo popita nthawi yaying’ono iwo akuyimapo anadza, nati kwa Petro, Zowonadi, iwenso uli m`modzi wa iwo; pakuti mayankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe. 74 Pamenepo iye adayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindimdziwa munthuyo. Ndipo nthawi yomweyo tambala adalira. 75 Ndipo Petro adakumbukira mawu a Yesu amene adati kwa iye, Asadalire tambala udzandikana Ine katatu. Ndipo adatuluka kunja, nalira ndi kuwawa mtima.

Mateyo 27

1 Ndipo pakudza m`mawa, ansembe akulu ndi akulu a anthu onse adakhala upo wakumchitira Yesu kuti amuphe: 2 Ndipo adam’manga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo. 3 Pamenepo Yudase yemwe adampereka Iye, powona kuti Iye adatsutsidwa, adalapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akulu ndi akulu a anthu. 4 Nanena, Ndidachita koyipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo adati, Tiri nacho chiyani ife? Udziwonere wekha izo. 5 Ndipo iye adataya pansi ndalamazo m`kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi. 6 Ndipo ansembe akulu adatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziyika izi m’chosungiramo ndalama, chifukwa ndizo za mtengo wa mwazi. 7 Koma adapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda wa alendo. 8 Chifukwa chake munda umenewu adautcha Munda-wa-Mwazi kufikira lero lino. 9 Pamenepo chidakwaniritsidwa chonenedwa ndi Yeremiya m’neneri, ndi kuti, Ndipo iwo adatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengeredwa mtengo wake, amene iwo ana a Israyeli adawerenga mtengo wake; 10 Ndipo adazipereka kugula munda wa woumba mbiya, monga Ambuye adandilamulira ine. 11 Ndipo Yesu adayimilira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo adamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu adati kwa iye, Mwatero ndinu. 12 Ndipo pakum’nenera Iye ansembe akulu ndi akulu a anthu, Iye sadayankha kanthu. 13 Pomwepo Pilato adanena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe? 14 Ndipo sadayankha Iye, ngakhale mawu amodzi, kotero kuti kazembe adazizwa ndithu. 15 Ndipo pa Paskha kazembe adazolowera kumasulira munthu m’modzi wandende, amene iwo adafuna. 16 Ndipo panthawi yomweyo adali ndi wandende wodziwika, dzina lake Baraba. 17 Chifukwa chake pamene adasonkhana pamodzi, Pilato adanena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu? 18 Pakuti adadziwa kuti adampereka Iye mwanjiru. 19 Ndipo pamene Pilato adalikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake adatumiza mawu kwa iye, nanena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m’kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye. 20 Koma ansembe akulu adakopa khamu kuti lipemphe Baraba, ndikuwononga Yesu. 21 Koma kazembe adayankha nati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo adati, Baraba. 22 Pilato adanena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Ndipo onse adati, Apachikidwe. 23 Ndipo kazembe adati, Chifukwa chiyani? Adachita choyipa chotani? Koma iwo adafuwulitsa kopambana nati, Apachikidwe. 24 Koma Pilato powona kuti sadafitse, koma kuti lidapambana phokoso, adatenga madzi, nasamba m`manja pamaso pa khamulo nati, Ine ndiribe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudziwonere nokha. 25 Ndipo anthu onse adayankha nati, Mwazi wake ukhale pa ife ndi pa ana athu. 26 Pomwepo iye adamasulira iwo Baraba, koma adakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike. 27 Pomwepo asilikali a kazembe adamuka naye Yesu ku bwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye gulu la asirikali lonse. 28 Ndipo adambvula malaya ake, nambveka malaya wofiyira achifumu. 29 Ndipo adaluka Korona waminga, nambveka pamutu pake, namgwiritsa bango m’dzanja lamanja lake; ndipo adagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda! 30 Ndipo adamulabvulira malobvu Iye, natenga bango, nampanda Iye pamutu. 31 Ndipo pamene adatha kumchitira Iye chipongwe, adambvula malaya aja, nambveka Iye malaya ake, namtsogoza Iye kukampachika. 32 Ndipo pakutuluka pawo adapeza munthu wa ku Kurene, dzina lake Simoni, namkangamiza iye kuti anyamule mtanda wake. 33 Ndipo pamene adadza kumalo dzina lake Gologota, ndiko kunena kuti, Malo a Chigaza, 34 Adampatsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye m’mene adalawa, sadafuna kumwa. 35 Ndipo pamene adampachika Iye, adagawana zobvala zake pakuchita mayere: kuti zikwaniritsidwe zonenedwa ndi aneneri, kuti, Iwo adagawana zobvala zanga mwa iwo wokha nachita mayere kuti aliyense adzatenga chiyani. 36 Ndipo adakhala iwo pansi namdikira Iye pamenepo. 37 Ndipo adayika pamwamba pa mutu pake mawu wolembedwa; UYU NDI YESU 38 Pamenepo adapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, m’modzi ku dzanja lamanja, ndi wina kulamanzere. 39 Ndipo anthu wodutsapo adamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yawo, 40 Nati, Nanga Iwe, wopasula, kachisi ndi kum’manganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo. 41 Chomwechonso ansembe akulu pamodzi ndi alembi ndi akulu adamchitira chipongwe, nati 42 Adapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ngati ndiye Mfumu ya Israyeli; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye. 43 Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti adati, Ine ndine Mwana wa Mulungu. 44 Ndiponso achifwambawo wopachikidwa pamodzi ndi Iye, adamlalatira Iye mawu amodzimodzi. 45 Ndipo ola lachisanu ndi chimodzi padali mdima padziko lonse, kufikira ola lachisanu ndi chinayi. 46 Ndipo poyandikira ola lachisanu ndi chinayi, Yesu adafuwula ndi mawu akulu nanena, Eli Eli, Lamasabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine? 47 Ndipo ena a iwo akuyimilira komweko, pamene adamva, adanena, munthu uyu ayitana Eliya. 48 Ndipo pomwepo m’modzi wa iwo adathamanga, natenga chinkhupule nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiyika pa bango, nampatsa Iye kuti amwe. 49 Koma ena adati, Taleka, tiwone ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa. 50 Ndipo Yesu pamene adafuwula ndi mawu akulu, adapereka Mzimu wake. 51 Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m’kachisi chidang’ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko lidagwedezeka, ndi miyala idang’ambika; 52 Ndipo manda adatseguka ndi matupi ambiri a anthu woyera mtima, akugona kale adawuka, 53 Ndipo adatuluka m’manda mwawo pambuyo pa kuuka kwake, nalowa mu mzinda woyera, nawonekera kwa ambiri. 54 Ndipo pamene Kenturiyo ndi iwo adali naye akuyang`ana Yesu, powona chibvomerezi, ndi zinthu zimene zidachitidwa, adawopa kwambiri, nanena, Indedi, Uyo ndiye Mwana wa Mulungu. 55 Ndipo adali pomwepo akazi ambiri, akuyang’anira patali, omwe adatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye; 56 Mwa iwo amene mudali Mariya wa Magadala, ndi Mariya amake wa Yakobo, ndi wa Yose, ndi amake a ana a Zebedayo. 57 Ndipo pamene padali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe, amene adalinso wophunzira wa Yesu; 58 Iyeyo adapita kwa Pilato, napempha thupi la Yesu. Pomwepo Pilato adalamulira kuti thupiulo liperekedwe. 59 Ndipo Yosefe atatenga thupilo, adalikulunga m’nsalu yabafuta yoyeretsetsa, 60 Naliyika m’manda ake atsopano, wosemedwa m’mwala, nakunkhumizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo. 61 Ndipo Mariya wa Magadala adali pamenepo, ndi Mariya winayo, adakhala pansi popenyana ndi mandawo. 62 Ndipo m’mawa mwake, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzekera, ansembe akulu ndi Afarisi adasonkhana kwa Pilato 63 Nanena, Mfumu takumbukira ife kuti wonyenga uja adati, pamene adali ndi moyo, ndidzawuka pakutha masiku atatu. 64 Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena wophunzira ake angadze usiku, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu kuti Iye adawuka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho. 65 Pilato adati kwa iwo, Tengani alonda; mukani kalondereni monga mudziwa. 66 Ndipo iwo adamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo. Naikapo woyang`anira.

Mateyo 28

1 Ndipo kumathero kwa tsiku la Sabata, mbanda kucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Mariya Magadalene, ndi Mariya winayo, kudzawona manda. 2 Ndipo onani, padali chibvomezi chachikulu; pakuti m’ngelo wa Ambuye adatsika kuchokera Kumwamba nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. 3 Kuwonekera kwake kudali ngati mphezi, ndi chobvala chake choyeretsetsa ngati matalala: 4 Ndipo ndikuwopsa kwake alondawo adanthunthumira, nakhala ngati anthu akufa. 5 Koma m’ngelo adayankha, nati kwa akaziwo, Musawope inu: pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene adapachikidwa. 6 Iye mulibe muno iyayi: pakuti adauka, monga adanena. Idzani munomudzawone malo m’mene adagonamo Ambuye. 7 Ndipo pitani msanga, muwuze wophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuwona Iye komweko; onani, ndakuwuzani inu. 8 Ndipo iwo adachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukawuza wophunzira ake. 9 Ndipo pamene amamka kukawuza wophunzira ake, onani, Yesu adakomana nawo, nanena, Tikuwoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, nampembedza Iye. 10 Pomwepo Yesu adanena kwa iwo, Musawope; pitani, kawuzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiwona Ine kumeneko. 11 Ndipo pamene iwo adalikupita, onani, ena a alonda adafika ku mzinda nawuza ansembe akulu zonse zimene zidachitidwa. 12 Ndipo pamene adasonkhana pamodzi ndi akulu, adakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri. 13 Nanena, Kadzinenani kuti wophunzira ake anadza usiku namuba Iye m’mene ife tidali mtulo. 14 Ndipo ngati ichi chidzamveka ku makutu a kazembe, ife tidzamunyengerera iye ndi kukutetezani inu. 15 Ndipo iwo adalandira ndalamazo, nachita monga adawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe. 16 Pamenepo wophunzira khumi ndi m’modziyo adamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu adapangana nawo. 17 Ndipo pamene adamuwona Iye, adamlambira; koma ena adakayika. 18 Ndipo Yesu anadza nayankhula nawo, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi dziko lapansi. 19 Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera: 20 Ndikuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndidakulamulirani inu: ndipo onani Ine ndiri pamodzi ndi inu nthawi zonse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. Ameni.

Marko 1

1 Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. 2 Monga mwalembedwa mwa aneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu. 3 Mawu a wofuwula, m’chipululu, Konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. 4 Yohane anadza nabatiza m’chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima woloza kuchikhululukiro cha machimo. 5 Ndipo adatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje wa Yordano, powulula machimo awo. 6 Ndipo Yohane amkabvala ubweya wangamila, ndi lamba lachikopa m’chuwuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wa kuthengo. 7 Ndipo adalalikira kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zake ine. 8 Ine zowonadi ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera. 9 Ndipo kudali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m’Yordano. 10 Ndipo pomwepo, potuluka m’madzi, adawona Iye thambo litatseguka ndipo Mzimu adatsikira pa Iye monga nkhunda: 11 Ndipo mawu adatuluka kumwamba, wonena, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa , mwa Iyeyu ndikondwera bwino. 12 Ndipo pomwepo Mzimu udampititsa Iye kuchipululu. 13 Ndipo adakhala m’chipululu masiku makumi anayi nayesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo adamtumikira Iye. 14 Tsopano atatha kuperekedwa Yohane mundende, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, 15 Nanena, nthawi yakwanira ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; lapani, khulupirirani Uthenga Wabwino. 16 Ndipo pakuyenda m’mbali mwa nyanja ya galileya, adawona Simoni ndi Andreya, mbale wake, alimkuponya khoka m’nyanja; pakuti adali asodzi. 17 Ndipo Yesu adanena nawo, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu 18 Ndipo pomwepo adasiya makoka awo, namtsata Iye. 19 Ndipo atapita patsogolo pang’ono, adawona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wake, iwonso adali m’chombo ali kusoka makoka awo: 20 Ndipo pomwepo adawayitana iwo; ndipo adasiya atate wawo Zebedayo m’chombomo pamodzi ndi antchito wolembedwa, namtsata Iye. 21 Ndipo iwo adalowa m’Kapernawo; ndipo pomwepo pa tsiku la sabata Iye adalowa m’sunagoge naphunzitsa. 22 Ndipo adazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti adaphunzitsa monga mwini mphamvu, simonga alembi. 23 Ndipo pomwepo padali munthu m’sunagoge mwawo adali ndi mzimu wonyansa; ndipo adafuwula iye, 24 Kuti, Tisiyeni, tiri ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzatiwononga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. 25 Ndipo Yesu adawudzudzula, kuti, Khala chete, nutuLuka mwa iye. 26 Ndipo pamene mzimu wonyansa, pom’ng’amba iye ndi kufuwula ndi mawu akulu, udatuluka mwa iye. 27 Ndipo adazizwa onse, kotero kuti adafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu Iye alamula ngakhale mizimu yonyansa, ndipo idamvera Iye. 28 Ndipo kutchuka kwake kudabuka pompaja ku dziko lonse la Galileya lozungulurapo. 29 Ndipo pomwepo, potuluka m’sunagoge, iwo adalowa m’nyumba ya Simoni ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane. 30 Ndipo mayi wake amkazi wa Simoni adali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo adamuwuza za iye! 31 Ndipo anadza namgwira Iye pa dzanja, namuwutsa; ndipo nthawi yomweyo malungo adamleka, ndipo adawatumikira iwo. 32 Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nawo kwa Iye onse wodwala, ndi wogwidwa ndi ziwanda. 33 Ndipo mzinda wonse udasonkhana pakhomo 34 Ndipo adachiritsa anthu ambiri wodwala nthenda za mitundu mitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sadalole ziwandazo kuyankhula, chifukwa zidamdziwa Iye. 35 Ndipo m’mawa mwake adawuka usikusiku, natuluka napita pa yekha, napemphera kumeneko. 36 Ndipo Simoni ndi amzake adali naye, adamtsata Iye. 37 Ndipo pamene adampeza Iye, adanena naye, Akufunani Inu anthu onse. 38 Ndipo adanena kwa iwo, Tiyeni kwina, ku mizinda ili pafupi apa, kuti ndikalalikire komweko; pakuti ndadzera ntchito imeneyi. 39 Ndipo adalowa m’masunagoge mwawo m’Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda. 40 Ndipo adadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira Iye, ndi kunena ndi Iye. Ngati mufuna mukhoza kundikonza. 41 Ndipo Yesu adagwidwa chifundo, natambasula dzanja lake namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa. 42 Ndipo atangoyankhula nthawi yomweyo, khate lidamchoka, ndipo adakonzedwa. 43 Ndipo adamulamulira iye, namtulutsa pomwepo; 44 Ndipo adanena kwa iye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense; koma pita, ukadziwonetse wekha kwa wansembe, nuperekepo makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo 45 Ndipo iye adatuluka nayamba kulengeza ndithu, ndi kubukitsa nkhaniyo, kotero kuti Yesu sadakhoze kulowanso poyera mu mzinda, koma adakhala padera m’zipululu; ndipo anadza kwa Iye anthu wochokera ku madera onse.

Marko 2

1 Ndipo Iye adalowanso m’Kapernawo atapita masiku ena, ndipo kudamveka kuti adali m’nyumba. 2 Ndipo ambiri adasonkhana pamodzi, kotero kuti adasowa malo wowalandirirapo, ngakhale pakhomo pomwe. Ndipo adawalalikira iwo mawu. 3 Ndipo anadza kwa Iye wotenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anayi. 4 Ndipo pamene sadakhoze kufika kudali Iye, chifukwa cha khamu la anthu, adasasula denga pokhala Iye; ndipo pamene adatha kulibowola adatsitsa kama amene wodwala manjenjeyo adagona. 5 Pamene Yesu adawona chikhulupiriro chawo, adanena kwa wodwala manjenjeyo, Mwana, machimo ako akhululukidwa. 6 Koma adakhalapo ena alembi pamenepo amene adaganizira mumtima mwawo, 7 Kodi n’chifukwa chiyani munthu ameneyu akuchitira Mulungu mwano wotere? Akhoza ndani kukhululukira machimo, koma m’modzi, ndiye Mulungu? 8 Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mu mzimu wake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, adanena nawo, Muganiza bwanji zinthu izi m’mitima yanu? 9 Chapafupi n’chiti, kapena kumuwuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende? 10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nazo mphamvu zakukhululukira machimo pa dziko lapansi (adanena ndi wodwala manjenjeyo,) 11 Ndikuwuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu. 12 Ndipo pomwepo adanyamuka iye, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, zotere sitidaziwonepo ndi kale lonse. 13 Ndipo adatulukanso kumka m’mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo adawaphunzitsa. 14 Ndipo popita adawona Levi mwana wa Alifeyo atakhala polandirira msonkho, ndipo adanena naye, Tsata Ine, ndipo adanyamuka namtsata Iye. 15 Ndipo kudali kuti Yesu atakhala pachakudya m’nyumba mwake, ndipo amisonkho, ndi wochimwa ambiri adakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi wophunzira ake, pakuti adali ambiri, ndipo adamtsata Iye. 16 Ndipo pamene Alembi ndi Afarisi adawona Iye kuti alimkudya nawo wochimwa ndi amisonkho, adanena ndi wophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nawo amisonkho ndi wochimwa? 17 Ndipo pamene Yesu adamva ichi, adanena nawo, Wolimba safuna sing’anga, koma wodwala ndiwo; sindidadza kudzayitana wolungama, koma wochimwa kuti alape. 18 Ndipo wophunzira a Yohane ndi Afarisi adalimkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya wophunzira a Yohane, ndi wophunzira Afarisi, koma wophunzira anu sasala kudya? 19 Ndipo Yesu adanena nawo, Kodi akhoza kusala kudya ana a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nawo? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala. 20 Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya m`masiku amenewo. 21 Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yatsopano pa chobvala chakale; mwina chigamba chatsopanocho chikhoza kuzomoka kuyakaleyo, ndipo chibowo chake chikhala chachikulu. 22 Ndipo palibe munthu amathira vinyo watsopano m’mabotolo akale; pena vinyo adzaswa mabotolo, ndipo akhoza kuwonongeka vinyo, ndi mabotolo omwe; koma vinyo watsopano, amathiridwa m’mabotolo atsopano. 23 Ndipo kunali kuti adapita Iye pakati pa minda ya tirigu tsiku la sabata; ndipo wophunzira ake poyenda adayamba kubudula ngala za tirigu. 24 Ndipo Afarisi adanena kwa Iye, Tawonani, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la sabata? 25 Ndipo adanena nawo, simudawerenga konse chimene adachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene adali pamodzi naye? 26 Kuti adalowa m’nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yowonetsera yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo adawapatsanso iwo amene adali naye? 27 Ndipo adanena kwa iwo, sabata lidayikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha sabata: 28 Motero Mwana wa munthu ali Mbuye wa Sabata.

Marko 3

1 Ndipo adalowanso m’sunagoge; ndipo mudali munthu m’menemo adali ndi dzanja lake lopuwala. 2 Ndipo adamuyang’anira Iye ngati adzamchiritsa iye tsiku la sabata; kuti amtsutse Iye. 3 Ndipo Iye adanena ndi munthu adali ndi dzanja lopuwala, Tayimilira. 4 Ndipo adanena kwa iwo, N’kololedwa tsiku la sabata kuchita zabwino, kapena zoyipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma adakhala chete. 5 Ndipo m’mene adawawunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuwuma kwa mitima yawo, adanena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo adalitambasula; ndipo lidachira dzanja monga limzake. 6 Ndipo Afarisi adatuluka, ndipo pomwepo adamkhalira upo ndi Aherode monga momwe angamuwonongere Iye. 7 Ndipo Yesu adachokako pamodzi ndi wophunzira ake namka kunyanja; ndipo lidamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi la aku Yudeya, 8 Ndi wochokera ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordano, ndi a kufupi ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo adazichita, linadza kwa Iye. 9 Ndipo adayankhula kwa wophunzira ake, kuti chombo chaching`ono chidikire Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye. 10 Pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse wokhala nayo miliri adamkanikiza Iye, kuti akamkhudze, 11 Ndipo mizimu yonyansa, m’mene idamuwona Iye, idagwa pansi pamaso pake, nifuwula, niyiti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. 12 Ndipo pomwepo Iye adayilamulira kuti isamuwulule Iye. 13 Ndipo Iye adakwera m’phiri, nadziyitanira iwo amene adawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. 14 Ndipo adasanjika manja pa khumi ndi awiri kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kukalalikira. 15 Ndi kuti akhale nazo mphamvu zochiritsa ndi zotulutsa ziwanda. 16 Ndipo Simoni adamutcha Petro. 17 Ndi Yakobo mwana wa Zebedeyo, ndi Yohane m’bale wake wa Yakobo, iwo adawatcha Boanerge, ndiko kuti Ana a bingu; 18 Ndi Andreya, ndi Filipo ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi ndi Yakobo mwana waAlifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani, 19 Ndi Yudase Isikariyote, ndiye amene adampereka Iye. Ndipo adalowa m’nyumba. 20 Ndipo khamulo lidasonkhananso, kotero kuti sadadye iwo konse mkate. 21 Ndipo pamene abwenzi ake adamva adadza kudzamgwira Iye; pakuti adati adayaluka. 22 Ndipo alembi amene adatsika kuchokera ku Yerusalemu adati, Ali ndi Belizebule, ndipo ndi mkulu wawo wa ziwanda atulutsa ziwanda. 23 Ndipo adawayitana iwo, nanena nawo m’mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana? 24 Ndipo ufumu ukagawanika pa wokha, sukhoza kukhazikika. 25 Ndipo ngati nyumba igawanika pa iyo yokha, siyikhoza kukhazikika nyumbayo payokha. 26 Ndipo ngati Satana adziwukira mwini yekha, nagawanika sakhoza kuyima payekha, koma atsirizika. 27 Palibe munthu akhoza kulowa m’nyumba ya munthu wa mphamvu, ndi kuwononga katundu wake, koma ayambe wamanga munthu wa mphamvuyo; ndipo pamenepo adzawononga za m’nyumba mwake. 28 Indetu, ndinena ndi inu, Machimo onse ana anthu, ndi zamwano zili zonse adzachita adzakhululukidwa, 29 Koma ali yense amene adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma ali m’chiweruziro chowopsa chosantha; 30 Chifukwa adanena, Ali ndi mzimu wonyansa. 31 Ndipo anadza amake ndi abale ake, nayima kunja, namtumizira uthenga kumuyitana. 32 Ndipo khamu lambiri lidakhala pansi momzungulira; nanena kwa Iye, Onani, amayi anu ndi abale anu ali kunja akukufunani Inu. 33 Ndipo adawayankha iwo nanena, Amayi wanga ndi abale anga ndani? 34 Ndipo adawunguza wunguza iwo amene adakhala momzungulira Iye, nanena, Tawonani, amayi wanga ndi abale anga. 35 Pakuti ali yense adzachita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga ndi mlongo, ndi amayi.

Marko 4

1 Ndipo adayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo adasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti adalowa Iye m`chombo, nakhala m’nyanja; ndipo khamu lonse lidakhala pamtunda m’bali mwa nyanja. 2 Ndipo adawaphunzitsa zinthu zambiri m’mafanizo, nanena nawo m’chiphunzitso chake, 3 Mverani; Tawonani, wofesa adatuluka kukafesa: 4 Ndipo kudali, zitapita izi pamene amkafesa, zina zidagwa m’mbali mwa njira ndi mbalame zamumlengalenga zinadza ndi kuzidya. 5 Ndipo zina zinagwa pa nthaka ya mwala pamene panalibe dothi lambiri, ndipo pomwepo zidamera, koma zinalibe dothi lakuya: 6 Ndipo pamene dzuwa lidakwera zidapserera; ndipo popeza zidalibe mizu zidafota 7 Ndipo zina zinagwa pakati pa minga, ndipo minga idakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso. 8 Ndipo zina zinagwa m’nthaka yabwino, ndipo zidapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi. 9 Ndipo adanena kwa iwo, Amene ali nawo makutu akumva amve. 10 Ndipo pamene adakhala pa yekha, iwo amene adali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo adamfunsa Iye za mafanizo. 11 Ndipo Iye adanena nawo, Kwa inu kwapatsidwa kudziwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonsezi zichitidwa m’mafanizo. 12 Kuti kupenya apenye koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwe; kuti pena angatembenuke mtima ndi kukhululukidwa machimo awo. 13 Ndipo adanena nawo, Simudziwa kodi fanizo ili? ndipo mudzazindikira bwanji mafanizo onse? 14 Wofesa afesa mawu. 15 Ndipo iwo ndiwo am’mbali mwa njira mofesedwamo mawu; ndipo pamene adamva, pomwepo anadza Satana nachotsa mawu wofesedwa m`mitima mwawo. 16 Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pamwala, atamva mawu, awalandira pomwepo ndi kusekerera; 17 Ndipo alibe mizu mwa iwo wokha, koma apilira kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mawu, pomwepo akhumudwa. 18 Ndipo awa ndiwo wofesedwa paminga; iwo ndiwo amene adamva mawu, 19 Ndipo chisamaliro cha dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mawu, ndipo akhala wopanda chipatso. 20 Ndipo awa ndiwo wofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mawu, nawalandira, nabala zipatso zopindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi. 21 Ndipo adanena ndi iwo, kodi atenga nyali kuti akayibvundikire mbiya, kapena akayiyika pansi pa kama, osati kuti akayiyike pa choyikapo chake? 22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, kamene sikadzawonetsedwa; kapena kulibe kanthu kakukhala m’seli, kamene sikadzawululidwa. 23 Ngati munthu aliyense ali nawo makutu akumva, amve. 24 Ndipo adanena nawo, Samalirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesa nawo udzayesedwa kwa inu; ndipo inu amene mukumva kudzawonjezeredwa kwa inu. 25 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kali konse ali nako. 26 Ndipo adanena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbewu panthaka; 27 Ndipo akagona ndi kuwuka, usiku ndi usana, ndipo mbewu zikamera ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira. 28 Pakuti nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba m’mera, zitsata ngala, pamenepo maso wokhwima m’ngalamo. 29 Zikakhwima zipatso, pamenepo atumiza chikwanje, pakuti nthawi yokolola yafika. 30 Ndipo adanena, Tidzafanizira ndi chiyani Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzawulinganiza ndi fanizo lotani? 31 Uli ngati mbewu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ili yaying’ono mwa mbewu zonse za padziko lapansi. 32 Koma pamene ifesedwa, imela nikula koposa zitsamba zonse, nichita nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za mu mlengalenga zikhoza kubindikira munthunzi mwake. 33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri adayankhula nawo mawu, monga adakhoza kumva; 34 Ndipo sadayankhule nawo wopanda fanizo: koma mseli adatanthawuzira zonse kwa wophunzira ake. 35 Ndipo tsiku lomwelo, pofika madzulo, adanena kwa iwo, Tiwolokere tsidya lina. 36 Ndipo pamene adalitumiza khamulo adamtenga Iye, monga momwe adali, chombo. Ndipo padali zombo zazing`ono zina pamodzi ndi Iye. 37 Ndipo padawuka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde adagabvira m`chombo, motero kuti chombo chidayamba kudzaza. 38 Ndipo Iye mwini adali ku chiwongolero, chachombo nagona tulo, pamtsamiro; ndipo adamudzutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti tiri kuwonongeka ife? 39 Ndipo adadzuka, nadzudzula mphepo,nati kwa nyanja kuti, Tonthola nukhale bata, ndipo kudagwa bata lalikulu ndipo mphepo idaleka ndikugwa bata lalikulu. 40 Ndipo adanena nawo, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi? 41 Ndipo iwo adachita mantha akulu, nanena wina ndi mzake, Munthu uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Marko 5

1 Ndipo adafika tsidya lina la nyanja, ku dziko la Agerasa. 2 Ndipo pamene adatuluka m`chombomo, pomwepo adakomana naye munthu wotuluka ku manda wogwidwa ndi mzimu wonyansa. 3 Amene adayesa nyumba yake kumanda; ndipo panalibe munthu adakhoza kum’manganso, inde ngakhale ndi unyolo. 4 Pakuti ankamangidwa kawiri kawiri ndi matangadza ndi unyolo, ndipo adamwetula unyolo, naduladula matangadza; ndipo panalibe munthu adali ndi mphamvu yakumgwira. 5 Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, adakhala m’mapiri ndi m’manda, nafuwula, nadzitematema ndi miyala. 6 Ndipo pamene adamuwona Yesu kutali, adathamanga nampembedza Iye, 7 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, nanena, Ndiri ndi chiyani ndi inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikulumbirirani pa Mulungu musandizunze. 8 Pakuti adanena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu. 9 Ndipo adamfunsa iye, Dzina lako ndani? Ndipo adayankha kuti, Dzina langa ndine Legiyo; chifukwa tiri ambiri. 10 Ndipo adampempha Iye kwambiri kuti asayitulutsire kunja kwake kwa dziko. 11 Ndipo pamenepo padali gulu lalikulu la nkhumba zidali kudya kuphiri. 12 Ndipo mizimu yonse yoyipa idampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. 13 Ndipo Yesu adayilola kuti ichoke. Ndipo mizimu yonyansa idatuluka, nilowa munkhumba; ndipo gulu lidatsika ndi liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zidatsamwa m’nyanja. 14 Ndipo woziweta adathawa, nakanena ku m`mzinda, ndi kudziko. Ndipo adatuluka kudzawona chochitikacho. 15 Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo atakhala pansi, wobvala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene adali ndi Legiyo; ndipo adawopa iwo. 16 Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo adachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. 17 Ndipo adayamba kumpempha Iye kuti achoke m’malire awo. 18 Ndipo m’mene Iye adali kulowa m`chombo, adampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. 19 Ndipo Yesu sadamulole, koma adanena naye, Pita kwanu kwa abwenzi ako, nuwawuze zinthu zazikulu adakuchitira Ambuye, ndi kuti adakuchitira chifundo. 20 Ndipo adachoka nayamba kulalikira ku Dekapolisi zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse adazizwa. Yesu achiritsa mkazi kunthenda yokha mwazi, naukitsa mwana 21 Ndipo pamene Yesu adawolokanso m`chombo kupita tsidya lina, khamu lalikulu lidasokhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja. 22 Ndipo wonani, adadzako m’modzi wa akulu a sunagoge dzina lake Yairo; ndipo pakuwona, iye adagwada pamapazi ake. 23 Ndipo nampepha Iye kwambiri nanena naye, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalimkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muyike manja anu pa iko, kuti kachiritsidwe, ndi kukhala ndi moyo. 24 Ndipo Yesu adamka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu lidamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye. 25 Ndipo mkazi wina amene adali ndi nthenda ya mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, 26 Ndipo adamva zowawa zambiri mwa a sing’anga ambiri, nalipira zonse adali nazo osachira m’pang’ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula, 27 Ndipo m’mene iye adamva mbiri yake ya Yesu, anadza m’khamu kumbuyo kwake, nakhudza chobvala chake. 28 Pakuti adanena iye, Ngati ndikhudza ngakhale zobvala zake ndidzachiritsidwa. 29 Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake ya mwazi idaphwa; ndipo adazindikira m’thupi kuti adachiritsidwa ku m`liri wake. 30 Ndipo pomwepo Yesu, pamene adazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, adapotolokera kwa womkanikizawo, nanena, Ndani adakhudza zobvala zanga? 31 Ndipo wophunzira ake adanena kwa Iye, Mukuwona kuti khamu liri kukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani? 32 Ndipo Iye adawunguzawunguza kuti awone iye amene adachita ichi. 33 Koma mkaziyo powopa ndi kunthunthumira, podziwa chimene adamchitira mwa iye, adadza, nagwa pa Iye, namuwuza Iye chowona chonse. 34 Ndipo Iye adati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; pita mu mtendere, nukhale wochira kumliri wako. 35 M’mene Iye adali chiyankhulire, adafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; ubvutiranjinso Mphunzitsi? 36 Mwamsanga atamva Yesu mawu adayankhulidwawo adanena kwa mkulu wa sunagoge, Usawope, khulupilira kokha. 37 Ndipo sadalole munthu aliyense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane m’bale wake wa Yakobo. 38 Ndipo adafika ku nyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo adawona chipiringu, ndi wochita maliro ndi wokuwa ambiri. 39 Ndipo m’mene adalowa, adanena nawo, Mubuma ndi kulira chifukwa chiyani? Buthuli silidafe koma liri m’tulo. 40 Ndipo adamseka Iye pwepwete, koma pamene Iye adawatulutsa onse, adatenga atate ndi amake abuthulo ndi ajawo adali naye, nalowa m’mene mudali buthulo 41 Ndipo adagwira dzanja lake la buthulo, nanena kwa iye, Talita koumi; ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe. Uka. 42 Ndipo pomwepo buthulo lidawuka niliyenda; pakuti lidali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu. 43 Ndipo adawalamulira kwambiri kuti asadziwe, ichi munthu m’modzi, nawawuza kuti ampatse iye kudya.

Marko 6

1 Ndipo Iye adatuluka kumeneko; nafika ku dziko la kwawo; ndipo wophunzira ake adamtsata. 2 Ndipo pofika tsiku la sabata, adayamba kuphunzitsa m’sunagoge; ndipo ambiri adamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani? Ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake? 3 Kodi uyu sim’misiri wa matabwa, mwana wa Mariya, m’bale wawo wa Yakobo, ndi Yosefe, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ake Sali nafe pano kodi? Ndipo adakhumudwa ndi Iye. 4 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, M’neneri sakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwawo ndimo ndi pakati pa abale ake, ndi m’nyumba yake. 5 Ndipo kumeneko sadakhoza Iye kuchita ntchito zamphamvu konse, koma kuti adayika manja ake pa anthu wodwala wowerengeka, nawachiritsa. 6 Ndipo adazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Ndipo adayendayenda m’midzi yozungulirapo, naphunzitsa 7 Ndipo adadziyitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa; 8 Ndipo adawalamulira kuti asatenge kanthu ka pa ulendo wawo, koma ndodo yokha; asatenge lamba, mkate, kapena ndalama m’matumba awo; 9 Koma abvale nsapato; ndipo osati abvale malaya awiri. 10 Ndipo adanena nawo, Kumalo kuli konse mukalowa m’nyumba, khalani komweko kufikira mutachokako. 11 Ndipo aliyense amene sakulandirani, kapena kumvera inu, pochoka kumeneko sansani fumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. Indetu ndinena ndi inu kuti patsiku la chiweruziro mlandu wa mzindawo udzakhala waukulu koposa wa Sodomu ndi Gomora. 12 Ndipo adatuluka nalalikira kuti anthu alape. 13 Ndipo adatulutsa mizimu yoyipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri, wodwala, nawachiritsa. 14 Ndipo mfumu Herode adamva za Iye; (pakuti dzina lake lidatchuka ponse ponse) ndipo adanena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake ntchito za mphamvuzi zichitachita mwa Iye. 15 Koma ena adanena kuti, Ndiye Eliya, Adati enanso, ndiye m’neneri, kapena m`modzi wa aneneriwo. 16 Koma pamene Herode adamva, adanena, Ndi Yohane amene ndinamdula mutu, wawuka kwa akufa. 17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nam’manga m’nyumba ya ndende, chifukwa cha Herodiya, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye. 18 Pakuti Yohane adanena kwa Herode, sikuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu. 19 Chifukwa cha ichi adakangana momtsutsa Herodiya nafuna kumumpha iye koma adalemphera. 20 Pakuti Herode adawopa Yohane podziwa kuti adali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo adamsunga iye. Ndipo pamene adamva iye, adachita zambiri, nakondwera pakumva iye. 21 Ndipo pamene lidafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye adawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu wotchuka a ku Galileya; 22 Ndipo pamene mwana wa mkazi wa Herodiya adalowa yekha nabvina, adakondweretsa Herode ndi iwo wokhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo idati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chiri chonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe. 23 Ndipo adamlumbirira iye, kuti, chiri chonse ukandipempha ndidzakupatsa, ngakhale kukugawira ufumu wanga. 24 Ndipo adatuluka, nati, kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye adati, Mutu wake wa Yohane M’batizi. 25 Ndipo pomwepo adalowa mwachangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane M’batizi m`mbale. 26 Ndipo mfumu idamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo wokhala pa chakudya, sadafune kumkaniza. 27 Ndipo pomwepo mfumu idatuma wokamumpha, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye adapita namdula mutu m’nyumba ya ndende. 28 Ndipo adamtengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthulo lidaupereka kwa amake. 29 Ndipo m’mene wophunzira ake adamva, anadza nanyamula mtembo wake nawuyika m’manda. 30 Ndipo atumwi adasonkhana mwa iwo wokha kwa Yesu; namuwuza zinthu ziri zonse adazichita, ndi kuziphunzitsa. 31 Ndipo Iye adanena nawo, Idzani inu nokha padera ku malo a chipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka adali piringu piringu ndipo adalibe nthawi yokwanira kuti adye 32 Ndipo adachoka pa chombo kupita ku malo achipululu padera. 33 Ndipo anthu adawawona ali kupita, ndipo ambiri adawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, nadza pamodzi kwa Iye wochokera m’mizinda yonse nawapitirira. 34 Ndipo Yesu pamene adatuluka, nawona khamu lalikulu la anthu, anagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa adali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo adayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. 35 Ndipo pamene tsiku lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye wophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yatha ndithu. 36 Muwatumize iwo kuti apite, alowe ku milaga ndi ku midzi yozungulira, kuti akadzigulire wokha kanthu kakudya. Pakuti alibe kanthu kakudya. 37 Koma Iye adayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo adanena naye, kodi tipite ife ndi kugula mikate ya makobiri mazana awiri ndi kuwapatsa kudya? 38 Ndipo Iye adanena kwa iwo, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani mukawone. Ndipo m’mene adadziwa adanena, Isanu ndi nsomba ziwiri. 39 Ndipo adawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulu magulu pawudzu. 40 Ndipo adakhala pansi mabungwe mabungwe a makumi khumi ndi a makumi asanu. 41 Ndipo pamene Iye adatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo adayang’ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa iyo kwa wophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri adagawira onsewo. 42 Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. 43 Ndipo adatola makombo, mitanga khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba. 44 Ndipo amene adadya mikateyo adali amuna zikwi zisanu. 45 Ndipo pomwepo Iye adalamulira wophunzira ake alowe m`chombo, ndi kutsogolera kupita kutsidya lija ku Betsayida, m’mene Iye yekha adali kuwuza khamulo kuti lichoke. 46 Ndipo atatsanzikana nalo, adachoka Iye, nalowa m’phiri kukapemphera. 47 Ndipo pofika madzulo chombo chidali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha adali pamtunda. 48 Ndipo pakuwawona ali kubvutika ndi kupalasa, pakuti mphepo idadza mokomana nawo, ndipo pa ulonda wachinayi wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire. 49 Koma iwo, pamene adamuwona Iye alikuyenda panyanja, adayesa kuti ndi mzukwa, nafuwula: 50 Pakuti iwo onse adamuwona Iye, nabvutika. Koma pomwepo adawayankhula nanena kwa iwo, Kondwerani; Ndinetu, musawope. 51 Ndipo Iye adakwera, nalowa kwa iwo chombo, ndipo mphepo idaleka; ndipo anadabwa kwakukulu koposa muyeso mwa iwo wokha. 52 Pakuti sadazindikire za chozizwitsa cha mikateyo, pakuti mitima yawo idawumitsidwa. 53 Ndipo atawoloka iwo, adafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padowoko. 54 Ndipo pamene adatuluka m’chombo adamzindikira Iye pomwepo. 55 Ndipo adathamanga dziko lonselo mozungulira nayamba kunyamula anthu wodwala pamphasa zawo, kufika nawo kumene adamva kuti analiko Iye. 56 Ndipo kumene kulikonse adalowa Iye m’midzi, kapena m’mizinda, kapena m’milaga, anthu adagoneka wodwala m`misewu, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chobvala chake; ndipo onse amene adamkhudza adachiritsidwa.

Marko 7

1 Ndipo adasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi ena alembi, wochokera ku Yerusalemu. 2 Ndipo pamene adawona ena a wophunzira ake akudya mkate ndi m’manja mwakuda, ndi mosasamba, adampezerapo chifukwa. 3 Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse samadya osasamba m’manja mwawo, kuti asunge mwambo wa akulu. 4 Ndipo pochokera ku m’sika, sakudya asanasambe m’thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri adazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa ndi magome. 5 Ndipo Afarisi ndi alembi adamfunsa Iye, Bwanji wophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wawo ndi m’manja mwakuda? 6 Iye adawayankha nati kwa iwo, Yesaya adanenera bwino za inu wonyenga, monga kwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ikhala kutali ndi Ine. 7 Koma andilambira Ine kwa chabe, ndi kuphunzitsa ziphunzitso za malamulo a anthu. 8 Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu, monga kutsuka miphika ndi zikho; ndi zinthu zina zambiri zimene muchita. 9 Ndipo adanena nawo, Mochenjera mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu. 10 Pakuti Mose adati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wonenera zoyipa atate wake kapena amayi wake, afe imfa: 11 Koma inu munena, Ngati munthu akati kwa atate wake, kapena amayi wake, Korbani, ndiko kuti mphatso imene ukadathandizidwa nayo ndi ine; adzakhala womasulidwa. 12 Ndipo simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amayi wake; 13 Muyesa achabe mawu a Mulungu monga mwa mwambo wanu, umene mudaupereka; ndi zinthu zotere zambiri muzichita. 14 Ndipo pamene adadziyitaniranso khamu la anthu kwa Iye, adanena nawo, Mverani Ine nonsenu ndipo mudziwitse: 15 Kulibe kanthu kunja kwa munthu kolowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zotuluka mwa iye, ndizo zomdetsa munthu. 16 Ngati munthu ali nawo makutu akumva, muloleni amve. 17 Ndipo m’mene Iye adalowa m’nyumba kusiyana ndi khamulo, wophunzira ake adamfunsa Iye za fanizolo. 18 Ndipo adanena nawo, Inunso mukhala wopanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kali konse kochokera kunja kolowa mwa munthu sikangathe kumdetsa iye; 19 Chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m’mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo ndipo potero adayeretsa zakudya zonse. 20 Ndipo adati, chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. 21 Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu mutuluka maganizo woyipa, za chigololo, chiwerewere, kupha, 22 Kuba, kusilira kuchita zoyipa, chinyengo, chinyanso, diso loyipa, mwano, kudzikuza, kupusa: 23 Zoyipa izi zonse zichokera mkati nizidetsa munthu. 24 Ndipo Iye adawuka nachoka kumeneko, nanka ku malire a ku Turo ndi Sidoni. Ndipo adalowa m’nyumba, nafuna kuti asadziwe munthu aliyense; ndipo sadakhoza kubisika. 25 Pakuti mkazi wina amene adali ndi kabuthu kake kamene kadali ndi mzimu wonyansa. Pamene adamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake. 26 Koma mkaziyo adali Mhelene, mtundu wake Msuro-Fonika. Ndipo adampempha Iye kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake. 27 Koma Yesu adanena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti sibwino kutenga mkate wa ana, ndi kuwutayira tiagalu. 28 Ndipo iye adayankha nati kwa Iye, Inde Ambuye: tingakhale tiagalu tapansi pa gome timadyako nyenyeswa za ana. 29 Ndipo adati kwa iye, Chifukwa cha mawu amenewa, Pita; chiwanda chatuluka mwa mwana wako wamkazi. 30 Ndipo pamene adafika kunyumba kwake, adapeza mwana wakeyo atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka. 31 Ndipo adatulukanso m’malire a ku Turo, ndi Sidoni, adafika ku nyanja ya Galileya, kupyola pakati pa mayiko a Dekapoli. 32 Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wa chibwibwi; ndipo adampempha Iye kuti ayike manja ake pa iye. 33 Ndipo adampatula pa khamu la anthu pa yekha, namulonga zala zake m’makutu mwake, nalabvula malobvu, nakhudza lilime lake; 34 Ndipo pakuyang`ana kumwamba, adawusa moyo, nanena kwa iye Efata ndiko kuti, Tatseguka. 35 Ndipo pomwepo makutu ake adatseguka, ndipo chomangira lilime lake chidamasulidwa ndipo adayankhula chilunjikire. 36 Ndipo adalengeza kopambana kuti asawuze munthu aliyense; koma monga momwe Iye adawalamulitsa momwenso makamaka adalengeza kopambana. 37 Ndipo anadabwa kwakukulu, koposa muyeso nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale wogontha awamvetsa, ndi wosayankhula awayankhulitsa.

Marko 8

1 Masiku amenewo pakukhalanso khamu lalikulu la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, Yesu adadziyitanira wophunzira ake kwa Iye yekha, nanena nawo. 2 Ndikumva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi Ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya. 3 Ndipo ngati ndiwawuza iwo kuti azipita kwawo osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali. 4 Ndipo wophunzira ake adamuyankha Iye, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yokhutitsa anthu awa m’chipululu muno? 5 Ndipo adawafunsa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo adati, Isanu ndi iwiri. 6 Ndipo adalamulira anthu kuti akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa wophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo adapereka kwa anthuwo. 7 Ndipo adali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anadalitsa, nalamulira kuti iwo atipereke itonso. 8 Ndipo adadya, nakhuta; ndipo adatola makombo madengu asanu ndi awiri. 9 Ndipo iwo amene adadya adali ngati zikwi zinayi; ndipo Iye adawatumiza apite. 10 Ndipo pomwepo adalowa m’chombo ndi wophunzira ake, ndipo adafika ku mbali ya ku Dalimanuta. 11 Ndipo Afarisi adatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera kumwamba, kumuyesa Iye. 12 Ndipo adawusa moyo mu mzimu wake, nanena, Anthu a m’badwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati Chizindikiro sichidzapatsidwa kwa m’badwo uno! 13 Ndipo adawasiya iwo, nalowanso m’chombo, nachoka kupita kutsidya lina. 14 Ndipo wophunzira adayiwala kutenga mikate, ndipo adalibe mkate m’chombo koma umodzi wokha. 15 Ndipo Iye adawalamulira iwo, nanena, chenjerani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode. 16 Ndipo adatsutsana wina ndi mzake, nanena kuti, chifukwa chakuti tiribe mikate. 17 Ndipo pamene Yesu adazindikira, adanena nawo, Bwanji mukutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, ndikudziwitsa? Kodi mitima yanu ndi yowuma? 18 Pokhala nawo maso simupenya kodi? Ndipokhala nawo makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi? 19 Pamene tidanyema mikate isanu ndi kugawira kwa anthu zikwi zisanu, Kodi mudatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Iwo adanena kwa Iye, khumi ndi iwiri. 20 Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinayi, mudatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Ndipo adanena, Isanu ndi iwiri. 21 Ndipo Iye adanena nawo, Nanga n’chifukwa chiyani simukuzindikira? 22 Ndipo anadza ku Betsaida; ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze iye. 23 Ndipo adamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mzinda; ndipo atamthira malobvu m’maso mwake, nayika manja pa iye, adamfunsa iye, Uwona kanthu kodi? 24 Ndipo adakweza maso, nanena ndikuwona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo. 25 Patatha izi adayikanso manja m’maso mwake, ndipo adampenyetsa kumwamba, nachiritsidwa, nawona munthu aliyense bwino bwino. 26 Ndipo adamtumiza apite kwawo, nanena, Usalowe konse m’muzinda kapena kuwuza wina ali yense mumzinda 27 Ndipo adatuluka Yesu ndi wophunzira ake, nalowa ku mizinda ya ku Kayisareya wa Filipi; ndipo panjira adawafunsa wophunzira ake, nanena nawo, Kodi anthu amanena kuti Ine ndine yani? 28 Ndipo adayankha nati, Yohane M`batizi; ndi ena Eliya; koma ena, M’modzi wa aneneri. 29 Ndipo Iye adati kwa iwo, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro adayankha nanena naye, Ndinu Khristu. 30 Ndipo adawalamulira iwo kuti asawuze munthu ndi m’modzi za Iye. 31 Ndipo adayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo pakutha masiku atatu akawuke. 32 Ndipo mawuwo adanena poyera. Ndipo Petro adamtenga Iye, nayamba kumdzudzula Iye. 33 Koma pamene adapotoloka, napenya wophunzira ake, adamdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu koma za anthu. 34 Ndipo pamene adadziyitanira anthu pamodzi ndi wophunzira ake, adati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine. 35 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya; ndipo yense wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino adzaupulumutsa. 36 Pakuti munthu apindulanji akadzilemeleretsa dziko lonse lapansi, natayapo moyo wake? 37 Kapena munthu adzapereka chiyani chosinthana ndi moyo wake? 38 Pakuti aliyense wochita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mawu anga mu m’badwo uno wachigololo ndi wochimwa. Mwana wa munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nawo angelo ake woyera, mu ulemerero wa Atate wake.

Marko 9

1 Ndipo adanena nawo, Indetu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena ayimilira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira atawona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu. 2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, ndi Yakobo ndi Yohane, nakwera nawo pa phiri lalitali padera pa wokha; ndipo adasinthika pamaso pawo: 3 Ndipo zobvala zake zidakhala zonyezimira, zoyera mbu kuposa; monga ngati muwomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsayi. 4 Ndipo adawonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikuyankhulana ndi Yesu. 5 Ndipo Petro adayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, Kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange mahema atatu; imodzi yanu, ndi wina wa Mose ndi wina wa Eliya. 6 Pakuti sadadziwa chimene adzanena; chifukwa adachita mantha ndithu. 7 Ndipo padadza mtambo wophimba iwo, ndipo mawu adatuluka mu mtambowo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye. 8 Ndipo dzidzidzi powunguzawunguza, sadapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni. 9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye adawalamulira kuti asawuze munthu aliyense zinthu zimene adaziwona kufikira pamene Mwana wa munthu akadzawuka kwa akufa ndipo. 10 Ndipo adasunga mawuwo mwa iwo wokha, nafunsana mwa iwo wokha, kuti kuwuka kwa akufa kutanthawuzanji? 11 Ndipo adamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena bwanji kuti adzayamba kufika Eliya? 12 Ndipo Iye adayankha nanena nawo, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzabwezeretsa zinthu zonse; nanga zalembedwa bwanji za Mwana wa munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe? 13 Koma ndinena ndi inu Kuti Eliya adabwera kale, ndipo adamchitiranso ziri zonse iwo adazifuna, monga kwalembedwa za iye. 14 Ndipo pamene anadza kwa wophunzira ake, adawona khamu lalikulu la anthu wozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nawo. 15 Ndipo pomwepo anthu onse, pakumuwona Iye, adazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namulonjera. 16 Ndipo adafunsa alembi, Mufunsana nawo chiyani? 17 Ndipo wina wa m’khamulo adamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nawo mzimu wosayankhula; 18 Ndipo ponse pamene umtenga iye, ung`amba iye; ndipo achita thobvu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndidayankhula nawo wophunzira anu kuti awutulutse; koma sadakhoza. 19 Ndipo Iye adawayankha iwo nanena, M`bado wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu nthawi yaitali yanji? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine. 20 Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuwona iye, pomwepo mzimuwo udam’ng’amba kowopsa; ndipo adagwa pansi nabvimbvinika ndi kuchita thobvu. 21 Ndipo Iye adafunsa atate wake, kuti chimenechi chidayamba liti kumgwira? Ndipo adati, akali mwana. 22 Ndipo kawiri kawiri umamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuwononga iye; koma ngati mukhoza kuchita kanthu tithandizeni, ndi kutichitira chifundo. 23 Ndipo Yesu adanena naye, Ngati mukhulupilirira, zinthu zonse zitheka kwa iye wokhulupirira. 24 Pomwepo atate wa mwana adafuwula, nanena ndi misozi, Ambuye, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga. 25 Ndipo pamene Yesu adawona kuti khamu la anthu liri kuthamangira pamodzi, adadzudzula mzimu woyipawo, nanena ndi uwo, mzimu wosayankhula ndi wongontha iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye. 26 Ndipo mzimu udafuwula, num’ngambitsa, udatuluka, ndipo mwana adakhala ngati wakufa, kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira. 27 Koma Yesu adagwira dzanja lake, nam’nyamutsa; ndipo adayimilira. 28 Ndipo pamene Iye adalowa m’nyumba, wophunzira ake adafunsa mtseri kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuwutulutsa? 29 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi pemphero ndi kusala kudya. 30 Ndipo adachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sadafune kuti munthu aliyense adziwe. 31 Pakuti adaphunzitsa wophunzira ake, nanena nawo kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzawukanso tsiku lachitatu. 32 Koma iwo sadazindikira mawuwo, nawopa kumfunsa Iye. 33 Ndipo Iye anadza ku Kapernao; ndipo pamene adakhala m’nyumba, Iye adawafunsa, Mudali kutsutsana chiyani panjira? 34 Koma iwo adakhala chete; pakuti adatsutsana wina ndi mzake panjira kuti, wamkulu ndani? 35 Ndipo m’mene adakhala pansi adayitana khumi ndi awiriwo; nanena nawo, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wa kuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse. 36 Ndipo adatenga kamwana, nakayika pakati pawo, ndipo pamene adakayangata m`manja, ananena nawo, 37 Munthu aliyense amene adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, adzalandira Ine; ndipo yense amene adzalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene adandituma Ine. 38 Ndipo Yohane adamuyankha Iye, nati: Mpulumutsi, tidawona munthu alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tidamletsa, chifukwa sadali kutsata ife. 39 Koma Yesu adati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita chozizwa m’dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoyipa. 40 Pakuti iye wosatsutsana ndi ife ali kumbali yathu. 41 Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake. 42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi katiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wa mphero ukolowekedwe m’khosi mwake, naponyedwe m’nyanja. 43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: n’kwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m’gehena, wa moto umene sudzakhoza kuzimitsidwa 44 Kumene mphutsi yawo siyifa, ndipo moto suzimitsidwa. 45 Ndipo ngati phazi likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m`moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino kuposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m’gehena wa moto umene sudzakhoza kuzimitsidwa. 46 Kumene mphutsi yawo simafa ndiponso moto suzimitsidwa. 47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe mu Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m’gehena wa moto. 48 Kumeneko mphutsi yawo siyikufa, ndipo moto suzimitsidwa. 49 Pakuti onse adzathiridwa ndi mchere wa moto, ndi nsembe ili yonse idzathiridwa ndi m’chere. 50 Mchere ndi wabwino; koma ngati mchere usukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mzake.

Marko 10

1 Ndipo adanyamuka Iye kumeneko, nadza ku malire a ku Yudeya ndi kutsidya lija la Yordano; ndipo adasonkhananso kwa Iye anthu ; ndipo monga adazolowera, adawaphunzitsanso. 2 Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, adamfunsa Iye: kodi nkololedwa kuti munthu achotse mkazi wake? kumuyesa Iye. 3 Ndipo Iye adayankha nati kwa iwo, Kodi Mose adakulamulirani inu chiyani? 4 Ndipo adati Mose adalola kulembera kalata wachilekaniro, ndi kumchotsa iye. 5 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu adakulemberani lamulo ili. 6 Koma kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe Mulungu adawapanga iwo mwamuna ndi mkazi. 7 Pachifukwa ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi ake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake; 8 Ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. 9 Chifukwa chake chimene Mulungu adachimanga pamodzi, asachilekenitse munthu. 10 Ndipo m’nyumba wophunzira adamfunsanso za chinthu ichi. 11 Ndipo Iye adanena nawo, munthu ali yense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo. 12 Ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu. 13 Ndipo adadza nato kwa Iye tiana, kuti atikhudze: ndipo wophunzira ake adawadzudzula iwo amene adadza nato. 14 Koma pamene Yesu adawona adakwiya kwambiri, ndipo adati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere. 15 Indetu ndinena ndi inu, munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse. 16 Ndipo Iye adatiyangata ndi manja ake, natidalitsa, ndi kuyika manja ake pa ito. 17 Ndipo pamene Iye adatuluka kutsata njira, adamthamangira m`modzi wolamulira, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha? 18 Ndipo Yesu adati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma m’modzi ndiye Mulungu. 19 Udziwa malamulo usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, usanyenge, lemekeza atate wako ndi amako. 20 Ndipo iye adayankha nati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndidazisunga kuyambira ndiri mwana. 21 Ndipo Yesu adamyang’ana, namkonda, nati kwa iye. Chinthu chimodzi chikusowa: pita gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m’mwamba; ndipo ukadze kuno,senza mtanda unditsate Ine. 22 Ndipo adakhumudwa ndi mawu awa, ndipo adachoka iye ali ndi chisoni; pakuti adali ndi chuma chambiri. 23 Ndipo Yesu adawunguzawunguza, nanena ndi wophunzira ake, Wokhala ndi chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu mobvutika kwambiri! 24 Ndipo wophunzirawo adazizwa ndithu ndi mawu ake. Koma Yesu adayankhanso nanena nawo, Ananu, nkobvuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu! 25 Ndi kwapafupi kuti ngamila ipyole pa diso la singano koposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu. 26 Ndipo anadabwa koposa muyeso, nanena kwa iwo wokha, ndipo angathe kupulumuka ndani? 27 Yesu adawayang’ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu: koma kutheka ndi Mulungu pakuti ndi Mulungu zinthu zonse zitheka. 28 Petro adayamba kunena naye, Onani, ife tidasiya zonse, ndipo tidakutsatani Inu. 29 Yesu adayankha nati, Indetu ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga wabwino. 30 Koma adzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale ndi alongo ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi ili mkudza, moyo wosatha. 31 Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala woyamba. 32 Ndipo iwo adali m’njira ali kupita kumka ku Yerusalemu; ndipo Yesu adalikuwatsogolera; ndipo iwo adazizwa; ndipo pamene adalikumtsata adachita mantha. Ndipo Iye adatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwawuza zinthu zimene zidzamchitikira Iye. 33 Nati, Tawonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi; ndipo iwo adzamuweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu. 34 Ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malobvu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo patsiku la chitatu adzawukanso. 35 Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chiri chonse tidzakhumba kwa Inu. 36 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani? 37 Ndipo iwo adati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale m’modzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, muulemerero wanu. 38 Koma Yesu adati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndidzabatizidwa nawo Ine? 39 Ndipo adati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu adati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamweradi; ndipo ubatizo ndibatizidwa nawo Ine, mudzabatizidwadi nawo. 40 Koma kukhala ku dzanja langa lamanja, kapena kulamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kudzapatsidwa kwa iwo amene kudakonzedweratu. 41 Ndipo pamene khumiwo adamva, adayamba kusasangalalitsidwa ndi Yakobo ndi Yohane. 42 Ndipo Yesu adawayitana, nanena nawo, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye wa amitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu awo amachita ulamuliro pa iwo. 43 Koma mwa inu sikutero ayi; koma amene aliyense afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu; 44 Ndipo amene ali yense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala mtumiki wa onse. 45 Pakuti ndithu, Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa ambiri. 46 Ndipo iwo adafika ku Yeriko; ndipo m’mene Iye adalikutuluka mu Yeriko, ndi wophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Tineyu, Bartimeyu wakhungu adakhala pansi m’mbali mwa njira kumapempha. 47 Ndipo pamene adamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuwula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo. 48 Ndipo ambiri adamudzudzula kuti atonthole; koma makamaka adafuwulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. 49 Ndipo Yesu adayima nati, Mwitaneni. Ndipo adayitana munthu wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka akuyitana. 50 Ndipo iye adataya chofunda chake, nadzuka, nadza kwa Yesu. 51 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo munthu wakhunguyo adati kwa Iye, Ambuye, ndilandire kuwona kwanga. 52 Ndipo Yesu adati kwa iye, Pita; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo adapenyanso; namtsata Yesu panjira.

Marko 11

1 Ndipo pamene iwo adayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, adatuma awiri mwa wophunzira ake. 2 Ndipo adati kwa iwo, Pitani lowani m’mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu adakhalapo kale lonse; m’masuleni iye, ndipo mubwere naye. 3 Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Mukati, Ambuye akumfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno. 4 Ndipo adachoka napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo pamphambano pamene njira ziwiri zakumana, nam`masula iye. 5 Ndipo ena woyima kumeneko adanena nawo, Muchita chiyani ndi kumasula mwana wa bulu? 6 Ndipo adati kwa iwo monga momwe adawalamulira Yesu: ndipo adawalola iwo apite naye. 7 Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, nayika zobvala zawo pa iye, ndipo Iye adakhala pamenepo. 8 Ndipo ambiri adayala zobvala zawo panjira; ndipo ena anadadula nthambi zamitengo naziyala njira. 9 Ndipo iwo amene adatsogola ndi iwo ankamtsata, adafuwula nanena, Hosana wodalitsika Iye amene akudza m`dzina la Ambuye. 10 Wodalitsika ukhale ufumu wa atate wathu Davide umene ukudza dzina la Ambuye: Hosana m` Mwambamwamba. 11 Ndipo Yesu adalowa mu Yerusalemu, ndipo nalowa m’kachisi; ndipo m’mene adawunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo adatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. 12 Ndipo m’mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye adamva njala. 13 Ndipo adawona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye mokondwera, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m’mene adafikako adapeza palibe kanthu koma masamba wokha; pakuti sidali nyengo yake ya nkhuyu. 14 Ndipo Yesu adayankha nanena ndi uwo, munthu sadzadyanso zipatso zako kuyambira tsopano mpaka nthawi zonse. Ndipo wophunzira ake adamva. 15 Ndipo adafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Yesu adalowa m’kachisi, nayamba kutulutsa wogulitsa ndi wogula malonda m’kachisimo, nagubuduza magome a wosinthana ndalama, ndi mipando ya wogulitsa nkhunda. 16 Ndipo sadalole kuti munthu aliyense anyamule chotengera kupyola pakati pa kachisi. 17 Ndipo adaphunzitsa, nanena nawo, Sikudalembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwayiyesa phanga la mbava. 18 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adamva, nafunafuna njira yomuwonongera Iye; pakuti adamuwopa, chifukwa khamu lonse la anthu lidazizwa ndi chiphunzitso chake. 19 Ndipo pakufika madzulo adatuluka Iye mumzinda. 20 Ndipo m’mene adapitapo m’mawa mwake, adawona kuti mkuyu uja udawuma kuyambira kumizu. 21 Ndipo Petro adakumbukira, nanena naye, Amphunzitsi, onani, wafota mkuyu uja mudautemberera. 22 Ndipo Yesu adayankha nanena nawo, Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23 Indetu ndinena ndi inu, Kuti munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupilira kuti chimene achinena chidzachitidwa, adzakhala nazo zonse zimene azinena. 24 Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu ziri zonse mukazikhumba pamene mupemphera, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo. 25 Ndipo pamene muyimilira ndi kupemphera, khululukirani ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu. 26 Koma ngati simukhululukira Atate wanu ali m’mwamba sadzakukhululukiranso inu zochimwa zanu. 27 Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m’mene Iye adali kuyenda m’kachisi, adafika kwa Iye ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu; 28 Ndipo adati kwa iye, Izi muzichita ndi ulamuliro wotani? Kapena adakupatsani ndani ulamuliro uwu wochita izi? 29 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Ndikufunsaninso inu funso limodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuwuzani ulamuliro umene ndichita nawo zinthu zimenezi. 30 Kodi ubatizo wa Yohane uchokera kumwamba kapena kwa anthu? Mundiyankhe Ine. 31 Ndipo adatsutsana mwa iwo wokha, nanena, Tikati, udachokera kumwamba; adzanena Iye, ndipo simudakhulupirira iye bwanji? 32 Koma tikati kwa anthu; iwo adawopa anthuwo; pakuti anthu onse adamuyesa Yohane m’neneri ndithu. 33 Ndipo iwo adayankha nati kwa Yesu, Sitingakuwuzeni. Ndipo Yesu adanena nawo, Inenso sindikuwuzani ulamuliro umene ndichita nawo zinthu zimenezi

Marko 12

1 Ndipo Iye adayamba kuyankhula nawo m’mafanizo. Munthu wina adalima munda wa mphesa, nawuzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa wolima munda, napita kudziko lakutali. 2 Ndipo m’nyengo yake adatuma mtumiki kwa wolimawo, kuti akalandireko kwa wolimawo zipatso za m’munda wamphesa. 3 Ndipo iwo adamgwira iye, nam’menya, namchotsa wopanda kanthu. 4 Ndipo adatumanso mtumiki wina kwa iwo; ndipo ameneyu adamponya miyala, namubvulaza m’mutu, namchotsa mwamanyazi wopanda kanthu. 5 Ndipo adatuma wina; iyeyu adamupha; ndi ena ambiri; ena adawamenya, ndi ena adawapha. 6 Adatsalira m’modzi, ndiye mwana wake wokondedwa; potsiriza adamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamchitira ulemu mwana wanga. 7 Koma wolima ajawo, adanena mwa iwo wokha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu. 8 Ndipo adamtenga namupha iye, namtaya kunja kwa munda. 9 Kodi pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzawononga wolimawo, nadzapereka mundawo kwa ena. 10 Kodi simudawerenga ngakhale lembo ili; Mwala umene adawukana womanga nyumba, womwewu udayesedwa mutu wa pangodya. 11 Awa ndi machitidwe Ambuye, ndipo ali wozizwitsa m’maso mwathu? 12 Ndipo adayesa kuti amgwire Iye; koma adawopa anthu, pakuti adazindikira kuti Iye adakamba fanizo ili potsutsa iwo; ndipo adamsiya Iye, nachoka. 13 Ndipo adatuma kwa Iye ena wa Afarisi ndi a Herode, kuti akamkole Iye m’kuyankhula kwake. 14 Ndipo pamene adafika, adanena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli wowona, ndipo simusamala munthu pakuti simuyang’ana nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu mowona: nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena ayi? 15 Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye podziwa chinyengo chawo, adati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni khobiri latheka, kuti ndiliwone. 16 Ndipo adalitenga. Ndipo adati kwa iwo, Chithunzi ichi, ndi chilembo chake ziri za yani? Ndipo adati kwa Iye, za Kaisara. 17 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo adazizwa naye. 18 Ndipo anadza kwa Iye Asaduki amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; ndipo adamfunsa Iye, nanena 19 Mphunzitsi, Mose adatilembera ife kuti, Akafa m`bale wake wa munthu, nasiya mkazi, wosasiyapo mwana, m`bale wake atenge mkazi wake namuukitsire mbale wakeyo mbewu. 20 Adalipo abale asanu ndi awiri; woyamba adakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbewu; 21 Ndipo wachiwiri adamkwatira iye nafa, wosasiya mbewu; ndipo wachitatunso adatero momwemo; 22 Ndipo asanu ndi awiriwo adakhala naye ndipo sadasiya mbewu. Potsiriza pake pa onse mkaziyo adafanso. 23 Chotero pakuwuka kwa akufa adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wawo. 24 Ndipo Yesu poyankha adati, simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu? 25 Pakuti pamene adzawuka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa, koma akhala ngati angelo akumwamba. 26 Koma za akufa, kuti adzaukitsidwa simudawerenga m’buku la Mose kodi, momwe adalikuthengo, kuti Mulungu adati kwa iye, nanena, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Mulungu wa Yakobo? 27 Iye sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu. 28 Ndipo anadza m’modzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo podziwa kuti adawayankha bwino, adamfunsa Iye, Lamulo loyamba la onse ndi liti? 29 Ndipo Yesu adamuyankha iye, Kuti lamulo loyamba la onse ndi ili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu ndiye m’modzi. 30 Ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse: Ili ndi lamulo loyamba. 31 Ndipo lachiwiri ndi ili, uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. Palibe lamulo lina loposa awa. 32 Ndipo mlembiyo adati kwa Iye, Chabwino, mphunzitsi, mwanena zowona kuti ndi Mulungu m’modzi; ndipo palibe wina, koma Iye. 33 Ndipo kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mzako monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa. 34 Ndipo Yesu pakuwona adayankha ndi nzeru adati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu adalimbanso mtima kumfunsa Iye ndithu. 35 Ndipo Yesu adayankha nati, pamene adali kuphunzitsa m’kachisi, Bwanji alembi akunena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide? 36 Pakuti Davide mwini yekha adati mwa Mzimu Woyera, Ambuye adati kwa Ambuye wanga, khala ku dzanja langa lamanja, kufikira nditawayika adani ako popondapo mapazi ako. 37 Chomwecho Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo adakondwa kumva Iye. 38 Ndipo Iye adati kwa iwo m’chiphunzitso chake, Chenjerani ndi alembi, akonda kubvala miyinjiro nakonda kulandira ulemu m’misika. 39 Nakhala nayo mipando yaulemu m’sunagoge, ndi malo a ulemu pamaphwando; 40 Amenewo alusira nyumba za akazi a masiye, napemphera monyenga mawu ambiri, amenewa adzalandira kulanga koposa. 41 Ndipo Yesu adakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya momwe anthu adali kuponyera ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri adaponyamo zambiri. 42 Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye adaponyamo tindalama tiwiri tating’ono topanga khobiri limodzi. 43 Ndipo adayitana wophunzira ake, nati kwaiwo, ndithu ndinena ndi inu, mkazi wamasiye amene waumphawi adaponya zambiri koposa onse woponya mosungiramo: 44 Pakuti onse adaponyamo mwa zochuluka zawo; koma iye adaponya mwa kusowa kwake zonse adali nazo, inde ndi za moyo wake wonse.

Marko 13

1 Ndipo pamene Iye adalikutuluka m’kachisi m’modzi wa wophunzira ake adanena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere. 2 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa umzake, umene sudzagwetsedwa pansi. 3 Ndipo pamene Iye adakhala pa phiri la Azitona, popenyana ndi kachisi adamfunsa Iye mseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane ndi Andreya kuti, 4 Tiwuzeni zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake pamene zinthu izi zonse zidzakwaniritsidwa? 5 Ndipo Yesu powayankha iwo adanena nawo, Chenjerani kuti munthu asakusocheretseni: 6 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu; nadzasocheretsa ambiri. 7 Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichidafike chimaliziro. 8 Pakuti mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina umzake; padzakhala zibvomerezi m’malo osiyanasiyana; padzakhala njala ndi mabvuto; Izi ndi zoyambira za zowawa. 9 Koma inu mudziyang’anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m’masunagoge mwao; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzayimilira chifukwa cha Ine, kukhala umboni kwa iwo. 10 Ndipo Uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. 11 Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa chimene mudzayankhula; kapena kulingalira koma chimene chidzapatsidwa kwa inu ora lomwelo, muchiyankhule; pakuti woyankhula si inu, koma Mzimu Woyera. 12 Ndipo m’bale adzapereka m`bale wake kuti aphedwe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzawukirana ndi akuwabala nadzawaphetsa. 13 Ndipo mudzadedwa ndi anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wopilira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa. 14 Ndipo pamene mudzawona chonyansa cha kupululutsa chimene chidayankhulidwa ndi Danieli m`neneri (iye amene awerenga azindikire ) chitayima pomwe sichiyenera kuyima pamenepo iwo ali mu Yudeya athawire ku mapiri: 15 Ndipo iye amene ali pamwamba pa denga asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m’nyumba mwake; 16 Ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake. 17 Koma tsoka kwa iwo wokhala ndi mwana ndi iwo akuyamwitsa m`masiku amenewo! 18 Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzakhale m’nyengo yozizira. 19 Pakuti masiku amenewo padzakhala chisautso, chonga sichidakhalepo chimzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu adachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso nthawi zonse. 20 Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu m’modzi yense; koma chifukwa cha wosankhidwa amene adawasankha, adafupikitsa masikuwo. 21 Ndipo pamenepo ngati munthu wina anena kwa inu, Onani Khristu ali pano; kapena Onani, ali uko; musakhulupirire; 22 Pakuti adzawuka Akhristu wonyenga ndi aneneri wonyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati n’kutheka, wosankhidwa omwe. 23 Koma inu chenjerani; Onani, ndakuwuziranitu zinthu zonse, zisadafike. 24 Koma m’masiku amenewo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa ndi mwezi sudzapatsa kuwunika kwake. 25 Ndipo nyenyezi zidzagwa kuchokera m’mwamba ndi mphamvu ziri m’mwamba zidzagwedezeka. 26 Ndipo pamenepo adzawona Mwana wa Munthu ali mkudza m’mitambo ndi mphamvu yayikulu, ndi ulemerero. 27 Ndipo pamenepo adzatuma angelo ake, nadzasonkhanitsa wosankhidwa ake wochokera ku mphepo zinayi, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo. 28 Tsopano phunzirani fanizo la mtengo wa mkuyu; pamene pafika kuti nthambi yake yanthete, ndipo akaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja. 29 Chomwecho inunso, pamene mudzawona zinthu izi zili kuchitika, zindikirani kuti ali pafupi, inde pakhomo. 30 Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika. 31 Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mawu anga sadzapita. 32 Koma za tsikulo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo m’mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye adziwa. 33 Chenjerani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake. 34 Pakuti Mwana wa Munthu ali monga ngati munthu wa pa ulendo, amene adachoka kunyumba kwake, nawapatsa atumiki ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamulira wapakhomo adikire. 35 Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa inu nthawi yake yobwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa; 36 Kuti angabwere modzidzimutsa nadzakupezani muli mtulo. 37 Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.

Marko 14

1 Ndipo popita masiku awiri kudali phwando la Paskha ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo ansembe akulu ndi alembi adafunafuna momwe angamgwirirre momchenjerera, ndi kumupha; 2 Koma adati, paphwando ayi, kuti pangakhale phokoso chipolowe cha anthu. 3 Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate, m’mene adasayama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabasitala ya mafuta wonunkhira bwino a nardo weni weni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake. 4 Koma adakhalako ena adabvutika mtima mwa iwo wokha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji? 5 Pakuti mafuta amene akadagulitsa makobiri oposa mazana atatu ndi mphambu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo adanyinyirika motsutsana ndi iye. 6 Ndipo Yesu adati, Mulekeni, mumbvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino. 7 Pakuti muli nawo aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo pali ponse pamene mufuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse. 8 Iye wachita chimene wakhoza; adandidzozeratu thupi langa ku kuyikidwa m’manda. 9 Indetu ndinena ndi inu; paliponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino ku dziko lonse lapansi, ichinso chimene adachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho. 10 Ndipo Yudasi Isikariyote, ndiye m’modzi wa khumi ndi awiriwo, adachoka napita kwa ansembe akulu,kuti akampereke Iye kwa iwo. 11 Ndipo pamene iwo adamva, adasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye adafunafuna momwe angamperekere Iye bwino. 12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paskha, wophunzira ake adanena naye, Mufuna tipite kuti, tikakonze mukadyereko Paskha? 13 Ndipo adatuma awiri awophunzira ake, nanena nawo, Lowani mu mzinda, ndipo mudzakomana ndi munthu wosenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye; 14 Ndipo kumene adzalowako iye, munene naye mwini nyumba wabwino, Mphunzitsi anena, chiri kuti chipinda cha alendo m’menemo ndidzadyera Paskha ndi wophunzira anga? 15 Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda, chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m’menemo mutikonzere ife. 16 Ndipo wophunzira adatuluka, nafika mu mzinda, napeza monga adati kwa iwo; ndipo adakonza Paskha. 17 Ndipo madzulo adafika, Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. 18 Ndipo pamene iwo adakhala pansi ndi kudya, Yesu adati, Indetu ndinena ndi inu, m’modzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi. 19 Ndipo iwo adayamba kukhala ndi chisoni, ndi kunena naye m’modzi m’modzi, kuti Ndine kodi? Ndipo wina adati kodi ndine? 20 Ndipo adati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo,ndiye wosunsa pamodzi ndi ine m’bale. 21 Pakuti Mwana wa munthu amukadi; monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa munthu! Kukadakhala kwabwino kwa munthu ameneyo akadakhala kuti sadabadwe. 22 Ndipo pamene analikudya, Yesu adatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, adanyema, napereka kwa iwo, nati: Tengani, idyani, ili ndi thupi langa. 23 Ndipo adatenga chikho, ndipo pamene adayamika, adapereka kwa iwo, ndipo iwo onse adamweramo. 24 Ndipo Iye adati kwa iwo, Uwu ndi mwazi wanga wa pangano latsopano, wokhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri. 25 Indetu ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu. 26 Ndipo atayimba nyimbo, adatuluka, napita ku phiri la Azitona. 27 Ndipo Yesu adati kwa iwo, mudzakhumudwa nonsenu usiku uno chifukwa cha Ine; pakuti kwalembedwa; Ndidzakantha m`busa, ndi nkhosa zidzabalalika. 28 Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya. 29 Koma Petro adati kwa Iye, Angakhale adzakhumudwa onse komatu ine ayi. 30 Ndipo Yesu adati kwa iye, Indetu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asadalire kawiri udzandikana Ine katatu. 31 Koma iye adayankhula molimbitsa mawu kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo adatero. 32 Ndipo iwo anadza ku malo dzina lake Getsemane; ndipo adanena kwa wophunzira ake, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera. 33 Ndipo adatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kulemedwa mtima ndithu. 34 Ndipo adati kwa iwo, Moyo wanga uli wa chisoni chambiri kufikira imfa. Bakhalani pano, nimudikire. 35 Ndipo Iye anapita m’tsogolo pang’ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati n’kutheka nthawi imeneyi indipitirire Ine. 36 Ndipo Iye adati, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu, mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu. 37 Ndipo anadza nawapeza iwo ali m’tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Ulibe mphamvu yakudikira ola limodzi kodi? 38 Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m’kuyesedwa; mzimutu ali wofuna, koma thupi liri lolefuka. 39 Ndipo adachokanso, napemphera, nanena mawu womwewo. 40 Ndipo anadzanso nawapeza ali m’tulo, pakuti maso awo adalemeradi; ndipo sadadziwe chomuyankha Iye. 41 Ndipo anadza kachitatu, nanena nawo, Gonani tsopano; nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m’manja wa anthu wochimwa. 42 Ukani, tidzipita; onani wondiperekayo ali pafupi. 43 Ndipo pomwepo Iye ali chiyankhulire, anadza Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nawo malupanga ndi zibonga, wochokera kwa ansembe akulu ndi alembi ndi akulu. 44 Ndipo wompereka Iye adawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsopsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire. 45 Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena Mphunzitsi, mphunzitsi: nampsopsonetsa Iye. 46 Ndipo adamthira manja, namgwira namtenga Iye. 47 Ndipo m’modzi wina wa iwo woyimilira pamenepo, adasolola lupanga lake, nakantha mtumiki wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake. 48 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi zibonga kundigwira Ine monga bava? 49 Masiku onse ndidali nanu m’kachisi ndiri kuphunzitsa, ndipo simudandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe. 50 Ndipo iwo onse adamsiya Iye, nathawa. 51 Ndipo m’nyamata wina adamtsata Iye, atafundira pathupi bafuta yekha kubisa umaliseche wake; ndipo anyamatawo adamuyimitsa Iye; 52 Ndipo iye adasiya bafutayo, nathawa wamaliseche. 53 Ndipo adamka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo adasonkhana kwa iye ansembe akulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi. 54 Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m’bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo adali kukhala pansi pamodzi ndi atumiki, ndi kuwotha moto. 55 Ndipo ansembe akulu ndi akulu a milandu onse adafunafuna umboni womutsutsa nawo Yesu kuti amuphe Iye; koma sadaupeze. 56 Pakuti ambiri adamchitira umboni wonama, ndipo umboni wawo sudalingane. 57 Ndipo adanyamukapo ena, namchitira umboni wonama, nanena kuti, 58 Ife tidamumva Iye alikunena kuti Ine ndidzawononga kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosamangidwa ndi manja. 59 Ndipo ngakhale momwemo umboni wawo sudafanane. 60 Ndipo mkulu wa ansembe adanyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira umboni mokutsutsa Iwe. 61 Koma adakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe adamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wodalitsika? 62 Ndipo Yesu adati, Ndine amene; ndipo mudzawona Mwana wa munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo yakumwamba. 63 Ndipo mkulu wa ansembe adang’amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina? 64 Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse adamtsutsa Iye kuti ayenera kufa. 65 Ndipo ena adayamba kumthira malobvu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kum’bwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo atumikiwo adampanda Iye khofi ndi manja awo. 66 Ndipo pamene Petro adali pansi m’bwalo, anadzapo m’modzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe; 67 Ndipo pamene adamuwona Petro alikuwotha moto, namuyang’ana iye, adanena, Iwenso udali naye Yesu ku Mnazarete. 68 Koma adakana, nanena, Sindimdziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo adatuluka kupita kuchipata; ndipo tambala adalira. 69 Ndipo mdzakaziyo adamuwonanso iye, nayambanso kunena ndi iwo akuyimilirapo, Uyu ndi m`modzi wa iwo. 70 Ndipo adakananso. Ndipo patapita mphindi, akuyimilirapo adanenanso ndi Petro, zowonadi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya. Pakuti ndi mayankhulidwe ako agwirizana ndi iwo. 71 Koma iye adayamba kutemberera, ndi kulumbira, ndikunena, Sindidziwa za munthuyu amene inu muyankhula za Iye. 72 Ndipo tambala adalira kachiwiri, Ndipo Petro adakumbukira umo Yesu adati kwa iye, kuti, Tambala asadalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo poganizira ichi adalira misozi.

Marko 15

1 Ndipo pomwepo m`mawa adakhala upo ansembe akulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato. 2 Ndipo Pilato adamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo poyankha adati kwa iye, Mwatero ndinu. 3 Ndipo ansembe akulu adamnenera Iye zinthu zambiri koma sadayakhe kanthu. 4 Ndipo Pilato adamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Tawona, akuchitira umboni Iwe mokutsutsa zinthu zambiri zotere. 5 Koma Yesu sadayankhenso kanthu; kotero Pilato adazizwa. 6 Tsopano amkawamasulira paphwando wa mndende m’modzi, amene iwo adamfuna. 7 Ndipo adalipo wina dzina lake Baraba, womangidwa pamodzi ndi ena wopanduka, amene adapha munthu mumpanduko. 8 Ndipo khamu lidafuwuula niliyamba kupempha Iye kuti achite monga adali kuwachitira iwo. 9 Koma Pilato adawayankha iwo, nanena Kodi mufuna ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda? 10 Pakuti adazindikira kuti ansembe akulu adampereka Iye mwa njiru. 11 Koma ansembe akulu adasonkhezera anthu, kuti makamaka awamasulire Baraba. 12 Ndipo Pilato adayankha natinso kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula Mfumu ya Ayuda? 13 Ndipo adafuwulanso, Mpachikeni Iye. 14 Pamenepo Pilato adanena nawo, Chifukwa chiyani, Iye adachita choyipa chotani? Koma iwo adafuwulitsatu, Mpachikeni Iyeyo. 15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazikitsa mtima anthuwo, adawamasulira Baraba, nampereka Yesu, atamkwapula kuti akapachikidwe. 16 Ndipo asilikali adachoka naye nalowa m’bwalo, ndilo Pretoriyo; nasonkhanitsa gulu lawo lonse. 17 Ndipo adambveka Iye chibakuwa, naluka korona wa minga, nambveka pa mutu pake. 18 Ndipo adayamba kumulonjera Iye, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda! 19 Ndipo adampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malobvu, nampindira mawondo, namlambira. 20 Ndipo atatha kum’nyoza adambvula chibakuwacho nam’bveka Iye zobvala zake. Ndipo adatuluka naye kuti akampachike Iye. 21 Ndipo adamkangamiza wina, Simoni wa ku Kerene, amene amapitirirapo kuchokera kumudzi, atate wawo wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake. 22 Ndipo adamtenga kupita naye ku malo Gologota, ndiwo wosandulika, Malo achigaza. 23 Ndipo adampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sadamlandire 24 Ndipo pamene adampachika Iye, adagawana zobvala zake, ndi kuchita mayere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani. 25 Ndipo lidali ora lachitatu ndipo iwo adampachika Iye. 26 Ndipo lembo la mlandu wake lidalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA. 27 Ndipo adampachika pamodzi ndi achifwamba awiri; m’modzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamazere. 28 Ndipo malemba adakwaniritsidwa, amene adati, Ndipo adawerengedwa pamodzi ndi omphwanya malamulo. 29 Ndipo iwo wodutsapo adamchitira Iye mwano, napukusa mitu yawo nanena, Ha! Iwe wopasula kachisi ndi kum’manga masiku atatu, 30 Udzipulumutse wekha, nutsike pamtandapo. 31 Moteronso ansembe akulu adamtoza mwa iwo wokha pamodzi ndi alembi’nanena, Adapulumutsa ena; Iye yekha sakhoza kudzipulumutsa. 32 Atsike tsopano pamtanda, Khristu Mfumu ya Israyeli, kuti tiwone ndipo tikhulupirire. Ndipo iwo wopachikidwa naye adamlalatira. 33 Ndipo pofika ola la chisanu ndi limodzi, padali mdima padziko lonse, kufikira ola la chisanu ndi chinayi. 34 Ndipo pa ola la chisanu ndi chinayi Yesu adafuwula ndi mawu wokweza, Eloi, Eloi, lamasabakitani? Ndiko kutathauza, Mulungu wanga Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine? 35 Ndipo ena woyimilirapo, pakumva adanena, Taonani akuyitana Eliya. 36 Ndipo adathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiyika pa bango, nampatsa kuti amwe, nanena, Mulekeni; tiwone ngati Eliya adza kudzamtsitsa. 37 Ndipo Yesu adafuula mokwezetsa mawu, napereka Mzimu wake. 38 Ndipo chinsalu chotchinga cha m’kachisi chidang’ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi. 39 Ndipo pamene Kenturiyo, woyimilirapo popenyana ndi Iye, adawona kuti adapereka Mzimu kotero, adati, Zowonadi, munthu uyu adali Mwana wa Mulungu. 40 Ndipo adaliponso pamenepo akazi akuyang’anira patali; mwa iwo padali Mariya wa Magadala ndi Mariya amake wa Yakobo wam’ng’ono ndi wa Yose, ndi Salome. 41 (Amene adamtsata Iye, pamene adali mu Galileya, namtumikira Iye;) ndi akazi ena ambiri, amene adakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu. 42 Ndipo tsono atafika madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa sabata. 43 Adadzapo Yosefe wa ku Arimateya, mkulu wa milandu wotchuka, amene yekha adali kuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. 44 Ndipo Pilato adazizwa ngati adamwaliradi; nayitana Kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale. 45 Ndipo pamene adachidziwa ndi Kenturiyo, adampatsa Yosefe mtembowo. 46 Ndipo adagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m’bafutamo, namuyika m’manda wosemedwa m’thanthwe; nakunkhunizira mwala pa khomo la manda. 47 Ndipo Mariya wa Magadala ndi Mariya amake a Yosefe adapenya pomwe adayikidwapo

Marko 16

1 Ndipo litapita sabata, Mariya wa Magadala, ndi Mariya amake wa Yakobo, ndi Salome, adagula zonunkhira, kuti akadze kumdzodza Iye. 2 Ndipo anadza kumanda m`mawa tsiku loyamba la Sabata, litatuluka dzuwa. 3 Ndipo adalikunena mwa wokha, Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda? 4 Ndipo pamene adakweza maso adawona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti udali waukulu ndithu. 5 Ndipo pamene adalowa m’manda, adawona m’nyamata atakhala kumbali ya ku dzanja lamanja, wobvala mwinjiro woyera; ndipo iwo Adachita mantha. 6 Ndipo iye adanena nawo, musaope: Muli kufuna Yesu Mnazarete amene adapachikidwa; adawuka; Sali pano; tawonani, mbuto m’mene adayikamo Iye. 7 Koma mukani uzani wophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolereni inu ku Galileya; kumeneko mudzamuwona Iye, monga adanena ndi inu. 8 Ndipo adatuluka mwamsanga, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndipo anadabwa; ndipo sadawuze kanthu munthu aliyense; pakuti adachita mantha. 9 Ndipo pamene Yesu adawuka mamawa tsiku loyamba la sabata, adayamba kuwonekera kwa Mariya wa Magadala, amene adamtulutsa ziwanda zisanu ndi ziwiri. 10 Ndipo Iye adapita kukawauza iwo amene amakhala naye, ali ndi chisoni ndipo kungolira. 11 Ndipo iwowo, pamene adamva kuti ali ndi moyo, ndi kuti adawonekera kwa iye, sadakhulupirire. 12 Ndipo zitatha izi; adawonekeranso iye m’mawonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali kupita kumudzi. 13 Ndipo iwowa adachoka nawauza wotsala; koma palibe amene adakhulupirira iwo. 14 Ndipo chitatha icho adawonekera kwa khumi ndi m; modzi, alikuseyama pachakudya; ndipo adawadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndi kuwumitsa mtima, popeza sadakhulupilira iwo amene adamuwona, atawuka Iye. 15 Ndipo adanena nawo, Mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa wolengedwa onse. 16 Amene akhulupilira nabatizidwa, adzapulumuka; koma amene sakhulupirira adzalangidwa. 17 Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupilira; m’dzina langa adzatulutsa ziwanda, adzayankhula ndi malilime atsopano; 18 Adzatola njoka ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzayika manja awo pa wodwala, ndipo adzachira. 19 Pamenepo Ambuye, atatha kuyankhula nawo, adalandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja la manja la Mulungu. 20 Ndipo iwowa adatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye adagwira ntchito nawo pamodzi, natsimikiza mawu ndi zizindikiro zakutsatapo. Ameni.

Luka 1

1 Popeza ambiri adayesa kulongosola nkhani ya zinthu zokhulupiridwa zimene zidachitika pakati pa ife, 2 Monga adazipereka kwa ife iwo amene kuyambira pachiyambi adakhala mboni yowona ndi maso ndi atumiki a mawu; 3 Kuyambira pachiyambi, ndidayesa nkokoma kwa inenso, amene ndidalondalonda mosamalitsa, zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe. 4 Kuti iwe udziwitse zowona zake za zinthu zimene iwe udaphunzitsidwa. Aneneratu za kubadwa kwa Yohane Mbatizi 5 Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kudali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana akazi a fuko la Aroni, dzina lake adali Elizabeti. 6 Ndipo onse awiri adali wolungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse a zoyikika za Ambuye wopanda banga. 7 Ndipo adalibe mwana, popeza Elizabeti adali wouma, ndipo onse awiri adali wokalamba. 8 Ndipo padali pakuchita iye ntchito yopereka nsembe m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu. 9 Monga mwa machitidwe a kupereka nsembe adamgwera mayere akufukiza zonunkhira polowa iye m’kachisi wa Ambuye. 10 Ndipo khamu lonse la anthu lidali kupemphera kunja nthawi ya zonunkhira. 11 Ndipo adamuwonekera iye m’ngelo wa Ambuye, nayimilira kudzanja la manja la guwa la nsembe la zonunkhira. 12 Ndipo Zakariya anadabwa pamene adamuwona,ndipo mantha adamgwira. 13 Koma m’ngelo adati kwa iye, Usawope Zakariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. 14 Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake. 15 Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena chakumwa cha ukali; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asadabadwe. 16 Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. 17 Ndipo adzamtsogolera iye, ndi Mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana awo, ndi wosamvera kuti atsate nzeru ya wolungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu wokonzeka. 18 Ndipo Zakariya adati kwa m’ngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka. 19 Ndipo m’ngelo poyankha adati kwa iye, Ine ndine Gabrieli; amene amayimilira pa maso pa Mulungu; ndipo ndidatumidwa kwa iwe kudzayankhula nawe, ndikuwuza iwe uthenga uwu wabwino. 20 Ndipo tawona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kuyankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi; popeza kuti sudakhulupirire mawu anga, amene adzakwaniritsidwa pa nyengo yake. 21 Ndipo anthu analikulindira Zakariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake m’kachisimo. 22 Ndipo pamene iye adatulukamo, sadathe kuyankhula nawo; ndipo adazindikira kuti iye adawona masomphenya m’kachisimo. Ndipo iye adalimkukodola iwo, nakhalabe wosayankhula. 23 Ndipo kudali, pamene masiku a utumiki wake adamalizidwa, adapita kunyumba kwake. 24 Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake adayima; nadzibisa miyezi isanu, nati, 25 Ambuye wandichitira chotero m’masiku omwe Iye adandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu. 26 Ndipo mwezi wa chisanu ndi umodzim’ngelo Gabrieli adatumidwa ndi Mulungu kupita ku mzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete. 27 Kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Mariya. 28 Ndipo m’ngelo polowa adati kwa iye, Tikuwoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe. Wodala iwe mwa amayi. 29 Ndipo pamene adamuwona iye, adanthunthumira ndi mawu awa, nasinkhasinkha kuyankhula uku nkutani. 30 Ndipo m’ngelo adati kwa iye, Usawope Mariya, pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. 31 Ndipo tawona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wa mwamuna, nudzamutcha dzina lake YESU 32 Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulu-kulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake. 33 Ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha. 34 Pamenepo Mariya adati kwa m’ngelo, ichi chidzachitika bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna. 35 Ndipo m’ngelo adayankhula, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulu-kulu idzakuphimba iwe; chifukwa chakenso choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36 Ndipo tawona, Elizabeti msuwani wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi umodzi wa iye amene adanenedwa wouma. 37 Chifukwa ndi Mulungu palibe zinthu zidzakhala zosatheka. 38 Ndipo Mariya adati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mawu anu. Ndipo m’ngelo adachoka kwa iye. 39 Ndipo Mariya adanyamuka masiku amenewo, napita ndi changu ku dziko la mapiri ku mzinda wa Yuda. 40 Ndipo adalowa m’nyumba ya Zakariya, nayankhula kwa Elizabeti. 41 Ndipo padali pamene Elizabeti adamva kuyankhula kwake kwa Mariya, mwana wosabadwayo, adatsalima m’mimba mwake; ndipo Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera. 42 Ndipo adayankhula mawu mokweza ndi mfuwu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako. 43 Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga? 44 Pakuti wona, pamene mawu akuyankhula kwako adalowa m’makutu anga, mwana adatsalima ndi msangalalo m’mimba mwanga. 45 Ndipo wodala ali iye amene adakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye adayankhula naye. 46 Ndipo Mariya adati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye. 47 Ndipo Mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga. 48 Chifukwa Iye adayang’anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti tawonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala. 49 Chifukwa Iye Wamphamvuyo adandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake liri loyera. 50 Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwo mibadwo pa iwo amene amuwopa Iye. 51 Iye adachita za mphamvu ndi mkono wake; Iye anabalalitsa wodzitama ndi malingaliro a mtima wawo. 52 Iye adatsitsa mafumu pa mipando yawo ya chifumu,ndipo adakweza aumphawi. 53 Adawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma adawachotsa wopanda kanthu. 54 Adathangatira Israyeli mtumiki wake, kuti akakumbukire chifundo chake; 55 Monga adayankhula kwa atate athu, kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake ku nthawi yonse. 56 Ndipo Mariya adakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabwereranso kunyumba kwake. 57 Tsopano idakwanira nthawi ya Elizabeti ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. 58 Ndipo anansi ake ndi abale ake adamva kuti Ambuye adakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi. 59 Ndipo padali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo adadza kudzadula kamwanako; ndipo amkati amutche dzina la atate wake Zakariya. 60 Ndipo amake adayankha, kuti, Ayi; koma adzatchedwa Yohane. 61 Ndipo iwo adati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili. 62 Ndipo adakodola atate wake, kuti afuna amutche dzina liti? 63 Ndipo iye adafunsa cholemberapo, nalemba kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo adazizwa onse. 64 Ndipo pomwepo padatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake lidamasuka, ndipo iye adayankhula, nalemekeza Mulungu. 65 Ndipo padagwa mantha pa iwo onse wokhala moyandikana nawo; ndipo adayankhulayankhula nkhani izi zonse m’dziko lonse la mapiri a Yudeya. 66 Ndipo onse amene adazimva adazisunga m’mitima mwawo, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye lidakhala pamodzi ndi iye. 67 Ndipo atate wake Zakariya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati, 68 Wodalitsika Ambuye, Mulungu wa Israyeli; chifukwa Iye adayang’ana, nachitira anthu ake chiwombolo. 69 Ndipo Iye adatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake. 70 Monga Iye adayankhula ndi m’kamwa mwa aneneri ake woyera mtima, akale lomwe; 71 Kuti tipulumuke kwa adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife; 72 Ndikuchitira atate wathu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika; 73 Chilumbiro chimene Iye adachilumbira kwa Abrahamu atate wathu. 74 Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, wopand 75 Mchiyero ndi m’chilungamo pamaso pake, masiku onse a moyo wathu. 76 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa m’neneri wa Wamkulukulu. Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake; 77 Kuwapatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso, ndi makhululukidwe amachimo awo. 78 Chifukwa cha mtima wa chifundo wa Mulungu wathu. M’menemo m’banda kucha wa Kumwamba udzatichezera ife; 79 Kuwalitsira iwo wokhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere. 80 Ndipo mwanayo adakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye adali m’zipululu, kufikira masiku akudziwonetsa yekha kwa Israyeli.

Luka 2

1 Ndipo kudali masiku aja, kuti lamulo lidatuluka kwa Kayisala Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe. 2 Ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya. 3 Ndipo onse adapita kukalembedwa, munthu aliyense ku mzinda wake. 4 Ndipo Yosefe yemwe adakwera kuchokera ku Galileya, ku mzinda wa Nazarete, kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, (chifukwa iye adali wa banja ndi fuko lake la Davide:) 5 Kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Mariya, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu adali ndi pakati. 6 Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala adakwanira kuti abeleke. 7 Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namukulunga Iye mu nsalu, namgoneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti adasowa malo m’nyumba ya alendo. 8 Ndipo padali abusa m’dziko lomwelo, wokhala kubusa ndi kuyang’anira zoweta zawo usiku. 9 Ndipo m’ngelo wa Ambuye adayimilira paiwo, ndi kuwala kwa Ambuye kudawaunikira mozungulira: ndipo adawopa ndi mantha akulu. 10 Ndipo m’ngelo adati kwa iwo, Musawope; pakuti onani, ndikuwuzani inu uthenga wabwino wa chikondwerero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse. 11 Pakuti wakubadwirani inu lero, m’mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye. 12 Ndipo ichi ndichizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera. 13 Ndipo dzidzidzi padali pamodzi ndi m’ngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu nanena, 14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo. 15 Ndipo padali, pamene angelo adachoka kwa iwo kupita Kumwamba, abusa adati wina ndi mzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikawone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye adatidziwitsira ife. 16 Ndipo iwo anadza mwachangu, napeza Mariya, ndi Yosefe ndi mwana wakhanda atagona modyera. 17 Ndipo pamene iwo adawona, adadziwitsa anthu za mawu adayankhulidwa kwa iwo a mwana uyu. 18 Ndipo anthu onse amene adamva adazizwa ndi zinthu zimene abusa adayankhula nawo. 19 Koma Mariya adasunga mawu awa onse, nawalingalira mumtima mwake. 20 Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse adazimva, naziwona, monga kudayankhulidwa kwa iwo. 21 Ndipo pamene adakwanira masiku asanu ndi atatu a kumdula Iye, adamutcha dzina lake YESU, limene adatchula m’ngeloyo asanalandiridwe Iye m’mimba. 22 Ndipo pamene adakwanira masiku a kukonza kwawo, monga mwa chilamulo cha Mose iwo adakwera naye kupita ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye; 23 (Monga mwalembedwa m’chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna ali yense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye;) 24 Ndikukapereka nsembe monga mwanenedwa m’chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri kapena mawunda awiri. 25 Ndipo onani, mu Yerusalemu mudali munthu, dzina lake Simioni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopembedza, adalikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera adali pa iye. 26 Ndipo adamuwululira Mzimu Woyera kuti sadzawona imfa, kufikira adzawona Khristu wake wa Ambuye. 27 Ndipo iye adalowa ku kachisi ndi Mzimu; ndipo pamene atate ndi amake adalowa ndi kamwanako Yesu kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo; 28 Ndipo pomwepo iye adamlandira Iye m’manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati, 29 Tsopano Ambuye monga mwa mawu anu aja; lolani ine mtumiki wanu, ndichoke mumtendere. 30 Chifukwa maso anga adawona chipulumutso chanu. 31 Chimene mudakonzera pamaso pa anthu onse; 32 Kuwunika kukawalire anthu amitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli. 33 Ndipo Yosefe ndi amake adali kuzizwa ndi zinthu zoyankhulidwa za Iye. 34 Ndipo Simioni adawadalitsa, nati kwa Mariya amake, tawona, Uyu wayikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israyeli; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; 35 ( Eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako;) manganizo a mitima yambiri ikawululidwe 36 Ndipo padali Anna, m’neneri wamkazi, mwana wa Fanuweli, wa fuko la Aseri; amene adali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziwiri. 37 Ndipo adali wamasiye kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi, amene sadachoke ku kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana. 38 Ndipo iye adafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Ambuye, nayankhula za Iye kwa anthu onse woyembekeza chiwombolo cha Yerusalemu. 39 Ndipo pamene iwo adatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mzinda kwawo, ku Nazarete. 40 Ndipo mwanayo adakula nalimbika, nadzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chidali pa Iye. 41 Tsopano makolo ake amkapita chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku phwando la Paskha. 42 Ndipo pamene Iye adali ndi zaka khumi ndi ziwiri, adakwera iwo ku Yerusalemu monga machitidwe a phwando. 43 Ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwerera iwo, mwanayo Yesu adatsalira m’mbuyo ku Yerusalemu; ndipo atate ndi amake sadadziwa. 44 Koma iwo adaganiza kuti Iye adali m’chipilingu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo adayamba kumfunafuna Iye mwa abale awo ndi mwa anansi awo. 45 Ndipo pamene sadampeza, adabwerera ku Yerusalemu, kukamfunafuna Iye. 46 Ndipo pakupita masiku atatu, adampeza Iye ali m’kachisi, alikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsa mafunso. 47 Ndipo onse amene adamva Iye adadabwa ndi kudziwa kwake, ndi mayankho ake. 48 Ndipo m’mene adamuwona Iye, anadabwa; ndipo amake adati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; tawona, atate wako ndi ine tidali kufunafuna iwe ndi kuda nkhawa. 49 Ndipo Iye adati kwa iwo, Kuli bwanji kuti mudali kundifunafuna Ine? Simudziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga? 50 Ndipo sadadziwitsa mawu amene Iye adayankhula nawo. 51 Ndipo adatsika nawo pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo; ndipo amake adasunga zinthu izi zonse mumtima mwake. 52 Ndipo Yesu adakulabe mu nzeru ndi mu msinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

Luka 3

1 Tsopano m’chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko l Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo chiwanga cha Abilene; 2 Anasi ndi Kayafa pakukhala ansembe akulu panadza mawu a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m’chipululu. 3 Ndipo iye anadza ku dziko lonse la mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wakulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo; 4 Monga mwalembedwa m’buku la mawu a Yesaya m’neneri, kuti, Mawu a wofuwula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. 5 Chigwa chiri chonse chidzadzazidwa,ndipo phiri liri lonse ndi mtunda uliwonse zidzachepetsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama. Ndipo njira za zigolowondo zidzakhala zosalala. 6 Ndipo anthu onse adzawona chipulumutso cha Mulungu. 7 Pamenepo iye adati kwa makamu amene anadza kudzabatizidwa ndi iye, Wobadwa anjoka inu, ndani adakulangizani kuthawa mkwiyo ulimkudza? 8 Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuwukitsira Abrahamu ana. 9 Ndipo tsopano lino nkhwangwa yayikidwa pamizu ya mitengo; chotero mtengo uli wonse wosabala chipatso cha bwino udulidwa, nuponyedwa pa moto. 10 Ndipo anthu adamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tidzichita chiyani? 11 Iye adayankha nati kwa iwo, Iye amene ali nawo malaya awiri agawireko iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho. 12 Pamenepo amisonkho anadza kwa iye kudzabatizidwanso, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani? 13 Ndipo iye adati kwa iwo, Musamawonjezerapo kanthu konse kakuposa chimene adakulamulirani. 14 Ndipo asilikali omwe adamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye adati kwa iwo, Musawopseze, musamanamize munthu ali yense; khalani wokhutitsidwa ndi kulipidwa kwanu. 15 Ndipo pamene anthu adali kuyembekezera, ndipo onse adaganizaganiza m’mitimu yawo za Yohane, ngati kapena iye adali Khristu kapena ayi: 16 Yohane adayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alimkudza amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: 17 Amene chowuluzira chake chiri m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndikusonkhanitsa tirigu m’nkhokwe yake; koma mankhusu adzatenthedwa m’moto wosazima. 18 Choteretu iye adawuza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri. 19 Koma Herode chiwangacho, m’mene Yohane adamdzudzula chifukwa cha Herodiya mkazi wa m’bale wake Filipo, ndi cha zinthu zonse zoyipa Herode adazichita. 20 Adawonjeza pa zonsezi ichinso, kuti adatsekera Yohane m’nyumba yandende. 21 Tsopano pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa nalikupemphera, pathambo padatseguka, 22 Ndipo Mzimu Woyera adatsika ndi mawonekedwe athupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo mudatuluka mawu m’thambo, kuti Iwe ndiwe Mwana wanga Wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera. 23 Ndipo Yesuyo, adali wa zaka makumi atatu, (monga momwe adali) mwana wa Yosefe amene adali, mwana wa Heli. 24 Mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Melki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe. 25 Amene adali mwana wa Matatio, mwana wa Amosi, mwana wa Naumi, mwana wa Esli, mwana wa Nagai, 26 Amene adali mwana wa Maati, mwana wa Matatio, mwana Semeini, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda, 27 Amene adali mwana wa Joanani, amene adali mwana wa Resa, mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, mwana wa Neri, 28 Amene adali mwana wa Melki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elmadama, mwana wa Ere, 29 Amene adali mwana wa Jose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi, 30 Amene adali mwana wa Sumioni, mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu, 31 Amene adali mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natanu, mwana wa Davide, 32 Amene adali mwana wa Jese, mwana wa Obede, mwana wa Boazi, mwana wa Salmoni, mwana wa Naasoni, 33 Amene adali mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni, mwana wa Ezironu, mwana wa Farese, mwana wa Yuda, 34 Amene adali mwana wa Yakobo, mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana waNakoro, 35 Amene adali mwana wa Seruki, mwana wa Reu, mwana wa Pelege, mwana wa Ebere, mwana wa Sala, 36 Amene adali mwana wa Kainane, mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameke, 37 Amene adali mwana wa Metusela, mwana wa Enoke, mwana wa Yaredi, mwana wa Malaleeli, mwana wa Kayinane, 38 Amene adali mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.

Luka 4

1 Ndipo Yesu wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kupita kuchipululu, 2 Ndipo pakukhala masiku makuni anayi nayesedwa ndi mdierekezi, sanadye kanthu kena kali konse m’masiku amenewo; ndipo pamen adatha adamva njala. 3 Ndipo mdierekezi adati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, lamulirani mwala uwu kuti ukhale mkate. 4 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Kwalembedwa kuti, munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu ali wonse a Mulungu. 5 Ndipo mdierekezi adamtenga Iye, nakwera naye pa phiri, namuwonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m’kamphindi kakang’ono. 6 Ndipo mdierekezi adati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wawo; chifukwa udaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupereka kwa iye amene ndifuna. 7 Chifukwa chake ngati Inu mudzandipembedza pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu. 8 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti Ambuye Mulungu wako udzipembedza ndipo Iye yekha yekha uzimtumikira. Choka kumbuyo kwanga Satana; 9 Ndipo adamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuyika Iye pamwamba pa msonga ya kachisi, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi; 10 Pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamulira angelo ake za inu kuti akusungeni. 11 Ndipo pa manja awo adzakunyamulani Inu, kuti mungagunde konse phazi lanu pamwala. 12 Ndipo Yesu adayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako. 13 Ndipo mdierekezi, m’mene adamaliza mayesero onse, adalekana naye kufikira nthawi yina. 14 Ndipo Yesu adabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira. 15 Ndipo Iye adaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalemekezedwa ndi anthu onse. 16 Ndipo anadza ku Nazarete, kumene adaleredwa; ndipo tsiku la sabata adalowa m’sunagoge, monga adazolowera, adayimiliramo kuwerenga. 17 Ndipo adapereka kwa Iye buku la Yesaya m’neneri. Ndipo m’mene Iye adafunyulula bukulo, adapeza pomwe padalembedwa, 18 Mzimu wa Ambuye ali pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiwuze anthu osauka Uthenga Wabwino: kukachiritsa a mtima wosweka, adandituma Ine kulalikira a m`singa mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyenso, kupatsa ufulu wobvulazidwa. 19 Kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye. 20 Ndipo m’mene adapinda bukulo, adalipereka kwa m’nyamata, adakhala pansi; ndipo maso awo wa anthu onse m’sunagogemo adam’yang’anitsa Iye. 21 Ndipo adayamba kunena kwa iwo, kuti Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu. 22 Ndipo onse adamchitira Iye umboni nazizwa ndi mawu a chisomo akutuluka m’kamwa mwake; nanena, kodi uyu simwana wa Yosefe? 23 Ndipo Iye adati, kwa iwo Kwenikweni mudzati kwa Ine mwambi uwu, Sing’anga iwe, tadzichiritsa wekha; zonse zija tazimva zidachitidwa ku Kapenawo, muzichitenso zomwezo kwanu kuno. 24 Ndipo Iye adati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, palibe m’neneri alandirika ku dziko la kwawo. 25 Koma zowonadi ndinena kwa inu, kuti, Mudali akazi a masiye ambiri mu Israyeli masiku ake a Eliya, pamene kudatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene padakhala njala yaikulu pa dziko lonselo; 26 Ndipo Eliya sadatumidwa kwa m’modzi wa iwo, koma ku Sarepta mzinda wa ku Sidoniya, kwa mkazi wa masiye. 27 Ndipo mudali akhate ambiri mu Israyeli masiku a Elisa m’neneri; ndipo palibe m’modzi wa iwo adakonzedwa, koma Namani, yekha wa ku Suriya. 28 Ndipo onse a m’sunagoge adadzala ndi m’kwiyo pakumva izi; 29 Ndipo adanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mzindawo, napita naye pamwamba pa phiri pamene padamangidwa mzinda wawo, kuti akamponye pansi. 30 Koma Iye adapyola pakati pawo, nachokapo. 31 Ndipo Iye adatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya, ndipo adali kuwaphunzitsa iwo m`masiku a Sabata 32 Ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake. Chifukwa mawu ake adali ndi mphamvu. 33 Ndipo m’sunagoge mudali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuwula ndi mawu wolimba, 34 Nanena, Tilekeni; kodi tiri ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi mudadza kudzatiwononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu. 35 Ndipo Yesu adamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuLuka mwa iye. Ndipo chiwandacho m’mene chidamgwetsa iye pakati, chidatuluka mwa iye chonsampweteka konse. 36 Ndipo anthu onse anadabwa, nayankhulana wina ndi mzake, nanena,Mawu amenewa ali wotani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka. 37 Ndipo mbiri yake ya Iye idafalikira ku malo onse a dziko loyandikira. 38 Ndipo Iye adanyamuka kuchokera m’sunagoge, nalowa m’nyumba ya Simoni. Ndipo momwemo mudali amai ake a mkazi wake wa Simoni, adagwidwa ndi nthenda yolimba ya malungo; ndipo adampempha Iye za iye. 39 Ndipo Iye adayimilira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo idamleka iye; ndipo adauka msangatu, nawatumikira. 40 Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene adali nawo wodwala ndi nthenda za mitundu mitundu, anadza nawo kwa Iye, ndipo Iye adayika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa. 41 Ndipo ziwanda zomwe zidatuluka mwa ambiri, ndi kufuwula, kuti, Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu! Ndipo Iye adazidzudzula wosazilola kuyankhula, chifukwa zidamdziwa kuti Iye ndiye Khristu. 42 Ndipo kutacha adatuluka Iye napita ku malo achipululu; ndipo anthu adalikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere. 43 Ndipo adati kwa iwo, kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku mizinda yinanso: chifukwa ndidatumidwa kudzatero. 44 Ndipo Iye adalalikira m’masunagoge aku Galileya.

Luka 5

1 Ndipo padali pakumkanikiza anthu, kudzamva mawu a Mulungu, Iye adali kuyimilira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete; 2 Ndipo adawona zombo ziwiri zitakhala m’mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m’menemo, nalikutsuka makoka awo. 3 Ndipo adakhala pansi naphunzitsa anthu kuchokera m`chombo. Ndipo Iye adalowa m`chombo chimodzi, ndicho chake cha Simoni, nampempha iye akankhe pang’ono kuchoka kumtunda. 4 Tsopano pamene Iye adaleka kuyankhula, adati kwa Simoni, kankhira kwakuya, nimuponye makoka anu kusodza. 5 Ndipo Simoni adayankha, nati kwa Iye, Ambuye, tidagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mawu anu ndidzaponya makoka. 6 Ndipo pamene adachita ichi, adazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka awo adalikung’ambika. 7 Ndipo adakodola amzawo amene adali m`chombo china kuti, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza zombo zonse ziwiri, motero kuti zidayamba kumila. 8 Ndipo pamene Simoni Petro adawona, adagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye chifukwa ndine munthu wochimwa. 9 Pakuti iye adazizwa ndi onse amene adali naye, pa zakasodzedwe kansomba zimene adazikola. 10 Ndipo chimodzi modzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene adali amzake a Simoni. Ndipo Yesu adati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu. 11 Ndipo m’mene iwo adakocheza zombo zawo pamtunda, adasiya zonse, namtsata Iye. 12 Ndipo padali pamene Iye adali m’mzinda wina, tawona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene adawona Yesu, adagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza. 13 Ndipo Iye adatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate lidachoka kwa iye. 14 Ndipo iye adawalamulira, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke nudziwonetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo. 15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo makamu adasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zawo. 16 Ndipo Iye adachoka mwini yekha napita kuchipululu kukapemphera. 17 Ndipo padali tsiku lina, pamene Iye adali kuphunzitsa, ndipo padali Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene adachokera ku mizinda yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu; ndipo mphamvu ya Ambuye idali ndi Iye yakuwachiritsa iwo. 18 Ndipo onani, anthu adanyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna njira yobwera naye, ndi kumuyika pamaso pa Iye. 19 Ndipo pamene adalemphera kupeza polowa naye, chifukwa cha khamu, adakwera pamwamba pa denga, namtsitsira iye pobowola pa denga ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu. 20 Ndipo Iye, pakuwona chikhulupiliro chawo, adati, kwa iye, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa . 21 Ndipo alembi ndi Afarisi adayamba kulingalira kuti, Ndani Uyu ayankhula zomchitira Mulungu mwano?ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha. 22 Koma pamene Yesu adadziwa malingaliro awo, nayankha, nati kwa iwo, mukulingalira chiyani m’mitima yanu? 23 Chapafupi n’chiti kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena Tawuka, nuyende? 24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira machimo (adati Iye kwa wodwala manjenjeyo). Ndinena kwa iwe, Tawuka, nusenze kama wako numuke kunyumba kwako. 25 Ndipo pomwepo adayimilira pamaso pawo, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kupita kunyumba kwake, ali kulemekeza Mulungu. 26 Ndipo onse adazizwa, ndipo adalemekeza Mulungu, nadzadzidwa ndi mantha, nanena kuti Lero tawona zodabwitsa. 27 Ndipo zitatha zinthu izi Iye adatuluka, nawona munthu wamsonkho dzina lake Levi, atakhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine. 28 Ndipo iye adasiya zonse, nanyamuka, namtsata Iye. 29 Ndipo Levi adamkonzera Iye mphwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo padali khamu lalikulu la a misonkho, ndi enanso amene adalikuseyama pa chakudya pamodzi nawo. 30 Ndipo Afarisi ndi alembi awo adang’ung’uza kwa wophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi wochimwa? 31 Ndipo Yesu adayankha, nati kwa iwo, Amene ali wolimba safuna sing’anga; koma wodwala ndiwo, 32 Sindinadza Ine kuyitana wolungama, koma wochimwa kuti alape. 33 Ndipo iwo adati kwa Iye, Wophunzira a Yohane a masala kudya kawiri kawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso a Afarisi; koma anu amangodya ndi kumwa. 34 Koma Iye adati kwa iwo, Kodi mungathe kuwapanga ana a ukwati kuti asale, pamene mkwati ali nawo pamodzi? 35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku amenewo. 36 Ndipo Iye adayankhulanso fanizo kwa iwo, kuti palibe munthu ayika chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong’ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo. 37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’mabotolo akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa mabotolowo, ndipo ameneyo adzatayika, ndipo mabotolo adzawonongeka. 38 Koma vinyo watsopano ayenera atsanulidwe m’mabotolo atsopano. Ndipo onse asungika. 39 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena wakale ali wokoma.

Luka 6

1 Ndipo kudali kuti tsiku la Sabata yachiwiri itatha yoyamba, Iye adalimkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo wophunzira ake adalimkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m’manja mwawo, nadya. 2 Ndipo Afarisi ena adati kwa iwo, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika m`masiku a Sabata? 3 Ndipo Yesu adayankha iwo nati, Kodi simudawerengenso ngakhale chimene adachita Davide, pamene paja adamva njala, iye ndi iwo adali naye pamodzi; 4 Kuti adalowa m’nyumba ya Mulungu, natenga mikate yowonetsera, nadya, napatsanso iwo adali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe wokha? 5 Ndipo Iye adati kwa iwo, kuti, Mwana wa munthu ali Mbuye wa tsiku la sabata. 6 Ndipo kudali tsiku lina la sabata, Iye adalowa m’sunagoge, naphunzitsa. Ndipo mudali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja lidali lopuwala. 7 Ndipo alembi ndi Afarisi adalikumzonda momuyang`anitsitsa Iye, ngati adzachiritsa pa tsiku la sabata; kuti akampeze choneneza motsutsa Iye. 8 Koma Iye adadziwa maganizo awo; nati kwa munthuyo wa dzanja lopuwala, Nyamuka, nuyimilire pakatipo. Ndipo iye adanyamuka, nayimilira. 9 Ndipo pamenepo Yesu adati kwa iwo, Ndikufunsani inu chinthu chimodzi, Kodi kuloleka tsiku la sabata kuchita zabwino, kapena kuchita zoyipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuwuwononga? 10 Ndipo pamene adaunguzaunguza paiwo onse, adati kwa munthuyo Tambasula dzanja lako. Ndipo iye adatero, ndipo dzanja lake lidabwerera monga limzake. 11 Ndipo iwo adagwidwa ndi misala; nayankhulana wina ndi mzake kuti adzamchitira Yesu chiyani. 12 Ndipo kudali masiku amenewo, Iye adatuluka napita kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m’kupemphera kwa Mulungu. 13 Ndipo kutacha adayitana wophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene adawatchanso dzina lawo atumwi; 14 Simoni (amene adamutchanso Petro) ndi Andreya mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo. 15 Mateyu, ndi Tomasi ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa Zelote. 16 Ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Isikariyote, amene adali wompereka Iye. 17 Ndipo Iye adatsika nawo, nayima pachidikha, ndi gulu la wophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a kumbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene adadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zawo. 18 Ndipo iwo amene adabvutika ndi mizimu yonyansa adachiritsidwa. 19 Ndipo khamu lonse lidafuna kumkhudza Iye; chifukwa mudatuluka mphamvu mwa Iye, nachiritsidwa onse. 20 Ndipo Iye adakweza maso ake kwa wophunzira ake nanena, Wodala wosauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu. 21 Wodala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Wodala inu akulira tsopano; chifukwa mudzasekera. 22 Wodala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loyipa, chifukwa cha Mwana wa munthu. 23 Kondwerani tsiku lomwelo, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo awo adawachitira aneneri zonga zomwezo. 24 Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandiriratu chisangalatso chanu. 25 Tsoka kwa inu wokhuta! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka kwa inu wosekerera tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi. 26 Tsoka kwa inu, pamene anthu adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo awo adawatero momwemo aneneri wonama. 27 Koma ndinena kwa inu akumva, kondanani nawo adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu. 28 Dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe. 29 Ndipo kwa Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso limzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya akonso. 30 Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso. 31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitireni inu, muwachitire iwo motero inu momwemo. 32 Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti wochimwa womwe akonda iwo akukondana nawo. 33 Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu wochimwa amachitanso chomwecho. 34 Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti onse anthu wochimwa amakongoletsa kwa wochimwa amzawo, kuti alandirenso momwemo. 35 Koma kondanani nawo adani anu, ndikuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekezera kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yayikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma osayamika ndi woyipa. 36 Khalani inu a chifundo monga Atate wanu ali wachifundo. 37 Ndipo musaweruze ndipo simudzaweruzidwa, musawatsutse ndipo simudzatsutsidwa, khululukirani ndipo mudzakhululukidwa. 38 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani pa chifuwa chanu, pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu. 39 Ndipo Iye adawayankhulira fanizo, kodi wa khungu angatsogolere wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m’dzenje? 40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, amene adzakhala wangwiro, adzafanana ndi mphunzitsi wake. 41 Ndipo uyang’anitsitsiranji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma mtengo wa m’diso la iwe mwini suwuzindikira? 42 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, leka ndichotse kachitsotso kali m’diso lako, wosayang’anitsitsa bwino iwe mwini mtengo uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtengowo uli m’diso lako, ndipo pomwepo udzayang’anitsitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m’diso la m’bale wako. 43 Pakuti palibe mtengo wabwino upatsa zipatso zobvunda; kapenanso mtengo woyipa upatsa zipatso zabwino. 44 Pakuti mtengo uli wonse uzindikirika ndi chipatso chake pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa. 45 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woyipa atulutsa zoyipa m’choyipa chake; pakuti m’kamwa mwake mwa munthu mungoyankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake. 46 Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene Ine ndizinena? 47 Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mawu anga, ndi kuwachita ndidzakusonyezani amene afanana naye. 48 Iye afanana ndi munthu womanga nyumba, amene adakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje udagunda pa nyumayo, ndipo sudakhoza kuyigwedeza; chifukwa idamangidwa pa thanthwe. 49 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo udagunda mtsinje, ndipo idagwa pomwepo; ndipo kugwa kwake kwa nyumbayo kudali kwakukulu.

Luka 7

1 Tsopano pamene adatsiriza mawu ake onse m’makutu wa anthu, Iye adalowa m’Kapernao. 2 Ndipo mtumiki wa Kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kufa. 3 Ndipo pamene iye adamva za Yesu, adatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa mtumiki wake. 4 Ndipo pamene iwo adafika kwa Yesu, adampempha Iye nthawi yomweyo, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi; 5 Pakuti akonda mtundu wathu, ndipo adatimangira ife sunagoge. 6 Pamenepo Yesu adapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi panyumba yake, Kenturiyo adatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzibvute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa denga langa. 7 Chifukwa chake ine sindidadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu; koma nenani mawu, ndipo mtumiki wanga adzachiritsidwa. 8 Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera ulamiliro, ndiri nawo asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, pita, napita; ndi kwa wina, idza, nadza; ndipo kwa mtumiki wanga tachita ichi, nachita. 9 Pamene Yesu adamva zinthu zimenezi adazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo womutsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindidapeza ngakhale mwa Israyeli, chikhulupiliro chachikulu chotere. 10 Ndipo pakubwera kunyumba wotumidwawo, adapeza mtumikiyo atachira ndithu. 11 Ndipo kudali, litapita tsiku ili, Iye adapita kumzinda, dzina lake Nayini; ndipo ambiri a wophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu udapita naye. 12 Ndipo pamene adayandikira ku chipata cha mzindawo, onani pamenepo padali munthu wakufa wonyamulidwa, mwana wamwamuna m’modzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amu mzindawo adali pamodzi naye. 13 Ndipo pamene Ambuye adamuwona, adagwidwa ndi chifundo cha iye, nanena naye, Usalire. 14 Ndipo adayandikira, nakhudza chithatha; ndi womunyamulawo adayima. Ndipo Iye adati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tawuka. 15 Ndipo wakufayo adakhala tsonga, nayamba kuyankhula. Ndipo adampereka kwa amake. 16 Ndipo mantha adagwira onsewo: ndipo adalemekeza Mulungu nanena kuti, Mneneri wamkulu wawuka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake. 17 Ndipo mbiri yake imeneyi inabuka ku Yudeya konse, ndi ku dziko lonse loyandikira. 18 Ndipo wophunzira a Yohane adamuwuza iye zonsezi. 19 Ndipo Yohane adayitana awiri a wophunzira ake, nawatuma kwa Yesu, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina? 20 Ndipo pamene anthuwo adafika kwa Iye, adati, Yohane M’batizi watituma ife kwa inu, kuti, kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina? 21 Ndipo nthawi yomweyo Iye adachiritsa ambiri nthenda zawo, ndi zobvuta, ndi mizimu yoyipa; napenyetsanso akhungu ambiri. 22 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Pitani, mumuwuze Yohane zimene mwaziwona, ndi kuzimva kuti; anthu akhungu alandira kuwona kwawo, wopunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, wogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino. 23 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine. 24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye adayamba kunena kwa anthu zokhudzana ndi Yohane, nati, Mudatuluka kupita kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? 25 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Munthu wobvala zobvala zofewa kodi? Onani, iwo wobvala zolemera, ndi wokhala modyerera, ali m’nyumba za mafumu. 26 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo woposa mneneri. 27 Uyu ndi uja amene adalembedwera za iye, ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakonzera njira yako pamaso pako. 28 Pakuti ndinena kwa inu, kuti Mwa wobadwa ndi akazi palibe m’modzi m`neneri wamkulu woposa Yohane M`batizi; koma iye amene ali wam’ng’ono mu Ufumu wa Mulungu ali wamkulu womposa iye. 29 Ndipo anthu onse amene adamva Iye ndi amisonkho omwe, adabvomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza adabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane. 30 Koma Afarisi ndi achilamulo adakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo wokha, popeza sadabatizidwa ndi iye. 31 Ndipo Ambuye adati, Ndidzafanizira ndi chiyani anthu am’badwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani? 32 Angofanana ndi ana wokhala pa msika, ndi kuyitanizana wina ndi mzake, ndi kunena, ife tidakulizirani chitoliro, ndipo inu simudabvine ayi; tinabuma maliro, ndipo simudalire ayi. 33 Pakuti Yohane M’batizi adafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo mudanena, Ali ndi chiwanda. 34 Mwana wa munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi kumwayimwa vinyo, bwenzi la amisokho ndi anthu wochimwa! 35 Koma nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse. 36 Ndipo m’modzi wa Afarisi adakhumba Iye kuti akadye naye. Ndipo adalowa m’nyumba ya Mfarisi, naseyama pachakudya. 37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene adali m’mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu adali kuseyama pachakudya m’nyumba ya Mfarisi, adatenga msupa ya alabastara ya mafuta wonunkhira bwino. 38 Ndipo adayimilira kumbuyo kwake, pa mapazi ake, nalira, nayamba nasambitsa mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsopsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta wonunkhira bwino. 39 Koma Mfarisi, amene adamuyitana Iye, pakuwona, adanena mwa iye yekha, nati, Munthu uyu, ngati akadakhala m’neneri, akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa. 40 Ndipo Yesu adayankha kwa iye, Simoni, ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye adati, Ambuye, nenani. 41 Munthu wokongoletsa ndalama adali nawo angongole awiri; m’modziyo adali ndi ngongole yake ya makobiri mazana asanu koma mzake makumi asanu. 42 Ndipo popeza adalibe chobwezera, iye adawakhululukira onse awiri. Tandiwuzani, ndani wa iwo adzaposa kumkonda? 43 Simoni adayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene adamkhululukira zoposa ndipo adanena kwa iye, Wayankha bwino. 44 Ndipo Iye adachewukira kwa mkaziyo, nati kwa Simoni, upenya mkazi ameneyu kodi? Ndidalowa m’nyumba yako, sudandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu wasambitsa mapazi anga ndi misozi nawapukuta ndi tsitsi lapamutu pake. 45 Sudandipatsa mpsopsono wa chibwenzi; koma uyu sadaleka kupsopsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine. 46 Sudandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma mkazi uyu adadzoza mapazi anga ndi mafuta wonunkhira bwino. 47 Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa adakonda kwambiri; koma munthu amene adamkhululukidwa pang’ono, iye akonda pang’ono. 48 Ndipo adati kwa mkaziyo, machimo ako akhululukidwa. 49 Ndipo iwo akuseyama naye pachakudya adayamba kunena mwa wokha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo? 50 Ndipo Iye adati kwa mkaziyo, chikhulupiliro chako chakupulumutsa iwe; pita ndi mtendere.

Luka 8

1 Ndipo kudali; katapita kamphindi adayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo. 2 Ndipo akazi ena amene adachiritsidwa mizimu yoyipa ndi nthenda zawo,ndiwo Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zidatuluka mwa iye. 3 Ndipo Jowana mkazi wake wa Kuza kapitawo wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene adawatumikira ndi chuma chawo. 4 Ndipo pamene anthu ambiri adasonkhana ndipo adadza kwa Iye ochokera kumidzi yonse ndipo adayankhula nawo mwa fanizo. 5 Wofesa adatuluka kukafesa mbewu zake; ndipo mkufesa kwake zina zidagwa m’mbali mwa njira; ndipo zidapondedwa ndi mbalame za mu mlengalenga zidatha kuzidya. 6 Ndipo zina zidagwa pathandwe; ndipo pakumera zidafota msanga, chifukwa zidalibe m’nyontho. 7 Ndipo zina zidagwa pakati pa minga; ndi mingayo idaphuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa. 8 Ndipo zina zidagwa pa nthaka yabwino, ndipo zidamera, ndi kupatsa zipatso za makumi khumi. Pakunena Iye izi adafuwula, iye amene ali ndi makutu akumva amve. 9 Ndipo wophunzira ake adamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili liri lotani? 10 Ndipo Iye adati, kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena wotsala ndinena nawo mwa mafanizo; kuti pa kuwona sangawone, kuti pakumva sangadziwitse. 11 Tsopano fanizolo ndi ili: Mbewuzo ndizo mawu a Mulungu. 12 Ndipo za m’mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mawu m’mitima yawo, kuti angakhulupirire ndi kupulumutsidwa. 13 Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mawu ndi kukondwera; koma alibe mizu, akhulupilira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesero amagwa. 14 Ndipo zija zidagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m’kupita kwawo atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo uno, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu. 15 Koma zija za m’nthaka yabwino, ndiwo amene adamva mawu nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupilira. 16 Palibe munthu, ayatsa nyali nayibvundikira ndi chotengera, kapena kuyiyika pansi pa kama; koma ayiyika pa choyikapo, kuti iwo akulowamo awone kuwala. 17 Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala chowonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziwika ndi kubvumbuluka. 18 Chifukwa chake samalirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija awoneka ngati ali nacho. 19 Ndipo adadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sadakhoza kufika kwa Iye, chifukwa cha khamu la anthu. 20 Ndipo adamuwuza Iye kuti Amayi anu ndi abale anu ayima kunja akufuna kuwonana ndi Inu. 21 Koma Iye adayankha, nati kwa iwo, Amayi anga ndi abale anga ndi awa amene akumva mawu a Mulungu, nawachita. 22 Ndipo pamene zidatha izi tsiku linalo, Iye adalowa m’chombo, ndi wophunzira ake; nati kwa iwo, Tiwolokere tsidya lija la nyanja. Ndipo adapita. 23 Ndipo m’mene iwo adali kupita pamadzi, Iye adagona tulo. Ndipo panyanja padatsira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, adawopsezedwa. 24 Ndipo adadza kwa Iye, namudzutsa, nanena, Ambuye, Ambuye tikuwonongeka. Ndipo adadzuka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zidaleka, ndipo padagwa bata. 25 Ndipo Iye adati kwa iwo, chikhulupiriro chanu chiri kuti? Ndipo m’kuchita mantha adazizwa iwo, nanena wina ndi mzake, Munthu uyu ndi wotani, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye? 26 Ndipo iwo adakocheza ku doko la dziko la Agerasa, ndilo lopenyana ndi Galileya. 27 Ndipo Iye adatuluka pamtunda, adakomana naye mwamuna wa mzinda, amene adali nazo ziwanda kwa nthawi yayitali; ndipo iye samabvala, ndipo samakhala m’nyumba, koma m’manda. 28 Pamene adamuwona Yesu, iye adafuwula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mawu akulu, Ndiri nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze ayi. 29 Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuLuka mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri amasungidwa womangidwa ndi unyolo ndi matangadza; ndipo adamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kuzipululu. 30 Ndipo Yesu adamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo adati, Legiyo, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye. 31 Ndipo zidampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa kupompho. 32 Ndipo pamenepo padali gulu la nkhumba zambiri zimadya m’phiri. Ndipo zidapempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo adazilola. 33 Ndipo ziwandazo zidatuluka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo lidatsika mwaliwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanjamo,ndipo zidamira . 34 Ndipo wowetawo m’mene adawona chimene chidachitika, adathawa, nawuza akumzinda ndi akumidzi. 35 Ndipo iwo adatuluka kukawona chimene chidachitika; ndipo adadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zidatuluka mwa iye, atakhala pansi ku mapazi a Yesu wobvala ndi wanzeru zake; ndipo iwo adawopa. 36 Ndipo iwo amene adawona adawawuza za machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo. 37 Ndipo khamu lonse la dziko la Agerasa loyandikira adamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa adagwidwa ndi mantha akulu ndipo adapita nalowa m`chombo nabwerera. 38 Tsopano munthu amene ziwanda zidatuluka mwa iye adampempha Iye akhale ndi Iye; koma Yesu adamuwuza kuti apite, nanena, 39 Pita kunyumba kwako, nukafotokozere zazikuluzo adakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye adachoka, nalalikira ku mzinda wonse zazikuluzo Yesu adamchitira iye. 40 Ndipo patapita izi pamene Yesu adabwerera, anthu adamulandira Iye mokondwera chifukwa onse adali kumuyembekezera Iye. 41 Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo adagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze ku nyumba kwake; 42 Chifukwa adali naye mwana wamkazi m’modzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo adalimkumwalira iye. Koma pakupita Iye anthu adakanikizana naye. 43 Ndipo mkazi, adali ndi nthenda zaka khumi ndi ziwiri yotaya mwazi, amene adalipira kwa asing’anga za moyo wake zonse, ndipo sadathe kuchiritsidwa ndi m’modzi yense, 44 Anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chobvala chake; ndipo pomwepo nthenda yake idaleka. 45 Ndipo Yesu adati, wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse adakana, Petro ndi iwo wokhala naye adati, Ambuye, khamu likukankhana pa Inu ndi kukanikizana, ndipo munena kuti, Ndani wandikhudza Ine? 46 Ndipo Yesu adati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine. 47 Ndipo pamene mkaziyo adawona kuti sadabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti adachiritsidwa pomwepo. 48 Ndipo Iye adati kwa iyeyu, Mwana wamkaziwe kondwera, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; pita ndi mtendere. 49 M’mene Iye adali chiyankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wamkazi wafa; usambvute Mphunzitsi. 50 Koma pamene Yesu adamva, adamuyankha iye, kuti, Usawope; khulupirira kokha, ndipo iye adzachiritsidwa. 51 Ndipo pamene iye adafika kunyumbako, sadaloleza munthu wina aliyense kulowa naye pamodzi, koma Petro ndi Yohane ndi Yakobo, ndi atate ndi amake amwanayo. 52 Ndipo onse adali kumlira iye ndi kudziguguda pa chifuwa. Koma Iye adati; Musalire; pakuti iye sadafe, koma wagona tulo. 53 Ndipo adamseka Iye pwepwete podziwa kuti adafa. 54 Ndipo Iye adawatulutsa onse kubwalo namgwira dzanja lake, nayitana, nati, Buthu, tawuka. 55 Ndipo mzimu wake udabwera, ndipo adauka pomwepo; ndipo Iye adawalamulira kuti ampatse kanthu kakudya. 56 Ndipo makolo ake anadabwa; ndipo adalamulira iwo asauze munthu ali yense chimene chidachitika.

Luka 9

1 Ndipo Iye adayitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda. 2 Ndipo adawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu wodwala. 3 Ndipo Iye adati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka pa ulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nawo malaya awiri. 4 Ndipo m’nyumba ili yonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko. 5 Ndipo onse amene sakakulandirani inu, m’mene mutuluka m’mzinda womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya pa iwo. 6 Ndipo iwo adatuluka, napita m’mizinda, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuchiritsa ponse. 7 Ndipo Herode chiwangacho adamva mbiri yake ya zonse zidachitika; ndi Iye: ndipo zidamthetsa nzeru, chifukwa adanena anthu ena, kuti Yohane adauka kwa akufa; 8 Koma ena, kuti Eliya adawoneka; ndipo ena, kuti m’neneri wina wa akale aja adauka. 9 Ndipo Herode adati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo adakhumba kumuona Iye. 10 Ndipo atumwi atabwera, adamfotokozera Iye zonse adazichita. Ndipo Iye adawatenga, napatuka nawo pa wokha kumka ku mzinda dzina lake Betsaida. 11 Ndipo anthu, pamene adadziwa, adamtsata Iye; ndipo Iye adawalandira, nayankhula nawo za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene adasowa kuchiritsidwa. 12 Koma pamene tsiku limapita kumapeto pamenepo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu amuke, kuti apite ku mizinda yoyandikira ndi kumidzi, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tiri ku malo a chipululu kuno. 13 Koma Iye adati kwa iwo, muwapatse chakudya ndinu. Koma adati, ife tiribe yochuluka koma isanu yokha ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya. 14 Pakuti adali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye adati kwa wophunzira ake, khalitsani iwo pansi m`magulu, a makumi asanu asanu. 15 Ndipo adatero, nawakhalitsa pansi onsewo. 16 Ndipo iye m’mene adatenga, mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri adayang’ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa wophunzira apereke kwa makamuwo. 17 Ndipo anadya nakhuta onsewo; natola makombo, mitanga khumi ndi iwiri. 18 Ndipo kudali, pamene Iye adali kupemphera payekha wophunzira adali naye; ndipo adawafunsa iwo, kuti, anthu anena kuti Ine ndine yani? 19 Iwo adayankha nati, Yohane M’batizi; koma ena ati Eliya; ndi ena ati, kuti adauka m’modzi wa aneneri akale. 20 Iye adati kwa iwo, koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo adayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu. 21 Ndipo Iye adawauzitsa iwo, nawalamulira kuti asanene ichi kwa munthu ali yense. 22 Nanena, kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi ndi kuphedwa, ndi kuwuka tsiku la chitatu. 23 Ndipo Iye adanena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine. 24 Pakuti amene adzapulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupulumutsa. 25 Pakuti munthu adzapindulanji akadzilemeretsa dziko lonse lapansi nadzatayapo, kapena kulipa moyo wake? 26 Pakuti amene ali yense adzachita manyazi chifukwa cha Ine, ndi mawu anga, Mwana wa munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika mu ulemerero wake ndi wa Atate ake ndi wa angelo woyera. 27 Koma Ine ndinena ndi inu zowonadi, pali ena a iwo ayima pano, amene sadzalawa imfa, kufikira kuti adzawona Ufumu wa Mulungu. 28 Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mawu amenewa, Iye adatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo adapita nawo, nakwera m’phiri kukapemphera. 29 Ndipo m’kupemphera kwake, mawonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndi chobvala chake chidayera ndi kunyezimira. 30 Ndipo onani, adalikuyankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya. 31 Amene adawonekera mu ulemerero, nanena za imfa yake imene Iye ati idzachitikira ku Yerusalemu. 32 Koma Petro ndi iwo adali naye adalemedwa ndi tulo; pamene adadzuka, adawona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo amene adayima ndi Iye. 33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro adati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tikhale pano; ndipo timange mahema atatu, imodzi ya Inu, ndi yina ya Mose, ndi yina ya Eliya; wosadziwa chimene iye adali kunena. 34 Ndipo ali chiyankhulire izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo adawopa pakulowa iwo mumtambowo. 35 Ndipo mudatuluka mawu mu mtambo nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa; mverani Iye. 36 Ndipo pakutha mawuwo, Yesu adapezeka ali yekha. Ndipo iwo adakhala chete, ndipo sadauza munthu ali yense masiku aja kanthu konse ka izo adaziwona. 37 Ndipo panali, m’mawa mwake atatsika m’phiri anthu ambiri adakomana naye. 38 Ndipo onani, munthu wa m’khamulo adafuwula, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang’anireni mwana wanga; chifukwa ndiye m’modzi yekha wa ine: 39 Ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuwula modzidzimuka; ndipo umam’ng’amba iye ndi kumchititsa thobvu pakamwa nubvulaza, nuchoka kwa iye. 40 Ndipo ndidawapempha wophunzira anu kuti awutulutse; koma sadathe. 41 Ndipo Yesu adayankha, nati, Ha! Wobadwa inu wosakhulupilira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndikulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako. 42 Ndipo pamene iye adali mkudza, chiwandacho chidamgwetsa pansi, ndi kum’ng’ambitsa. Koma Yesu adadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mwanayo, nam’bwezera iye kwa atate wake. 43 Ndipo onse anadabwa ndi mphamvu ya ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse adalikuzizwa ndi zonse zimene Yesu adazichita, Iye adati kwa wophunzira ake, 44 Alowe mawu amenewa m’makutu anu; pakuti mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja a anthu. 45 Koma iwo sadadziwitse mawu awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo adawopa kumfunsa za mawu awa. 46 Ndipo adayamba kutsutsana mwa iwo wokha kuti wa mkulu mwa iwo ndani. 47 Koma Yesu pakuwona kutsutsana kwa mitima yawo, adatenga kamwana, nakayimika pambali pake, nati kwa iwo. 48 Ndipo Iye adati kwa iwo, Amene ali yense adzalandira kamwana aka m’dzina langa alandira Ine; ndipo amene aliyense andilandira Ine alandira Iye amene adandituma Ine; pakuti iye wakukhala wam’ng’onong’ono wa inu nonse yemweyu ndiye adzakhala wamkulu. 49 Ndipo Yohane adayankha nati, Ambuye, tidawona wina ali kutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tidamletsa , chifukwa sadatsatana nafe. 50 Koma Yesu adati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nafe athandizana nafe. 51 Ndipo padali pamene adayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye Kumwamba, Iye adatsimikiza kuloza nkhope yake kumka ku Yerusalemu. 52 Ndipo adatumiza a mithenga patsogolo pake; ndipo adamka, nalowa m’mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo. 53 Ndipo iwo sadamlandire Iye, chifukwa nkhope yake idali yoloza kumka ku Yerusalemu. 54 Ndipo pamene wophunzira ake Yakobo ndi Yohane adawona izi , adati, Ambuye, kodi mufuna kuti ife tiwuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo monga Eliya adachitira? 55 Koma Iye adapotoloka nawadzudzula iwo, nati, Inu simukudziwa za mtundu wa mzimu muli nawo. 56 Pakuti Mwana wa munthu sanadza kudzawononga miyoyo ya anthu, koma kuwapulumutsa iwo. Ndipo adapita kumudzi kwina. 57 Ndipo m’mene iwo adalikuyenda m’njira, munthu wina adati kwa Iye, Ambuye, Ine ndidzakutsatani kumene kuli konse mukapitako. 58 Ndipo Yesu adati kwa iye, Nkhandwe ziri nazo mayenje, ndi mbalame za mulengalenga zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamila mutu wake. 59 Ndipo adati kwa wina, Unditsate Ine. Koma iye adati, Ambuye, Mundilole ine; choyamba ndi yambe ndapita kukayika maliro a atate wanga. 60 Koma Yesu adati kwa iye, Leka akufa ayike akufa awo wokha; koma muka iwe nukalalikire Ufumu wa Mulungu. 61 Ndipo winanso adati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muyambe mwandilola kulawirana nawo a kunyumba kwanga. 62 Koma Yesu adati kwa iye, palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ali woyenera Ufumu wa Mulungu.

Luka 10

1 Zitatha izi Ambuye adasankha ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiri awiri pamaso pake ku mzinda uli wonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini yekha. 2 Chifukwa chake adanena kwa iwo, Zokolola zichulukadi, koma antchito ali wochepa; potero pemphererani kwa Mbuye wa zokolola, kuti atumize antchito kukakolola. 3 Mukani; tawonani Ine ndituma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; ndipo musayankhule munthu panjira. 5 Ndipo m’nyumba ili yonse mukalowamo muyambe mwanena kuti, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. 6 Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m’menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu. 7 Ndipo m’nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa zamomwemo monga akupatsani; pakuti wantchito ayenera kulandira mphotho yake; musachoka kupita m’nyumba ina ndi ina. 8 Ndipo mumzinda uli wonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani; 9 Ndipo chiritsani wodwala ali momwemo nimunene nawo, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. 10 Koma kumzinda uli wonse mukalowako, ndipo salandira inu pitani kunjira za kumakhwalala ake a kumeneko ndi kunena. 11 Lingakhale fumbi lochokera kumzinda kwanu, lomamatika ku mapazi athu, tilisansiramotsutsana ndi inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. 12 Koma ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodoma kudzapilirika kuposa mzinda umenewo. 13 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikachitika m’Turo ndi Sidoni ntchito zamphamvuzi zimene zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi wobvala chiguduli ndi phulusa. 14 Koma ku Turo ndi ku Sidoni kudzapiririka, pachiweruziro, koposa inu. 15 Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku gehena. 16 Iye womvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wonyoza inu, andinyoza Ine; ndipo iye wonyoza Ine am`nyoza Iye amene adandituma Ine. 17 Ndipo makumi asanu ndi awiriwo anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zidatigonjera ife m’dzina lanu. 18 Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndidawona Satana alimkugwa ngati mphenzi wochokera kumwamba. 19 Tawonani, ndakupatsani inu mphamvu yoponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu ili yonse ya m’daniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakupwetekani konse. 20 Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti mayina anu alembedwa m’Mwamba. 21 Nthawi yomweyo Yesu adakondwera mu mzimu, nati, Ndiyamika Inu, Atate, Ambuye wa Kumwamba ndi wa dziko la pansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi wozindikira, ndipo mudaziwululira ana amakanda; indedi; Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu. 22 Zinthu zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma atate, ndi iye amene Mwana afuna kumuwululira Iye. 23 Ndipo Iye m’mene adapotolokera kwa wophunzira ake, ali pa wokha, adati, Wodala masowo akuwona zimene muwona. 24 Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri adafuna kuwona zimene inu muziwona, koma sadaziwona; ndi kumva zimene mukumva, koma sadazimva. 25 Ndipo tawonani, wachilamulo wina adayimilira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani? 26 Ndipo adati kwa iye, M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji? 27 Ndipo Iye adayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi m’nansi wako monga iwe mwini. 28 Ndipo Iye adati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo. 29 Koma iye, pofuna kudziyesa wolungama yekha, adati kwa Yesu, Ndipo m’nansi wanga ndani? 30 Ndipo Yesu adayankha, nati, Munthu wina adatsika kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja wa achifwamba amene adambvula zobvala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa. 31 Ndipo kudangotero kuti wansembe wina adatsika njirayo, ndipo pakumuwona iye anadutsa mbali yina. 32 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuwona Iye, anadutsa mbali yina. 33 Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake adafika padali iye; ndipo pakumuwona, adagwidwa chifundo ndi iye, 34 Ndipo anadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo adamuyika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye ku nyumba ya alendo, namsamalira iye. 35 Ndipo pamene m’mawa mwake amapita adatulutsa makobiri nampatsa mwini nyumba ya alendo, nati, kwa iye msamalireni iye, ndipo chiri chonse muononga koposa, ine, pobweranso ndidzakubwezera iwe. 36 Uti wa awa atatu, uyesa iwe, adakhala m’nansi wa iye uja adagwa m’manja mwa achifwamba? 37 Ndipo Iye adati, Iye amene adachita chifundo. Ndipo Yesu adati kwa iye, Pita, nuchite iwe momwemo. 38 Tsopano pakupita pa ulendo pawo Iye adalowa m’mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita adamlandira Iye kunyumba kwake. 39 Ndipo iye adali ndi mbale wake wotchedwa Mariya, ndiye wakukhala pa mapazi a Yesu, namva mawu ake. 40 Koma Marita adatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo adadza kwa Iye, nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga wandisiya nditumikire ndekha? Mumuwuze iye tsono kuti andithandize. 41 Koma Yesu adayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nubvutika ndi zinthu zambiri: 42 Koma chifunika chinthu chimodzi, pakuti Mariya wasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.

Luka 11

1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m’mene adaleka, wina wa wophunzira ake adati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane adaphunzitsa wophunzira ake. 2 Ndipo Iye adati kwa iwo, pamene mupemphera nenani, Atate wathu, amene muli m’Mwamba, dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze; kufuna kwanu kuchitidwe monga Kumwamba chomwecho pansi pano. 3 Tipatseni ife tsiku ndi tsiku mkate wa pa tsiku. 4 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa; koma mutipulumutse ife kuchoka kwa woyipayo. 5 Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu; 6 Popeza wandidzera bwenzi langa lochokera pa ulendo, ndipo ndiribe chompatsa. 7 Ndipo iyeyu wa m’katimo poyankha adati, Usandibvuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pakama; sindikhoza kuwuka ndi kukupatsa. 8 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma lake adzauka nadzampatsa iye ziri zonse azifuna. 9 Ndipo Ine ndinena ndi inu, pemphani, ndipo adzakupatsani, funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani. 10 Pakuti yense wopempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira. 11 Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, kodi adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzam’ninkha njoka m’malo mwa nsomba kodi? 12 Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? 13 Potero inu, ngati inu, wokhala woyipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye? 14 Ndipo adali kutulutsa chiwanda chosayankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosayankhulayo adayankhula; ndipo anthu adazizwa. 15 Koma ena mwa iwo adati, Ndi Belezebule mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda. 16 Koma ena adamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba. 17 Koma Iye, podziwa zolingilira zawo, adati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m’kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m’kati mwake igwa. 18 Ndiponso ngati satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzayima bwanji Ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi belezebule. 19 Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi belezebule, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala woweruza anu. 20 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu popanda kukayika, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu. 21 Pamene pali ponse munthu wa mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake ziri mumtendere; 22 Koma pamene pali ponse akamdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka amchotsera zida zake zonse, zimene adazikhulupirira, nagawa zofunkha zake. 23 Iye wosabvomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza. 24 Pamene mzimu wonyansa utuluka mwa munthu, upyola malo wopanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera ku nyumba kwanga kumene ndidatulukako, 25 Ndipo pofika, uyipeza yosesa ndi yokonzeka. 26 Pomwepo upita nutenga mizimu yina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe wotsiriza a munthu uyu ayipa koposa woyambawo. 27 Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina wa khamu la anthu adakweza mawu, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene mudayamwa. 28 Koma Iye adati, Inde, koma wodala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga. 29 Ndipo pamene adasonkhana anthu, adayamba kunena, mbado uno ndi mbado woyipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona m`neneri. 30 Pakuti monga ngati Yona adali chizindikiro kwa Anineve, chotero adzakhalanso Mwana wa munthu kwa mbado uno. 31 Mfumu yaikazi ya kumwera idzayimilira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbado uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera ku malekezero adziko kudzamva nzeru za Solomo; ndipo onani wamkulu, woposa Solomo ali pano. 32 Amuna aku Nineve adzayimilira pakuweruza kotsiriza pamodzi ndi anthu a mbado uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo adalapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani wamkulu, woposa Yona ali pano. 33 Palibe munthu, atayatsa nyali, ayiyika malo obisika, kapena pansi pa muyeso, koma pa choyikapo chake, kuti iwo akulowamo awone kuwala. 34 Nyali yathupi ndiyo diso; pamene pali ponse diso lako liri langwiro thupi lako lonse liwunikidwanso monsemo; koma likakhala loyipa, thupi lako lomwe liri la mdima wokha wokha. 35 Potero yang’anira kuti kuwunika kuli mwa iwe kungakhale mdima. 36 Pamenepo ngati thupi lako lonse liwunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lowunikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuwunikira iwe. 37 Ndipo pakuyankhula Iye, adamuyitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo Iye adakhala pansi nadya. 38 Ndipo pamene Mfarisiyo adawona adazizwa, pakuwona kuti adayamba kudya asadasambe. 39 Koma Ambuye adati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’kati mwanu mudzala zolanda ndi zoyipa. 40 Wopusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapanganso m’kati mwake? 41 Koma patsani mphatso ya chifundo za m’katimo; ndipo onani, zonse ziri zoyera kwa inu. 42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruziro ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo. 43 Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando ya ulemu m’masunagoge, ndi kuyankhulidwa m’misika. 44 Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda wosawoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pawo sadziwa. 45 Ndipo m’modzi wa a chilamulo adayankha, nanena kwa Iye, mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso. 46 Ndipo Iye adati, Tsoka inunso, a chilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu wosautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi. 47 Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda wa aneneri, ndi makolo anu adawapha. 48 Chomwecho muli mboni, ndipo mubvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu adawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda. 49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu idati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza; 50 Kuti mwazi wa aneneri onse, udakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno; 51 Kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zakariya, amene adamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno. 52 Tsoka inu, a chilamulo! Chifukwa mumachotsa chifungulo cha nzeru; inu simudalowamo nokha, ndipo mudawaletsa iwo adalinkulowa. 53 Ndipo pamene Iye adanena zinthu izi kwa iwo, alembi ndi Afarisi adayamba kutsutsana naye kolimba, ndi kumputa Iye kuti ayankhule zinthu zambiri; 54 Nadikirira Iye ndikufuna kuti akakole kanthu kotuluka m’kamwa mwake, ndi kuti akamtsutse

Luka 12

1 Pomwepo pamene anthu a zikwi zikwi a khamu adasonkhana, pamodzi, kotero kuti adapondana, Iye adayamba kunena kwa wophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chiri chinyengo. 2 Pakuti kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika. 3 Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mu mdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwayankhula m’khutu, m’zipinda za mkati chidzalalikidwa pa madenga a nyumba. 4 Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musawope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita. 5 Koma ndidzakulangizani amene muzimuwopa; tawopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kugehena, inde, ndinena ndi inu wopani ameneyo. 6 Kodi mpheta zisanu sizigulitsidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iyiwalika pamaso pa Mulungu. 7 Komatu ngakhale tsitsi lonse la pamutu panu liwerengedwa. Musawopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri. 8 Ndiponso ndinena kwa inu, Amene ali yense adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa munthu adzambvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu: 9 Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu. 10 Ndipo ali yense amene adzanenera Mwana wa munthu zoyipa adzakhululukidwa; koma amene adzanenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa. 11 Ndipo pamene pali ponse adzapita nanu ku mlandu wa m’sunagoge ndi kwa akulu, ndi a mphamvu, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo mawu wotani, kapena mukanena chiyani; 12 Pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena. 13 Ndipo munthu wa m’khamulo adati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma cha masiye. 14 Ndipo adati kwa iye, Munthu iwe, ndani adandiyika Ine ndikhale woweruza, kapena wogawira inu? 15 Ndipo Iye adati kwa iwo, Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiliro uli wonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo. 16 Ndipo Iye adanena nawo fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma udapatsa zambiri: 17 Ndipo adaganizaganiza mwa yekha, nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga? 18 Ndipo iye adati, Ndidzatere; ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiranso dzinthu zanga zonse, ndi katundu wanga. 19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli ndi katundu wambiri wosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere, 20 Koma Mulungu adati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene udazisunga zidzakhala za yani? 21 Atero iye wodziwunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu. 22 Ndipo Iye adati kwa wophunzira ake, chifukwa chake ndinena ndi inu, musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzabvala. 23 Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chobvala. 24 Lingilirani makungubwe, kuti samafesayi, kapena kutemayi, alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu amawadyetsa: nanga inu simuziposa mbalame kwambiri? 25 Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuwonjeza mkono pa msinkhu wake? 26 Kotero ngati simungathe ngakhale chaching’onong’ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija? 27 Lingalirani maluwa, makulidwe awo; sagwilitsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wake wonse sadabvala ngati limodzi la awa. 28 Koma ngati Mulungu abveka kotere udzu wa kuthengo wokhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu wokhulupirira pang’ono. 29 Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima. 30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi inu. 31 Makamaka tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuwonjezerani. 32 Musawopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu. 33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba andalama amene sakutha, chuma chosatha m’Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete sizichiwononga. 34 Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu. 35 Khalani wodzimangira m’chiwuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka; 36 Ndipo inu nokha khalani wofanana ndi anthu woyembekezera mbuye wawo, pamene ati abwera kuchokera ku ukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo. 37 Wodala atumikiwo amene mbuye wawo, pakudza iye, adzawapeza wodikira; indetu ndinena ndi inu, kuti iye adzadzimangira m’chiwuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira. 38 Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, wodala atumiki amenewa. 39 Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba wabwino akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibowoledwe. 40 Khalani wokonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingilira, Mwana wa munthu adzadza. 41 Ndipo Petro adati kwa Iye, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse? 42 Ndipo Ambuye adati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wa nzeru, amene mbuye wake adzamuyika kapitawo wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lawo pa nthawi yake? 43 Wodala mtumikiyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero. 44 Ndinena ndi inu zowona, kuti adzamuyika iye kapitawo wa pa zonse ali nazo. 45 Koma mtumiki uyo akanena mu mtima mwake, mbuye wanga achedwa azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera; 46 Mbuye wa mtumiki uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera ndi nthawi yakuti sayidziwa, nadzamdula iye pakati, nadzamuyika dera lake pamodzi ndi anthu wosakhulupirira. 47 Ndipo mtumiki uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sadakonza, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri. 48 Koma iye amene sadachidziwa, ndipo adazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang’ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene adamuyikizira zambiri, adzamuwuza abwezere zoposa. 49 Ine ndinadzera kuponya moto pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati udatha kuyatsidwa? 50 Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nawo; ndipo ndikakamizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa! 51 Kodi muyesa kuti ndidadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapansi? Ndinena kwa inu, Ayitu, komatu kungawanikana; 52 Pakuti kuyambira tsopano adzakhala m’nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu. 53 Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake, amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wa mkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake. 54 Ndipo Iye adatinso kwa anthu, pamene pali ponse muwona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti ikudza mimvumbi; ndipo itero. 55 Ndipo pamene muwona mphepo ya kumwera iwomba; munena, kuti kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi. 56 Wonyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino? 57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama? 58 Pakuti pamene uli kupita naye m`dani wako kwa woweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m’nyumba yandende. 59 Ine ndinena kwa iwe, sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri komaliza.

Luka 13

1 Ndipo adakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene adamuwuza Iye za Agalileya, amene Pilato adasanganiza mwazi wawo ndi nsembe zawo. 2 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, kodi muyesa kuti Agalileya aja adali anthu wochimwa koposa, Agalileya onse, chifukwa adamva zowawa izi? 3 Ndinena kwa inu, Iyayitu, koma ngati inu simulapa, mudzawonongeka nonse momwemo. 4 Kapena aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yayitali ya m’Siloamu idawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo adali wochimwa koposa anthu onse wokhala m’Yerusalemu? 5 Ndinena kwa inu, Iyayitu; koma ngati simulapa mudzawonongeka nonse chimodzimodzi. 6 Iye adanenanso fanizo ili: Munthu wina adali ndi mtengo wa mkuyu wowoka m’munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma adapeza palibe. 7 Ndipo adati kwa wosungira munda wa mphesa, Tawona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mtengo wa mkuyu uwu; ndipo ndimapeza palibe: tawulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? 8 Ndipo iye adayankha nati kwa Iye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe. 9 Ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino koma ngati ayi, mudzaulikhatu. 10 Ndipo adalikuphunzitsa m’sunagoge mwina, tsiku la Sabata. 11 Ndipo tawonani, padali mkazi amene adali nawo mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopweteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka. 12 Ndipo Yesu m’mene adamuwona, adamuyitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kuzopweteka zako. 13 Ndipo adayika manja ake pa iye; ndipo pomwepo adawongoledwa, nalemekeza Mulungu. 14 Ndipo mkulu wa sunagoge adabvutika mtima, chifukwa Yesu adachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa anthuwo, Alipo masiku asanu ndi limodzi m’menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ayi. 15 Koma Ambuye adamyankha iye, nati Wonyenga iwe, kodi munthu aliyense wa inu samayimasula ng’ombe yake, kapena bulu wake kuchodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukayimwetsa madzi? 16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana adam’manga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata? 17 Ndipo pamene Iye adatero, onse aja wotsutsana naye adanyanzitsidwa; ndipo anthu onse adakondwera ndi zinthu zonse za ulemerero zidachitidwa ndi Iye. 18 Pamenepo Iye adanena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani? 19 Ufanana ndi kambewu kampiru, kamene munthu adatenga, nakaponya m’munda wake wake, ndipo kadamera, ndikukhala mtengo wa ukulu; ndipo mbalame za mumlengalenga zinabindikira mu nthambi zake. 20 Ndiponso Iye adati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? 21 Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi adatenga, nachibisa mu miyeso itatu yaufa, kufikira udatupa wonsewo. 22 Ndipo Iye adapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kumkabe ku Yerusalemu. 23 Ndipo munthu adati kwa Iye, Ambuye wopulumutsidwa ndiwo wowerengeka kodi? Koma Iye adati kwa iwo, 24 Yesetsani kulowa chipata chopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuwuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza. 25 Pamene atawuka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuyima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati kwa inu; sindidziwa inu kumene muchokerako: 26 Pomwepo mudzayamba kunena, ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo mudaphunzitsa m’makwalala a kwathu. 27 Ndipo Iye adzati, Sindikudziwani kumene inu muchokera. Chokani kwa Ine inu akuchita kusaweruzika. 28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzawona Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mukutulutsidwa kunja. 29 Ndipo anthu adzachokera kum’mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu. 30 Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala woyamba, ndipo alipo woyamba adzakhala akuthungo. 31 Tsiku lomwelo adadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha inu. 32 Ndipo Iye adati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Tawonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa,ndipo mkucha ndidzakhalitsidwa wangwiro. 33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi m’kucha, chifukwa sikuloleka kuti m’neneri awonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu. 34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi woponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawiri kawiri ndidafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simudafuna ayi! 35 Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, simudzandiwona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m’dzina la Ambuye.

Luka 14

1 Ndipo padali pamene Iye adalowa m’nyumba ya m’modzi wa akulu afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo adalikumzonda Iye. 2 Ndipo onani, padali pamaso pake munthu wambulu. 3 Ndipo Yesu adayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena ayi? 4 Koma iwo adakhala chete. Ndipo adamtenga namchiritsa, namuwuza apite. 5 Ndipo adati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzayitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi? 6 Ndipo iwo sadatha kumuyankha pa zinthu izi. 7 Ndipo Iye adanena fanizo kwa woyitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo. 8 Pamene pali ponse wayitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usakhale pa mpando wa ulemu; kuti kapena wina wa ulemu woposa iwe adzayitanidwa ndi iye, 9 Ndipo pakufika iye amene adayitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba kuchita manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo. 10 Koma pamene pali ponse wayitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye adakuyitana iwe akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse, akuseyama pachakudya pamodzi ndi iwe. 11 Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wodzichepetsa adzakulitsidwa. 12 Pamenepo Iye adanenanso kwa iye amene adamuyitana, pamene ukonza chakudya cha pa usana kapena cha madzulo, usayitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuyitana iwe, ndipo udzakhala nako kubwezeredwa. 13 Koma pamene ukonza phwando uyitane a umphawi, wopunduka, wotsimphina, akhungu; 14 Ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuwuka kwa wolungama. 15 Ndipo pamene wina wa iwo akukhala pachakudya pamodzi ndi Iye atamva izi, adati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu. 16 Koma adati kwa iye, Munthu wina adakonza phwando lalikulu; nayitana anthu ambiri; 17 Ndipo adatumiza mtumiki wake pa nthawi ya mphwando kukanena kwa woyitanidwawo, idzani chifukwa zonse zakonzeka tsopano. 18 Ndipo onse ndi mtima umodzi adayamba kuwilingula. Woyamba adati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituLuka ndikawuwone; ndikupempha undilole ine ndisafike. 19 Ndipo wina adati, Ine ndagula ng’ombe za magoli asanu, ndipo ndimka kukaziyesa; ndikupempha undilole ndisafike. 20 Ndipo wina adati, ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza. 21 Ndipo mtumikiyo pakubwera adawuza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba adakwiya, nati kwa mtumiki wakeyo, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mudzi, nubwere nawo muno aumphawi ndi wopunduka ndi akhungu ndi wotsimphina. 22 Ndipo mtumikiyo adati, ‘Ambuye, chimene mudachilamulira chachitika, ndipo malo akadalipobe’. 23 Ndipo mbuye adanena kwa mtumikiyo, Tuluka, nupite ku misewu ndi njira za kuminda, nuwawumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale. 24 Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe m’modzi wa amuna woyitanidwa aja adzalowa phwando langa. 25 Ndipo khamu lalikulu lidapita naye; ndipo Iye adapotoloka nati kwa iwo, 26 Ngati munthu adza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale ake, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga. 27 Ndipo amene ali yense sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga. 28 Pakuti ndani wa inu amene akufuna kumanga nsanja yayitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo zakuyimaliza? 29 Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya maziko ake, wosakhoza kuyimaliza, anthu onse woyang’ana adzayamba kumseka iye. 30 Ndikunena kuti, Munthu uyu adayamba kumanga, koma sadathe kumaliza. 31 Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu imzake, siyiyamba yakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikari ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikari zikwi makumi awiri? 32 Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere. 33 Chomwecho ndinena kwa inu, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga. 34 Mchere ndi wa bwino; koma ngati mchere usukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani? 35 Suyenera kuwuthira pamunda kapena padzala, anthu autaya kunja. Amene ali nawo makutu akumva amve.

Luka 15

1 Pamenepo adayandikira kwa Iye a misonkho onse ndi anthu wochimwa kudzamva Iye. 2 Ndipo Afarisi ndi alembi adanyinyirika nati, Munthu uyu alandira anthu wochimwa, nadya nawo. 3 Ndipo Iye adayankhula fanizo ili kwa iwo, nanena, 4 Munthu ndani wa inu, ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, nalondola yotaikayo, kufikira atayipeza? 5 Ndipo pamene ayipeza, ayisenza pa mapewa ake mokondwera. 6 Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nawo, kondwerani ndi ine, chifukwa ndayipeza nkhosa yanga yotayikayo. 7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa m’modzi wolapa, koposa anthu wolungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusowa kulapa. 8 Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama za siliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira atayipeza? 9 Ndipo m’mene ayipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndidayipeza ndalama ndidatayayo. 10 Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa m’modzi amene walapa. 11 Ndipo Iye adati, Munthu wina adali ndi ana amuna awiri: (Kuyenda ulendo) 12 Ndipo wam’ng’onoyo adati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye adamugawira za moyo wake. 13 Ndipo pakupita masiku wowerengeka mwana wam’ng’ono adasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake ku dziko lakutali; ndipo komweko adamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko. ( Umphawi wa kudziko lakutali ) 14 Ndipo pamene adatha zake zonse, padakhala njala yayikulu m’dziko muja, ndipo iye adayambakusowa. 15 Ndipo adapita nadziphatikiza kwa mfulu imodzi yadziko lija; ndipo uyu adamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba. 16 Ndipo adalakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu adam’ninkha kanthu. (Kulapa) 17 Koma pamene adakumbukira mumtima, adati, Antchito wolipidwa ambiri wa atate wanga, ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndiwonongeke kuno ndi njala? 18 Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndidachimwira kumwamba ndi pamaso panu. 19 Ndipo sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati m’modzi wa antchito anu. 20 Ndipo iye adanyamuka, nadza kwa atate wake, koma pakudza iye kutali, atate wake adamuwona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsopsonetsa. 21 Ndipo mwanayo adati kwa iye, Atate ndidachimwira kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. 22 Koma atateyo adati kwa atumiki ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni mphete ku dzanja lake ndi nsapato ku mapazi ake; ( Chisangalalo ) 23 Ndipo idzani naye mwana wa ng’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere. 24 Chifukwa mwana wanga uyu adali wokufa, ndipo tsopano wakhala ndi moyo. Ndipo adayamba kusekera. ( Mfarisi ) 25 Koma mwana wake wamkulu adali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, adamva kuyimba ndi kubvina. 26 Ndipo iye adayitana m’modzi wa mtumiki, namfunsa, zinthu izi nzotani? 27 Ndipo iye adati kwa iye, M’ng’ono wako wafika; ndipo atate wako adapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa adamlandira iye wamoyo. 28 Koma iye adakwiya ndipo sadafuna kulowanso. Ndipo atate wake adatuluka namdandaulira. 29 Koma iye adayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndidakhala mtumiki wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindidalakwira lamulo lanu nthawi ili yonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. 30 Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha za moyo zanu ndi akazi achiwerewere, mudamphera iye mwana wa ng’ombe wonenepa. 31 Koma iye adanena naye, Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthawi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako. 32 Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwera: chifukwa m’ng’ono wako uyu adali wakufa ndipo ali ndi moyo; adatayika, ndipo wapezeka.

Luka 16

1 Ndipo Iye adanenanso kwa wophunzira ake, padali munthu mwini chuma, adali ndi kapitawo wake; ndipo ameneyu adanenezedwa kwa iye kuti adali kumwaza chuma chake. 2 Ndipo adamuyitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitawo wako, pakuti sungathe kukhalabe kapitawo. 3 Ndipo kapitawo uyu adati mumtima mwake, ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga wandichotsera ukapitawo? Kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. 4 Ndidziwa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene anditulutsa mu ukapitawo, anthu akandilandire kunyumba kwawo. 5 Ndipo adadziyitanira m’modzi ndi m’modzi amangawa onse a mbuye nati kwa woyamba, udakongola chiyani kwa mbuye wanga? 6 Ndipo adati, mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye adanena naye, tenga, nukhale pansi msanga, nulembere, makumi asanu. 7 Pomwepo adati kwa wina, ndipo iwe uli nawo mangawa wotani? Ndipo uyu adati; Mitanga ya tirigu zana. Iye adanena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu. 8 Ndipo mbuye wake adatama kapitawo wonyengayo, kuti adachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m’mbadwo wawo koposa ana a kuwunika. 9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani; iwo akalandire inu m’mahema wosatha. 10 Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’ono alinso wosalungama m’chachikulu. 11 Chifukwa chake ngati simukhala wokhulupirika m’chuma chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma chowona? 12 Ndipo ngati simudakhala wokhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni? 13 Palibe m’mtumiki wa m’nyumba akhoza kukhala mtumiki wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina; nadzakonda winayo kapena adzakangamira winayo; nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala mtumiki wa Mulungu ndi wa chuma. 14 Koma Afarisi, ndiwo wokonda ndalama, adamva izi zonse; ndipo adamseka Iye. 15 Ndipo Iye adati kwa iwo, Inu ndinu wodziyesera nokha wolungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa chake ichi chimene chilemekezedwa koposa pakati pa anthu ndi chonyansa pamaso pa Mulungu. 16 Chilamulo ndi aneneri adalipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu ali yense akangamira kulowamo. 17 Kuti Kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang’ono kachilamulo kagwe nkwapatali. 18 Aliyense wosudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo. 19 Ndipo padali munthu mwini chuma amabvala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse: 20 Ndipo padali wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adayikidwa pachipata pake wodzala ndi zilonda, 21 Ndipo adafuna kukhuta ndi zakugwa pagome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zironda zake; 22 Ndipo kudali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti adatengedwa iye ndi angelo kupita ku chifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, nayikidwa m’manda. 23 Ndipo m’gehena adakweza maso ake, pokhala nawo mazunzo, nawona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’chifukwa mwake. 24 Ndipo adakweza mawu nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti abviyike msonga ya chala chake m’madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m’lawi ili lamoto. 25 Koma Abrahamu adati, Mwana, kumbukira kuti udalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemonso Lazaro zoyipa; ndipo tsopano iye atonthozedwa pano, koma iwe uzunzidwadi. 26 Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo wofuna kuwoloka kuchokera kuno kupita kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife sangathenso. 27 Koma iye adati, pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; 28 Pakuti ndiri nawo abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze ku malo ano a mazunzo. 29 Abrahamu adati; Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. 30 Koma iye adati, Iyayi, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa akufa adzalapa. 31 Koma adati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akawuka kwa akufa.

Luka 17

1 Ndipo adati Iye kwa wophunzira ake, sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo. 2 Ndi kwabwino kwa iye kukolowekedwa mwala wa mphero m’khosi mwake ndi kuponyedwa iye m’nyanja nkwapafupi koposa, kukhumudwitsa m’modzi wa ang’ono awa. 3 Kadzichenjerani akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire. 4 Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; Udzimkhululukira. 5 Ndipo atumwi adati kwa Ambuye, wonjezerani chikhulupiriro chathu. 6 Koma Ambuye adati ngati, Mukadakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wa mkuyu, Uzulidwe, nuwokedwe m’nyanja; ndipo ukadamvera inu. 7 Koma ndani mwa inu ali naye mtumiki wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi udye; 8 Wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe? 9 Kodi ayamika mtumikiyo chifukwa kuti adachita molamulidwa sindinganiza choncho? 10 Chotero inunso m’mene mutachita zonse zimene adakulamulirani, nenani, Ife ndife atumiki wosapindula tangochita zimene tayenera kuzichitazo. 11 Ndipo kudali, popita ku Yerusalemu Iye adalikudutsa pakati pa Samariya ndi Galileya. 12 Ndipo m’mene adalowa Iye m’mudzi wina, adakomana naye amuna khumi akhate, amene adayima kutali; 13 Ndipo iwo adakweza mawu, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire ife chifundo. 14 Ndipo pakuwawona adati kwa iwo, Pitani, kadziwonetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kudali, m’kupita kwawo, adakonzedwa. 15 Ndipo m’modzi wa iwo, pakuwona kuti adachiritsidwa, adabwerera m’mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mawu akulu; 16 Ndipo adagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo adali Msamariya ameneyo. 17 Ndipo Yesu adayankha nati, Kodi sadakonzedwa khumi? Koma ali kuti asanu ndi anayi aja? 18 Sadapezeka wobwera kudzalemekeza Mulungu koma mulendo uyu yekha. 19 Ndipo adati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. 20 Ndipo pamene Afarisi adamfunsa Iye, kuti Ufumu wa Mulungu ukudza liti; adawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi mawonekedwe; 21 Ndipo sadzanena, Tawonani uwu, kapena uwo! Pakuti, tawonani, Ufumu wa Mulungu uli m’kati mwa inu. 22 Ndipo Iye adati kwa wophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuwona limodzi la masiku a mwana wa munthu, koma simudzaliwona ilo. 23 Ndipo adzanena ndi inu, Tawonani ilo! Tawonani ili! Musachoka kapena kuwatsata. 24 Pakuti monga mphezi ing’anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niwunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu m’tsiku lake. 25 Koma ayenera ayambe wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi m’badwo uno 26 Ndipo monga kudakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu. 27 Anadya adamwa, adakwatira, adakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa adalowa m’chombo, ndipo chinadza chigumula, nichiwawononga onsewo. 28 Monga momwenso kudakhala masiku a Loti; anadya, adamwa, anagula adagulitsa, adadzala, adamanga nyumba; 29 Koma tsiku limene Loti adatuluka m’Sodoma udabyumbwa moto ndi Sulfure zochokera kumwamba, ndipo zidawawononga onsewo. 30 Momwemo kudzakhala tsiku lakubvumbuluka Mwana wa munthu. 31 Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa denga, ndi akatundu ake m’nyumba, asatsike kukatenga; ndipo iye amene ali m’munda chimodzimodzi asabwere ku zake za m’mbuyo. 32 Kumbukirani mkazi wa Loti. 33 Iye ali yense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye ali yense adzautaya, adzausunga. 34 Ndinena ndi inu, usiku womwewo anthu adzakhala awiri pakama m’modzi; m’modzi adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa. 35 Padzakhala akazi awiri wopera pamodzi, m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. 36 Padzakhala amuna awiri m’munda; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. 37 Ndipo iwo adayankha nanena kwa Iye, kuti Ambuye? Ndipo adati kwa iwo kumene kulikonse kuli mtembo, pomweponso mbalame za miyimba zidzasonkhana.

Luka 18

1 Ndipo adawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima; 2 Nanena, mumzinda mwa kuti mudali woweruza wosawopa Mulungu ndi wosasamala munthu. 3 Ndipo m’mumzinda mudali mkazi wa masiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane. 4 Ndipo sadafuna pa nthawiyo; koma bwino bwino adati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusasamala munthu; 5 Koma chifukwa cha kundibvuta ine mkazi wa masiye ameneyu ndidzamuweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kubwerabwera kwake. 6 Ndipo Ambuye adati; Tamverani chonena woweruza wosalungama. 7 Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo wosankhidwa ake akumuyitana usana ndi usiku popeza aleza nawo mtima? 8 Ndinena ndi inu, Adzawachitira chilungamo mwachangu. Koma mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi? 9 Ndipo adatinso kwa ena amene adadzikhulupirira mwa iwo wokha kuti adali wolungama, napeputsa onse ena: 10 Anthu awiri adakwera kupita kukachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mzake wamsonkho. 11 Mfarisi adayimilira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, wopambapamba, wosalungama, achigololo, kapenanso monga wa msonkho uyu. 12 Ndimasala chakudya kawiri Sabata limodzi, ndimapereka limodzi la magawo khumi la zonse ndiri nazo. 13 Koma wamsonkhoyo adayima patali sadafuna kungakhale kukweza maso Kumwamba, komatu adadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu mundichitire chifundo, ine wochimwa. 14 Ndinena ndi inu, Munthu uyu adatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama osati uja ayi: pakuti yense wodzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa. 15 Ndipo adadza nawo kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene wophunzira adawona, adawadzudzula. 16 Koma Yesu adawayitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa wotere. 17 Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu. 18 Ndipo mkulu wina adamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha? 19 Koma Yesu adati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji, palibe wabwino, koma m’modzi, ndiye Mulungu. 20 Udziwa malamulo Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako. 21 Ndipo adati, Izi zonse ndazisunga kuyambira pa ubwana wanga. 22 Tsopano pamene Yesu adamva izi, adati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi; gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma cheni cheni m’Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. 23 Koma pamene adamva izi adagwidwa ndi chisoni chambiri; pakuti adali nacho chuma chambiri. 24 Ndipo Yesu pomuwona iye kuti adali ndi chisoni, Iye adati Ha! Nkobvuta kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! 25 Pakuti nkwapafupi kwa ngamila ipyole pa diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali. 26 Koma akumvawo adati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa? 27 Ndipo Iye adati, zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu. 28 Pamenepo Petro adati, Tawonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu. 29 Koma adati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum’bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu. 30 Koma adzalandira zobwezedwa koposatu m’nthawi yino; ndipo m’nthawi ili nkudza moyo wosatha. 31 Ndipo adadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Tawonani, tikwera kumka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa munthu zonse zolembedwa ndi aneneri. 32 Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malobvu. 33 Ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo pa tsiku la chitatu adzawukanso. 34 Ndipo sadadziwitsa kanthu ka izi: ndi mawu awa adawabisikira ndipo sadazindikira zonenedwazo. 35 Ndipo kunali pamene adayandikira ku Yeriko, msawona wina adakhala m’mbali mwa njira, napemphapempha: 36 Ndipo pakumva khamu la anthu alimkupita, adafunsa; Ichi nchiyani? 37 Ndipo adamuwuza iye, Yesu wa ku Nazarete ali kudutsa apa. 38 Ndipo adafuwula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo. 39 Ndipo iwo wotsogolera adamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye adafuwulitsa kwambiri, Mwana wa Davide, Mundichitire ine chifundo. 40 Ndipo Yesu adayima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m’mene adafika pafupi, adamfunsa iye, 41 Nanena, ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo iye adati, Ambuye, kuti ndipenyenso. 42 Ndipo Yesu adati kwa iye, penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. 43 Ndipo pomwepo adapenyanso, namtsata Iye, nalemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuwona, adachitira Mulungu mayamiko.

Luka 19

1 Ndipo Yesu adalowa, napyola pa Yeriko. 2 Ndipo tawonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyu; ndipo iye adali mkulu wa amisonkho, adali wachuma. 3 Ndipo adafuna kuwona Yesu ndiye uti, ndipo sadathe, chifukwa cha kupanikizana, pakuti adali wamfupi msinkhu. 4 Ndipo adathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuwona Iye; pakuti adati apita njira yomweyo. 5 Ndipo m’mene anadza pamalopo Yesu adakweza maso nati kwa iye, Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m’nyumba mwako. 6 Ndipo adafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera. 7 Ndipo m’mene adachiwona adang`ung`udza onse, nanena, Adalowa amchereze munthu ali wochimwa. 8 Ndipo Zakeyu adayimilira nati kwa Ambuye, Tawonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndidalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndidzambwezera kanayi. 9 Ndipo Yesu adati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu. 10 Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho. 11 Ndipo pakumva izi iwo, Iye adawonjeza nanena fanizo, chifukwa adali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo adayesa kuti Ufumu wa Mulungu udzawonekera pomwepo . 12 Pamenepo Iye adati, Munthu wa fuko lomveka adamka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. 13 Ndipo adayitana atumiki ake khumi, nati kwa iwo, chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. 14 Koma mfulu za pa mudzi pake zidamuda, nizituma akazembe amtsate m’mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyu akhale mfumu yathu. 15 Ndipo kunali pakubwera iye, atalandira ufumuwo, adati ayitanidwe kwa iye atumiki aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo adapindulira pochita malonda. 16 Ndipo adafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu idachita niwonjeza ndalama khumi. 17 Ndipo adati kwa iye, Chabwino mtumiki wa bwino iwe; popeza udakhala wokhulupirika m’chaching’ono, khala nawo ulamuliro pa mizinda khumi. 18 Ndipo adadza wachiwiri, nanena, Mbuye ndalama yanu yapindula ndalama zisanu. 19 Ndipo adati kwa iyenso, khala iwenso woweruza mizinda isanu. 20 Ndipo wina adadza, nanena, Mbuye, tawonani, siyi ndalama yanu, ndayisunga m’kasalu: 21 Pakuti ndidakuwopani, popeza inu ndinu munthu wowuma mtima: munyamula chimene simudachiyika pansi, mututa chimene simudachifesa. 22 Ndipo adanena kwa iye, Pakamwa pako ndi kuweruza, mtumiki woyipa iwe, udadziwa kuti ine ndine munthu wowuma mtima, wonyamula chimene sindidachiyimika, ndi wotuta chimene sindidachifesa; 23 Ndipo sudapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadayitenga ndi phindu lake? 24 Ndipo adati kwa iwo akuyimilirapo, Mchotsereni ndalamayo, nimupatse iye wokhala nazo ndalama khumi. 25 Ndipo iwo adati kwa Iye, Ambuye, ali nazo ndalama khumi. 26 Ndinena ndi inu, kuti yense wokhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa. 27 Koma adani anga aja wosafuna kuti ndidzakhale mfumuyawo, bwerani nao kuno nimuwaphe pamaso panga. 28 Ndipo m’mene adanena izi adawatsogolera nakwera kumka ku Yerusalemu. 29 Ndipo kudali, m’mene Iye adayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lotchedwa la Azitona, adatuma awiri a wophunzira ake. 30 Nanena, Pitani ku mudzi uli pandunji panu; m’menemo, polowa, mudzapeza mwana wabulu womangidwa, pamenepo palibe munthu adakwerapo nthawi ili yonse; mum’masule iye nimubwere naye. 31 Ndipo munthu akati kwa inu, mum’masuliranji? Mudzatero naye, Ambuye amfuna iye. 32 Ndipo adachoka wotumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo. 33 Ndipo pamene adamasula mwana wa bulu, eni ake adati kwa iwo, Mum’masuliranji mwana wa bulu? 34 Ndipo iwo adati, Ambuye amfuna iye. 35 Ndipo adadza naye kwa Yesu; ndipo adayalika zobvala zawo pa mwana wabuluyo, nakwezapo Yesu. 36 Ndipo pakupita Iye, adayala zobvala zawo m’njira. 37 Ndipo poyandikira Iye tsono potsetsereka pake pa phiri la Azitona, khamu lonse la wophunzira lidayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mawu akulu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu adaziwona; 38 Nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye; mtendere m’Mwamba, ndi ulemerero m’Mwambamwamba. 39 Ndipo Afarisi ena a m’khamu la anthu adati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani wophunzira anu. 40 Ndipo Iye adayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa akhala chete miyala idzafuwula pomwepo. 41 Ndipo m’mene adayandikira, adawona mzindawo nawulirira. 42 Nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako. 43 Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; 44 Ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala umodzi pa umzake; popeza sudazindikira nyengo yakuyenderedwa kwako. 45 Ndipo Iye adalowa m’kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa ndi kugula malonda; 46 Nanena kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga ndi nyumba yakupemphereramo; koma inu mwayiyesa iyo phanga la achifwamba. 47 Ndipo adalikuphunzitsa m’kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu a anthu adafunafuna njira yomuwonongera Iye; 48 Ndipo sadapeza chimene adzamchitira: pakuti anthu onse adali ndi chidwi pakumva Iye.

Luka 20

1 Ndipo kudali lina la masiku awo m’mene Iye adalikuphunzitsa anthu m’kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe akulu ndi alembe adadza kwa Iye. 2 Ndipo iwo adati kwa Iye, nanena, Mutiwuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene adakupatsani ulamuliro umenewu? 3 Ndipo Iye adayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani Inenso chinthu chimodzi mundiwuze. 4 Ubatizo wa Yohane udachokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? 5 Ndipo adakambirana mwa wokha, nanena, Ngati tinena udachokera Kumwamba; adzati, simudamkhulupilira chifukwa ninji? 6 Ndiponso ngati tikanena, Udachokera kwa anthu, anthu onse adzatiponya miyala; pakuti adakopeka mtima, kuti Yohane adali m’neneri. 7 Ndipo iwo adayankha kuti sitikuwuzani kumene udachokera. 8 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ndingakhale Inenso sindikuwuzani za ulamuliro umene ndichita zinthu izi. 9 Ndipo Iye adayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu wina adalima munda wa mphesa, nawukongoletsa kwa wolima munda, napita kudziko lakutali nagonerako nthawi yayikulu. 10 Ndipo pa nyengo ya zipatso adatumiza mtumiki wake kwa wolima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo: koma wolimawo adampanda, nambweza wopanda kanthu. 11 Ndipo adatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso adampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu. 12 Ndipo adatumizanso wina wa chitatu; ndipo iyenso adamvulaza, namtaya kunja. 13 Ndipo adati mwini mundawo, Ndidzachita chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga amene ndikondana naye; kapena adzamchitira iye ulemu. 14 Koma wolimawo, pamene adamuwona, adawuzana wina ndi mzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba, tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu. 15 Ndipo adamponya kunja kwa mundawo, namupha. Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawachitira chiyani? 16 Iye adzafika nadzawononga wolima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo adamva, adati Mulungu asatero! 17 Koma Iye adawapenyetsetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chidalembedwa, Mwala umene womanga nyumba adawukana, womwewo udakhala mutu wa pangodya. 18 Munthu ali yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupera ngati ufa. 19 Ndipo alembi ndi ansembe akulu adafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo adawopa anthu; pakuti adazindikira kuti adanenera pa iwo fanizo ili. 20 Ndipo adamyang’anira, natumiza wozonda, amene adadziwonetsera ngati wolungama mtima, kuti akamkole pa mawu ake, kotero kuti akampereke Iye kwa akulu ndi aulamuliro wa kazembe. 21 Ndipo adamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu kowonadi. 22 Kodi mkuloledwa kwa ife kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 23 Koma Iye adazindikira Chinyengo chawo, nati kwa iwo, chifukwa chiyani mukundiyesa? 24 Tandiwonetsani Ine khobiri. Chithunzithunzi ndi cholemba chake nchayani? Adati iwo, cha Kayisala. 25 Ndipo Iye adati kwa iwo, chifukwa chake perekani kwa Kayisala zake za Kayisala, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. 26 Ndipo sadakhoza kugwira mawuwo pamaso pa anthu; ndipo adazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete. 27 Ndipo anadza kwa Iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; ndipo adamfunsa Iye, 28 Nanena, Mphunzitsi, Mose adatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuwukitsira mbale wake mbewu. 29 Tsono padali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba adakwatira mkazi , nafa wopanda mwana; 30 Ndipo wachiwiri adamkwatira mkaziyo, nafa, nasiya wopanda mwana,, 31 Ndipo wachitatu adamtenga mkaziyo; ndipo choteronso asanu ndi awiri onse, sadasiya mwana, namwalira. 32 Pomalizira adamwaliranso mkaziyo. 33 Chotero pa kuwuka kwa akufa iye adzakhala mkazi wayani wa iwo? Pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye. 34 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ana adziko lapansi akwatira nakwatiwa: 35 Koma iwo akuyesedwa woyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuwuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa: 36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuwuka kwa akufa. 37 Tsopano popeza akufa awuka, adasonyeza ngakhale Mose, pa chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. 38 Pakuti Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye. 39 Ndipo alembi ena adayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino. 40 Pakuti sadalimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu kena. 41 Koma Iye adati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye Mwana wa Davide? 42 Pakuti Davide yekha anena m’buku la Masalmo, Ambuye adanena kwa Ambuye wanga, khala padzanja langa lamanja. 43 Kufikira Ine ndidzayika adani ako pansi pa mapazi ako. 44 Chotero Davide adamtchula Iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake bwanji? 45 Ndipo pamene anthu onse adalimkumva Iye, adati kwa wophunzira. 46 Chenjerani nawo alembi, amene afuna kuyendayenda wobvala miyinjiro, nakonda kuyankhulidwa m’misika, ndi mipando ya ulemu m`masunagoge ndi zipinda za ulemu m`maphwando; 47 Amene awononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.

Luka 21

1 Ndipo Yesu adakweza maso, nawona anthu eni chuma alikuyika zopereka zawo mosungiramo ndalama. 2 Ndipo adawona mkazi wina wamasiye waumphawi akuyika momwemo timakobiri tiwiri. 3 Ndipo Iye adati, Zowonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi adayikamo koposa onse; 4 Pakuti onse amenewa adayika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma Iye mwa kusowa kwake adayikamo za moyo wake, zonse adali nazo. 5 Ndipo pamene ena adalikunena za kachisiyo, kuti adakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, adati Iye, 6 Zinthu izi mukuziwona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala umzake, umene sudzagwetsedwa. 7 Ndipo iwo adamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzawoneka liti? Ndipo chizindikiro chake ndi chiyani pamene izi ziti zidzachitike? 8 Ndipo Iye adati, Yang’anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m’dzina langa, nadzanena, Ndine Khristu ndipo, nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pawo. 9 Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mipanduko, musawopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo. 10 Pamenepo Iye adanena kwa iwo, Mtundu wa anthu udzawukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: 11 Ndipo kudzakhala zibvomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akuti akuti, ndipo kudzakhala zowopsa ndi zizindikiro zazikulu zochokera kumwamba. 12 Koma zisadachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzapita nanu kwa mafumu ndi akazembe chifukwa cha dzina langa. 13 Ndipo kudzakhala kwa inu ngati umboni. 14 Chifukwa chake tsimikizani mumtima mwanu, kuti usadafike mlandu musalingilire chimene mudzayankha. 15 Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa. 16 Ndipo mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi afuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani. 17 Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa. 18 Ndipo silidzawonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu. 19 Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiliro. 20 Koma pamene pali ponse mudzawona, Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a nkhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira. 21 Pamenepo iwo ali m’Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumilaga asalowemo. 22 Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zikwaniritsidwe. 23 Koma tsoka iwo akukhala ndi mwana ndi akuyamwitsa masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa. 24 Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kumka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zawo za anthu akunja zakwanira . 25 Ndipo kudzakhala zizindikiro padzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkokomo wake pa nyanja ndi mafunde ake; 26 Anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirimkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27 Ndipo pamenepo adzawona Mwana wa munthu alimkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. 28 Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira. 29 Ndipo adanena nawo fanizo; Onani mtengo wa mkuyu ndi mitengo yonse; 30 Pamene iphuka, muyipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo. 31 Inde, chotero inunso pakuwona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. 32 Indetu ndinena ndi inu, M`bado uno sudzapitirira, kufikira zonse zitakwaniritsidwa. 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mawu anga sadzapita. 34 Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyayidya ndi kuledzera ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa. 35 Pakuti ngati msampha lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi. 36 Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera nthawi zonse, kuti inu mudzayesedwa woyenera ndi kupulumuka kuzinthu izi zonse zimene zidzachitika, ndi kuyimilira pamaso pa Mwana wa Munthu. 37 Ndipo usana uli wonse Iye adalikuphunzitsa m’kachisi; ndi usiku uli wonse adatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona. 38 Ndipo anthu onse adalawira m`mamawa kudza kwa Iye ku kachisi kudzamvera Iye.

Luka 22

1 Tsopano phwando la mikate yopanda chotupitsa lidayandikira, ndilo lotchedwa Paskha. 2 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adafunafuna njira yomuphera Iye chifukwa adawopa anthuwo. 3 Pamenepo Satana adalowa mwa Yudase wonenedwa Isikariyote, amene adawerengedwa m’modzi wa khumi ndi awiriwo. 4 Ndipo iye adachoka nayankhulana ndi ansembe akulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo. 5 Ndipo adakondwera, napangana naye kumpatsa Iye ndalama. 6 Ndipo iye adalonjeza, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu. 7 Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa lidafika, limene idayenera kuphedwa nsembe ya paskha. 8 Ndipo Iye adatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife Paskha, kuti tidye. 9 Ndipo iwo adanena naye, Mufuna tikakonzere kuti? 10 Ndipo Iye adati kwa iwo, Onani, mutalowa m’mzinda, adzakomana ndi inu munthu atasenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye. 11 Ndipo mukanene kwa mwini nyumba wabwinoyo, Mphunzitsi anena nawe, chipinda cha alendo chiri kuti, m’mene ndikadye Paskha pamodzi ndi wophunzira anga? 12 Ndipo iyeyo adzakuwonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko. 13 Ndipo adapita iwo, napeza monga adatero nawo; ndipo adakonza Paskha. 14 Ndipo itadza nthawi yake, Iye adakhala pachakudya, pansi ndi atumwi khumi ndi awiri pamodzi naye. 15 Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndidalakalaka ndithu kudya paskha uyu pamodzi ndi inu, ndisadayambe kusautsidwa. 16 Pakuti ndinena ndi inu, Sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu. 17 Ndipo adatenga chikho, ndipo pamene adayamika, adati; Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha. 18 Pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika. 19 Ndipo adatenga mkate, nayamika, adaunyema, nawapatsa, nanena, ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa. 20 Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu. 21 Koma onani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi ine. 22 Pakuti zowonadi Mwana wa munthu amukatu, monga kudayikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka Iye! 23 Ndipo adayamba kufunsana mwa iwo wokha, ndiye yani mwa iwo amene adzachita ichi. 24 Ndipo kudakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu. 25 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, ochitira zabwino. 26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wang’ono; ndi iye ali mfumu, akhale ngati wotumikira. 27 Pakuti wamkulu ndani, iye wakukhala pachakudya kapena wotumikirapo? Si ndiye wakukhala pachakudya kodi? Koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira. 28 Koma inu ndinu amene mudakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga. 29 Ndipo Ine ndikuyikirani ufumu, monganso Atate wanga adandiyikira Ine, 30 Kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli. 31 Ndipo Ambuye adati, Simoni, Simoni, tawona, Satana adafuna akutenge kuti akupete ngati tirigu: 32 Koma ndidakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ulimbikitse abale ako. 33 Ndipo adati kwa Iye, Ambuye ndiri wokonzeka kupita ndi Inu, kundende ndi kuimfa. 34 Ndipo Iye adati, Ndikuwuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine. 35 Ndipo Iye adati kwa iwo, pamene ndidakutumizani wopanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba ndi nsapato, mudasowa kanthu kodi? Ndipo iwo sadanene kanthu. 36 Ndipo pamenepo adati kwa iwo, Koma tsopano iye amene ali ndi thumba la ndalama alitenge, ndi thumba lakamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga. 37 Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwaniritsidwa mwa Ine, Ndipo adawerengedwa ndi anthu wophwanya lamulo; pakuti izi zakwa Ine ziri nacho chimaliziro. 38 Ndipo iwo adati, Ambuye, tawonani, malupanga awiri awa. Ndipo Iye adati kwa iwo, Chakwanira. 39 Ndipo Iye adatuluka, napita monga adafuchita, ku phiri la Azitona; ndipo wophunzira adamtsata Iye. 40 Ndipo pofika pamalopo, adati kwa iwo, pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa. 41 Ndipo adapatukana nawo kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera. 42 Nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike. 43 Ndipo adamuwonekera Iye m’ngelo wa Kumwamba namlimbikitsa Iye. 44 Ndipo pokhala Iye m’chipsinjo mtima adapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake lidakhala ngati madontho akulu a mwazi ali mkugwa pansi. 45 Ndipo pamene adanyamuka pakupemphera anadza kwa wophunzira, nawapeza ali m’tulo ndi chisoni. 46 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mugoneranji? Dzukani, pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa. 47 Pamene Iye adali chiyankhulire, tawonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, adawatsogolera; nayandikira Yesu nampsopsona Iye. 48 Koma Yesu adati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi chimpsopsono kodi? 49 Ndipo m’mene iwo akumzinga Iye adawona chimene chiti chichitike, adati, Ambuye tikanthe ndi lupanga kodi? 50 Ndipo wina wa iwo adakantha mtumiki wa mkulu wa nsembe, namdula khutu lake lamanja. 51 Koma Yesu adayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo adakhudza khutu lake, namchiritsa. 52 Ndipo pamenepo Yesu adati kwa ansembe akulu ndi akapitawo a kachisi, ndi akulu amene anadza kumgwira Iye, mudatuluka ndi malupanga ndi zibonga kodi monga ngati mugwira wachifwamba? 53 Masiku onse, pamene ndidali ndi inu m’kachisi, simudatansa manja anu kundigwira: koma nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa m’dima ndi wanu. 54 Ndipo pamenepo adamtenga Iye, napita naye, nalowa m’nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro adamtsata patali. 55 Ndipo pamene adasonkha moto m’kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro adakhala pakati pawo. 56 Ndipo m’dzakazi wina adamuwona iye alikukhala m’kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso adali naye. 57 Koma iye adakana, nati, mkaziwe, Sindimdziwa Iye. 58 Ndipo popita kamphindi, adamuwona wina, nati, Iwenso uli m’modzi wa iwo. Koma Petro adati, Munthu iwe, sindine. 59 Ndipo patapita ngati ola limodzi, wina adanenetsa, kuti, Zowonadi, munthu uyunso adali naye, pakuti ndiye Mgalileya. 60 Koma Petro adati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chiyankhulire tambala adalira. 61 Ndipo Ambuye adapotoloka, nayang’ana Petro. Ndipo Petro adakumbukira mawu a Ambuye, kuti adati kwa iye, Asadalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu. 62 Ndipo Petro adatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima. 63 Ndipo amuna amene adalikusunga Yesu adam’nyoza Iye, nampanda. 64 Ndipo adamkulunga Iye m’maso nampanda Iye kumaso namfunsa, nati; Nenera wakupanda Iwe ndani? 65 Ndipo zambiri zina adam’nenera Iye, namchitira mwano. 66 Ndipo pamene kudacha, bungwe la akulu a anthu lidasonkhana, ndiwo ansembe akulu ndi alembi; ndipo adapita naye ku bwalo lawo, nanena, 67 Ngati uli Khristu, utiwuze. Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndikakuwuzani, simukhulupirira: 68 Ndipo ndikakufunsani kanthu, simundiyankha ndipo simundilola kupita. 69 Koma kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala pa dzanja la manja la mphamvu ya Mulungu. 70 Pamenepo onse adati, Kodi ukutero uli Mwana wa Mulungu? Ndipo Iye adati kwa iwo, Inde munena kuti ndine amene. 71 Ndipo iwo adati, Tifuniranjinso mboni? Pakuti ife tokha tamva m’kamwa mwa Iye mwini.

Luka 23

1 Ndipo khamu lonselo lidanyamuka kupita naye kwa Pilato. 2 Ndipo adayamba kum’nenera Iye, kuti, Tidapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Khristu Mfumu. 3 Ndipo Pilato adamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye adamyankha nati, Mwatero. 4 Ndipo Pilato adati kwa ansembe akulu ndi makamu a anthu, ndiribe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu. 5 Ndipo iwo adawopseza kwambiri nanena kuti, Amasonkhezera anthuwo, naphunzitsa m’Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe. 6 Koma pamene Pilato adamva, adanfunsa ngati munthuyu adali M’galileya. 7 Ndipo m’mene adadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, adamtumiza Iye kwa Herode, amene adali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa. 8 Ndipo Herode, pamene adawona Yesu, adakondwa ndithu; pakuti adayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa adamva zinthu zambiri za Iye; nayembekeza kuwona chozizwitsa china chochitidwa ndi Iye. 9 Ndipo adamfunsa Iye mawu ambiri; koma Iye sadamyankha kanthu. 10 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adayimilira, nam’nenera Iye kolimba. 11 Ndipo Herode ndi asilikari ake ankhondo adampeputsa Iye, nam’nyoza, nambveka Iye chofunda chonyezimila, nambwezera kwa Pilato. 12 Ndipo Herode ndi Pilato adachita chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana. 13 Ndipo Pilato pamene adayitana ansembe akulu, ndi olamulira ndi anthu, kuti asonkhane, 14 Nati kwa iwo, mudadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wopandutsa anthu; ndipo tawonani, Ine ndidamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindidapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mum’nenera Iye: 15 Inde ngakhale Herode yemwe; pakuti iye adambwezera Iye kwa ife; ndipo tawonani, sadachita Iye kanthu koyenera kufa. 16 Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kum’masula Iye. 17 (Popeza kuti amkawamasulira iwo munthu m’modzi pa phwando) 18 Koma iwo onse pamodzi adafuwula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Baraba. 19 Ndiye munthu amene adaponyedwa m’ndende chifukwa cha mpanduko m’mudzi ndi cha kupha munthu. 20 Ndipo Pilato adayankhulanso nawo, nafuna kumasula Yesu. 21 Koma iwo adafuwula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni. 22 Ndipo iye adati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu adachita choyipa chanji? Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kum’masula. 23 Koma adamkakamiza ndi mawu wokweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo ndi mawu awo, mawu akulu a nsembe adalakika. 24 Ndipo Pilato adaweruza kuti chimene adali kufunsa chichitidwe. 25 Ndipo adawamasulira amene adaponyedwa m’ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo, adampempha; koma adapereka Yesu mwa chifuniro chawo. 26 Ndipo popita naye, adagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikuchokera kumidzi, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu. 27 Ndipo udamtsata unyinji wa ukulu a anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye. 28 Koma Yesu adawapotolokera iwo nati, Ana akazi inu aku Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu. 29 Chifukwa tawonani masiku alimkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa. 30 Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, bisani ife. 31 Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma? 32 Ndipo adalinso awiri ena, ndiwo wochita zoyipa, adatengedwa pamodzi ndi Iye kuti aphedwe. 33 Ndipo pamene adafika ku malo dzina lake Kalivari, adampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi wochita zoyipa omwe, m’modzi ku dzanja lamanja ndi wina kulamanzere. 34 Ndipo Yesu adanena, Atate muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo adagawana zobvala zake, poyesa mayere. 35 Ndipo anthu amene adayima adalikupenya. Ndi akulunso adamlalatira Iye, nanena, Adapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake. 36 Ndipo asilikalinso adamnyoza, nadza kwa Iye nampatsa vinyo wosasa. 37 Nanena, ngati Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha. 38 Ndipo lembo lidalembedwa m`malembedwe a Chigriki, Latini ndi Chi Hebri pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA. 39 Ndipo m’modzi wa wochita zoyipa adapachikidwawo adamchitira Iye mwano nanena , Ngati uli Khristu Iwe: Udzipulumutse wekha ndi ife. 40 Koma winayo adayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suwopa Mulungu, powona uli m’kulangika komweku? 41 Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tirikulandira zoyenera zimene tidazichita: koma munthu uyu sadachita kanthu kolakwa. 42 Ndipo iye adati kwa Yesu, Ambuye, mundikumbukire pamene mukudza mu Ufumu wanu. 43 Ndipo Yesu adanena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m’Paradayiso. 44 Ndipo ola lake pamenepo lidali ngati lachisanu ndi chimodzi: ndipo padali m’dima padziko lonse kufikira ola la chisanu ndi chinayi; 45 Ndipo dzuwa linada, ndipo chinsalu chotchinga cha m’kachisi chadang’ambika pakati. 46 Ndipo pamene Yesu adafuwula ndi mawu akulu, adati, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo atanena motero, adapereka mzimu wake. 47 Ndipo pamene Kenturiyo adawona chidachitikacho, adalemekeza Mulungu nanena, Zowonadi munthu uyu adali wolungama. 48 Ndipo makamu onse adasonkhana kudzapenya ichi, pamene adawona zidachitikazo, adapita kwawo ndi kudziguguda pachifuwa. 49 Ndipo womdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, adayima kutali, nawona zinthu izi. 50 Ndipo tawonani, padali munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama: 51 (Amene sadabvomereza kuweruza kwawo ndi ntchito yawo) wa ku Arimateya, muzinda wa Ayuda ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu. 52 Iyeyu adapita kwa Pilato napempha mtembo wake wa Yesu. 53 Ndipo adawutsitsa, naukulunga m’salu ya bafuta, nawuyika m’manda wosemedwa m’mwala, m’menemo sadayika munthu ndi kale lonse. 54 Ndipo tsiku limenero lidali lokonzekera, ndipo sabata lidayandikira. 55 Ndipo akazi, amene adachokera naye ku Galileya, adamtsata m’mbuyo, nawona manda, ndi mayikidwe a mtembo wake. 56 Ndipo adapita kwawo, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa sabata adapumula monga mwa lamulo.

Luka 24

1 Koma tsiku loyamba la sabata, m’banda kucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira zimene adazikonza ndi ena pamodzi nawo. 2 Ndipo adapeza mwala utakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda. 3 Ndipo m’mene adalowa sadapezamo mtembo wa Ambuye Yesu. 4 Ndipo kudali, m’mene adathedwa nzeru nacho, tawonani amuna awiri adayimilira pafupi pawo atabvala zonyezimira: 5 Ndipo m’mene adakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zawo, adati kwa iwo, Mufuniranji wa moyo pakati pa akufa? 6 Iye kulibe kuno, koma wawuka Iye, komatu kumbukirani muja adayankhula nanu, pamene adali m’Galileya, 7 Ndi kunena kuti Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m’manja a anthu wochimwa, ndi kupachikidwa, ndi kuwuka tsiku lachitatu. 8 Ndipo adakumbukira mawu ake. 9 Ndipo anabwerera kuchokera kumanda nafotokonzera zonse khumi ndi m’modziyo, ndi wotsala onse. 10 Koma padali Mariya wa Magadala, ndi Jowana, ndi Mariya amake a Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nawo amene adanena izi kwa atumwiwo. 11 Ndipo mawu awo adawoneka pamaso pawo ngati nkhani chabe, ndipo sadawakhulupirire iwo. 12 Koma Petro adanyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama adawona nsalu zoyera pazokha; ndipo adachoka napita kwawo, nazizwa ndi chija chidachitikacho. 13 Ndipo tawonani, awiri a mwa iwo adali kupita tsiku lomwelo ku mudzi dzina lake Emawu, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi. 14 Ndipo adali kukambirana nkhani za izi zonse zidachitika. 15 Ndipo kudali m’kukambirana kwawo ndi kufunsana, Yesu mwini adayandikira natsagana nawo. 16 Koma maso awo adagwidwa kuti asamzindikire Iye. 17 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mawu awa ndi wotani muli kukambirana wina ndi mzake pamene mukuyenda ndi chisoni? Ndipo adayima ndi nkhope zawo zachisoni. 18 Ndipo m’modzi wa iwo, dzina lake Kleopa, adayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m’Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano? 19 Ndipo Iye adati kwa iwo, zinthu zanji? Ndipo adati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarete, ndiye munthu m’neneri wamphamvu m’ntchito, ndi m’mawu, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse; 20 Ndi kuti ansembe akulu ndi olamulira athu adampereka Iye ku chiweruzo cha imfa ndipo, adampachika Iye. 21 Ndipo tidayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzawombola Israyeli. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi. 22 Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene adalawirira m`mamawa kumanda; 23 Ndipo m’mene sadaupeza mtembo wake, anadza, nanena kuti adawona m’masomphenya angelo, amene adanena kuti ali ndi moyo Iye. 24 Ndipo ena mwa iwo adali nafe adachoka kumka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sadamuwona. 25 Ndipo Iye adati kwa iwo, Opusa inu, ndi wozengereza mtima kusakhulupirira zonse adaziyankhula aneneri! 26 Kodi sadayenera Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake? 27 Ndipo adayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha. 28 Ndipo adayandikira ku mudzi umene adalikupitako; ndipo adachita ngati adafuna kupitirira. 29 Ndipo adamuwumiriza Iye, nati, khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo adalowa kukhala nawo. 30 Ndipo kudali m’mene Iye adakhala nawo pachakudya, adatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo. 31 Ndipo maso awo adatseguka, ndipo adamzindikira Iye; ndipo adawakanganukira iye nawachokera. 32 Ndipo adati wina ndi mzake, mtima wathu sudali wotentha m’kati mwathu nanga m’mene adayankhula nafe m’njira, m’mene adatitsegulira malembo? 33 Ndipo adanyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi m’modziwo, ndi iwo adali nawo atasonkhana pamodzi, 34 Nanena, Ambuye adawuka ndithu, nawonekera kwa Simoni. 35 Ndipo iwo adawafotokozera za m’njira, ndi umo adadziwika nawo m’kunyema kwa mkate. 36 Ndipo pakuyankhula izi iwowa, Yesu mwini yekha adayimirira pakati pawo; nanena nawo, Mtendere ukhale nanu. 37 Koma adawopsedwa ndi kuchita mantha, nayesa kuti adalikuwona mzimu. 38 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mukhala bwanji wobvutika? Ndipo mtsutso wanu uwuka bwanji m’mitima mwanu? 39 Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe m’nofu ndi mafupa monga muwona ndiri nazo Ine. 40 Ndipo m’mene adanena ichi, adawawonetsera iwo manja ake ndi mapazi ake. 41 Koma pokhala iwo chikhalire wosakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno? 42 Ndipo adampatsa Iye chidutswa cha nsomba yokazinga ndi uchi. 43 Ndipo adachitenga, nachidya pamaso pawo. 44 Ndipo Iye adati kwa iwo, Awa ndi mawuwo ndidayankhula ndi inu pamene ndidali nanu kuti ziyenera kukwaniritsidwa za Ine m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi masalmo. 45 Ndipo Iye adawatsegulira chidziwitso chawo, kuti adziwitse malembo, 46 Ndipo Iye adati kwa iwo, kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nawuke kwa akufa tsiku lachitatu: 47 Ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machismo kwa mitundu yonse, kuyambira kuYerusalemu. 48 Inu ndinu mboni zazinthu izi. 49 Ndipo onani, Ine nditumiza kwa inu lonjezano la Atate wanga: koma khalani inu mumzinda wa Yerusalemu muno kufikira mwabvekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba. 50 Ndipo Iye adatuluka nawo kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa. 51 Ndipo kudali, pakuwadalitsa Iye adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba. 52 Ndipo adamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu: 53 Ndipo adakhala chikhalire m’kachisi kuyamika ndi kudalitsa Mulungu. Ameni.

Yohane 1

1 PACHIYAMBI panali Mawu, ndipo Mawu adali ndi Mulungu, ndipo Mawu adali Mulungu. 2 Awa adali pachiyambi ndi Mulungu. 3 Zinthu zonse zidalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikadalengedwa kanthu kena kali konse kolengedwa. 4 Mwa Iye mudali moyo; ndi moyowu udali kuwunika kwa anthu. 5 Ndipo kuwunikaku kudawala mumdima; ndi mdimawu sudakuzindikira. 6 Kudali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane. 7 Iyeyu adadza mwa umboni, kudzachita umboni za kuwunikaku, kuti anthu onse kudzera mwa iye akakhulupirire. 8 Iye sindiye kuwunikaku, koma adatumidwa kukachita umboni wa kuwunikaku. 9 Uku ndiko kuwunika kwenikweni kumene kuwunikira anthu onse akulowa m’dziko lapansi. 10 Adali m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye, koma dziko lapansi silidamzindikira Iye. 11 Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sadamlandira Iye. 12 Koma onse amene adamlandira Iye, kwa iwo adapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; 13 Amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu. 14 Ndipo Mawu adasandulika thupi nakhazikika pakati pa ife, ( ndipo tidawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate), wodzala ndi chisomo ndi chowonadi. 15 Yohane achita umboni za Iye, nafuwula nati, Uyu ndiye amene ndidanena za Iye, wakudzayo pambuyo panga adalipo ndisanabadwe ine; chifukwa adakhala woyamba wa ine. 16 Chifukwa mwa kudzala kwake tilandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo. 17 Chifukwa chilamulo chidapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Khristu. 18 Kulibe munthu adawona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pachifuwa cha Atate, Iyeyu adafotokozera. 19 Ndipo uwu ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda adatuma ansembe ndi alembi aku Yerusalemu ankamfunse iye, Ndiye yani? 20 Ndipo adabvomera, wosakana; nalola kuti, sindine Khristu. 21 Ndipo adamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, sindine. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha Iyayi. 22 Chifukwa chake adati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mawu kwa iwo adatituma ife unena chiyani za iwe wekha? 23 Iye adati, ndine mawu a wofuwula m’chipululu, Lungamitsani njira ya Ambuye, monga adati Yesaya m’neneriyo. 24 Ndipo wotumidwawo adali a kwa Afarisi. 25 Ndipo adamfunsa iye, nati kwa iye, nanga ukubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo? 26 Yohane adawayankha, nati, Ine ndikubatiza ndi madzi, koma pakati pa inu payimilira amene simumdziwa. 27 Ndiye wakudza pambuyo panga, amene adalipo ndisanabadwe ine sindiyenera kumasula lamba wa nsapato yake. 28 Zinthu izi zidachitika mu Betaniya tsidya lija la Yordano, komwe adalikubatiza Yohane. 29 M’mawa mwake Yohane adawona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi! 30 Ndiye amene ndidati za Iye, pambuyo panga palinkudza munthu amene adalipo ndisanabadwe ine; pakuti adali woyamba wa ine. 31 Ndipo sindidamdziwa Iye; koma kuti awonetsedwe kwa Israyeli, chifukwa cha ichi ndidadza ine kudzabatiza ndi madzi. 32 Ndipo Yohane adachita umboni, nati, Ndidawona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhala pa Iye. 33 Ndipo sindidamdziwa Iye, koma Iye Wonditumayo kudzabatiza ndi madzi. Iyeyu adanena ndi ine, Amene udzawona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. 34 Ndipo ine ndidawona, ndikuchita umboni kuti uyu ndiye Mwana wa Mulungu. 35 M’mawa mwake Yohane adayimiliransondi ophunzira ake awiri; 36 Ndipo poyang’ana Yesu alikuyenda, adati, Onani Mwana wankhosa wa Mulungu! 37 Ndipo wophunzira awiri adamva iye alimkuyankhula, natsata Yesu. 38 Koma Yesu adachewuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nawo, Mufuna chiyani? Ndipo adati kwa Iye, Rabi (ndiko kutanthauza, Mphunzitsi), mumakhala kuti? 39 Ndipo adati kwa iwo, Tiyeni, mukawone. Pamenepo anadza nawona kumene amakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; popeza kuti linali Ola la khumi. 40 M’modzi wa awiriwo amene adamva Yohane akuyankhula, namtsata Iye adali Andreya m’bale wake wa Simoni Petro. 41 Iye adayamba kupeza m’bale wake yekha Simoni, nanena naye, tapeza ife Mesiya ndiko kutanthauza Khristu. 42 Anadza naye kwa Yesu. M’mene adamuyang’ana iye, adati, Ndiwe Simoni mwana wa Yona; udzatchedwa Khefa ndiko kutanthauza Thanthwe. 43 M’mawa mwake adafuna kutuluka kupita ku Galileya, nampeza Filipo. Ndipo Yesu adanena naye, Tsata Ine. 44 Tsopano Filipo adali wa ku Betisayida, mzinda wa Andreya ndi Petro. 45 Filipo adapeza Natanayeli, nanena naye, Iye amene Mose adalembera za Iye m’chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe. 46 Natanayeli adati kwa iye, ku Nazarete mkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo adanena naye, Tiye ukawone. 47 Yesu adawona Natanayeli alimkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, mu Israyeli ndithu, mwa iye mulibe chinyengo! 48 Natanayeli adanena naye, Mudandidziwira kuti? Yesu adayankha nati kwa iye, Asadakuyitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mtengo wa mkuyu paja, ndidakuwona iwe. 49 Natanayeli adayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli: 50 Yesu adayankha nati kwa iye, chifukwa ndidati kwa iwe kuti ndidakuwona pansi pa mtengo wa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzawona zinthu zoposa izi. 51 Ndipo adanena naye, Indetu indetu, ndinena ndi inu, Mudzawona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa munthu.

Yohane 2

1 Ndipo tsiku lachitatu padali ukwati mu Kana wa Galileya; ndipo amake a Yesu adali komweko. 2 Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake adayitanidwa ku ukwatiwo. 3 Ndipo pamene adafuna vinyo, amake a Yesu adanena ndi Iye, Alibe vinyo. 4 Yesu adanena naye, mkazi, ndiri ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga sidafike. 5 Amake adanena kwa atumiki, chiri chonse chimene akanena kwa inu, chitani. 6 Ndipo padali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoyikidwako monga mwa mayeretsedwe wa Ayuda, yonse ya myeso iwiri kapena itatu. 7 Yesu adanena nawo, Dzadzani mitsukoyo ndi madzi. Ndipo adayidzadza nde, nde, nde. 8 Ndipo adanena nawo, Tungani tsopano, mupite nawo kwa mkulu wa phwando. Ndipo adapita nawo. 9 Koma pamene mkuluyo adalawa madzi osandulika vinyowo, ndipo sadadziwa kumene adachokera; (koma atumiki amene adatunga madzi adadziwa), mkuluyo adayitana mkwati. 10 Nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuyika vinyo wokoma; ndipo anthu amwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino. 11 Chiyambi ichi cha zozizwitsa zake Yesu adazichita mu Kana wa Galileya, adawonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake adakhulupilira Iye. 12 Zitapita izi adatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka. 13 Ndipo Paskha wa Ayuda adayandikira, ndipo Yesu adakwera kupita ku Yerusalemu. 14 Ndipo adapeza m’kachisi iwo akugulitsa ng’ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama ali kukhala pansi. 15 Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, adatulutsa onse mu kachisimo, ndi nkhosa ndi ng’ombe, nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagudubuza magome; 16 Nati kwa iwo akugulitsa nkhunda; chotsani izi muno, musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda. 17 Ndipo ophunzira ake adakumbukira kuti kudalembedwa, changu cha pa nyumba yanu chandidya ine. 18 Ndipo Ayuda adayankha nati kwa Iye, Mutiwonetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi? 19 Yesu adawayankha, nati, Pasulani kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuwutsa. 20 Pamenepo Ayuda adati, zaka makumi anayi kudza zisanu ndi chimodzi adali mkumanga kachisiyu, kodi inu mudzamuwutsa masiku atatu? 21 Koma Iye adali kunena za kachisi wa thupi lake. 22 Chifukwa chake atawuka kwa akufa, ophunzira ake adakumbukira kuti adanena ichi; ndipo adakhulupirira cholemba, ndi mawu amene Yesu adanena. 23 Tsopano pamene Iye adali mu Yerusalemu pa Paskha paphwando, ambiri adakhulupirira dzina lake, pakuwona zozizwitsa zake zimene adachitazi. 24 Koma Yesu sadzipereka mwini yekha kwa iwo; chifukwa Iye adadziwa anthu onse. 25 Ndipo sadasowa wina achite umboni za munthu; pakuti adadziwa Iye yekha chimene chidali mwa munthu.

Yohane 3

1 Padali munthu wa afarisi dzina lake Nikodemo, wolamulira Ayuda; 2 Iyeyu adadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zozizwitsa izi zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye. 3 Yesu adayankha nati kwa iye, Indetu, indetu ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuwona Ufumu wa Mulungu. 4 Nikodemo adanena kwa Iye, munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso kachiwiri m’mimba ya amake ndi kubadwa? 5 Yesu adayankha, Indetu, indetu ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu. 6 Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu. 7 Usadabwe chifukwa ndidati kwa iwe, uyenera kubadwa mwatsopano. 8 Mphepo iwomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mawu ake, koma sudziwa kumene yichokera, ndi kumene yipita; chotero ali yense wobadwa mwa mzimu. 9 Nikodemo adayankha nati kwa iye, izi zingatheke bwanji? 10 Yesu adayankha nati kwa iye, kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi? 11 Indetu, indetu ndinena kwa iwe, Tiyankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiwona; ndipo umboni wathu simuwulandira. 12 Ngati ndakuwuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuwuzani za kumwamba? 13 Ndipo kulibe munthu adakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala m’Mwambayo. 14 Ndipo monga Mose adakweza njoka m’chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezekedwa; 15 Kuti yense wakukhulupirira mwa Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. 16 Pakuti Mulungu adakonda dziko lapansi, kotero kuti adapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wokhulupirira mwa Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu sadatume Mwana wake ku dziko lapansi; kuti akatsutse dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe kupyolera mwa Iye. 18 Wokhulupirira pa Iye satsutsidwa: wosakhulupirira watsutsidwa ngakhale tsopano, chifukwa sadakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. 19 Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuwunika kudadza ku dziko lapansi, ndipo anthu adakonda mdima koposa kuwunika; pakuti ntchito zawo zidali zoipa. 20 Pakuti yense wochita zoipa adana ndi kuwunika, ndipo sabwera kwa kuwunika, kuti ntchito zake zingatsutsidwe. 21 Koma wochita chowonadi abwera kukuwunika, kuti ntchito zake ziwonekere kuti zidachitidwa mwa Mulungu. 22 Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo adaswela nawo pamodzi, ndipo anabatizidwa. 23 Ndipo Yohane adalinkubatiza mu Ayinoni pafupi pa Salemu, chifukwa padali madzi ambiri pamenepo; ndipo adafika nabatizidwa. 24 Pakuti Yohane adali asadayikidwe m’ndende pamenepo. 25 Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ake a Yohane ndi a Yuda zokhudza mayeretsedwe. 26 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene adali ndi inu tsidya lija la Yordano, amene mudachitira umboni, taonani yemweyu akubatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye. 27 Yohane adayankha nati, Munthu sakhoza kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. 28 Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndidati, Sindine Khristu, koma kuti ndiri wotumidwa m’tsogolo mwake mwa Iye. 29 Iye amene ali naye mkwatibwi ali ndi mkwati, koma mzake wa mkwatiyo, wakuyimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mawu a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe change chimene chikwaniritsidwa. 30 Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe. 31 Iye wochokera kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse. 32 Chimene adachiwona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wake. 33 Iye amene alandira umboni wake adayikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona. 34 Pakuti Iye amene Mulungu adamtuma alankhula mawu a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu kwa Iye ndi muyeso. 35 Atate akonda Mwana,ndipo wapatsa zinthu zonse m’dzanja lake. 36 Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzawona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.

Yohane 4

1 Chifukwa chake pamene Ambuye adadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu adapanga ndipo adabatiza ophunzira ambiri koposa Yohane. 2 (Angakhale Yesu sanabatiza mwiniyo koma ophunzira ake.) 3 Iye adachoka ku Yudeya, ndipo adapitanso ku Galileya. 4 Ndipo adayenera kudutsa pakati pa Samariya. 5 Chifukwa chake adadza ku mudzi wa Samariya, dzina lake Sukari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe. 6 Ndipo pamenepo padali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu popeza adatopa ndi ulendo wake motero adakhala pachitsime: kunali ngati ola lachisanu ndi chimodzi. 7 Kunadza mkazi wa ku Samariya kudzatunga madzi; Yesu adanena naye, Undipatse Ine ndimwe. 8 (Pakuti ophunzira ake adachoka kupita kumzinda kuti akagule chakudya.) 9 Pamenepo mkazi wa ku Samariyayo adanena ndi Iye, Bwanji Inu, muli m’Yuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? Pakuti Ayuda sayenderana nawo a Samariya. 10 Yesu adayankha nati kwa iye. Ukadadziwa mphatso ya Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo. 11 Mkaziyo adanena ndi Iye, Ambuye, mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chiri chakuya; ndipo mwatenga kuti madzi a moyo? 12 Kodi muli wamkulu kuposa atate wathu Yakobo amene adatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake ndi ng’ombe zake? 13 Yesu adayankha nati kwa iye, yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu. 14 Koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira m’moyo wosatha. 15 Mkaziyo adanena kwa Iye, Ambuye , ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisabwere kuno kudzatunga. 16 Yesu adanena kwa iye, pita, kamuyitane mwamuna wako, nubwere kuno. 17 Mkaziyo adayankha nati kwa Iye, ndiribe mwamuna. Yesu adanena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe; 18 Pakuti wakhala nawo amuna asanu; ndipo iye amene ukukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zowona. 19 Mkazi adanena ndi Iye, Ambuye ndazindikira kuti ndinu Mneneri. 20 Makolo athu ankalambira m’phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu. 21 Yesu adanena naye mkazi, khulupirira Ine, ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri ili, kapena mu Yerusalemu. 22 Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso cha kwa Ayuda. 23 Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo imene olambira wowona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. 24 Mulungu ndi Mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi. 25 Mkazi adanena ndi Iye, ndidziwa kuti Mesiya abwera wotchedwa Khristu: akadzabwera Iyeyu, adzatiwuza zinthu zonse. 26 Yesu adanena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene. 27 Ndipo pamenepo adabwera ophunzira ake nazizwa kuti adalimkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina adati, Mukufuna chiyani? Kapena, mukulankhula naye chiyani? 28 Pamenepo mkazi adasiya mtsuko wake wa madzi napita kumzinda, nanena ndi anthu, 29 Idzani mudzawone munthu amene adandiwuza zinthu ziri zonse ndidazichita: kodi uyu sindiye Khristu? 30 Ndipo iwo adatuluka mumzinda nabwera kwa Iye. 31 Pa mphindikati iyi ophunzira ake adampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani. 32 Koma Iye adati kwa iwo, Ine ndiri nacho chakudya chimene inu simuchidziwa. 33 Chifukwa chake ophunzira adanena wina ndi mzake, kodi pali wina adamtengera Iye kanthu kakudya? 34 Yesu adanena nawo, chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene adandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake. 35 Kodi simunena inu, kuti, yatsala miyezi inayi, ndipo kudza kukolola? Onani ndinena kwa inu, kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kuti mukololedwe. 36 Wakukolola alandira kulipira, nasonkhanitsira zipatso ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi wokololayo. 37 Pakuti m’menemo chonenacho chiri chowona, wofesa ndi wina, womweta ndi winanso 38 Ine ndidatuma inu kukamweta chimene simudagwirirapo ntchito: ena adagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yawo kukakolola. 39 Ndipo mumzinda muja Asamariya ambiri adamkhulupirira Iye, chifukwa cha mawu a mkazi wochita umboniyo kuti, adandiwuza ine zinthu ziri zonse ndidazichita. 40 Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, adamfunsa akhale nawo; ndipo adakhala komweko masiku awiri. 41 Ndipo ambiri oposa adakhulupirira chifukwa cha mawu ake; 42 Ndipo adanena kwa mkazi, kuti, tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kuyankhula kwako; pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti uyu ndithu ndi Khristu, Mpulumutsi wadziko lapansi. 43 Tsopano atapita masiku awiriwo adachoka komweko kupita ku Galileya. 44 Pakuti Yesu mwini adachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m’dziko la kwawo. 45 Ndipo pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira Iye, atakawona zonse zimene adazichita mu Yerusalemu pamphwando; pakuti iwonso adapita kuphwando. 46 Choncho Yesu adabweranso ku Kana wa ku Galileya, kumene adasandutsa madzi vinyo. Ndipo kudali nduna yina ya mfumu mwana wake adadwala mu Kapernao. 47 Iyeyu pamene adamva kuti Yesu wachoka ku Yudeya nafika ku Galileya, adapita kwa Iye nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti adali pafupi imfa. 48 Pamenepo Yesu adati kwa iye, ngati simuwona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira. 49 Nduna ya mfumuyo idanena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga. 50 Yesu adanena naye, Pita, mwana wako ali ndi moyo. Munthuyo adakhulupirira mawu amene Yesu adanena naye, napita. 51 Ndipo m’mene tsopano iye adalikutsika, atumiki ake adakomana naye, nanena, kuti mwana wanu ali ndi moyo. 52 Ndipo adawafunsa ola lake limene adayamba kuchilalo, pamenepo adati kwa iye, kuti, Dzulo, ola la chisanu ndi chiwiri malungo adamsiya. 53 Choncho atateyo adadziwa kuti ndi ola lomwelo limene Yesu adati kwa iye, mwana wako ali ndi moyo; ndipo adakhulupirira iye yekha ndi a pabanja lake onse. 54 Ichi ndi chozizwa chachiwiri Yesu adachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa mu Galileya.

Yohane 5

1 Zitapita izi padali phwando la Ayuda; ndipo Yesu adakwera kupita ku Yerusalemu. 2 Koma padali thamanda mu Yerusalemu pa chipata cha nkhosa, lotchedwa mu Chihebri lilime Betsaida, liri ndi makumbi asanu. 3 M’menemo mumagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, wosayenda, opuwala, kudikira madzi kuti avundulidwe. 4 Ndipo m’ngelo amatsika nyengo yina mu thamandalo, nabvundula madzi; aliyense amene amayambirira kulowamo m’madzi atabvundulidwa amakhala wokonzedwa kumatenda ali wonse adali nawo. 5 Ndipo padali munthu wina apo, wodwala kwa zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. 6 Pamene Yesu adamuwona iye atagona pamenepo, adadziwa kuti adatero kwa nthawi yayitali, adanena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi? 7 Wodwalayo adayankha Iye, Ambuye, ndiribe munthu wondibviyika ine muthamanda, pakuti panthawi imene madzi abvundulidwa; wina amakhala atatsika kale, ine ndisadatsike. 8 Yesu adanena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende. 9 Ndipo pomwepo munthuyo adachira, nayalula mphasa yake, nayenda; ndipo tsiku lomwelo lidali la sabata. 10 Chifukwa chake Ayuda adanena kwa wochiritsidwayo, Ndi sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako. 11 Koma iyeyu adayankha iwo, Iye amene adandichiritsa, yemweyu adati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende. 12 Ndipo iwo adamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe. Yalula mphasa yako nuyende. 13 Koma wochiritsidwayo sanadziwa ngati ndani, pakuti Yesu adachoka kachetechete, popeza padali khamu pa malo paja. 14 Zitapita izi Yesu adampeza iye m’kachisi, nati kwa iye, Tawona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa. 15 Munthuyo adachoka, nawuza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa. 16 Ndipo chifukwa cha ichi, Ayuda adalondalonda Yesu, nafuna kumupha chifukwa adachita zinthu izi padzuwa la sabata. 17 Koma Yesu adayankha iwo, atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito. 18 Chifukwa cha ichi Ayuda adawonjeza kufuna kumupha, sichifukwa cha kuswa tsiku la sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu. 19 Pamenepo Yesu adayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza mwana kuchita kanthu pa yekha koma chimene awona Atate achichita ndicho pakuti zinthu zimene Iye azichita zomwezonso mwananso azichita momwemo. 20 Pakuti Atate akonda namuwonetsa Iye zinthu zimene zonse azichita yekha; ndipo adzamuwonetsa Iye ntchito za zikulu zoposa izi, kuti mukazizwe. 21 Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna. 22 Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma adapereka kuweruza konse kwa Mwana. 23 Kuti anthu onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene adamtuma Iye. 24 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mawu anga, ndi kukhulupirira Iye amene adandituma Ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo iye satsutsidwa, koma wachokera ku imfa, kulowa m’moyo. 25 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo. 26 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso adapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha. 27 Ndipo adampatsa Iye ulamuliro wakuzenga milandunso, pakuti Iye ali Mwana wa munthu. 28 Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake. 29 Ndipo adzatuluka; amene adachita zabwino, kukuwuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuwuka kwa chiwonongeko. 30 Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali wolungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Atate wondituma Ine. 31 Ngati ndichita umboni mwa Ine ndekha, umboni wanga suli wowona. 32 Pali wina wochita umboni wa Ine; ndipo ndidziwa kuti umboni umene Iye andichitira Ine uli wowona. 33 Inu mudatuma kwa Yohane, ndipo iye adachitira umboni chowonadi. 34 Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu; koma ndinena zinthu izi, kuti inu mukapulumutsidwe. 35 Iyeyo adali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu mudafuna kukondwera m’kuwunika kwake kanthawi. 36 Koma Ine ndiri nawo umboni wa ukulu woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate adandipatsa Ine ndizitsirize ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate adandituma Ine. 37 Ndipo Atate mwini yekha wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simudamva mawu ake nthawi iri yonse kapena kuwona mawonekedwe ake. 38 Ndipo mulibe mawu ake wokhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu adamtuma, inu simumkhulupirira. 39 Musanthula m’malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo; 40 Ndipo simufuna kubwera kwa Ine, kuti mukhale ndi moyo. 41 Ine sindilandira ulemu kwa anthu. 42 Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha. 43 Ndabwera Ine m’dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; koma akabwera wina m’dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamulandira. 44 Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mzake ndipo ulemu wochokera kwa Mulungu yekha simuwufuna? 45 Musaganize kuti Ine ndidzakutsutsani inu kwa Atate; pali m`modzi wakukutsutsani, ndiye Mose amene inu mumkhulupirira 46 Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu adalembera za Ine. 47 Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mawu anga?

Yohane 6

1 Zitapita zinthu izi adachoka Yesu kupita kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiya. 2 Ndipo khamu lalikulu lidamtsata Iye, chifukwa adawona zozizwitsa zimene adachita pa wodwala. 3 Koma Yesu adakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi wophunzira ake. 4 Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, adayandikira. 5 Pamenepo Yesu pokweza maso ake ndi kuwona kuti khamu lalikulu lirimkudza kwa Iye, adanena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa? 6 Koma adanena ichi kuti amuyese; pakuti adadziwa yekha chimene adzachita. 7 Filipo adayankha Iye, mikate ya mazana awiri siyikwanira iwo, kuti yense atenge pang’ono. 8 M’modzi wa wophunzira ake Andreya, m’bale wake wa Simoni Petro, adanena ndi Iye. 9 Pali m’nyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabalere, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere? 10 Ndipo Yesu adati, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo padali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo adakhala pansi, chiwerengero chawo chinali zikwi zisanu. 11 Pomwepo Yesu adatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, adagawira kwa ophunzira ake: ndipo ophunzira kwa iwo akukhala pansi momwemonso ndi tinsomba monga iwo adafuna. 12 Ndipo pamene adakhuta, Iye adanena kwa wophunzira ake, sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu. 13 Pomwepo adasonkhanitsa, nadzadza mitanga khumi ndi iwiri ndi makombo a mikate isanuyo yabalere, imene idatsalira amadyawo. 14 Chifukwa chake anthu, powona chozizwa chimene Yesu adachita, adanena, ichi ndiye chowonadi kuti m’neneri ndithu wadza ku m’dziko lapansi. 15 Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kubwera kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, adachokanso kupita ku phiri pa yekha. 16 Koma pofika madzulo, wophunzira ake adatsikira kunyanja; 17 Ndipo adalowa muchombo, nawoloka nyanja kupita ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu adali asanadze kwa iwo. 18 Ndipo nyanja idawuka chifukwa cha mphepo yayikulu idawomba. 19 Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, adawona Yesu akuyenda pamwamba panyanja, ndi kuyandikira chombo; ndipo adachita mantha. 20 Koma Iye adati kwa iwo, Ndine; musawope. 21 Pamenepo adalola kumlandira m’chombo; ndipo pomwepo chombo chidafika kumtunda kumene adalikunkako. 22 M’mawa mwake pamene anthu adayima tsidya lija la nyanja adawona kuti padalibe chombo china koma chimodzi chimne ophunzira ake adalowa ndi kuti Yesu sadalowa pamodzi ndi wophunzira m`chombomo, koma wophunzira ake adachoka pa wokha; 23 ( Koma zombo zina zidachoka ku Tiberiya, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate pamene Yesu adayamika;) 24 Chifukwa chake pamene anthu adawona kuti padalibe Yesu, ndi wophunzira akenso padalibe, iwo wokha adalowa m`zombozo nadza ku Kapernao, alikumfuna Yesu. 25 Ndipo pamene adampeza Iye tsidya lina la nyanja, adati kwa Iye, Rabi, munadza kuno liti? 26 Yesu adayankha iwo nati, indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa mudawona zozizwitsa, koma chifukwa mudadya mkate, ndipo mudakhuta. 27 Gwirani ntchito sichifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chatsalira ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro. 28 Pamenepo adati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu? 29 Yesu adayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo adamtuma. 30 Chifukwa chake adati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tiwone ndi kukhulupirira Inu? 31 Atate athu adadya mana m’chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera kumwamba adawapatsa iwo kudya. 32 Chifukwa chake Yesu adati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, si Mose amene adakupatsani inu mkate wakumwamba; koma Atate wanga anakupatsani inu mkate wowona wa Kumwamba. 33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye Iye wotsika pansi kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo ku dziko lapansi. 34 Pamenepo adati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umenewu nthawi zonse. 35 Yesu adati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala ndi iye wokhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse. 36 Koma ndidati kwa inu, Kuti ngakhale mwandiwona, simukhulupirira. 37 Onse amene andipatsa Ine Atate adzadza kwa Ine; ndipo iye wakudza kwa Ine sindidzamtaya konse kunja. 38 Pakuti ndidatsika Kumwamba, sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene adandituma Ine. 39 Ndipo ichi ndicho chifuniro cha Atate amene adandituma Ine, kuti za ichi chonse Iye adandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma kuti ndichiwukitse ichi tsiku lomaliza. 40 Ichi ndicho chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, kuti yense woyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira pa Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza. 41 Ndipo Ayuda adang’ung’udza za Iye, chifukwa adati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba. 42 Ndipo iwo adanena, Si Yesu uyu mwana wa Yosefe, atate wake ndi amayi wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndidatsika Kumwamba? 43 Yesu adayankha nati kwa iwo, Musang’ung’udze mwa inu nokha. 44 Palibe munthu angathe kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza. 45 Zalembedwa mwa aneneri, ndipo iwo onse adzakhala wophunzitsidwa za Mulungu. Chifukwa chake munthu ali yense amene adamva ndipo waphunzira za Atate adza kwa Ine. 46 Sikuti munthu wina wawona Atate, koma kupatula Iye amene ali wchokera kwa Mulungu, ameneyo wawona Atate. 47 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira pa Ine ali nawo moyo wosatha. 48 Ine ndine mkate wa moyo. 49 Makolo anu adadya mana m’chipululu, ndipo adamwalira. 50 Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. 51 Mkate wamoyo wotsika Kumwamba, Ndine amene. Ngati munthu aliyense akadyako mkate umenewu, adzakhala ndi moyo kosatha, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine. Ndiwo thupi langa limene ndidzapereka, likhale moyo wa dziko lapansi. 52 Pamenepo Ayuda adatetana wina ndi mzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake? 53 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. 54 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza. 55 Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu. 56 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye. 57 Monga Atate wamoyo adandituma Ine, ndipo Inenso ndiri ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58 Uwu ndiwo mkate wotsika Kumwamba: si monga makolo anu, adadya mana namwalira; iye wakudya mkate umenewu adzakhala ndi moyo nthawi zonse. 59 Zinthu izi adanena musunagoge, Iye pophunzitsa mu Kapernao. 60 Pamenepo ambiri akuphunzira ake pakumva izi, adati, Mawu awa ndi wosautsa; akhoza kumva awa ndani? 61 Koma Yesu podziwa mwa Iye yekha kuti wophunzira ake alikung’ung’udza chifukwa cha ichi, adati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho? 62 Nanga bwanji mukadzawona Mwana wa Munthu alikukwera kumene adali kale lomwe? 63 Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mawu amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo. 64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupilira. Pakuti Yesu adadziwiratu poyamba amene ali wosakhulupirira, ndi amene adzampereka Iye. 65 Ndipo adanena chifukwa cha ichi ndidati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate wanga. 66 Pa ichi ambiri wophunzira ake adabwerera m’mbuyo, ndipo sadayendayendanso ndi Iye. 67 Chifukwa chake Yesu adati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka? 68 Simoni Petro adamuyankha Iye, Ambuye, tidzapita kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. 69 Ndipo ife tikukhulupirira, ndipo tatsimikiza kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wa moyo. 70 Yesu adawayankha iwo, Kodi sindidakusankhani khumi ndi awiri, ndipo wa inu m’modzi ali m`dierekezi? 71 Koma adanena za Yudasi Isikariyote, mwana wa Simoni, pakuti iye ndiye amene adzampereka Iye, wokhala m’modzi wakhumi ndi awiri.

Yohane 7

1 Ndipo zitapita izi Yesu, adayendayenda mu Galileya; pakuti sadafuna kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda adafuna kumupha Iye. 2 Koma phwando la Ayuda la misasa, lidayandikira. 3 Choncho abale ake adati kwa Iye, chokani pano, mupite ku Yudeya, kuti wophunzira anunso akapenye ntchito zanu zimene mukuchita. 4 Pakuti palibe munthu amachita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati mukuchita izi, dziwonetsereni eni nokha ku dziko lapansi. 5 Pakuti angakhale abale ake sadakhulupirira Iye. 6 Chifukwa chake Yesu adanena nawo, nthawi yanga siyidafike; koma nthawi yanu yakonzeka kale. 7 Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake ziri zoyipa. 8 Kwerani inu kupita kuphwando; sindikwera Ine ku phwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siyidakwanire. 9 Ndipo pamene adanena nawo mawu awa adakhalabe mu Galileya. 10 Koma pamene abale ake adakwera kupita kuphwando, pomwepo Iyenso adakwera, si mowonekera koma monga mobisika. 11 Pomwepo Ayuda adalikumfuna Iye paphwando, nanena, Ali kuti uja? 12 Ndipo kudali kung’ung’udza kwambiri za Iye pakati pa anthu; popeza kuti ena adanena, kuti Ali wabwino; koma ena adanena, Iyayi, koma asocheretsa anthu. 13 Ngakhale adatero padalibe munthu adalankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuwopa Ayuda. 14 Koma pamene padafika pakati pa phwando Yesu adakwera nalowa m’kachisi, naphunzitsa. 15 Chifukwa chake Ayuda adazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, koma wosaphunzira. 16 Yesu adayankha iwo, nati, chiphunzitso changa sichiri changa, koma cha Iye amene adandituma Ine. 17 Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa ine ndekha. 18 Iye wolankhula zochokera kwa Iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wofuna ulemu wa Iye amene adamtuma, yemweyu ali wowona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. 19 Si Mose kodi adakupatsani chilamulo, ndipo palibe m’modzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha Ine chifukwa chiyani? 20 Anthu adayankha nati, Muli ndi chiwanda: ndani afuna kukuphani Inu? 21 Yesu adayankha nati kwa iwo, Ndachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa nonse. 22 Chifukwa cha ichi Mose adakupatsani inu mdulidwe (sikuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo) ndipo mudula munthu tsiku la sabata. 23 Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku lasabata? 24 Musaweruze monga mwamawonekedwe, koma weruzani chiweruzo cholungama. 25 Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu adanena, kodi suyu amene afuna kumupha? 26 Ndipo tawona amayankhula molimba mtima, ndipo sadanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi aulamuliro akudziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo? 27 Koma ameneyo tidziwa kumene akuchokera koma pamene Khristu adzabwera palibe munthu: m’modzi adzadziwa kumene adzachoka. 28 Pamenepo Yesu adafuwula m’kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, mundidziwa Ine, ndiponso mukudziwa Ine kumene ndichokera; ndipo sindidadza kwa Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali wowona. 29 Ine ndimdziwa Iye; chifukwa ndiri wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu. 30 Pamenepo adafuna kumgwira Iye; koma padalibe wina adamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake idali isadafike. 31 Koma ambiri anthu adakhulupirira Iye; ndipo adanena, pamene Khristu akabwera, kodi adzachita zozizwa zambiri zoposa zimene munthu uyu akuzichita? 32 Afarisi adamva anthu ali kung’ung’udza za Iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi adatuma asilikari kuti akamgwire Iye. 33 Pamenepo Yesu adati kwa iwo, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine. 34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo komwe ndiri Ine, inu simungathe kudzako. 35 Chifukwa chake Ayuda adati mwa iwo wokha, Adzapita kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzapita kwa Amitundu wobalalikawo, ndi kuphunzitsa Amitunduwo? 36 Mawu awa amene adanena ndi wotani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine; ndipo komwe ndiri Ine, inu simungathe kudzako? 37 Koma tsiku lomaliza, lalikululo laphwando, Yesu adayimilira nafuwula ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, abwere kwa Ine, namwe. 38 Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chidati, mitsinje ya madzi a moyo idzayenda, kutuluka m’kati mwake. 39 (Koma ichi adati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye adati adzalandire; pakuti Mzimu padalibe pamenepo, chifukwa Yesu sadalemekezedwa panthawi pomwepo). 40 Pamenepo ambiri mwa anthu pakumva mawu awa, adanena, M’neneriyo ndi uyu ndithu. 41 Ena adanena, Uyu ndi Khristu. Koma ena adanena, kodi Khristu abwera kutuluka mu Galileya? 42 Kodi sichidati chilembo kuti Khristu adzabwera kutuluka mwa mbewu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kudali Davide? 43 Tsono kudakhala kusiyana pakati pawo chifukwa cha Iye. 44 Koma ena mwa iwo adafuna kumgwira Iye; koma padalibe munthu adamgwira kumanja. 45 Pamenepo asilikariwo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa adati kwa iwo, simudamtenga Iye bwanji? 46 Asilikariwo adayankha, chiyambire padalibe munthu adayankhula chotero. 47 Pamenepo Afarisi adayankha iwo, kodi mwanyengedwanso inunso? 48 Kodi wina wa olamulira kapena wa Afarisi adakhulupirira Iye.? 49 Koma anthu awa osadziwa chilamulo, akhala wotembereredwa. 50 Nikodemo adanena kwa iwo, ( iye uja adadza kwa Yesu ndi usiku wokhala m’modzi wa iwo,) 51 Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene akuchita? 52 Adayankha nati kwa iye, kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuwone kuti m’Galileya sadawuka m’neneri. 53 Ndipo munthu aliyense adapita ku nyumba yake.

Yohane 8

1 Yesu adapita ku phiri la Azitona. 2 Ndipo m’mawa adabweranso kukachisi, ndipo anthu adadza kwa Iye; ndipo m’mene anthu onse adakhala pansi adawaphunzitsa. 3 Ndipo alembi ndi Afarisi adabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m’chigololo, ndipo pamene adamuyimika iye pakati, 4 Iwo adanena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa ali mkati mochita chigololo. 5 Koma m’chilamulo Mose adatilamulira, tiwaponye miyala otere. Nanga Inu munena chiyani za iye? 6 Koma ichi adanena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomtsutsa Iye. Koma Yesu, m’mene adawerama pansi adalemba pansi ndi chala chake ngati kuti Iye sakuwamva iwo. 7 Koma pamene adakhalakhala alikufunsabe Iye, adaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala. 8 Ndipo m’mene adaweramanso adalemba ndi chala chake pansi. 9 Ndipo iwo amene adamva ichi, adatsutsika m’chikumbumtima chawo, natulukamo m’modzi m’modzi, kuyambira akulu, kufikira wotsiriza; ndipo Yesu adatsala yekha ndi mkazi alichiyimile pakati. 10 Koma pamene Yesu adaweramuka, adati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti aja adakutsutsa? Palibe munthu adakutsutsa kodi? 11 Iye adati, Palibe Ambuye. Ndipo Yesu adati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usakachimwenso. 12 Pamenepo Yesu adalankhulanso nawo, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuwunika kwa moyo. 13 Chifukwa chake Afarisi adati kwa Iye, muchita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli wowona. 14 Yesu adayankha nati kwa iwo, Ngakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli wowona; chifukwa ndidziwa kumene ndidachokera ndi kumene ndimukako koma inu simudziwa kumene ndichokera ndi kumene ndipita. 15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu. 16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruzo changa chiri chowona; pakuti sindiri ndekha, koma Ine ndi Atate amene adandituma Ine. 17 Zidalembedwanso m’chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli wowona. 18 Ine ndine wochita umboni wa ine ndekha, ndipo Atate amene adandituma Ine achita umboni wa Ine. 19 Chifukwa chake adanena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu adayankha, simudziwa, kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga. 20 Mawu awa adalankhula Yesu ali m’nyumba ya chuma cha Mulungu pophunzitsa m’kachisi; ndipo padalibe munthu adagwira Iye, pakuti nthawi yake siyidafike. 21 Pamenepo adatinso kwa iwo; ndipita Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo mutchimo lanu mudzafa; kumene ndipita Ine, simungathe kufikako. 22 Ndipo Ayuda adanena, kodi adzadzipha yekha? Pakuti akunena, kumene ndipita Ine, simungathe kufikako. 23 Ndipo Iye adanena nawo, Inu ndinu wochokera pansi; ine ndine wochokera kumwamba; inu ndinu adziko lino lapansi; sindiri Ine wadziko lino lapansi. 24 Chifukwa chake ndidati kwa inu, kuti mudzafa m’machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m’machimo anu. 25 Pamenepo adanena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu adati kwa iwo, chimene ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pa chiyambi. 26 Ndiri nazo zambiri zolankhula ndi zoweruza za inu; koma wondituma Ine ali wowona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi. 27 Iwo sadazindikira kuti adalikunena nawo za Atate. 28 Chifukwa chake Yesu adati, pamene mudzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga adandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi. 29 Ndipo Iye wondituma Ine ali ndi Ine; Atate sadandisiye Ine ndekha; chifukwa ndichita Ine zinthu zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse. 30 Pamene Iye adalankhula mawu awa, ambiri adakhulupirira pa Iye. 31 Pamenepo Yesu adanena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli wophunzira anga ndithu; 32 Ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani. 33 Adamuyankha Iye, tiri mbewu ya Abrahamu, ndipo sitidakhala akapolo a munthu nthawi ili yonse; munena bwanji, Mudzayesedwa a ufulu? 34 Yesu adayankha iwo, nati, indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wochita tchimo ali kapolo wa tchimolo. 35 Koma kapolo sakhala m’nyumba nthawi yonse koma; mwana ndiye amakhala nthawi yonse. 36 Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu. 37 Ndikudziwa kuti muli mbewu ya Abrahamu; koma mukufuna kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38 Ine ndilankhula zimene ndidawona kwa Atate, ndipo inunso muchita chimene mudawona kwa Atate wanu. 39 Adamuyankha nati kwa Iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu adanena nawo, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu. 40 Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndidalankhula ndi inu chowonadi, chimene ndidamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sadachita. 41 Inu muchita ntchito za atate wanu. Adati kwa Iye, sitinabadwe ife m’chiwerewere; tiri naye Atate m’modzi ndiye Mulungu. 42 Yesu adati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukakonda Ine; pakuti Ine ndidatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindidadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu adandituma Ine. 43 Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa chiyani? Chifukwa simungathe kumva mawu anga. 44 Inu muli wochokera mwa atate wanu m’dierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu adali wakupha kuyambira pachiyambi, ndipo sadayima m’chowonadi, pakuti mwa iye mulibe chowonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake, pakuti ali wabodza, ndi atate wake wabodza. 45 Ndipo chifukwa ndinena ndi inu chowonadi, simukhulupirira Ine. 46 Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ndipo ngati Ine ndinena chowonadi, simukhulupirira Ine chifukwa chiyani? 47 Iye wochokera kwa Mulungu akumva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu. 48 Ayuda adamuyankha nati kwa Iye, kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda? 49 Yesu adayankha, Ndiribe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa. 50 Koma Ine sinditsata ulemerero wanga; ndipo alipo m` modzi woutsata ndi woweruza. 51 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, munthu akasunga mawu anga, sadzawona imfa nthawi yonse. 52 Ayuda adati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu adamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, munthu akasunga mawu anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse. 53 Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene adamwalira? Ndi aneneri adamwalira: mudziyesera nokha muli yani? 54 Yesu adayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu; 55 Ndipo inu simudamdziwa Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye; ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mawu ake. 56 Atate wanu Abrahamu adakondwera kuwona tsiku langa; ndipo adawona, nasangalala. 57 Ayuda pamenepo adati kwa Iye, Inu simudafikire zaka makumi asanu, ndipo inu mudawona Abrahamu kodi? 58 Yesu adati kwa iwo, indetu, indetu, ndinena kwa inu, asadakhale Abrahamu, Ine ndilipo. 59 Pamenepo adatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka m’kachisi, nawadutsa iwo pakati pawo, napita.

Yohane 9

1 Ndipo pamene Yesu amadutsa, adawona munthu wosawona chibadwire. 2 Ndipo wophunizra ake adamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, adachimwa ndani mwini wake, makolo ake, kuti adabadwa wosawona? 3 Yesu adayankha, Sadachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikawonetsedwe mwa iye. 4 Ndiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, akadali masana; ukadza usiku palibe munthu angathe kugwira nchito. 5 Pakukhala Ine m’dziko lapansi, ndiri kuwunika kwa dziko lapansi. 6 Pamene adanena izi, adalabvulira pansi, nakanda thope ndi malobvuwo, napaka thopelo m’maso mwa munthu wosawonayo. 7 Ndipo adati kwa iye, Pita, ukasambe muthamanda la Siloamu (ndilo losandulika, wotumidwa) pamenepo adapita nakasamba, nabwera akuyang’ana. 8 Ndipo amzake ndi iwo adamuwona kale, kuti adali wopemphapempha, adanena, Kodi si uyu uja adakhala ndi wosaona? 9 Ena adanena, kuti, Ndiyeyu; ena adanena, Iyayi, koma afanana naye. Iyeyu adati, Ndine amene. 10 Pamenepo adanena ndi iye, Nanga maso ako adatseguka bwanji? 11 Iyeyu adayankha, nati, Munthu wotchedwa Yesu adakanda thope, napaka m’maso mwanga, nati kwa ine, pita ku thamanda la Silowamu ukasambe, ndipo ndidapita ndikukasamba, ndipo ndinapenya. 12 Ndipo adati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Adati, sindikudziwa ine. 13 Adapita naye kwa Afarisi iye amene adali wosawona kale. 14 Ndipo lidali tsiku la sabata limene Yesu adakanda thope, namtsegulira iye maso ake. 15 Ndipo Afarisi adamfunsanso, m’mene adapenyera. Ndipo adati kwa iwo, adapaka thope m’maso mwanga, ndidasamba, ndipo ndidapenya. 16 Choncho ena mwa Afarisi adanena, Munthu uyu sadachokere kwa Mulungu, chifukwa sasunga tsiku la sabata. Koma ena adanena, Ngati munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zozizwitsa zotere? Ndipo padali kugawanikana pakati pa iwo. 17 Ndipo adanenanso kwa wosawonayo, Iwe unenanji za Iye? Pakuti adakutsegulira maso ako. Iye adati, Ali m`neneri. 18 Koma Ayuda sadakhulupirira za iye kuti adali wosawona, napenya, kufikira pamene adayitana atate wake ndi amake a iye amene adapenya. 19 Ndipo adawafunsa iwo, nanena kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosawona? Ndipo apenya bwanji tsopano? 20 Makolo ake adayankha nati, Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosawona. 21 Koma sitidziwa umo wapenyera tsopano; kapena sitimdziwa amene adamtsegula maso ake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha. 22 Mawu awa adanena makolo ake chifukwa adawopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzabvomereza Iye kuti ndiye Khristu, adzachotsedwa m’sunagoge. 23 Chifukwa cha ichi makolo ake adati, mufunseni; ali wamsinkhu. 24 Pamenepo adamuyitananso munthu adali wosawonayo, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa. 25 Iye adayankha nati, kaya iye ndi wochimwa kapena ayi, sindikudziwa: chinthu chimodzi ndichidziwa, ndi ichi kuti ndidali wosawona, tsopano ndipenya. 26 Pamemnepo adati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Adatsegula motani iye maso ako? 27 Iye adayankha iwo, Ndidakuwuzani kale, ndipo simudamva; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala wophunzira ake? 28 Ndipo adamulalatira iye, nati, Iwe ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife wophunzira a Mose. 29 Ife tikudziwa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose; koma za ameneyo, sitikudziwa kumene akuchokera. 30 Munthuyo adayankha nati kwa iwo, chifukwa chiyani mwa Iye muli chozizwitsa ndi kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo kuti Iye adanditsegulira maso anga. 31 Tsopano tidziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake amvera ameneyo. 32 Kuyambira pachiyambi cha dziko lapansi sikudamveka kuti munthu wina adatsegulira maso munthu wosawona chibadwire. 33 Ngati munthuyu sadachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu. 34 Adayankha nati kwa iye, Wobadwa iwe konse m`zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo adamponya kunja. 35 Yesu atamva kuti adamponya kunja; ndipo atampeza iye, adati kwa iye, Kodi ukhulupirira Mwana wa Mulungu? 36 Iyeyu adayankha nati, Ndani Iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire Iye? 37 Yesu adati kwa iye, Wamuwona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iye amene. 38 Ndipo iye adati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo adampembedza Iye. 39 Ndipo Yesu adati, Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo openya akhale osawona. 40 Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye atamva izi, adati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osawona? 41 Yesu adati kwa iwo, Mukadakhala osawona simukadakhala ndi tchimo; koma tsopano munena, kuti, tikupenya: choncho tchimo lanu likhala chikhalire.

Yohane 10

1 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowera pakhomo mkhola la nkhosa koma akwerera pena iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda. 2 Koma iye wolowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa. 3 Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndipo nkhosa zimva mawu ake; ndipo ayitana nkhosa za iye yekha mayina awo, nazitsogolera kunja. 4 Pamene atulutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mawu ake. 5 Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziwa mawu a alendo. 6 Fanizo ili Yesu adanena kwa iwo; koma sadazindikira zinthu zimene Yesu adalikuyankhula nawo. 7 Pamenepo Yesu adanenanso nawo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ine ndine khomo lankhosa. 8 Onse amene adadza m’tsogolo mwa ine ali akuba, ndi wolanda; ndipo nkhosa sizidamva iwo. 9 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza msipu. 10 Siyikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuwononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka. 11 Ine ndine mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa. 12 Koma iye amene ali mbusa wolipidwa, nkhosa sizikhala zake za iye, akawona m’mbulu ulimkudza, amasiya nkhosazo, nathawa; ndipo m’mbulu uzikwatula, nuzibalalitsa; 13 Wolipidwa amathawa, chifukwa iye ndi wolipidwa, ndipo sasamalira nkhosa. 14 Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira nkhosa zanga, ndi zanga zindizindikira Ine. 15 Monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16 Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala khola limodzi, ndi mbusa m’modzi. 17 Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikawutengenso. 18 Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiwutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuwutaya ndiponso ndiri nayo mphamvu yakuwutenganso; lamulo ili ndidalandira kwa Atate wanga. 19 Padakhalanso kugawanika pakati pa Ayuda chifukwa cha mawu awa. 20 Ndipo ambiri mwa iwo adanena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumvera Iye bwanji? 21 Ena adanena, Mawu awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosawona? 22 Ndipo kudali ku Yerusalemu, paphwando la kudzipereka; idali nyengo yozizira. 23 Ndpo Yesu adalimkuyendayenda m’kachisi m’khumbi la Solomo. 24 Pamenepo Ayuda anadza namzungulira Iye, nanena ndi Iye, kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiwuzeni momveka. 25 Yesu adayankha iwo, Ndakuwuzani, ndipo simukhulupirira. Ntchitozi ndizichita Ine m’dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni. 26 Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa Nkhosa zanga monga ndidanenera kwa inu. 27 Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo Ine ndizizindikira izo, ndipo zinditsata Ine. 28 Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzawonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa. 29 Atate wanga, amene adandipatsa izo ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m’dzanja la Atate wanga. 30 Ine ndi Atate ndife amodzi. 31 Pamenepo Ayuda adatolanso miyala kuti amponye Iye. 32 Yesu adayankha iwo, Ndakuwonetsani ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala Ine? 33 Ayuda adamuyankha Iye, chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu. 34 Yesu adayankha iwo, Kodi sikudalembedwa m’chilamulo chanu, ndidati Ine, Muli milungu? 35 Ngati adawatcha milungu iwo, amene mawu a Mulungu adawadzera ndipo malembo sangathe kuthyoledwa; 36 Kodi inu munena za Iye, amene Atate adampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndidati, ndiri Mwana wa Mulungu? 37 Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine. 38 Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate. 39 Choncho adafunanso kumgwira Iye; koma adapulumuka m’dzanja lawo. 40 Ndipo adachoka napitanso tsidya lija la Yordano, kumalo kumene kudali Yohane adalikubatiza poyamba paja; ndipo adakhala komweko. 41 Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, sadachita chozizwa Yohane; koma zinthu ziri zonse Yohane adanena za Iye zidali zowona. 42 Ndipo ambiri adakhulupirira pa Iye komweko.

Yohane 11

1 Tsopano munthu wina adadwala dzina lake Lazaro wa ku Betaniya, wa’mudzi wa Mariya ndi mbale wake Marita. 2 (Adali Mariya uja adadzoza Ambuye ndi mafuta wonunkhila bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake amene mlongo wake Lazaro adadwala.) 3 Choncho alongo ake adatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, wonani, amene mumkonda wadwala. 4 Koma Yesu pamene adamva, adati, kudwala kumeneku sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako. 5 Tsopano Yesu adakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro. 6 Pamene adamva kuti Iye akudwala, adakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri. 7 Ndipo pambuyo pake adanena kwa wophunzira ake, Tiyeni tipitenso ku Yudeya. 8 Wophunzira ake adanena kwa Iye, Ambuye, Ayuda adalikufuna kukuponyani miyala, tsopano apa; ndipo mupitanso komweko kodi? 9 Yesu adayankha, kodi sikuli maola khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuwunika kwa dziko lino lapansi. 10 Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuwunika mwa iye. 11 Zinthu izi Iye adati, ndipo zitatha izi adanena nawo, Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndipita kukamuwukitsa iye m’tulo take. 12 Chifukwa chake wophunzira ake adati kwa Iye Ambuye, ngati ali m’tulo adzakhala bwino. 13 Koma Yesu adanena za imfa yake: koma iwowa adayesa kuti adanena za mpumulo wa tulo. 14 Pamenepo Yesu adati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. 15 Ndipo ndikondwera chifukwa cha Inu kuti kudalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye. 16 Pamenepo Tomasi wotchedwa Didimo, adati kwa wophunizra anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi. 17 Ndipo pamene Yesu adadza, adapeza kuti pamenepo atakhala kale m’manda masiku anayi. 18 Ndipo Betaniya adali pafupi pa Yerusalemu, kutalika kwake ngati mitunda khumi ndi isanu. 19 Koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wawo. 20 Pamenepo Marita, pakumva mwamsanga kuti Yesu alinkudza, adapita kukakomana ndi Iye; koma Mariya adakhalabe m’nyumba. 21 Ndipo Marita adati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala Inu kuno mlongo wanga sakadafa. 22 Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. 23 Yesu adanena naye, Mlongo wako adzawukanso. 24 Marita adanena kwa Iye, Ndidziwa kuti adzawuka mkuwukitsidwa kwa tsiku lomaliza. 25 Yesu adati kwa iye, Ine ndine kuwuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; 26 Ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira Ichi? 27 Adanena kwa Iye, inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, wakudza m’dziko lapansi. 28 Ndipo m’mene adati ichi adachoka nayitana Mariya m’bale wake m’seri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuyitana iwe. 29 Koma iyeyo, pakumva, adanyamuka nsanga, nabwera kwa Iye. 30 Tsopano Yesu adali asadafike kumudzi, koma adali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye. 31 Pamenepo Ayuda wokhala naye m’nyumba ndi kumtonthoza iye, pakuwona Mariya adanyamuka msanga, natuluka, namtsata iye nanena kuti apita ku manda kukalira komweko. 32 Pamene Mariya adafika pamene padali Yesu, m’mene adamuwona Iye, adagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. 33 Pamenepo Yesu, pakumuwona iye alikulira, adadzuma mumzimu, nabvutika mwini. 34 Adati, Mwamuyika kuti iye? Adanena ndi Iye, Ambuye, tiyeni, mukawone. 35 Yesu adalira. 36 Ndipo Ayuda adanena, Tawonani momwe, adamkondera! 37 Koma ena mwa iwo adati, Uyu wotsegulira maso wosawona uja, sakadakhoza kodi kuchita kuti sakadafa ameneyunso? 38 Pamenepo Yesu adadzumanso mwa Iye yekha nafika kumanda. Koma padali phanga, ndipo mwala udayikidwa pamenepo. 39 Yesu adanena, chotsani mwala. Marita, mlongo, wake wa womwalirayo adanena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anayi. 40 Yesu adanena naye, Kodi sindinati kwa iwe kuti ngati, ukhulupirira, udzawona ulemerero wa Mulungu. 41 Ndipo adachotsa mwala, kuchokera pa malo pamene adayikapo womwalirayo. Ndipo Yesu adakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti mudamva Ine. 42 Ndipo ndidadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuyimilira pozungulira ndidanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu mudandituma Ine. 43 Ndipo m’mene adanena izi, adafuwula ndi mawu akulu, Lazaro, tuluka. 44 Ndipo womwalirayo adatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake idazingidwa ndi kamsalu. Yesu adati kwa iwo, M’masuleni iye, ndipo mlekeni apite. 45 Ndipo ambiri a mwa Ayuda amene adadza kwa Mariya, m’mene adawona zinthu zimene Yesu adachita adakhulupirira Iye. 46 Koma ena a mwa iwo adapita kwa Afarisi, nawauza zinthu zimene Yesu adazichita. 47 Pamenepo ansembe akulu, ndi Afarisi adasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu akuchita zozizwitsa zambiri! 48 Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzabwera Aroma nadzamtenga malo athu ndi mtundu wathu. 49 Koma wina wa m’modzi wa iwo, dzina lake Kayafa, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho adati kwa iwo, simudziwa kanthu konse inu. 50 Kapena simuganiza kuti mkokoma kwa inu kuti munthu m’modzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usawonongeke. 51 Koma ichi sadanena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho adanenera kuti Yesu adzafera mtunduwo; 52 Ndipo sichifukwa cha mtunduwo wokha ayi; koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu wobalalitsidwawo. 53 Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo adapangana kuti amuphe Iye. 54 Chifukwa chake Yesu sadayendayendanso mowonekera mwa Ayuda, koma adachokapo kupita kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efraimu; nakhala komweko pamodzi ndi wophunzira ake. 55 Koma Paskha wa Ayuda adali pafupi; ndipo ambiri adakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku milaga, usanafike Paskha kukadziyeretsa iwo wokha. 56 Pamenepo adali kumfuna Yesu, nanena wina ndi mzake poyimilira iwo m’kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzabwera kuphwando kodi? 57 Koma ansembe akulu ndi afarisi adalamulira, kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, awulule, kuti akamgwire Iye.

Yohane 12

1 Pomwepo atatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paskha, Yesu adabwera ku Betaniya kumene Lazaro adaukitsidwa kwa akufa. 2 Kumeneko iwo adamkozera Iye chakudya; ndipo Marita adatumikira; koma Lazaro adali m’modzi wa iwo akukhala pachakudya pamodzi ndi Iye. 3 Pamenepo Mariya m’mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta wonunkhira bwino a nardo a mtengo wake wapatali, adadzodza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake ndipo nyumba idadzazidwa ndi m’nunkho wake wa mafutawo. 4 Koma Yudase Isikariyote, mwana wa Simon m’modzi wa wophunzira ake, amene adzampereka Iye, adanena, 5 Bwanji mafuta wonunkhirawa sadagulitsidwe ndi makobiri mazana atatu, ndi kuwapatsa wosauka? 6 Koma adanena ichi sichifukwa adalikusamalira wosauka, koma chifukwa adali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoyikidwamo. 7 Pamenepo Yesu adati, Mlekeni iye, pakuti adachisungira ichi tsiku la kuyikidwa kwanga. 8 Pakuti wosauka muli nawo pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi ine nthawi zonse. 9 Pamenepo ambiri amwa Ayuda adadziwa Iye kuti adali pomwepo; ndipo adabwera, sichifukwa cha Yesu yekha, koma kuti akawonenso Lazaro, amene Iye adamuwukitsa kwa akufa. 10 Koma ansembe akulu adapangana kuti akaphe Lazaronso. 11 Pakuti ambiri a Ayuda adachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu 12 Tsiku limzake anthu ambiri adabwera kuphwando, atamva kuti Yesu alikubwera ku Yerusalemu. 13 Adatenga nthambi za mitengo ya kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuwula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m’dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli. 14 Ndipo Yesu, m’mene adapeza kabulu adakhala pamenepo; monga kwalembedwa; 15 Usawope, mwana wamkazi wa Ziyoni; tawona Mfumu yako idza wokhala pa mwana wa bulu. 16 Zinthu izi sadazidziwa wophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu adalemekezedwa, pamenepo adakumbukira kuti izi zidalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi 17 Pamenepo anthu amene adali pamodzi ndi Iye, m’mene adayitana Lazaro kutuluka m’manda, namuwukitsa kwa akufa, adachitira umboni. 18 Chifukwa cha ichinso anthu adabweranso kudzakomana ndi Iye, chifukwa adamva kuti Iye adachita chozozwitsa ichi. 19 Chifukwa chake Afarisi adanena wina ndi mzake, Muwona kuti simupindula kanthu konse; wonani dziko litsata pambuyo pa Iye. 20 Ndipo padali Ahelene ena mwa iwo akukwera kupita kukalambira paphwando. 21 Ndipo iwo adabwera kwa Filipo wa ku Betsaida wa m’Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuwona Yesu. 22 Filipo adabwera nanena kwa Andreya; nabwera Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu. 23 Ndipo Yesu adayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe. 24 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbewu ya tirigu siyigwa m’nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri. 25 Iye wokonda moyo wake adzawutaya; ndipo wodana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. 26 Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu. 27 Moyo wanga wabvutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndidadzera nthawi iyi. 28 Atate, Lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mawu wochokera kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso. 29 Choncho anthu amene adayimilira ndi kumva mawu adanena kuti kwagunda. Ena adanena, m’ngelo wayankhula ndi Iye. 30 Yesu adayankha nati, Mawu awa sadafike chifukwa cha Ine, koma cha inu. 31 Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano. 32 Ndipo Ine, m’mene ndikwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha. 33 Adanena ichi kuzindikiritsa kuti imfa yanji adzafa nayo. 34 Anthu adayankha Iye, Tidamva ife m’chilamulo kuti Khristu akhalakunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu ameneyu ndani? 35 Pamenepo Yesu adati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang’ono ndipo kuwunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuwunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene apita. 36 Pokhala muli nako kuwunika, khulupirirani kuwunikako, kuti mukakhale ana a kuwunikako. Zinthu izi Yesu adalankhula, nachoka nabisala mwini yekha kwa iwo. 37 Koma angakhale adachita zozizwitsa zambiri zotere pamaso pawo iwo sadakhulupirira Iye. 38 Kuti mawu a Yesaya m’neneri akakwaniritsidwe, amene adati, Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu? Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulukira kwa yani? 39 Chifukwa cha ichi sadathe kukhulupirira, pakuti Yesaya adatinso, 40 Wadetsa maso awo, nawumitsa mtima wawo; kuti angawone ndi maso, angazindikire ndi mtima, Nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse. 41 Zinthu izi adanena Yesaya chifukwa adawona ulemerero wake; wayankhula za Iye. 42 Ngakhale kudali tero,akulu olamulira ambiri adakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sadabvomereza, kuti angaletsedwe m’sunagoge. 43 Pakuti adakonda ulemerero wa anthu koposa ulemu wa Mulungu. 44 Koma Yesu adafuwula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine. 45 Ndipo wondiwona Ine awona amene adandituma Ine. 46 Ndadza Ine kuwunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima. 47 Ndipo ngati wina akumva mawu anga, ndi kusawakhulupirira, Ine sindimuweruza; pakuti sindinabwera kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi. 48 Iye amene andikana Ine, ndikusalandira mawu anga, ali naye womuweruza iye; mawu amene ndayankhula, iwowa adzamuweruza iye tsiku lomaliza. 49 Pakuti sindinayankhula mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu adandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikayankhule. 50 Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake liri moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndiyankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndiyankhula.

Yohane 13

1 Tsopano pasadafike phwando la Paskha Yesu, podziwa kuti nthawi yake idafika yochoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kupita kwa Atate, m’mene adakonda ake a Iye yekha a m’dziko lapansi, adawakonda kufikira chimariziro. 2 Ndipo utangotha mgonera, mdierekezi adatha kuyika mu mtima wake wa Yudase Isikariyote, mwana wamwamuna wa Simoni, kuti ankampereke Iye. 3 Yesu podziwa kuti Atate adampatsa Iye zinthu zonse m’manja mwake, ndi kuti adachokera kwa Mulungu, napita kwa Mulungu, 4 Iye adanyamuka pa mgonero, nabvula malaya ake; ndipo m’mene adatenga chopukutira adadzimanga m’chiwuno. 5 Pomwepo adathira madzi mu chosambira, nayamba kusambitsa mapazi a wophunzira ake ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene adadzimanga nacho. 6 Adadza pomwepo kwa Simoni Petro; Ndipo Petro adanena ndi Iye, Ambuye, Kodi Inu mundisambitsa ine mapazi? 7 Yesu adayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine, suchidziwa tsopano; koma udzadziwa mtsogolo mwake. 8 Petro adanena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu adamuyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe gawo pamodzi ndi Ine 9 Simoni Petro adanena ndi Iye, Ambuye, Simapazi anga wokha ayi, komanso manja anga ndi mutu wanga. 10 Yesu adanena naye, Amene adatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse; ndipo inu ndinu woyera, koma si nonse ayi. 11 Pakuti adadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi adati, simuli woyera nonse. 12 Pamenepo atatha Iye kusambitsa mapazi awo, ndi kubvala malaya ake, adakhalanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? 13 Inu munditcha Ine Mphunzitsi ndi Ambuye; ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. 14 Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mzake. 15 Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite. 16 Indetu, indetu ndinena ndi inu, Mtumiki sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye. 17 Ngati mudziwa zinthu izi, wodala inu ngati muzichita izo. 18 Sindinena za inu nonse; ndikudziwa ndawasankha; koma kuti cholemba chikwaniritsidwe, Iye wakudya mkate adatsamilitsa chidendene chake molimbana ndi Ine. 19 Tsopano ndinena kwa inu, Chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene. 20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene aliyense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine. 21 Yesu m’mene adanena izi, adabvutika mumzimu, nachitira umboni, nati, Indetu, Indetu, ndinena ndi inu, kuti m’modzi wa inu adzandipereka Ine. 22 Wophunzira adalimkupenyana wina ndi mzake ndi kusinkhasinkha kuti adanena za yani. 23 Ndipo m’modzi wa wophunzira ake, amene Yesu adamkonda, adatsamira pa chifuwa cha Yesu. 24 Pamenepo Simoni Petro adamkodola nanena naye, Utiwuze ndiye yani amene anena za iye. 25 Iyeyu potsamira pomwepo, pa chifuwa cha Yesu, adanena ndi Iye, Ambuye, ndiye yani? 26 Ndipo Yesu adayankha, Ndi iyeyu amene Ine ndidzamsunzira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo m’mene adasunsa nthongo adayitenga nampatsa Yudase Isikariyote mwana wa Simoni. 27 Ndipo pambuyo pa nthongoyo, Satana adalowa mwa Iyeyu. Pamenepo Yesu adanena naye, Chimene uchita, chita msanga. 28 Koma padalibe m’modzi wa iwo akukhalapo adadziwa chimene adafuna, poti adatere naye. 29 Pakuti popeza Yudase adali nalo thumba, ena adalikuyesa kuti Yesu adanena kwa iye, gula zimene zitisowa paphwando; kapena kuti apatse kanthu kwa awumphawi; 30 Iye pamene adalandira nthongo, adatuluka pomwepo. Koma udali usiku. 31 Choncho pamene adatuluka Yesu adanena, Tsopano Mwana wa munthu alemekezedwa, ndipo Mulungu alemekezedwa mwa Iye; 32 Ndipo ngati Mulungu adzalemekeza Iye.Mulungu adzamlemekeza Iye mwa Iye yekha,ndipo adzalemekeza Iye tsopano apa. 33 Tiyana, katsala kanthawi ndi khala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndidanena kwa Ayuda, kuti kumene ndimkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano. 34 Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mzake. 35 Mwa ichi anthu onse adzazindikira kuti muli wophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mzake. 36 Simoni Petro adanena ndi Iye,Ambuye mupita kuti? Yesu adayankha, Kumene ndipita sungathe kunditsata Ine tsopano; koma udzanditsata pambuyo pake. 37 Petro adanena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu. 38 Yesu adayankha, Moyo wako kodi udzawutaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asadalire tambala udzandikana Ine katatu.

Yohane 14

1 Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. 2 M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuwuzani inu; pakuti ndipita kukakukonzerani inu malo. 3 Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. 4 Ndipo kumene ndipita Ine, mukukudziwa, ndipo njira yake mukuyidziwa. 5 Tomasi adanena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene mukupita; tidziwa njira bwanji? 6 Yesu adanena naye, Ine ndine njira, ndi chowonadi ndi moyo. Palibe munthu abwera kwa Atate, koma mwa Ine. 7 Ngati mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuwona Iye. 8 Filipo adanena ndi Iye, Ambuye, tiwonetseni ife Atate, ndipo chitikwanira. 9 Yesu adanena naye, kodi ndiri ndi inu nthawi yayikulu yotere, ndipo sudandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine wawona Atate; unena iwe bwanji, Mutiwonetsere Atate? 10 Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mawu amene ndinena Ine kwa inu sindiyankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake. 11 Khulupirirani Ine, kuti Ine ndiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati sichomwecho, khulupirirani Ine chifukwa cha ntchito zomwe. 12 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupurira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate. 13 Ndipo chiri chonse mukafunse m’dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. 14 Ngati mudzapempha kanthu m’dzina langa, ndidzachita. 15 Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga. 16 Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse. 17 Ndiye Mzimu wa chowonadi, amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuwona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye, chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu. 18 Sindidzakusiyani inu mukhale amasiye; ndibwera kwa inu. 19 Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindiwonanso Ine; koma inu mundiwona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo. 20 Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. 21 Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadziwonetsa ndekha kwa iye. 22 Yudasi, amene sindiye Isikariyote, adanena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudziwonetsa nokha kwa ife, koma sikwa dziko lapansi? 23 Yesu adayankha nati kwa iye, Ngati munthu akonda Ine, adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzabwera kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. 24 Wosandikonda Ine sasunga mawu anga; ndipo mawu amene mumva sali mawu anga, koma a Atate wondituma Ine. 25 Zinthu izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. 26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zinthu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndidanena kwa inu. 27 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usabvutike, kapena usachite mantha. 28 Mwamva kuti Ine ndidanena kwa inu, ndipita, ndipo ndibwera kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu koposa Ine. 29 Ndipo tsopano ndakuwuzani chisadachitike kuti pamene chitachitika mukakhulupirire. 30 Sindidzayankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wadziko lapansi adza; ndipo alibe gawo pa Ine; 31 Koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate anga adandipatsa ine lamulo, chotero ndichita.

Yohane 15

1 Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye mlimi. 2 Nthambi ili yonse ya mwa Ine yosabala chipatso Iye ayichotsa; ndi ili yonse yobala chipatso,Iye ayisadza, kuti yikabale chipatso chochuluka. 3 Tsopano mwayeretsedwa inu chifukwa cha mawu amene ndayankhula ndi inu. 4 Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siyingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siyikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. 5 Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake; wokhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6 Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo anthu azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha. 7 Ngati mukhala mwa Ine, ndi mawu anga akhala mwa inu,mudzapempha chimene chiri chonse muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu. 8 Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala wophunzira anga. 9 Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalanibe m’chikondi changa. 10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake. 11 Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhalebe mwa inu, ndikuti chimwemwe chanu chikhale chodzadza. 12 Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mzake, monga ndakonda inu. 13 Palibe munthu ali nacho chikondi chachikulu choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu muli abwenzi anga, ngati muzichita ziri zonse zimene ndikulamulirani inu. 15 Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi, chifukwa zinthu zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. 16 Inu simudandisankha Ine, koma Ine ndidakusankhani inu, ndipo ndidakuyikani, kuti mukapite inu ndikubala chipatso; ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chiri chonse mukapempha Atate m’dzina langa akakupatseni inu. 17 Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mzake. 18 Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti linada Ine lisadayambe kuda inu. 19 Mukadakhala adziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndidakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. 20 Kumbukirani mawu amene Ine ndidanena kwa inu, kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati adandisautsa Ine, adzakusautsani inunso; ngati adasunga mawu anga, adzasunga anunso. 21 Koma zinthu izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa; chifukwa sadziwa wondituma Ine. 22 Ngati sindikadadza ndi kulankhula nawo sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chobisala pa machimo awo. 23 Iye wondida Ine, adanso Atate wanga. 24 Ngati sindikadachita pakati pa iwo ntchito zimene palibe munthu wina adazichita,iwo sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano iwo pamodzi adawowona, ndipo adandida Ine pamodzi ndi Atate wanga. 25 Koma kutero, kuti mawu wolembedwa m’chilamulo chawo akwaniritsidwe, kuti, Adandida Ine kopanda chifukwa. 26 Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa chowonadi amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni. 27 Ndipo inunso mudzachitira umboni, chifukwa mudali ndi Ine kuyambira pachiyambi.

Yohane 16

1 Zinthu izi ndayankhula kwa inu kuti musakhumudwitsidwe. 2 Adzakutulutsani m’masunagoge; koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu. 3 Ndipo zinthu izi adzachita, chifukwa sadadziwa Atate, kapena Ine. 4 Koma zinthu izi ndayankhula ndi Inu kuti pamene ikudza nthawi , mukakumbukire kuti ndidakuwuzani. Koma izi sindidanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndidali pamodzi ndi inu. 5 Koma tsopano ndipita kwa Iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Mupita kuti? 6 Koma chifukwa ndayankhula izi ndi inu chisoni chadzadza mumtima mwanu. 7 Koma ndinena Ine chowonadi ndi inu; kuti kuli phindu kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzabwera kwa inu; koma ngati ndichoka ndidzamtuma Iye kwa inu. 8 Ndipo akadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro; 9 Za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine; 10 Za chilungamo chifukwa ndipita kwa Atate, ndipo simundiwonanso Ine; 11 Za chiweruzo chifukwa mfumu ya dziko lino lapansi yaweruzidwa. 12 Ndiri nazo zambirinso zonena kwa inu, koma simungathe kuzidziwa tsopano lino. 13 Koma akabwera Iyeyo, Mzimu wa chowonadi, adzakutsogolerani inu m’chowonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu ziri zones adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilimkudza adzakuwonetserani. 14 Iyeyo adzalemekeza Ine; chifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzawonetsa kwa inu izo. 15 Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; chifukwa chake ndidati, kuti adzatenga za mwa Ine, nadzaziwonetsa izo kwa inu. 16 Katsala kanthawi, ndipo simundiwonanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiwona Ine, chifukwa ndipita kwa Atate. 17 Pamenepo wophunzira ake tsono adati mwa iwo wokha, Ichi chiyani chimene anena kwa ife, kanthawi ndipo simundiwona; ndipo kanthawi mudzandiwona chifukwa ndipita kwa Atate? 18 Chifukwa chake adanena, Ichi n’chiyani chimene anena, kanthawi? Sitidziwa chimene ayankhula. 19 Yesu adazindikira kuti adalikufuna kumfunsa Iye, ndipo adati kwa iwo, Kodi muli kufunsana wina ndi mzake za ichi, kuti ndidati, kanthawi ndipo simundiwona Ine, ndiponso kanthawi mudzandiwona Ine? 20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21 Mkazi pamene ali mu zowawa ali ndi chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wangobala mwana, sakumbukiranso chisawutso, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi. 22 Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuwonaninso, ndipo mtima wanu, udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu. 23 Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa Ine kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa. 24 Kufikira tsopano simudapempha kanthu m’dzina langa, pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniritsidwe. 25 Zinthu izi ndiyankhula ndi inu m’miyambi; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m’miyambi, koma ndidzakuwonetsani inu momveka bwino za Atate. 26 Tsiku limenelo mudzapempha m’dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzapemphera inu kwa Atate; 27 Pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndidatuluka kwa Mulungu. 28 Ndidatuluka kuchokera kwa Atate, ndipo ndabwera kudziko lapansi; ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate. 29 Wophunzira ake adanena, Onani, tsopano muyankhula zomveka, ndipo mulibe kunena miyambi. 30 Tsopano tidziwa kuti mudziwa zinthu zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti mudatuluka kuchokera kwa Mulungu. 31 Yesu adayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano? 32 Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense kuzake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine. 33 Zinthu izi ndayankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chisautso, koma kondwerani chifukwa; ndalilaka dziko lapansi Ine.

Yohane 17

1 Mawu awa adayankhula Yesu; ndipo adakweza maso ake kumwamba, ndipo adati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu; 2 Monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi liri lonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha. 3 Ndipo moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Khristu, amene Inu mudamtuma. 4 Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m’mene ndidatsiriza ntchito imene mudandipatsa kuti ndichite. 5 Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndidali nawo ndi Inu lisadakhale dziko lapansi. 6 Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m’dziko lapansi; adali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mawu anu. 7 Azindikira tsopano kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine ndi zanu; 8 Pakuti ndawapatsa iwo mawu amene mudandipatsa Ine; ndipo adalandira, nazindikira kowona kuti ndidatuluka kwa Inu, ndipo adakhulupirira kuti Inu mudandituma Ine. 9 Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine pakuti iwo alia nu. 10 Ndipo zanga zonse ziri zanu, ndi zanu ziri zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo. 11 Sindikhalanso m’dziko lapansi, koma iwo ali m’dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m’dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale m’modzi, monga ife. 12 Pamene ndidakhala nawo, Ine m`dziko la pansi ndidalikuwasunga iwo m’dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndidawasunga, ndipo sadatayika m’modzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniritsidwe. 13 Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo zinthu izi ndiyankhula m’dziko lapansi; kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo wokha. 14 Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi, linadana nawo, chifukwa sali adziko lapansi, monga Ine sindiri wadziko lapansi. 15 Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woyipayo. 16 Pakuti siali a dziko lapansi monga Ine sindiri wadziko lapansi. 17 Patulani iwo m’chowonadi; mawu anu ndi chowonadi. 18 Monga momwe mwandituma Ine kudziko lapansi Inenso ndituma iwo kudziko lapansi. 19 Ndipo chifukwa cha iwo, Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale wopatulidwa m’chowonadi. 20 Koma sindipempherera iwo wokha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mawu awo; 21 Kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa ife; kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu mudandituma Ine. 22 Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale m`modzi, monga ife tiri m’modzi. 23 Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa m’modzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu mudandituma Ine, nimudawakonda iwo, monga momwe mudakonda Ine. 24 Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndiri Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti mudandikonda Ine lisadakhazikike dziko lapansi. 25 Atate wolungama, dziko lapansi silidadziwa Inu, koma Ine ndidadziwa Inu; ndipo awa azindikira kuti Inu mudandituma Ine; 26 Ndipo ndidazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene mudandikonda nacho Ine chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.

Yohane 18

1 Pamene Yesu adanena mawu awa, adatuluka ndi wophunzira ake, kupita tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kudali munda, umene adalowamo Iye ndi wophunzira ake. 2 Ndipo Yudase amene adampereka Iye, adadziwa malowa; chifukwa Yesu ankapitako kawirikawiri ndi wophunzira ake. 3 Pamenepo Yudase, m’mene adalandira gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, adafika komweko ndi nyali ndi miwuni ndi zida. 4 Pamenepo Yesu, podziwa zinthu zonse ziri nkudza pa Iye, adatuluka nati kwa iwo, Mufuna yani? 5 Iwo adamyankha Iye, Yesu Mnazarete. Yesu adanena nawo, Ndine. Ndipo Yudase yemwe wompereka Iye, adayima nawo pamodzi. 6 Ndipo nthawi yomweyo adanena ndi iwo, Ndine, adabwerera m’mbuyo, nagwa pansi. 7 Pamenepo adawafunsanso, Mufuna yani? Ndipo iwo adati, Yesu Mnazarete. 8 Yesu adayankha, Ndati Ndine, chifukwa chake ngati mufuna Ine, lekani awa apite; 9 Kuti akwaniritsidwe mawu amene adayankhula kuti, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindidataya ndi m’modzi. 10 Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, adalisolola nakantha kapolo wa mkulu wa nsembe, namdula khutu lake lamanja. Dzina la kapoloyo lidali Malikasi. 11 Pamenepo Yesu adati kwa Petro, Longa lupanga m’chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindiyenera kumwera ichi kodi? 12 Ndipo gululo ndi kapitawo ndi asilikari a Ayuda adagwira Yesu nam’manga Iye; 13 Nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti adali mpongozi wa Kayafa, amene adali mkulu wa ansembe chaka chomwecho. 14 Tsopano Kayafa ndiye uja adalangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu m’modzi afere anthu. 15 Ndipo Simoni Petro ndi wophunzira wina adatsatira Yesu, koma wophunzira ameneyo adali wodziwika kwa mkulu wa nsembe, nalowa pamodzi ndi Yesu m’bwalo la mkulu wa ansembe; 16 Koma Petro adayima pakhomo kunja, chifukwa chake wophunzira winayo amene adadziwika kwa akulu a nsembe, adatuluka nayankhula ndi wapakhomo nalowetsa Petro. 17 Pamenepo buthu lapakhomolo lidanena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa wophunzira a munthu uyu? Iyeyu adanena, Sindine. 18 Koma atumiki ndi asilikari adalikuyimirirako ; adasonkha moto wamakala; pakuti kudali kuzizila; ndipo adalikuwotha moto; koma Petronso adali nawo alikuyimilira ndi kuwotha moto. 19 Ndipo mkulu wa ansembe adafunsa Yesu za wophunzira ake, ndi chiphunzitso chake. 20 Yesu adayankha iye, Ine ndayankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndidaphunzitsa Ine nthawi zonse m’sunagoge ndi m’kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindidayankhula kanthu. 21 Undifunsiranji Ine? Funsa iwo amene adamva chimene ndidayankhula nawo, tawona, amenewo adziwa chimene ndidanena Ine. 22 Koma m’mene Iye adanena izi, m’modzi wa asilikari akuyimilirako adapanda Yesu khofi, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa nsembe chomwecho? 23 Yesu adayankha iye, Ngati ndayankhula choyipa, chitira umboni wa choyipacho, koma ngati bwino, undipandiranji? 24 Tsopano Anasi adamtumiza Iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa nsembe. 25 Ndipo Simoni Petro adalikuyimilira ndi kuwotha moto. Pomwepo adati kwa iye, Suli iwenso wa wophunzira ake kodi? Iyeyu adakana nati, Sindine. 26 M’modzi wa atumiki a mkulu wansembe ndiye m’bale wake wa uja amene Petro adamdula khutu, adanena, Ine sindidakuwona iwe kodi m’munda pamodzi ndi iye? 27 Pamenepo Petro adakananso; ndipo pomwepo adalira tambala. 28 Pamenepo adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku nyumba ya chiweruzo; koma kudali mamawa; ndipo iwo sadalowa ku nyumba ya chiweruzo, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paskha. 29 Ndipo Pilato adatulukira kunja kwa iwo, nati, chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu? 30 Iwo adayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoyipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu. 31 Ndipo Pilato adati kwa iwo, Mutengeni Iye inu, ndi kumuweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda adati kwa iye, Tiribe ulamuliro wakupha munthu aliyense. 32 Kuti mawu a Yesu akwaniritsidwe, amene adanena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo. 33 Chifukwa chake Pilato adalowanso m’nyumba ya chiweruzo, nayitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda kodi? 34 Yesu adayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha kapena ena adakuwuzani za Ine? 35 Pilato adayankha, Ndiri Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe akulu adakupereka kwa ine; wachita chiyani? 36 Yesu adayankha, Ufumu wanga suli wapadziko lino lapansi; Ufumu wanga ukadakhala wa dziko lapansi, atumiki anga akadamenya nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera komkuno. 37 Pomwepo Pilato adati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu adayankha, munena kuti ndine Mfumu. Ndidabadwira ichi Ine, ndipo ndidadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni za chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga. 38 Pilato adanena kwa Iye, chowonadi ndi chiyani? Ndipo pamene adanena ichi, adatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nawo, Ine sindikupeza chifukwa chiri chonse mwa Iye. 39 Koma muli nawo machitidwe akuti ndimamasulira inu m’modzi pa Paskha; Kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu Mfumu ya Ayuda? 40 Pomwepo iwo adafuwulanso, nanena, Si munthu uyu, koma Baraba. Koma Baraba adali wachifwamba.

Yohane 19

1 Pamenepo tsono Pilato adamtenga Yesu, namkwapula. 2 Ndipo asilikali adaluka chisoti chaminga nabveka pa mutu pake, namfunda Iye mwinjiro wa papu; 3 Nadza kwa Iye, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda! Ndipo adampanda Iye khofi ndi manja awo. 4 Ndipo Pilato adatulukanso kunja, nanena nawo, Tawonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chiri chonse. 5 Pamenepo Yesu adatuluka kunja, atabvala chisoti cha minga, ndi mwinjiro wa papu. Ndipo Pilato adanena nawo, Tawonani munthuyu! 6 Ndipo pamene ansembe akulu ndi asilikari adamuwona Iye, adafuwula nanena, Mpachikeni, Iye, mpachikeni Iye. Pilato adanena nawo, Mtengeni inu Iye, nimumpachike; pakuti ine sindikupeza chifukwa mwa Iye. 7 Ayuda adayankha iye, Tiri nacho chilamulo ife, ndipo monga mwachilamulocho ayenera kufa, chifukwa adadziyesera yekha Mwana wa Mulungu. 8 Ndipo pamene Pilato adamva mawu awa, adachita mantha kwambiri. 9 Ndipo adalowanso ku nyumba ya chiweruzo, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sadamyankha kanthu. 10 Ndipo Pilato adanena kwa Iye, Simulankhula kwa ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndiri nawo wakukumasulani, ndipo ndiri nawo ulamuliro wakukupachikani? 11 Yesu adamyankha iye, Simukadakhala nawo ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa Kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo lalikulu. 12 Kuchokera pa ichi Pilato adafuna kum’masula Iye; koma Ayuda adafuwula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara. 13 Pamene Pilato adamva kunena kotero, adatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira; kumalo amene amatchedwa bealo la miyala, koma m’chihebri, Gabata. 14 Ndipo lidali tsiku lokonzekera Paskha; padali monga ola lachisanu ndi chimodzi. Ndipo adanena kwa Ayuda, Tawonani, mfumu yanu! 15 Pamenepo adafuwula iwowa, Chotsani, chotsani, mpachikeni Iye! Pilato adanena nawo, Ndipachike Mfumu yanu kodi? Ansembe akulu adayankha, tiribe mfumu koma Kayisala. 16 Ndipo pamenepo adampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Ndipo adamtenga Yesu, namutsogoza m’njira. 17 Ndipo Iye adasenza mtanda wake, natuluka kupita ku malo wotchedwa Malo a Chigaza, amene atchedwa m’Chihebri, Gologota; 18 Kumene adampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, mbali yina ndi yina, koma Yesu pakati. 19 Ndipo Pilato adalemba dzina naliyika pamtanda. Ndipo padalembedwa kuti YESU MNAZARETE, MFUMU YA AYUDA. 20 Ndipo lembo ilo adaliwerenga ambiri wa Ayuda; chifukwa malo amene Yesu adapachikidwapo adali pafupi pa mzindawo; ndipo lidalembedwa m’Chihebri, m’Chigriki, ndi m’Chilatini. 21 Pamenepo ansembe akulu a Ayuda, adanena kwa Pilato, Musalembe Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu adati, Ndiri Mfumu ya Ayuda. 22 Pilato adayankha, Chimene ndalemba, ndalemba. 23 Pamenepo asilikali, atampachika Yesu, adatenga zobvala zake nazigawa panayi, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malayawo adawombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, adalibe msoko. 24 Iwo adati wina kwa mzake, Tisang’ambe awa, koma tichite mayere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniritsidwe limene linena, Adagawana zobvala zanga mwa iwo wokha, ndi pa malaya anga adachitira mayere. Ndipo asilikari adachita izi. 25 Koma pa mtanda wa Yesu adayimilira amake ndi m’bale wa amake, Mariya, mkazi wa Klewopa, ndi Mariya wa Magadala. 26 Pamenepo Yesu pakuwona amake ndi wophunzira amene adamkonda, alikuyimilirako, adanena kwa amake, Mayi, wonani, mwana wanu! 27 Pamene adanena kwa wophunzirayo, Tawona, amayi ako! Ndipo kuyambira ola lomweli wophunzirayo adapita nawo kwawo. 28 Chitapita ichi, Yesu podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniritsidwe, adanena, Ndimva ludzu. 29 Tsopano adatenga chotengera chodzala ndi vinyo wosasa ndipo adazenenga chinkhupule chodzadza ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake. 30 Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo adati, kwatha; ndipo adaweramitsa mutu wake napereka mzimu. 31 Pomwepo Ayuda popeza padali tsiku lokonzekera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la sabata, pakuti tsiku lomwelo la sabata lidali lalikulu, adapempha Pilato kuti miyendo yawo ithyoledwe, ndipo achotsedwe. 32 Ndipo adabwera asilikari nathyola miyendo ya woyambayo, ndi winayo wopachikidwa pamodzi ndi Iye; 33 Koma pofika kwa Yesu, m’mene adamuwona Iye, kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake; 34 Koma m’modzi wa asilikali adamgwaza ndi nthungo m’nthiti yake, ndipo padatuluka pomwepo mwazi ndi madzi. 35 Ndipo iye amene adawona, wachita umboni, ndi umboni wake uli wowona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zowona, kuti inunso mukakhulupirire. 36 Pakuti izi zidachitika kuti lembo likwaniritsidwe, fupa la Iye silidzathyoledwa. 37 Ndipo linenanso lembo lina, Adzayang’ana pa Iye amene adampyoza. 38 Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuwopa Ayuda, adapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato adalola. Chifukwa chake adadza, nachotsa mtembo wake. 39 Koma adadzanso Nikodemo, amene adabwera kwa iye usiku poyamba paja, adatenga chisanganizo cha mule ndi aloye, monga miyeso zana 40 Pamenepo adatenga mtenbo wa Yesu, nawukulunga ndi nsalu za bafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa mayikidwe a maliro a Ayuda. 41 Tsopano pamene Iye adapachikidwapo padali munda; ndi m’mundamo mudali manda atsopano m’mene sadayikidwamo munthu aliyense nthawi zonse. 42 Pomwepo ndipo adayika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzekera la Ayuda, pakuti mandawo adali pafupi.

Yohane 20

1 Tsiku loyamba la sabata adadza Mariya wa Magadalena m’mamawa, kusadayambe kucha pamanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda. 2 Pomwepo adathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu adamkonda, nanena nawo. Adamchotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene adamuyika Iye. 3 Choncho Petro adapita ndi wophunzira winayo, nafika kumanda. 4 Choncho adathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo adathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda; 5 Ndipo m’mene adawerama chosuzumira adawona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sadalowamo; 6 Pamenepo adadzanso Simoni Petro alinkutsata iye, nalowa m’manda; ndipo adawona nsalu zabafuta zitakhala. 7 Ndipo kansalu kamene kadali pamutu pake, kosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma kopindika padera pamalo pena. 8 Pamenepo tsono adalowanso wophunzira winayo, amene adayamba kufika kumanda, ndipo adawona, nakhulupirira. 9 Pakuti kufikira pomwepo sadadziwa malembo akuti ayenera Iye kuwuka kwa akufa. 10 Pamenepo wophunzirawo adachokanso, kupita kwawo. 11 Koma Mariya adalikuyimilira kumanda kuja, alikulira. Ndipo m’mene adali kulira adawerama nasuzumira m’manda; 12 Ndipo adawona angelo awiri atabvala zoyera alikukhala m’modzi kumutu, ndi wina kumiyendo, pamene mtembo wa Yesu udagona. 13 Ndipo iwowa adanena kwa iye, Mkazi, uliranji? Adanena nawo, chifukwa adachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene adamuyika Iye. 14 Ndipo m’mene adanena izi, adachewuka m’mbuyo, nawona Yesu ali chiliri, ndipo sadadziwa kuti ndiye Yesu. 15 Yesu adanena naye, Mkazi, Uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumanda adanena ndi Iye, Mbuye ngati mwamunyamula Iye, ndiwuzeni kumene mwamuyika Iye, ndipo ndidzamchotsa. 16 Yesu adanena naye, Mariya. Iyeyu m’mene adacheuka, adanena ndi Iye m’Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi. 17 Yesu adanena naye, Usandikhudza, pakuti sindidathe kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, ndikwera kupita kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu. 18 Mariya Magadalene adapita, nawuza wophunzirawo, kuti, Ndawona Ambuye; ndi kuti adanena zinthu izi kwa iye. 19 Pamenepo pokhala madzulo, tsiku lomwelo loyamba la sabata, makomo ali hitsekere, kumene adakhala wophunzira, chifukwa cha kuwopa Ayuda, Yesu adadza nayimilira pakati pawo, nanena nawo, Mtendere ukhale ndi inu. 20 Ndipo pamene adanena ichi, adawonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo wophunzira adakondwera pakuwona Ambuye. 21 Chifukwa chake Yesu adatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu. 22 Ndipo pamene adanena ichi, adawapumira, nanena nawo, Landirani Mzimu Woyera. 23 Zochimwa za aliyense muzikhululukira, zidzakhululukidwa kwa iwo; ndipo za aliyense muzigwiritsa, zidzagwiridwa. 24 Koma Tomasi, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sadakhala nawo pamodzi, pamene Yesu adadza. 25 Choncho wophunzira ena adanena naye, Tamuwona Ambuye. Koma iye adati kwa iwo, Ndikapanda kuwona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuyika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, kuyika dzanja langa ku nthiti yake; sindidzakhulupirira. 26 Ndipo patapita masiku asanu ndi atatu, wophunzira ake adalinso m’nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nawo. Yesu adadza, makomo ali chitsekere, nayimilira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu. 27 Pomwepo adanena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuwone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliyike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira. 28 Tomasi adayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga. 29 Yesu adanena kwa iye, Chifukwa wandiwona Ine, wakhulupirira; Wodala iwo akukhulupirira angakhale sadawona 30 Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu adazichita pamaso pa wophunzira ake zimene sizidalembedwa m’buku ili. 31 Koma zidalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nawo moyo kupyolera m’dzina lake.

Yohane 21

1 Zitapita izi Yesu adadziwonetseranso kwa wophunzira ake ku nyanja ya Tiberiya. Koma adadziwonetsera mwini yekha chotere. 2 Adali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedayo, ndi awiri ena a wophunzira ake. 3 Simoni Petro adanena nawo, ndinka kukasodza. Adanena naye, ifenso tipita nawe. Adatuluka, nalowa m’chombo; ndipo mu usiku uja sadagwira kanthu. 4 Koma pakuyamba kucha, Yesu adayimilira pambali pa nyanja, komatu wophunzira sadadziwa kuti ndiye Yesu. 5 Yesu adanena nawo, Ananu muli nako kanthu kakudya kodi? Adamyankha Iye, Ayi. 6 Ndipo Iye adati kwa iwo, ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja la chombo, ndipo mudzapeza. Pamenepo adaponya, ndipo adalibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba. 7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu adamkonda adanena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, adadzibveka malaya a pathupi, pakuti adali wamaliseche, nadziponya yekha m’nyanja. 8 Ndipo wophunzira ena adabwera m’chombo, pakuti sadali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo. 9 Ndipo pamene adatulukira pamtunda, adapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate. 10 Yesu adanena nawo, Bweretsani nsomba zimene mwazigwira tsopano. 11 Simoni Petro adakwera m’chombo nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu; zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zidachuluka kotere; khoka silidang’ambika. 12 Yesu adanena nawo, Idzani mudye. Koma palibe m’modzi wa wophunzira adatha kumfunsa Iye, ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye. 13 Yesu adadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba. 14 Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudziwonetsera Yesu kwa wophunzira ake m’mene adauka kwa akufa. 15 Pamene adadya adanena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Adanena ndi Iye, Inde Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Adanena naye, Dyetsa ana a nkhosa zanga. 16 Adanena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Adanena ndi Iye, Inde,Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Adanena naye, dyetsa nkhosa zanga. 17 Adanena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro adamva chisoni kuti adati kwa Iye kachitatu, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu adanena naye, Dyetsa nkhosa zanga. 18 Indetu, indetu ndinena ndi iwe, pamene udali m’nyamata udadzimangira wekha m’chiuno lamba, ndipo udayenda kumene udafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina nadzakunyamula kumene sufuna. 19 Koma ichi adanena ndikuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m’mene adanena ichi, adati kwa iye, Nditsate Ine. 20 Petro m’mene adachewuka, adapenya wophunzira amene Yesu adamkonda alikutsata, amenenso adatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, Ndani iye wakupereka Inu? 21 Pamenepo Petro pakumuwona, adanena kwa Yesu, Ambuye, zidzakhala bwanji ndi munthu uyu? 22 Yesu adanena naye, ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Nditsate Ine. 23 Chifukwa chake mawu awa adatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa; koma Yesu sadanena kwa iye kuti sadzafa. Koma ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe? 24 Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni wa zinthu izi, ndipo adalemba zinthu izi, ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi wowona. 25 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu adazichita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nawo malo a mabuku amene akadalembedwa. Ameni.

Ntchito 1

1 Zolemba zoyamba ndidakulembera Teofilo, mawu aja ndidakonza, za zonse Yesu adayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa, 2 Kufikira tsiku lija adatengedwa kumka Kumwamba, atatha Iye kuwalamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha. 3 Kwa iwonso amene adadziwonetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, nawonekera kwa iwo masiku makumi anayi, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu: 4 Ndiponso posonkhana nawo pamodzi, adawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu adikire lonjezano la Atate, limene, adati, mudalimva kwa Ine. 5 Pakuti Yohane adabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asadapite masiku ambiri. 6 Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, adamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli? 7 Koma Iye adati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate adaziyika muwulamuliro wake wa Iye yekha. 8 Komatu mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake adziko. 9 Ndipo m’mene adanena zinthu izi, ali chipenyerere iwo, adanyamulidwa; ndipo mtambo udamlandira Iye kumchotsa pamaso pawo. 10 Ndipo pakukhala iwo chipenyerere Kumwamba pomuwona Iye alimkupita kumwamba, tawonani, amuna awiri wobvala zoyera adayimilira pambali pawo; 11 Amenenso adati; Amuna inu a ku Galileya, muyimiranji ndi kuyang’ana Kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzabwera momwemo monga mudamuwona ali mkupita Kumwamba. 12 Pamenepo iwowa anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri lonenedwa la Azitona, limene kuchokera ku Yerusalemu, ndi ulendo woyendako pa tsiku la sabata. 13 Ndipo pamene adalowa, adakwera ku chipinda cha pamwamba, kumene adali kukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyu, ndi Simoni Zelota ndi Yuda mwana wa Yakobo. 14 Iwo onse adali kukangalika ndi mtima umodzi m’kupemphera, ndi kupembedzera pamodzi ndi akazi,ndi Mariya, amake a Yesu, ndi abale ake omwe. 15 Ndipo m’masiku awa adayimilira Petro pakati pa wophunzira, nati (nambala ya maina a anthu wosonkhana pamalo pomwepo ndiwo ngati zana limodzi ndi makumi awiri) 16 Amuna inu, abale, kudayenera kuti lemba likwaniritsidwe, limene Mzimu Woyera adayamba kunena mwa m’kamwa mwa Davide za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu. 17 Chifukwa adali wowerengedwa mwa ife, ndipo adalandira gawo lake la utumiki uwu. 18 Munthu uyu tsono adadzigulira munda ndi mphotho ya zoipa; ndipo adagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse adakhuthuka; 19 Ndipo chidadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti mundawo m’chinenedwe chawo umatchedwa Akeldana, ndiwo munda wa mwazi. 20 Pakuti kwalembedwa m’buku la Masalmo, pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang’aniro wake autenge wina. 21 Potero kuyenera kuti wina wa amunawo adatsatana nafe nthawi yonseyi imene Ambuye Yesu adalowa ndikutuluka mwa ife, 22 Kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija Iye adatengedwa kumka Kumwamba kutisiya ife, m’modzi ayenera kusankhidwa akhale mboni ya kuwuka kwake pamodzi ndi ife. 23 Ndipo adayimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba, amene adatchedwanso Yusto, ndi Matiya. 24 Ndipo adapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri m’modziyo amene mudamsankha, 25 Kuti alowe malo a utumiki uwu ndi Utumwi, kuchokera komwe Yudase adapatuka, kuti apite ku malo a iye yekha. 26 Ndipo adayesa mayere pa iwo; ndipo adagwera Matiya; ndipo adawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi m’modzi wa Atumwi.

Ntchito 2

1 Ndipo pamene tsiku la Pentekoste lidafika, iwo onse adali amtima umodzi pa malo amodzi. 2 Ndipo mwadzidzidzi adamveka mawu wochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene adalikukhalamo. 3 Ndipo pamenepo adawonekera kwa iwo malilime wogawanika, wonga a moto; ndipo udakhala pa iwo onse wayekha wayekha. 4 Ndipo iwo adadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula ndi malilime ena, monga Mzimu adawayankhulitsa. 5 Ndipo adali mu Yerusalemu wokhalako Ayuda, amuna wopembedza, wochokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo. 6 Koma pochitika mawu awa, khamu la lidasonkhanalo, lidasokonezeka popeza aliyense wa iwo adamva iwowa alikuyankhula m’chiyankhulidwe chake cha iye yekha. 7 Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena wina ndi mzake, Tawonani, awa onse ayankhulawa sali Agalileya kodi? 8 Ndipo nanga, ife tikumva bwanji munthu aliyense, m’chiyankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho? 9 Aparti ndi Amedi, ndi Ayelami, ndi iwo wokhala m’Mesopotamiya, m’Yudeya ndiponso m’Kapadokiya, m’Ponto, ndi m’Asiya; 10 M’Frugiya, ndiponso m’Pamfuliya, m’Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo wochokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso wopinduka, 11 Akrete ndi Aarabu tikuwamva iwo alikuyankhula m’malilime athu za ntchito zodabwitsa za Mulungu. 12 Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mzake, kodi ichi n’chiyani? 13 Koma ena adawaseka, nanena kuti anthu awa Akhuta vinyo wa lero. 14 Koma Petro, adayimilira pamodzi ndi khumi ndi m’modziwo, nakweza mawu ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Akuyudeya, ndi inu nonse wokhala m’Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu ku mawu anga. 15 Pakuti awa sadaledzere monga muyesa inu; pakuti ndi ola lachitatu lokha la tsiku; 16 Komatu ichi ndi chimene chidanenedwa ndi m’neneri Yoweli; 17 Ndipo kudzali m’masiku wotsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi liri lonse ndipo ana anu amuna, ndi a akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzawona masomphenya, akulu anu adzalota maloto: 18 Ndiponso pa atumiki anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa; ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera. 19 Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa pansi pa thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pansi pa dziko lapansi Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi; 20 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi lowonekera; 21 Ndipo kudzali,kuti yense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa. 22 Amuna inu Aisrayeli, mverani mawu awa; Yesu Mnazarate, mwamuna wobvomerezedwa ndi Mulungu pakati pa inu, mwa zozizwa ndi zizindikiro, zimene Mulungu adazichita mwa Iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha. 23 Ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woyikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwamtenga ndi kumupha ndi manja a anthu wosayeruzika; 24 Yemweyo Mulungu adamuwukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikudali kotheka kuti Iye agwidwe nayo. 25 Pakuti Davide anena za Iye, ndidawona Mbuye pamaso panga nthawi zonse, chifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndisasunthike. 26 Mwa ichi udakondwera mtima wanga, ndipo lidasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo. 27 Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Gehena, kapena simudzapereka woyera wanu awone chibvunde. 28 Mundidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu. 29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posawopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira nayikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino. 30 Potero pokhala m’neneri iye, ndi kudziwa kuti Mulungu adamulumbirira Iye lumbiro, kuti mwa chipatso cha m’chuwuno mwake, kolingana ndi thupi, adzamuwukitsira Khristu, kuti adzakhale pa mpando wachifumu wake; 31 Iye powona ichi kale, adayankhula za kuwuka kwa Khristu, kuti sadasiyidwa m’Gehena, ndipo thupi lake silidawona chibvunde. 32 Yesu ameneyo, Mulungu adamuwukitsa za ichi tiri mboni ife tonse. 33 Potero, popeza adakwezedwa ndi dzanja la manja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, adatsanulira ichi, chimene inu tsopano mupenya ndi kumva. 34 Pakuti Davide sadakwera Kumwamba ayi; koma iye mwiniyekha adati, Ambuye adati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa. 35 Kufikira ndikayike adani ako chopondapo mapazi ako. 36 Chifukwa chake lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu adamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu mudampachika. 37 Koma pamene adamva ichi, adalaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale? 38 Pamenepo Petro adati kwa iwo, lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39 Pakuti lonjezano liri kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, ngakhale onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitana. 40 Ndipo ndi mawu ena ambiri adachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse nokha kwa m’bado uno wokhotakhota. 41 Pamenepo iwo amene adalandira mawu ake mokondwera anabatizidwa; ndipo adawonjezeka tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. 42 Ndipo iwo adali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano, m’kunyema mkate ndi mapemphero . 43 Koma padadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zidachitika mwa atumwi. 44 Ndipo onse wokhulupirira adali pamodzi, nakhala nazo zinthu zonse zodyerana. 45 Ndipo zimene adali nazo, ndi chuma chawo, adazigulitsa nazigawira kwa anthu onse, monga yense adasowera. 46 Ndipo tsiku ndi tsiku adali chikhalire ndi mtima umodzi m’kachisi, ndipo adanyema mkate kuchokera nyumba ndi nyumba, nalandira chakudya ndi chisangalalo, ndi mtima umodzi. 47 Nalemekeza Mulungu ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye adawawonjezera mumpingo tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Ntchito 3

1 Tsopano Petro ndi Yohane adalikukwera kupita kukachisi pa ola lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinayi 2 Ndipo munthu wina wosayenda chibadwire adanyamulidwa, amene amkamuyika tsiku ndi tsiku pakhomo la kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zachifundo kwa iwo wolowa m’kachisi; 3 Ameneyo pakuwona Petro ndi Yohane akuti alowe m’kachisi, adapempha alandire zachifundo. 4 Ndipo, Petro pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane adati, Tiyang’ane ife. 5 Ndipo iye adabvomereza iwo, nalingilira kuti adzalandira kanthu kuchokera kwa iwo. 6 Pamenepo Petro adati, siliva ndi golide ndiribe; koma chimene ndiri nacho, ichi ndikupatsa, M’dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, nyamuka nu yende. 7 Ndipo adamgwira iye ku dzanja lake lamanja, nam’nyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zidalimbikitsidwa. 8 Ndipo adazunzuka, nayimilira, nayenda; ndipo adalowa pamodzi nawo m’kachisi, nayenda nalumpha, nayamika Mulungu. 9 Ndipo anthu onse adamuwona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu; 10 Ndipo iwo adamzindikira iye, kuti ndiye wopempha zachifundo amene adakhala pa khomo lokongola la kachisi: ndipo adadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera. 11 Koma m’mene munthu wosayenda amene adachiritsidwa uja adagwira Petro ndi Yohane, adawathamangira pamodzi anthu onse kukhumbi lotchedwa la Solomo alikudabwa kwakukulu ndithu. 12 Koma m’mene Petro adachiwona, adayankha kwa anthu, Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamuyendetsa iye ndi mphamvu yathu, kapena ndi chiyero ndi chipembedzo chathu? 13 Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu; adalemekeza Mwana wake Yesu; amene inu mudampereka ndi kumkana Iye pamaso pa Pilato, pamene iyeyu adafuna kum’masula. 14 Koma inu mudakana Woyera ndi Wolungamayo, ndipo mudapempha munthu wakupha apatsidwe kwa inu. 15 Ndipo mudapha Mkulu wa moyo, amene Mulungu adamuwukitsa kwa akufa; za ichi ife ndife mboni. 16 Ndipo mudzina lake kupyolera mu chikhulupiliro cha munthu uyu, chamlimbikitsa iye amene mumuwona, nimumdziwa; inde, chikhulupiriro chimene cha mwa Iye chidampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse. 17 Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti mudachita izi mosadziwa monganso wolamulira anu. 18 Koma zinthu zimenezo zimene Mulungu kale adaziwonetseratu m’kamwa mwa aneneri ake onse, kuti Khristu adzamva zowawa, choteroIye adakwaniritsa. 19 Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye; 20 Ndipo adzatuma Khristu amene poyamba adalalikidwa kwa inu; 21 Amene thambo la Kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu adayankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake onse woyera chiyambire cha dziko lapansi. 22 Pakuti Mosetu adati kwa makolo, Mbuye Mulungu wanu adzawukitsira inu m’neneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m’zinthu zonse akayankhula nanu. 23 Ndipo kudzali, kuti moyo uli wonse wosamvera m’neneri ameneyu, udzasakazidwa kuchotsedwa pakati pa anthu. 24 Inde, ngakhale ndi aneneri onse kuyambira Samueli ndi womutsatira, onse amene adayankhula adanenera za masiku awa. 25 Inu ndinu ana a aneneri, ndi apanganolo Mulungu adapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, ndipo mu mbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa. 26 kwa inu choyamba, Mulungu, atatha kuwukitsa Mwana wake Yesu, adamutuma Iye kukudalitsani inu, kukubwezani yense wa inu ku zoyipa zanu.

Ntchito 4

1 Koma pamene adalikuyankhula ndi anthu, ansembe ndi m’dindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadza kwa iwo, 2 Ali wobvutika mtima chifukwa adaphunzitsa anthuwo, nalalikira za Yesu za kuwuka kwa akufa. 3 Ndipo adawathira manja, nawayika mundende kufikira m’mawa; pakuti adali madzulo amenewo. 4 Koma ambiri a iwo amene adamva mawuwo adakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chidali ngati zikwi zisanu. 5 Zitapita izi m’mawa mwake, oweruza awo, ndi akulu, ndi alembi; 6 Ndipo Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Alesandro, ndi onse amene adali afuko la mkulu wa ansembe, adasonkhana pamodzi ku Yerusalemu. 7 Ndipo m’mene adawayimika pakati, adafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m’dzina lanji, mwachita ichi inu? 8 Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera adati kwa iwo, oweruza a anthu inu, ndi akulu a Israyeli, 9 Ngati ife lero tiweruzidwa chifukwa cha ntchito yabwino imene yachitika pa munthu wolumalayu, ndi momwe wachiritsidwira iye; 10 Chidziwike bwino kwa inu nonse, ndi kwa anthu onse a Israyeli, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu mudampachika, amene Mulungu adamuwukitsa kwa akufa, mwa Iyeyo munthuyu ayimira pamaso panu wamoyo. 11 Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu womanga nyumba, umene wakhala mutu wa pangodya. 12 Ndipo palibe chipulumuso mwa wina yense: pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la Kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo. 13 Tsopano pamene adawona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu wosaphunzira ndi wopulukira, adazizwa ndipo adawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu. 14 Ndipotu pakuwona munthu wochiritsidwayo alikuyimilira pamodzi nawo, analibe kanthu kakunena kotsutsa. 15 Koma pamene adawalamulira iwo achoke m’bwalo la akulu, adanena wina ndi mzake. 16 Nanena kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chawoneka kwa onse akukhala m’Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana. 17 Komatu tiwawopseze asayankhulenso m’dzina ili kwa munthu ali yense, kuti chisabukenso kwa anthu. 18 Ndipo adawayitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu. 19 Koma Petro ndi Yohane adayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. 20 Pakuti sitingathe ife kuleka kuyankhula zinthu zimene tidaziwona ndi kuzimva. 21 Koma m’mene adawawopsanso adawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse adalemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika. 22 Pakuti adali wa zaka zake zoposa makumi anayi munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidawonetsedwa. 23 Ndipo m’mene adamasulidwa, anadza kwa anzawo a iwo wokha, nawawuza ziri zonse woweruza ndi akulu adanena nawo. 24 Ndipo m’mene adamva, adakweza mawu kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mbuye Inu ndinu Mulungu wolenga Kumwamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja ndi zonse ziri momwemo: 25 Amene mwa pakamwa pa Davide mtumiki wanu, mudati,Amitundu asokoseranji ndi anthu alingilira zopanda pake? 26 Adadzindandalitsa mafumu adziko ndipo woweruza adasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake. 27 Pakuti zowonadi adasonkhana pamodzi Herode, ndi Pontiyo Pilato ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumchitira choyipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene mudamdzoza, 28 Kuti adzachite zimene dzanja lanu ndi uphungu wanu mudazikonzeratu kale kuti zidzachitike. 29 Ndipo tsopano Ambuye, penyani kuwopsa kwawo, ndipo patsani kwa atumiki anu kuti ayankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse. 30 M’mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina laMwana wanu wopatulika Yesu. 31 Ndipo m’mene iwo adapemphera, padagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo adadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayankhula mawu a Mulungu molimbika mtima. 32 Ndipo unyinji wa iwo wokhulupilira adali a mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sadanena m’modzi kuti kanthu kachuma adali nacho ndi kakeka iye yekha; koma adali nazo zonse zofanana. 33 Ndipo atumwi adachita umboni ndi mphamvu yayikulu za kuwuka kwa Ambuye Yesu; ndipo padali chisomo chachikulu pa iwo onse. 34 Pakuti mwa iwo mudalibe wosowa; pakuti onse amene adali nayo minda, kapena nyumba, adazigulitsa nabwera nawo malonda ake a izo adazigulitsa, 35 Ndipo adaziyika pa mapazi a atumwi; ndipo adagawira yense monga kusowa kwake. 36 Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnaba (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kupro, 37 Pokhala nawo munda, adaugulitsa, nabwera nazo ndalama zake, naziyika pamapazi a atumwi.

Ntchito 5

1 Koma munthu wina dzina lake Hananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake, adagulitsa katundu wawo, 2 Napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe adadziwa, natenga chotsala, nachiyika pa mapazi a atumwi. 3 Koma Petro adati, Hananiya, Satana adadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, kupatula pa mtengo wake wa mundawo? 4 Pamene udali nawo sudali wako kodi? Ndipo pamene udawugulitsa sudali m’manja mwako kodi? Bwanji chidalowa ichi mumtima mwako?sudanyenga anthu, komatu Mulungu. 5 Ndipo Hananiya pakumva mawu awa adagwa pansi namwalira: ndipo mantha akulu adagwera pa iwo onse amene adamva zinthu izi. 6 Ndipo anyamata adanyamuka, namkulunga, nam’nyamula, natuluka naye amuyika. 7 Koma atapita monga maola atatu, ndipo mkazi wake, wosadziwa chidachitikacho, adalowa. 8 Ndipo Petro adanena naye, Undiwuze, ngati mudagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo adanena, Inde, wakuti. 9 Pamenepo Petro adati kwa iye, mudapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Tawona, mapazi awo a iwo amene adayika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe. 10 Ndipo adagwa pansi pomwepo pamapazi ake, namwalira; ndipo adalowa anyamatawo, nampeza iye atafa, ndipo adam’nyamula kutuluka naye, namuyika iye pambali pa mwamuna wake. 11 Ndipo mantha akulu adadza pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumva izi. 12 Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zidachitidwa pa anthu; (ndipo adali onse ndi mtima umodzi m’khumbi la Solomo. 13 Koma palibe m’modzi wa wotsalawo adalimba mtima kuphatikana nawo: komatu anthu adawakuzitsa. 14 Ndipo wokhulupirira adachuluka kuwonjezekabe kwa Ambuye, makamu a amuna ndi akazi). 15 Kotero kuti adanyamulanso natuluka nawo wodwala kumakwalala, nawayika pamakama ndi pa mphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chinthunzi chake chigwere wina wa iwo. 16 Pamenepo lidadzanso khamu kuchokera kumizinda yozungulira Yerusalemu, litatenga wodwala, ndi wobvutika ndi mizimu yonyansa; ndipo adachiritsidwa onsewa. 17 Pamenepo adawuka mkulu wa ansembe ndi onse amene adali naye, ndiwo ampatuko wa Asaduki, ndipo adali wodzazidwa ndi mkwiyo. 18 Ndipo adawathira manja atumwi, nawayika m’ndende ya anthu wamba. 19 Koma m’ngelo wa Ambuye adatsegula makhomo a ndende usiku, nawatulutsa iwo, nati; 20 Pitani, ndipo imilirani, nimuyankhule m’kachisi kwa anthu onse mawu a Moyo umenewu. 21 Ndipo pamene adamva ichi, adalowa m’Kachisi m’banda kucha, naphunzitsa. Koma adadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene adali naye, nasonkhanitsa abwalo la akulu, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo. 22 Koma asilikali amene adafikako sadawapeza m’ndende, ndipo pobwera adafotokoza, 23 Nanena, Nyumba ya ndende zowonadi tidapeza chitsekere ndi chitetezo chonse ndi alonda ali chiyimilire pakhomo; koma pamene tidatsegula sitidapezamo m’modzi yense. 24 Koma m’mene adamva mawu awa m’dindo wa Kachisi ndi ansembe akulu adathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani. 25 Ndipo pamenepo padadza wina nawafotokozera, kuti Tawonani, amuna aja mudawayika m’ndende ali m’Kachisi, alikuyimilira ndi kuphunzitsa anthu. 26 Pamenepo adachoka mdindo pamodzi ndi asilikali; nadza nawo, koma osawagwiritsitsa, pakuti adawopa anthu, kuti angaponyedwe miyala. 27 Ndipo m’mene adadza nawo, adawayika pa bwalo la akulu. Ndipo adawafunsa mkulu wa ansembe. 28 Nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitse kutchula dzina ili; ndipo tawonani mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja. 29 Pamenepo Petro ndi atumwi ena adati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu. 30 Mulungu wa makolo athu adawukitsa Yesu, amene mudamupha inu, ndi kumpachika pa mtengo. 31 Ameneyo Mulungu adamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mfumu ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israyeli kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo. 32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; ndi Mzimu Woyeranso, amene Mulungu adapereka kwa iwo akumvera Iye. 33 Koma m’mene adamva ichi, iwo adapsa mtima, nafuna kuwapha. 34 Koma adanyamukapo wina pa bwalo la akulu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliyeli, mphuniztsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang’ono. 35 Ndipo iye adati kwa iwo, amuna inu a Israyeli, tamachenjerani mwa inunokha za anthu awa, chimene muti muwachitire. 36 Pakuti asadafike masiku ano adawuka Tewuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu adaphatikana naye, chiwerengero chawo ngati mazana anayi; ndipo adaphedwa; ndi onse amene adamvera iye adamwazika, napita pachabe. 37 Atapita ameneyo, adawuka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso adawonongeka, ndi onse amene adamvera iye adabalalitsidwa. 38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umenewu kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka: 39 Koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke wotsutsana ndi Mulungu. 40 Ndipo adabvomerezana ndi iye; ndipo m’mene adayitana atumwi, adawakwapula nawalamulira asayankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo adawamasula. 41 Ndipo pamenepo iwo adapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti adayesedwa woyenera kunzunzidwa chifukwa cha dzina lake. 42 Ndipo masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba sadaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.

Ntchito 6

1 Koma masiku awo, pakuchulukitsa wophunzira, kudabuka madandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo adayiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. 2 Ndipo khumi ndi awiri adayitana khamu la wophunzira, nati, sikuyenera ife kuti tisiye mawu a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. 3 Chifukwa chake, abale yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri ambiri yabwino, wodzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawayike agwire ntchito iyi. 4 Koma ife eni tokha tidzapitiriza chilimbikire kupemphera, ndi kutumikira mawu. 5 Ndipo mawu amenewa adakonda khamu lonse; ndipo adasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo ndi Prokoro, ndi Nikanora, ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolawo, ndiye wopinduka wa ku Antiyokeya: 6 Amenewo adawayika pamaso pa atumwi; ndipo m’mene adapemphera, adayika manja pa iwo. 7 Ndipo mawu a Mulungu adakula; ndipo chiwerengero cha wophunzira chidachuluka kwakukulutu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe lidamvera chikhulupirirocho. 8 Ndipo Stefano, wodzala ndi chikhu lupiriro ndi mphamvu, adachita zodabwitsa zazikulu ndi zozizwa pakati pa anthu. 9 Pamenepo adawuka ena a m’sunagoge wotchedwa wa Alibertino, ndi Akurenayo, ndi wa Alesandreyo, ndi mwa iwo a ku Kilikiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano. 10 Ndipo sadathe kuyitsutsa nzeru ndi Mzimu amene adayankhula naye. 11 Pamenepo iwo adanyengerera anthu amene adati, tidamumva iye alikunenera motsutsana ndi Mose ndi Mulungu mawu amwano. 12 Ndipo adawutsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu, 13 Nayimika mboni zonama, zonena. Munthu ameneyo saleka kunenera mwano malo ano woyera, ndiponso chilamulo; 14 Pakuti tidamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo adzawononga malo ano, nadzasintha miyambo imene Mose adatipatsa. 15 Ndipo adampenyetsetsa onse wokhala m’bwalo la akulu, nawona nkhope yake ngati kuti akuwona nkhope ya m’ngelo.

Ntchito 7

1 Ndipo mkulu wa nsembe adati, zitero zinthu izi kodi? 2 Ndipo iye adati, amuna inu abale, ndi atate, tamverani, Mulungu wa ulemerero adawonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m’Mesopotamiya, asadayambe kukhala m’Harana; 3 Ndipo adati kwa iye, Tuluka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe. 4 Pamenepo iye adatuluka m’dziko la Akaldayo namanga m’Harana; ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Iye adamsuntha alowe m’dziko lino, m’mene mukhalamo tsopano. 5 Ndipo sadampatsa cholowa chake m’menemo, ngakhale popondapo phazi lake iyayi; ndipo adamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale cholowa chake, ndi la mbewu yake yomtsatira, angakhale adalibe mwana pamenepo. 6 Koma Mulungu adalankhula chotero, kuti mbewu yake idzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choyipa, zaka mazana anayi. 7 Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzawuweruza Ine, adatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine pamalo pano. 8 Ndipo adampatsa iye pangano la mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isake adabala Yakobo, ndi Yakobo adabala makolo akulu aja khumi ndi awiri. 9 Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, adamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu adali naye, 10 Namlanditsa iye m’zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farawo mfumu ya ku Aigupto; ndipo adamuyika iye kazembe pa nyumba yake yonse. 11 Tsopano idadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi chisautso chachikulu; ndipo sadapeza chakudya makolo athu. 12 Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu mu Aigupto, adatuma makolo athu ulendo woyamba. 13 Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe adazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe lidazindikirika kwa Farawo. 14 Ndipo Yosefe adatumiza, nayitana Yakobo atate wake, ndi a pabanja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu. 15 Ndipo Yakobo adatsikira ku Aigupto; ndipo adamwalira, iye ndi makolo athu; 16 Ndipo adawanyamula kupita nawo ku Shekemu, nawayika m’manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Emori m’Shekemu. 17 Koma m’mene idayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo adakula nachuluka m’Aigupto, 18 Kufikira idawuka mfumu yina ya Aigupto imene siyidamdziwa Yosefe. 19 Imeneyo idachenjerera fuko lathu, niwachitira choyipa makolo athu, niwatayitsa tiana tawo, kuti tingakhale ndi moyo. 20 Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokongola ndithu; ndipo adamlera miyezi itatu m’nyumba ya atate ake; 21 Ndipo pakutayika iye, adamtola mwana wa mkazi wa Farawo, namlera akhale mwana wake. 22 Ndipo Mose adaphunzira nzeru zonse za a Aigupto; nakhala wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake. 23 Koma pamene zaka zake zidafikira ngati makumi anayi, kudalowa kumtima kwake kuzonda abale ake ana a Israyeli. 24 Ndipo powona wina woti alikumchitira choyipa, iye adamchinjiriza, nam’bwezera chilango wozunzayo, nakantha m’Aigupto. 25 Ndipo adayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sadazindikira. 26 Ndipo m’mawa mwake adawawonekera alikulimbana ndewu, ndipo adafuna kuti, awayanjanitsenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitira choyipa bwanji? 27 Koma iye wakumchitira mzake choyipa adamkankha, nati, Wakuyika iwe ndani mkulu ndi wotiweruza? 28 Kodi ufuna kundipha ine, monga muja udaphera m’Aigupto dzulo? 29 Ndipo Mose adathawa pa mawu awa, nakhala mlendo m’dziko la Midyani; kumeneko adabala ana amuna awiri. 30 Ndipo zitatha zaka makumi anayi, adamuwonekera m’ngelo m’chipululu cha Sina, m’lawi la moto wa chitsamba. 31 Koma Mose pakuwona adazizwa pachowonekachi; ndipo pakuyandikira iye kukawona, kudadza mawu wa Ambuye. 32 Akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose adanthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako. 33 Pamenepo Ambuye adati kwa iye, bvula nsapato zako ku mapazi ako; pakuti pa malo pamene uyimapo mpopatulika. 34 Kuwona ndawona kupsinjidwa kwa anthu anga ali m’Aigupto, ndipo ndamva kubuwula kwawo; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano tiye kuno, ndikutume ku Aigupto. 35 Mose uyu amene adamkana, ndi kuti, Wakuyika iwe ndani mkulu ndi wotiweruza? Ameneyo Mulungu adamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la m’ngelo womuwonekera pachitsamba. 36 Ameneyo adawatsogolera, natuluka nawo atachita zozizwa ndi zizindikiro m’Aigupto, ndi m’nyanja yofiyira, ndi m’chipululu zaka makumi anayi. 37 Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, Mulungu adzakuwukitsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine. Inu mudzamvere ameneyo. 38 Uyu ndiye amene adali mu Mpingo m’chipululu pamodzi ndi m’ngelo wakuyankhula naye m’phiri la Sinai, ndi makolo athu; amene adalandira maneno amoyo akutipatsa ife; 39 Amene makolo athu sadafuna kumvera iye, koma adamkankha achoke, nabwerera m’mbuyo mumtima mwawo ku Aigupto. 40 Nati kwa Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene adatitulutsa m’Aigupto, sitidziwa chomwe chamgwera. 41 Ndipo adapanga mwana wa ng’ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja awo. 42 Koma pamenepo Mulungu adatembenuka, nawapereka iwo apembedze gulu la Kumwamba; monga kwa lembedwa m’buku la aneneri, kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zake makumi anayi m’chipululu, nyumba ya Israyeli inu? 43 Ndipo mudatenga chihema cha Moloki, ndi nyenyezi ya Mulungu wanu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira izo; ndipo ndidzakutengani kumka nanu m’tsogolo mwake mwa Babulo. 44 Chihema cha umboni chidali ndi makolo athu m’chipululu, monga adalamula Iye wakuyankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiwona. 45 Chimenenso makolo athu akudza m’mbuyo adalowa nacho ndi Yoswa polandira iwo cholowa chawo cha kwa amitundu, amene Mulungu adawayingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide; 46 Amene adapeza chisomo pamaso pa Mulungu, nakhumba kupeza chihema cha Mulungu wa Yakobo. 47 Koma Solomo adam’mangira Iye nyumba. 48 Komatu Wam’mwamba-mwambayo sakhala m’kachisi womangidwa ndi manja; monga m’neneri anena, 49 Thambo la Kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga; mudzandimangira nyumba yotani? Ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi wotani? 50 Kodi silidapanga dzanja langa zinthu izi zonse? 51 Owuma makosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga adachita makolo anu, momwemo inu. 52 Ndiye yani wa aneneri amene makolo anu sadamzunza? Ndipo adawapha iwo amene adawonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha: 53 Inu amene mudalandira chilamulo monga chidayikidwa ndi m’ngelo, ndipo simudachisunga. 54 Koma pakumva zinthu izi adapsa mtima, adamkukutira iye mano awo. 55 Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, adapenyetsetsa Kumwamba, nawona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuyimilira padzanja lamanja la Mulungu. 56 Ndipo adati, Tawonani, ndipenya m’Mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu alikuyimilira pa dzanja la manja la Mulungu. 57 Pamenepo iwo adafuwula ndi mawu akulu, natseka m’makutu mwawo, namkhamukira iye ndi mtima umodzi, 58 Ndipo adamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zidayika zobvala zawo pa mapazi a m’nyamata dzina lake Saulo. 59 Ndipo adamponya miyala Stefano, alikuyitana Mulungu, ndi kunena Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga. 60 Ndipo m’mene adagwada pansi, adafuwula ndi mawu akulu, Ambuye, musawayikire iwo tchimo ili. Ndipo m’mene adanena ichi, adagona tulo.

Ntchito 8

1 Ndipo Saulo adalikubvomerezana nawo pa imfa yake. Ndipo panthawiyo kudayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo udali m’Yerusalemu; ndipo adabalalitsidwa onse m’mayiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ayi. 2 Ndipo adamuyika Stefano anthu wopembedza, namlira maliro akulu. 3 Ndipo Saulo adapasula Mpingo, nalowa m’nyumba iriyonse, nakokamo amuna ndi akazi, nawayika m’ndende. 4 Pamenepo iwo wobalalitsidwawo adapitapita nalalikira mawuwo. 5 Ndipo Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya nawalalikira Khristu kwa iwo. 6 Ndipo anthuwo ndi mtima umodzi adasamalira zinthu zonenedwa ndi Filipo, pamene adamva, napenya zozizwa zimene iye adazichita. 7 Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa idatuluka, yofuwula ndi mawu akulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi wopunduka, adachiritsidwa. 8 Ndipo padakhala chimwemwe chachikulu m’muzindamo. 9 Koma padali munthu wina dzina lake Simoni amene adachita matsenga m’mundzimo kale, nadabwitsa anthu a ku Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye adali munthu wamkulu: 10 Ameneyo adamsamalira onsewo, kuyambira wam’ng’ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa yayikulu. 11 Ndipo adamsamalira iye, popeza nthawi yayikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake. 12 Koma pamene adakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, adabatizidwa, amuna ndi akazi. 13 Ndipo Simoni mwini wake adakhulupiriranso; ndipo m’mene adabatizidwa, dakhara ndi Filipo; ndipo pakuwona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zirikuchitika, anadabwa. 14 Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu adamva kuti Samariya adalandira mawu a Mulungu, adawatumizira Petro ndi Yohane: 15 Amenewo, m’mene adatsikirako, adawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera; 16 (Pakuti kufikira pamenepo nkuti asadagwe pa wina m’modzi wa iwo; koma adangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.) 17 Pamenepo adayika manja pa iwo, ndipo adalandira Mzimu Woyera. 18 Koma pakuwona Simoni kuti mwa kuyika manja kwa atumwi adapatsidwa Mzimu Woyera, adawatengera ndalama. 19 Nanena, Ndipatseni inenso mphamvu yimeneyi, kuti amene aliyense ndikayika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera. 20 Koma Petro adati kwa iye, Ndalama yako iwonongeke nawe, chifukwa udalingilira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. 21 Ulibe gawo kapena cholandira ndi mawu awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu. 22 Chifukwa chake lapa choyipa chako ichi, pemphera kwa Mulungu, kuti kapena akukhululukire iwe cholingilira cha mtima wako. 23 Pakuti ndiwona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama. 24 Ndipo Simoni adayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi. 25 Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kuyankhula mawu a Ambuye, adabwerera kumka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino ku midzi yambiri ya Asamariya. 26 Koma m’ngelo wa Ambuye adayankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kumka ku Gaza; ndiyo ya chipululu. 27 Ndipo adanyamuka napita; ndipo tawona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yayikazi ya a Ethiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene adadza ku Yerusalemu kudzapembedza, 28 Ndipo iye adalimkubwerera, nalikukhala pa gareta wake, nawerenga m’neneri Yesaya. 29 Pamenepo Mzimu adati kwa Filipo, yandikira, nudziphatike ku gareta uyu. 30 Ndipo Filipo adamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya m’neneri, ndipo adati, Kodi muzindikira chimene muwerenga? 31 Ndipo iye adati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo adapempha Filipo akwere nakhale naye. 32 Koma palembo pamene adalikuwerengapo ndipo, Ngati nkhosa adatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga, kotero sadatsegula pakamwa pake; 33 M’kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chidachotsedwa; m’bado wake adzawubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake. 34 Ndipo mdindoyo adayankha Filipo, nati, Ndikupemphani m’neneri anena ichi za yani? Za yekha kapena za munthu wina? 35 Ndipo Filipo adatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu. 36 Ndipo monga adapita panjira pawo, adadza kumadzi ena; ndipo mdindoyo adati, Tawonapo pano pali madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe? 37 Ndipo Filipo adati, ngati ukhulupirira ndi mtima wako wonse; ukhoza kubatizidwa. Ndipo iye adayankha nati, Ndikhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu. 38 Ndipo adamuwuza kuti ayimitse gareta; ndipo adatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo adam’batiza iye. 39 Ndipo pamene adakwera kutuluka m’madzi, Mzimu wa Ambuye adakwatula Filipo; ndipo mdindoyo sadamuwonanso, pakuti adapita njira yake wokondwera. 40 Koma Filipo adapezedwa ku Azotu; ndipo popitapita adalalikira Uthenga Wabwino m’mizinda yonse, kufikira adadza iye ku Kayisareya.

Ntchito 9

1 Koma Saulo wosaleka kupumira pa akuphunzira wa Ambuye kuwopsa ndi kupha, adamka kwa mkulu a ansembe. 2 Napempha kwa iye akalata akumka nawo ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena wotsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nawo womangidwa ku Yerusalemu. 3 Ndipo poyenda ulendo wake, kudali kuti iye adayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuwunika kochokera kumwamba: 4 Ndipo adagwa pansi, namva mawu akunena naye, Saulo, Saulo, undinzunziranji Ine? 5 Koma iye adati, Ndinu yani Ambuye? Ndipo adati, Ndine Yesu amene umnzunza. Ndikobvuta kwa iwe kumenyana ndi zisonga zakuthwa kwambiri. 6 Ndipo iye adanthunthumira ndikudabwa nati, Ambuye, kodi mufuna kuti ine ndichite chiyani? Ndipo Ambuye adati kwa iye, Uka, nulowe m’mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita. 7 Ndipo amunawo akumperekeza iye adayima du, atamvadi mawu, koma osawona munthu. 8 Ndipo Saulo adawuka pansi; koma potseguka maso ake, sadapenya munthu aliyense; ndipo adamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m’Damasiko. 9 Ndipo adakhala masiku atatu wosawona, ndipo sadadya kapena kumwa. 10 Koma ku Damasiko kudali wophunzira wina dzina lake Hananiya; ndipo Ambuye adati kwa iye m’masomphenya, Hananiya. Ndipo adati, Ndiri pano, Ambuye. 11 Ndipo Ambuye adati kwa iye, Tawuka, pita kukhwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m’nyumba ya Yuda, ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso; pakuti tawona, alikupemphera, 12 Ndipo adawonam’masomphenya mwamuna dzina lake Hananiya, alikulowa, nayika manja ake pa iye, kuti apenyenso. 13 Ndipo Hananiya adayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti adachitiradi choyipa woyera mtima anu m’Yerusalemu. 14 Ndi kuti pano ali nawo ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuyitana pa dzina lanu. 15 Koma Ambuye adati kwa iye, Pita, pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa a mitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli. 16 Pakuti Ine ndidzamuwonetsa iye zinthu zazikulu zimene ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa. 17 Ndipo adachoka Hananiya, nalowa m’nyumbayo; ndipo adayika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene adakuwonekera pa njira wadzerayo, wandituma ine, kuti ulandire kuwona kwako ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera. 18 Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m’maso mwake ngati mamba, ndipo adapenyanso; nipo adawuka nabatizidwa. 19 Ndipo adalandira chakudya, nawona nacho mphamvu. Ndipo adakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena. 20 Ndipo pomwepo iye adalalikira Khristu m’masunagoge, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu. 21 Koma onse amene adamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene adawononga m’Yerusalemu onse akuyitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nawo womangidwa kwa ansembe akulu. 22 Koma Saulo adakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda wokhala m’Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndiye Khristu. 23 Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda adapangana kuti amuphe iye: 24 Koma chiwembu chawo chidadziwika ndi Saulo. Ndipo iwo anamdikiriranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe. 25 Koma wophunzira adamtenga iye usiku, namtsitsira pakhoma la linga, mumtanga. 26 Koma m’mene adafika ku Yerusalemu, adayesa kudziphatika kwa wophunzira; ndipo adamuwopa iye onse, osakhulupirira kuti iye adali wophunzira. 27 Koma Barnaba adamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adawonera Ambuye m’njira, ndi kuti adayankhula naye, ndi kuti m’Damasiko adalalikira molimbika mtima m’dzina la Yesu. 28 Ndipo iye adali nawo pamodzi iwo nalowa ndikutuluka ku Yerusalemu. 29 Ndipo iye adayankhula molimbika mtima m’dzina la Ambuye Yesu; ndipotu adayankhula natsutsana ndi Ahelene; koma adapita nafuna kuti amuphe iye. 30 Koma m’mene abale adachidziwa, adapita naye ku Kayisareya, namtumiza achoke kumka ku Tariso. 31 Pamenepo mipingo ya m’Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya idapumula nikhala yolimbikitsidwa ndi mtendere, nikhazikika; ndipo idayenda m’kuwopa kwa Ambuye ndi m’chitonthozo cha Mzimu Woyera, nichuluka. 32 Koma kudali, pakupita Petro ponseponse, adatsikiranso kwa woyera mtima akukhala ku Luda. 33 Ndipo adapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene adagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene adagwidwa manjenje. 34 Ndipo Petro adati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo adawuka pomwepo. 35 Ndipo adamuwona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa Ambuye amenewa. 36 Koma m’Yopa mudali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo adadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene adazichita. 37 Ndipo kudali m’masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye adamgoneka m’chipinda chapamwamba. 38 Ndipo popeza Luda ndi pafupi ndi Yopa, m’mene adamva wophunzirawo kuti Petro adali pomwepo, adamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwe mudze kwa ife. 39 Ndipo Petro adanyamuka, napita nawo. M’mene adafikako, adapita naye kuchipinda cha pamwamba; ndipo amasiye onse adayimilirapo pali iye, nalira, namuwonetsa malaya ndi zobvala zimene Dorika adasoka, pamene adali nawo pamodzi. 40 Koma Petro adawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo adati, Tabita, uka. Ndipo adatsegula maso ake; ndipo pakuwona Petro, adakhala tsonga. 41 Ndipo Petro adamgwira dzanja, nam’nyamutsa; ndipo m’mene adayitana woyera mtima ndi amasiye, adampereka iye wamoyo. 42 Ndipo kudadziwika ku Yopa konse; ndipo ambiri adakhulupirira Ambuye. 43 Ndipo kudali, kuti adakhala iye m’Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Ntchito 10

1 Ndipo kudali munthu ku Kayisareya, dzina lake Korneliyo, Kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya. 2 Ndiye munthu wopembedza, ndi wakuwopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene adapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kwambiri nthawi zonse. 3 Iye adapenya masomphenya poyera, m’ngelo wa Mulungu alimkudza kwa iye, ngati ola lachisanu ndi chinayi la usana, nanena naye, Korneliyo. 4 Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuwopa, adati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo adati kwa iye, mapemphero ako ndi zachifundo zako zidakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu. 5 Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, ayitane munthu Simoni, wotchedwanso Petro: 6 Iye adacherezedwa ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m’mbali mwa nyanja. Iye adzakuwuza iwe zoyenera kuchita. 7 Ndipo m’mene adachoka m’ngelo amene adayankhula ndi Korneliyo, adayitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene adamtumikira kosalekeza; 8 Ndipo m’mene adawafotokozera zonse, adawatuma ku Yopa. 9 Koma m’mawa mwake, pokhala pa ulendo pawo iwowa, m’mene adayandikira mudzi, Petro adakwera padenga kukapemphera, ngati pa ola lachisanu ndi chimodzi; 10 Ndipo adagwidwa njala, nafuna kudya. Koma m’mene adalikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka; 11 Ndipo adawona pathambo patatseguka, ndipo chotengera chirimkutsika, chonga ngati nsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinayi, ndi kutsikira padziko la pansi. 12 M’menemo mudali nyama za miyendo inayi za mitundu yonse, ndi zokwawa za pa dziko ndi mbalame za m’lengalenga. 13 Ndipo adamdzera mawu, Tawuka, Petro; ipha, nudye. 14 Koma Petro adati, iyayitu, Mbuye; pakuti sindidadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa. 15 Ndipo mawu adamdzeranso nthawi yachiwiri, chimene Mulungu adayeretsa, usachiyesa chinthu wamba. 16 Ndipo chidachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chidatengedwa kumka Kumwamba. 17 Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawawona akuti chiyani, tawonani, amuna aja wotumidwa ndi Korneliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, adayima pa chipata. 18 Ndipo adayitana nafunsa ngati Simoni wotchedwanso Petro, acherezedwako. 19 Ndipo m’mene Petro adalingilira za masomphenya, Mzimu adanena naye, Tawona, amuna atatu akufuna iwe. 20 Tawuka, nutsike, Ndipo upite nawo, wosakayika kayika; pakuti ndawatuma ndine. 21 Pamenepo Petro adatsikira kwa anthuwo amene adatumizidwa kwa iye ndi Korneliyo, nati, Tawonani, ine ndine mumfuna; chifukwa chake mwadzera chiyani? 22 Ndipo iwo adati, Korneliyo, munthu wolungama ndi wakuwopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, adachenjezedwa ndi Mulungu mwa m’ngelo woyera kuti atumize nakuyitaneni mumuke ku nyumba yake, ndi kumumvetsa mawu anu. 23 Pamenepo adawalowetsa nawachereza. Ndipo m’mawa mwake adanyamuka natuluka nawo, ndi ena wa abale a ku Yopa adamperekeza iye. 24 Ndipo m’mawa mwake atatha kulowa m’Kayisareya. Koma Korneliyo adalikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi abwenzi ake eni eni. 25 Ndipo padali m’mwawa mwake pakulowa Petro, Korneliyo adakomana naye, nagwa pamapazi ake, namlambira iye. 26 Koma Petro adamuwutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu. 27 Ndipo pakukamba naye, adalowa napeza ambiri atasonkhana; 28 Ndipo iye adati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu adandiwonetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa. 29 Chifukwa chakenso ndidadza wosakana, m’mene mudatuma kundiyitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiyitaniranji? 30 Ndipo Korneliyo adati, Atapita masiku anayi ndidali kusala chakudya kufikira ora iri, ndikupemphera m’nyumba yanga pa ola lachisanu ndi chinayi; ndipo tawonani, padayimilira pamaso panga munthu wobvala chobvala chonyezimira. 31 Ndipo adati, Korneliyo, lamveka pemphero lako, ndipo zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu. 32 Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akayitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m’nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, mbali mwa nyanja, ameneyo akadza adzayankhula ndi iwe. 33 Pamenepo ndidatumiza kwa inu wosachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake tawonani tiri tonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zinthu zonse Mulungu adakulamulirani. 34 Pamenepo Petro adatsegula pakamwa pake, nati, Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu pakati pa anthu: 35 Koma m’mitundu yonse, wakumuwopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye. 36 Mawu amene adatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse) 37 Mawuwo muwadziwa inu, adamvekawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane adawulalikira: 38 Za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene adapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse wosautsidwa ndi mdiyerekezi, pakuti Mulungu adali pamodzi ndi Iye. 39 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse adazichita m’dziko la Ayuda ndi m’Yerusalemu; amenenso adamupha, nampachika pamtengo. 40 Ameneyo, Mulungu adamuwukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti awonetsedwe poyera; 41 Si kwa anthu onse ayi, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atawuka iye kwa akufa. 42 Ndipo adatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti, uyu ndiye amene ayikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa. 43 Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti mwa dzina lake yense wokhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ake, mwadzina lakelo. 44 Pamene Petro adali chiyankhulire, Mzimu Woyera adagwa pa onse akumva mawuwo. 45 Ndipo iwo onse wokhulupirirawo akumdulidwe amene adadza ndi Petro anadadwa, chifukwa pa amitundunso padathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. 46 Pakuti adawamva iwo alikuyankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu pamenepo Petro adayankha, 47 Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? 48 Ndipo adalamulira iwo abatizidwe mdzina la Ambuye. Pamenepo adampempha iye atsotse masiku.

Ntchito 11

1 Koma atumwi ndi abale wokhala m’Yudeya adamva kuti amitundunso adalandira mawu a Mulungu. 2 Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo akumdulidwe adatsutsana naye, 3 Nanena kuti, Mudalowa kwa anthu wosadulidwa, ndi kudya nawo. 4 Koma Petro adayamba kuwafotokozera chilongosolere, kuyambira poyambirira pa nkhani nanena, 5 Ndidali ine muzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo mkukomoka ndidawona masomphenya, chotengera chirikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pa ngodya zake zinayi; ndi kutsika kumwamba, ndipo chidadza pa ine: 6 Chimenecho ndidachipenyetsetsa ndichilingilira, ndipo ndidawona nyama za miyendo inayi zapadziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za mlengalenga. 7 Ndipo ndidamvanso mawu akunena ndi ine, Tawuka Petro; ipha, nudye. 8 Koma ndinati, Iyayitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikadalowe m’kamwa mwanga ndi kale lonse. 9 Koma mawu adayankha nthawi yachiwiri wotuluka m’mwamba, chimene Mulungu adachiyeretsa, usachiyesa chinthu wamba. 10 Ndipo ichi chidachitika katatu; ndipo zidakwezekanso zonse kumwamba. 11 Ndipo tawonani, pomwepo amuna atatu adali atayima kale pa khomo la nyumba m’mene mudali ife, adatumidwa kwa ine wochokera ku Kayisareya. 12 Ndipo Mzimu adandiwuza ndinke nawo, wosakayika konse. Ndipo abale awa asanu ndi m’modzi adandiperekezanso adamuka nane; ndipo tidalowa m’nyumba ya munthuyo: 13 Ndipo adatiwuza ife kuti adawona m’ngelo atayimilira m’nyumba yake, ndikuti, Tumiza anthu ku Yopa, akayitane Simoni, wonenedwanso Petro; 14 Amene adzayankhula nawe mawu, amene udzapulumutsidwa nawo iwe ndi apabanja ako onse. 15 Ndipo m’mene ndidayamba kuyankhula, Mzimu Woyera adawagwera, monga adatero ndi ife poyamba paja, 16 Ndipo pamenepo ndidakumbukira mawu a Ambuye, kuti adanena, Yohane anabatizatu ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera. 17 Ngati tsono Mulungu adawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu? 18 Ndipo pamene adamva zinthu izi, adakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, potero Mulungu adapatsa kwa a mitundunso kutembenukira mtima kumoyo. 19 Tsopano iwotu, wobalalikawo chifukwa cha chinzunzocho chidadza pa Stefano, adafikira ku Foyinike, ndi Kupro, ndi Antiyokeya, wosayankhula mawu kwa wina yense koma kwa Ayuda wokha wokha. 20 Ndipo padali mwa iwo, amuna aku Kupro, ndi Kurena, amenewo, m’mene adafika ku Antiyokeya, adayankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira za Ambuye Yesu. 21 Ndipo dzanja la Ambuye lidali nawo; ndi chiwerengero chachikulu chidakhulupirira ndi kutembenukira kwa Ambuye. 22 Ndipo mbiri ya zinthu izi idamveka m’makutu a Mpingo wakukhala m’Yerusalemu; ndipo adatuma Barnaba apite kufikira ku Antiyokeya. 23 Ameneyo m’mene adafika, nawona chisomo cha Mulungu, adakondwera; ndipo adawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kumamatira kwa Ambuye. 24 Chifukwa adali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidawonjezeka kwa Ambuye. 25 Pamenepo Barnaba adatuluka kumka ku Tariso kukafunafuna Saulo: 26 Ndipo m’mene adampeza, adadza naye ku Antiyokeya. Ndipo kudali, kuti chaka chonse adasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo wophunzira adayamba kutchedwa Akhristu ku Antiyokeya. 27 Koma masiku awa aneneri adatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiyokeya. 28 Ndipo adayimirira m’modzi wa iwo, dzina lake Agabo, nalosera mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza m’masiku a Klaudiyo Kaisara. 29 Pamenepo wophunzira, yense monga adakhoza, adatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale wokhala m’Yudeya; 30 Ndipo adazichita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnaba ndi Saulo.

Ntchito 12

1 Tsopano pa nyengo imeneyo Herode mfumu adathira manja ena a mu Mpingo kuwachitira zoyipa. 2 Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane. 3 Ndipo pakuwona kuti kudakondweretsa Ayuda, adawonjezapo nagwiranso Petro. (Ndipo awo adali masiku a mkate wopanda chotupitsa). 4 Ndipo m’mene adamgwira, adamuyika m’ndende, nampereka kwa magulu anayi wa alonda, lonse anayi anayi, amdikire iye; ndipo adafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha. 5 Pamenepo ndipo Petro adasungika m’ndende; koma Mpingo udampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza. 6 Ndipo pamene Herode adati amtulutse, usiku womwewo Petro adalikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi unyolo uwiri; ndipo alonda wokhala pakhomo adadikira ndende. 7 Ndipo tawonani, m’ngelo wa Ambuye adayimilirapo, ndipo kuwunika kudawala mokhalamo iye; ndipo adakhoma Petro m’nthiti, namuwutsa iye, nanena, Tawuka msanga. Ndipo unyolo udagwa kuchoka m’manja mwake. 8 Ndipo m’ngelo adati, Dzimangire m’chuwuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo adanena naye, Funda chobvala chako nunditsate ine. 9 Ndipo adatuluka namtsata; ndipo sadadziwa kuti mchowona chochitidwa ndi m’ngelo, koma adayesa kuti alikuwona masomphenya. 10 Ndipo m’mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, adadza ku chitseko chachitsulo chakuyang’ana kumzinda; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo adatuluka, napitilira khwalala limodzi; ndipo pomwepo m’ngelo adamchokera. 11 Ndipo Petro atatsitsimuka adati, Tsopano ndidziwa zowona, kuti Ambuye adatuma m’ngelo wake nandilanditsa ine m’dzanja la Herode, ndi ku chilingiliro chonse cha anthu a chiyuda. 12 Ndipo m’mene adalingilirapo, adadza ku nyumba ya Mariya amake a Yohane wonenedwanso Marko; kumene ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo ankapemphera. 13 Ndipo pamene Petro adagogoda pa chitseko cha khomo, lidadza kudzabvomera buthu, dzina lake Roda. 14 Ndipo pamene adazindikira mawu ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sadatsegula pakhomo, koma adathamanga nalowanso, nawawuza kuti Petro alikuyima pakhomo. 15 Koma adati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo adalimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo adanena, ndiye m’ngelo wake. 16 Koma Petro adapitiriza kugogoda; ndipo m’mene adamtsegulira, adamuwona iye, nadabwa. 17 Koma m’mene adawatambasulira dzanja akhale chete, adawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m’ndende. Ndipo adati, Muwawuze Yakobo ndi abale izi. Ndipo adatuluka napita kwina. 18 Tsopano kutacha, padali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti. 19 Ndipo pamene Herode adamfunamfuna wosampeza, adafunsitsa wodikira nalamulira aphedwe. Ndipo adatsikira ku Yudeya kumka ku Kayisareya, nakhalabe kumeneko. 20 Ndipo Herode adayipidwa nawo a ku Turo ndi Sidoni; ndipo adamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m’mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, adapempha mtendere, popeza dziko lawo lidapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu. 21 Ndipo tsiku lopangira Herode adabvala zobvala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mawu a pabwalo. 22 Ndipo wosonkhanidwawo adafuwula, ndiwo mawu a Mulungu, si a munthu ayi. 23 Ndipo pomwepo m’ngelo wa Ambuye adamkantha, chifukwa sadampatsa Mulungu ulemerero; ndipo adadyedwa ndi mphutsi natsirizika. 24 Koma mawu a Mulungu adakula, nachuluka. 25 Ndipo Barnaba ndi Saulo adabwerera kuchokera ku Yerusalemu m’mene adatsiriza utumiki wawo natenga pamodzi nawo Yohane wonenedwanso Marko.

Ntchito 13

1 Ndipo kudali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiyokeya mu mpingo wa komweko, ndiwo Barnaba, ndi Simeoni, wonenedwa Nigeri, ndi Lukiya wa ku Kurene, Manayeni woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo. 2 Ndipo pakutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera adati, Mundipatulire Ine Barnaba ndi Saulo ku ntchito imene ndidawayitanira. 3 Ndipo pamene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuyika manja pa iwo, adawatumiza amuke. 4 Pamenepo iwo, wotumidwa ndi Mzimu Woyera, adatsikira ku Selukeya; ndipo pochokera kumeneko adapita m’chombo ku Kupro. 5 Ndipo pamene adakhala ku Salami, adalalikira m’masunagoge a Ayuda; ndipo adali nayenso Yohane monga wakuwathangatira iwo. 6 Ndipo m’mene adapitilira chisumbu chonse kufikira Pafo, adapezapo munthu, wamatsenga m’neneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Baryesu: 7 Ameneyo adali ndi kazembe Sergiyo Paulo, ndiye munthu wa nzeru. Yemweyo adayitana Barnaba ndi Saulo, nafunitsa kumva mawu a Mulungu. 8 Koma Elima watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) adawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe kuchikhulupiriro. 9 Koma Saulo, (ndiye Paulo) wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adampenyetsetsa iye, 10 Ndipo adati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuyipsa njira zolunjika za Ambuye? 11 Ndipo tsopano tawona, dzanja la Ambuye liri pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa ndi nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo adamukamuka nafuna wina womgwira dzanja. 12 Pamenepo kazembe pakuwona chochitikacho adakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye. 13 Tsopano pamene Paulo ndi gulu lake adamasuka kuchokera ku Pafo, iwo adafika ku Perge wa ku Pamfuliya; koma Yohane adapatukana nawo nabwerera kumka ku Yerusalemu. 14 Koma pamene iwowa adachoka ku Perge adafika ku Antiyokeya wa m’Pisidiya; ndipo adalowa m’sunagoge tsiku la sabata, nakhala pansi. 15 Ndipo m’mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge adatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nawo mawu akudandawulira anthu, nenani. 16 Ndipo Paulo adanyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israyeli, ndi inu akuwopa Mulungu, mverani. 17 Mulungu wa anthu awa Israyeli adasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m’dziko la Egupto, ndipo ndi dzanja lokwezeka adawatulutsa iwo m’menemo. 18 Ndipo monga nthawi ya zaka, makumi anayi adawalekerera m’chipululu. 19 Ndipo m’mene adawononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m’kanani, adawapatsa dziko cholowa pakuchita mayere. 20 Ndipo zitatha izi iye adawapatsa iwo, woweruza kwa zaka mazana anayi kudza makumi asanu, kufikira Samueli m’neneriyo. 21 Ndipo kuyambira pamenepo adapempha mfumu; ndipo Mulungu adawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, mpata wa zaka makumi anayi. 22 Ndipo m’mene adamchotsa iye, adawawutsira Davide akhale mfumu yawo; amenenso adamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse. 23 Wochokera mu mbewu yake ya munthu uyu, Mulungu, monga mwa lonjezano, adautsira Israyeli Mpulumutsi, Yesu. 24 Pamenepo Yohane adalalikira asadafike Iye, ubatizo wakulapa kwa anthu onse a Israyeli. 25 Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, adanena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma tawonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kumasura nsapato za kumapazi ake. 26 Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo a mwa inu akuwopa Mulungu, kwa inu atumidwa mawu a chipulumutso ichi. 27 Pakuti iwo akukhala m’Yerusalemu, ndi oweruza awo, popeza sadamzindikira Iye, ngakhale mawu a aneneri wowerengedwa masabata onse, adakwaniritsa pakumtsutsa Iye 28 Ndipo ngakhale kuti sadapeza chifukwa chakumuphera, adapempha Pilato kuti Iye aphedwe. 29 Ndipo atakwaniritsa zonse zolembedwa za Iye, adamtsitsa kumtengo, namuyika m’manda. 30 Koma Mulungu adamuwukitsa Iye kwa akufa. 31 Ndipo adawonekera masiku ambiri ndi iwo amene adamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu. 32 Ndipo ife tikulalikirani inu za Uthenga Wabwino wa lonjezano lochitidwa kwa makolo, 33 Kuti Mulungu wakwaniritsa ili kwa ana athu pakuwukitsa Yesu; monganso mulembedwa m’Salmo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala. 34 Ndipo monga ndi kunkhudzana ndikuti Iye adawukitsa Iye kwa akufa, wosabwereranso kuchibvundi, adateronso, ndidzakupatsani inu madalitso woyera ndi wotsimikizika a Davide. 35 Chifukwa anenanso m’Salmo lina, simudzapereka Woyera wanu awone chibvundi. 36 Pakutitu, Davide, m’mene adautumikira uphungu wa Mulungu mu m’bado mwake mwa iye yekha, adagona tulo, nayikidwa kwa makolo ake, nawona chibvundi: 37 Koma Iye amene Mulungu adamuwukitsanso sadawona chibvundi. 38 Chotero kudziwike kwa inu amuna ndi abale, kuti mwa munthu uyu, kulalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo: 39 Ndipo mwa Iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama kumchotsera zimene simudakatha kudzichotsera poyesedwa wolungana ndi chilamulo cha Mose. 40 Chifukwa chake chenierani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo; 41 Tawonani, inu wopeputsa, ndikuzizwa ndi kuwonongeka; kuti ine ndigwira, ntchito imene m’masiku anu, simudzayikhulupira wina ngakhale munthu wina adzakuwuzani. 42 Ndipo pamene Ayuda adatuluka m’sunagoge, amitundu adapempha kuti adzayankhule nawonso mawu awa Sabata likudzalo. 43 Ndipo m’mene anthu a m’sunagoge adabalalika, Ayuda ambiri ndi wopinduka wopembedza adatsata Paulo ndi Barnaba; amene poyankhula nawo, adawawumiriza akhale m’chisomo cha Mulungu. 44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mzinda wonse kudzamva mawu a Mulungu. 45 Koma Ayuda, pakuwona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zinthu zoyankhulidwa ndi Paulo, monga zosemphana komanso za mwano. 46 Ndipo Paulo ndi Barnaba adalimbika mtima ponena, nati, Kudafunika kuti mawu a Mulungu ayambe ayankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, tawonani, ife titembenukira kwa amitundu. 47 Pakuti kotero adatilamulira Ambuye ndi kuti, Ndakuyika iwe kuwunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero adziko lapansi. 48 Ndipo pakumva ichi amitundu adakondwera, nalemekeza mawu a Mulungu; ndipo onse amene adayikidwiratu ku moyo wosatha adakhulupirira. 49 Ndipo mawu a Ambuye anabukitsidwa m’dziko lonselo. 50 Koma Ayuda adautsa akazi wopembedza ndi wolemekezekeka, ndi zika zazikulu za muzindawo, nawawutsira chizunzo Paulo ndi Barnaba, ndipo adawapitikitsa iwo m’malire awo. 51 Koma iwo, adawasansira fumbi la kumapazi awo nadza ku Ikoniyo. 52 Ndipo akuphunzira adadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.

Ntchito 14

1 Ndipo kudali pa Ikoniyo kuti adalowa pamodzi m’sunagoge wa Ayuda, nayankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene lidakhulupirira. 2 Koma ayuda wosakhulupirira adawutsa mitima ya amitundu ndikupangitsa maganizo awo kuti achitire zoipa abale athu. 3 Chifukwa chake adakhala nthawi yayikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene adachitira umboni mawu a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja awo. 4 Ndipo khamu la mumzinda lidagawikana; ena adali ndi Ayuda koma ena adali ndi atumwi. 5 Ndipo pamene padakhala chigumukiro cha amitundu ndi cha ayuda ndi cha oweruza awo, kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala. 6 Iwo adamva, nathawira ku mizinda ya Lukawoniya, Lustra ndi Derbe, ndi dziko lozungulirapo. 7 Ndipo kumeneko adalalikira Uthenga Wabwino. 8 Ndipo pa Lustra padakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m’mapazi mwake, wopunduka chibadwire m’mimba ya amake, amene sadayendepo nthawi zonse: 9 Ameneyo adamva Paulo alimkuyankhula; ndipo Paulo pomyang’anitsitsa, ndi kuwona kuti adali ndi chikhulupiriro cholandira nacho machiritso, 10 Adati ndi mawu akulu, tayimilira. Ndipo iyeyu adazunzuka nayenda. 11 Ndipo pamene anthu adawona chimene adachita Paulo, adakweza mawu awo, nati m’chinenero cha Lukawoniya, Milungu yatsikira kwa ife yokhala monga anthu. 12 Ndipo adamutcha Barnaba, Jupitala; ndi Paulo, Merkasi, chifukwa adali wotsogola kunena. 13 Pamenepo wansembe wa Jupitala wokhala kumaso kwa mzinda, adadza nazo ng’ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi anthu. 14 Pamene adamva atumwi Paulo ndi Barnaba, adang’amba zofunda zawo, nathamangira m’kati mwa anthu nafuwula, 15 Nati, Anthunu, bwanji mukuchita zinthu zimenezi? Ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene adalenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo. 16 M’mibadwo yakale Iye adaleka mitundu yonse iyende m’njira zawo. 17 Koma sadadzisiyira Iye mwini wopanda mboni, popeza adachita zabwino, natipatsa ife zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yathu ndi chakudya ndi chikondwerero. 18 Ndipo pakunena zinthu izi, anthuwo adachita mantha naleka wosapereka nsembe kwa iwo. 19 Ndipo adafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiyokeya ndi Ikoniyo; nakopa anthu, ndipo adamponya Paulo miyala, namkokera kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa. 20 Koma pamene adamzinga akuphunzirawo, adawuka iye, nalowa m’mumzinda; m’mawa mwake adatuluka ndi Barnaba kumka ku Derbe. 21 Pamene atatha kulalikira Uthenga Wabwino pamzinda umenewo, ataphunzitsa ambiri, anabweranso ku Lustra ndi Ikoniyo ndi Antiyokeya. 22 Nalimbikitsa mitima ya wophunizra, nawadandawulira iwo kuti akhalebe m’chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri. 23 Ndipo pamene adawayikira akulu mosankha pa Mpingo uliwonse atatha kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, adayikiza iwo kwa Ambuye amene adamkhulupirirayo. 24 Ndipo adapitilira pa Pisidiya, nafika ku Pamfuliya. 25 Ndipo atalalikira mawu m’Perge, adatsikira ku Ataliya: 26 Komweko adachoka m’chombo kumka ku Antiyokeya, kumene adayikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adayimalizayo. 27 Pamene adafika nasonkhanitsa Mpingo adabwerezanso zomwe Mulungu adachita nawo, kuti adatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro. 28 Ndipo adakhala komweko ndi wophunzira nthawi yayitali.

Ntchito 15

1 Ndipo adadza ena wotsikira ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwa mwambo wa Mose, simungathe kupulumutsidwa. 2 Ndipo pamene Paulo ndi Barnaba adachitana nawo makani ndi mafunsano, abale adapatula Paulo ndi Barnaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kumka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo. 3 Ndipo iwo adaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Foyinika ndi Samariya, nawafotokozera za kutembenuka mtima kwa amitundu; anakondweretsa kwambiri abale onse. 4 Pamene adafika ku Yerusalemu, adalandiridwa ndi mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo adawafotokozeranso zonse zimene Mulungu adachita nawo. 5 Koma adawuka ena a mpatuko wa Afarisi wokhulupirira, nati, kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwawuza kuti asunge chilamulo cha Mose. 6 Ndipo adasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo. 7 Ndipo pamene padali mafunsano ambiri, Petro adayimilira, nati, kwa iwo, amuna inu, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu adasankha mwa inu, kuti m’kamwa mwanga amitundu amve mawu a Uthenga Wabwino nakhulupirire. 8 Ndipo Mulungu amene adziwa mitima, adawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga adatipatsa ife; 9 Ndipo sadalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yawo m’chikhulupiriro. 10 Nanga bwanji tsopano muli kumuyesa Mulungu, kuti muyike pa khosi la wophunzira goli, limene sadatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife? 11 Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe. 12 Ndipo khamu lonse lidatonthola; ndipo adamvera Barnaba ndi Paulo akuwafotokozeranso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu adachita nawo pa amitundu. 13 Ndipo pamene iwo adatonthola Yakobo adayankha, nati, Abale, Mverani ine: 14 Simoni wafotokoza kuti poyamba Mulungu adayang’anira a mitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake. 15 Ndipo zinthu izi zigwirizana ndi mawu a aneneri; monga kudalembedwa. 16 Zikadzatha izi, ndidzabwera, ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chidagwa; ndidzamanganso zopasula zake, ndipo ndidzachiyimikanso: 17 Kuti anthu wotsalira afunefune Ambuye, ndi amitundu onse amene dzina langa lidatchulidwa pa iwo, ati Ambuye amene achita zinthu zonse. 18 Chodziwika kwa Mulungu ndi ntchito zake zonse kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi. 19 Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisabvute a mwa amitundu amene adatembenukira kwa Mulungu: 20 Koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi chiwerewere, ndi zopotola, ndi mwazi. 21 Pakuti Mose, kuyambira nthawi yakale ali nawo m’mizinda yonse iwo amene amlalikira iye, akuwerenga mawu ake m’masunagoge masabata onse. 22 Pamenepo chidakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse yense kusankha anthu a m’gulu lawo, ndi kuwatumiza ku Antiyokeya ndi Paulo ndi Barnaba; ndiwo Yuda wotchedwa Barnaba, ndi Sila, akulu a mwa abale; 23 Ndipo iwo adalemba makalata natumiza kwa iwo mmalembedwe wotere, Atumwi ndi akulu ndi abale atumiza moni kwa abale a mwa amitundu a mu Antiyokeya, ndi Suriya, ndi Kilikiya. 24 Popeza tamva kuti ena amene adatuluka mwa ife adakubvutani ndi mawu, nasocheretsa mitima yanu; amene adanena nanu kuti muyenera kuti mudulidwe ndi kusunga chilamulo, amenewo ife sitinawatume: 25 Chidatikomera ife ndi mtima umodzi, kusankha anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi wokondedwa athu Barnaba ndi Paulo. 26 Amuna amene adapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu. 27 Tatumiza tsono Yuda ndi Sila, omwenso adzakuwuzani ndi mawu zinthu zomwezo. 28 Pakuti chidakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; 29 Kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi chiwerewere; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino. 30 Tsono pamene iwo adamuka adatsikira ku Antiyokeya; ndipo adasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo. 31 Imene pamene adayiwerenga, adakondwera chifukwa cha kusangalatsa chake. 32 Ndipo Yuda ndi Sila, wokhala eni wokha aneneri, anadandaulira abale ndi mawu ambiri, nawalimbikitsa iwo. 33 Ndipo pamene iwo adakhala nthawi, abale adalawirana nawo ndi mtendere amuke kwa iwo amene adawatumiza. 34 Komabe zidasangalatsa Sila kuti akhalebe komweko. 35 Koma Paulo ndi Barnaba adakhalabe m’Antiyokeya, akuphunzitsa, ndi kulalikira mawu a Ambuye pamodzi ndi ena ambirinso. 36 Patapita masiku, Paulo adati kwa Barnaba, Tibwererenso, tizonde abale m’mizinda yonse m’mene tidalalikiramo mawu a Ambuye, tiwone mkhalidwe wawo. 37 Ndipo Barnaba adafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko. 38 Koma sikudamkomera Paulo kumtenga iye amene adawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nawo ku ntchito. 39 Ndipo padali kupsetsana mtima, kotero kuti adalekana wina ndi mzake; ndipo Barnaba adatenga Marko nalowa m’chombo, namka ku Kupro. 40 Koma Paulo adasankha Sila namuka, woyamikiridwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye. 41 Ndipo iye adapita kupyola pa Suriya ndi Kilikiya, natsimikizira Mipingo.

Ntchito 16

1 Ndipo adafikanso ku Derbe ndi Lustra: ndipo tawonani, padali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mhelene: 2 Ameneyo adamchitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo. 3 Iyeyo Paulo adafuna kuti amuke naye, ndipo adamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene adakhala m’mayikomo; pakuti onse adadziwa kuti atate wake adali Mhelene. 4 Pamene adapita kupyola pamizinda, adapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene adalamulira atumwi ndi akulu wokhala mu Yerusalemu. 5 Kotero mipingoyo idakhazikika m’chikhulupiriro, ndipo inachuluka m’chiwerengero chake tsiku ndi tsiku. 6 Ndipo pamene iwo adapita kupyola pa dziko la Frugiya ndi dera la Galatiya, pamenepo adaletsedwa ndi Mzimu Woyera kuti asalalikire mawu m’Asiya; 7 Adayesa atafika ku Musiya, kumka ku Bituniya; koma Mzimu sadawaloleze. 8 Ndipo iwo podutsa pa Musiya, adatsikira ku Trowa. 9 Ndipo masomphenya adawonekera kwa Paulo usiku; padali munthu wa ku Makedoniya alimkuyimilira, namdandaulira kuti, muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithandize ife. 10 Ndipo atawona masomphenya, pomwepo adayesa kutulukira kumka ku Makedoniya, potsimikizira kuti Mulungu adayitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo. 11 Chotero tidachokera ku Trowa m’chombo, m’mene tidalunjikitsa ku Samotrake, ndipo m’mawa mwake ku Neapoli; 12 Pochokera kumeneko tidafika ku Filipi, mzinda wa ku Makedoniya, waukulu wa m’dzikomo, wa milaga ya Aroma; ndipo tidakhala mumzindawo masiku ena. 13 Ndipo pa tsiku la sabata tidatuluka kumzinda kumka ku mbali ya mtsinje, kumene tidaganizira kuti amapempherako; ndipo tidakhala pansi ndi kuyankhula ndi akazi amene adasonkhana. 14 Ndipo adatimva mkazi wina dzina lake Lidiya, wogulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiyatira, amene adapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye adatsegula, kuti amvere zimene adazinena Paulo. 15 Ndipo pamene adabatizidwa iye ndi a pabanja pake adatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m’nyumba yanga, mugone m’menemo. Ndipo adatiwumiliza ife. 16 Ndipo panali, pamene tidalikupita kukapemphera, adakomana ndi ife namwali wina amene adali ndi mzimu wambwembwe, amene adapindulira ambuye ake zambiri pa kubwebweta pake. 17 Ameneyo adatsata Paulo ndi ife, nafuwula, kuti, Anthu awa ndi atumiki a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso. 18 Ndipo adachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo adabvutika mtima ndithu, nachewuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m’dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo udatuluka nthawi yomweyo: 19 Koma pamene Ambuye ake adawona kuti kulingalira kwa kupindula kwawo kwatha, adagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kumalo a msika kubwalo la woweluza. 20 Ndipo adamka nawo kwa woweruza, nati; Anthu awa wokhala Ayuda abvutitsa kwambiri mzinda wathu, 21 Ndipo aphunzitsa miyambo imene siyiloleka ife kuyilandira, kapena kuyichita, chifukwa ndife Aroma. 22 Ndipo lidagumukira iwo khamulo; ndipo woweruza adawang’ambira malaya awo; nalamulira kuti awakwapule. 23 Ndipo pamene adawawonetsa mikwingwirima yambiri, adawayika m’ndende, nawuza mdindo kuti awasunge bwino. 24 Pakumva iye kulamulira kotero adawayika m’chipinda cha m’kati, namangitsa mapazi awo m’zigologolo. 25 Ndipo pakati pa usiku, Paulo ndi Sila adalimkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m’ndendemo adalimkuwamva. 26 Ndipo mwadzidzidzi padali chibvomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende adagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse padatseguka; ndi unyolo wonse udamasuka. 27 Ndipo pamene adadzuka kutulo mdindoyo, adawona kuti pa makomo a ndende padatseguka, ndipo adasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am’ndende adathawa. 28 Koma Paulo adafuwula ndi mawu akulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tiri muno. 29 Ndipo mdindo adayitanitsa nyali, natumphira mkati, alimkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Sila, 30 Ndipo adawatulutsa iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke? 31 Ndipo iwo adati; khulupirira pa Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi apabanja ako. 32 Ndipo adayankhula naye mawu a Ambuye, pamodzi ndi onse a mnyumba mwake. 33 Ndipo adawatenga ola lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yawo; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a mnyumba mwake. 34 Ndipo pamene iye adawatenga iwo kulowa nawo kunyumba kwake, anawakhazikira chakudya,anasangalala kwambiri, pamodzi ndi a panyumba yake yonse pokhulupirira Mulungu. 35 Ndipo pamene kudacha, woweruza adatumiza asilikali, kuti Mukamasule anthu aja adzipita. 36 Ndipo mdindo wa ndende adawafotokozera mawuwo kwa Paulo, nati, Woweruza atumiza mawu kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere. 37 Koma Paulo adati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tiri Aroma, natiyika m’ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m’seri? Iyayi, ndithu; koma adze wokha atitulutse. 38 Ndipo asilikaliwo adafotokozera mawuwo kwa woweruza; ndipo iwowo adawopa, pakumva kuti adali Aroma. 39 Ndipo adadza nawapembedza; ndipo pamene adawatulutsa, adawapempha kuti achoke muzinda wawo. 40 Ndipo adatuluka m’ndendemo, nalowa m’nyumba ya Lidiya: ndipo pamene adawona abale, adawatonthoza iwo ndipo adachoka.

Ntchito 17

1 Tsopano pamene adapitilira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, adafika ku Tesalonika, kumene kudali sunagoge wa Ayuda. 2 Ndipo Paulo, monga amachita, adalowa kwa iwo; ndipo masabata atatu adanena ndi iwo za m’malembo, natanthauzira, 3 Natsimikiza, kuti kudayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuwuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu. 4 Ndipo ena a iwo adakhulupirira, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akulu osati wowerengeka. 5 Koma Ayuda amene sadakhulupirire anadukidwa mtima, natenga anthu ena woyipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso mzinda wonse; ndipo adagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu. 6 Ndipo pamene sadawapeza adakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa oweruza a muzinda, nafuwula kuti, omwe aja amene anatembenuza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso; 7 Amene Yasoni wawalandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kayisala; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu. 8 Ndipo iwo adabvuta anthu, ndi oweruza a muzinda, pamene adamva zinthu zimenezi. 9 Ndipo pamene adalandira chikole kwa Yasoni ndi enawo adawamasula. 10 Pomwepo abale adatumiza Paulo ndi Sila usiku kumka ku Bereya; pamene iwo adafika komweko adalowa m’sunagoge wa Ayuda. 11 Amenewa adali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza adalandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zidali zotero. 12 Ndipo ambiri a iwo adakhulupirira; ndi akazi a chihelene wolemekezeka ndi amuna, osati wowerengeka. 13 Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika adazindikira kuti mawu a Mulungu adalalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, adadza komwekonso, nawutsa, kubvuta anthu. 14 Pomwepo abale adatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Sila ndi Timoteo adakhalabe komweko. 15 Koma iwo amene adaperekeza Paulo adadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Sila ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, adachoka. 16 Tsopano pamene Paulo adalindira iwo pa Atene, adabvutidwa mtima pamene adawona mudzi wonse wadzala ndi mafano. 17 Chotero tsono adatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m’sunagoge, ndi m’bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene adakomana nawo. 18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoyiki adatengana naye. Ena adati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa adalalikira Yesu ndi kuwuka kwa akufa. 19 Ndipo adamgwira, namka naye ku Arewopagi, nati, kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi cha tsopano uchinena iwe? 20 Pakuti ufika nazo ku makutu athu zinthu za chilendo; tifuna tsono kudziwa, zinthu izi ndizotani? 21 (Pakuti Aatene onse ndi alendo akukhalamo amataya nthawi yawo, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva zinthu zatsopano.) 22 Ndipo Paulo adayimilira pakati pa phiri la Masi nati, Amuna inu a Atene, mzinthu zonse ndiwona kuti muli wopembedzetsa. 23 Pakuti popita, ndi kuwona zinthu zimene muzipemphedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa motere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA.chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu. 24 Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja. 25 Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; 26 Ndipo ndiye m’modzi adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo. 27 Kuti afunefune Ambuye, kapena akamfufuze ndi kumpeza Iye,ngakhale kuti Iye sakhala patali ndi yense wa ife; 28 Pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a kuyimba anu ati, pakuti ifenso tiri mbadwa zake. 29 Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu sitiyenera kulingalira kuti Umulungu uli wofanafana ndi golidi, kapena Siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu. 30 Ndipo nthawi za kusadziwako tsono Mulungu adalekerera; koma tsopanotu alimkulamulira anthu onse ponse ponse alape. 31 Chifukwa adapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene adamuyikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene adamuwukitsa Iye kwa akufa. 32 Ndipo pamene adamva za kuwuka kwa akufa ena adaseka pwepwete; koma ena adati, Tidzakumvanso iwe za nkhani iyi. 33 Choncho Paulo adachoka pakati pawo. 34 Koma ena adadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso mudali Diyonisiyo M-arewopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nawo.

Ntchito 18

1 Zitapita zinthu izi, Paulo adachoka ku atene, nadza ku Korinto; 2 Ndipo adapeza Myuda wina dzina lake Akula, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Priskila, (chifukwa cha Klaudiyo adalamulira Ayuda onse achoke m’Roma;) ndipo Paulo adadza kwa iwo; 3 Ndipo popeza adali wa ntchito imodzimodzi, adakhala nawo, ndipo iwowa adagwira ntchito; pakuti ntchito yawo idali yosoka mahema. 4 Ndipo adafotokozera m’sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene. 5 Koma pamene Sila ndi Timoteo adadza potsika ku Makedoniya, Paulo adapsinjidwa mu mzimu, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. 6 Koma pamene iwo adamkana, nachita mwano, adakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe nanu chifukwa; kuyambira tsopano ndimka kwa amitundu. 7 Ndipo adachoka kumeneko, nalowa m’nyumba ya munthu wina, dzina lake Tito Yustro, amene adapembedza Mulungu, nyumba yake idayandikizana ndi sunagoge. 8 Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, adakhulupirira pa Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri adamva, nakhulupirira, nabatizidwa. 9 Ndipo Ambuye adati kwa Paulo usiku m’masomphenya, Usawope, koma yankhula, usakhale chete: 10 Chifukwa Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuyipse; chifukwa ndiri ndi anthu ambiri muzinda uno. 11 Ndipo adakhala komweko chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mawu a Mulungu mwa iwo. 12 Tsono pamene Galiyo adali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi adamuwukira Paulo, namka naye ku mpando wachiweruziro. 13 Nanena, uyu akopa anthu apembedze Mulungu mosemphana ndi chilamulo. 14 Koma Paulo pamene adati atsegule pakamwa pake, Galiyo adati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loyipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu; 15 Koma akakhala mafunso a mawu ndi mayina ndi chilamulo chanu; muyang’ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi. 16 Ndipo adawapitikitsa pa mpando wa chiweruziro. 17 Ndipo ahelene onse adagwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda iye kumpando wa chiweruziro. Ndipo Galiyo sadasamalira zimenezi. 18 Ndipo Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, adatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m’chombo ku Suriya, pamodzi naye Priskila ndi Akula; popeza adameta mutu wake m’Kokreya; pakuti adawinda. 19 Ndipo iye adafika ku Aefeso, ndipo iye adalekana nawo pamenepo: koma iye yekha adalowa m’sunagoge, natsutsana ndi Ayuda. 20 Ndipo pamene iwo adamfunsa iye kuti akhale nthawi yina yowonjezerapo sadawabvomereza; 21 Ndipo adawatsazika, nati, ndiyenera ine mwanjira iriyonse kusunga mphwando iri limene likudza ku Yerusalemu: koma ndidzabweranso kwa inu ngati akalola Mulungu. Ndipo adayenda pamadzi kuchoka ku Aefeso. 22 Ndipo pamene adakocheza pa Kayisareya, adakwera nalankhula ndi mpingo, natsikira ku Antiyokeya. 23 Ndipo atakhala kumeneko nthawi, adachoka, napita pa dziko lonse la Galatiya ndi Frugiya ndicholinga, cholimbikitsa akuphunzitsa onse. 24 Ndipo adafika ku Aefeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Alesandreya, munthu woyankhula mwanzeru; ndipo adali wamphamvu m’malembo. 25 Munthu ameneyu adalangizidwa m’njira ya Ambuye; pokhala nawo mzimu wachangu, adanena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Ambuye, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha. 26 Ndipo iye adayamba kuyankhula molimba mtima m’sunagoge, koma pamene adamumva iye Priskila ndi Akula, adamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa. 27 Ndipo pamene iye adafuna kuwoloka kumka ku Akaya, abale adamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa akuphunzira kuti amlandire: ndipo pamene adafika, iye adathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo; 28 Pakuti ndi mphamvu adakopa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.

Ntchito 19

1 Ndipo patapita nthawi, pamene Apolo adali ku Korinto, Paulo anadutsa kupyola magombe amumtunda nafika ku Aefeso: ndipo adapeza wophunzira ena; 2 Iye adati kwa iwo, kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira? Ndipo iwo adati iyayi, sitidamva konse kuti kudzakhalanso Mzimu Woyera. 3 Ndipo iye adati, Nanga munabatizidwa ndi chiyani? Ndipo adati, Mu ubatizo wa Yohane. 4 Pamenepo adati Paulo, Yohane indetu anabatiza ndi ubatizo wa kulapa, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Khristu Yesu. 5 Ndipo pamene adamva ichi, adabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu. 6 Ndipo pamene Paulo adayika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera adadza pa iwo; ndipo adayankhula ndi malilime ndi kunenera. 7 Ndipo amuna onse adalipo ngati khumi ndi awiri. 8 Ndipo iye adalowa m’sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu. 9 Koma pamene ena adawumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoyipa Njirayo pamaso pa khamu, adawachokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m’sukulu ya Turano. 10 Ndipo adachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse wokhala m’Asiya adamva mawu a Ambuye Yesu, Ayuda ndi Ahelene onse. 11 Ndipo Mulungu adachita zozizwitsa zapaderadera ndi manja a Paulo: 12 Kotero kuti adamuka nazo kwa wodwala msalu zopukutira ndi za pa ntchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zidawachokera, ndi mizimu yoyipa idatuluka. 13 Koma Ayuda enanso woyendayenda, wotulutsa ziwanda, adadziyesera wokha kutchula pa iwo amene adali ndi mizimu yoyipa dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo. 14 Ndipo padali ana a amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkulu wa ansembe amene adachita chotero. 15 Ndipo udayankha mzimu woyipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu yani? 16 Ndipo munthu, mwa iye amene mudali mzimu woyipa, adawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti adathawa m’nyumba amaliseche ndiwobvulazidwa. 17 Ndipo zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene adakhala ku Aefeso; ndipo mantha adagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu lidakuzika. 18 Ndipo ambiri a iwo wokhulupirirawo adadza, nabvomereza, nawonetsa ntchito zawo. 19 Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga adasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa anthu onse; ndipo adawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu. 20 Chotero mawu a Ambuye adakula mwamphamvu nalakika. 21 Ndipo zitatha zinthu izi, Paulo adatsimikiza mu mzimu wake, atapita kupyola pa Makedoniya ndi Akaya, kumka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuwonanso ku Roma. 22 Pamenepo adatuma ku Makedoniya awiri a iwo adamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini adakhalabe nthawi m’Asiya. 23 Nthawi yomweyo kudali phokoso lambiri lakunena za Njirayo. 24 Pakuti munthu wina dzina lake Demetriyo wosula siliva, amene adapanga tiakachisi tasiliva ta Diyana, adawonetsera amisili phindu lambiri; 25 Amenewo iye adawasonkhanitsa pamodzi ndi amisili a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife timapeza chuma chathu. 26 Ndipo muwona ndi kumva, kuti si pa Aefeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, aulo uyu akopa ndi kutembenuza anthu ambiri, ndi kuti, Sindiyo milungu iyi imene ipangidwa ndi manja; 27 Sikuti ndi ntchito yathu yokhayi imene iri pachiwopsezo ndi kunyonyosoka; komanso kuti kachisi wa mulungu wathu wamkazi Diyana adzayamba kunyozedwa; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m’Asiya onse, ndi onse a m’dziko lokhalamo anthu, ampembedza. 28 Ndipo pamene adamva zonenazi, adadzala ndi mkwiyo, nafuwula, nati, Wamkulu ndi Diyana wa ku Aefeso. 29 Ndipo muzinda monse mudadzaza ndi chisokonezeko, ndipo adagwira Gayondi Arstarko, amuna Akumakedoniya, anzake a Paulo woyenda nawo, nathamanga iwo onse ndi mtima umodzi kunka kubwalo la masewera. 30 Ndipo pamene Paulo adafuna kulowa kwa anthu, akuphunzira ake sadamloleza. 31 Ndipo akulu ena a m’Asiyanso, popeza adali abwenzi ake, adatumiza mawu kwa iye, namupempha kuti asadziponye yekha ku bwalo lamasewera. 32 Ndipo ena adafuwula za chinthu china, ndi enanso chinthu china; ndikuti mnsonkhano wonse udasokonezeka; ndipo unyinji sudadziwa chifukwa chake cha chimene adasonkhanira. 33 Ndipo adatuluka Alesandro m’khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro adatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo. 34 Koma pozindikira kuti ali Myuda, kudali mawu amodzi a kwa onse akufuwula monga maola awiri, Wamkulu ndi Diyana wa Aefeso. 35 Ndipo pamene mlembi wa mzinda adatontholetsa anthuwo, adati, Amuna a Aefeso inu, munthu uyu ndindani wosadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wopembedza Mulungu wamkazi wamkulu Diyana, ndi fano limene lidagwa pansi kuchokera ku Jupita? 36 Powona pamenepo kuti zinthu izi. Sizingalankhulidwe mozitsutsa, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu mothamanga. 37 Pakuti mwatenga anthu awa, wosakhala wolanda za m’kachisi, kapena wochitira Mulungu wanu wamkazi mwano. 38 Ngati tsono Demetriyo ndi amisili wokhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; asiyeni adandaulirane wina ndi mzake. 39 Koma ngati mufuna kanthu kazinthu zina, kadzaganiziridwa pa m’sonkhano wina wolamulidwa. 40 Pakuti mpotiwopsa kuti tachita chipolowe lero; popanda chifukwa chake chachipolowechi. 41 Ndipo pamene adanena izi, anabalalitsa msonkhanowo.

Ntchito 20

1 Ndipo litaleka phokoso, Paulo adayitana wophunzirawo, ndipo m’mene adawakupatira, adalawirana nawo, natuluka kumka ku Makedoniya. 2 Ndipo m’mene adapitapita m’mbali zijazo, nawadandaulira, adadza ku Girisi. 3 Ndipo adakhalako miyezi itatu, ndipo kumeneko Ayuda adapangira chiwembu, pomudikirira pamene iye ankati apite mchombo ku Suriya, naganizira zobwerera kudzera ku Makedoniya. 4 Ndipo adamperekeza kufikira ku Asiya Sopatro mwana wa Puro, wa ku Bereya; ndi Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Derbe, ndi Timoteo; ndi aku Asiya, Tukiko ndi Trofimo. 5 Koma iwowa anatitsogolera, natiyembekezera ife pa Trowa. 6 Ndipo tidapita m’chombo kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tidawapeza ku Trowa; pamenepo tidatsotsa masiku asanu ndi awiri. 7 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana akuphunzira kunyema mkate, Paulo adalalikira kwa iwo, popeza adati achoka m’mawa mwake; ndipo adanena chinenere kufikira pakati pa usiku. 8 Ndipo mudali nyali zambiri m’chipinda cha pamwamba m’mene adasonkhanamo pamodzi. 9 Ndipo pamenepo pazenera padali m’nyamata wina dzina lake Utiko adakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo iyeyu, adagwa posanja pachiwiri, ndipo adamtola wakufa. 10 Ndipo potsikirako Paulo, adamgwera iye namfungatira, nati Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo. 11 Ndipo m’mene adakweranso, nanyema mkate, nadya, nakamba nawo nthawi, kufikira kucha, adachoka. 12 Ndipo adadza naye m’nyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu. 13 Ndipo ife tidatsogolera kumka ku mchombo, ndipo tidapita ku Aso, pamenepo tidati timtenge Paulo; pakuti adatipangira chomwecho, koma adati ayenda pamtunda yekha. 14 Ndipo pamene adakomana ndi ife ku Aso, tidamtenga, ndipo tidafika ku Mitilene. 15 Ndipo m’mene tidachokerapo, m’mawa mwake tidafika pandunji pa Kiyo; ndipo m’mawa mwake tidafika ku Samo, ndipo tidakhala pa Trogiliamu; ndi m’mawa mwake tidafika ku Mileto. 16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima kudzera ku Aefeso, chifukwa sadafune kuti ataye nthawi m’Asiya; chifukwa adafulumira iye, kuti ngati mkotheka, akakhale ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste. 17 Ndipo pokhala ku Mileto adatuma ku Aefeso, nayitana akulu a Mpingo. 18 Ndipo pamene adafika kuli iye, adati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndidafika ku Asiya, ndi makhalidwe wotani amene ndinakhala pamodzi ndi inu nthawi zonse, 19 Wotumikira Ambuye ndi mtima wodzichepetsa ndi misozi, ndi mayesero adandigwera ndi ziwembu za Ayuda. 20 Kuti sindidakubisirani zinthu zopindulitsa kwa inu, koma ndakuwonetserani, ndi kuphunzitsa inu pabwalo, ndi kuchokera nyumba ndi nyumba, 21 Kuchitira umboni pamodzi kwa Ayuda ndi Ahelene wakulapa kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro chakulinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 22 Ndipo tsopano, tawonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zinthu zimene zidzandigwera ine kumeneko. 23 Koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m’mizinda yonse, ndi kunena kuti msinga ndi zisautso zindilindira. 24 Komatu palibe chimodzi cha zinthu izi chingathe kundisuntha ine, sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi chimwemwe, ndi utumiki umene ndidaulandira kwa Ambuye Yesu, kukachitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu. 25 Ndipo tsopano, tawonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndidapitapita mwa inu kulalikira za ufumuwo, wa Mulungu simudzawonanso nkhope yanga. 26 Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndiribe chifukwa ndi mwazi wa munthu aliyense. 27 Pakuti sindidakubisirani pa kukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu. 28 Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera adakuyikani woyang’anira, kuti mudyetse Mpingo wa Mulungu, umene adaugula ndi mwazi wa Iye yekha. 29 Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, idzalowa mimbulu yolusa, yosalekerera gululo. 30 Ndipo mwa inu nokha adzawuka anthu, woyankhula zokhotakhota, kupatutsa wophunzira awatsate. 31 Chifukwa chake chenjerani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindidaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi. 32 Ndipo tsopano, abale, ndikuyikizani kwa Mulungu, ndi kwa mawu a chisomo chake, chimene chiri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse woyeretsedwa. 33 Sindidasilira siliva, kapena golidi, kapena chobvala cha munthu ali yense. 34 Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa adatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine. 35 M’zinthu zonse ndidakupatsani chitsanzo, chakuti pogwira ntchito, kotero muyenera kuthandiza wofowoka ndi kukumbukira mawu wa Ambuye Yesu, kuti adati yekha, kupatsa kutidalitsa koposa kulandira. 36 Ndipo m’mene adanena izi, iye adagwada pansi, napemphera ndi iwo onse. 37 Ndipo onsewa adalira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona. 38 Nalira makamaka chifukwa cha mawu adanenawa, kuti sadzawonanso nkhope yake. Ndipo adamperekeza iye kuchombo.

Ntchito 21

1 Ndipo kudali, titalekana nawo ndi kukankha chombo, tinadza molunjika ku Kowo, ndi m’mawa mwake ku Rode, ndipo pochokera ku Patara: 2 Ndipo m’mene tidapeza chombo chakuwoloka kumka ku Foyinike, tidalowamo, ndi kupita nacho. 3 Tsopano pamene tidafika popenyana ndi Kupro, tidamsiya kudzanja lamanzere, ndipo tidapita ku Suriya; ndipo tidakocheza ku Turo; pakuti pamenepo chombo chidafuna kutula akatundu wake. 4 Ndipo m’mene tidapeza wophunzira, tidakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa adanena ndi Paulo mwa Mzimu kuti asakwera kunka ku Yerusalemu. 5 Ndipo kudali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kumka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, adatiperekeza kufikira kutuluka mumzinda; ndipo pogwadwa pa m’chenga wa kunyanja, tidapemphera. 6 Ndipo pamene tidalawirana wina ndi mzake tidalowa m’chombo, koma iwo adabwerera kwawo. 7 Ndipo pamene tidatsiriza ulendo wathu wochokera ku Turo, tidafika ku Ptolemayi; ndipo m’mene tidayankhula abale, tidakhala nawo tsiku limodzi. 8 Ndipo m’mawa mwake ife amene tidali amgulu lake la Paulo, tidachoka, ndipo tidafika ku Kayisareya, ndipo m’mene tidalowa m’nyumba ya Filipo mlaliki, m’modzi wa asanu ndi awiri aja, tidakhala naye. 9 Ndipo munthuyu adali nawo ana akazi anayi, anamwali, amene adanenera. 10 Ndipo pokhalapo masiku ambiri, adatsika ku Yudeya m’neneri dzina lake Agabo. 11 Ndipo adadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, munthu mwini lamba ili, adzam’manga kotero Ayuda a m’Yerusalemu, nadzampereka m’manja a amitundu. 12 Koma pamene tidamva zinthu izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko kuti asakwere iye kumka ku Yeursalemu. 13 Pamenepo Paulo adayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine sikumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu. 14 Ndipo pokana iye kukopeka, tidamleka, ndi kumalizira kunena kuti, kufuna kwa Ambuye kuchitidwe. 15 Ndipo atapita masiku awa tidakonza akatundu athu, ndikukwera ku Yerusalemu. 16 Ndipo adamuka nafenso ena a wophunzira a ku Kayisareya, natenganso wina Nasoni wa ku Kupro, wophunzira wakale, amene adzatichereza. 17 Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale adatilandira mokondwera. 18 Ndipo m’mawa mwake Paulo adalowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse adali pomwepo. 19 Ndipo atawayankhula iwo, adawafotokozera chimodzi chimodzi zinthu zimene Mulungu adachita kwa amitundu mwa utumiki wake. 20 Ndipo pamene adazimva, izi adalemekeza Mulungu; nati, kwa iye, Uwona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirire; ndipo ali nacho changu onsewa cha pa chilamulo: 21 Ndipo iwo adamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana awo, kapena asayende monga mwa miyambo. 22 Chingachitike ndi chiyani tsono? Khamu lidzafuna kudza pamodzi: pakuti Adzamva kuti iwe wafika. 23 Chifukwa chake uchite ichi tikuwuza iwe; tiri nawo amuna anayi amene adachita chowinda; 24 Amenewa uwatenge nudziyeretse nawo pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, ndipo usunga chilamulo. 25 Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tidalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi chiwerewere. 26 Pamenepo Paulo adatenga anthuwo, ndipo m’mawa mwake m’mene adadziyeretsa nawo pamodzi, adalowa m’Kachisi, kukatsimikizira za chimarizidwe cha masiku a kuyeretsedwa, kufikira kuti nsembe yiperekedwe ya aliyense wa iwo. 27 Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri adati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuwona iye m’kachisi, adawutsa anthu, namgwira, 28 Nafuwula, Amuna a Israyeli, tithandizeni, ameneyu ndi munthu uja adaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso adatenga Ahelene nalowa nawo m’Kachisi, nadetsa malo ano woyera. 29 (Pakuti adawona Trofimo wa ku Aefeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo adayesa kuti Paulo adamtenga nalowa naye m’Kachisi). 30 Ndipo mzinda wonse udasokonezeka, ndipo anthu adathamanga pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa m’Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo padatsekedwa. 31 Ndipo m’mene adafuna kumupha iye, wina adamuwuza kapitawo wamkulu wa gululo kuti m’Yerusalemu monse muli chisokonezo. 32 Ndipo pamenepo iye adatenga asilikali ndi a Kenturiyonso, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuwona kapitawo wamkulu ndi asilikali, adaleka kumpanda Paulo. 33 Pamenepo poyandikira kapitawo wamkulu adamgwira iye, nalamulira am’mange ndi unyolo uwiri; ndipo adamfunsa kuti ndi yani uyu ndipo wachita chiyani? 34 Koma wina adafuwula chinthu china, wina china, m’khamulo; ndipo m’mene sadathe kudziwa zowona chifukwa cha phokoso adalamulira amuke naye kulinga. 35 Ndipo pamene adafika pamakwerero, kudatero kuti adamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa anthu. 36 Pakuti khamu la anthu lidatsata, ndikufuwula, Mchotseni iye. 37 Ndipo poti alowe naye m’linga, Paulo adanena kwa kapitawo wamkulu, mundilole ndi kuwuzeni kanthu? Ndipo adati, kodi udziwa chihelene? 38 Si ndiwe Mu Aigupto uja kodi, udachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinayi kuchipululu? 39 Koma Paulo adati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa mzinda wa Kilikiya, mfulu ya mzinda womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndiyankhule ndi anthu. 40 Ndipo m’mene adamlola, Paulo adayimilira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, adayankhula nawo m’chinenedwe cha Chihebri, nanena,

Ntchito 22

1 Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu. 2 (Ndipo pakumva kuti adayankhula nawo m’chinenedwe cha Chihebri, adaposa kukhala chete; ndipo adati,) 3 Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m’Tariso mzinda wa Kilikiya, koma ndaleredwa mu mzinda muno, pa mapazi a Gamaliyeli; wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndidali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero. 4 Ndipo ndidanzunza Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi. 5 Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu: kwa iwo amenenso ndidalandira akalata kumka nawo kwa abale, ndipo ndidapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nawo womangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe. 6 Ndipo kudali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kudandiwalira pondizungulira ine kuwunika kwakukulu kuchokera kumwamba. 7 Ndipo ndidagwa pansi, ndipo ndidamva mawu akunena nane, Saulo, Saulo, undinzunziranji Ine? 8 Ndipo ndidayankha, Ndinu yani Ambuye? Ndipo adati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete amene umzunza. 9 Ndipo iwo wokhala nane adawonadi kuwunika, ndipo adachita mantha; koma sadamva mawu akuyankhula nane. 10 Ndipo ndidati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye adati kwa ine, Tawuka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zinthu zonse zoyikika kwa iwe uzichite. 11 Ndipo popeza sindidapenya, chifukwa cha ulemerero wa kuwunikako, adandigwira dzanja iwo amene adali ndi ine, ndipo ndidafika ku Damasiko. 12 Ndipo munthu dzina lake Hananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene am’chitira umboni wabwino Ayuda onse akukhala kumeneko. 13 Adadza kwa ine, ndipo poyimilirapo adati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ola lomwelo ndidapenya. 14 Ndipo adati, Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake, nuwone Wolungamayo, numve mawu wotuluka m’kamwa mwake. 15 Ndipo udzakhara mboni yake kwa anthu onse, za zimene udaziwona ndi kuzimva. 16 Ndipo tsopano uchedweranji? Tawuka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuyitane pa dzina la Ambuye. 17 Ndipo kudali, nditabwera ku Yerusalemu ndidalikupemphera m’kachisi, ndidachita ngati kukomoka; 18 Ndipo ndidamuwona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga m’Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wonena za Ine. 19 Ndipo ndidati ine, Ambuye, adziwa iwo wokha kuti ndidali kuyika m’ndende ndi kuwapanda m’masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu: 20 Ndipo pamene adakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndine ndidalikuyimirirako, ndi kubvomerezana nawo, ndi kusunga zobvala za iwo amene adamupha iye. 21 Ndipo adati kwa ine,nyamuka; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kumka kutali kwa amitundu. 22 Ndipo adamumva kufikira mawu awa; ndipo adakweza mawu awo nanena, Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo. 23 Ndipo pofuwula iwo, ndi kutaya zobvala zawo, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga, 24 Kapitawo wamkulu adalamulira kulowa naye kunyumba ya kulinga; nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake chiyani kuti amfuwulira chomwecho. 25 Ndipo m’mene adam’manga iye ndi msingazo, Paulo adati kwa Kenturiyo wakuyimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, wosalakwa? 26 Ndipo pamene adamva ichi Kenturiyo, adamka kwa kapitawo wamkulu, namuwuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyu ndi Mroma. 27 Ndipo kapitawo wa mkuluyo adadza, nati kwa iye, ndiwuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo adati, Inde. 28 Ndipo kapitawo wa mkulu adayankha, Ine ndalandira ufulu ndi mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo adati; ine ndinabadwa Mroma. 29 Pamenepo iwo amene adati amfunsefunse, adamsiya: ndipo kapitawo wamkulunso adawopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adam’manga iye. 30 Koma m’mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti adam’nenera Ayuda, adam’masula iye, nalamulira asonkhane ansembe akulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo adatsika naye Paulo, namuyika pamso pawo.

Ntchito 23

1 Ndipo Paulo popenyetsetsa a m’bwalo la akulu adati, Amuna, abale ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbu mtima chokoma chonse kufikira lero lomwe. 2 Ndipo mkulu wa ansembe Hananiya adalamulira akuyimirirako ampande pakamwa pake. 3 Pamenepo Paulo adati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe: ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza ine monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine mosemphana ndi chilamulo? 4 Ndipo iwo akuyimirirako adati, ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu? 5 Ndipo Paulo adati, sindidadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wansembe; pakuti kwalembedwa, usamnenera choyipa oweruza wa anthu ako. 6 Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena, Afarisi, adafuwula m’bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuwuka kwa akufa. 7 Ndipo pamene adatero, kudakhala malekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo khamulo lidagawikana. 8 Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuwuka kwa akufa, kapena m’ngelo, kapena mzimu; koma Afarisi abvomereza zonse ziwiri. 9 Ndipo chidawuka chipolowe chachikulu; ndipo alembi ena a kwa Afarisi adayimilira, natsutsana, nanena, sitipeza choyipa chiri chonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena m’ngelo wayankhula naye; sitiyenera kulimbana ndi Mulungu. 10 Ndipo pamene padawuka chipolowe chachikulu, kapitawo wamkulu adawopa kuti angamkhadzule Paulo, ndipo adalamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pawo, nadze naye kulowa naye mnyumba ya m’linga. 11 Ndipo usiku wake Ambuye adayimirira pa iye, nati, khala wokondwa; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma. 12 Ndipo kutacha, Ayuda adapangana za chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo. 13 Ndipo iwo amene adachita chilumbiro ichi adali woposa makumi anayi. 14 Ndipo iwo adadza kwa ansembe akulu ndi kwa akulu nati tadzimanga tokha ndi temberero lalikulu kuti sitidzadya kapena kumwa kanthu kufikira titamupha Paulo. 15 Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu muzindikiritse kapitawo wamkulu kuti atsike naye kwa inu, mawa monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asadayandikire iye. 16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo adamva za chiwembu chawo, ndipo anadza nalowa m’linga, namfotokozera Paulo. 17 Ndipo Paulo adadziyitanira Kenturiyo wina, nati, Pita naye m’nyamata uyu kwa kapitawo wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokonzera iye. 18 Pamenepo adamtenga, napita naye kwa kapitawo wamkulu, nati, Wamsinga Paulo adandiyitana, nandipempha ndidze naye m’nyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakuyankhula ndi inu. 19 Ndipo kapitawo wamkulu adamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m’seri, chiyani ichi uli nacho kundifotokozera? 20 Ndipo adati, Ayuda adapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa ku bwalo la milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye. 21 Koma musakopedwe nawo: pakuti amlalira iye woposa makumi anayi a iwo amene adadzitemberera wokha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekera tsopano nayang’anira lonjezano lanu. 22 Pamenepo kapitawo wamkulu adamuwuza m’nyamatayo apite, namlamulira kuti asawuze munthu ali yense kuti wandizindikiritsa zinthu izi. 23 Ndipo adayitana a Kenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira ku Kayisareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ola lachitatu la usiku. 24 Ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felike kazembeyo. 25 Ndipo adalembera kalata m’malembedwe wotere: 26 Klawudiya Lusiya kwa kazembe womveketsa Felike, ndikuyankhulani. 27 Munthu uyu adagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndidafikako ine ndi asilikali, ndipo ndidamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma. 28 Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa cha kuti adamnenera iye, ndidatsikira naye ku bwalo la akulu awo: 29 Ndipo ndidapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chawo; koma adalibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena kumangigwa. 30 Ndipo m’mene adandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndidamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera amnenere kwa inu.Tsalani bwino. 31 Ndipo pamenepo asilikali, monga adawalamulira, adatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri. 32 Koma m’mawa mwake adasiya apakavalo amperekeze, nabwera kunyumba ya kulinga: 33 Iwowo, m’mene adafika ku Kayisareya, adapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye. 34 Ndipo m’mene adawerenga adafunsa achokera m’dera liti; ndipo pozindikira kuti adali wa ku Kilikiya; 35 Ndidzamva mlandu wake adatero, pamene akukunenera afika. Ndipo adalamulira kuti amdikire iye m’nyumba yoweruzira mlandu ya Herode.

Ntchito 24

1 Ndipo atapita masiku asanu adatsika mkulu wa ansembe Hananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo adafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo. 2 Ndipo pamene adamuyitana, Tertulo adayamba kumnenera ndi kunena, popeza tiri nawo mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muwukonzera mtundu wathu zabwino. 3 Tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felike womveka inu. 4 Koma kuti ndingawonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu. 5 Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woyambitsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mapanduko wa Anazarene: 6 Amenenso adayesa kuyipsa kachisi; amene tamgwira ndipo ayenera kuweruzidwa molingana ndi chilamulo chathu. 7 Koma kapitawo wamkulu Lusiya adafika kwa ife ndipo ndi chisokonezo chachikulu adamtenga iye m’manja athu. 8 Nalamulira womnenera ake kuti adze kwa inu; kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za zinthu izi zonse timnenerazi. 9 Ndipo Ayudanso adabvomerezana naye, natsimikiza kuti zinthu izi zidali chomwecho. 10 Ndipo pamene kazembe adamkodola kuti anene, Paulo adayankha, podziwa inu kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera: 11 Popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri wokha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira. 12 Ndipo sadandipeza m’kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuwutsa khamu la anthu, kapena m’sunagoge kapena mu mzinda: 13 Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano. 14 Koma ichi ndibvomera kwa inu kuti monga mwa njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse ziri monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri: 15 kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo wokhanso achilandira, kuti kudzakhala kuwuka kwa wolungama ndi wosalungama. 16 M’menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu. 17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndidadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka. 18 Popeza izi adandipeza woyeretsedwa m’kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma padali Ayuda ena a ku Asiya. 19 Ndipo kukadakhala bwino atakhala pano pamaso panu ndi kunenera ngati ali nako kanthu kotsutsa ine. 20 Kapena iwo amene ali kunowa anene ngati adapeza chosalungama chirichonse, poyimirira ine pamaso pa bwalo la akulu, 21 Koma mawu awa amodzi wokha, amene ndidafuwula poyimilira pakati pawo, kunena za kuwuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino. 22 Ndipo pamene Felike adamva zinthu izi, pokhala nacho chidziwitso chonse cha Njirayo, iye adawachedwetsa nati, pamene Lusiya kapitawo wamkulu akadzatsika ndidzazindikira momveka za nkhani yanu. 23 Ndipo adalamulira Kenturiyo ansunge Paulo, ndipo akhale nawo ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira. 24 Koma atapita masiku ena, adadza Felike ndi Drusila mkazi wake, ndiye Myuda, nayitana Paulo, ndipo adamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu. 25 Ndipo m’mene adamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chirimkudza, Felike adagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikawona nthawi, ndidzakuyitana iwe. 26 Adayembekezanso kuti Paulo adzampatsa iye ndalama kuti mwina amasule iye; chifukwa chakenso adamuyitana iye kawiri kawiri, nakamba naye. 27 Koma zitapita zaka ziwiri Porkiyo Festo adalowa m’malo a Felike; ndipo Felike pofuna kuti Ayuda amkonde adamsiya Paulo mndende,

Ntchito 25

1 Tsopano pamene Festasi adalowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, adakwera kumka ku Yerusalemu kuchokera ku Kayisareya. 2 Pamenepo wamkulu wa ansembe ndi wakulu wa Ayuda, adamuuza iye za Paulo ndikumpempha iye, 3 Nampempha kukonderedwa kuti amtumize iye adze ku Yerusalemu; iwo atamchitira chifwamba kuti amuphe panjira. 4 Koma Festasi adayankha, kuti Paulo asungike ku Kayisareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa. 5 Chifukwa chake, anati kwa iwo kuti, amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo kuti ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo am’nenera iye. 6 Ndipo m’mene adatsotsa kwa iwo masiku woposera khumi wokha adatsikira ku Kayisareya; ndipo m’mawa mwake adakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti amtenge Paulo. 7 Ndipo m’mene adafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu adayimilira pomzinga iye, nam’nenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sadakhoza kuzitsimikizira. 8 Koma Paulo podzikanira adanena, Sindidachimwa kanthu kapena kamchilamulo, kapena kamkachisi, kapena Kayisala. 9 Koma Festasi pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, adayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kumka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine komweko kunena za zinthu izi. 10 Koma Paulo adati, Ndiri kuyimirira pa mpando wa chiweruziro cha Kayisala, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindiwachitira kanthu koyipa, monga nokha mudziwa bwino. 11 Pamenepo ngati ndiri wochita zoyipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zachabe, palibe m’modzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kayisala. 12 Pamenepo Festasi atakamba ndi aphungu ake, adayankha, Wanena, nditulukira kwa Kayisala; kwa Kayisala udzapita. 13 Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bernike adafika kuKayisareya, kudzamuyankhula Festasi. 14 Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festasi adafotokozera mfumuyo mlandu wake wa Paulo, nanena, pali munthu adamsiya m’ndende Felike: 15 Amene ansembe akulu ndi akulu wa Ayuda adamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha kuti ndiyipse mlandu wake. 16 Koma ndidawayankha, kuti machitidwe wa Aroma satero, kupereka munthu asadayambe woneneredwayo kupenyana nawo womnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho. 17 Potero pamene adasonkhana pano, sindidachedwa, koma m’mawa mwake ndidakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndidalamulira adze naye munthuyo. 18 Ndipo pamene adayimirira womneneza, sadamtchulira konse chifukwa cha zoyipa zonga ndizilingilira ine: 19 Koma adali nawo mafunso ena wotsutsana naye a chipembedzo cha iwo wokha, ndi mafunso a za wina Yesu, amene adafa, za amene Paulo adati kuti ali ndi moyo. 20 Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndidamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za nkhani iyi. 21 Koma Paulo pakunena kuti asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndidaweruza kuti asungidwe iye kufikira ndidzamtumiza kwa Kayisala. 22 Ndipo Agripa adati kwa Festasi, Ndifuna nanenso ndimve ndekha munthuyo. Adati, Mawa mudzamva iye. 23 M’mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Bernike ndi chimwambo chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitawo akulu, ndi amuna womveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Festasi, adadza naye Paulo. 24 Ndipo Festasi adati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muwona munthu uyu amene unyinji wonse wa Ayuda adandiwuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuwula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo. 25 Koma ndidapeza ine kuti sadachita kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha adati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako. 26 Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti ndikatha kumfunsafunsa ndikhale nako kanthu kolemba. 27 Pakuti chiwoneka kwa ine chopanda nzeru, potumiza wamsinga, posatchulanso zifukwa za mlandu wake.

Ntchito 26

1 Ndipo Agripa adati kwa Paulo, kwaloledwa udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, adatambasula dzanja nadzikanira: 2 Ndidziyesera wamwayi, mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo: 3 Makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima. 4 Mayendedwe amoyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene adakhala chiyambire mwa mtundu wanga m’Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse; 5 Andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndidakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzo chathu. 6 Ndipo tsopano ndiyimilira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu adalichita kwa makolo athu: 7 Mwalonjezano limene mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, adayembekezera chiyembekezo chimene chikudza, ndipo Chifukwa cha chiyembekezo chimenecho, Mfumu, Agripa, ndi zomwe nditsutsidwa ndi Ayuda. 8 Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu awukitsa akufa? 9 Indetu, ndi ine ndekha, kuti ndikhala ngati kuti ndichita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu m’nazarayo. 10 Chimenenso ndidachita m’Yerusalemu: ndipo ndidatsekera ine woyera mtima ambiri m’ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndidabvomerezapo. 11 Ndipo ndidawalanga kawirikawiri m’masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndikuwanzunza ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku mizinda yakunja. 12 M’menenso popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe akulu kuli masana. 13 Ndidawona panjira, Mfumu, kuwunika kuchokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa,kudawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza. 14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndidamva mawu akunena kwa ine m’chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undinzunziranji Ine? Mkobvuta kwa iwe kumenyana ndi zisonga zakuthwa kwambiri. 15 Ndipo ndidati, ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye adati, Ine ndine Yesu amene iwe umnzunza. 16 Komatu uka, yimilira pamapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndidawonekera iwe, kukuyika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya zinthu izi zidzakuwonekera iwe;ndi zinthu zina zimene ndidzakuwonetsa iwe. 17 Ndi kukulanditsa iwe kwa anthu, ndi kwa a mitundu, amene ndikutuma kwa iwo. 18 Kukawatsegulira maso awo, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuwunika, ndi kuchokera ku ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo a kuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine. 19 Potero, Mfumu Agripa, sindidakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba. 20 Komatu kuyambira kwa iwo a m’Damasiko, ndi a m’Yerusalemu, ndi m’dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndidalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima. 21 Chifukwa cha izi Ayuda adandigwira m’Kachisi, nayesa kundipha. 22 Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiyimilira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang’ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzafika: 23 Kuti Khristu amve zowawa, kuti Iye, akhale woyamba wa akuwuka kwa akufa, awonetsere kuwunika kwa anthu ndi kwa amitundu. 24 Koma pakudzikanira mwiniyekha momwemo, Festasi adati ndi mawu akulu, Uli ndi misala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala. 25 Koma Paulo adati, Ndiribe misala, Festasi womvekatu; koma nditulutsa mawu achowonadi ndi umunthu weni weni.. 26 Pakuti mfumuyo idziwa zinthu izi, kwa iye amene ndiyankhula nayenso mosawopa; pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadam’bisikira; pakuti ichi sichidachitika m’seri. 27 Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ndidziwa mumawakhulupirira. 28 Ndipo Agripa adati kwa Paulo, Iwetu uli pafupi kundikopa kuti ndikhale Mkhristu. 29 Ndipo Paulo adati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang’ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero wonga ndiri ine kupatulapo kumangidwaku.. 30 Ndipo pamene iye adanena izi, mfumu ndi kazembe ndi Bernike, ndi iwo akukhala nawo adanyamuka: 31 Ndipo atapita padera adayankhula wina ndi mzake, nanena, Munthu uyu sadachita kanthu koyenera imfa, kapena kumangidwa. 32 Pamenepo Agripa adati kwa Festasi, Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukire kwa Kayisala.

Ntchito 27

1 Ndipo pamene padatsimikiza kuti tipite m’chombo kumka ku Italiya, adapereka Paulo ndi andende ena kwa Kenturiyo dzina lake Yuliyo, wa gulu la Augusto. 2 Ndipo m’mene tidalowa m’chombo cha ku Adramatiyo chikati chipite kumka ku malo a ku mbali ya Asiya, tidayenda, ndipo Aristarko M’makedoniya wa ku Tesalonika, adali nafe. 3 Ndipo m’mawa mwake tidangokocheza ku Sidoni; ndipo Yuliyo adachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze. 4 Ndipo pochokanso pamenepo, tidapita kutseri kwa Kupro, popeza mphepo idawomba mokomana nafe. 5 Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Kilikiya ndi Pamfuliya, tidafika ku Mura mzinda wa Lukiya. 6 Ndipo pamenepo Kenturiyo adapezako chombo cha ku Alesandriya, chilikupita ku Italiya, ndipo tidakweramo. 7 Ndipo m’mene tidapita pang’onopang’ono masiku ambiri,ndi kufika mobvutika pandunji pa Knido, ndipo popeza siyidatilolanso mphepo, tidapita mtseri mwa Krete, pandunji pa Salimone. 8 Ndipo popazapaza mobvutika, tidafika ku malo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo padali mzinda wa Laseya. 9 Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo udayamba kukhala wowopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo adawachenjeza iwo. 10 Nanena kwa iwo, Amuna inu, ndiwona ine kuti ulendo udzatitengera kuwonongeka ndi kutayika kwambiri, sikwa akatundu wokha kapena chombo chokha, komatunso kwa miyoyo yathu. 11 Koma Kenturiyo adakhulupirira wa chiwongolero ndi mwini chombo makamaka, wosasamala mawu a Paulo. 12 Ndipo popeza dowoko silidakoma kugonapo nyengo yachisanu, unyinji udachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Foyinika, ndi kugonako, ndilo dowoko la ku Krete, loloza kumpoto ndikumwera. 13 Ndipo powomba pang’ono mwera, poyesa kuti adachita chifuniro, adakoka nangula, napita m’mbali mwa Krete. 14 Koma patapita pang’ono idawombetsa kuchokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo. 15 Ndipo pogwidwa nacho chombo, chosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tidangotengedwa. 16 Ndipo popita kuseri kwa chisumbu chaching’ono dzina lake Kauda, tidali ndi ntchito yambiri kuti tibwere kuchombo koma mobvutika: 17 Ndipo m’mene adawukweza, adachita nazo zothandizira, nakulunga chombo; ndipo pakuwopa kuti angatayike pa Surti, adatsitsa. mathanga, natengedwa motero. 18 Ndipo mobvutika kwakukulu ndi namondweyo, m’mawa mwake adayamba kutaya akatundu; 19 Ndipo tsiku lachitatu adataya ndi manja awo a iwo eni zipangizo za mchombo. 20 Ndipo m’mene dzuwa kapena nyenyezi sizidatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng’ono adatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuka chidatichokera pomwepo. 21 Ndipo pamene atakhala nthawi yayikulu wosadya kanthu, Paulo adayimilira pakati pawo, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, sitikadadzitengera kuwonongeka ndi kutayika kotereku. 22 Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo m’modzi mwa inu, koma chombo ndicho. 23 Pakuti adayimilira kwa ine usiku walero m’ngelo wa Mulungu amene ndiri wake, amenenso ndimtumikira. 24 Nanena, Usawope Paulo; ukayimilira pamaso pa Kayisala, ndipo tawona, Mulungu adakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi. 25 Chifukwa chake, amuna inu, limbikani mtima; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe adanena ndi ine. 26 Koma tiyenera kuponyedwa pa chisumbu china chake. 27 Koma pofika usiku wakhumi ndi chinayi, potengedwa ife kwina ndi kwina m’nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amalinyero adazindikira kuti adalikuyandikira pafupi ndi dziko lina: 28 Ndipo adayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri, ndipo katapita kanthawi , adayesanso napeza mikwamba khumi ndi isanu. 29 Ndipo pakuwopa tingatayike pamiyala, adaponya anangula anayi kumakhaliro, nakhumba kuti kuche. 30 Ndipo m’mene amalinyero adafuna kuthawa m’chombo, natsitsira bwato m’nyanja, monga ngati adati aponye anangula kulikulu, 31 Paulo adati kwa Kenturiyo ndi kwa asilikali, ngati awa sakhala m’chombo inu simukhoza kupulumuka. 32 Pamenepo asilikali adadula zingwe za bwato, nalisiya kuti ligwe. 33 Ndipo popeza kudalikucha, Paulo adawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinayi limene mudalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu. 34 Chomwecho ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; kuti mukhale ndi thanzi: pakuti sadzatayika m’modzi wa inu. 35 Ndipo atanena izi, adatenga mkate, nayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m’mene adaunyema adayamba kudya. 36 Ndipo adakhala wolimba mtima onse, ndipo sadatenga chakudya china . 37 Ndipo ife tonse tiri m’chombo ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi m’modzi. 38 Ndipo m’mene adakhuta, adapepuza chombo, nataya tirigu m’nyanja. 39 Ndipo kutacha sadazindikira dzikolo; koma adawona pali bondo la m’chenga; kumeneko adafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako chombo. 40 Ndipo m’mene adataya anangula adawasiya m’nyanja, namasulanso zingwe zomanga chiwongolero; ndipo pokweza thanga la kumutu, pamenepo analunjikitsa kum’chenga. 41 Koma adakwama pamalo pamene padakumana nyanja ziwiri, ndipo chombo chidatsamitsidwapo ndipo kulikulu kwa chombo, kudakhala kosasunthika, koma kumakhaliro kudasweka ndi mphamvu ya mafunde. 42 Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa. 43 Koma Kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, adawaletsa angachite cha uphungu wawo; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m’nyanja, nafike pamtunda; 44 Ndipo wotsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m’chombo. Ndipo kudatero kuti onse adapulumukira pamtunda.

Ntchito 28

1 Ndipo atapulumuka, pamenepo adadziwa kuti chisumbucho chidatchedwa Melita. 2 Ndipo akunja adatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti adasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula idalimkugwa, ndi chifukwa cha kuzizira. 3 Koma pamene Paulo adawola chisakata cha nkhumi, nachiyika pa moto, idatulukamo njoka, chifukwa cha kutentha, idaluma dzanja lake. 4 Koma pamene akunjawo adawona chirombocho chiri lende pa dzanja lake, adanena wina ndi mzake, zowona munthuyu ndiye wambanda, angakhale adapulumuka m’nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo. 5 Koma adakutumulira chirombocho kumoto, wosamva kupweteka. 6 Koma adayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa pansi ndi kufa pomwepo; koma m’mene adalindira nthawitu, nawona kuti sadampweteke, adasintha maganizo awo, nati, iye adali Mulungu. 7 Koma pafupi pamenepo padali minda, mwini wake ndiye mkulu wa chisumbucho, dzina lake Popliyo; amene adatilandira ife, natichereza mokoma masiku atatu. 8 Ndipo kudatero kuti atate wake wa Popliyo adagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo adalowa, napemphera, nayika manja pa iye, namchiritsa. 9 Ndipo patachitika ichi, enanso a m’chisumbu, wokhala nazo nthenda, adadza nachiritsidwa: 10 Amenenso adatichitira ulemu wambiri; ndipo pochoka ife adatiyikira zotisowa. 11 Ndipo itapita miyezi itatu tidayenda m’chombo cha ku Alesandriya,chidagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, chidali kuti, Ana –a – mapasa. 12 Ndipo pamene tidakocheza ku Surakusa, tidatsotsako masiku atatu. 13 Ndipo pochokapo tidapaza ntifika ku Regiyo; ndipo lidapita tsiku limodzi adayamba mwera, ndipo m’mawa mwake tidafika ku Potiyolo: 14 Pamenepo tidakomana ndi abale, amene adatiwumilira tikhale nawo masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tidafika ku Roma. 15 Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, adadza kukomana nafe kubwalo la Apiyo, ndi ku nyumba za Alendo zitatu; ndipo pamene Paulo adawawona adayamika Mulungu, nalimbika mtima. 16 Ndipo pamene tidafika ku m’Roma, Kertuliyo adapereka amndende kwa woyang’anira wamkulu. Koma Paulo sadaperekedwe koma adakhala pa yekha ndi msilikali womdikira iye 17 Ndipo kudali atapita masiku atatu, Paulo,adayitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, adanena nawo, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindidachita kanthu kakuyipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, adandipereka wam’singa kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma. 18 Ndipo atandifunsafunsa ine adafuna kundimasula, popeza padalibe chifukwa cha kundiphera. 19 Koma pakukanapo Ayuda, ndidafulumidwa mtima kutulukira kwa Kayisala: sikunena kuti ndidali nako kanthu kakunenera mtundu wanga. 20 Chifukwa cha ichi tsono ndikupemphani inu mundiwone ndi kuyankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israyeli ndamangidwa ndi unyolo uwu. 21 Ndipo adati kwa iye, Ife sitidalandira akalata wonena za inu wochokera ku Yudeya, kapena sadadza kuno wina wa abale ndi kutiwuza kapena kuyankhula kanthu koyipa ka inu. 22 Koma tifuna kumva mutiwuze muganiza chiyani; pakuti za gulu la mpatuko uwu, tidziwa kuti awunenera mutsutsana nawo ponseponse. 23 Ndipo pamene adampangira tsiku, adadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo adawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m’chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo. 24 Ndipo ena adakhulupirira zonenedwazo, koma ena sadakhulupirira. 25 Koma popeza sadabvomerezana, adachoka atanena Paulo mawu amodzi, kuti, Mzimu Woyera adayankhula kokoma mwa Yesaya M’neneri kwa makolo anu. 26 Ndikuti, Pita kwa anthu awa, nuti, Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; ndipo pakupenya mudzapenya, koma wosawona konse; 27 Pakuti ndi mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m’makutu mwawo m’molema kumva, ndipo maso awo adawatseka; kuti angawone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse iwo. 28 Potero dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzachimva. 29 Ndipo pamene adanena mawu awa, Ayuda adachokapo, ndipo adakambirana mwa iwo wokha. 30 Ndipo Paulo adakhala zaka ziwiri za mphumphu m’nyumba yake yolipira nalandira onse akufika kwa iye. 31 Ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za zinthu zokhudzana ndi Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.

Aroma 1

1 Paulo mtumiki wa Yesu Khristu woyitanidwa kukhala mtumwi, wopatulidwa ku Uthenga Wabwino wa Mulungu. 2 (Umene Iye adalonjeza kale ndi mawu a aneneri ake m’malembo woyera) 3 Wakunena za Mwana wake Yesu Khristu Ambuye wathu, amene adabadwa ku mbewu ya Davide, monga mwa thupi; 4 Ndipo adatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndi Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, mwa kuwuka kwa akufa; 5 Mwa amene ife tidalandira naye chisomo ndi utumwi kukamvera chikhulupiriro pakati pa mitundu yonse chifukwa cha dzina lake ; 6 Mwa amenewo muli inunso, woyitanidwa a Yesu Khristu. 7 Kwa onse a ku Roma, wokondedwa a Mulungu, Woyitanidwa kuti akhale woyera mtima; chisomo chikhale ndi inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. 8 Poyamba ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka pa dziko lonse lapansi. 9 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu, masiku onse m’mapemphero anga; 10 Kupempha kwanga ngati m’kutheka tsopano kapena mtsogolo mwa chifuniro cha Mulungu, ndikhale ndi ulendo wabwino, wakudza kwa inu. 11 Pakuti ndilakalaka kuwonana ndi inu, kuti ndikagawire kwa inu mphatso zina za uzimu, kuti inu mukhale okhazikika. 12 Ndiko kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa. 13 Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mukhale wosadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikawone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu yina. 14 Ine ndine wangongole kwa Ahelene ndi kwa akunja, kwa anzeru ndi wopanda nzeru. 15 Kotero, momwe ndingakhozere mwa ine, ndirikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma. 16 Pakuti sindichita manyazi ndi Uthenga wa Khristu; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wokhulupirira; kuyambira kwa Myuda, ndiponso Mhelene. 17 Pakuti m’menemo chawonetsedwa chilungamo cha Mulungu chobvumbulutsidwa kuchokera kuchikhulupiriro kupita kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro. 18 Pakuti mkwiyo wa Muulngu, wochokera Kumwamba, wabvumbulutsidwa pa chisapembedzo chonse chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi chowonadi m’chosalungama chawo; 19 Chifukwa chodziwika cha Mulungu chawonekera m’kati mwawo; pakuti Mulungu adachiwonetsera kwa iwo. 20 Pakuti chilengedwere dziko lapansi zawoneka bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi Umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhala opanda mawu akuwiringula; 21 Chifukwa kuti, ngakhale adadziwa Mulungu, sadamchitira ulemu woyenera Mulungu, ndipo sadamuyamika; koma adakhala wopanda pake m’maganizo awo, ndipo unada mtima wawo wopulukira. 22 Pobvomereza eni wokha kuti ali anzeru iwo adakhala wopusa. 23 Ndipo adasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, nawufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu wowonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zinthu zokwawa. 24 Chifukwa chake Mulungu adawapereka iwo m’zilakolako za mitima yawo, kuzonyansa, kuchititsana matupi awo wina ndi mzake zamanyazi. 25 Amene adasandutsa chowonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wodalitsika nthawi yosatha. Amen. 26 Chifukwa cha ichi Mulungu adawapereka iwo kuzilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi awo adasandutsa machitidwe awo achilengedwe akakhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe. 27 Ndipo chimodzimodzinso amuna adasiya machitidwe a chilengedwe cha akazi, natenthetsana ndi chilakolako chawo wina ndi mzake, amuna wokhawokha adachitirana chamanyazi, ndipo adalandira mwa iwo wokha mphotho yoyenera kulakwa kwawo. 28 Ndipo monga iwo adakana kukhala naye Mulungu m’chidziwitso chawo, adawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera; 29 Wodzadzidwa ndi zosalungama zonse, chiwerewere kuyipa, kusilira, dumbo; wodzala ndi kaduka, kupha, ndewu, chinyengo, udani, miseche; 30 Akazitape, wosinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, wodzitama, amatukutuku, woyamba zoyipa, wosamvera akuwabala awo, 31 Wopanda nzeru, wosasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, wosayanjanitsika, wopanda chifundo; 32 Amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zinthu zotere ayenera imfa, azichita iwo wokha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzichita.

Aroma 2

1 Chifukwa chake ali wopanda mawu wowilingula munthu iwe, amene uli yense woweruza; pakuti m’mene uweruza wina:-momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zinthu zomwezo. 2 Koma tidziwa kuti chiweruzo cha Mulungu chili chowona kwa iwo amene akuchita motsutsana ndi zinthu zotere. 3 Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zinthu zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa chiweruzo cha Mulungu? 4 Kapena upeputsa kodi chuma cha ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukutsogolera kuti ulape? 5 Koma kolingana ndi kuwuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziwunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kubvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu; 6 Amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake. 7 Kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisawonongeko, mwa kupilira pa ntchito zabwino; adzabwezera moyo wosatha: 8 Koma kwa iwo andewu, ndi wosamvera chowonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi ukali, 9 Chisautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoyipa, kwa Myuda, komanso Mhelene. 10 Koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira kwa Myuda, ndiponso Mhelene; 11 Pakuti Mulungu alibe tsankhu. 12 Pakuti onse amene adachimwa opanda lamulo adzawonongeka wopanda lamulo; ndi onse amene adachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo; 13 Pakuti womvera lamulo sakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzalungamitsidwa. 14 Pakuti pamene anthu amitundu akhala opanda lamulo amachita mwa iwo wokha zalamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira wokha ngati lamulo; 15 Popeza iwo awonetsa ntchito yalamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mzake anenezana kapena akanirana; 16 Tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Khristu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga wabwino. 17 Tawona iwe wakudzitcha wekha Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu, 18 Nudziwa chifuniro chake, nubvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m’chilamulo, 19 Nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima. 20 Mlangizi wa wopanda nzeru, mphunzitsi wa tiwana, wakukhala nacho chidziwitso ndi chowonadi cha m`chilamulo.. 21 Iwe tsono wophunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wolalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? 22 Iwe wonena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wodana nawo mafano, umafunkha za m’kachisi kodi? 23 Iwe wodzitamandira pa chilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo? 24 Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga kwalembedwa. 25 Inde pakuti mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa. 26 Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoyikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe? 27 Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi uweruza iwe, amene mwa malembo ndi mdulidwe womwe, ulakwira lamulo? 28 Pakuti sali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupi: 29 Koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mu mzimu, si m’malembo ayi; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu koma kwa Mulungu.

Aroma 3

1 Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapena mdulidwe upindulanji? 2 Zambiri monse monse; choyamba, kuti mawu a Mulungu adaperekedwa kwa iwo. 3 Nanga bwanji ngati ena sadakhulupirira? Kodi kusakhulupirira kwawo kupangitsa chabe chikhulupiriro cha Mulungu chopanda mphamvu? 4 Msatero ayi, koma Mulungu akhale wowona, ndipo anthu onse akhale wonama: monga kwalembedwa; kuti Inu mukayesedwe wolungama m’maneno anu, ndi kuti mukalakike m’mene muweruzidwa. 5 Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu amene afikitsa mkwiyo? (ndilankhula monga munthu). 6 Msatero ayi; ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wadziko lapansi? 7 Pakuti ngati chowonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa? 8 Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoyipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama. 9 Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iyayi ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo; 10 Monga kwalembedwa, palibe m’modzi wolungama, inde palibe m’modzi; 11 Palibe m’modzi wakudziwitsa, palibe m’modzi wakufunafuna Mulungu; 12 Onsewa apatuka njira, wonsewa pamodzi akhala wopanda phindu; palibe m’modzi wochita zabwino, inde, palibe m’modzi ndithu. 13 M’mero mwawo muli manda apululu; Ndi lilime lawo amanyenga; ululu wa njoka uli pansi pa milomo yawo; 14 M’kamwa mwawo mudzala ndi zotemberera ndi zowawa; 15 Miyendo yawo ichita liwiro kukhetsa mwazi; 16 Kusakaza ndi kusawuka kuli m’njira zawo; 17 Ndipo njira ya mtendere sadayidziwa; 18 Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pawo. 19 Ndipo tidziwa kuti zinthu zili zonse chizinena chilamulo zichiyankhulira iwo ali pansi pa chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi likatsutsidwe pamaso pa Mulungu. 20 Chifukwa chake pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo. 21 Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chopanda lamulo chawonetsedwa, chochitiridwa umboni ndi lamulo ndi aneneri; 22 Ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana; 23 Pakuti onse adachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; 24 Alungamitsidwa kwa ulere ndi chisomo chake, mwa chiwombolo cha mwa Khristu Yesu; 25 Amene Mulungu adamuyika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m’mwazi wake, kuti awonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m’kulekerera kwake adalekerera machimo wochitidwa kale lomwe; 26 Kuti awonetse chilungamo chake m’nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu. 27 Pamenepo kudzitamandira kuli kuti? Kwaletsedwa ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iyayi; koma ndi lamulo lachikhulupiriro. 28 Chifukwa chake timalizira ndikunene kuti munthu alungamitsidwa mwa chikhulupiriro, wopada ntchito za lamulo. 29 Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda wokhawokha kodi? Si wawo wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso: 30 Powona kuti ndiye Mulungu m’modzi, amene adzawayesa amdulidwe wolungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro. 31 Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ayi; koma tikhazikitsa lamulo.

Aroma 4

1 Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, adalandira chiyani? 2 Pakuti ngati Abrahamu adalungamitsidwa mwa ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga pamaso pa Mulungu ayi. 3 Pakuti lembo likuti chiyani? Ndipo Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo chidaweregedwa kwa iye chilungamo. 4 Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siyiwerengedwa ya chisomo koma ya ngongole. 5 Koma kwa iye amene sagwira ntchito, koma akhulupirira Iye amene ayesa wosapembedza ngati wolungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo. 6 Monganso Davide anena za mdalitso wake wa munthu, amene Mulungu amuwerengera chilungamo chopanda ntchito, 7 Ndi kuti, wodala iwo amene akhululukidwa zoyipa zawo, nakwiriridwa machimo awo. 8 Wodala munthu amene Ambuye samuwerengera tchimo 9 Mdalitso umenewu tsono uli kwa wodulidwa kodi kapena kwa wosadulidwa womwe? Pakuti timati, chikhulupiriro chidawerengedwa kwa Abrahamu chilungamo. 10 Tsono chidawerengedwa bwanji? M’mene iye adali wodulidwa kapena wosadulidwa ? sipamene adali wodulidwa ayi, koma wosadulidwa. 11 Ndipo iye adalandira chizindikiro cha mdulidwe ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye adali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhala tate wa onse wokhulupirira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso; 12 Ndiponso tate wa mdulidwe wa iwo amene siyali a mdulidwe wokha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe achikhulupiriro chija cha tate wathu Abrahamu, chimene iye adali nacho asanadulidwe. 13 Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silidapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake mwa lamulo; koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro. 14 Pakuti ngati iwo alamulo akhala wolowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndipo lonjezo layesedwa lopanda mphamvu; 15 Pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo pamenepo palibe kulakwa, 16 Chifukwa chake chilungamo chichokera m’chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbewu zonse; si kwa iwo a chilamulo wokhawokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye tate wa ife tonse. 17 Monga kwalembedwa, ndidakukhazika iwe tate wa mitundu yambiri ya anthu pamanso pa Mulungu amene iye adamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndikuyitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo. 18 Amene adakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale tate wa mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi; mbewu yako idzakhala yotere. 19 Ndipo iye wosafoka m’chikhulupiriro sadalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, pokhala iye ngati zaka makumi khumi, ndi mimba ya Sara imene idali yowuma. 20 Ndipo poyang’anira lonjezo la Mulungu sadagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma adalimbitsa m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemerero; 21 Nakhazikikanso mumtima kuti, chimene iye adalonjeza, adali nayonso mphamvu yakuchichita. 22 Chifukwa chake ichi chidawerengedwa kwa iye chilungamo. 23 Tsopano ichi sichidalembedwa chifukwa cha iye yekha yekha, kuti chidawerengedwa kwa iye; 24 Koma chifukwa cha ifenso, kwa iwo amene chidzawerengedwa ngati tikhulupirira pa Iye amene adawukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu kuchokera kwa akufa; 25 Amene adaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, nawukitsidwanso chifukwa cha chilungamitso chathu.

Aroma 5

1 Chifukwa chake pokhala wolungamitsidwa mwa chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; 2 Amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m’chisomo ichi m’mene tilikuyimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. 3 Ndipo sichotero chokha, komanso tikondwera m’zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiliro: 4 Ndi chipiliro, chizolowezi; ndi chizolowezi, chiyembekezo; 5 Ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chidatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife. 6 Pakuti pamene tidali chikhalire wofoka, pa nyengo yake Khristu adawafera wosapembedza. 7 Pakuti ndi chibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. 8 Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire wochimwa, Khristu adatifera ife. 9 Ndipo tsono popeza tidayesedwa wolungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka ku mkwiyo mwa Iye. 10 Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tidayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake. 11 Ndipo sichotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa iye talandira tsopano chiwombolo. 12 Chifukwa chake monga uchimo udalowa m’dziko lapansi mwa munthu m’modzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa idafikira anthu onse; chifukwa kuti onse adachimwa. 13 ( Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo udali m’dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo. 14 Komatu imfa idachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sadachimwe monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la Iye wakudzayo. 15 Koma mphatso yaulere siyilingana ndi kulakwa pakuti ngati ambiriwo adafa chifukwa cha kulakwa kwa m’modziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere yochokera ndi munthu m’modziyo Yesu Khristu, idachulukira anthu ambiri. 16 Ndipo mphatso siyinadza monga mwa m’modzi wochimwa, pakuti mlandu ndithu udachokera kwa munthu m’modzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere idachokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa wolungama. 17 Pakuti ngati, ndikulakwa kwa m’modzi, imfa idachita ufumu mwa m’modziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso yachilungamo, adzachita ufumu m’moyo mwa m’modzi, ndiye Yesu Khristu.) 18 Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kudafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chidafikira anthu onse. 19 Pakuti ndi kusamvera kwa munthu m’modzi ambiri adayesedwa wochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa m’modzi ambiri adzayesedwa wolungama. 20 Momwemo lamulo lidalowa, kuti kulakwa kukachuluke. Koma pamene uchimo udachuluka, pomwepo chisomo chidachuluka koposa: 21 Kuti, monga uchimo udachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

Aroma 6

1 Tidzanena chiyani tsono? Tidzakhalabe mu uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke? 2 Msatero ayi. Ife amene tili akufa ku uchimo tidzakhala bwanji chikhalire m’menemo? 3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tidabatizidwa mwa Khristu Yesu; tidabatizidwa mu imfa yake? 4 Chifukwa chake tidayikidwa m’manda pa modzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu adaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano. 5 Pakuti ngati ife tidakhala pamodzi ndi Iye m’chifanizo cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizo cha kuwuka kwake. 6 Podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale udapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likawonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo. 7 Pakuti iye amene adafa adamasulidwa ku uchimo. 8 Koma ngati ife tidafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye; 9 Podziwa kuti Khristu adawukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siyichitanso ufumu pa Iye. 10 Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi, ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. 11 Chotero inunso mudziwerengere inu nokha wofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 12 Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa kumvera zilakolako zake. 13 Ndipo musapereke ziwalo zanu ku uchimo, zikhale zida zachosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo. 14 Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma achisomo. 15 Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitiri a lamulo, koma a chisomo. Msatero ayi. 16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala atumiki ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo? 17 Koma ayamikike Mulungu, kuti ngakhale mudakhala atumiki a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja achiphunzitso chimene chidakumasulani inu. 18 Ndipo pamene mudamasulidwa ku uchimo, mudakhala atumiki a chilungamo. 19 Ndiyankhula manenedwe a anthu chifukwa cha kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu mudapereka ziwalo zanu zikhale atumiki a chonyansa ndi akusayeruzika kuti zichite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale atumiki achilungamo kuti zichite chiyeretso. 20 Pakuti pamene inu mudali atumiki a uchimo, mudali wosatumikira chilungamo. 21 Ndipo mudali nazo zabala zanji nthawi ija, m’zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano pakuti chimaliziro cha zinthu zimenezo chili imfa? 22 Koma tsopano, pamene mudamasulidwa ku uchimo, ndi kukhala atumiki a Mulungu, muli nacho chobala chanu, chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha. 23 Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Aroma 7

1 Nanga kodi simudziwa, abale ( pakuti ndiyankhula ndi anthu wodziwa lamulo,) kuti lamulolo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo? 2 Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. 3 Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa kulamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina. 4 Chotero, abale anga inunso mudayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukwatiwe ndi wina, ndiye amene adawukitsidwa kwa akufa, kuti ife tim’balire Mulungu zipatso. 5 Pakuti pamene tidali m’thupi, zilakolako za machimo, zimene zidali mwa chilamulo, zidali kuchita m’ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso. 6 Koma tsopano tidamasulidwa kuchilamulo, popeza tidafa kwa ichi chimene tidagwidwa nacho kale; chotero kuti, titumikire mu mzimu watsopano, si m’chilembo chakale ayi. 7 Tidzanena chiyani tsono? Kodi chilamulo chiri uchimo? Msatero ayi.. Ayi, koma ine sindikadazindikira uchimo; koma mwa lamulo ndimo: pakuti sindikadazindikira chilakolako, chikadapanda chilamulo kunena kuti usasilire. 8 Koma uchimo, pamene udapeza chifukwa, udachita m’kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo uchimo uli wakufa. 9 Ndipo kale ine ndidali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo lidadza, uchimo udatsitsimuka, ndipo ine ndidafa. 10 Ndipo lamulo, limene lidali lopatsa moyo, ndidalipeza lopatsa imfa. 11 Pakuti uchimo, pamene udapeza chifukwa mwa lamulo, udandinyenga ine, ndikundipha. 12 Chotero chilamulo chiri choyera, ndi chilangizo chake n’choyera ndi cholungama, ndi chabwino. 13 Ndipo tsopano chabwino chija chidandikhalira imfa kodi? Msatero ayi. Koma uchimo, kuti uwoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa kwambiri mwa lamulo. 14 Pakuti tidziwa kuti chilamulo chiri chauzimu; koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa, ku uchimo. 15 Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi. 16 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndibvomerezana nacho chilamulo kuti chiri chabwino. 17 Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wokhalabe m’kati mwanga ndiwo. 18 Pakuti ndidziwa kuti m’kati mwanga, (ndiko m’thupi langa), simukhala chinthu chabwino: pakuti kufuna ndiri nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. 19 Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choyipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. 20 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndichichita, koma uchimo wokhalabe m’kati mwanga ndiwo. 21 Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti pamene ndifuna chabwino, choyipa chiriko mwa ine. 22 Pakuti ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu. Mwa munthu wa m’kati mwanga. 23 Koma ndiwona lamulo lina m’ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundibweretsa ine mu ukapolo wa lamulo la chimo umene uli mziwalo zanga. 24 Ho! munthu wosauka ine! Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi? 25 Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtima nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.

Aroma 8

1 Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa amene iwo akuyenda osati mwa thupi koma mwa Mzimu. 2 Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa. 3 Pakuti chimene chilamulo sichidathe kuchita popeza chidafoka mwa thupi, Mulungu adatumiza Mwana wake wa Iye yekha m’chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m’thupi: 4 Kuti chilungamo cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5 Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu zathupi; koma iwo ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu. 6 Pakuti chisamaliro cha thupi chiri imfa; koma chisamaliro cha mzimu chiri moyo ndi mtendere. 7 Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja kuchilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero. 8 Chomwecho iwo amene ali m’thupi sangathe kukondweretsa Mulungu. 9 Koma inu simuli m’thupi ayi, koma mumzimu ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Tsopano ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, si ali wake wa Khristu. 10 Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu ali wa moyo chifukwa cha chilungamo. 11 Koma ngati Mzimu wa Iye amene adawukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adawukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu. 12 Chifukwa chake, abale, ife tiri angongole si ake a thupi ayi, kukhala ndi moyo monga mwa thupi. 13 Pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. 15 Pakuti inu simudalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma mudalandira mzimu wa umwana, umene tifuwula nawo, kuti, Abba, Atate. 16 Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu: 17 Ndipo ngati ana, pomweponso wolowa m’nyumba; inde wolowa m’nyumba ake a Mulungu, ndi wolowa amzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. 18 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzabvumbulutsidwa kwa ife. 19 Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira kuwonekera kwa ana a Mulungu. 20 Pakuti cholengedwacho chigonjetsedwa ku utsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene adachigonjetsa, mchiyembekezo. 21 Pakuti cholengedwacho chidzamasulidwa ku ukapolo wachibvundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. 22 Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuwula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano. 23 Ndipo sichotero, koma ife tomwe; tiri nazo zowundukula za Mzimu, inde ifenso tibuwula m’kati mwathu, ndi kulindilira umwana wathu, ndiwo chiwomboledwe cha thupi lathu. 24 Pakuti ife tidapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chiwoneka si chiri chiyembekezo ayi; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? 25 Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindilira ndi chipiriro. 26 Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti chimene tichipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuwula zosatheka kuneneka. 27 Ndipo Iye asanthula m’mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera woyera mtima monga mwa chifuniro cha Mulungu . 28 Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene ali woyitanidwa ku cholinga chake. 29 Chifukwa kuti iwo amene Iye adawadziwiratu, iwowa adawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri. 30 Ndipo amene Iye adawalamuliratuwo, Iye adawayitana ndipo iwo amene adawayitana adawalungamitsa,ndipo iwo amene adawalungamitsa adawapatsanso ulemerero. 31 Ndipo tidzanena chiyani kuzinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatitsutsa ndani? 32 Iye amene sadatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma adampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye? 33 Ndani adzaneneza wosankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene adawalungamitsa. 34 Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adawafera, inde makamaka, ndiye amene adawuka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja la manja la Mulungu, amenenso atipembedzera ife. 35 Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunzidwa, kapena njala, kapena usiwa, kapena zowopsa, kapena lupanga? 36 Monga kwalembedwa, chifukwa cha inu tiri kuphedwa dzuwa lonse; tidayesedwa monga nkhosa zokaphedwa. 37 Ayi, koma mzinthu zonsezi, ife ndife oposa agonjetsi, mwa Iye amene adatikonda. 38 Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale mphamvu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilimkudza, 39 Ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chili chonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu chimene chiri mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Aroma 9

1 Ndinena zowona mwa Khristu, sindikunama ayi, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndi ine mwa Mzimu Woyera. 2 Kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphweteka mtima kosalekeza. 3 Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi: 4 Ndiwo a Israyeli, ali nawo umwana ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m’kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo; 5 Iwo ali makolo, ndi kwa iwo ndiko adachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka ku nthawi zonse. Amen. 6 Koma sikuli ngati mawu a Mulungu adakhala chabe ayi. Pakuti onse wochokera kwa Israyeli siali onse a Israyeli: 7 Sikuti chifukwa ali mbewu ya Abrahamu, ali onse ana; koma adati, mwa Isake, mbewu yako idzayitanidwa. 8 Ndiko kuti, ana athupi sakhala iwo ana a Mulungu ayi; koma ana a lonjezo awerengedwa mbewu. 9 Pakuti mawu a lonjezo ndi amenewa, panyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana. 10 Ndipo si chotero chokha, koma Rabekanso pamene adali ndi pakati pam’ modzi, ndiye kholo lathu Isake; 11 (Pakuti anawo asanabadwe, kapena asadachite kanthu kabwino kapena koyipa, kuti cholinga cha Mulungu monga mwa kusankha kukhale, sichifukwa cha ntchito ayi, koma chifukwa cha wakuyitanayo); 12 Pakuti kudanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala wotumikira wam’ng’ono. 13 Monga kwalembedwa, ndidakonda Yakobo, koma ndidamuda Esawu. 14 Ndipo tsono tidzanena chiyani? Kodi chiripo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ayi. 15 Pakuti adati ndi Mose, ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni. 16 Chotero sichichokera kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo. 17 Pakuti lembo linena kwa Farawo, chifukwa cha cholinga chomwechi, ndidakuutsa iwe, kuti ndikawonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi. 18 Chotero iye achitira chifundo amene iye afuna, ndipo amene iye afuna amuwumitsa mtima. 19 Ndipo iwe pamenepo udzanena kwa ine chifukwa chiyani iye wapeza cholakwa? Pakuti ndani adakaniza chifuno chake? 20 Ayi, koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mawu? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene adachipanga, Undipangiranji ine chotero? 21 Kodi kapena wowumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuwumba ndi ntchintchi yomweyo chotengera chimodzi cha ulemu ndi china chamanyazi? 22 Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuwonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, adalekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko? 23 Ndikuti iye akadziwitse chuma cha ulemerero wake wawukulu pa zotengera za chifundo, zimene iye adazikonzeratu kuulemerero wake. 24 Ndiwo ife amenenso iye adatiyitana, si a mwa Ayuda wokhawokha, komanso a mwa anthu amitundu? 25 Monga iye adatinso mwa Hoseya, Ndidzawatcha anthu anga amene sadakhala anthu anga, ndi wokondedwa wake amene sadali wokondedwa. 26 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kudanenedwa kwa iwo, simuli anthu anga ayi, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo. 27 Ndipo monga Yesaya afuwula za Israyeli, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga m’chenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka. 28 Pakuti iye adzatsiriza ntchito, ndi kuyichita mwa chidule m`chilungamo: chifukwa Ambuye adzatsiliza ntchito yake mwachidule pa dziko lapansi. 29 Ndipo monga Yesaya adati kale , Ngati Ambuye wa makamu adakapanda kutisiyira ife mbewu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora. 30 Kodi tidzanena chiyani tsono? Kuti amitundu amene sadatsata chilungamo, adafikira kuchilungamo, ndicho chilungamo cha m`chikhulupiriro. 31 Koma Israyeli, potsata lamulo la chilungamo, sadafikira lamulo la chilungamo. 32 Chifukwa chiyani? Chifukwa kuti sadalitsata ndi chikhulupiro, koma monga ndi ntchito za lamulo. Adakhumudwa pamwala wokhumudwitsa. 33 Monganso kwalembedwa kuti; Onani ndikhazika m’Ziyoni mwala wokhumudwitsa nawo, ndi thanthwe lopunthwitsa; Ndipo wokhulupirira pa iye sadzachita manyazi.

Aroma 10

1 Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero la kwa Mulungu kwa Israyeli ndilo kuti iwo apulumuke. 2 Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso. 3 Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo wokha, iwo sadagonja kuchilungamo cha Mulungu. 4 Pakuti Khristu ndi chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa amene aliyense akhulupirira. 5 Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m’lamulo, adzakhala nacho moyo. 6 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mumtima mwako. Adzakwera ndani kumwambako? (Ndiko kutsitsako Khristu:) 7 Kapena adzatsikira ndani kudzenjeko? (Ndiko kukweza Khristu kwa akufa.) 8 Koma akuti chiyani? Mawu ali pafupi ndi iwe, m’kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mawu achikhulupiriro, amene ife tiwalalikira; 9 Kuti ngati udzabvomereza m’kamwa mwako, Ambuye Yesu, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuwukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m’kamwa abvomereza kutengapo chipulumutso. 11 Pakuti lembo likuti, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi. 12 Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene ayitana pa Iye; 13 Pakuti amene aliyense adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. 14 Ndipo iwo adzayitana bwanji pa Iye amene sadamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwnaji Iye amene sadamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? 15 Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Wokometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga wa mtendere wobweretsa chisangalalo muzinthu zabwino. 16 Koma sadamvera uthenga onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye , ndani adakhulupirira zonena zathu? 17 Chomwecho chikhulupiriro chidza, mwa kumvera ndi kumva mwa mawu a Mulungu. 18 Koma ine nditi, sadamva iwo kodi! Indetu, liwu lawo lidatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi mawu awo kumalekezero adziko lapansi. 19 Koma nditi, kodi Israyeli alibe kudziwa? Poyamba Mose anena, Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu, ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira. 20 Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndidapezedwa ndi iwo amene sadandifune; ndidawonekera kwa iwo amene sadandifunsa. 21 Koma kwa Israyeli anena, Tsiku lonse ndidatambalitsira manja anga kwa anthu wosamvera ndi wotsutsana.

Aroma 11

1 Chifukwa chake ndinena, Mulungu adataya anthu ake kodi? Msatero ayi. Pakuti inenso ndiri mu Israyeli, wa mbewu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini. 2 Mulungu sadataya anthu ake amene Iye adawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Pomwe Iye amachita mapembedzero kwa Mulungu chifukwa cha Israeyeli, ndi kuti, 3 Ambuye, adawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga. 4 Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndidadzisiyira ndekha anthu amuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sadagwadira Baala. 5 Choteronso nthawi yatsopano chiripo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo. 6 Ndipo ngati ndi chisomo mwa pamenepo sindi ntchito ayi; ndipo pakutero, chisomo sichikhalanso chisomo. Koma ngati chiri mwa ntchito pamenepo sichisomonso: ndipo pakutero ntchito sikhalanso ntchito. 7 Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israyeli afunafuna sadachipeza; koma osankhidwawo adachipeza, ndipo wotsalawo adachititsidwa khungu; 8 Monga kudalembedwa kuti, Mulungu adawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino. 9 Ndipo Davide akuti, Gome lawo likhale kwa iwo ngati msampha, ndi ngati diwa, ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango iwo: 10 Maso awo adetsedwe, kuti asapenye, ndipo muweramitse msana wawo. 11 Chifukwa chake ndinena, Adakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ayi; koma ndi kugwa kwawo chipulumutso chidadza kwa amitundu, kudzachititsa iwo nsanje. 12 Ndipo ngati kugwa kwawo kwatengera dziko lapansi chuma, ndipo kuchepa kwawo kutengera anthu a mitundu chuma; koposa kotani nanga kudzaza kwawo? 13 Koma ndiyankhula ndi inu amitundu popeza ine ndiri mtumwi wa kwa amitundu, ndilemekeza utumiki wanga; 14 Kuti ngati mkutheka ndikachititse mkwiyo iwo amene ndi a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo. 15 Pakuti ngati kuwataya kwawo kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwawo kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa? 16 Ndipo ngati zipatso zoyamba ziri zopatulika, choteronso zonse; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi. 17 Koma ngati nthambi zina zidathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wakuthengo, udamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo. 18 Usadzitama iwe wekha motsutsana ndi nthambizo; Koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ayi, koma muzu ukunyamula iwe. 19 Ndipo kapena udzanena, nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwemo. 20 Chabwino; chifukwa chakusakhulupirira iwo adakhala wothyoledwa, ndipo iwe uyima mwa chikhulupiriro. Usamadzikuza mumtima, koma wopatu: 21 Pakuti ngati Mulungu sadalekerera nthambi za mtundu wake, sadzakulekerera iwe. 22 Chifukwa chake wonani ubwino wake wa Mulungu ndi kuwuma mtima kwake kwa Mulungu; kwa iwo adagwa, kuwuma kwake; koma kwa iwe ubwino wake wa Mulungu, ngati ukhala chikhalire ubwinowo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe. 23 Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire ndi chisakhulupiriro, adzawamezanitsanso pakuti Mulungu ndi wokwaniritsa kuwamezanitsanso. 24 Pakuti ngati iwe udasadzidwa ku mtengo wazitona wa mtundu wa kuthengo mwa chilengedwe, ndipo udamezetsanidwa kosiyana ndi chilengedwe ku mtengo wa azitona wabwino, mokaniza; koposa kotani nanga iwo, ndiwo wokhala chilengedwe nthambi zake, adzamezetsedwa ku mtengo wawo womwewo wa azitona? 25 Pakuti sindifuna, abale kuti mukhale wosadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nakha, kuti khungu lakusawona kudadza pang’ibi oa Usratekum kufikira a mitundu akwanire kulowamo. 26 Ndipo chotero Israyeli yense adzapulumuka; monganso kudalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo: 27 Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo pamene ndidzachotsa machimo awo. 28 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ndi adani, chifukwa cha inu; koma ngati kunena za chisankhidwe, ali wokondedwa, chifukwa cha makolo. 29 Pakuti mphatso zake ndikuyitana kwake kwa Mulungu sizilapika. 30 Pakuti monga inunso kale simudakhulupirira Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusakhulupirira kwao. 31 Choteronso iwo sadakhulupirira tsopano, kuti iwonso mwa chifundo chawo kuti iwonso akalandire chifundo. 32 Pakuti Mulungu adatsekera pamodzi onse m’kusakhulupirira, kuti akachitire onse chifundo. 33 Ha! Kuya kwake kwa m`chuma pamodzi ndi nzeru ndi chidziwitso cha Mulungu.! Wosasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake mzosalondoleka! 34 Pakuti adadziwa ndani mtima wa Ambuye? Kapena adakhala phungu wake ndani? 35 Ndipo adayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzam’bwezeranso Iye? 36 Pakuti kuchokera kwa Iye ndi mwa Iye, ndi kwa Iye muli zinthu zonse: kwa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse.

Aroma 12

1 Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. 2 Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe apansi pano; koma mukhale wosandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi cholandirika ndi changwiro. 3 Pakuti ndinena kupyolera mwa chisomo chopatsidwa kwa ine. Kwa munthu aliyense pakati pa inu, kuti asaganize mwa iye yekha koposa kumene ayenera kuganiza; koma aganize modziletsa yekha, kolingana ndi Mulungu wampatsila aliyense muyeso wa chikhulupiriro. 4 Pakuti monga m’thupi limodzi tiri nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo siziri nayo ntchito imodzimodzi; 5 Chomwecho ife, ndife ambiri tiri thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zimzake wina ndi wina. 6 Ndipo pokhala nazo ife mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chopatsidwa kwa ife, kapena mphatso yonenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro. 7 Kapena yotumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wophunzitsa, akaphunzitse; 8 Kapena iye wodandaulira, kukudandaulirako; wogawira achite ndi mtima wowona; iye woweruza, aweruze ndi changu; iye wochita chifundo, achite ndi kukondwa mtima. 9 Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwirizana nacho chabwino. 10 M’chikondano cha anzanu wina ndi mzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; 11 Musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; 12 Kondwerani m’chiyembekezo, pilirani m’masautso; limbikani chilimbikire m’kupemphera. 13 Patsani zosowa woyera mtima; cherezani, aulendo. 14 Dalitsani iwo akuzunza inu, dalitsani, musawatemberere. 15 Kondwani nawo iwo akukondwera; ndipo lirani nawo akulira. 16 Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mzake; musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nawo wodzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. 17 Musabwezere munthu aliyense choyipa chosinthana ndi choyipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. 18 Ngati mkutheka monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. 19 Wokondedwa, musabwezere choyipa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. 20 Chifukwa chake ngati mdani wako akumva njala, um’dyetse, ngati akumva ludzu, umwetse; pakuti pakutero udzawunjika makala amoto pamutu pake. 21 Musagonje ku choyipa, koma ndi chabwino gonjetsani choyipa.

Aroma 13

1 Anthu onse aliyense agonje ku mphamvu za udindo: pakuti palibe mphamvu za udindo wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo mphamvu za udindo zilipo ziyikidwa ndi Mulungu. 2 Kotero kuti aliyense wotsutsana nazo mphamvu za udindo, akaniza choyikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga. 3 Pakuti woweruza sakhala wowopsa ku ntchito zabwino koma ku zoyipa. Ndipo ufuna kodi kusawopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m’menemo: 4 Pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, wochitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choyipa, wopatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoyipa. 5 Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale wogonja, sichifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima. 6 Pakuti chifukwa cha ichi muperekenso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi. 7 Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake akulipidwa; kuwopa kwa eni ake akuwawopa; ulemu kwa eni ake aulemu. 8 Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mzake wakwaniritsa lamulo. 9 Pakuti ili, usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, usasilire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m’mawu amenewa, kuti, udzikonda mzako monga udzikondera iwe wekha. 10 Chikondano sichichitira mzake choyipa; chotero chikondanocho chiri chokwanitsa lamulo. 11 Ndipo kuti, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuwuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chiri pafupi koposa pamene tidayamba kukhulupirira. 12 Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; chifukwa chake tibvule ntchito za mdima, ndi tibvale chida cha kuwunika. 13 Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’madyerero ndi kuledzera ayi, si m’chigololo ndi chonyansa ayi, si mundewu ndi nkhwidzi ayi. 14 Koma bvalani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.

Aroma 14

1 Ndipo iye amene ali wofoka m’chikhulupiriro mumlandire, koma sikuchita naye makani wotsutsana ayi. 2 Munthu m’modzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofoka angodya zitsamba. 3 Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira iye. 4 Ndani iwe woweruza m’nyamata wa mwini wake? Iye ayimilira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzayimiliritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuyimiliritsa. 5 Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa limzake, wina aganizira kuti masiku onse wofanana. Munthu aliyense akhazikike konse mumtima mwake. 6 Iye wosamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye; ndipo iye wosasamalila tsiku salisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu. 7 Pakuti palibe m’modzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha, ndipo palibe m’modzi adzifera yekha. 8 Pakuti tingakhale tiri ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye. 9 Pakuti chifukwa cha ichi Khristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti Iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo 10 Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzayimilira ku mpando wakuweruza wa Mulungu. 11 Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzabvomereza Mulungu. 12 Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu. 13 Chifukwa chake tisaweruzanenso wina ndi mzake, koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asayike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wake, kapena chompunthwitsa. 14 Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa. 15 Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe yendayendanso ndi chikondano. Usamuwononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera. 16 Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire. 17 Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala m`chakudya ndi m`chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. 18 Pakuti iye amene atumikira Khristu mu zinthu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu. 19 Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mzake. 20 Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koyipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa. 21 Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chiri chonse chokhumudwitsa ndi chopunthwitsa ndi kufowoketsa mbale wako. 22 Chikhulupiriro chimene uli nacho, ukhale nacho kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndiye amene sadziweruza mwini yekha m’zinthu zomwe iye wazibvomereza. 23 Koma iye amene akayika kayika pakudya, atsutsika chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chiri chonse chosatuluka m’chikhulupiriro, ndicho uchimo.

Aroma 15

1 Ndipo ife amene tiri wolimba, tiyenera kunyamula zofoka za wopanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. 2 Yense wa ife akondweretse mzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa. 3 Pakuti Khristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, minyozo ya iwo amene adakunyoza iwe idagwera pa Ine. 4 Pakuti zonse zidalembedwa kale zidalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiliro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo. 5 Ndipo Mulungu wa chipiliro ndi wachitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mzake, monga mwa Khristu Yesu. 6 Kuti nonse pamodzi, m’kamwa m’modzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 7 Chifukwa chake mulandirane wina ndi mzake, monganso Khristu anatilandira ife, ku ulemerero wa Mulungu. 8 Ndipo ndinena kuti Khristu adakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha chowonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo wopatsidwa kwa makolo, 9 Ndikuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo chake; monga kwalembedwa, chifukwa cha ichi ndidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzayimbira dzina lanu. 10 Ndiponso anena, kondwerani amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. 11 Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande Iye. 12 Ndiponso, Yesaya anati, Padzakhala muzu wa Jese, ndi Iye amene adzauka kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu a mitundu adzamukhulupirira. 13 Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupirira, kuti mukachuLuka ndi chiyembekezo, mumphamvu ya Mzimu Woyera. 14 Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli wodzala ndi ubwino, wodzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mzake. 15 Koma mwina abale ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu. 16 Kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Khristu kwa amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kudzipereka kwao kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. 17 Chifukwa chake ndiri nacho chodzitamandira cha mwa Khristu Yesu mu zinthu zimene zili kwa Mulungu. 18 Pakuti sindingathe kulimba mtima kuyankhula zinthu zimene Khristu sadazichita mwa ine zakuwamvetsa anthu amitundu, ndi mawu ndi ntchito. 19 Kupyolera mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu wa Mulungu; kotero kuti kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndakwanitsa kulalikira Uthenga wa Khristu; 20 Inde chotero tidalimbika kulalikira Uthenga Wabwino, pamalopo Khristu sadatchulidwe kale, kuti ndisamange pa maziko a munthu wina. 21 Koma monga kwalembedwa kwa iwo amene sadayakhulidwe adzawona, ndipo kwa iwo amene sadamve adzazindikira. 22 Chifukwa chakenso ndidaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu; 23 Koma tsopano pamene ndiribe malo m’mayiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero. 24 Pamene pali ponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndidzadza kwa inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kudzazidwa ndi gulu lanu. 25 Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, kukatumikira woyera mtima. 26 Pakuti kudakondweretsa aku Makedoniya ndi Akaya kusonkha chopereka cha wosauka a kwa woyera mtima aku Yerusalemu. 27 Pakuti chidakondweretsa iwo ndithu; ndipo iwo ali ndi ngongole nawo, Pakuti ngati amitundu wokhala wotengapo gawo pa zinthu zawo za uzimu, ntchito yawonso ndiyo kutumikira iwo ali mu zinthu zathupi. 28 Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzadutsa kwanu kupita ku Spaniya. 29 Ndipo ndidziwa kuti pamene ndidza kwanu, ndidzafika m’kudzaza kwake kwa m’dalitso wa uthnga wa Khristu. 30 Ndipo ndikudandaulirani, abale, chifukwa cha Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chifukwa cha chikondi cha Mzimu, kuti mumalimbika pamodzi ndi ine m’mapemphero anu a kwa Mulungu chifukwa cha ine; 31 Kuti ndikapulumutsidwe kwa wosamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi woyera mtima; 32 Pakuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuno cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu. 33 Ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.

Aroma 16

1 Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wa mkazi wa mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya; 2 Kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera woyera mtima, ndi kuti mumthandize m’zinthu ziri zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha adali wothandiza ambiri, ndi ine ndemwe. 3 Apatseni moni Priska ndi Akula, antchito amzanga mwa Khristu Yesu. 4 Amene adapereka makosi awo chifukwa cha moyo wanga: amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu. 5 Ndipo patsani moni Mpingo wa Ambuye wa m’nyumba mwawo. Patsani moni Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso chowundukura cha Asiya cha kwa Khristu. 6 Patsani moni Mariya amene adadzilemetsa ndi ntchito zambiri zothandiza inu. 7 Patsani moni Androniko ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende amzanga, amene ali womveka mwa atumwi, amenenso adali mwa Khristu ndisadakhale ine. 8 Patsani moni Ampliyato wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9 Patsani moni Urbano wantchito mzathu mwa Khristu, ndi Staku wokondedwa wanga. 10 Patsani moni Apele, wobvomerezedwayo mwa Khristu. Patsani moni iwo a m`nyumba ya Aristobulo. 11 Patsani moni Herodiyona, mbale wanga. Patsani moni iwo a kwa Narikiso, amene ali mwa Ambuye. 12 Patsani moni Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Patsani moni Persida, wokondedwayo amene adagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye. 13 Patsani moni Rufo, wosankhidwayo mwa Ambuye ndi amayi ake ndi wanga. 14 Patsani moni Asunkrito, Felego, Herme, Partoba, Herma ndi abale amene ali nawo. 15 Patsani moni Filologo ndi Yuliya, Nereya ndi mlongo wake, ndi Olumpa, ndi woyera mtima onse ali pamodzi nawo. 16 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsompsono chopatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni inu. 17 Ndipo ndikudandaulirani, abale, zindikirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho mudachiphunzira inu; ndipo patukani pa iwo. 18 Pakuti wotere satumikira Ambuye wathu Yesu Khristu, koma mimba zawo; ndipo ndi mawu osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa. 19 Pakuti kumvera kwanu kudabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pazabwino, koma opanda nzeru pa zoyipa. 20 Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwa. Chisomo cha Ambuye wathu Khristu chikhale ndi inu. Ameni 21 Timoteo wa ntchito mnzanga, ndi Lukiyo, ndi Yasoni, ndi Sosipatro abale anga akupatsani moni inu. 22 Ine Tertiyo, amene ndikulemba kalatayi ndi kupatsani moni mwa Ambuye. 23 Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupatsani moni inu. Erasto, msungachuma wa mzinda akupatsani moni, ndiponso Kwarto m`baleyo. 24 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Amen. 25 Tsopano kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwabvumbulutso la chinsinsi chimene mobisika kuyambira chilengedwere dziko lapansi. 26 Koma chawonetsedwa tsopano mwa malembo a aneneri, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti kudziwitsidwe kwa mitundu yonse kumvera kwa chikhulupiriro: 27 Kwa Mulungu wa nzeru yekhayo, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu ku nthawi zonse. Ameni.

1 Akorinto 1

1 Paulo, woyitanidwa akhale mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sositene m’bale wathu, 2 Kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m’Korinto, ndiwo woyeretsedwa mwa Khristu Yesu, woyitanidwa akhale woyera mtima, pamodzi ndi onse akuyitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m’malo monse, ndiye wawo, ndi wathu: 3 Chisomo chikhale kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. 4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu; 5 Kuti m’zonse muli achuma mwa Iye, m’mawu onse, ndi chidziwitso chonse; 6 Monga momwe umboni wa Khristu udakhazikika mwa inu: 7 Kotero kuti siyikusowani inu; mphatso pakulindira inu kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu: 8 Amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale wopanda chilema m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu. 9 Mulungu ali wokhulupirika amene mudayitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu. 10 Koma ndikudandawulirani inu, abale mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzi modzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mwangwiro mu m`mtima umodzi womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho. 11 Pakuti zidamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu. 12 Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu. 13 Kodi Khristu wagawika? Kodi Paulo adapachikidwa chifukwa cha inu? Kapena kodi mudabatizidwa m’dzina la Paulo? 14 Ndiyamika Mulungu kuti sindidabatiza m’modzi yense wa inu, koma Krispo ndi Gayo; 15 Kuti anganene m’modzi kuti mwabatizidwa m’dzina langa. 16 Koma ndidabatizanso a pa banja la Stefana; za ena, sindidziwa ngati ndidabatiza wina yense. 17 Pakuti Khristu sadandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mawu, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake. 18 Pakuti kulalikira kwa mtanda kuli ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tiri kupulumutsidwa ndi mphamvu ya Mulungu. 19 Pakuti kwalembedwa, Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa wochenjera ndidzakutha. 20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sadayipusitsa nzeru ya dziko lapansi? 21 Pakuti popeza m’nzeru ya Mulungu dziko la pansi, mwa nzeru yake, silidadziwa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa wokhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira. 22 Ndipo popeza Ayuda afuna zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru: 23 Koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa a helene chinthu chopusa: 24 Koma kwa iwo woyitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu. 25 Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zawo; ndipo chofowoka cha Mulungu chiposa anthu mphamvu zawo. 26 Pakuti penyani mayitanidwe anu, abale, kuti sayitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, ayi: 27 Koma Mulungu adasankhula zopusa za dziko lapansi kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo Mulungu adazisankhula zinthu zofowoka za dziko la pansi kuti akachititse manyazi zamphamvu; 28 Ndipo zinthu zopanda pake za dziko lapansi, ndi zinthu zonyozeka, adazisankhula Mulungu, inde ndi zinthu zoti kulibe kuti zikathere zinthu zoti ziliko. 29 Kuti thupi liri lonse lisadzitamande pamaso pake. 30 Koma kwa iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene adayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiwombolo: 31 Kuti monga kwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamandire mwa Ambuye.

1 Akorinto 2

1 Ndipo ine, abale, m’mene ndidadza kwa inu, sindidadza ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru, poyankhula kwa inu umboni wa Mulungu. 2 Pakuti ndidatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu pakati pa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa. 3 Ndipo ine ndidakhala nanu mu ufowoko ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri. 4 Ndipo mawu anga ndi kulalikira kwanga sikudakhala ndi mawu wokopa anzeru, koma m’chiwonetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; 5 Kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu. 6 Koma tiyankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu anthawi yino ya pansi pano, amene alimkuthedwa: 7 Koma tiyankhula nzeru ya Mulungu m’chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu adayikiratu, pasadakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu: 8 Imene sadayidziwa m’modzi wa akulu anthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero. 9 Koma monga kwalembedwa, zimene diso silidaziwona, ndi khutu silidazimva, nisizidalowa mu mtima wa munthu, zimene zili zonse Mulungu adakonzereratu iwo akumkonda Iye. 10 Koma kwa ife Mulungu wabvumbulutsa adatiwonetsera izo kwa ife mwa Mzimu wake; pakuti Mzimu asanthula zinthu zonse, inde zinthu zakuya za Mulungu. 11 Pakuti ndani wa anthu adziwa zinthu za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwenso zinthu za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu. 12 Koma sitidalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zinthu zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwa ulere. 13 Zinthu zimenenso tiyankhula, si ndi mawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma wophunzitsidwa ndi Mzimu; kulinganiza zinthu za mzimu ndi za mzimu. 14 Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwa uzimu. 15 Koma iye amene ali wa uzimu ayesa zinthu zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi munthu. 16 Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tiri nawo mtima wa Khrstu.

1 Akorinto 3

1 Ndipo ine, abale sindidakhoza kuyankhula ndi inu monga ndi a uzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. 2 Ndidadyetsa inu mkaka, sichakudya cholimba ayi; pakuti simudachikhoza; ngakhale tsopano lino simuchikhoza; pakuti muli athupi. 3 Pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndewu ndi mpatuko pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu? 4 Pakuti wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mzake, ndine wa Apolo; simuli athupi kodi? 5 Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene mudakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye adampatsa. 6 Ndidadzala ine, adathilira Apolo; koma Mulungu adakulitsa. 7 Chotero sali kanthu iye wobzala kanthu kalikonse kapena wothilirayo; koma Mulungu amene akulitsa. 8 Tsopano Iye wobzalayo ndi iye wothilirayo ali amodzi; ndipo munthu aliyense adzalandira mphotho yake ya iye yekha monga mwa ntchito yake ya iye. 9 Pakuti ife ndife antchito pamodzi ndi Mulungu; olima a Mulungu, nyumba ya Mulungu ndi inu. 10 Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndidayika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang’anire umo amangira pamenepo. 11 Pakuti palibe munthu wina akhoza kuyika maziko ena, koma amene ayikidwako, ndiwo Yesu Khristu. 12 Tsopano ngati munthu wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu. 13 Ntchito ya munthu aliyense idzawonetsedwa; pakuti tsikulo lidzayisonyeza, chifukwa kuti idzabvumbuluka mmoto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya munthu ali yense idzakhala yotani. 14 Ngati ntchito ya munthu ali yense ikhala imene adayimangako pamenepo, adzalandira mphotho. 15 Ngati ntchito ya munthu wina idzatenthedwa, zidzawonongeka zake zonse; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto. 16 Kodi simudziwa kuti muli kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu akhala mwa inu? 17 Ngati munthu aliyense awononga kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuwononga; pakuti kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu. 18 Munthu aliyense asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu dziko lino la pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. 19 Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m’chenjerero lawo. 20 Ndiponso Ambuye azindikira zolingalira za anzeru, kuti ziri zopanda pake. 21 Chifukwa chake palibe munthu m’modzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse mzanu. 22 Ngakhale Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena ziri mkudza; zonse ndi zanu; 23 Koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.

1 Akorinto 4

1 Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu. 2 Komatu pano pakufunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika. 3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang’ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu, kuweruzidwa ndi munthu: inde sindidziweruza ndekha. 4 Pakuti sindidziwa kanthu mwa ine ndekha chotero sindiri pano monga wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye. 5 Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzawonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nawo uyamiko wake wa kwa Mulungu. 6 Koma izi abale ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitilira zimene zilembedwa; kuti pasakhale m’modzi wodzitukumulira wina ndi mzake. 7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani ndi wina? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sudachilandira? 8 Tsopano mwakhuta, tsopano mwalemerera kale, mwalamulira monga mafumu wopanda ife; ndipo ndidakakonda kwa Mulungu kuti inu mulamulire kuti ifenso tikalamulire limodzi ndi inu. 9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu adakhazikitsa ife atumwi wotsiriza, monga kudayikidwa ku imfa monga tili ife; pakuti takhala ife chowonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu. 10 Tiri wopusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli wanzeru inu mwa Khristu; tiri ife wofowoka, koma inu amphamvu; inu ndinu wolemekezeka, koma ife ndife wonyozeka. 11 Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tiri amaliseche, tikhomedwa, tiribe malo okhala; 12 Ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipilira; 13 Ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa zadziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano. 14 Sindilembera zinthu izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga wokondedwa. 15 Pakuti mungakhale muli nawo aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndabala inu mwa Uthenga Wabwino. 16 Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine. 17 Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo m’Mipingo yonse. 18 Koma ena adzitukumula, monga ngati sindidalimkudza kwa inu. 19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mawu a iwo wodzitukumula, koma mphamvuyi. 20 Pakuti ufumu wa Mulungu siuli m’mawu, koma mumphamvu. 21 Mufuna chiyani? Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

1 Akorinto 5

1 Kwamveka ndithu kuti kuli chiwerewere pakati pa inu, ndipo chiwerewere chotere chonga sichimveka mwa a mitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake. 2 Ndipo mukhala wodzitukumula, osati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene adachita ntchito iyi. 3 Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndidaliko, zokhudzana ndi iye adachita ntchito iyi, 4 M’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu. 5 Kumpereka iye wochita chotere kwa satana, kuti liwonongeke thupi, kuti mzimu, upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye Yesu. 6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse? 7 Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli wosatupa. Pakuti Khristu Pasakha wathu waperekedwa chifukwa cha ife: 8 Chifukwa cake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuyipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuwona mtima, ndi chowonadi: 9 Ndidalembera inu, m’kalata uja, kuti musayanjana ndi achiwerewere; 10 Si konse konse ndi a chiwerewere a dziko lino lapansi, kapena osirira, ndi wolanda kapena ndi wopembedza mafano; pakuti mkutero mukatuLuka m’dziko lapansi. 11 Koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachiwerewere, kapena wosilira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, ayi: 12 Pakuti nditani nawo akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m’katimo simuwaweruza ndi inu? 13 Koma iwo akunja awaweruza Mulungu? Chotsani munthu woyipayo pakati pa inu nokha.

1 Akorinto 6

1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nawo mlandu pa mzake, kupita kukaweruzidwa kwa wosalungama, osati kwa woyera mtima? 2 Kapena kodi simudziwa kuti woyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi lidzaweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? 3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno? 4 Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe mu Mpingo. 5 Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe m’modzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale? 6 Koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa wosakhulupirira. 7 Koma pamenepo pali chosowa konse konse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuyipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa? 8 Koma muyipsa, nimunyenga, ndipo mutero nawo abale anu. 9 Kapena simudziwa kuti wosalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; achiwerewere, kapena wopembedza mafano, kapena achigololo, kapena akudzipsa okha ndi manthanyula. 10 Kapena mbala, kapena wosilira, kapena woledzera, kapena wolalatira, kapena wolanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 11 Ndipo ena a inu mudali wotere: koma mudasambitsidwa, koma mudayeretsedwa, koma mudayesedwa wolungama, m’dzina la Ambuye Yesu ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu. 12 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi. 13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzawononga iyi ndi izi. Koma thupi siliri la chiwerewere, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi. 14 Koma Mulungu adawukitsa Ambuye, ndiponso adzawukitsa ife mwa mphamvu yake. 15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero ayi. 16 Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi. 17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi. 18 Thawani chiwerewere. Tchimo liri lonse munthu akalichita liri kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. 19 M`chiyani kodi? simudziwa kuti thupi lanu liri kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu ndipo simukhala a inu nokha? 20 Pakuti mudagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu, ndi mu mzimu wanu, zimene ziri zake za Mulungu.

1 Akorinto 7

1 Koma za izi mudandilembera inezi: kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi. 2 Komabe poletsa chiwerewere munthu aliyense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha. 3 Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna. 4 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; ndipo momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mkazi ndiye. 5 Musamakanizana wina ndi mzake koma kubvomerezana kwanu, ndiko kwa nthawi, kuti mukadzipereke kukasala ndi kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu. 6 Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa lamulo. 7 Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti. 8 Koma ndinena kwa wosakwatira ndi kwa akazi a masiye, kuti kuli bwino iwo ngati akhala monganso ine. 9 Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha thupi. 10 Koma wokwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ayi, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna: 11 Komanso ngati amsiya akhale wosakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi. 12 Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye: ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. 13 Ndipo mkazi ngati ali naye mwamuna wosakhulupira, nabvomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo 14 Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mwamunayo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala woyera. 15 Koma ngati wosakhulupirayo achoka, achoke, m’milandu yotere samangidwa ukapolo mwamunayo, kapena mkaziyo: koma Mulungu watiyitana ife mumtendere. 16 Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi? 17 Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu ayitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiyika m’Mipingo yonse. 18 Kodi wayitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi wayitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe. 19 Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusungu kwa malamulo a Mulungu. 20 Munthu ali yense akhale m’mayitanidwe m’mene adayitanidwamo. 21 Kodi udayitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko. 22 Pakuti iye amene adayitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woyitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu. 23 Mudagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu. 24 Abale, munthu aliyense akhale m’mene adayitanidwamo momwemo akhale ndi Mulungu. 25 Koma kunena za anamwali, ndiribe lamulo la Ambuye; koma ndipereka kuweruza kwanga, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika. 26 Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chibvuto cha nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali. 27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi. 28 Koma ungakhale ukwatira, sudachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sadachimwa. Koma wotere adzakhala nacho chibvuto m’thupi, ndipo ndikulekani. 29 Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe; 30 Ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu. 31 Ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti mawonekedwe adziko ili apita. 32 Koma ndifuna kuti mukhale wosalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye. 33 Koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. 34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo. 35 Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, wopanda chochewukitsa. 36 Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wa mkazi chosamuyenera, ngati pali kupitilira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. 37 Koma iye amene ayima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nawo ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wa mkazi unamwali wake, adzachita bwino. 38 Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita bwino koposa. 39 Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, pokhapokha mwa Ambuye. 40 Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuweruza kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri naye Mzimu wa Mulungu.

1 Akorinto 8

1 Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: tidziwa kuti tiri nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chidzitukumula, koma chikondi chimangilira. 2 Ngati munthu aliyense ayesa kuti adziwa kanthu sadayambe kudziwa monga ayenera kudziwa. 3 Koma ngati munthu aliyense akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye. 4 Tsono kunena za kudya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano siliri kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma m’modzi. 5 Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m’mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri. 6 Koma kwa ife kuli Mulungu m’modzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye m’modzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse ziri mwa Iye, ndi ife mwa Iye. 7 Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, wozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chawo, popeza nchofowoka, chidetsedwa. 8 Koma chakudya sichitibvomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tiribe kupindulako. 9 Koma yang’anirani kuti ufulu wanu umene ungakhale chokhumudwitsa wofowokawo. 10 Pakuti ngati munthu aliyense akawona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya m’kachisi wa fano, kodi chikumbumtima chake, popeza ali wofowoka, sichidzalimbikitsidwa kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano? 11 Pakuti mwa chidziwitso chako wofowokayo atayika, ndiye mbale amene Khristu adamfera. 12 Koma pakuchimwira abale, ndi kubvulaza chikumbumtima chawo chofowoka, muchimwira kotero Khristu. 13 Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama ku nthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse m`bale wanga.

1 Akorinto 9

1 Kodi sindine mtumwi? Kodi sindine mfulu? Kodi sindidawona Yesu Khristu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye? 2 Ngati sindiri mtumwi kwa ena, komatu ndiri kwa inu: pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye. 3 Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi, 4 Kodi tiribe ulamuliro wa kudya ndi kumwa? 5 Kodi tiribe ulamuliro wakuyendayenda naye mulongo mkazi, monganso atumwi ena, ndi abale wa Ambuye ndi Kefa? 6 Kapena kodi ife tokha, Barnaba ndi ine, tiribe ulamuliro wakusagwira ntchito? 7 Msilikari ndani achita nkhondo, nthawi ili yonse nadzifunira zake yekha? Awoka mpesa ndani, wosadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, wosadya mkaka wake wa gululo? 8 Kodi ndiyankhula izi monga mwa anthu? ndinena zinthu izi monga munthu? Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo? 9 Pakuti m’chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamiza ng’ombe pakupuntha iyo tirigu. Kodi Mulungu asamalira ng’ombe? 10 Kapena achinena ichi konse konse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nawo. 11 Ngati takufeserani inu zinthu za uzimu, ndi chithu chachikulu ngati ife tituta za thupi lanu? 12 Ngati ena ali nawo ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitidachita nawo ulamuliro umene; koma timalola tonse, kuti tingachite chotchinga Uthenga Wabwino wa Khristu. 13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za kachisi amadya za m’kachisi, ndi iwo akuyimilira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe? 14 Chomwechonso Ambuye adalamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino. 15 Koma ine sindidachita nako kanthu ka zinthu izi: ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti, kundikomera ine kufa, koma wina asayesa kwachabe kudzitamanda kwanga. 16 Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndiribe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; inde tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino. 17 Pakuti ngati ndichita ichi chibvomerere, mphotho ndiri nayo; koma ngati si chibvomerere, adandikhulupirira ine mu udindo wa uthenga wabwino umene udaperekedwa kwa ine. 18 Mphotho yanga nchiyani tsono? Indetu kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale wa ulere, kuti ndisayipse ulamuliro wanga mu Uthenga Wabwino. 19 Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa anthu onse, ndidadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule wochuluka. 20 Ndipo kwa Ayuda ndidakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo womvera lamulo monga womvera lamulo kuti ndipindule iwo womvera malamulo; 21 Kwa iwo wopanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo wopanda lamulo. 22 Kwa wofowola ndidakhala ngati wofowoka, kuti ndipindule iwo wofowoka. Ndakhala zinthu zonse kwa anthu onse, kuti pali ponse ndikapulumutse ena. 23 Koma ndichita izi zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale wogawana naye.. 24 Kodi simudziwa kuti iwo akuchita mpikisano wa liwiro, athamangadi onse, koma m’modzi alandira mphotho? Motero thamangani, kuti mukalandire. 25 Koma munthu ali yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wobvunda koma ife wosabvunda. 26 Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati modzi womenyana wopanda kanthu.; 27 Koma ndisunga thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wosayenera ndekha kulandira mphoto.

1 Akorinto 10

1 Pakuti sindifuna, kuti mukhale wosadziwa, abale, kuti makolo athu onse adali pansi pa mtambo, nawoloka nyanja onse; 2 Nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m’nyanja, 3 Ndipo nadya onse chakudya cha uzimu chimodzimodzi; 4 Ndipo namwa onse chakumwa cha uzimu chimodzimodzi; pakuti adamwa mwa thandwe la uzimu lakuwatsata; koma thandwelo ndiye Khristu. 5 Koma wochuluka a iwo Mulungu sadakondwera nawo; pakuti adawataya m’chipululu. 6 Koma zinthu izi ndi chitsanzo chathu ndi cholinga kuti tisalakalake zoyipa ife, monganso iwowo adalakalaka. 7 Kapena musakhale wopembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu adakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera. 8 Kapena tisachite dama monga ena a iwo adachita chiwerewere, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu. 9 Kapena tisayese Khristu monga ena a iwo adayesa, nawonongeka ndi njoka zija. 10 Kapena musadandaule, monga ena a iwo anadandaula, nawonongeka ndi wowonongayo. 11 Koma izi zidachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zidalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife. 12 Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiliri, ayang’anire kuti angagwe. 13 Sichidakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzayikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupilirako. 14 Chifukwa chake, wokondedwa anga, thawani kupembedza mafano. 15 Ndinena monga kwa anthu anzeru; lingilirani inu chimene ndinena ndi ziwanda. 16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa sichiri chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi? 17 Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse tigawana ku mkate umodzi. 18 Tapenyani Israyeli monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe kugawana ndi guwa la nsembe? 19 Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chiri kanthu? Kapena kuti fano liri kanthu kodi? 20 Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda;ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda. 21 Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye ndi ku gome la ziwanda. 22 Kodi kapena tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye? 23 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse, zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse. 24 Munthu asafune zake za iye yekha koma za mzake. 25 Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima. 26 Pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwake. 27 Ngati wina wa wosakhulupirira akuyitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiyikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbumtima. 28 Koma ngati wina akati kw ainu, yoperekedwa nsembe kwa mafano iyi, musadye, chifukwa cha iye wakuwuzayo, ndi chifukwa cha chikumbumtima; pakuti dziko lapansi liri la Ambuye ndi zonse za mkati mwake. 29 Ndinena chikumbumtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbumtima cha wina? 30 Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji zoipa chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo? 31 Chifukwa chake, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena Mpingo wa Mulungu. 33 Monga inenso ndikondweretsa onse m’zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha ambiri, kuti apulumutsidwe.

1 Akorinto 11

1 Khalani wonditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu. 2 Ndipo ndikutamandani inu abale kuti m’zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndidapereka kwa inu. 3 Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa mwamuna aliyense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu. 4 Mwamuna aliyense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake. 5 Koma mkazi aliyense popemphera kapena kunenera wobvula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa. 6 Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde. 7 Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna. 8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna. 9 Pakutinso mwamuna sadalengedwa chifukwa cha mkazi; koma mkazi chifukwa cha mwamuna. 10 Chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nawo ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo. 11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi mwa Ambuye. 12 Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mulungu. 13 Lingilirani mwa inu nokha; kodi nkuyenera kuti mkazi apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu? 14 Kodi chibadwidwe sichitiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chimnyozetsa iye? 15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba. 16 Koma akawoneka munthu wina achita ngati motetana, tiribe makhalidwe wotere, kapena ife, kapena mipingo ya Mulungu. 17 Tsopano pakulengeza ichi mwa inu sindikutamani inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choyipa. 18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndibvomereza penapo. 19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo wobvomerezedwa awonetsedwe pakati pa inu. 20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi simusonkhanira kudya mgonero wa Ambuye. 21 Pakuti pakudyaku aliyense ayambe watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera. 22 Chiyani? mulibe nyumba zodyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m’menemo? Sindikutamani. 23 Pakuti ine ndidalandira kwa Ambuye, chimenenso ndidapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja adaperekedwa, adatenga mkate. 24 Ndipo m’mene adayamika, adawunyema, ndipo adati, Tengani, idyani, ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa. 25 Koteronso chikho chitatha chakudya, ndi kuti, chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse; mukamwa chikhale chikumbukiro changa. 26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye. 27 Chifukwa chake, yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye. 28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate umenewo, ndi kumwera chikho chimenecho. 29 Pakuti iye wakudya ndi kumwa kosayenera, akadya ndi kumwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupi la Ambuyelo. 30 Chifukwa chake ambiri mwa inu afowoka, nadwala, ndipo ambiri agona. 31 Koma ngati tikadakaziweruza tokha sitikadaweruzidwa. 32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi. 33 Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani. 34 Ngati wina ali ndi njala adye kwawo; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.

1 Akorinto 12

1 Koma zamphatso za uzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa. 2 Mudziwa kuti pamene mudali amitundu, mudatengedwa kumka kwa mafano aja wosayankhula, monga mudatsogozedwa. 3 Chifukwa chake, ndikuwuzani inu, kuti palibe munthu wakuyankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera. 4 Ndipo pali mphatso zosiyana koma Mzimu yemweyo. 5 Ndipo pali utumiki wosiyana, koma Ambuye yemweyo. 6 Ndipo pali machitidwe wosiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse. 7 Koma kwa onse kwapatsidwa mawonekedwe a Mzimu kuti apindule nawo, 8 Pakuti kwa m’modzi kwapatsidwa mwa Mzimu mawu a nzeru; koma kwa mzake mawu a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo. 9 Ndi kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu m’modziyo; 10 Ndi kwa wina zozizwitsa za mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime; 11 Koma zonse za izi achita Mzimu m’modzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afunira. 12 Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonse zathupi limodzilo zili thupi limodzi momwemonso Khristu. 13 Pakutinso mwa Mzimu m’modzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m’thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tidmwetsedwa Mzimu m’modzi. 14 Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi , koma zambiri. 15 Ngati phazi likati, popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi chifukwa cha ichi? 16 Ndipo ngati khutu likati, popeza sindiri wa diso, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi chifukwa cha ichi? 17 Ngati thupi lonse likadakhala diso kukadakhala kuti kumvera. Ngati thupi lonse lidakakhala khutu kukada khala kuti kununkhiza? 18 Koma tsopano, Mulungu adayika ziwalo zonsezo m’thupi, monga kudamkondweretsa. 19 Koma ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi; likadakhala kuti thupi? 20 Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi. 21 Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, sindikufunani inu. 22 Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofowoka m’thupi, zifunika kwambiri: 23 Ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m’thupi, pa izi tiyika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa. 24 Koma zokoma zathu ziribe kusowa; koma Mulungu adalumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho; kuti kusakhale chisiyano m’thupi. 25 Kuti pasakhale kugawanika m`thupi koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chimzake. 26 Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva zowawa ziwalo zina zimva kuwawa pamodzi nacho, chingakhale chiwalo chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi. 27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha. 28 Ndipotu Mulungu adayika ena mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, kulongosola ntchito, malilime a mitundu mitundu. 29 Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali onse aphunzitsi kodi? Ali wonse wochita zozizwa? 30 Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse ayankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira? 31 Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuwonetsani njira yokoma yoposatu.

1 Akorinto 13

1 Ndingakhale ndiyankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe chikondi, ndikhala mkuwa wowomba, kapena nguli yolira. 2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi ndiri chabe. 3 Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa wosawuka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndiribe chikondi, sindipindula kanthu ayi. 4 Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikudza, 5 Sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima msanga, sichilingilira zoyipa; 6 Sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi chowonadi; 7 Chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipilira zinthu zonse. 8 Chikondi sichimalephera, koma kapena zonenera zidzalephera, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzatha 9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. 10 Koma pamene changwiro chafika, tsono cha mderamdera chidzamalizika. 11 Pamene ndidali mwana ndidayankhula monga mwana, ndidamvetsa monga mwana, ndidanganiza monga mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa zinthu chabe za chibwana. 12 Pakuti tsopano tipenya m’kalilore, ngati m`chilape; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. 13 Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi:

1 Akorinto 14

1 Tsatani chikondi, koma funitsitsani mphatso za uzimu, koma koposa kuti mukanenere. 2 Pakuti iye wakuyankhula lilime sayankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu ayankhula zinsinsi. 3 Koma iye wakunenera ayankhula ndi anthu chomangilira ndi cholimbikitsa, ndi chotothoza. 4 Iye wakuyankhula lilime, adzimangilira yekha, koma iye wakunenera amangilira Mpingo. 5 Ndipo ndifuna inu nonse muyankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakuyankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangilira. 6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kuyankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindiyankhula ndi inu kapena m’bvumbulutso, kapena m’chidziwitso, kapena m’chinenero, kapena m’chiphunzitso. 7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mawu, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa malilidwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiwombedwa kapena kuyimbidwa? 8 Pakuti ngati lipenga lipereka mawu wosazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo? 9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mawu womveka bwino, chidzazindikirika bwanji chimene chiyankhulidwa? Pakuti mudzayankhula mosapindulitsa. 10 Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mawu pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa tanthawuzo 11 Chifukwa chake, ngati sindidziwa tanthawuzo la mawuwo ndidzakhala kwa iye woyankhulayo wakunja, ndipo woyankhulayo adzakhala wakunja kwa ine. 12 Momwemo inunso, popeza muli wofunitsitsa mphatso za uzimu, funani kuti mukachuLuka kukumangilira kwa Mpingo. 13 Chifukwa chake iye woyankhula lilime, apemphere kuti iye amasulire. 14 Pakuti ngati ndipemphera m’lilime mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu. 15 Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi chidziwitso. 16 Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala nawe m`chipinda wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena? 17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiliridwa. 18 Ndiyamika Mulungu kuti ndiyankhula malilime koposa inu nonse; 19 Koma mu mpingo ndifuna kuyankhula mawu asanu ndi chidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kuyankhula mawu zikwi khumi m’malilime. 20 Abale, musakhale ana m’chidziwitso, koma m’choyipa khalani makanda, koma m’chidziwitso akulu misinkhu. 21 Kwalembedwa m’chilamulo, ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzayankhula nawo anthu awa: ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. 22 Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo wosakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira. 23 Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akayankhule malilime, ndipo akalowemo anthu wosaphunzira, kapena wosakhulupira, kodi sadzanena kuti mwachita misala? 24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, akhutitsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; 25 Chotero zobisika za mtima wake zidzawonetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu. 26 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangilira. 27 Ngati munthu wina ayankhula malilime, achite ndi awiri, koma woposa atatu ayi, ndipo motsatana; ndipo m’modzi amasulire. 28 Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma ayankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu. 29 Ndipo aneneri ayankhule awiri kapena atatu, ndi ena aweruze. 30 Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo. 31 Pakuti mukhoza nonse kunenera m’modzi m’modzi, kuti onse aphunzire, ndi onse aatonthozedwe. 32 Ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; 33 Pakuti Mulungu sali woyambitsa chisokonezo koma wa mtendere, monga mwa Mipingo yonse ya woyera mtima. 34 Akazi anu akhale chete m’Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kuyankhula. Koma akhale womvera, monganso chilamulo chinena. 35 Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna awo a iwo wokha kwawo: pakuti kunyanzitsa mkazi kuyankhula mu Mpingo. 36 Chiyani? Mawu a Mulungu adatuluka kwa inu? Kapena adafika kwa inu nokha? 37 Ngati wina ayesa kuti ali m’neneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye. 38 Koma ngati wina akhala wosadziwa, akhale wosadziwa. 39 Chifukwa chake, abale anga funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kuyankhula malilime. 40 Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.

1 Akorinto 15

1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani inu, umenenso mudalandira, umenenso muyimamo. 2 Umenenso mupulumutsidwa nawo ngati muwusunga monga momwe ndidalalikira kwa inu; ngati simudakhulupira chabe. 3 Pakuti ndidapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndidalandira, kuti Khristu adafera zoyipa zathu, monga mwa malembo; 4 Ndi kuti adayikidwa; ndi kuti adawukitsidwa tsiku la chitatu, monga mwa malembo; 5 Ndi kuti adawonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo; 6 Pomwepo adawoneka pa nthawi imodzi kwa abale woposa mazana asanu, amene wochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena adagona. 7 Pomwepo adawonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse. 8 Ndipo potsiriza pake pa onse, adawoneka kwa inenso monga mtayo. 9 Pakuti ine ndiri wam’ng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndidazunza mpingo wa Mulungu. 10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichidakhala chopanda pake, koma ndidagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine. 11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero mudakhulupira. 12 Koma ngati Khristu alalikidwa kuti wawukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuwuka kwa akufa? 13 Koma ngati kulibe kuwuka kwa akufa, Khristunso sadawukitsidwa; 14 Ndipo ngati Khristu sadawukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chiri chabe. 15 Inde ndipo ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tidachita umboni kunena za Mulungu kuti adawukitsa Khristu; amene sawukitsidwa, ngati kuli tero kuti akufa sadawukitsidwa: 16 Pakuti ngati akufa sadawukitsidwa, Khristunso sadawukitsidwa 17 Ndipo ngati Khristu sawukitsidwa, chikhulupiriro chanu chiri chopanda pake; muli chikhalire m’machimo anu. 18 Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu adatayika. 19 Ngati tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tiri ife aumphawi woposa wa anthu onse. 20 Koma tsopano Khristu wawukitsidwa kwa akufa, chipatso chowundukura cha iwo akugona. 21 Pakuti monga imfa idadza mwa munthu kuwuka kwa akufa kudadzanso mwa munthu. 22 Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, chotero mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo. 23 Koma munthu aliyense m’dongosolo lake la iye yekha, Khristu chipatso choyamba pambuyo pake iwo a Khristu; pomwepo iwo a Khristu pakubwera kwake. 24 Pomwepo padzafika chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, pamene adzathetsa ulamuliro wonse,ndi mphamvuzonse. 25 Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira atayika adani onse pansi pa mapazi ake. 26 Mdani wotsiriza amene adzawonongedwa ndiye imfa. 27 Pakuti Iye adagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene adagonjetsa zonsezo kwa Iye. 28 Ndipo pamene zonsezi zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene adamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse. 29 Ngati sikutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa sawukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha akufa? 30 Nanga ifenso tiri m’mowopsa bwanji nthawi zonse? 31 Nditsutsa chifukwa cha chimwemwe chanu chimene ndiri nacho mwa Khristu Yesu Ambuye wathu, ndifa tsiku ndi tsiku. 32 Ngati mwa khalidwe la wathu ndidalimbana ndi zirombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa sawukitsidwa tidye, timwe pakuti mawa timwalira. 33 Musanyengedwe; chiyanjano choyipa chiyipsa makhalidwe wokoma. 34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu: ndiyankhula kunyazitsa inu. 35 Koma munthu wina adzati, Akufa awukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani? 36 Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa: 37 Ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbewu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina: 38 Koma Mulungu ayipatsa thupi longa afuna; ndi kwa mbewu yonse thupi lake lake. 39 Nyama yonse siyili imodzimodzi; koma yina ndi ya anthu, ndi yina ndiyo nyama ya zoweta, ndi yina ndiyo nyama ya mbalame, ndi yina ya nsomba. 40 Palinso matupi a m’mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa la m’mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso. 41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi ina mu ulemerero. 42 Chomwechonso kudzakhala kuwuka kwa akufa. Lifesedwa m’chibvundi, liwukitsidwa m’chisabvundi: 43 Lifesedwa mu m’nyozo, liwukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m’chifowoko, liwukitsidwa mumphamvu. 44 Lifesedwa thupi la chibadwidwe, liwukutsidwa thupi la uzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu. 45 Koteronso kwalembedwa, munthu woyamba Adamu, adakhala mzimu wamoyo; Adamu wotsiriza adakhala mzimu wakupatsa moyo. 46 Koma cha uzimu sichiri choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo cha uzimu. 47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka; munthu wachiwiri ndiye Ambuye wakumwamba. 48 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba. 49 Ndipo monga tabvala fanizo la wanthakayo, tidzabvalanso fanizo la wakumwambayo. 50 Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chibvundi sichilowa chisabvundi. 51 Tawonani ndikuwuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, 52 M’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzawukitsidwa wosabvunda, ndipo ife tidzasandulika. 53 Pakuti chobvunda ichi chiyenera kubvala chisabvundi, ndi cha imfa ichi kubvala chosafa. 54 Ndipo pamene chobvunda ichi chikadzabvala chisabvundi ndi cha imfa ichi chikadzabvala chosafa, pamenepo padzachitika mawu wolembedwa, Imfayo yamezedwa mchigonjetso. 55 Haa imfa ululu wako uli kuti?Haa imfa,manda ako ali kuti? chigonjetso chako chiri kuti? 56 Koma ululu wa imfa ndiwo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndicho chilamulo. 57 Koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khris 58 Chifukwa chake, abale anga wokondedwa, khalani wokhazikika, wosasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

1 Akorinto 16

1 Tsopano kunena za chopereka cha kwa woyera mtima, monga ndidalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso. 2 Pa tsiku loyamba la sabata aliyense wa inu asunge yekha, monga momwe adapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine. 3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa woyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu. 4 Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane. 5 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya; pakuti ndidzapyola Makedoniya. 6 Ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yozizira kuti mukandiperekeze ine kumene kuli konse ndipitako. 7 Pakuti sindifuna kukuwonani tsopano popitilira: pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye. 8 Koma ndidzakhala ku Aefeso kufikira Pentekoste. 9 Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo woletsana nafe ndi ambiri. 10 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha: pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine. 11 Chifukwa chake munthu aliyense asampeputse: koma mumperekeze mumtendere kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera ine pamodzi ndi abale. 12 Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuwumiliza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichidali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene awona nthawi. 13 Dikirani, chirimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani. 14 Zinthu zanu zonse zichitike m’chikondi. 15 Koma ndikupemphani inu, abale (mudziwa banja la Stefana, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti adadziyika wokha kutumikira woyera mtima.) 16 Kuti inunso mubvomere wotere, ndi yense wakuchita nawo, ndi kugwiritsa ntchito. 17 Koma ndikondwera pa kudza kwawo kwa Stefana, ndi Fortunato, ndi Akayiko; chifukwa iwo adandikwaniritsa chotsalira chanu. 18 Pakuti adatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muwazindikire wotere. 19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni inu. Akupatsani ndithu moni mwa Ambuye, Akula ndi Priska, pamodzi ndi mpingo wa m’nyumba yawo. 20 Abale onse akupatsani moni Patsanani moni ndi kupsopsonana kopatulika. 21 Moni wa ine Paulo ndi dzanja langa. 22 Ngati munthu wina sakonda Ambuye Yesu Khristu, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye. 23 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu. 24 Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Ameni.

2 Akorinto 1

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu ndi Timoteo m’bale wathu, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi woyera mtima onse amene ali mu Akaya lonse: 2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. 3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse; 4 Wotitonthoza ife mu msautso yathu yonse , kuti tikathe ife kutonthoza iwo wokhala mu msautso uli yonse, mwa chotonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu. 5 Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu. 6 Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupilira kwa masautso womwewo amene ifenso timva kuti ngati titonthozedwa ndi chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu. 7 Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli woyanjana ndi masautsowo, koteronso chitonthozo. 8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale wosadziwa za chisautso chathu tidakomana nacho mu Asiya, kuti tidathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu: 9 Koma tokha tidakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuwukitsa akufa: 10 Amene adatilanditsa mu imfa yayikulu yotere, nadzatilanditsa ife; Amene timyembekezera kuti adzatilanditsanso; 11 Pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife. 12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m’chiyero ndi kuwona mtima kwa Umulungu, si mu nzeru ya thupi, koma m’chisomo cha Mulungu tidadzisunga m’dziko lapansi, koma koposa kwa inu. 13 Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga kapenanso mubvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti kuzindikira kufikira chimaliziro; 14 Monganso mudatizindikira ife pena, kuti ife ndife chimwemwe chanu, monga momwe inunso muli chimwemwe chathu m’tsiku la Ambuye Yesu. 15 Ndipo m’kulimbika kumene ndidafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nalo phindu lachiwiri; 16 Ndipo popyola kwanu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kuchokera ku Makedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya. 17 Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndidachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, inde, inde ndi ayi, ayi? 18 Koma monga Mulungu ali wowona, kuti mawu athu kwa inu sakhala inde ndi ayi. 19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene adalalikidwa mwa inu ndi ife ine ndi Silivano ndi Timoteo, sadakhala inde ndi ayi, koma adakhala inde mwa Iye. 20 Pakuti monga mwa mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye inde; chifukwa chakenso ali mwa Iye Ameni, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife. 21 Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu mwa Khristu, natidzodza ife, ndiye Mulungu; 22 Amenenso adatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu. 23 Komanso ine ndiyitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti ndidalekerera inu kuti ndisafikenso ku Korinto. 24 Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala wothandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muyimadi.

2 Akorinto 2

1 Koma ndidatsimikiza mtima mwa ine ndekha ndisadzenso kwa inu ndi chisoni. 2 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndam’mvetsa chisoni? 3 Ndipo ndidalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chimwemwe cha inu nonse. 4 Pakuti m’chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndidalembera inu ndi misozi yambiri; sikuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndiri nacho koposa. 5 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sadachititsa chisoni ine, koma pena kuti ndisasenzetse inu nonse. 6 Chilango ichi ndi chokwanira kwa munthu wotere .Chimene chidakhudza ambiri. 7 Kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo angamizidwe ndi chisoni chocholuka. 8 Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu. 9 Pakuti chifukwa cha mathero ano ndalemba, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli womvera m’zonse. 10 Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu mu umunthu wa Khristu. 11 Kuti asatichenjerere Satata; pakuti sitikhala wosadziwa machenjerero ake. 12 Kuwonjezera apa ndinadza ku Trowa kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamenepo padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye. 13 Ndidalibe mpumulo mu mzimu wanga; posapeza ine Tito Mbale wanga; koma polawirana nawo ndidamka ku Makedoniya. 14 Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m’chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo lachidziwitso chake mwa ife pamalo ponse. 15 Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu mwa iwo kupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuwonongeka; 16 Koma kwa ena fungo la imfa ku imfa; ndi kwa ena fungo lamoyo ku moyo. Ndipo azikwanira ndani izi? 17 Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuwononga mawu a Mulungu; koma monga mwa chowona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tiyankhula mwa Khristu.

2 Akorinto 3

1 Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata wotibvomerezetsa kwa inu, kapena wochokera kwa inu? 2 Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse: 3 Popeza mwawonetsedwa kuti muli kalata wa Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi inki, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome a miyala koma m’magome a mitima yathupi. 4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Khristu. 5 Sikuti tiri wokwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu. 6 Amenenso adatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo,komala mzimu pakuti chilembo chipha, koma mzimu apatsa moyo. 7 Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m’miyala, udakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sadathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene udalikuchotsedwa: 8 Nanga utumiki wa Mzimu udzakhala ndi ulemerero wotani? 9 Pakuti ngati utumiki wa chitsutso udali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira mu ulemerero kwambiri. 10 Pakuti chimene chidachitidwa cha ulemerero sichidachitidwa cha ulemerero m’menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo. 11 Pakuti ngati chimene chirikuchotsedwa chidakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chiri mu ulemerero. 12 Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tiyankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu; 13 Ndipo si monga Mose, amene adayika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israyeli asayang’anitse pa chimaliziro cha chimene chidalikuchotsedwa: 14 Koma mitima yawo idachititsidwa khungu; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosabvundukuka, chimene chirikuchotsedwa mwa Khristu. 15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pa mtima pawo. 16 Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, chophimbacho chichotsedwa. 17 Koma Ambuye ndiye Mzimuyo: ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu. 18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirore ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera ku ulemerero kumka ku ulemerero, monga mwa mzimu wa Ambuye .

2 Akorinto 4

1 Chifukwa chake popeza tiri nawo utumiki umenewu, monga talandira chifundo, sitifowoka; 2 Koma takaniza zobisika za manyazi, wosayendayenda mochenjerera kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi mawonekedwe a chowonadi tidzibvomerezetsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu. 3 Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; 4 Mwa amene Mulungu wa nthawi yino yapansi pano udachititsa khungu maganizo awo a wosakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire. 5 Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Khristu Yesu Ambuye ndi ife tokha atumiki anu, chifukwa cha Yesu. 6 Pakuti Mulungu amene adalamulira kuwala kutuLuka mumdima, ndiye amene adawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope ya Yesu Khristu. 7 Koma tiri nacho chuma ichi m’zotengera za dothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife. 8 Ndife wosautsika monsemo, koma wosapsinjika; wosinkhasinkha koma wosakhala kakasi; 9 Wozunzidwa, koma wosatayika; wogwetsedwa, koma wosawonongeka; 10 Nthawi zonse tiri kusenzasenza m’thupi kufa kwake kwa Ambuye Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi mwathu. 11 Pakuti ife amene tiri ndi moyo tiperekeka ku imfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi lathu lakufa. 12 Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu. 13 Koma pokhala nawo mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndidakhulupirira, chifukwa chake ndidayankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tiyankhula; 14 Podziwa kuti Iye amene adawukitsa Ambuye Yesu adzawukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiwonetsa pamodzi ndi inu. 15 Pakuti zinthu zonsezi n`chifukwa cha kwa inu, kuti chisomo, chochulukitsa mwa unyinjiwo, chochulukitsidwa mwakudzera m`mayamiko ambiri akasefukire ku ulemerero wa Mulungu. 16 Chifukwa chake sitifowoka; koma ungakhale umunthu wathu wa kunja ubvunda, munthu wa m’kati mwathu akonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. 17 Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; 18 Popeza sitipenyerera zinthu zowoneka, koma zinthu zosawoneka; pakuti zinthu zowoneka ziri za nthawi, koma zinthu zosawoneka ziri zosatha.

2 Akorinto 5

1 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu yipasuka, tiri nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha m’Mwamba. 2 Pakuti m’menemo tibuwula, ndi kukhumbitsa kubvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera kumwamba. 3 Ngatitu pobvekedwa sitipezedwa amaliseche. 4 Pakutinso ife wokhala mu msasawu tibuwula pothodwa; sikunena kuti tifuna kubvulidwa, koma kubvekedwa, kuti cha imfacho chimezedwe ndi moyo. 5 Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu amene adatipatsa ife chikole cha Mzimu 6 Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tiri kwathu m’thupi, sitiri kwa Ambuye. 7 (Pakuti tiyendayenda chikhulupiriro si mwa mwamawonekedwe:) 8 Koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye. 9 Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye. 10 Pakuti ife tonse tiyenera kuwonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi; monga momwe adachita, kapena chabwino kapena choyipa. 11 Podziwa tsono kuwopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tiwonetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndikhulupirira kuti tiwonetsedwa m’zikumbu mtima zanu. 12 Sitidzibvomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nawo iwo akudzitamandira powoneka pokha, wosati mumtima. 13 Pakuti ngati tiri woyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tiri anzeru zathu, titero kwa inu. 14 Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti m’modzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; 15 Ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo wokha, koma kwa Iye amene adawafera iwo nawuka. 16 Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi koma tsopano sitimzindikiranso chotero. 17 Chifukwa chake ngati munthu ali yense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, tawonani, zakhala zatsopano. 18 Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene adatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Yesu Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso. 19 Ndiko kunena kuti Mulungu adali mwa Khristu, alimkuyanjanitsa dziko lapansi kwa iye yekha, wosawawerengera zolakwa zawo; ndipo adayikiza kwa ife mawu a chiyanjanitso. 20 Chifukwa chake tiri atumiki m’malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu ali kudandaulira mwa ife; tiwumiriza inu m’malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Ameneyo sadadziwa uchimo adamyesera uchimo m’malo mwathu: kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.

2 Akorinto 6

1 Ife pamenepo monga antchito pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu. 2 (Pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndidamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza; tawonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, tawonani, tsopano ndilo tsiku lachipulumutso.) 3 Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chiri chonse, kuti utumikiwo usanenezedwe: 4 Koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu; m’kupilira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja, 5 M’mikwingwirima, m’ndende, m’mapokoso, m’mabvutitso, m’madikiriro, m’masalo a chakudya; 6 M’mayeredwe, m’chidziwitso, m’chilekerero, m’kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m’chikondi chosanyenga, 7 M’Mawu a chowonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa chamuna cha chilungamo kulamanja ndi kulamanzere, 8 Mwa ulemerero, ndi mwa m’nyozo, mwa mbiri yoyipa ndi mbiri yabwino; monga wosocheretsa, ngakhale ali wowona; 9 Monga wosadziwika, ngakhale adziwika bwino; monga ali kufa, ndipo tawonani tiri ndi moyo; monga wolangika, ndipo wosaphedwa; 10 Monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga a umphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga wokhala wopanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse. 11 M’kamwa mwathu m’motseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa. 12 Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu. 13 Ndipo kukhala chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso. 14 Musakhale womangidwa m’goli ndi wosakhulupirira wosiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuwunika kuyanjana bwanji ndi m’dima? 15 Ndipo Khristu abvomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira? 16 Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti inu ndinu kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu adati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga. 17 Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudze kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu, 18 Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana amuna ndi akazi, anena Ambuye Wamphamvu yonse.

2 Akorinto 7

1 Pokhala nawo tsono malonjezano amenewa, wokondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu. 2 Tipatseni malo; sitidamchitira munthu chosalungama, sitidayipsa munthu, sitidachenjerera munthu. 3 Sindinena ichi kuti ndikutsutseni; pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi. 4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m’chisautso chathu chonse. 5 Pakutinso pakudza ife m’Makedoniya thupi lathu lidalibe mpumulo, koma tidasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, mkatimo mantha. 6 Komabe Mulungu amene atonthoza wodzichepetsa, ndiye Mulungu, adatitonthoza ife pa kufika kwake kwa Tito; 7 Koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene adatonthozedwa nacho mwa inu, pamene adatiwuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndidakondwera koposa. 8 Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata uja, sindilapa; ndingakhale ndidalapa; pakuti ndiwona kuti kalata uja adakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yochepa. 9 Tsopano ndikondwera si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni cha kukulapa; pakuti mwamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m’kanthu kali konse. 10 Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuziramtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni, koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa. 11 Pakuti, tawonani, ichi chomwe chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, inde chodzikonza, inde mkwiyo, inde mantha, inde kukhumbitsa inde changu, inde kubwezera chilango! M’zonse mudatsimikizira nokha kuti muli woyera mtima m’menemo. 12 Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindidachita chifukwa cha iye amene adachita choyipa, kapena chifukwa cha iye amene adachitidwa choyipa, koma kuti khama lanu la kwa ife liwonetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu. 13 Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m’chitonthozo chanu,inde tidakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake udatsitsimutsidwa ndi inu nonse. 14 Pakuti ngati ndazitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindidamvetsedwa manyazi; koma monga tidayankhula zonse ndi inu m’chowonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene ndidapanga pamaso pa Tito, kudakhala chowonadi. 15 Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti mudamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira. 16 Ndikondwera kuti mzinthu zonse ndilimbika mtima za inu.

2 Akorinto 8

1 Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwa Mipingo ya ku Makedoniya; 2 Kuti m’chitsimikizo chachikulu cha chisawutso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chawo, ndi kusawuka kwawo kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuwolowa mtima wawo. 3 Pakuti monga mwa mphamvu yawo, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yawo; 4 Adachita eni ake natiwumiriza ndi kutidandawulira za mphatsozo, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa woyera mtima. 5 Ndipo izi adachita, si monga tidayembekeza; koma adayamba kudzipereka wokha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu. 6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga adayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso. 7 Koma monga muchulukira m’zonse m’chikhulupiriro ndi m’mawu, ndi m’chidziwitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m’chisomo ichi. 8 Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena chowonadi cha chikondi chanunso. 9 Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu kuti, chifukwa cha inu adakhala wosawuka, angakhale adali wachuma, kuti inu ndi kusawuka kwake mukakhale wachuma. 10 Ndipo m’menemo ndipereka malangizo anga : pakuti chimene chipindulira inu, amene mudayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira. 11 Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kudali chibvomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m’chimene muli nacho. 12 Pakuti ngati chibvomerezocho chiri pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa. 13 Pakuti sinditero kuti anthu ena akamasuke, ndi inu mulemetsedwe. 14 Koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwawo nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwawo kukwanire kusowa kwanu: kuti pakhale chilingano: 15 Monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichidamtsalira; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichidamsowa. 16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito. 17 Pakutitu adalandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, adatulukira kumka kwa inu mwini wake. 18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli m’Mipingo yonse; 19 Ndipo si ichi chokha, komanso adasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m’chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuwonetsa chibvomerezo chathu; 20 Ndi kupewa ichi kuti munthu asatidandaule za kuchulukira kumene tikutumikira. 21 Pakuti tikonzeretu zinthu zokoma, si pa maso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu. 22 Ndipo tidatumiza mbale wathu awaperekeze iwo amene tamtsimikizira kawiri kawiri ali wakhama m’zinthu zambiri; koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ndiri nako kwa inu. 23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali aumiki a Mipingo, ndi ulemerero wa Khristu. 24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.

2 Akorinto 9

1 Pakuti za utumiki wa kwa woyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu; 2 Pakuti ndidziwa chibvomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amakedoniya, kuti Akaya adakonzekeratu chitapita chaka ndi changu chanu chidautsa wochulukawo. 3 Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m’menemo; kuti monga ndidanena, mukakhale wokonzeratu: 4 Kuti kapena akandiperekeze aku Makedoniya nadzakupezani inu wosakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m’kulimbika kumeneku. 5 Chifukwa chake tidayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati m’dalitso, ndipo si monga mwa kuwumiriza. 6 Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mowuma manja, mowuma manjanso adzatula. Ndipo iye wakufesa mowolowa manja, mowolowa manjanso adzatula. 7 Munthu aliyense achite monga adatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza: pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera. 8 Ndipo Mulungu akonza kuchulukitsa chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m’zinthu zonse, mukachulukire ku ntchito yonse yabwino; 9 (Monga kwalembedwa; Anabalalitsa, adapatsa kwa wosawuka: chilungamo chake chikhala ku nthawi yonse. 10 Ndipo iye wopatsa mbewu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbewu yanu yofesa, nadzawonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu:) 11 Polemeretsedwa inu m’zonse ku kuwolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu. 12 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za woyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri. 13 Popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chibvomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuwolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse; 14 Ndipo iwo, mwa pempherero lawo la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu. 15 Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yosatheka kuneneka.

2 Akorinto 10

1 Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu: 2 Koma ndipempha ine kuti pokhala ndiri pomwepo ndisalimbike mtima ndi kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi. 3 Pakuti pakuyendayenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi. 4 (Pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi; koma zamphamvu mwa Mulungu za kupasula malinga;) 5 Ndikugwetsa malingaliro, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera Khristu; 6 Ndikukhala wokonzeka kubwezera chilango kusamvera konse kudzakwaniridwa. 7 Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati munthu wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, muloleni iye mwa iye yekha aganizirenso ichi, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife tiri a Khristu. 8 Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene adatipatsa Ambuye ku kumangilira, ndipo si ku kugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa: 9 Kuti ndisawoneke monga ngati kukuwopsani mwa akalatawo. 10 Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo wolemera, ndi amphamvu; koma mawonekedwe athupi lake ngofowoka, ndi mawu ake ngachabe. 11 Wotereyo ayese ichi kuti monga tiri ife ndi mawu mwa akalata, pokhala palibe ife, tiri woterenso m’machitidwe pokhala tiri pomwepo. 12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerengera, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomerezetsa wokha; koma iwowa, podziyesera wokha mwa iwo wokha, ndi kudzifananitsa iwo wokha pakati pa iwo wokha ndipo sazindikira. 13 Koma ife sitidzazitamandira popitilira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu adatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso. 14 Pakuti sititambalitsiradi moposa muyeso tokha, monga ngati sitidafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mwa kulalikira Uthenga Wabwino wa Khristu: 15 Wosadzitamandira popitilira muyeso mwa machititso wa ena; koma tiri nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira, 16 Kukalalikira Uthenga Wabwino kupyola m’mayiko a mtsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale. 17 Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye. 18 Pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wobvomerezeka.

2 Akorinto 11

1 Mwenzi kwa Mulungu mutandilola pang’ono ndi chopusacho; komanso mundilole. 2 Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Umulungu; pakuti ndidakupalitsani ubwenzi kwa mwamuna m’modzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu. 3 Koma ndiwopa, kuti pena, monga njoka idanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angayipsidwe kusiyana nako kuwona mtima ndi kuyera mtima ziri mwa Khristu. 4 Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitidalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simudalandira, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simudalandira, mulolana naye bwino lomwe. 5 Pakuti ndiyesa kuti sindidaperewera konse ndi atumwi woposatu. 6 Ndipo ndingakhale ndiri wosadziwa manenedwe abwino, koma sinditero m’chidziwitso, koma mzinthu zonse taziwonetsa bwino pakati panu 7 Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndidalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwa ufulu? 8 Ndidalanda za Mipingo yina, ndikulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu. 9 Ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindidalemetse munthu ali yense; pakuti chimenechidandisowa kwa ine abale akuchokera ku Makedoniya, adakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo mzinthu zonse ndidachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo. 10 Pakuti chowonadi cha Khristu chiri mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya. 11 Chifukwa chiyani? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu. 12 Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m’mene adzitamandiramo, apezedwe monga ife. 13 Pakuti wotere ali atumwi wonyenga, wochita mochenjerera, wodziwonetsa ngati atumwi a Khristu. 14 Ndipo kulibe kudabwa; pakuti satana yemwe adziwonetsa ngati m’ngelo wa kuwunika. 15 Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumwi ake adziwonetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo. 16 Ndinenanso, munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang’ono. 17 Chimene ndiyankhula sindiyankhula monga mwa Ambuye koma monga wopanda nzeru, m’kulimbika kumene kwa kudzitamandira. 18 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira. 19 Pakuti mulolana nawo wopanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru nokha. 20 Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu,ngati wina adzikweza yekha, ngati wina akupandani pankhope. 21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tidakhala wofowoka, koma m’mene wina alimbika mtimamo, (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso. 22 Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali a Israyeli? Inenso. Kodi ali mbewu ya Abrahamu? Inenso. 23 Kodi ali atumiki a Khristu? (ndiyankhula monga moyaluka), makamaka ine; m’zibvutitso mochulukira, m’ndende mochulukira, m’mikwingwirima mosawerengeka, mu imfa kawiri kawiri. 24 Kwa Ayuda ndidalandira kasanu mikwingwirima makumi anayi kuperewera umodzi. 25 Katatu ndidamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndidaponyedwa miyala, katatu ndidatayika posweka chombo, ndidakhala m’kuya tsiku limodzi usana ndi usiku; 26 M’maulendo kawiri kawiri, mowopsa mmadzi,mowopsa mwake mwa wolanda, mowopsa modzera kwa mtundu wanga, mowopsa modzera kwa amitundu, mowopsa mumzinda,mowopsa mchipululu, mowopsa m’nyanja, mowopsa mwa abale wonyenga; 27 Mzolemetsa ndi mzowawa, m’madikiro kawirikawiri, m’njala ndi ludzu, m’masalo a chakudya kawiri kawiri, mkuzizidwa ndi umaliseche. 28 Popanda zakunjazo chimene chimadza kwa ine chondisindikiza tsiku ndi tsiku chilabadiro cha Mipingo yonse. 29 Afoka ndani wosafowoka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine? 30 Ngati ndiyenera kudzitamandira ndidzazitamandira mu zinthu zokhudzana ndi kufowoka kwanga. 31 Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathuYesu Khristu, Iye amene alemekezeka ku nthawi yonse, adziwa kuti sindinama. 32 M’damasiko kazembe wa mfumu Areta adalindizitsa mudzi wa Adamasiko kuti andigwire ine; 33 Ndipo mwazenera, mumtanga, adanditsitsa pakhoma, ndipo ndidapulumuka m’manja mwake.

2 Akorinto 12

1 Ndiyenera kudzitamandira kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumansomphenya ndi mabvumbulutso a Ambuye. 2 Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m’thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kumka naye Kumwamba kwachitatu. 3 Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m’thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu:) 4 Kuti anakwatulidwa kumka ku paradiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula. 5 Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; koma chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m’zofoka zanga. 6 Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru, pakuti ndidzanena choonadi, koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine. 7 Ndipo kuti ndingakwezeke koposa mwa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa 8 Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine. 9 Ndipo ananena kwa ine, chisomo changa chikukwanira pakuti mphamvu yanga ikonzedwa m’ufoka chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondwera m’maufoko anga kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. 10 Chifukwa chake ndisangalala m’mmaufoko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’manzunzo, m’zipsinjo, chifukwa cha Khristu, pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wa mphamvu. 11 Ndakhala wopusa mwakuzitamandira; pakuti inu mwandikakamiza; Pakuti muyenera kundibvomereza ine; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m’kanthu konse ndingakhale ndiri chabe. 12 Indetu zizindikiro za mtumwi zinachitika pakati pa inu m’chipiriro chonse; ndi zizindikiro ndi zozizwa, machitidwe amphamvu. 13 Pakuti kuli chiani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala yina; ngati si ichi kuti ine ndekha sindidakulemetsani inu? Ndikhululukireni pa choipa ichi. 14 Taonani nthawi yachitatu iyi ndakonzeka ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakulemetsani pakuti sindifuna za inu koma inu: pakuti ana sayenera kuwunjikira makolo, koma makolo kuwunjikira ana. 15 Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngakhale ndikonda inu kwambiri koma ine ndidzakondedwa pang`ono. 16 Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wochenjera ine, ndinakugwirani ndi chinyengo. 17 Ndinapindula kwa inu mwa wina aliyense amene ndidamtuma kwa inu. 18 Ndidakhumba Tito ndipo pamodzi ndi iye ndidatumiza m`mbale. Kodi Tito adakuchenjererani. Sitidayendayenda naye mzimu yemweyo kodi? Kodi sitidayenda m`mapazi womwewo. 19 Mumayesa tsopanolino kuti tirikuwiringula kwa inu. Tiyankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Tiyankhula pamso pa Mulungu mwa Khristu, Koma tichita zinthu zonse okondedwa chifukwa chakumangirira kwanu. 20 Pakuti ndi zaopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuma; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikudza, mapokoso; 21 Kuti pakudzanso ine Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalilire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chiwerewere, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.

2 Akorinto 13

1 Nthawi yachitatu iyi ndiri nkudza kwa inu mkamwa mwa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika. 2 Ndinanena kale, ndipo ndidanena ndisanafikeko, monga pamene ndidali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe ndidalembera, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti ngati ndidzanso sindidzawaleka; 3 Popeza mufuna chitsimikizo cha Khristu, wakuyankhula mwa ine; amene safoka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu; 4 Pakuti ngakhale Iye adapachikidwa m’ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tiri ofoka mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu. 5 Dziyeseni nokha ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizireni nokha kapena simudazindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu, mukhala opanda kudzitsimikizira.? 6 Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitiri osatsimikizidwa. 7 Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koyipa; sikuti ife tikaoneke obvomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa. 8 Pakuti sitikhoza kuchita kanthu pokana choonadi, koma kwa chowonadi. 9 Pakuti tikondwera pamene ife tifoka ndi inu muli amphamvu; ndi ichinso tikhumba, ndicho ungwiro wanu. 10 Chifukwa cha ichi ndakulembera zinthu izi pokhala palibe, Kuti pokhala ndiri pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye adandipatsa ine, wakumangilira, ndipo siwakuwononga. 11 Chotsalira, abale, tsalani bwino. Khalani angwiro, mutonthozedwe; khalani amtima umodzi khalani mumtendere; ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu. 12 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsompsono chopatulika. 13 Oyera mtima onse akupatsani moni inu. 14 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse. Ameni.

Agalatiya 1

1 Paulo, mtumwi, (wosachokera kwa anthu, kapena kwa munthu koma kwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene adamuwukitsa Iye kwa akufa;) 2 Ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya: 3 Chisomo chikhale kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi wochokera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, 4 Amene adadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m’nyengo yino ya pansi pano yoyipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu: 5 Kwa Iye ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen. 6 Ndizizwa kuti msanga motere mulikutunsika kuchoka kwa iye amene adakuyitanani m’chisomo cha Khristu, kutsata ku Uthenga wina: 7 Umene suli wina; koma pali ena akubvuta inu, nafuna kuyipsa Uthenga Wabwino wa Khristu. 8 Koma ngakhale ife, kapena m’ngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife akhale wotembereredwa. 9 Monga tidanena kale, kotero ine ndinenanso tsopano, ngati wina akulalikirani uthenga wabwino wosati umene mudawulandira, akhale wotembereredwa. 10 Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala mtumiki wa Khristu. 11 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu. 12 Pakutitu sindidawulandira kwa munthu, kapena sindidauphunzira, komatu udadza mwa bvumbulutso la Yesu Khristu. 13 Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa chipembedzo cha chiyuda, kuti ndidazunza Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuwupasula: 14 Ndipo ndidakhala wopindulitsa mchipembedzo cha chiyuda kuposa ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndidakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga. 15 Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene adandipatula, ndisanabadwe, nandiyitana ine mwa chisomo chake. 16 Ndikuti abvumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndikamlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindidafunsana ndi thupi ndi mwazi; 17 Kapena kukwera kumka ku Yerusalemu sindidamkako kwa iwo amene adakhala atumwi ndisadakhale mtumwi ine, komatu ndidapita ku Arabiya, ndipo ndidabweranso ku Damasiko. 18 Pamenepo patapita zaka zitatu, ndidakwera kumka ku Yerusalemu kukawonana naye Petro, ndipo ndidakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu. 19 Koma wina wa atumwi sindidamuwona, koma Yakobo mbale wa Ambuye. 20 Ndipo tsopano zinthu ndikulembera kwa inu, tawonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine. 21 Pamenepo ndinadza kumbali za Suriya ndi Kilikiya. 22 Koma ndidali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu: 23 Koma adalimkumva kokha, kuti iye wakutizunza ife kale, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene adachipasula kale. 24 Ndipo iwo adalemekeza Mulungu mwa ine.

Agalatiya 2

1 Pamenepo popita zaka khumi ndi zinayi ndidakweranso kumka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnaba, ndidamtenganso Tito. 2 Koma ndidakwera kumkako mwabvumbulutso; ndipo ndidawawuza iwo Uthenga Wabwino umene ndiulalikira pakati pa amitundu; koma m’seri kwa iwo womveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga chabe. 3 Komatu ngakhale Tito, amene adali ndi ine, ndiye Mhelene, adakakamizidwa kuti adulidwe: 4 Ndicho chifukwa cha abale wonyenga wolowezedwa m’seri amene adalowa m’seri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nawo mwa khristu Yesu,kuti tikhale mgoli: 5 Kwa iwo sitidawapatse mpata mowagonjera ngakhale ola limodzi; kuti chowonadi cha Uthenga Wabwino chipitirirebe mwa inu. 6 Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati adali wotani kale, kulibe kanthu kwa) ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu iwo womvekawo sadandiwonjezera ine kanthu. 7 Koma pena, pakuwona kuti adayikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe: 8 (Pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa wodulidwa yemweyo adachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu:) 9 Ndipo pakuzindikira chisomocho chidapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa, ndi Yohane amene adayesedwa mizati adapatsa ine ndi Barnaba dzanja lamanja lachiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa a mdulidwe 10 Pokhapo kuti tikumbukire a umphawi; ndicho chomwe ndidafulumira kuchichita. 11 Koma pamene Kefa anadza ku Antiyokeya ndidatsutsana naye pamaso pake, pakuti adatsutsika wolakwa. 12 Pakuti asadafike ena wochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, kuwopa iwo amene adali a ku mdulidwe. 13 Ndipo Ayuda wotsala adapusitsidwa pamodzi naye; kotero kuti Barnabanso adatengedwa ndi chinyengo chawo. 14 Komatu pamene ndidawona kuti sadali kuyenda kowongoka, monga mwa chowonadi cha Uthenga Wabwino, ndidati kwa Petro pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe wa amitundu, ndipo si wa Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe wa Ayuda? 15 Ife amene tiri Ayuda pachibadwidwe ndipo osati wochimwa a kwa amitundu, Gal 2:16 Koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama mwa ntchito za lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tidakhulupirira mwa Yesu Khristu, kuti tikayesedwe wolungama mwa chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si mwa ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama mwa ntchito za lamulo. 17 Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa wolungama mwa Khristu, tipezedwanso tiri wochimwa tokha, kodi Khristu ali mtumiki wa uchimo chifukwa chake? Msatero ayi. 18 Pakuti ngati ndimanganso zinthu zimene ndaziwononga. Ndidzipangitsa ndekha kukhala wolakwa. 19 Pakuti ine mwa lamulo ndafa ku lamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. 20 Ndapachikidwa pamodzi ndi Khristu: sindikhalanso ndi moyo mwa ine ndekha, koma sindinenso koma Khristu akhala mwa ine: Ndipo moyo umene ndiri nawo tsopano m’thupi, ndikhala nawo mwa chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene adandikonda ine, nadzipereka yekha chifukwa cha ine. 21 Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chidadza mwa lamulo,pamenepo Khristu adafa chabe.

Agalatiya 3

1 Agalatiya wopusa inu adakulodzani ndani, kuti musamvere chowonadi, inu amene Yesu Khristu adawonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa? 2 Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, kodi mudalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro? 3 Kodi muli wopusa wotere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mwakhalitsidwa angwiro mwa thupi? 4 Kodi mudamva zinthu zowawa zambiri zotere kwachabe? Ngati ndi choncho ndiye kwachabe. 5 Iye amene atumikira kwa inu Mzimu, nachita zozizwitsa pakati pa inu, atero Iye kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva mwa chikhulupiriro? 6 Monga choteronso Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo. 7 Chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro omwewo ndiwo ana a Abrahamu. 8 Ndipo malembo pakuwoneratu kuti Mulungu adzayesa wolungama amitundu ndi chikhulupiriro, adayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse; 9 Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo. 10 Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa ali yense wosakhala m’zonse zolembedwa m’buku la chilamulo, kuzichita izi. 11 Ndipo chidziwikiratu kuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu, pakuti; Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro. 12 Koma chilamulo sindicho chochokera kuchikhulupiriro koma munthu wakuchita adzakhala ndi moyo ndi icho. 13 Khristu watiwombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu; pakuti kwalembedwa, wotembereredwa ali yense wopachikidwa pamtengo. 14 Kuti dalitso la Abrahamu mwa Yesu Khristu, likadze kwa a mitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimu, mwa chikhulupiriro. 15 Abale ndinena monga mmanenedwe a anthu. Pangano, lingakhale la munthu, litatsimikizika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuwonjezerapo. 16 Ndipo tsopano malonjezano adanenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Sadanena, Ndipo kwa mbewu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, ndipo kwa mbewu yako ndiye Khristu. 17 Ndipo ichi ndinena, pangano limene lidatsirizika kale ndi Mulungu mwa Khristu,lamulo lidadza zitapita zaka silingathe kufafaniza kuti lonjezo likhale lopanda ntchito . 18 Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma Mulungu adampatsa Abrahamu mwa lonjezano. 19 Nanga kutumikira kwa chilamulo tsono? Chidawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu ya Iye amene adamulonjeza imene adayilonjezera; ndipo chidakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe. 20 Koma nkhoswe siyikhala nkhoswe ya m’modzi; koma Mulungu ali m’modzi. 21 Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nawo malonjezano a Mulungu? Msatero ayi. Pakuti ngati chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kupatsa moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo. 22 Komatu lembo lidatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa wokhulupirirawo. 23 Koma chisanadze chikhulupiriro tidasungidwa pomvera lamulo wotsekedwa ku chikhulupiriro chimene ku nthawi yake chidzakhala chibvumbulutsidwa. 24 Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe wolungama ndi chikhulupiriro. 25 Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso womvera namkungwi. 26 Pakuti inu nonse ,muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. 27 Pakuti nonse amene munabatizidwa mwa Khristu mudabvala Khristu. 28 Muno mulibe Myuda kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna kapena mkazi; pakuti muli nonse m’modzi mwa Khristu Yesu. 29 Koma ngati muli a Khristu, muli mbewu ya Abrahamu,ndiwolowa m’nyumba monga mwa lonjezano.

Agalatiya 4

1 Tsopano ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali mwana, sasiyana ndi kapolo, angakhale iye ali mwini mbuye wa zonse; 2 Komatu ali wakumvera womsungira, ndi adindo, kufikira nthawi yoyikika kale ndi atate wake. 3 Koteronso ife, pamene tidali ana, tidali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi: 4 Koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu adatuma Mwana wake wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo, 5 Kuti akawombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana. 6 Ndipo popeza muli ana, Mulungu adatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m’mitima yanu, wofuwula Abba, Atate. 7 Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati ndi mwana,pamenepo wolowa nyumbanso ya Mulungu mwa Khristu. 8 Komatu pajapo posadziwa Mulungu inu, mudachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m’chibadwidwe chawo; 9 Koma tsopano podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofowoka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuyichitira ukapolo. 10 Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka. 11 Ndiwopera inu kuti kapena ndagwira ntchito pa inu pachabe. 12 Abale, ndikupemphani, khalani monga ine pakuti inenso ndiri monga inu. Simudandichitira choyipa ine. 13 Koma mudziwa kuti m’kufowoka kwa thupi ndidakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba. 14 Ndipo yeselo langa la thupi m’thupi inu simudalipeputsa, kapena simulikana, komatu mudandilandira ine monga m’ngelo wa Mulungu, monga khristu Yesu mwini; 15 Pamenepo dalitso lanu liri kuti? Limene mudaliyankhula. Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadakhala kotheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine. 16 Kotero kodi ndasanduka m’dani wanu, chifukwa ndikuwuzani zowona? 17 Achita changu pa inu koma sikokoma ayi, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu. 18 Koma nkwabwino kuchita changu m’zabwino nthawi zonse, sipokha pokha pokhala nanu pamodzi ine. 19 Tiyana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu awumbika mwa inu. 20 Ndikhumba nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mawu anga; chifukwa ndikayikira za inu. 21 Ndiwuzeni, inu akukhumba kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo? 22 Pakuti kwalembedwa, kuti Abrahmu adali nawo ana amuna awiri, m’modzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi m’modzi wobadwa mwa mfulu. 23 Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. 24 Zinthu izi ndizo zophiphiritsa: pakuti awa ndi mapangano awiri, m’modzi wa ku phiri la Sinayi, akubalira ukapolo, ndiye Hagara. 25 Koma Hagara ndiye phiri la Sinayi, m’Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wa Kumwamba uli wa ufulu, ndiwo amayi a ife tonse.. 27 Pakuti kwalembedwa, Kondwera chumba iwe wosabala; yimba nthungululu, nufuwule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna. 28 Tsopano ife, abale, monga Isake, tiri ana a lonjezano. 29 Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi adazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano. 30 Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu. 31 Chifukwa chake, abale, sitiri ana a mdzakazi, komatu a mfulu.

Agalatiya 5

1 Khristu adatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu, chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo. 2 Tawonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mudulidwa, Khristu simudzapindula naye kanthu. 3 Ndichitanso umboni kwa munthu yense wodulidwa, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse. 4 Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa wolungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo. 5 Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera mwa chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo. 6 Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro chakuchita mwa chikondi. 7 Mudathamanga bwino; adakuletsani mdani kuti musamvere chowonadi? 8 Kukopa uku sikuchokera kwa Iye amene adakuyitanani. 9 Chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse. 10 Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nawo mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chiweruzo chake. 11 Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chokhumudwitsa cha mtanda chidatha. 12 Ndidakakonda iwo ngakhale adakachotsedwa amene abvuta inu. 13 Pakuti adakuyitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nawo ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwa chikondi tumikiranani wina ndi mzake. 14 Pakuti mawu amodzi monga awa akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo: Uzikonda mzako monga udzikonda iwe mwini. 15 Koma ngati mulumana ndi kudyana wina ndi mzake, chenjerani mungamezane. 16 Koma ine ndinena, muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. 17 Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zinthu zimene muzifuna musazichite. 18 Ngati Mzimu akusogolerani, simuli womvera lamulo. 19 Ndipo ntchito za thupi ziwonekera, ndizo chigololo, chiwerewere, chodetsa, kukhumba zonyansa. 20 Kupembedza mafano, ufiti, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, 21 Njiru, kupha, kuledzera, mchezo ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo monga ndachita, kuti iwo akuchita zinthu zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 22 Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro. 23 Chifatso, chiletso; pochita zimenezi palibe lamulo. 24 Koma iwo a Khristu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake. 25 Ngati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. 26 Tisakhale wokhumba ulemerero wachabe woyambana wina ndi mzake, akuchitirana njiru wina ndi mzake.

Agalatiya 6

1 Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu a uzimu mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. 2 Nyamuliranani zothodwetsa za wina ndi mzake, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu. 3 Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha. 4 Koma munthu aliyense ayesere ntchito yake, ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina. 5 Pakuti munthu aliyense adzasenza katundu wake wa iye mwini. 6 Koma iye amene aphunzira mawu, ayenera agawire wophunzitsayo m’zinthu zonse zabwino. 7 Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso iye adzachituta. 8 Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha. 9 Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufowoka. 10 Chifukwa chake, monga tili ndi mwayi tichitira anthu onse zabwino, makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro. 11 Tawonani, malembedwe akuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. 12 Onse amene akhumba kuwonekera wokoma m’thupi, iwowa akukangamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti akuwopa kuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. 13 Pakuti angakhale iwo womwe wodulidwa sasunga lamulo; komatu akhumba inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m’thupi lanu. 14 Koma Mulungu akukana kuti ndisadzitamandire ine konse konse, iyayi, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. 15 Pakuti mwa Khristu Yesu, mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. 16 Koma onse amene ayenda monga mwa chilamulo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu. 17 Kuyambira tsopano palibe munthu andibvute, pakuti ndiri nazo ine m’thupi mwanga zipsera za AmbuyeYesu. 18 Abale mtendere wa Ambuye wathu Yesu Khristu ukhale ndi mzimu wanu. Ameni.

Aefeso 1

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, kwa woyera mtima amene ali mu Aefeso, ndi kwa iwo wokhulupirika mwa Khristu Yesu: 2 Chisomo chikhale kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi wochokera, kwa Ambuye Yesu Khristu. 3 Wolemekezeka Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Khristu: 4 Monga adatisankha ife mwa Iye, asadakhazikike maziko a dziko lapansi, kuti tikhale ife woyera mtima, ndi wopanda chilema pamaso pake m’chikondi. 5 Adatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kudakomera chifuniro chake. 6 Kuti uyamikike ulemerero wa chisomo chake, chimene adatichitira ife kukhala wolandiridwa mwa wokondedwayo 7 Mwa Iye tiri ndi mawomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa chuma cha chisomo chake. 8 Chimene adatichulukitsira ife mu nzeru zonse, ndi chisamaliro. 9 Adatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kudamkomera ndi monga adatsimikiza mtima kale mwa Iye yekha. 10 Kuti pamakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zinthu zonse mwa Khristu, za Kumwamba ndi za padziko: ngakhale zili mwa Iye: 11 Mwa Iye tidayesedwa cholowa chake, popeza tidakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse mwa uphungu wa chifuniro chake; 12 Kuti ife amene tidakhulupirira mwa Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake. 13 Mwa Iyeyo inunso, mutamva mawu a chowonadi; Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, mudasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, 14 Ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti ake ake akawomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike. 15 Mwa ichi inenso, m’mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu, ndi chikondi cha kwa oyera mtima onse. 16 Sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m’mapemphero anga; 17 Kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire Iye: 18 Ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuyitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa woyera mtima, 19 Ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife wokhulupira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba. 20 Imene adachititsa mwa Khristu, m’mene adamuwukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba. 21 Pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lotchedwa, si m’nyengo yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza: 22 Ndipo adakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu wa zonse ku mpingo. 23 Limene liri thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m’zonse.

Aefeso 2

1 Ndipo inu adakupatsani moyo, pokhala mudali akufa ndi zolakwa ndi zochimwa zanu; 2 Zimene mudayendamo kale, monga mwa mayendedwe adziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wamlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana akusamvera. 3 Amene ife tonsenso tidagonera pakati pawo kale, mzilakolako za thupi lathu, ndi kuchita chifuniro cha thupi, ndi za maganizo, ndipo tidali ana a mkwiyo chibadwire, monganso wotsalawo. 4 Koma Mulungu amene ali wachuma mu chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene adatikonda nacho, 5 Tingakhale tidali akufa m’zolakwa zathu, adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli wopulumutsidwa ndi chisomo;) 6 Ndipo adatiwukitsa pamodzi, natikazikitsa pamodzi m’zakumwamba mwa Khristu Yesu: 7 Kuti akawonetsere m’nyengo ziri mkudza chuma choposa cha chisomo chake, mkukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu. 8 Pakuti muli wopulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu; chiri mphatso ya Mulungu: 9 Chosachokera ku ntchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense. 10 Pakuti ife ndife opangidwa ake, wolengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu adazipangiratu, kuti tikayende m’menemo. 11 Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m’thupi, wotchedwa kusadulidwa ndi iwo wotchedwa a mdulidwe umene udachitika ndi manja; 12 Kuti nthawi ija mudali wopanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, wopanda chiyembekezo, ndi wopanda Mulungu m’dziko lapansi: 13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene mudali kutali kale, adakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Khristu. 14 Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene adachita kuti onse awiri akhale m’modzi, nagumula khoma lotchinga pakati pa ife. 15 Atachotsa udani m’thupi lake, ndiwo mawu a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu m’modzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere; 16 Ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m’thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nawo udaniwo: 17 Ndipo adadza, adalalikira mtendere kwa inu amene mudali kutali, ndi kwa iwo amene adali pafupi. 18 Kuti mwa Iye ife tonse awiri tiri nawo malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu m’modzi. 19 Tsopano simulinso alendo ndi wongobwera, komatu muli a mudzi womwewo wa woyera mtima ndi abanja la Mulungu; 20 Ndi womangidwa pa maziko wa atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya; 21 Mwa Iye mamangidwe onse akhala wolumikizika pamodzi bwino, akula, akhale kachisi wopatulika mwa Ambuye; 22 Mwa Iye inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.

Aefeso 3

1 Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu, 2 Ngatitu mudamva za machitidwe a chisomo cha Mulungu chimene adandipatsa ine cha kwa inu: 3 Ndi umo adandizindikiritsa chinsinsicho mwa bvumbulutso, ( monga ndidalemba kale mwachidule, 4 Chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m’chinsinsi cha Khristu.) 5 Chimene sadazindikiritsa ana a anthu m’mibado yina, monga adachibvumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake woyera mwa Mzimu: 6 Kuti amitundu ali wolowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zimzathu zathupilo, ndi wolandira nafe pamodzi malonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino; 7 Umene adandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene adandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake. 8 Kwa ine, wochepa ndi wochepetsa wa onse woyera mtima, adandipatsa chisomo ichi, ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu; 9 Ndikuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chidabisika kuyambira kale kale mwa Mulungu wolenga zonse mwa Yesu Khristu: 10 Kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m’zakumwamba nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu, 11 Monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene adachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu: 12 Amene tiri naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye. 13 Mwa ichi ndikhumba kuti musade nkhawa m’zisautso zanga chifukwa cha inu ndiwo ulemerero wanu. 14 Chifukwa cha ichi ndipinda mawondo anga kwa Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, 15 Amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina, 16 Kuti akupatseni inu monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, mwa munthu wamkati mwanu. 17 Kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m’mitima yanu; kuti mukhale wozika mizu ndi wotsendereka m’chikondi, 18 Kuti mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi woyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndikuzama kwake ndi kukwera. 19 Ndikuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu. 20 Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife, 21 Kwa Iye kukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu kufikira mibado yonse ya nthawi za nthawi. Ameni.

Aefeso 4

1 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera mayitanidwe amene mudayitanidwa nawo, 2 Ndikuwonetsera kudzichepetsa konse ndi chifatso , ndi kuwonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mzake, mwa chikondi. 3 Ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere 4 Pali thupi limodzi ndi Mzimu m’modzi, monganso adakuyitanani m’chiyembekezo chimodzi cha mayitanidwe anu; 5 Ambuye m’modzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, 6 Mulungu m’modzi ndi Atate wa onse, amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m’kati mwa inu nonse. 7 Ndipo kwa yense wa ife chapatsidwa chisomo, monga mwa muyeso wamphatso ya Khristu. 8 Chifukwa chake anena, m’mene adakwera Kumwamba adamanga ndende undende, naninkha za mphatso kwa anthu. 9 (Koma ichi, chakuti, adakwera, nchiyani nanga koma kuti Iye adatsikiranso ku madera akunsi kwa dziko? 10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso adakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.) 11 Ndipo Iye adapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa; ndi ena aphunzitsi; 12 Kuti akonzere woyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; 13 Kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, munthu wangwiro, ku muyeso wamsinkhu wachidzalo cha Khristu: 14 Kuti tisakhalenso makanda, wogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi matsenga a anthu, ndi kuchenjera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa. 15 Koma pakuyankhula chowonadi mwa chikondi; tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye; amene ali mutu ndiye Khristu: 16 Kuchokera mwa Iye m’thupi lonse, logwirizana ndi kulumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe athupi, kufikira chimangiriro chake mwa chikondi. 17 Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye kuti simuyendanso inu monganso amitundu ayendera, m’chitsiru cha mtima wawo, 18 Wodetsedwa m’nzeru zawo, woyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chiri mwa iwo, chifukwa cha kuchititsidwa khungu kwa mitima yawo: 19 Amenewo popeza sadazindikiranso kanthu konse, adadzipereka wokha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso pamodzi ndi umbombo. 20 Koma inu simudaphunzira Khristu chotero. 21 Ngatitu mudamva Iye, ndipo mudaphunzitsidwa mwa Iye monga chowonadi chiri mwa Yesu; 22 Kuti mubvule kunena za makhalidwe anu woyamba a munthu, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za chinyengo; 23 Koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu. 24 Ndipo mubvale munthu watsopano, amene adalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha chowonadi. 25 Mwa ichi, mutataya zonama, yankhulani zowona yense ndi mzake: pakuti tiri ziwalo wina ndi mzake. 26 Kwiyani, koma musachimwe: dzuwa lisalowe muli chikwiyire: 27 Ndiponso musampatse malo mdiyerekezi. 28 Wakubayo asabenso: koma makamaka agwiritse ntchito nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. 29 Nkhani yonse yobvunda isatuLuka m’kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira, kuti ikatumikire chisomo kwa iwo akumva. 30 Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene mudasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la mawomboledwe. 31 Chiwawo chonse ndi kupsa mtima ndi mkwiyo ndi chiwawa ndi mayakhulidwe oyipa zichotsedwe kwa inu pamodzi ndi zoyipa zonse. 32 Ndipo mukhalirane a chikondi wina ndi mzake amtima wabwino akukhululukirana nokha, monganso Mulungu chifukwa cha Khristu adakhululukira inu.

Aefeso 5

1 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana wokondedwa; 2 Ndipo yendani m’chikondi monganso Khristu adakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. 3 Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiliro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu monga kuyenera woyera mtima. 4 Kapena chinyanso ndi kuyankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. 5 Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosilira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. 6 Asakunyengeni inu munthu ndi mawu wopanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera. 7 Chifukwa chake musakhale wolandirana nawo. 8 Pakuti kale mudali mdima, koma tsopano muli kuwunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuwunika; 9 Pakuti chipatso cha Mzimu tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo ndi chowonadi;) 10 Kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani. 11 Ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu; koma makamakanso muzitsutse. 12 Pakuti zochitidwa nawo m’seri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi 13 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuwunika, ziwonekera; pakuti chonse chakuwonetsa chiri kuwunika 14 Mwa ichi anena khala maso wogona iwe, nuwuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. 15 Potero penyani bwino umo muyendera, si monga wopanda nzeru, koma monga anzeru. 16 Akuchita mwachangu, popeza masiku ali woyipa. 17 Chifukwa chake musakhale wosadziwa koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani! 18 Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu; 19 Ndikudziyankhulira nokha ndi masalmo, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba mokometsera Ambuye mumtima mwanu. 20 Ndikupereka mayamiko kwa Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zinthu zonse, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu; 21 Ndi kumverana wina ndi mzake m’kuwopa Mulungu. 22 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. 23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo; ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. 24 Choncho monga Mpingo umvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse. 25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu adakonda Mpingo, adzipereka yekha m’malo mwake; 26 Kuti akaupatule, atauyeretsa ndi kuusambitsa ndi madzi mwa mawu, 27 Kuti Iye akadziyikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere: komatu kuti ukhale woyera, ndi wopanda chilema. 28 Koteronso amuna azikonda akazi awo a iwo wokha monga ngati matupi a iwo wokha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha. 29 Pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Ambuye ndi Mpingo. 30 Pakuti ife tiri ziwalo za thupi lake, za m’nofu wake ndi mafupa ake. 31 Chifukwa cha ichi munthu adzasiya atate ake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi. 32 Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo. 33 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo awonetsetse kuti akulemekeza mwamuna wake.

Aefeso 6

1 Ananu mverani akukubalani mwa Ambuye: pakuti ichi nchabwino. 2 Lemekeza atate wako ndi amako; (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano;) 3 Kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yayikulu padziko. 4 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu: komatu muwalere iwo ndi chilangizo cha Ambuye. 5 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwawopa ndi kunthunthumira nawo, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu; 6 Simonga mwa kutumikira mwachinyengo, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima; 7 Akuchita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye, si anthu ayi. 8 Podziwa kuti chinthu chabwino chiri chonse munthu aliyense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu. 9 Ndipo ambuye inu, muwachitire zinthu zomwezi iwowa; nimuleke kuwawopsa; podziwa kuti Ambuye wawo ndi wanu ali m’Mwamba ndipo palibe tsankhu kwa Iye. 10 Chotsalira abale, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake. 11 Tabvalani zida zonse za Mulungu; kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdiyerekezi. 12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika adziko lapansi a mdima uno, ndi a mizimu yoyipa yamulengalenga. 13 Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuyima chitsutsire pofika tsiku loyipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. 14 Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m’chuwuno mwanu ndi chowonadi mutabvalanso chapachifuwa cha chilungamo; 15 Ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere. 16 Koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoze kuzima nacho mibvi yonse yoyaka moto ya woyipayo. 17 Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mawu a Mulungu. 18 Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo kudikirira m`menemo ndi chipiriro chonse ndi kupembedzera woyera mtima onse. 19 Ndi kwa ine ndemwe kuti andipatse mawu, kuti ndikatsegule pakamwa panga molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, 20 Chifukwa cha umene ndiri kazembe wa mu unyolo, kuti m’menemo ndikayankhule molimbika, monga ndiyenera kuyankhula. 21 Koma kuti mukadziwe inunso za makhalidwe anga, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tukiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye. 22 Amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. 23 Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. 24 Chisomo chikhale ndi iwo onse amene akonda Ambuye wathu Yesu Khristu mowonadi. Ameni.

Afilipi 1

1 Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa woyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi woyang’anira ndi atumiki: 2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi zochokera kwa Ambuye Yesu Khristu. 3 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu nonse. 4 Nthawi zonse m’pembedzero langa la kwa inu nonse ndichita ndipemphera mokondwera. 5 Chifukwa cha chiyanjano chanu mu Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino; 6 Pokhala wotsimikizika, kuti Iye amene adayamba mwa inu ntchito yabwino, adzayitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu: 7 Monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako mu mtima mwanga, kuti inu m’zomangira zanga, ndipo m’chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli woyanjana nane chisomo changa. 8 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m’chikondi cha mwa Khristu Yesu. 9 Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezeke, m’chidziwitso, ndi kuzindikira konse; 10 Kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima wowona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu; 11 Wodzala nacho chipatso chachilungamo, chimene chiri ,mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko. 12 Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zinthu zija za ine zidachitika makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino; 13 Kotero kuti zomangira zanga zidawonekera mwa Khristu m`nyumba ya chifumu ndi malo ena onse; 14 Ndi kuti ambiri mwa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kuyankhula mawu a Mulungu wopanda mantha. 15 Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndewu; koma enanso chifukwa cha kukoma. 16 Koma ena alalikira Khristu mochokera m’chotetana, kosati kowona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m’zomangira zanga. 17 Ena atero ndi chikondi, podziwa kuti ndidayikidwa kuti ndikateteze Uthenga Wabwino; 18 Nchiyani kodi? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m’chowonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m’menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera. 19 Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu, 20 Monga mwakulingiliritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m’thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa. 21 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula. 22 Koma ngati kukhala ndi moyo m’thupi, ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha; 23 Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho chokhumba cha kuchoka kukakhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposa posatu: 24 Koma kukhalabe m’thupi ndiko kufunika koposa, chifukwa cha inu. 25 Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuwonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu; 26 Kuti kudzitamandira kwanu kuchuLuka mwa Yesu Khristu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu. 27 Chokhachi, mayendedwe anu ayenera Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndiri mkudza ndi kuwona inu, ndingakhale nditi ndiri kwina, ndikamva zakwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino. 28 Wosawopa adani m’kanthu konse, chimene chiri kwa iwowa chisonyezo cha chiwonongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu; 29 Kuti kwapatsidwa kwa inu kwa ufulu chifukwa cha Khristu, siku khulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha lye; 30 Ndikukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiwona mwa ine, nimukumva tsopano chiri mwa ine.

Afilipi 2

1 Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati chikondi, ndi chisoni, 2 Kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chofanana, amoyo umodzi, wolingalira mtima umodzi, 3 Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndikudzichepetsa mtima yense ayese mzake womposa iye mwini. 4 Munthu aliyense asapenyerere zinthu zake za iye yekha, koma aliyense apenyererenso za mzake. 5 Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene udalinso mwa Khristu Yesu: 6 Ameneyo pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sadachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu: 7 Koma adadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu: 8 Ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, adadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda. 9 Mwa ichinso Mulungu adamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa mayina onse: 10 Kuti m’dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko; 11 Ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. 12 Potero, wokondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano ine palibe, gwirani ntchito ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira. 13 Pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. 14 Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani. 15 Kuti mukakhale wopanda chilema ndi wowona, ana a Mulungu wopanda chilema pakati pa mbadwo wokhokhota ndi wopotoka, mwa iwo amene monga nyali m’dziko lapansi. 16 Akuwonetsera mawu a moyo; kuti ine ndikakhale wachimwemwe nawo m’tsiku la Khristu, kuti sindidathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. 17 Inde komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse. 18 Momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. 19 Koma ndikhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. 20 Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima wowona. 21 Pakuti onsewa atsata za iwo wokha, si zinthu za Yesu Khristu. 22 Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, adatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino. 23 Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posachedwa m’mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani. 24 Koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidza msanga. 25 Koma ndidayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mzanga, ndi msilikali mzanga, ndiye mthenga wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa. 26 Popeza adali wolakalaka inu nonse, nabvutika mtima chifukwa mudamva kuti adadwala. 27 Pakutinso adadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu adamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chowonjezera pa chisomo. 28 Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuwona mukakondwerenso, ndi inenso, chindichepere chisoni. 29 Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu woterewa: 30 Pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu adafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa ine.

Afilipi 3

1 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundibvuta ine, koma kwa inu ndi chitetezo kukhazikitsa. 2 Chenjerani ndi agalu, chenjerani ndi wochita zoyipa, chenjerani ndi a mdulidwe. 3 Pakuti ife ndife mdulidwe, amene tipembedza Mulungu mu Mzimu ndi a chimwemwe mwa Yesu Khristu, ndipo tilibe kukhulupirira mthupi. 4 Ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m’thupi; ngati munthu wina yense aganiza kukakhulupirira m’thupi, inenso kwambiri: 5 Wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa m’bado wa Israyeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa ahebri, monga mwa lamulo; Mfarisi; 6 Monga mwa changu, wozunza mpingo; monga mwa chilungamo cha m’lamulo wokhala wosalakwa ine. 7 Komatu zinthu zonse zimene zidandipindulira, zomwezo ndidaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu. 8 Inde nzosakayikitsa komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe achizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndidatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikapindule Khristu. 9 Ndikupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro. 10 Kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu yakuwuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake; 11 Ngati nkotheka ndikafikire kuwuka kwa akufa. 12 Sikunena kuti ndidalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene adandigwirira Khristu Yesu. 13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poyiwaladi zinthu za m’mbuyo, ndikutambalitsira zinthu za m’tsogolo, 14 Ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa mayitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu. 15 Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli chinthu mulingirira nacho mumtima, ichinso Mulungu adzabvumbulutsira inu. 16 Chokhachi,monga ndidachirandira kale tiyeni mu lamulo lomweli tiyende tiganizire chinthu chomwechi. 17 Abale, khalani pamodzi akutsunza anga, ndipo yang’anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu. 18 (Pakuti ambiri amayenda, za amene ndidakuwuzani kawiri kawiri, ndipo tsopano ndikuwuzani ndi kulira, kuti ali adani a mtanda wa Khristu: 19 Amene chitsiriziro chawo ndicho kuwonongeka, amene Mulungu wawo ndiyo mimba yawo, ulemerero wawo uli m’manyazi awo, amene alingirira za zinthu za padziko. 20 Pakuti ubadwa wathu uli kumwamba; kuchokera komwekonso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu. 21 Amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nawo zinthu zonse.

Afilipi 4

1 Potero, abale anga wokondedwa, wolakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi Korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, wokondedwa anga. 2 Ndidandaulira Euodiya, ndidandaulira Suntuke, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye. 3 Inde ndikupemphaninso, mzanga wa m’goli wowona, muthandize akazi awa amene adakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klementonso, ndi wotsala aja antchito amzanga, amene mayina awo ali m’buku la moyo. 4 Kondwerani mwa Ambuye, nthawi zonse; ndibwerezanso kotero kondwerani. 5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi: 6 Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. 7 Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khiristu Yesu. 8 Chotsatira abale, zinthu ziri zonse zowona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zomveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingilireni izi. 9 Zinthu zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziwona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu. 10 Koma ndidakondweradi mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano mudatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso mudalingirirako, koma mudasowa mpata. 11 Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire ziri zonse ndiri nazo. 12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa. 13 Ndikhoza kuchita zinthu zonse mwa Khristu wondipatsa mphamvuyo. 14 Koma mudachita bwino kuti mudayanjana nane m’chisautso changa. 15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m’chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndidachoka kutuluka m’Makedoniya, siwudayanjana nane Mpingo umodzi wonse m’makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha. 16 Pakuti m’Tesalonikanso mudanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri. 17 Sikuti chifukwa nditsata mphatso, komatu ndikhumba chipatso kuti mukachulukire ku mdalitso wanu. 18 Koma ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, m’nunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu. 19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chiri chonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu. 20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero ku nthawi za nthawi, Amen. 21 Patsani moni kwa woyera mtima ali yense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine akupatsani moni inu. 22 Woyera mtima onse akupatsani oni inu, koma maka maka iwo a banja la Kayisara. 23 Chisomo cha Ambuye Yesu hristu chikhale ndi inu nonse.

Akolose 1

1 Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu mwachifuniro cha Mulungu,ndi Timoteo mbale wathu. 2 Kwa woyera mtima ndi abale wokhulupirika,mwa Khristu aku Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.. 3 Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi kupempherera inu nthawi zonse, 4 Kuyambira pamene tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu,ndi chikondi muli nacho kwa woyera mtima onse, 5 Chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu m’Mwamba,chimene mudachimva kale m’mawu a chowonadi cha Uthenga Wabwino; 6 Umene udafikira kwa inu;monganso m’dziko lonse lapansi umabala zipatso,numakula monganso mwa inu,kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira Chisomo cha Mulungu m’chowonadi; 7 Monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mzathu wokondedwa,ndiye mtumiki wokhulupirika wa Khristu chifukwa cha ife; 8 Amenenso adatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu. 9 Mwa ichi ifenso,kuyambira tsiku limene tidamva,sitileka kupempherera inu, ndi kukhumba kuti mukadzadzidwe ndichizindikiritso cha chifuniro chake munzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu; 10 Kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo,ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino,ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu; 11 Wolimbikitsidwa m’chilimbiko chonse,monga mwa mphamvu ya ulemerero wake,kuchitira chipiliro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe; 12 Ndikuyamika Atate,amene adatiyeneretsa ife kulandirana nawo cholowa cha woyera mtima m’kuwunika: 13 Amene adatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima,natisunthitsa kutilowetsa m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake. 14 Amene tiri nawo mawomboledwe mwa mwazi wa m’kukhulukidwa kwa zochimwa zathu: 15 Amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo,wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; 16 Pakuti mwa iye ,zidalengedwa zonse za m’mwamba,ndi za padziko zowoneka ndi zosawoneka,kapena mipando ya chifumu, kapena maufumu kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zidalengedwa mwa iye ndi kwa iye. 17 Ndipo iye ali woyamba wa zonse;ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye. 18 Ndipo Iye ali mutu wathupi, Mpingo ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa;kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba. 19 Pakuti kudamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire; 20 Mwa iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye yekha, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu ndinena, kapena pali zinthu za padziko,kapena za m’mwamba. 21 Ndipo inu, wokhala alendo akale ndi adani m’chifuwa chanu m’ntchito zoyipazo,koma tsopano adakuyanjanitsani. 22 M’thupi lake la imfayo,kukayimika inu woyera,ndi wopanda chilema ndi wosatsutsika pamaso pake; 23 Ngatitu mukhalabe m’chikhulupiriro,wochilimika ndi wokhazikika ndi wosasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva,wolalikidwa cholengedwa chonse chapansi pa thambo;umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake. 24 Amene tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu; ndi kukwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khritsu mthupi langa chifukwa cha thupi lake; ndiwo Mpingo; 25 Amene ndidakhala mtumiki wake monga mwa udindo wa Mulungu umene adandipatsa ine wakuchitira inu,wakukwaniritsa mawu aMulungu; 26 Ndiwo chinsinsicho chidabisika kuyambira pa nthawizo,ndi kuyambira pa mibadoyo;koma adachiwonetsa tsopano kwa woyera mtima ake; 27 Kwa iwo amene Mulungu adafuna kuwazindikiritsa chuma chimene chiri chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu ,ndiye Khritsu mwa inu,chiyembekezo cha ulemerero; 28 Amene timlalikira ife,ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyenze mu nzeru zonse, kuti tiwonetsere munthu aliyense wangwiro mwa Khritsu Yesu: 29 Kuchita ichi ndidzibvutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.

Akolose 2

1 Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndiri nayo chifukwa cha inu,ndi iwowa a m’Lawodikaya,ndi onse amene sadawone nkhope yanga m’thupi; 2 Kuti itonthozeke mitima yawo,nalumikizike pamodzi iwo m’chikondi kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso,kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu ndi cha Atate ndiye Khristu; 3 Amene chuma chonse cha nzeru ndi chidziwitso chibisika mwa Iye. 4 Ichi ndinena kuti munthu asakusocheletseni inu ndi mawu wokopa kopa. 5 Pakuti ndingakhale ndiri kwina m’thupi,komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu,wokondwera pakupenya makonzedwe anu,ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu. 6 Chifukwa chake monga momwe mudalandira Khristu Yesu Ambuye chotero muyende mwa Iye. 7 Wozika mizu ndi womangiririka mwa Iye,ndi wokhazikika m’chikhulupiriro,monga mudaphunzitsidwa,ndi kuchulukitsa chiyamiko. 8 Chenjerani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma,mwa kukonda nzeru kwake,ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu,potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu. 9 Pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m’thupi. 10 Ndipo inu muli angwiro mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro; 11 Amenenso mumadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m’mabvulidwe a thupi, mu m’dulidwe wa Khristu: 12 Popeza mudayikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mu ubatizo,momwemonso mudaukitsidwa pamodzi ndi Iye m’chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene adamuwukitsa Iye kwa akufa. 13 Ndipo inu, pokhala akufa m’zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, adakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m’mene adakhululukira inu zolakwa zonse; 14 Adatha kutifanizira cha pa ifecho cholembedwa m’zoyikikazo,chimene chidali chotsutsana nafe;ndipo adachichotsera pakatipo,ndi kuchikhomera ichi pamtanda wake; 15 Atabvula maukulu ndi maulamuliro, adawawonetsera poyera, nawagonjetsera iwo m`menemo. 16 Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m’chakudya, kapena m`chakumwa, kapena m’kunena za tsiku la phwando, kapena lokhala mwezi kapena masiku asabata: 17 Zimene ndizo mthunzi wa zinthu zilimkudzazo; koma thupi ndi la Khristu. 18 Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphoto yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo,ndi kukhalira mu izi zimene sadaziwona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake. 19 Wosagwira mutuwo kuchokera kwa Iye amene thupi lonse limodzi lilumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu. 20 Chiyani nanga ngati mudafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji ku zoyikikazo,monga ngati moyo wanu mukhala nawo m’dziko lapansi. 21 (Usayikapo dzanja;usalawa;usakhudza; 22 Ndizo zonse zakuwonongedwa pochita nazo)monga mwa malangizo ndi maphunziro wa anthu? 23 Zimene ziri nawotu manenedwe anzeru m` chifuniro chakudzipembedza ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma ziribe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.

Akolose 3

1 Chifukwa chake ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu,funani za kumwamba,kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu. 2 Lingalirani zakumwamba osati za padziko lapansi ayi. 3 Pakuti mudafa,ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. 4 Pamene Khristu adzawoneka amene ndi moyo wathu, pamenepo inunso mudzawonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero. 5 Chifukwa chake fetsani ziwalozo ziri padziko; chiwerewere, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choyipa, ndi chisiliro, chimene chiri kupembedza mafano: 6 Chifukwa cha zinthu izi zomwe umadza m’kwiyo wa Mulungu pa ana akusamvera: 7 Zimene mudayendamo inunso kale, pamene mudakhala ndi moyo wanu m’menemo. 8 Koma tsopano mudataya inunso zonse: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m’kamwa mwanu. 9 Musamanamizana wina ndi mzake;popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake; 10 Ndipo mudabvala munthu watsopano, amene alikukonzeka m’nzeru mwa chifaniziro cha Iye adamlenga iye: 11 Pamene palibe Mhelene ndi Myuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wotchedwa wakunja, Msikuti, kapolo,mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m’zonse. 12 Chifukwa chake bvalani monga wosankhika a Mulungu, woyera mtima ndi wokondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso kuleza mtima; 13 Kulolerana wina ndi mzake, ndi kukhululukirana eni nokha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mzake; monganso Khristu, adakhululukira inu, teroni inunso. 14 Koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima waungwiro wonse. 15 Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m’mitima yanu, kulingakonso mudayitanidwa m’thupi limodzi ndipo khalani akuyamika. 16 Aloleni Mawu a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndikuphunzitsa ndi kuyambirirana eni nokha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo za uzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi Chisomo mumtima mwanu. 17 Ndipo chiri chonse, mukachichita m’mawu kapena muntchito, chitani zones m’dzina la Ambuye Yesu, ndikuyamika Mulungu Atate mwa Iye. 18 Akazi inu mverani amuna anu,monga kuyenera mwa Ambuye. 19 Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. 20 Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho. 21 Atate inu,musaputa ana anu,kuti angataye mtima. 22 Akapolo inu, mverani m’zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga wokondweretsa anthu, komatu amtima umodzi, akuopa Ambuye; 23 Chiri chonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, wosati kwa anthu ayi; 24 Podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; pakuti mutumikira Ambuye Khristu mwa ukapolo. 25 Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama adachitacho; ndipo palibe tsankhu pakati pa anthu.

Akolose 4

1 Ambuye inu chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana, podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m’Mwamba. 2 Chitani khama m’kupemphera,nimudikire momwemo ndi chiyamiko; 3 Ndikutipemphereranso ife pomwepo, kutiMulungu atitsegulire ife pakhomo pa mawu,kuti tiyankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m’ndende; 4 Kuti ndichiwonetse ichi monga ndiyenera kuyankhula. 5 Muyende mu nzeru ndi iwo akunja, kuchita changu nthawi ingatayike. 6 Mawu anu akhale m’chisomo nthawi zonse wokoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani. 7 Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko,m’bale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mzanga mwa Ambuye: 8 Amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe,kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu; 9 Pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali m`modzi wa inu zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu zinthu zonse zimene zachitika kuno. 10 Aristarko wa m’ndende mzanga akupatsani moni, ndi Marko,msuweni wa Barnaba (amene mudalandira malamulo ngati abwera kwa inu; ) 11 Ndi Yesu,wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo wokha ndiwo antchito amzanga a mu Ufumu wa Mulungu;ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima. 12 Akupatsani moni Epafra ndiye m`modzi wa inu, ndiye mtumiki wa Yesu Khristu, wakulimbika chifukwa cha inu m’mapemphero ake masiku onse,kuti mukayime angwiro ndi wodzazidwa m’chifuniro chonse cha Mulungu. 13 Pakuti ndimachitira Iye umboni ali ndi changu chachikulu cha kwa inu, ndi iwo a m’Lodikaya, ndi iwo a m’Herapoli. 14 Luka sing’anga wokondedwa,ndi Dema,akupatsani moni. 15 Patsani moni abale ali m’Lodikaya, ndi Numfa, ndi Mpingowo wa m’nyumba yawo. 16 Ndipo pamene muwerenga kalata uyu,amuwerengenso ku Mpingo wa ku Lodikaya, ndi inunso momwemo muwerenge wa ku Lodikaya. 17 Ndipo nenani kwa Arkipo, samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye kuti uwukwanitse. 18 Moni wa dzanja langa ine Paulo, kumbukirani nsinga zanga. Chisomo chikhale nanu. Ameni.

1 Atesalonika 1

1 Paulo, Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. 2 Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kukumbukira inu m’mapemphero athu; 3 Ndikukumbukira kosalezeka ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu ndi Atate wathu; 4 Podziwa, abale wokondedwa chisankhidwe chanu cha kwa Mulungu. 5 Pakuti Uthenga Wabwino wathu sudadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’zitsimikizo zazikulu; monga mudziwa tidakhala wonga wotani mwa inu chifukwa cha inu. 6 Ndipo mudayamba kukhala akutsanza athu, ndi wa Ambuye, m’mene mudalandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera: 7 Kotero kuti mudayamba kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupirira m’Makedoniya ndi m’Akaya. 8 Pakuti kuchokera kwa inu kudamveka mawu wa Ambuye, osati m’Makedoniya ndi Akaya mokha, komatu m’malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidafalikira; kotero kuti sikufunika kwa ife kuyankhula kanthu. 9 Pakuti iwo wokha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu adali wotani; ndi momwe mudatembenukira kwa Mulungu posiyana nawo mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo; 10 Ndikulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene adamuukitsa kwa akufa, ndiye Yesu wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulimkudza.

1 Atesalonika 2

1 Pakuti abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sadakhala wopanda pake; 2 Koma ngakhale tidamva zowawa kale, ndipo adatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Afilipi, tidalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kuyankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri. 3 Pakuti kudandaulira kwathu sikuchokera kukusochera kapena kuchidetso, kapena m’chinyengo: 4 Komatu monga Mulungu adatibvomereza kutiyikiza Uthenga Wabwino, kotero tiyankhula; osati monga wokondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu. 5 Pakuti sitidagwiritsa ntchito nawo mawu wosyasyalika nthawi ili yonse, monga mudziwa, kapena kusilira, mboni ndi Mulungu; 6 Kapena sitidafuna kukhala wofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa ena, tingakhale tidali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu. 7 Komatu tidakhala wofatsa pakati pa inu, monga m’mene mlezi afukata ana ake a iye yekha: 8 Potero pokhara wokhudzidwa ndichikhumbo cha kwa inu tidabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala wokondedwa kwa ife. 9 Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chibvuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tidalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu. 10 Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tidakhala woyera mtima ndi wolungama ndi wosalakwa kwa inu akukhulupirira: 11 Monga mudziwa momwe tidalimbikitsidwira ndi kutonthozedwa ndi kulamulira wina aliyense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, 12 Kuti muyende koyenera Mulungu, amene adakuyitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha ndi ulemerero. 13 Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza chifukwa, pamene mudalandira mawu a Mulungu, amene mudawamva kwa ife, simudawalandire monga mawu a anthu, komatu monga ali chowonadi ndithu, mawu a Mulungu amenenso agwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira. 14 Pakuti inu, abale, mudayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m’Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zonsezi inu mudazimva kuwawa ndi anthu a mdziko lanu la inu nokha, monganso iwo adachitira a Ayuda. 15 Amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri awo, natinzunza ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nawo anthu onse; 16 Natiletsa ife kuti tisayankhule ndi amitundu kuti apulumutsidwe; kudzazitsa machimo awo nthawi zonse: chifukwa mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro. 17 Koma ife, abale, angakhale adatichotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ayi, tidayesetsa koposa kuwona nkhope yanu ndi chikhumbo chachikulu. 18 Chifukwa tidafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana adatiletsa. 19 Pakuti chiyembekezo chathu, mchiyani kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye n’chiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu Khristu pakufika kwake? 20 Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.

1 Atesalonika 3

1 Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidabvomereza mtima atisiye tokha ku Atene; 2 Ndipo tidatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m’Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu: 3 Kuti asasunthike munthu aliyense ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiyika ife tichite izi. 4 Pakutinso, pamene tidali ndi inu tidakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa. 5 Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndidatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo ntchito yathu yikadakhala yopanda pake. 6 Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiwona ife, monganso ife kukuwonani inu: 7 Chifukwa cha ichi, abale, tatonthozedwa pa inu m’kupsinjika kwathu konse ndi chisautso chathu chonse, mwa chikhulupiriro chanu: 8 Pakuti tsopano tiri ndi moyo ngati inu muchilimika mwa Ambuye. 9 Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu; 10 Ndikuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikawone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewerera pa chikhulupiriro chanu? 11 Koma tsopano Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu atitsogolere m’njira yakufika kwa inu. 12 Koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m’chikondano wina kwa mzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu: 13 Kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m’chiyero pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu Khristu pamodzi ndi woyera mtima ake onse.

1 Atesalonika 4

1 Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga mudalandira kwa ife mayendedwe wokoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo. 2 Pakuti mudziwa malangizo amene tidakupatsani mwa Ambuye Yesu. 3 Pakuti ichi ndichifuniro cha Mulungu ndicho chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kuchiwerewere: 4 Aliyense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu; 5 Kosati m’chisiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu: 6 Asapitilireko munthu, nanyenge mbale wake m’menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tidakuchenjezani, ndipo tidachitapo umboni. 7 Pakuti Mulungu sadayitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso. 8 Chifukwa chake iye wonyoza ichi, sanyoza munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa ife. 9 Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani inu ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mzake; 10 Ndipo zowonadi, mudawachitira ichi abale onse a m’Makedoniya lonse. Koma tikupemphani, abale, kuti muchuLuka ndi kuchuluka koposa; 11 Ndikuti muphunzire, kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tidakulamulirani; 12 Kuti mukayende mowona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu. 13 Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona, kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. 14 Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu. 15 Pakuti ichi tinena kwa inu m’mawu wa Ambuye, kuti ife wokhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera wogonawo. 16 Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuwu, ndi mawu a m’ngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu: ndipo akufa mwa Khristu adzawuka choyamba. 17 Pamenepo ife wokhala ndi moyo wotsalafe tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. 18 Chomwecho, tonthozanani wina ndi mzake ndi mawu awa.

1 Atesalonika 5

1 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale sikufunika kuti ndikulembereni. 2 Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. 3 Pamenepo adzangonena, Mtendere ndi chitetezo, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera iwo, monga zowawa za mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse. 4 Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala. 5 Pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; simuri a usiku, kapena amdima; 6 Chifukwa chake tsono tisagone monga achitira enawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere. 7 Pakuti iwo akugona, agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku. 8 Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titabvala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi, ndi chisoti chimene ndi chiyembekezo cha chipulumutso. 9 Pakuti Mulungu sadatiyika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, 10 Amene adafa m’malo mwathu, kuti, pamene tidzuka kapena kugona, tikhale ndi moyo pamodzi ndi Iye. 11 Mwa ichi tonthozanani, ndipo mangiliranani wina ndi mzake, monganso mumachita. 12 Koma abale, tikupemphani, adziweni iwo amene amagwira ntchito mwa inu, nakhala akulu akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; 13 Ndipo muwachitire ulemu wapamwambatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo, ndipo khalani ndimtendere mwa inu nokha. 14 Ndipo tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, tonthozani amantha mtima, chilikizani wofoka, mukhale woleza mtima pa anthu onse. 15 Penyani kuti wina asabwezere choyipa womchitira choyipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa anthu onse. 16 Kondwerani nthawi zonse. 17 Pempherani kosalekeza. 18 Mzinthu m’zonse yamikani: pakuti ichi ndichifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu. 19 Musazime Mzimuyo. 20 Musanyoze manenero. 21 Yesani zinthu zonse; sungani chokomacho. 22 Mupewe mawonekedwe onse a choyipa. 23 Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konse konse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 24 Wakuyitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita. 25 Abale, tipempherereni ife. 26 Patsani moni abale onse ndi chipsompsono chopatulika. 27 Ndikulamurirani mwa Ambuye kuti kalatayu awerengedwe kwa abale onse woyera mtima. 28 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu. Ameni.

2 Atesalonika 1

1 Paulo, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu: 2 Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. 3 Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera, pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mzake mochuluka. 4 Kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m’mipingo ya Mulungu chifukwa cha chipiliro chanu ndi chikhulupiriro chanu, m’mazunzo anu onse ndi zisautsozo zimene mupirira nazo; 5 Ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu, kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu umenenso mudamva nawo zowawa; 6 Powona kuti ndicho chilungamo kwa Mulungu kuti abwezere chinzunzo kwa iwo akukuchitirani inu chisautso. 7 Ndi kwa inu amene munzunzidwa pumulani pamodzi ndi ife, ndipo pamene Ambuye Yesu adzabvumbuluka kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. 8 M’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osadziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 9 Amene adzalangidwa ndicho chiwonongeko chosatha chochokera ku nkhope ya Ambuye ndi ku ulemerero wa mphamvu yake. 10 Pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake ndi kukhala woyamikiridwa ndi onse wokhulupirira (pakuti mudakhulupirira umboni wathu tidauchita kwa inu) m’tsiku lija. 11 Chomwechonso tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kumayitanidwe awa, ndikukwaniritsa chokoma chonse cha ubwino wake ndi ntchito yachikhulupiriro ndi mphamvu; 12 Kuti dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

2 Atesalonika 2

1 Ndipo tikupemphani abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye. 2 Kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mawu, kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika. 3 Munthu asakunyengeni kwina kulikonse, kuti tsikulo silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho nabvumbulutsike munthu wawuchimoyo mwana wa chionongeko. 4 Amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembezeka, kotero kuti iye monga Mulungu wakhala pansi ku kachisi wa Mulungu nadziwonetsera yekha kuti ali Mulungu. 5 Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani zinthu izi. 6 Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akabvumbulutsidwe iye m’nyengo yake ya iye yekha. 7 Pakuti chinsinsi cha kusayeruzika chayambadi kuchita, chokhachi pa womletsa tsopano, kufikira a kam’chotsa pamenepo. 8 Ndipo pamene adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo amene Ambuye Yesu adzamuwononga ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuwononga ndi mawonekedwe a kudza kwake. 9 Ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozwizwa zonama, 10 Ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo. 11 Ndipo chifukwa cha ichi Mulungu adzatumiza kwa iwo molimba machitidwe akusocheretsa, kuti akhulupirire bodza, 12 Kuti onse awonongeke amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama. 13 Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi. 14 Kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 15 Chifukwa chake tsono, abale, chirimikani, gwiritsitsani miyambo imene tinakuphunzitsani kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu. 16 Tsopano Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyekha, ndi Mulungu amene ndi Atate wathu amene adatikonda ife natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo, 17 Atonthoze mitima yanu nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mawu onse abwino.

2 Atesalonika 3

1 Chotsalira, abale mutipempherere kuti mawu a Ambuye afalikire nalemekezedwe, monganso kwanu, 2 Ndi kuti tilanditsidwe m’manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro. 3 Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu nadzakusungani kuletsa woyipayo. 4 Koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani. 5 Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m’chikondi cha Mulungu ndi m’chipiriro poyembekezera Khristu. 6 Tsopano tikulamulirani, abale m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu kuti, musiye kuyenda pamodzi ndi m’bale aliyense woyenda mosalongosoka, wosatsata mwambo umene adaulandira iye kwa ife. 7 Pakuti mudziwa inu nokha momwe muyenera kutitsatira ife: pakuti sitidakhala ife pakati pa inu mosalongosoka; 8 Kapena sitinadya mkate chabe pa dzanja la munthu ali yense komatu ndi chibvuto ndi chipsinjo tidagwira ntchito usiku ndi usana kuti tingalemetse wina wa inu: 9 Si chifukwa kuti tiribe ulamuliro, komatu tidadziyika tokha, tikhale chitsanzo kwa inu, kuti mukatsatire ife. 10 Pakutinso pamene tidali nanu tidakulamulirani ichi kuti, ngati munthu safuna kugwira ntchito asadyenso. 11 Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti akuyenda mosalongosoka osafuna kugwira ntchito konse koma ali ochita mwina ndi mwina. 12 Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo wokha. 13 Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino. 14 Koma ngati wina samvera mawu athu m’kalata uyu, m’dziweni bwino bwino ameneyo. Kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi: 15 Koma musamuyese m’dani, koma mumuyambirire ngati m’bale. 16 Ndipo Ambuye wa mtendere yekha akupatseni inu mtendere nthawi zonse, omwemo Ambuye akhale ndi inu nonse. 17 Moni wa Paulo ndipo ndi dzanja langa mwini, chimene ndi chizindikiro m’kalata aliyense ndiko kulemba kwanga. 18 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.

1 Timoteo 1

1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamulo cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, chiyembekezo chathu: 2 Kwa Timoteo mwana wanga weniweni m’chikhulupiriro: chisomo, chifundo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu. 3 Monga ndidakulamulira iwe kuti ukhalebe ku Aefeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse chiphunzitso china. 4 Kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, amene atumikira mafunso, koposatu kumangirira kwa Umulungu kumene kuli m’chikhulupiriro: 5 Tsopano chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi, chochokera mu mtima woyera ndi m’chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga: 6 Zimenezo, ena pozilambalala adapatukira kutsata mawu wopanda pake: 7 Pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena kapena azilimbikirazi. 8 Koma tidziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo; 9 Koma podziwa ichi, kuti lamulo siliyikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi am’nyozo, akupha atate ndi akupha amayi, akupha amzawo. 10 Achigololo, akuchita zoyipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, wolumbira zonama, ndipo ngati kuli kanthu kena kamene ndikosemphana ndi chiphunzitso cholamitsa; 11 Monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene udaperekedwa mkukhulupirika kwanga. 12 Ndiyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu Ambuye wathu, kuti adandiyesa wokhulupirika, nandiyika kuutumiki; 13 Amene kale ndidali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu adandichitira chifundo, popeza ndidazichita wosazindikira, wosakhulupirira. 14 Koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chiri mwa Khristu Yesu. 15 Mawuwa ali wokhulupirika ndi woyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa wochimwa wa iwowa ine ndine woposa. 16 Komatu mwa ichi adandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akawonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m’tsogolo kufikira moyo wosatha. 17 Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosabvunda, yosawoneka, Mulungu wa nzeru yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen. 18 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino. 19 Ndikukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chawo chidatayika: 20 A iwo amene ali Humenayo ndi Alesandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusayankhula zamwano.

1 Timoteo 2

1 Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; 2 Chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale wodekha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekezeka monsemo. 3 Pakuti ichi n’chokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; 4 Amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi. 5 Pakuti pali Mulungu m’modzi ndi Mtetezi m’modzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu; 6 Amene adadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse; kuti akachitidwe umboni m’nyengo zake. 7 Umene adandiyika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zowona mwa Khristu, wosanama ine;) mphunzitsi wa a mitundu m’chikhulupiriro ndi chowonadi. 8 Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja woyera, wopanda mkwiyo ndi makani: 9 Momwemonso, akazi adzibveke wokha ndi chobvala choyenera, ndi manyazi, ndi chiletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; 10 Komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu) mwa ntchito zabwino. 11 Mkazi aphunzire akhale wachete m’kumvera konse. 12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. 13 Pakuti Adamu adayamba kulengedwa, pamenepo Heva. 14 Pakuti Adamu sadanyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa adalowa m’kulakwa. 15 Koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.

1 Timoteo 3

1 Mawuwa ali wokhulupirika, ngati mwamuna akhumba udindo wa woyang’anira, ayifuna ntchito yabwino. 2 Ndipo kuyenera woyang’anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi m’modzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa; 3 Wosati woledzera, kapena womenyana ndewu; komatu wofatsa, wopanda ndewu, wosakhumba chuma; 4 Woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nawo ana ake womvera iye ndi kulemekeza konse; 5 (Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba yake ya iye yekha, adzasamalira bwanji Mpingo wa Mulungu?) 6 Asakhale amene watembenuka mtima kumene, kuti podzitukumula ndi kunyada, ngagwe ndi kutsutsa kwa mdierekezi. 7 Kuyeneranso kuti iwo a kunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi. 8 Momwemonso atumiki akhale wolemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati achisiliro chonyansa; 9 Wokhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m’chikumbumtima chowona. 10 Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala wopanda chifukwa. 11 Momwemo akazi awonso akhale wolemekezeka, wosadierekeza, wodzisunga, wokhulupirika m’zonse. 12 Atumiki akhale mwamuna wa mkazi m’modzi woweruza bwino ana awo, ndi iwo a m’nyumba yawo ya iwo wokha. 13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera wokha mbiri yabwino ndi kulimbika kwakukulu m’chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. 14 Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, 15 Koma ngati ndichedwa kuti udziwe momwe: uyenera kukhalira m’nyumba ya Mulungu, umene uli Mpingo wa Mulungu wamoyo, m’zati ndi maziko a m’chilikizo wa chowonadi. 16 Ndipo pobvomereza chinsinsi chakuchitira Umulungu ulemu n’chachikulu: Mulungu amene adawonekera m’thupi, adayesedwa wolungama mumzimu, adapenyeka ndi angelo, adalalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.

1 Timoteo 4

1 Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda; 2 M’mawonekedwe wonyenga a iwo onena mabodza, wosindikizidwa m’chikumbumtima mwawo monga ndi chitsulo chamoto; 3 Akuletsa ukwati; wosiyitsa zakudya zina, zimene Mulungu adazilenga kuti achikhulupiriro ndi wozindikira chowonadi azilandire ndi chiyamiko. 4 Pakuti cholengedwa chiri chonse cha Mulungu n’chabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kukanidwa ngati kalandiridwa ndi chiyamiko: 5 Pakuti kayeretsedwa ndi Mawu a Mulungu ndi pemphero: 6 Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Yesu Khristu, woleledwa bwino m’mawu achikhulupiriro, ndi chiphunzitso chabwino chimene iwe wachitsata. 7 Koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba uzikane. Ndipo udzizolowetse kuchita chipembedzo. 8 Pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la moyo uno, ndi la moyo uli mkudza. 9 Wokhulupirika mawuwa ndi woyenera kulandiridwa ndi onse. 10 Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tiri nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa wokhulupirira. 11 Lamulira izi, nuziphunzitse. 12 Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo wokhulupirira, m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, mu mzimu, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima. 13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga kuchenjeza, ndi kuphunzitsa. 14 Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuyika kwa manja a akulu. 15 Uzilingalire zinthu izi; mu izi ukhale; kuti phindu lako liwonekere kwa onse. 16 Udziyang’anire iwemwini ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.

1 Timoteo 5

1 Wamkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale; 2 Akazi akulu ngati amayi; akazi ang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse. 3 Chitira ulemu amasiye amene ali a masiye ndithu. 4 Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi n’cholandirika pamaso pa Mulungu. 5 Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m’mapembedzero usiku ndi usana. 6 Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo. 7 Ndipo zinthu izi ulamulire kuti akhale iwo wopanda chilema. 8 Koma ngati wina sadziwa kugawira mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo akhala woyipa kuposa wosakhulupirira. 9 Asawerengedwe wamasiye ngati sadafike zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wamwamuna m’modzi. 10 Wambiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsapo mapazi wa woyera mtima, ngati adathandizapo wosautsidwa , ngati adatsatadi ntchito zonse zabwino. 11 Koma amasiye ang’ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa; 12 Pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chawo choyamba. 13 Ndipo aphunziranso kuchita ulesi, aderuderu; koma wosati ulesi wokha, komatunso ayankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, woyankhula zosayenera. 14 Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye a ang’ono, nabale ana, nawatsogolere mnyumba, osapatsa chifukwa kwa m’daniyo chakulalatira. 15 Pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana. 16 Ngati pali mwamuna kapena mkazi ali nawo amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu. 17 Akulu akuweruza bwino awerengedwe woyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso. 18 Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng’ombe yophuntha tirigu. Ndipo wogwira ntchito ayenera kulandira malipiro ake. 19 Pamkulu usalandire chom’nenezera koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu. 20 Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti wotsalawo ena achite mantha. 21 Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Ambuye Yesu Khristu, ndi angelo wosankhidwa, kuti usunge zinthu izi kopanda kusiyanitsa, wosachita kanthu monga mwa tsankhu. 22 Usafulumira kuyika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoyipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima. 23 Usakhalenso wakumwa madzi wokha, koma ugwiritse ntchito vinyo pang’ono, chifukwa cha m’mimba mwako ndi zofowoka zako zobwera kawiri kawiri. 24 Zochimwa za anthu ena ziri zowoneka kale, zitsogola kumka kumlandu; koma enanso ziwatsata. 25 Momwemonso pali ntchito zabwino zidawonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika.

1 Timoteo 6

1 Onse amene ali akapolo am’goli, ayesere ambuye a iwo wokha woyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano. 2 Ndipo iwo akukhala nawo ambuye akukhulupira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali wokhulupira ndi wokondedwa, ndi woyanjana nawo pa chokomacho. Izi uziphunzitse, nuchenjeze. 3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosabvomerezana nawo mawu a moyo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitso chiri monga mwa chipembedzo; 4 Iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mawu, kumene zichokerako njiru, ndewu, zamwano, mayerekezo woyipa, 5 Makani wopanda pake a anthu woyipsika nzeru ndi wochotseka chowonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa: kwa iwo udzipatule. 6 Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu. 7 Pakuti sitidatenga kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano. 8 Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire. 9 Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi mu msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. 10 Pakuti muzu wa zoyipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, adasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri. 11 Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu izi: nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiliro, chifatso. 12 Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuyitanira, ndipo wabvomereza chibvomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri. 13 Ndikulamulira pa maso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene adachitira umboni chibvomerezo chabwino kwa Pontiyo Pilato; 14 Kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira mawonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu. 15 Limene adzaliwonetsa m’nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye; 16 Amene Iye yekha ali nawo moyo wosatha, wakukhala m’kuwunika kosakhoza kufikako; amene munthu sadamuwona, kapena sadakhoza kumuwona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Ameni. 17 Lamulira iwo a chuma m’nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, komatu Mulungu, amene atipatsa ife chuma cha zinthu zonse kochuluka, kuti tikondwere nazo; 18 Kuti achite zabwino, nachuLuka ndi ntchito zabwino, nakonzekere kugawira ena, ndikuyanjana; 19 Ndikudziyikira wokha maziko abwino kunyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo wosatha. 20 Timoteo iwe; sunga, chimene chayikizidwa kuchikhulupiriro chako, nupewe zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama: 21 Chimene ena pochibvomereza, adalakwa m’chikhulupiriro. Chisomo chikhale nanu. Ameni.

2 Timoteo 1

1 Paulo mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa mwa Khristu Yesu. 2 Kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu. 3 Ndiyamika Mulungu amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m’mapemphero anga usiku ndi usana; 4 Kukhumba kwakukulu kofuna kuwona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndikadzadzidwe nacho chimwemwe; 5 Pamene ndikumbukira chikhulupiriro chako chosafowoka chiri mwa iwe, chimene chidayamba kukhala mwa ambuyako Loisi, ndi mwa mayi wako Yunisi; ndipo ndakopeka mtima, mwa iwenso. 6 Chifukwa chake, ndikukumbutsa iwe kuti uyitakase mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe ya mwa kuyika kwa manja anga. 7 Pakuti Mulungu sadatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi woganiza bwino. 8 Potero usachita manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wa ndende wake; komatu ukhale olandirana nawo masautso a Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu; 9 Amene adatipulumutsa ife, natiyitana ife ndi mayitanidwe woyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu zisadayambe nthawi zosayamba. 10 Koma chawonetsedwa tsopano mwa kuwonekera kwa Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, amene wagonjetsa imfa, nawonetsera poyera moyo ndi chosabvunda mwa Uthenga Wabwino: 11 Umene ndayikikapo ine mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake. 12 Chifukwa cha ichinso ndimva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndidziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndakopeka kuti lye ndiwokwanitsa kusunga chimene ndadzipereka nacho kwa lye kufikira tsiku lijalo. 13 Gwira chitsanzo cha mawu omveka bwino, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chiri mwa Khristu Yesu. 14 Kuti chinthu chabwino chidaperekedwa kwa iwe, uchisunge mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife. 15 Ichi uchidziwa, kuti onse a mu Asiya abwerere kusiyana nane; a iwo ali Fugelo ndi Hermogene. 16 Ambuye achitire banja la Onesiforo chifundo; pakuti adatsitsimutsa ine kawiri kawiri, ndipo sadachita manyazi ndi unyolo wanga: 17 Koma pamene ndidali ku Roma ine, iye adandifunafuna ine ndi khama, nandipeza. 18 Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye mtsiku lijalo: ndi muja danditumikira m’zinthu zambiri mu Aefeso, uzindikira iwe bwino.

2 Timoteo 2

1 Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m’chisomo cha mwa Khristu Yesu. 2 Ndipo zinthu zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uyikize kwa amuna wokhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso. 3 Umve zowawa pamodzi nane monga m’silikali wabwino wa Yesu Khristu. 4 Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akamkondweretse iye amene adamlemba usilikali. 5 Koma ngatinso wina ayesana nawo m’makani a masewero, sabvekedwa korona ngati sadayesana monga adapangana. 6 Wam’munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo. 7 Lingilira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m’zinthu zonse. 8 Kumbukira kuti Yesu Khistu,wochokera mu mbewu ya Davide, adawukitsidwa kwa akufa monga mwa Uthenga wanga Wabwino. 9 M’mene ine ndimva mabvuto a zowawa, monga wochita zoyipa; ngakhale mpaka kumangidwa, koma mawu a Mulungu samangidwa. 10 Mwa ichi ndipilira mzinthu zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutso cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha. 11 Wokhulupirika mawuwa: pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso ndi moyo mwa Iye: 12 Ngati tipilira tidzachitanso ufumu ndi Iye; ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife. 13 Ngati tikhala wosakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha. 14 Uwakumbutse zinthu izi, ndi kuwachitira umboni pa maso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mawu wosapindulitsa kanthu, koma wogwetsa iwo akumva. 15 Phunzira kuti udziwonetsere wekha kwa Mulungu wobvomerezeka, mwamuna wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wogawa molunjika nawo bwino mawu a chowonadi. 16 Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzachulukirabe kutsata chisapembedzo. 17 Ndipo mawu awo adzanyeka chironda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto. 18 Ndiwo amene adasokera kunena za chowonadi, ponena kuti kuwuka kwa akufa kwachitika kale napasula chikhulupiriro cha ena. 19 Komatu maziko a Mulungu ayimikidwa mokhazikika, wokhala ndi chosindikizira ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo adzipatule kuchoyipa aliyeyense wakutchula dzina la Khristu. 20 Koma m’nyumba yayikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndi zina za ulemu, koma zina zopanda ulemu. 21 Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa zinthu izi, adzakhala chotengera cha ulemu, chopatulika, choyenera kuchigwiritsa ntchito Ambuye, chokonzekeretsedwa kuntchito yonse yabwino. 22 Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuyitana pa Ambuye ndi mitima yoyera. 23 Koma mafunso wopusa ndi wosaphunzirapo kanthu upewe, podziwa kuti abala ndewu. 24 Ndipo kapolo wa Ambuye asalimbane; koma akhale waulere pa anthu onse wodziwa kuphunzitsa, woleza, 25 Wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenukiro, kukazindikira chowonadi; 26 Ndikuti akadzipulumutse ku msampha wa mdierekezi, amene adagwidwa naye, ukapolo kukachita chifuniro chake.

2 Timoteo 3

1 Koma zindikira ichi, kuti masiku wotsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. 2 Pakuti anthu adzakhala wodzikonda wokha, wokonda ndalama, wodzitamandira, wodzikuza, amwano, wosamvera, akuwabala, wosayamika, wosayera mtima 3 Wopanda chikondi chachibadwidwe, wosayanjanitsika, akudierekeza, wosakhoza kudziletsa, awukali, wosakonda abwino. 4 Achiwembu, aliwuma, wolimbirira, wotukumuka mtima, wokonda zokondweretsa munthu, wosati wokonda Mulungu; 5 Akukhala nawo mawonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adayikana; kwa iwonso udzipatule. 6 Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m’nyumba nagwira akazi wopusa, wosenza akatundu a zoyipa zawo, wotengedwa nazo zilakolako za mitundu mitundu, 7 Wophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufika ku chizindikiritso cha chowonadi. 8 Ndipo monga momwe Yane ndi Yambre adatsutsana naye Mose, kotero iwonso adzatsutsana nacho chowonadi: ndiwo anthu wobvunditsitsa mtima, wosatsimikizidwa pachikhulupiriro. 9 Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwawo kudzawonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja. 10 Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiliro. 11 Mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga adandichitira mu Antiyokeya, mu Ikoniya, mu Lustro, mazunzo wotere wonga ndawamva; ndipo m’zonsezi Ambuye adandilanditsa. 12 Ndipo onse akufuna kukhala wopembedza m’moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo. 13 Koma anthu woyipa ndi wonyenga, adzayipa chiyipile, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa. 14 Koma ukhalebe iwe mu zinthu zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa. 15 Ndi kuti kuyambira umwana wako wadziwa malembo wopatulika, wokhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. 16 Lemba liri lonse adaliwuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo; 17 Kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito ili yonse yabwino.

2 Timoteo 4

2 Timothy 4 not available

Tito 1

1 Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha wosankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha chowonadi chiri monga mwa chipembedzo. 2 M’chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, adalonjeza lisadakhale dziko lapansi; 3 Koma panyengo za Iye yekha adawonetsa mawu ake mu ulalikiro, umene adandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu; 4 Kwa Tito mwana wanga weni weni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse; chisomo, chifundo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu Mpulumutsi wathu. 5 Chifukwa cha ichi ndidakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukayike akulu m’mizinda yonse, monga ndidakulamulira: 6 Ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wamkazi m’modzi, wokhala nawo ana wokhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mawu. 7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliwuma, wosapsa mtima msanga, wosamwetsa vinyo, wosati wa chiwawa, wopanda ndewu, wosati wa chisiliro chonyansa. 8 Komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda anthu abwino, wosaledzera wolungama, woyera mtima, wodziletsa; 9 Wogwira mawu wokhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m’chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa wotsutsana naye. 10 Pakuti alipo ambiri wosamvera mawu, woyankhula zopanda pake, ndi wonyenga maka maka iwo a kumdulidwe: 11 Amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiliro chonyansa. 12 Wina wa mwa iwo, ndiye m’neneri wa iwo wokha, adati, Akrete ndiwo abodza masiku onse, zirombo zoyipa, aulesi ndi adyera. 13 Umboni uwu uli wowona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale wolama m’chikhulupiriro. 14 Osasamala nthano zachabe za chiyuda, ndi malamulo wa anthu wopatuka kusiyana nacho chowonadi. 15 Kwa oyera mtima zonse ndi zoyera: koma mwa iwo wodetsedwa ndi wosakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zawo ndi chikumbumtima chawo. 16 Abvomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana Iye, popeza ali wonyansitsa, ndi wosamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino wosatsimikizidwa.

Tito 2

1 Koma iwe, yankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa: 2 Wokalamba akhale wodzisunga, wolemekezeka, wodziletsa, wolama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiliro. 3 Momwemonso akazi wokalamba akhale nawo makhalidwe woyenera anthu woyera, wosasinjirira,wosamwetsa vinyo, akuphunzitsa zinthu zokoma. 4 Kuti akalangize akazi ang’ono kuti akhale wodziletsa akonde amuna awo, akonde ana awo,anzeru wosati achiwerewere. 5 Akhale wosunga nyumba abwino, akumvera amuna a iwo okha, kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano. 6 Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale wodziletsa. 7 Mzinthu zonse udziwonetsere wekha chitsanzo cha ntchito za bwino; m`chiphunzitso chako uwonetsere chosabvunda, ulemekezeko, ndi ulemu. 8 Mawu olama, wosatsutsika; kuti iye wakutsutsana nawe achite manyazi, posakhala nako kanthu koyipa kunenera inu. 9 Uwalimbikitse akapolo amvere ambuye wawo wa iwo wokha, nawakondweretse m`zinthu zonse; wosawiringula mawu awo; 10 Akhale wosaba, koma awonetsere kukhulupirika konse kwa bwino: kuti akakometsere chiphunzitso cha Mulungu Mpulumutsi wathu mzinthu zonse. 11 Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chibweretsa chipulumutso chawonekera kwa anthu onse, 12 Ndikutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo mdziko lino wodziletsa, ndi wolungama, ndi wopembedza; 13 Akulindirira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Khristu Yesu: 14 Amene anadzipereka yekha m`malo mwa ife, kuti akatiwombole ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake apaderadera achangu pa ntchito zabwino. 15 Izi yankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse iwe.

Tito 3

1 Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro awamvere woweruza ndi kukhala okonzeka ku ntchito iliyonse yabwino, 2 Asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale odekha, nawonetsere chifatso chonse pa anthu onse. 3 Pakuti kale ifenso tidali opusa, osamvera, wonyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, wokhala m`dumbo, ndi njiru, wodanidwa, wodana wina ndi mzake. 4 Koma zitapita izo kukoma mtima, ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chidawonekera kwa anthu. 5 Zosati zochokera m`ntchito za m`chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake adatipulumutsa ife, mwakutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe atsopano a Mzimu Woyera: 6 Amene adatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu: 7 Kuti poyesedwa wolungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe wolowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha. 8 Wokhulupirika mawuwa, ndipo za izi ndifuna ulimbitse mawu kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri antchito za bwino. Izi ndi zokoma ndi zopindulitsa anthu. 9 Koma pewa mafunso opusa ndi mawerengedwe amibado ndi ndewu, ndi makani apamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe. 10 Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize; 11 Podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha. 12 Pamene ndituma Artema kwa iwe, kapena Tukiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako kumeneko nyengo yozizira. 13 Bweretsani Zena woyimirirra milandu ndi Apolo mwachangu. Akonzereni za ulendo, kuti asasowe kanthu. 14 Ndipo anthu athu aphunzirenso kusunga ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale wosabala zipatso. 15 Akupatsani moni iwo wonse ali ndi ine. Apatseni moni wotikondawo m`chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse. Ameni.

Filemoni 1

Philemon not available

Hebreo 1

1 Kale Mulungu adayankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, 2 Koma pakutha pake pa masiku ano adayankhula kwa ife mwa Mwana amene adamuyika wolowa nyumba wa zinthu zonse, mwa Iyenso adalenga mayiko ndi am’mwamba omwe. 3 Ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zones ndi mawu a mphamvu yake, m’mene adachita chiyeretso cha machimo athu, adakhala padzanja lamanja ;la Ukulu m’Mwamba; 4 Atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo. 5 Pakuti kwa m’ngelo uti adati nthawi ili yonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala iwe? Ndiponso Ine ndidzakhala kwa Iye Atate? Ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana? 6 Ndiponso pamene atenga wobadwa woyamba kulowa naye m’dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu. 7 Ndipo za angelo anenadi, Amene ayesa angelo ake mizimu, ndi womtumikira Iye akhale lawi lamoto. 8 Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi. Ndipo ndodo yachifumu yowongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu. 9 Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choyipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerera chenicheni. 10 Ndipo, Inu Ambuye, pachiyambipo mudayika maziko ake a dziko, ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu pamwamba pa anzanu: 11 Iyo idzawonongeka; komatu Inu mudzakhalitsa; ndipo iyo yonse idzasuluka monga achitira malaya; 12 Monga chofunda mudapinda, monga malaya, ndipo idzasanduka: koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha. 13 Koma za m’ngelo uti adati nthawi ili yonse, khala pa dzanja lamanja langa, kufikira ndikayika adani ako chopondapo mapazi ako? 14 Kodi siyili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?

Hebreo 2

1 Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo. 2 Pakuti ngati mawu adayankhulidwa ndi angelo adakhala wokhazikika, ndipo cholakwira chiri chonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama. 3 Kodi tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchiyankhula, ndipo iwo adachimva adatitsimikizira ife; 4 Pochitira umboni pamodzi nawo Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa ndi zozizwitsa za mitundu mitundu ndi mphatso za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake. 5 Pakuti sadagonjetsera angelo dziko liri mkudza limene tinenali. 6 Koma wina adachita umboni pena nati, “Munthu nchiyani kuti mumkumbukira iye? Kapena mwana wa munthu kuti mucheza naye? 7 Mudamchepsa pang’ono kuposa angelo, mudambveka iye Korona waulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuyika iye woyang’anira ntchito za manja anu: 8 Koma inu mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake. Pakutero Iye adayika zinthu zonse pansi pa iye, sadasiye kanthu kosamugonjera iye. Koma tsopano sitiziwona zinthu zonse zomgonjera iye. 9 Koma tiwonaYesu, amene adamchepsa pang’ono ndi angelo, chifukwa cha zowawa za imfa, wobvala Korona wa ulemerero ndi ulemu, ndikuti Iye mwa chisomo cha Mulungu alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense. 10 Pakuti kudamuyenera Iye, amene mwa Iye muli zinthu zonse, potenga ana ambiri alowe ulemerero, kupanga mtsogoleri wa chipulumutso chawo wangwiro mwa zowawa. 11 Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa m’modzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale, 12 Ndikunena, ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuyimbirani. 13 Ndiponso ndidzayika chikhulupiliro changa mwa Iye. Ndiponso, tawonani, Ine ndi ana amene Mulungu adandipatsa Ine. 14 Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nawo makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuwononge iye amene adali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; 15 Ndikuwombola iwo onse amene pochita mantha ndi imfa m’moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo. 16 Ponena zowona Iye sadatenge pa iye chilengedwe cha angelo; koma iye adatenga pa iye mbewu ya Abrahamu. 17 Potero kudamuyenera iye kufanizidwa ndi abale ake, kuti akakhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kukapanga chiyanjanitso cha anthu chifukwa cha uchimo. 18 Pakuti mwa ichi iye popeza adamva zowawa, poyesedwa mwiniyekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

Hebreo 3

1 Potero abale woyera mtima, wolandirana nawo mayitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wansembe wa chibvomerezo chathu, Khristu Yesu; 2 Amene adakhala wokhulupirika kwa Iye adamuyikayo, monganso Mose m’nyumba yake yonse. 3 Pakuti munthu ameneyu wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga iye amene amanga nyumba ali ndi ulemu woposa nyumbayo. 4 Pakuti nyumba ili yonse ili naye munthu adayimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu. 5 Ndipo Mosetu ndithudi adali wokhulupirika m’nyumba yake yonse, monga m’tumiki, kuchitira umboni wa zinthuzo zimene zidzayankhulidwa mtsogolo; 6 Koma Khristu monga Mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa chitsimikiziro ndi chimwemwe cha chiyembekezo, kuchigwira mpaka kumapeto. 7 Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, lero ngati mudzamva mawu ake, 8 Musaumitse mitima yanu, monga kudawawawa mtima, mtsiku la mayesero m’chipululu: 9 Pamene makolo anu adandiyesa Ine, ndikundibvomereza Ine, ndikuwona ntchito zanga zaka makumi anayi. 10 Momwemo ndidakwiya nawo m’bado uwu, ndipo ndidati, nthawi zonse amalakwa mmitima yawo; ndipo sadazindikire njira zanga. 11 Chotero ndidalumbira mu ukali wanga, Sadzalowa mpumulo wanga. 12 Tapenyani, abale, kuti kapena ungakhale mwa wina wa inu mtima woyipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo; 13 Koma dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo. 14 Pakuti takhala ife wolandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsitsa chiyambi cha chitsimikizo chathu kuchigwira mpaka kumapeto; 15 Umo anena, Lero ngati mudzamva mawu ake, musaumitse mitima yanu, monga kuwawidwa mtima. 16 Pakuti ena,pamene adamva, adawawidwa mtima: kodi si onse aja adatuluka mu Aigupto ndi Mose? 17 Koma ndi ayani adakwiya nawo zaka makumi anayi? Kodi siamene adachimwa aja, amene mitembo yawo yidagwa m’chipululu? 18 Ndipo ndi ayani adawalumbirira Iye kuti asalowe mpumulo wake, koma kwa iwo amene sadakhulupirire? 19 Chotero tawona kuti sadakhoza kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.

Hebreo 4

1 Chifukwa chake tiwope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angawoneke ngati adaliperewera. 2 Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo: koma iwowa sadapindula nawo mawu wolalikidwawo, popeza sadasanganizika ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva. 3 Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga iye adanena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga: zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuchikhazikitso cha maziko a dziko lapansi. 4 Pakuti iye wanena za malo ena a tsiku lachisanu ndi chiwiri, naterodi, Ndipo Mulungu adapumula tsiku la chisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse. 5 Ndipo m’malo awanso, ngati adzalowa mpumulo wanga. 6 Powona pamenepo tsono patsalanso kuti ena alowe mmenemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino udalalikidwa koyamba kwa iwo sadalowamo chifukwa cha kusakhulupirira. 7 Alangizanso tsiku lina, ndi kunena m’Davide, itapita nthawi yayikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mawu ake, musaumitse mitima yanu. 8 Pakuti ngati Yesu akadawapumitsa iwo, sakadayankhulanso mtsogolomo za tsiku lina. 9 Momwemo utsalira mpumulo kwa anthu a Mulungu. 10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini ku ntchito zake, monganso Mulungu ku zake za Iye. 11 Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwechi cha kusamvera. 12 Pakuti mawu a Mulungu ali a moyo, ndi wochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima. 13 Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye. 14 Popeza tsono tiri naye mkulu wansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chibvomerezo chathu. 15 Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofoka zathu; koma anayesedwa m’zonse monga ife, koma wopanda uchimo. 16 Potero tiyeni ife tilimbike poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tikalandire chifundo, ndi kupeza chisomo chakuthandiza mnthawi yakusowa.

Hebreo 5

1 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense, wotengedwa mwa anthu, amayikika chifukwa cha anthu m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mphatso, ndiponso nsembe, chifukwa cha machimo: 2 Akhale wokhoza kumva chifundo ndi wosadziwa ndi wolakwa popeza iye yekhanso amagwidwa ndi chifowoko. 3 Ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m’malo a anthuwo, moteronso m’malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo. 4 Ndipo palibe munthu adzitengera mwiniyekha ulemu uwu, komatu iye amene ayitanidwa ndi Mulungu, monga unaliri ndi Aroni. 5 Koteronso Khristu sadadzilemekeza yekha kukhala mkulu wansembe; koma Iye amene adati kwa Iye, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe. 6 Monga iye adanenanso mmalo ena, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melikizedeke. 7 Ameneyo m’masiku athupi lake, pamene adapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kolimba ndi misozi kwa Iye amene akhoza kumpulumutsa Iye mu imfa, ndipo adamvedwa chifukwa adawopa; 8 Angakhale adali Mwana, komabe iye adaphunzira kumvera mwa zinthu zimene iye adamva nazo kuwawa; 9 Ndipo popangidwa kukhala wangwiro, adakhala iye woyambitsa chipulumutso chosatha kwa iwo onse amene amvera iye; 10 Wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke. 11 Kwa Iye tiri nazo zinthu zambiri zonena, ndizobvuta kuzitanthawuzira, powona inu kuti muli wogontha mmamvedwe. 12 Pakuti ngakhale mwakhala aphunzitsi chifukwa cha nthawiyi, muli nako kusowanso kuti wina akuphunzitseninso zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala wonga wofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. 13 Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mawu achilungamo: pakuti ali khanda. 14 Koma chakudya chotafuna chiri cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo adazoloweretsa zizindikiritso zawo posiyanitsa chabwino ndi choyipa.

Hebreo 6

1 Mwa ichi, posiya mfundo za chiphunzitso cha Khristu, tiyeni ife tipite chitsogolo ku ungwiro; osayikanso maziko akulapa kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi achikhulupiliro cha kwa Mulungu, 2 Achiphunzitso cha ubatizo, ndi a chakuyika manja, ndi a chakuuka kwa akufa, ndi a chachiweruziro chosatha. 3 Ndipo ichi tidzachita, ngati atatilola Mulungu. 4 Pakuti sikutheka kwa iwo amene adaunikidwa panthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala wolandirana naye Mzimu Woyera, 5 Ndipo analawa mawu wokoma a Mulungu, ndi mphamvu za dziko lirimkudza, 6 Ngati akagwa m’chisokero posiya njirayo; kuwakonzanso iwo kuti alapenso; powona iwo alikudzipachikiranso iwowokha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera. 7 Pakuti nthaka imene idamwa mvula imene imadza kawiri kawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adayilimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu: 8 Koma ikabala minga ndi mitungwi, ikanidwa, ndipo yatsala pang’ono kutembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa. 9 Koma, wokondedwa, takopeka nanu ndi zinthu zabwino, ndizo zinthu zimene zigwirizana pamodzi ndi chipulumutso, chotero titero pakuyankhula kwathu. 10 Pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzayiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachiwonetsera ku dzina lake, muja mudatumikira woyera mtima ndipo mutumikirabe. 11 Koma tikhumba kuti yense wa inu awonetsere nzeru yomweyi kuchidzalo chachitsimikizo cha chiyembekezo mpaka chimariziro: 12 Kuti musakhale aulesi, koma wotsatira a iwo amene mwa chikhulupiriro ndi mopirira adalandira malonjezano. 13 Pakuti pamene Mulungu adapanga malonjezano ndi Abrahamu, chifukwa iye analibe cholumbirira chachikulu,adadzilumbirira mwa Iye yekha. 14 Ndikuti, zowona kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa ndidzachulukitsa iwe. 15 Ndipo chotero, iye atatha ndi chifatso kupirira, adalandira lonjezano. 16 Pakuti anthu ndithudi alumbirira pa wamkulu: ndipo lumbiro lachitsimikizo kwa iwo litsiriza matsutsano onse. 17 Choteronso Mulungu, pofuna kuwonetsa kuchuluka kwa wolowa a lonjezano ku uphungu wake wosasinthika, adatsimikizira izi mwa lumbiro. 18 Kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, mwa zimenezo kudali kobvuta kuti Mulungu aname, tiyenera ife tikakhale nacho chitonthozo cholimba, ife amene tidapulumuka pothawa kuti tikagwiritsitse chiyembekezo choyikika pamaso pathu. 19 Ndicho chiyembekezo chimene tiri nacho monga nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndichimene tilowa nacho m’katikati mwa chophimba. 20 M’mene Yesu wotitsogolera adatsogola kulowa chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.

Hebreo 7

1 Pakuti Melikizedeke uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene adakomana ndi Abrahamu, pobwerera iye atawapha mafumu aja, namdalitsa; 2 Amenenso Abrahamu adamgawira limodzi la magawo khumi la zonse ndiye posandulika poyamba ali Mfumu ya chilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiyo Mfumu ya mtendere; 3 Wopanda atate ake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu, iyeyu wakhala wansembe kosalekeza. 4 Koma tapenyani ukulu wake wa munthu uyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, adampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo. 5 Ndipo indetu iwowa mwa ana a Levi, akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale awo, angakhale adatuluka m’chiwuno cha Abrahamu; 6 Koma iye amene mawerengedwe achibadwidwe chake sachokera mwa iwo, adatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene adali nawo malonjezano. 7 Ndipo popanda chitsutsano konse wam’ngono adalitsidwa koposa wamkulu. 8 Ndipo pano anthu amene amafa amalandira chakhumi; koma kumeneko iye alandira iwo, kwa amene kudachitiridwa umboni kuti ali ndi moyo. 9 Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzi limodzi la magawo khumi adapereka limodzi lamagawo khumi; 10 Pakuti pajapo adali m’chuuno cha atate wake, pamene Melikizedeke adakomana naye. 11 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa chilevi, (pakuti momwemo anthu adalandira chilamulo) pakadatsala kusowa kotani kuti awuke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melikizedeke, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni? 12 Pakuti pakusintha unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisinthike. 13 Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe. 14 Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu adatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sadayankhula kanthu ka ansembe. 15 Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke, 16 Amene wakhala si monga mwa lamulo la thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka; 17 Pakuti amchitira umboni, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke. 18 Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufoka kwake, ndi kusapindulitsa kwake. 19 Pakuti chilamulo sichidachitira kanthu kakhale kopanda chilema, koma kubweretsa kwa chiyembekezo chabwino kudachitadi; mwa chimenecho ife tiyandikira nacho chifupi kwa Mulungu. 20 Monga momwe kudachitika sikopanda lumbiro iye adakhala wansembe: 21 (Chifukwa ansembe ajawa adapangidwa kopanda lumbiro; koma uyu ndi lumbiro mwa iye amene adanena kwa iye, walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.) 22 Momwemonso Yesu wapangidwa kukhala chitsimikizo cha pangano labwino. 23 Ndipo iwo zowonadi ambiri adakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe: 24 Koma munthu uyu, chifukwa kuti akhalabe Iye nthawi yosatha ali nawo unsembe wosasinthika. 25 Chifukwa chake kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo. 26 Pakuti mkulu wa ansembe wotere adatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choyipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi wochimwa, wakukhala wopitirira miyamba. 27 Amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyamba chifukwa cha zoyipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoyipa za anthu; pakuti ichi adachita kamodzi kwatha, podzipereka yekha. 28 Pakuti chilamulo chimayika akulu a ansembe anthu, wokhala nacho chifoko; koma mawu a lumbiro, amene adafika chitapita chilamulo, ayika Mwana, woyesedwa wopanda chilema ku nthawi zonse.

Hebreo 8

1 Tsopano mutu wa izi tanenazi ndi uwu; Tiri naye mkuru wansembe wotere, amene adakhala pa dzanja la manja la mpando wachifumu wa Ukulu m’Mwamba; 2 Mtumiki wa malo wopatulika, ndi wa chihema chowona, chimene Ambuye adachimanga, simunthu ayi. 3 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense ayikidwa kupereka mphatso, ndiponso nsembe; potero mkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka. 4 Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mphatso monga mwa lamulo. 5 Amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa ndi Mulungu m’mene adafuna kupanga chihema; pakunena kuti, onetsetsa, atero iye kuti, uchite zinthu zonse monga mwa chitsanzocho chawonetsedwa kwa iwe m’phiri. 6 Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka choposa, umonso ali nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano woposa. 7 Pakuti pangano loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo. 8 Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena, Tawonani, akudza masiku, anena Ambuye, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; 9 Losati longa pangano ndidalichita ndi makolo awo, tsikuli ndidawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuLuka m’dziko la Aigupto; kuti iwo sadakhalebe mpangano langa, ndipo Ine sindidawasamalira iwo, anena Ambuye. 10 Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga mnzeru zawo, ndipo pamtima pawo ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu: ndipo adzandikhalira Ine anthu: 11 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu m’nzake, ndipo yense mbale wake, ndi kuti zindikira Ambuye: pakuti onse adzadziwa Ine kuyambira wam’ng’ono kufikira wamkulu wa iwo. 12 Pakuti ndidzachitira chifundo zosalungama zawo, ndipo machimo ndi zoyipa zawo sindidzazikumbukanso. 13 Pakunena Iye pangano latsopano, adagugitsa loyambali. Tsopano chimene chiri mkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.

Hebreo 9

1 Ndipo zowonadi kuti chipangano choyambachi chidali nazo zoyikika za kutumikira Umulungu, ndi malo wopatulika a pa dziko lapansi. 2 Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m’menemo mudali choyikapo nyali, ndi gome, ndi mkate wowonekera; amene atchedwa malo wopatulika. 3 Koma m’kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chimene chitchedwa Malo Wopatulikitsa; 4 Wokhala nayo mbale ya zofukiza yagolidi ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golidi, momwemo mudali mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo; ndi magome a chipangano; 5 Ndi pamwamba pake aKerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera. 6 Tsopano pamene zinthu izi zidakonzeka kotero, ansembe amalowa m’chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kugwira ntchito ya Mulungu. 7 Koma kulowa m’chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene amapereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu: 8 Mzimu Woyera adatsimikizira ichi, kuti njira yolowa nayo kumalo wopatulikitsa siyidawonetsedwe, pokhala chihema choyamba chiri chiyimire: 9 Ndicho chiphiphiritso cha ku nthawi yomweyi, m’mene mphatso ndi nsembezo zidaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kumuyesa wamgwiro wotumikirayo. 10 Chimene chikhala m’zoyikika za thupi zokha ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe wosiyanasiyana, woyikidwa kufikira nthawi yakukonzanso. 11 Koma atafika Khristu, Mkulu wansembe wa zabwino ziri mkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi; 12 Kosati mwa mwazi wa mbuzi ndi ana ang’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, adalowa kamodzi kumalo wopatulika, atalandirapo chiwombolo chosatha chifukwa cha ife. 13 Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, ndi makala ang’ombe yamthandi wowazawaza pa iwo wodetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi: 14 Koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene adadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo? 15 Ndipo mwa ichi Iye ali nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti popeza kudachitika imfa yakuwombola zolakwa za pa chipangano choyamba kuti iwo, woyitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha. 16 Pakuti pamene pali pangano pafunika pafike imfa ya mwini panganolo. 17 Pakuti chipangano chikhala ndi mphamvu atafa mwini wake; pakuti sichikhala ndi mphamvu konse pokhala mwini pangano ali ndi moyo; 18 Momwemonso chipangano choyambacho sichidakonzeka chopanda mwazi. 19 Pakuti pamene Mose adayankhulira anthu onse lamulo liri lonse monga mwa chilamulo, adatenga mwazi wa ana a ng’ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiyira ndi hisope, nawaza buku, ndi anthu onse, 20 Nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulirani. 21 Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro adaziwaza momwemo ndi mwaziwo. 22 Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo popanda kukhetsa mwazi palibe kumasuka. 23 Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za m’Mwamba ziyeretsedwe ndi izi:- koma za m’mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zabwino zoposa izi. 24 Pakuti Khristu sadalowa m’malo wopatulika womangika ndi manja, amene ndi chinthunzinthu-nzi cha enieniwo; komatu m’Mwamba momwe kuwonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife: 25 Kosati kuti adzipereke yekha kawiri kawiri; monga mkulu wa nsembe alowa m’malo wopatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake; 26 Chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawiri kawiri kuyambira makhazikitsidwe a maziko a dziko lapansi: koma tsopano kamodzi kokha kumatsiriziro a nthawi wawonekera Iye kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Mwiniyekha. 27 Ndipo monga kwayikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro: 28 Chotero Khristunso adaperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri; adzawonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.

Hebreo 10

1 Pakuti chilamulo, pokhala nacho chithunzithunzi cha zabwino zirimkudza, wosati chifaniziro chenicheni cha zinthunzo, sizikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira. 2 Pakutero iwo sakadasiya kupereka nsembe? Chifukwa kuti wopembedzawo atatha kuyeretsadwa kamodzi sakadatha kukhala nacho chikumbumtima cha machimo. 3 Komatu mu nsembe izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. 4 Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotse machimo. 5 Chotero ichi polowa m’dziko lapansi anena Nsembe ndi chopereka simudazifuna, koma thupi mudandikonzera Ine. 6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simudakondwera nazo; 7 Pamenepo ndidati, Tawonani ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu Mulungu. 8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simudazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo), 9 Pamenepo adati Iye, Tawonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu Mulungu. Iye anachotsa choyambacho, kuti akayike chachiwiricho. 10 Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi kwatha. 11 Ndipotu wansembe aliyense amayima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kuchotsa machimo: 12 Koma munthu uyu, m’mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, adakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire. 13 Kuchokera pamenepa adikira kufikira Adani ake ayikidwa akhale chopondapo mapazi ake. 14 Pakuti ndi nsembe imodzi adawayesera angwiro chikhalire iwo woyeretsedwa. 15 Pameneponso Mzimu Woyeranso achita umboni kwa ife: pakuti adatha kunena kale, 16 Iri ndi pangano ndidzapangana nawo, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: ndidzapereka malamulo anga akhale pa mtima pawo; ndipo pa nzeru zawo ndidzawalemba; 17 Ndipo machimo awo ndi zoyipa zawo sindidzakumbukiranso. 18 Tsopano pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo. 19 Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m’malo wopatulika, ndi mwazi wa Yesu. 20 Panjira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera ife, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; 21 Ndipo popeza tiri naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; 22 Tiyeni tiyandikire ndi mtima wowona, m’chitsimikizo chokwana chachikhulupiriro, ndi mitima yathu yowazidwa kuchotsa chikumbumtima choyipa, ndi matupi athu wosambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritse chibvomerezo chosagwedera chachikhulupiriro chathu; (pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika:) 24 Ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino. 25 Wosaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandawulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku liri kuyandika. 26 Pakuti tikachimwa ife eni ake mwadala, titatha kulandira chidziwitso cha chowonadi, palibenso nsembe ina yotsalira Chifukwa cha machimo, 27 Koma kulindira kwina kowopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuwononga wotsutsana nawo. 28 Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa wopanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu: 29 Ndipo kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene adapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene adayeretsedwa nawo chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo? 30 Pakuti timdziwa Iye amene adati, kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Aterotu Ambuye adzaweruza anthu ake. 31 Kugwa m’manja a Mulungu wamoyo nkowopsa. 32 Koma takumbukirani masiku akale, m’menemo mudaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa: 33 Pena pochitidwa chinthu chowawitsidwa mwa matonzo ndi zisautso; pamene mudalawana nawo iwo wochitidwa zotere. 34 Pakuti mudamva chifundo ndi iwo a m’ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho chuma choposa chachikhalire m’mwamba. 35 Potero musataye kulimbika mtima kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu. 36 Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano. 37 Pakuti katsala kanthawi kakang’ono ng’ono, ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa. 38 Tsopano wolungama adzakahla ndi moyo mwa m’chikhulupiriro: ndipo ngati munthu aliyense abwerera m’mbuyo, moyo wanga udzakhala wosa kondwera mwa iye. 39 Koma ife si ndife a iwo a kubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.

Hebreo 11

1 Tsopano chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka. 2 Pakuti mwa ichi akulu adalandira umboni wabwino. 3 Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti mayiko ndi a m’mwamba womwe adakonzedwa ndi mawu a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizidapangidwa zochokera mwa zinthu zowonekazo. 4 Ndi chikhulupiriro Abeli adapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kayini, imene adachitidwa umboni nayo kuti adali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mphatso yake; ndipo mwa ichi iye, angakhale adafa ayankhulabe. 5 Ndi chikhulupiriro Enoki adatengeka kuti angawone imfa; ndipo sadapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asadamtenge, adachitidwa umboni kuti adakondweretsa Mulungu. 6 Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa Iye; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye mwa khama. 7 Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisadapenyeke, ndi pochita mantha, adamanga chombo cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene adatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chiri monga mwa chikhulupiriro. 8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu poyitanidwa adamvera kutuluka kumka ku malo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo adatuluka wosadziwa kumene ankamukako. 9 Ndi chikhulupiriro adakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhala m’mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, wolowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo. 10 Pakuti adayembekezera mzinda wokhala nawo maziko, m’misiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu. 11 Ndi chikhulupiriro Saranso adalandira mphamvu yakukhala ndi pakati, pa mbewu ndipo adabereka mwana patapita nthawi yake. Popeza adamuwerengera Iye wokhulupirika amene adalonjeza. 12 Mwa ichinso kudachokera kwa m’modzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji, ngati nyenyezi za m’mwamba, ndi ngati mchenga uli m’mbali mwa nyanja wosawerengeka. 13 Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, wosalandira malonjezano, komatu adawawona ndi kuwayankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi wogonera padziko. 14 Pakuti iwo akunena zinthu zotere awonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lawo. 15 Ndipo zowonadi, ngati iwo akadakhala wosamalira za dziko limene iwo adachokeralo, iwo akadakhala ndi mwayi wokhoza kubwerera. 16 Koma tsopano adakhumba dziko labwino, ndilo la Kumwamba: mwa ichi Mulungu sachita nawo manyazi pomuyitana Mulungu wawo; pakuti adawakonzera mzinda. 17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, adapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano adapereka mwana wake wayekha; 18 Amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbewu yako idzayitanidwa: 19 Powerengera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, adamlandiranso. 20 Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zokhudzana ndi zinthu ziri nkudza. 21 Ndi chikhulupiriro Yakobo, pamene adalimkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yake. 22 Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, adatchula za matulukidwe a ana a srayeli; nalamulira za mafupa ake. 23 Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akumbala, popeza adawona kuti ali mwana woyenera; ndipo sadawopa ulamuliro wa mfumu. 24 Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu adakana kutchulidwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farawo: 25 Nasankhula kuchitidwa zoyipa pamodzi ndi anthu a Mulungu kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoyipa zakanthawi kochepa; 26 Nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa chuma cha Aigupto; pakuti adapenyerera chobwezera cha mphotho. 27 Ndi chikhulupiriro adasiya a Aigupto, wosawopa mkwiyo wa mfumu; pakuti adapirira molimbika, monga ngati kuwona wosawonekayo. 28 Ndi chikhulupiriro adachita Paskha, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuwononga ana woyamba angawakhudze iwo. 29 Ndi chikhulupiriro adawoloka Nyanja Yofiyira kuyenda ngati pamtunda; ndipo a Aigupto poyesanso adamizidwa. 30 Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri. 31 Ndi chikhulupiriro Rahabu wachiwerewere uja sadawonongeka pamodzi ndi wosamverawo, popeza adalandira wozonda ndi mtendere. 32 Ndipo ndinena chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideyoni, Baraki, Samsoni, Yefita; za Davide ndi Samueli ndi aneneri. 33 Amene mwa chikhulupiriro adagonjetsa ma ufumu, adachita chilungamo, adalandira malonjezano adatseka pakamwa mikango. 34 Nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, nalimbikitsidwa pokhala wofoka, adakula mphamvu kunkhondo, adapitikitsa magulu a nkhondo ya chilendo. 35 Akazi adalandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena adanzunzidwa, wosalola kuwomboledwa, kuti akalandire chiwukitso chabwino. 36 Koma ena adayesedwa ndi matonzo ndi mikwapulo, inde nsinganso, ndi kuwatsekera m’ndende: 37 Adaponyedwa miyala, adachekedwa pakati, adayesedwa, adaphedwa ndi lupanga, adayendayenda wobvala zikopa za nkhosa, ndi zikopa za mbuzi, nakhala wosowa, wosautsidwa, wochitidwa zoyipa. 38 (Amenewo dziko lapansi silidayenera iwo:) wosokerera m’zipululu, ndi m’mapiri, ndi m’mapanga, ndi m’mawuna adziko. 39 Ndipo iwo onse atatha kulandira umboni mwa chikhulupiriro, sadalandira lonjezanolo. 40 Mulungu potikonzera ife zinthu zabwino, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.

Hebreo 12

1 Chifukwa chake ifenso popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chiri chonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiyikira ife ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, 2 Poyang’ana Yesu amene ali woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu, chifukwa cha chimwemwe choyikidwa pamaso pake, adapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. 3 Pakuti talingilirani Iye amene adapirira ndi wochimwa ndi wotsutsana naye kotere kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu. 4 Simudakana kufikira mwazi pomenyana nalo tchimo. 5 Ndipo mwayiwala dandauliro limene linena nanu monga ana, Mwana usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye: 6 Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira. 7 Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake samlanga? 8 Koma ngati mukhala wopanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli a m’thengo, si ana ayi. 9 Komanso tidali nawo atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tidawalemekeza: kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo? 10 Pakutitu iwo adatilanga masiku wowerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nawo pachiyero chake. 11 Chotero chilango chiri chonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa: koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere kwa iwo wozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. 12 Mwa ichi limbitsani manja wogowoka, ndi mawondo wolobodoka; 13 Ndipo lambulani misewu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m’njira, koma chichiritsidwe. 14 Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe m’modzi adzawona Ambuye; 15 Ndi kuyang’anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungaphuke muzu wina wakuwawa mtima ungabvute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nawo; 16 Kuti pangakhale wachiwerewere, kapena wam’nyozo, ngati Esau, amene adagulitsa ukulu wake wobadwa nawo ndi mtanda umodzi wachakudya. 17 Pakuti mudziwa kutinso pamene adafuna kulowa dalitsolo, adakanidwa pakuti sadapeza malo wolapa ngakhale adalifunafuna ndi misozi. 18 Pakuti simudayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe. 19 Ndi mawu a lipenga, ndi manenedwe a mawu, manenedwe amene iwo adamvawo adapempha kuti asawonjezerepo mawu: 20 (Pakuti sadakhoza kupirira nacho chimene adalamulidwacho, kuti ngati nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala kapena kulasidwa ndi mibvi: 21 Ndipo mawonekedwewo adali woopsa wotere, kuti Mose adati, Ndiwopatu ndi kunthunthumira:) 22 Komatu mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi unyinji wochuluka wa angelo, 23 Ndi kwa mnsonkhano wa onse ndi mpingo wa wobadwa woyamba wolembedwa m’Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya wolungama woyesedwa angwiro, 24 Ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakuyankhula chokoma choposa mwazi wa Abeli. 25 Penyani kuti musamkane iye woyankhulayo. Pakuti ngati iwowa sadapulumuka, pomkana Iye amene adawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife ngati tipatuka kwa Iye woyankhula kuchokera Kumwamba: 26 Amene mawu ake adagwedeza dziko lapansi; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lapansi lokha, komanso la Kumwamba. 27 Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale. 28 Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha. 29 Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.

Hebreo 13

1 Chikondi cha pa abale chikhalebe 2 Musayiwale kuchereza alendo: pakuti mwa ichi ena adachereza angelo wosachidziwa. 3 Kumbukirani am’singa, monga am’singa anzawo; wochitidwa zoyipa, monga ngati inunso adatero nanu m’thupi. 4 Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa: pakuti achiwerewere ndi achigololo adzaweruzidwa ndi Mulungu. 5 Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zinthu zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye adati, sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. 6 Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzawopa chimene munthu adzandichitira. 7 Kumbukirani atsogoleri anu, amene adayankhula nanu Mawu a Mulungu: ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo. 8 Yesu Khristu ali yemweyo dzulo ndi lero, ndi ku nthawi zonse. 9 Musatengedwe ndi ziphunzitso za mitundu mitundu, ndi zachilendo: pakuti mkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sadapindula nazo. 10 Tiri nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako. 11 Pakuti matupi anyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa nsembe kulowa m’malo wopatulika, chifukwa cha zoyipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. 12 Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva zowawa kunja kwa chipata. 13 Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa msasa wosenza tonzo lake. 14 Pakuti pano tiribe mzinda wokhalitsa, komatu tikufunafuna uli mkudzawo. 15 Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yobvomereza dzina lake. 16 Koma musayiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena: pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo. 17 Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere: pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu. 18 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri nacho chikumbu mtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino. 19 Koma ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe. 20 Tsopano Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wa mkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu. 21 Mukhale inu angwiro muntchito iri yonse yabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa inu zomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Ameni. 22 Ndipo ndikudandaulirani inu, abale, lolani mawu a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu kalata mwachidule. 23 Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga ndidzakuwonani inu. 24 Apatseni moni atsogoleri anu onse, ndi woyera mtima onse. Iwo onsenso a ku Italiya akupereka moni. 25 Chisomo chikhale ndi inu nonse. Ameni.

Yakobo 1

1 Yakobo mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m’chibalaliko: ndikupatsani moni. 2 Abale anga, muchiyese chimwemwe chokha, pamene mukugwa m’mayesero a mitundu mitundu; 3 Pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiliro. 4 Koma chipiliro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi wopanda chilema, osasowa kanthu konse. 5 Ngati wina wa inu inkasowa nzeru, apemphere kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, ndi mosatonza; ndipo adzampatsa iye. 6 Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse. Pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. 7 Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye. 8 Munthu wa mitima iwiri akhala wosakhazikika pa njira zake zonse. 9 Lolani m;bale wokhala modzichepetsa akondwere m’mene iye wakwezedwa. 10 Pamene achuma adzatsitsidwa pansi: pakuti adzapita monga duwa la udzu. 11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa mawonekedwe ake awonongeka; koteronso wachuma adzafota m’mayendedwe ake. 12 Wodala munthu wakupilira poyesedwa; pakuti pamene wabvomerezeka, adzalandira Korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye. 13 Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu: pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoyipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: 14 Koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera nichim’nyenga. 15 Pamenepo chilakolakocho chitayima, chibala uchimo: ndipo uchimo utakula msinkhu, ubala imfa. 16 Musanyengedwe, abale anga wokondedwa. 17 Mphatso ili yonse yabwino, ndi chininkho chiri chonse changwiro zichokera kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko amene alibe chisanduliko, kapena m’thunzi wa chitembenukiro. 18 Mwa chifuniro chake mwini adatibala ife ndi mawu a chowonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake. 19 Mudziwa abale anga wokondedwa, kuti munthu aliyense akhale watcheru, wodekha poyankhula, wodekha pakupsa mtima. 20 Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. 21 Mwa ichi, mutabvula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choyipa, landirani ndi chifatso mawu wowokedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. 22 Koma khalani akuchita mawu, wosati akumva wokha, ndi kudzinyenga nokha. 23 Pakuti ngati munthu ali wa kumva mawu, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake mkalilore: 24 Pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, nayiwala pompaja adali wotani. 25 Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo la ufulu, natero chipenyerere, ameneyo posakhala wakumva wakuyiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake. 26 Ngati wina adziyesera kuti ali wopembedza, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthu uyu nkopanda pake. 27 Mapembedzedwe woyera ndi wosadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

Yakobo 2

1 Abale anga, musakhale nacho chikhulupiliro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero ndi kusamala mawonekedwe a munthu. 2 Pakuti akalowa munsonkhano wanu munthu wobvala mphete yagolide, ndi chobvala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chobvala chalitsiro; 3 Ndipo mukalemekeza iye wobvala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe ima uko, kapena khala pansi pa mpando wa mapazi anga: 4 Kodi simudasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala woweruza woganizira zoyipa? 5 Mverani, abale anga wokondedwa; kodi Mulungu sadasankha osauka a dziko lapansi akhale wolemera m’chikhulupiliro, ndi wolowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye? 6 Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwo ku mabwalo a milandu? 7 Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muyitanidwa nalo? 8 Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, uzikonda mzako monga uzikonda wekha, muchita bwino: 9 Koma ngati musamala mawonekedwe a munthu, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga wolakwa. 10 Pakuti aliyense amene asunga malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. 11 Pakuti Iye wakuti, usachite chigololo, adatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo. 12 Yankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. 13 Pakuti chiweruziro chiribe chifundo kwa iye amene sadachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro. 14 Chipindulo chake n’chiyani, abale anga, munthu akanena. Ndiri nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? 15 Mchimwene kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake. 16 Ndipo wina wa inu akanena nawo, mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake n’chiyani? 17 Momwemonso chikhulupiliro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo. 18 Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiliro, ndipo ine ndiri nazo ntchito; undiwonetse ine chikhulupiliro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuwonetsa iwe chikhulupiliro changa chotuluka m’nchito zanga. 19 Ukhulupilira iwe kuti Mulungu ali m’modzi; uchita bwino: ziwanda zikhulupiliranso, ndipo zinthunthumira. 20 Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiliro chopanda ntchito chiri chakufa? 21 Abrahamu kholo lathu, sadayesedwa wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake isake nsembe pa guwa la nsembe? 22 Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro? 23 Ndipo adakwaniridwa malembo wonenawa, ndipo Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo adatchedwa bwenzi la Mulungu. 24 Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. 25 Ndipo momwemonso sadayesedwa wolungama Rahabi mkazi wadamayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira yina? 26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.

Yakobo 3

1 Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa tidzalandira kutsutsidwa kwakukulu 2 Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse. 3 Tawonani, tiyikira akavalo zogwirira m’kamwa mwawo kuti atimvere, tipotolozanso thupi lawo lonse. 4 Tawonani, zombonso; zingakhale ndi zazikulu zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigilo laling’ono ndithu kumene kuli konse afuna wogwira tsigilo. 5 Kotero lilimenso monga chiwalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zinthu zazikulu. Tawonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri! 6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu layikika lilime, limene lidetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe achibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena. 7 Pakuti mtundu uli wonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa za m’nyanja, zimazolowetsedwa, ndipo zizoloweretsedwa ndi anthu. 8 Koma lilime palibe munthu akhoza kulizolowezetsa; liri choyipa chotaktata, lodzala ndi ululu wakupha. 9 Timayamika nalo Ambuye ndi Atate; timatemberera nalonso anthu, wokhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu. 10 Kuchokera m’kamwa m;modzi momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. 11 Kodi kasupe atulutsira pa una womwewo madzi wokoma ndi owawa? 12 Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sakhoza kutulutsa wokoma. 13 Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Awonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake munzeru yofatsa. 14 Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho chowonadi. 15 Nzeru iyi sindiyo yotsika Kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda. 16 Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi ntchito ya choyipa chiri chonse. 17 Koma nzeru yochokera Kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomveka bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, ndi yopanda chinyengo. 18 Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mu mtendere kwa iwo akuchita mtendere.

Yakobo 4

1 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zilakolako zanu zochita nkhondo m’ziwalo zanu? 2 Mulakalaka, ndipo zikusowani: mukupha, ndipo mukhumba simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha. 3 Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koyipa, kuti mukachimwaze pochita zilakolako zanu. 4 Inu amuna ndi akazi achigololo, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziyika kukhala mdani wa Mulungu. 5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita kaduka? 6 Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza wodzikuza, koma apatsa chisomo wodzichepetsa. 7 Potero mverani Mulungu. Koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. 8 Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, wochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu. 9 Khalani wosautsidwa, lirani, lirani misozi: kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. 10 Dzichepetseni nokha pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani. 11 Musamanenerana zoyipa, wina ndi mzake, abale,wonenera zoyipa mbale wake, kapena woweruza m’bale wake, anenera choyipa lamulo naweruza lamulo:koma ngati uweruza lamulo: suli wochita lamulo, komatu woweruza. 12 Woyika lamulo, ndiye m’modzi ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga; koma iwe woweruza mzako ndiwe yani? 13 Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mzinda wakuti wakuti, ndikukhala komweko chaka ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nawo: 14 Inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Uli monga nthunzi, wakuwonekera kanthawi kakang’ono, ndi pamenepo ukanganuka. 15 Mudayenera kunena motere, akalola Ambuye tikakhala ndi moyo, tidzachita ichi kapena icho. 16 Koma tsopano mudzitamandira m’kudzikuza kwanu: kudzitamandira kuli konse kotero nkoyipa. 17 Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.

Yakobo 5

1 Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. 2 Chuma chanu chawola ndi zobala zanu zijiwa ndi njenjete. 3 Golidi wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku wotsiriza. 4 Tawonani, malipiro a antchitowo adakolola m’minda yanu, wosungidwa ndi inu powanyenga, afuwula; ndipo mafuwulo a wokololawo adalowa makutu a Ambuye wa makamu. 5 Mwadyerera padziko lapansi, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha. 6 Mudatsutsa, ndipo mudapha wolungamayo, Iye sadakaniza inu. 7 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Tawonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya myundo ndi masika. 8 Lezani mtima inunso, khazikitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira. 9 Musayipidwe wina ndi mzake, abale, kuti mungatsutsidwe. Tawonani, woweruza ayima pakhomo. 10 Tengani, abale chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene adayankhula m’dzina la Ambuye. 11 Tawonani, tiwayesera wodala wopilirawo. Mudamva za chipiliro cha Yobu, ndipo mwawona chitsirizo cha Ambuye kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. 12 Koma pamwamba pa zinthu zonse, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula m’mwamba kapena dziko lapansi, kapena lumbiro lina liri lonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iyayi wanu akhale iyayi; kuti mungagwe m’chitsutso. 13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Ayimbire masalmo. 14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziyitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye: 15 Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ngati adachita machimo, adzakhululukidwa kwa iye. 16 Chifukwa chake mubvomerezane wina ndi mzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mzake kuti muchiritsidwe. Pemphero lokhudza kwambiri la munthu wolungama lichita kwakukulu m’machitidwe ake. 17 Eliya adali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo adapemphera motsimikizira kuti mvula isabvumbwe: ndipo siyidagwa mvula pa dziko lapansi zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. 18 Ndipo adapempheranso, ndipo m'mwamba mudatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. 19 Abale, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi chowonadi, ndipo ambweza iye mzake; 20 Azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa ku njira yake yosochera adzapulumutsa munthu ku imfa, ndipo adzabvundikira machismo awunyinji.

1 Petro 1

1 Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa wosankhidwa akukhala alendo achibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya. 2 Wosankhidwa mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m’chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: chisomo, ndi mtendere zichulukire inu. 3 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chochuluka, adatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu, 4 Kuti tilandire cholowa chosabvunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu, 5 Amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiliro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza: 6 M’menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu: 7 Kuti mayesedwe a chikhulupiliro chanu, ndiwo amtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe wochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa kuwonekera kwa Yesu Khristu: 8 Amene mungakhale simudamuwona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, mukhulupirira inde, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: 9 Ndikulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu. 10 Mwa chipulumutso ichi chimene aneneri adachifunafuna, nafufuza mosamalitsa amene adanenera mwa chisomocho chimene chidzadza pa inu. 11 Ndikufufuza nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo adalozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nawo. 12 Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sadadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene adakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba: zinthu izi angelo adakhumba kusuzumiramo. 13 Mwa ichi, podzimanga m’chuuno, kunena za mtima wanu; mukhale wodzisunga, nimuyembekeze konse konse chisomo chiri kutengedwa kudza nacho kwa inu m’bvumbulutso la Yesu Khristu; 14 Monga ana womvera wosadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala wosadziwa inu: 15 Komatu monga Iye wakuyitana inu ali woyera mtima, khalani inunso woyera mtima m’makhalidwe anu onse: 16 Popeza kwalembedwa, mudzikhala woyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima: 17 Ndipo mukamuyitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho pakati pa anthu, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu: 18 Podziwa kuti simudawomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe wochokera kwa makolo anu; 19 Koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu: 20 Amene adazindikirikatu asadakhazikike maziko a dziko lapansi, koma adawonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi. 21 Chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiliro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu. 22 Powona mwayeretsa moyo wanu pomvera chowonadi mwa Mzimu mu chikondi choyera cha pa abale, mukondane kwenikweni wina ndi mzake ndi mtima wa ngwiro: 23 Wokhala wobadwanso, osati ndi mbewu yofeka, komatu yosawola, mwa mawu a Mulungu a moyo ndi wokhalitsa. 24 Popeza, anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wawo wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa: 25 Koma Mawu wa Ambuye akhala chikhalire. Ndiwo mawu a Uthenga Wabwino wolalikidwa kwa inu.

1 Petro 2

1 Momwemo pakutaya choyipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi mawonekedwe wonyenga, ndi kaduka ndi mayankhulidwe aliwonse woyipa., 2 Monga makanda obadwa lero khumbani mkaka wa mawu kuti mukakule nawo: 3 Monga mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima. 4 Amene pakudza kwa Iye, monga mwala wa moyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu. 5 Inunso ngati miyala ya moyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe woyera mtima, akupereka nsembe za uzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. 6 Chifukwa chake kwalembedwa m’lembo, tawonani, ndiyika m’ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa. 7 Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo wosamvera mwala umene womangawo adaukana, womwewo udayesedwa mutu wa pa ngodya, 8 Ndipo mwala wakukhumudwa nawo, ndi thanthwe lopunthwitsa; kwa iwo akukhumudwa ndi mawu, pokhala wosamvera, kumenekonso adayikidwako. 9 Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu amwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene adakuyitanani mutuLuka mumdima, mulowe kuwunika kwake kodabwitsa; 10 Inu amene mu nthawi yakale simudali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simudalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo. 11 Wokondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi wogonera, mudzikanize ku zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo; 12 Ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale wokoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati wochita zoyipa, akalemekeze Mulungu pakuwona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira. 13 Tadzigonjani kwa zoyikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye: ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; 14 Kapena kwa akazembe, monga wotumidwa ndi iye kukalanga wochita zoyipa, koma kuyamikira wochita zabwino. 15 Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti, ndikuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu wopusa: 16 Monga mfulu, koma wosakhala nawo ufulu monga chobisira choyipa, koma ngati atumiki a Mulungu. 17 Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Wopani Mulungu. Chitirani mfumu ulemu. 18 Akapolo inu, gonjerani ambuye anu ndi kuwopa konse, osati abwino ndi aulere wokha, komanso aukali. 19 Pakuti ichi ndi choyamikirika ngati munthu, chifukwa cha chikumbu mtima pa Mulungu apirira mu zophweteka pakumva zowawa wosaziyenera. 20 Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapilira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapilira, ichi ndi chobvomerezeka pa maso paMulungu. 21 Pakuti mwa ichi mudayitanidwa: pakutinso Khristu adamva zowawa m’malo mwathu, natisiyirani chitsanzo kuti tikalondore mapazi ake. 22 Ngakhale sadachita tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichidapezedwa chinyengo: 23 Amene pochitidwa chipongwe, sadabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sadawopsa, koma adapereka mlandu kwa Iye woweruza molungama: 24 Amene adasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake pamtengo, kuti ife, akufa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo: ameneyo mikwingwirima yake mudachiritsidwa nayo. 25 Pakuti mudali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwatembenukira kwa M’busa ndi Woyang’anira wa moyo wanu.

1 Petro 3

1 Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti ngatinso ena samvera mawu, akakodwe wopanda mawu mwa mayendedwe a akazi; 2 Pakuwona mayendedwe anu woyera ndi kuwopa kwanu: 3 Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kwa kubvala chobvala; 4 Koma kukhale munthu wobisika wa mtima, m’chobvala chosawola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu. 5 Pakuti koteronso kale akazi woyera mtima, amene adakhulupirira mwa Mulungu, adadzikometsera wokha, pokhala womvera amuna awo a iwo wokha: 6 Monganso Sara adamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake a akazi ngati muchita bwino osawopa chowopsa chiri chonse. 7 Momwemonso amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chofowoka, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe. 8 Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, wochitirana chifundo wina ndi mzake, wokondana ndi abale, achisoni, wodzichepetsa: 9 Osabwezera choyipa ndi choyipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzachita ichi mwayitanidwa, kuti mulandire dalitso. 10 Pakuti iye wofuna kukonda moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choyipa, ndi milomo yake isayankhule chinyengo: 11 Ndipo apatuke pa choyipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuwulondola. 12 Pakuti maso, a Ambuye ali pa wolungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye itsutsana ndi iye wochita zoyipa. 13 Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choyipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino? 14 Komatu ngatinso mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, wodala inu; ndipo musawope pakuwopsa kwawo, kapena musadere nkhawa; 15 Koma mumpatulikitse kwa Ambuye Mulungu mitima yanu; wokonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha. 16 Ndikukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani inu zoyipa monga wochita zoyipa kuti akachite manyazi ndi mayendedwe anu abwino mwa Khristu. 17 Pakuti, kumva zowawa kwanu chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoyipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa chakuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu. 18 Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, wolungama m’malo mwa wosalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mu mzimu: 19 M’menemonso adapita, nalalikira mizimu idali m’ndende; 20 Imene m’nthawi yakale idakhala yosamvera, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kudalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka kwa chombo, m’menemo wowerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, adapulumutsidwa mwa madzi: 21 Chimenenso chiri chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, (kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu,) mwa kuuka kwa Yesu Khristu: 22 Amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu; atalowa m’Mwamba; pali angelo, ndi ma ulamuliro, ndi zimphamvu, zopangidwa zikhale zomgonjera Iye.

1 Petro 4

1 Popeza Khristu adamva zowawa m’thupi chifukwa cha ife, mudzikonzere inunso mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m’thupi walekana nalo tchimo; 2 Kuti nthawi yotsalira asakhalenso Iye ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma kuchifuniro cha Mulungu. 3 Pakuti m’nthawi yakale idatifikira ife kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, mzilakolako, kuledzera, madyerero, mamwayimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka: 4 M’menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, akuyankhula zoyipa pa inu: 5 Amenewo adzadziwerengera wokha kwa Iye amene ndi wokonzeka kuweruza a moyo ndi akufa. 6 Chifukwa cha ichi ndi chifukwa chake udalalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m’thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu. 7 Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chiri pafupi: chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero: 8 Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chidzakwiriritsa unyinji wa machimo. 9 Mucherezane wina ndi mzake, opanda udani. 10 Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo wina ndi mzake, ngati adindo wokoma a chisomo cha mitundu mitundu cha Mulungu. 11 Akayankhula wina, ayankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nawo ulemerero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Ameni. 12 Wokondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu cha chilendo chakuchitikirani inu: 13 Koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wake mukasangalale ndikukondwera kwakukulukulu. 14 Ngati munyozedwa pa dzina la Khristu, wodala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi wa Mulungu apuma pa inu: kumbali yawo amuyankhulira Iye zoyipa, koma kumbali yanu Iye alemekezedwa. 15 Koma asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena ngati mbala, kapena ngati wochita zoyipa, kapena ngati wodudukira nkhani za anthu ena. 16 Koma ngati munthu wina akumva zowawa chifukwa choti ndi Mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili. 17 Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba pa ife, chitsiriziro cha iwo wosamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chotani? 18 Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndikuyesetsa kokha kokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzawoneka kuti? 19 Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu ayike moyo wawo kwa Iye ndi kuchita zokoma monga kwa Wolenga wokhulupirika.

1 Petro 5

1 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nawo ulemerero umene udzabvumbulutsidwawo: 2 Dyetsani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza; koma mwa ufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu. 3 Osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma wokhala zitsanzo za gululo. 4 Ndipo pakuwonekera M’busa wamkulu, mudzalandira Korona wa ulemerero, wosafota. 5 Momwemonso anyamata inu, mverani akulu.Koma nonsenu mubvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza wodzikudza, koma apatsa chisomo kwa wodzichepetsa. 6 Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni: 7 Ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu. 8 Khalani wodzisunga, dikirani chifukwa mdani wanu mdierekezi, monga ngati mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina kuti akam’meze: 9 Ameneyo mumkanize pokhazikika m’chikhulupiliro, podziwa kuti zowawa zomwezo ziri mkukwaniritsidwa pa abale anu ali m’dziko lapansi. 10 Ndipo Mulungu wa chisomo chonse amene adakuyitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu Yesu, mutamva zowawa kanthawi, adzapanga inu angwiro,adzakhazikitsa,adzalimbikitsa,adza chirikiza inu. 11 Kwa Iye kukhale ulemerero ndi ulamuliro ku nthawi za nthawi. Ameni. 12 Mwa Silvano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwa chidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo chowona cha Mulungu ndi ichi mwa chimenechi muyimemo. 13 Mpingo wa ku Babulo wosankhidwa pamodzi nanu ukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga. 14 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsopsono cha chikondi: mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu Yesu. Ameni.

2 Petro 1

1 Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m’chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu: 2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m’chidziwitso cha Mulungu, ndi cha Yesu Ambuye wathu. 3 Popeza mphamvu ya Umulungu wake idatipatsa ife zinthu zonse za moyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiyitana ife ku ulemerero ndi ukoma. 4 Mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi ukulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale wogawana nawo Umulungu wake, mudapulumuka ku chibvundi chiri pa dziko lapansi m’chilakolako. 5 Ndipo mwa ichi, pakutengeraponso changu chonse, muwonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi pa ukoma chizindikiritso. 6 Ndi pa Chizindikiritso chodziletsa; ndi chodziletsa chipiliro; ndi pachipiliro chipembedzo; 7 Ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; chikondi, cha pa abale chikondi. 8 Pakuti ngati zinthu izi zikhala mwa inu, ndipo zikachuluka, zidzapanga kuti musakhale wosabala inu zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Khristu. 9 Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, ndipo sangathe kuwona patali ndipo wayiwala matsukidwe ake potaya zoyipa zake zakale. 10 Momwemo abale wonjezani kuchita changu kukhazikitsa mayitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita zinthu izi simudzagwa nthawi zonse: 11 Chotero polowerera padzakhala matumikiridwe akwa inu, khomo lolowera ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu. 12 Mwa ichi, sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za zinthu izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m’chowonadi chiri ndi inu. 13 Inde, ndichiyesa chokoma, pokhala ine mu msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani; 14 Podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu adandiwonetsa ine. 15 Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira zinthu izi. 16 Pakuti sitidatsata miyambi yachabe, pamene tidakudziwitsani mphamvu ndi mabweredwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tidali mboni zopenya ndi maso ukulu wake. 17 Pakuti adalandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mawu wotere wochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene mwa Iye ndikondwera naye. 18 Ndipo mawu awa wochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija. 19 Ndipo tiri nawo mawu a chinenero wokhazikika koposa: amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikawuka nyenyezi yanthanda pa mtima wanu: 20 Ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha. 21 Pakuti kale lonse chinenero sichidadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu woyera a Mulungu adayakhulidwa pamene adagwidwa ndi Mzimu Woyera.

2 Petro 2

1 Koma pakadakhalanso pakati pa anthuwo aneneri wonama, monganso padzakhala aphunzitsi wonama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m’seri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo wokha chitayiko chakudza msanga. 2 Ndipo ambiri adzatsata njira yawo ya zonyansa; chifukwa cha iwo njira ya chowonadi idzanenedwa za mwano. 3 Ndipo m’chisiliro adzakuyesani malonda ndi mawu wonyenga; amene chiweruzo chawo sichidachedwa ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chawo sichiwodzera. 4 Pakuti ngati Mulungu sadalekerera angelo adachimwawo, koma adawaponya kundende nawayika ku mayenje amdima, asungike kufikira chiweruziro; 5 Ndipo sadalekerera dziko lapansi lakale, koma adasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi amzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko lapansi lawosapembedza chigumula; 6 Ndipo pakuyisandutsa makala mizinda ya Sodoma ndi Gomora adayitsutsa poyigwetsa, atayiyika chitsanzo cha iwo akukhala wosapembedza; 7 Ndipo adapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe wonyansa a woyipa aja. 8 (Pakuti wolungamayo pokhala pakati pawo ndi kuwona ndi kumva zawo, adadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika) 9 Ambuye adziwa kupulumutsa wopembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga wosalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe: 10 Koma makamaka iwo akutsata zathupi, m’chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osawopa kanthu, wotsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemu wawo. 11 Popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano. 12 Koma iwo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuwonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu wosazidziwa, adzawonongeka m’kuwononga kwawo; 13 Ndipo adzalandira mphoto ya chosalungama; amene akondwera mkudyerera zowononga ndiwo amawanga ndi zilema, akudyerera m’madyerero anu achinyengo pamene akudyerera nanu; 14 Wokhala nawo maso wodzala ndi chigololo, wosakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; wokhala nawo mtima wozolowera kusilira; ana a temberero. 15 Posiya njira yolunjika adasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene adakonda malipiro a chosalungama; 16 Koma adadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mawu, woyankhula ndi mawu a munthu, adaletsa misala ya m’neneriyo. 17 Iwo ndiwo akasupe wopanda madzi, mitambo yotengedwa, ndi mphepo yamkuntho amene mdima wakuda bii uwasungikira kosatha. 18 Pakuti poyankhula mawu wotukumuka wopanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe wolakwawo. 19 Ndikuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo eni wokha ali atumiki achibvundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake. 20 Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akodwanso nazo m`menemo, nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzayipa koposa zoyambazo. 21 Pakuti pakadakhala chinthu chabwino kwa iwo akadapanda kudziwa njira ya chilungamo, ndi poyizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo. 22 Chidawayenera iwo cha mwambi wowona, Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulika m’thope.

2 Petro 3

1 Wokondedwa, uyu ndiye kalata wachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu wowona ndi kukukumbutsani: 2 Kuti mukumbukire mawu wonenedwa kale ndi aneneri woyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa ife atumwi anu: 3 Ndi kuyamba ku chizindikira ichi kuti masiku wotsiriza adzafika wonyoza ndi kuchita zonyoza, woyenda monga mwa zilakolako za iwo eni. 4 Ndi kunena,liri kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe. 5 Pakuti ichi ayiwala dala, kuti miyamba idakhala kale lomwe, ndi dziko lidawungika ndi madzi ndi mwa madzi, mawu a Mulungu: 6 Mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka: 7 Koma miyamba ndi dziko lapansi la masiku ano, ndi mawu womwewo zayikika, zosungikira kumoto kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu wosapembedza. 8 Koma ichi chimodzi musayiwale, wokondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi. 9 Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. 10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala usiku; m’mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi za m’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko lapansi ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa. 11 Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu wotani nanga, m’mayendedwe wopatulika ndi m’chipembedzo. 12 Akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m’menemo miyamba potentha moto idzakanganuka ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu. 13 Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo. 14 Momwemo, wokondedwa, popeza muyembekezera izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, wopanda banga ndi wopanda chilema. 15 Ndipo dziwerengereni kuti kupirira kwa Ambuye wathu ndicho chipulumutso; monganso m’bale wathu wokondedwa Paulo kolingana ndi nzeru zopatsidwa kwa iye wakulemberani; 16 Monganso mu akalata ake onse pokamba momwemo za zinthu izi, m’menemo muli zinthu zina zobvuta kuzizindikira, zimene anthu wosaphunzira ndi wosakhazikika apotoza, monganso atero nawo malembo ena, ndi kudziwononga nawo eni okha. 17 Inu, tsono, wokondedwa, pozizindikira zinthu izi, chenjerani kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo wosayeruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu. 18 Koma kulani mu chisomo ndi m`chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Ameni.

1 Yohane 1

1 Chimene chidaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiwona m’maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mawu a moyo. 2 (Ndipo moyowo udawonekera, ndipo tidawona ndipo tichita umboni, ndipo tikukuwonetsani moyo wosathawo, umene udali kwa Atate nuwonekera kwa ife) 3 Chimene tidachiwona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife: ndipo ndithu chiyanjano chathu chirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu. 4 Ndipo zinthu izi tilemba ife, kwa inu kuti chimwemwe chanu chikwaniritsidwe. 5 Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye monse mulibe mdima. 6 Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita chowonadi: 7 Koma ngati tiyenda m’kuwunika, monga Iye ali m’kuwunika, tiyanjana wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Khristu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse. 8 Tikati kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe chowonadi. 9 Ngati tibvomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chiri chonse. 10 Ngati tinena kuti sitidachimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mawu ake sakhala mwa ife.

1 Yohane 2

1 Tiana tanga, zinthu izi ndalembera inu, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama: 2 Ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu: koma osati athu wokha, komanso machimo adziko lonse lapansi. 3 Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. 4 Iye wonena kuti, Ndimdziwa Iye, koma sasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe chowonadi. 5 Koma iye amene asunga mawu ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chikhala changwiro. M’menemo tizindikira kuti tiri mwa Iye. 6 Iye wonena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga adayenda Iyeyo. 7 Wokondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene mudali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo lakalelo ndilo mawu amene mudawamva kuyambira pachiyambi. 8 Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chiri chowona mwa Iye ndi mwa inu: kuti mdima wapita, ndi kuwunika kowona kwayamba kuwala. 9 Iye amene anena kuti ali m’kuwunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino. 10 Iye amene akonda mbale wake akhala m’kuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake. 12 Ndikulemberani, tiana, popeza machimo anu adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake. 13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pa chiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woyipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate. 14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi Mawu a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woyipayo. 15 Musakonde dziko lapansi, kapena zinthu za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. 16 Pakuti chiri chonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17 Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake: koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse. 18 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi: ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo wokana Khristu ambiri.M’menemo muzindikira kuti ndi nthawi yotsiriza iyi. 19 Adatuluka mwa ife, komatu sadali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma adatuluka kuti awonekere kuti sadali onse a ife. 20 Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse. 21 Sindidakulemberani chifukwa simudziwa chowonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera ku chowonadi. 22 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu sali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana. 23 Yense wokana Mwana, alibe Atate: (koma) iye wobvomereza Mwana ali ndi Atatenso. 24 Koma inu, chimene mudachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala chimene mudachimva kuyambira pa chiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana ndi mwa Atate. 25 Ndipo ili ndi lonjezano Iye adatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha. 26 Zinthu izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu. 27 Ndipo inu kudzoza kumene mudalandira kuchokera kwa Iye, kukhala kwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli kowona, sikuli bodza ayi, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye. 28 Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akadzawonekera Iye tidzakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake. 29 Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti ali yensenso wochita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.

1 Yohane 3

1 Tawonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife wotere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silidamzindikire Iye. 2 Wokondedwa, tsopano tiri ana a Mulungu, ndipo sichidawoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuwoneka Iye, tidzakhala wofanana ndi Iye, pakuti tidzamuwona Iye monga ali. 3 Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera. 4 Yense wakuchita tchimo achimwira lamulo: ndipo tchimo ndilo kuswa lamulo. 5 Ndipo mudziwa kuti Iyeyu adawonekera kudzachotsa machimo athu; ndipo mwa Iye mulibe tchimo. 6 Yense wokhala mwa Iye sachimwa: yense wakuchimwa sadamuwona Iye, ndipo sadamdziwa Iye. 7 Tiana, munthu asakusokeretseni inu: iye wochita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama. 8 Iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi adachimwa kuyambira pachiyambi. Chifukwa cha ichi Mwana wa Mulungu adawonekera, ndiko kuti akawononge ntchito za mdierekezi. 9 Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbewu yake ikhala mwa iye: ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu. 10 M’menemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo sali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. 11 Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake. 12 Osati monga Kayini adali wochokera mwa woyipayo, namupha mbale wake. Ndipo adamupha iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zidali zoyipa, ndi za mbale wake zolungama. 13 Musazizwe, abale, likadana nanu dziko lapansi. 14 Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka mu imfa kulowa m’moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda m’bale wake akhala mu imfa. 15 Yense wodana ndi mbale wake ali wakupha munthu: ndipo mudziwa kuti wakupha munthu ali yense alibe moyo wosatha wakukhala mwa lye. 16 Umo tizindikira chikondi cha Mulungu, popeza Iyeyu adapereka moyo wake chifukwa chaife: ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale. 17 Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, nawona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pom’mana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? 18 Tiana, tanga, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’chowonadi. 19 Umo tidzazindikira kuti tiri wochokera m’chowonadi, ndipo tidzakhazikitsa mitima yathu pamaso pake. 20 M’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zinthu zonse. 21 Wokondedwa mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu. 22 Ndipo chimene chiri chonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zinthu zomkondweretsa pamaso pake. 23 Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mzake, monga Iye adatipatsa lamulo. 24 Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m’menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene adatipatsa ife.

1 Yohane 4

1 Wokondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri wonyenga ambiri adatuluka kulowa m’dziko lapansi. 2 M’menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uli wonse umene ubvomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi, uchokera mwa Mulungu; 3 Ndipo mzimu uliwonse umene subvomereza kutiYesu Khristu adadza mthupi, suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m’dziko lapansi tsopano lomwe. 4 Inu ndinu wochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo mudayilaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu ali wamkulu kuposa iye wakukhala m’dziko lapansi 5 Iwo ndiwo wochokera m’dziko lapansi: mwa ichi ayankhula monga wochokera m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera. 6 Ife ndife wochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa chowonadi, ndi mzimu wachisokeretso. 7 Wokondedwa tikondane wina ndi mzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, nazindikira Mulungu. 8 Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi: 9 Umo chidawoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu adatuma Mwana wake wobadwa yekha alowe m’dziko lapansi kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. 10 Umo muli chikondi, sikuti ife tidakonda Mulungu, koma kuti Iye adatikonda ife, ndipo adatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu. 11 Wokondedwa, ngati Mulungu adatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mzake. 12 Palibe munthu adamuwona Mulungu nthawi ili yonse. Ngati tikondana wina ndi mzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife. 13 M’menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye ndi Iye mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake. 14 Ndipo ife tawona, ndipo tichita umboni kuti Atate adatuma Mwana kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15 Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu. 16 Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndi Mulungu akhala mwa iye. 17 M’menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m’tsiku la chiweruziro: chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tiri ife m’dziko lino lapansi. 18 Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango. Ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m’chikondi. 19 Tikonda Iye, chifukwa adayamba Iye kutikonda. 20 Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye m’bale wake, ali wabodza; pakuti iye wosakonda m’bale wake amene wamuwona, akonda Mulungu bwanji amene sadamuwona? 21 Ndipo lamulo iri tiri nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso m’bale wake.

1 Yohane 5

1 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu: ndipo yense wakukonda Iye amene adabala akondanso iye amene adabadwa wochokera mwa Iye. 2 Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kusunga malamulo ake. 3 Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sakhala wolemetsa. 4 Pakuti chirichonse chimene chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi: ndipo ichi ndi chigonjetso tigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. 5 Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi; koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. 6 Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi wokha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye chowonadi. 7 Pakuti pali atatu akuchita umboni, M’mwamba, Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera: ndipo iwo atatu ali m’modzi. 8 Ndipo pali atatu, akuchita umboni m’dziko lapansi, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi: ndipo awa atatu agwirizana mu m’modzi. 9 Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti adachita umboni za Mwana wake. 10 Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboni mwa iye yekha: iye wosakhulupirira Mulungu adamuyesa Iye wonama; chifukwa sadakhulupirira umboni wa Mulungu adauchita wa Mwana wake. 11 Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu adatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. 12 Iye wakukhala ndi Mwana ali nawo moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo. 13 Zinthu izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.Kuti mukhulupirire padzina la mwana wa Mulungu. 14 Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake atimvera ife: 15 Ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chiri chonse tichipempha, tidziwa kuti tiri nazo zinthu izi tazikhumba kwa Iye. 16 Ngati wina akawona m’bale wake alikuchimwa tchimo losati la ku imfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo wosati a ku imfa. Pali tchimo la ku imfa: za ilo sindinena kuti mupemphere. 17 Chosalungama chiri chonse chiri uchimo: ndipo pali tchimo losati la ku imfa. 18 Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woyipayo samkhudza. 19 Ndipo tidziwa kuti tiri ife wochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woyipayo. 20 Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Wowonayo, ndipo tiri mwa Wowonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Uyu ndiye Mulungu wowona ndi moyo wosatha. 21 Ana, dzisungeni eni nokha kupewa mafano. Ameni.

2 Yohane 1

1 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikonda m’chowonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira chowonadi; 2 Chifukwa cha chowonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife kunthawi yosatha. 3 Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m’chowonadi ndi m’chikondi. 4 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena wa ana anu alikuyenda m’chowonadi, monga ndidalandira lamulo lochokera kwa Atate. 5 Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tidali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake. 6 Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulo monga mudalimva kuyambira pachiyambi kuti mukayende momwemo. 7 Pakuti wonyenga ambiri adatuluka, kulowa m’dziko lapansi, ndiwo amene sabvomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu. 8 Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira. 9 Aliyense wochimwa ndi, wosakhala m’chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m’chiphunzitso, iyeyo ali nawo Atate ndi Mwana. 10 Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamulandire iye kunyumba kwanu, ndipo musamuyankhule. 11 Pakuti iye wakumuyankhula ayanjana nazo ntchito zake zoyipa. 12 Pokhala ndiri nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kuyankhula nanu maso ndi maso, kuti chimwemwe chanu chikwaniritsidwe. 13 Ana a mlongo wanu wosankhika, akupereka moni. Ameni.

3 Yohane 1

1 Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m’chowonadi. 2 Wokondedwa, ndikhumba kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino monga mzimu wako ulemera. 3 Pakuti ndidakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za chowonadi chako, monga umayenda m’chowonadi. 4 Ndiribe chimwemwe choposa ichi chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’chowonadi. 5 Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chiri chonse, uwachitira abale ndi alendo womwe; 6 Amene adachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wawo koyenera Mulungu, udzachita bwino; 7 Pakuti chifukwa cha dzinali adatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu. 8 Chifukwa chake ife tiyenera kulandira wotere, kuti tikakhale wothandizana nacho chowonadi. 9 Ndalemba kwa Mpingo; komatu Diyotrofe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, sanatilandira ife. 10 Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mawu woyipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo wofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo. 11 Wokondedwa, usatsatire chimene chiri choyipa komatu chimene chiri chabwino. 12 Demetriyo ali ndi mbiri yabwino kwa anthu onse, ndichowonadi chomwe; inde, ndipo ife tichita umboni; ndipo mudziwa kuti umboni wathu uli wowona. 13 Ndinali nazo zambiri za kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndicholembera cha kapezi. 14 Koma ndiyembekezera kukuwona iwe msanga, ndipo tidzayankhulana maso ndi maso. Mtendere ukhale ndi iwe, akukupatsa moni abwenzi athu. Undiperekere moni mowatchula mayina awo.

Yuda 1

1 Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo woyitanidwa ndi opatulidwa mwa Mulungu Atate, ndi wosungidwa mwa Yesu Khristu. 2 Chifundo chikhale kwa inu ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni. 3 Wokondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbane motsimikiza chifukwa kuti chikhulupiliro chapatsidwa kamodzi kwa woyera mtima. 4 Pakuti pali anthu ena adakwawira m’seri, ndiwo amene aja adalembedwa mayina awo kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, namkaniza Ambuye Mulungu yekha ndi Ambuye wathu Yesu Khristu. 5 Koma ndifuna kukukumbutsani kuti ngakhale mudadziwa zonse kale, kuti Ambuye atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m’dziko la a Aigupto, adawononganso iwo wosakhulupilira. 6 Angelonso amene sadasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu adasiya pokhala pawo pawo, adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu. 7 Monga Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuyizungulira, yotsatana nayoyo, idadzipereka kuchiwerewere, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iyikidwa chitsanzo, yobwezeredwa chilango cha moto wosatha. 8 Momwemonso iwo m’kulota kwawo adetsa matupi awo, napeputsa ufumu nachitira mwano maukulu awulemerero. 9 Koma Mikayeli mkulu wa angelo pakuchita makani ndi mdierekezi adatsutsana za thupi la Mose, sadalimbika mtima kutchulira chifukwa chomchitira mwano, koma adati, Ambuye akudzudzule. 10 Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika nazo eni. 11 Tsoka kwa iwo! Pakuti adayenda m’njira ya Kayini, ndipo adadziwononga m’chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m’chitsutsano cha Kore. 12 Iwo ndiwo wokhala mawanga pa maphwando anu achikondano, pakudya nanu pamodzi, akudzidyetsa wokha mopanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu; 13 Mafunde woopsa a nyanja, akuwinduka thobvu la manyazi a iwo wokha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha. 14 Ndipo kwa iwo, Enoke, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, adanenera za izi kuti, Tawona, akudza Ambuye ndi woyera ake zikwi makumi, 15 Kudzachitira onse chiweruziro ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zawo zonse zosapembedza, zimene adazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene wochimwa osapembedza adayankhula pa Iye. 16 Amenewo ndiwo wodandaula, wodelera, akuyenda monga mwa zilakolako zawo; ndipo pakamwa pawo ayankhula zazikuluzikulu, akutama anthu chifukwa cha kupindula nako. 17 Koma, wokondedwa, mukumbukire mawu wonenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu. 18 Kuti adanena nanu, panthawi yotsiriza padzakhala wotonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo wokha. 19 Iwo ndiwo wopatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, wosakhala naye Mzimu. 20 Koma inu, wokondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiliro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mwa Mzimu Woyera, 21 Mudzisunge nokha, m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha. 22 Ndipo kwa ena khalani ndi chifundo musiyanitse; 23 Koma ena muwapulumutse ndi mantha kuwakwatula ku moto podana nawonso, malaya wochitidwa mawanga ndi thupi. 24 Tsopano kwa Iye amene akhoza kukusungani kuti mungagwe, ndi kukuyimikani pamaso pa ulemerero wake wopanda chilema ndi chimwemwe chopitirira, 25 Kwa Mulungu wanzeru yekha Mpulumutsi wathu, kukhale ulemerero,ndi ukulu ndi ulamuliro ndi mphamvu, tsopano ndi kufikira nthawi zonse. Ameni.

Chivumbulutso 1

1 “Chibvumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu adabvumbulutsira achiwonetsere atumiki ake, ndicho cha zinthu izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa m’ngelo wake adazindikiritsa izi kwa mtumiki wake Yohane: 2 Amene adachita umboni za mawu a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, ndi zinthu zonse zimene adaziwona. 3 Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mawu a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo: pakuti nthawi yayandikira. 4 Yohane kwa mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Iye amene ali, ndi adali, ndi amene alimkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala ku mpando wachifumu wake. 5 Ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu adziko lapansi. Kwa Iye amene adatikonda ife, natimasula ku machimo athu ndi mwazi wake. 6 Ndipo adatiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemererro ndi ulamuriro kufikira nthawi za nthawi. Ameni. 7 Tawonani adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya Iye, iwonso amene adampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Ameni. 8 Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, atero Ambuye amene ali, amene adali, ndi amene alimkudza, wamphamvu yonse. 9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m’chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu Khristu ndidakhala pa chisumbu chotchedwa Patimo, chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu. 10 Ndidagwidwa ndi Mzimu pa tsiku la Ambuye, ndipo ndidamva kumbuyo kwanga mawu akulu, ngati a lipenga, 11 Ndikunena kuti, Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza: ndipo chimene upenya, lemba m’buku, nulitumize kwa mipingo isanu ndi iwiri, imene iri mu Asiya, Aefeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya. 12 Ndipo ndidacheuka kuwona wonena mawu amene adayankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndidawona zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi; 13 Ndipo pakati pa zoyikapo nyali zisanu ndi ziwirizo wina wonga Mwana wa munthu atabvala chobvala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolidi pachifuwa. 14 Ndipo tsitsi lapa mutu pake lidali loyera ngati ubweya woyera, kuyera ngati chipale chofewa; ndipo maso ake ngati lawi la moto; 15 Ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m’ng’anjo; ndi mawu ake ngati mkokomo wa madzi ambiri. 16 Ndipo m’dzanja lake lamanja mudali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi mkamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konse konse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake. 17 Ndipo pamene ndidamuwona Iye, ndidagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo adayika dzanja lake la manja pa ine, nati, Usawope, Ine ndine woyamba ndi wotsiriza. 18 Ndine wamoyoyo; ndipo ndidali wakufa, ndipo tawona ndiri wamoyo ku nthawi zonse. Ameni; ndipo ndiri nawo mafungulo a gahena ndi imfa. 19 Lemba zinthu zimene udaziwona, ndi zinthu zimene ziripo, ndi zinthu zimene zidzawoneka mtsogolomo; 20 Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri udaziwona pa dzanja langa la manja, ndi zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri za golidi. Nyenyezi zisanu ndi ziwirizo ndiwo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndiyo Mipingo isanu ndi iwiri.

Chivumbulutso 2

1 Kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Aefeso lemba; zinthu izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m’dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi; 2 Ndidziwa ntchito zako ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sukhoza kulola woyipa, ndipo udayesa iwo amene adzitcha wokha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza iwo abodza. 3 Ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema. 4 Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, chifukwa kuti udataya chikondi chako choyamba. 5 Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, msanga ndipo ndidzatulutsa choyikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa. 6 Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolayi, zimene Inenso ndidana nazo. 7 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli pakati pa Paradiso wa Mulungu. 8 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Smurna lemba; zinthu izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene adali wakufa, koma ali ndi moyo; 9 Ndidziwa ntchito zako, ndi chisautso chako, ndi umphawi wako, (komatu uli wachuma), ndipo ndidziwa za mwano wa iwo akunena za iwo wokha kuti ali Ayuda, koma sali Ayuda, komatu sunagoge wa Satana. 10 Usawope zimene uti udzamve kuwawa; tawona, mdierekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe Korona wa moyo. 11 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzachitidwa choyipa ndi imfa yachiwiri. 12 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba; zinthu izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konse konse; 13 Ndidziwa ntchito zako, ndi kumene ukhalako kuja kuli mpando wa chifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, wosakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m’masiku wa Antipasi mboni yanga, wophedwa, wokhulupirika wanga, amene adaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana. 14 Komatu ndiri nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nawo komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene adaphunzitsa Balaki kuyika chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, ndikuti achite chiwerewere. 15 Kotero uli nawo akugwira chiphunzitso cha Anikolayi momwemonso. Chinthu chimene ndidana nacho. 16 Lapa; ndipo ngati sutero ndidzadza kwa iwe msanga, ndipo ndidzachita nawo nkhondo ndi lupanga la mkamwa mwanga. 17 Iye wakukhala nalo khutu amve chimeme Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa adye mana wobisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira. 18 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Tiyatira lemba; zinthu izi anena Mwana wa Mulungu, wakukhala nawo maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira; 19 Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi utumiki ndi chikhulupiriro, ndi chipiriro chako,ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo. 20 Koma ndiri nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebeli, wodzitcha yekha m’neneri; ndipo aphunzitsa, nasokeretsa atumiki anga, kuti achite chiwerewere ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano. 21 Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chiwerewere chake. 22 Tawona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m’chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zawo. 23 Ndipo ndidzapha ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu. 24 Koma ndinena kwa iwe, kwa wotsala a ku Tiyatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sadazindikira zakuya za Satana, monga anena, sindidzakusanjikizani katundu wina. 25 Koma chimene uli nacho, gwiritsa kufikira ndidza. 26 Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzampatsa ulamuliro wa pa a mitundu. 27 Ndipo adzawalamulira iwo ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga. 28 Ndipo ndidzampatsa iye nyenyezi ya nthanda, yam’bandakucha. 29 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Chivumbulutso 3

1 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa Sarde lemba; zinthu izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu; ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo ndiwe wakufa. 2 Khala wodikira, ndipo limbikitsa zinthu zotsalira, zimene zidafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zangwiro pamaso pa Mulungu. 3 Chifukwa chake kumbukira momwe udalandirira ndikumvera; nusunge nulape: chifukwa chake ukapanda kudikira, ndidzafika kwa iwe ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe. 4 Komatu uli nawo mayina wowerengeka mu Sardisi; amene sanadetsa zobvala zawo; ndipo adzayenda ndi Ine m’zoyera; chifukwa ali woyenera. 5 Iye amene alakika adzabvekedwa zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m’buku lamoyo, koma ndidzabvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake. 6 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa mipingo. 7 Ndipo kwa m’ngelo wa mpingo wa ku Filadelfeya lemba; zinthu izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula; 8 Ndidziwa ntchito zako; tawona ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo; kuti uli nayo mphamvu pang’ono, ndipo udasunga mawu anga, osakana dzina langa. 9 Tawona, ndikupatsa ena wotuluka m’sunagoge wa Satana, akudzinenera wokha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; tawona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda. 10 Popeza udasunga mawu a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko lapansi. 11 Tawona, ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande Korona wako. 12 Iye wakulakika, ndidzamuyesa iye mzati wa mkachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m’Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndipo ndidzalemba pa iye dzina langa latsopano. 13 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa mipingo. 14 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Leodikaya lemba; zinthu izi anena Ameni, mboni yokhulupirika ndi yowona, woyamba wa chilengo cha Mulungu; 15 Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizila kapena wotentha; mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha. 16 Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula mkamwa mwanga. 17 Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndiri nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu ndi wausiwa: 18 Ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyenga m’moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukabvekedwe, ndi kuti manyazi a umaliseke wako usawonekere; ndi mankhwala wopaka m’maso mwako, kuti ukawone. 19 Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nulape. 20 Tawona, ndayima pakhomo, ndigogoda: ngati wina akumva mawu anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine. 21 Iye wakulakika, ndidzampatsa akhale pansi pamodzi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndidalakika, ndipo ndidakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake. 22 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Chivumbulutso 4

1 Zitatha izi ndidapenya, ndipo tawonani, khomo lidatseguka m’Mwamba: ndipo mawu woyamba ndidawamva, ngati lipenga lakuyankhula ndi ine; amene adati, kwera kuno, ndipo ndidzakuwonetsa zinthu zimene ziyenera kuchitika mtsogolomo. 2 Ndipo nthawi yomweyo ndidali mu Mzimu: ndipo, tawonani padayikika mpando wachifumu m’Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina. 3 Ndipo mawonekedwe a Iye wokhalapo adafanana ndi mwala wa Jaspa, ndi Sardiyo: ndipo padali utawaleza wozinga mpando wachifumu, mawonekedwe ake ngati emaralido. 4 Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inayi: ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anayi atabvala zobvala zoyera ndipo pa mutu pawo padali a Korona agolidi. 5 Ndipo kuchokera kumpando wachifumuwo, mudatuluka mphezi ndi mawu ndi mabingu: Ndipo padali nyali zisanu ndi ziwiri zoyaka moto ku mpando wachifumu, ndiyo Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu. 6 Ndipo kumpando wachifumuwo, kudali nyanja yamandala yonga kusitalo; ndipo pakati pa mpando wachifumuwo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinayi zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo. 7 Ndipo chamoyo choyamba chidafanana nawo mkango, ndi chamoyo chachiwiri chidafanana ndi mwana wang’ombe, chamoyo chachitatu chidali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinayi chidafanana ndi chiwombankhanga chakuwuluka. 8 Ndipo zamoyo zinayi, chonse pa chokha chidali nawo mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m’katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, Woyera, Woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, amene adali, amene ali ndi amene alimkudza. 9 Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pampando wa chifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi. 10 Akulu makumi awiri mphambu anayi amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, naponya pansi a Korona awo kumpando wachifumu, nanena, 11 Muyenera inu, Ambuye wathu kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu: chifukwa inu mudalenga zinthu zonse ndipo mwachifuniro chanu zidakhala ndipo zidalengedwa.

Chivumbulutso 5

1 Ndipo ndidawona m’dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wa chifumu buku lolembedwa mkati ndi kunja kwake, losindikizidwa ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri. 2 Ndipo ndidawona m’ngelo wamphamvu wakulalikira ndi mawu akulu, ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake? 3 Ndipo padalibe munthu m’modzi m’Mwamba, kapena padziko lapansi, kapena pansi pa dziko wakutsegula buku, kapena kulipenya; 4 Ndipo ndidalira kwambiri, chifukwa sadapezeke munthu woyenera kutsegula ndi kuwerenga buku kapena kulipenya. 5 Ndipo m’modzi wa akulu adanena ndi ine, Usalire: tawona, mkango wochokera mfuko la Yuda, muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi kumasula zosindikizira zake zisanu ndi ziwiri. 6 Ndipo ndidawona, ndipo tawonani pakati pa mpando wachifumu ndi wa zamoyo zinayi, ndi pakati pa akulu, mwana wankhosa ali chiliri ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m’dziko lonse lapansi. 7 Ndipo adadza, natenga buku ku dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu. 8 Ndipo pamene iye adatenga bukulo, zamoyo zinayi, ndi akulu makumi awiri mphambu anayi zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nawo, azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zonunkhira, ndizo mapemphero a woyera mtima. 9 Ndipo adayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo ndi kumasula zosindikizira zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi a manenedwe onse, ndi mitundu ndi mafuko onse; 10 Ndipo mwatipanga ife mafumu ndi ansembe a kwa Mulungu wathu: ndipo tidzalamulira padziko lapansi. 11 Ndipo ndidawona, ndipo ndidamva mawu wa angelo ambiri pozinga mpando wachifumu ndi zamoyo ndi akulu: ndipo mawerengedwe awo adali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi; 12 Akunena ndi mawu akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kuti alandire mphamvu, ndi chuma, ndi nzeru, ndi chilimbiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi madalitso. 13 Ndipo cholengedwa chiri chonse chiri m’mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m’nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndidazimva ziri kunena, kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale madalitso, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi. 14 Ndipo zamoyo zinayi zidati, Ameni. Ndipo akulu makumi awiri mphambu anayi adagwa pansi nalambira Iye amene akhala ndi moyo kunthawi za nthawi.

Chivumbulutso 6

1 Ndipo ndidawona pamene Mwanawankhosa adatsegula chimodzi cha zosindikizira, ndipo ndidamva chimodzi mwa zamoyo zinayi, nichinena, ngati mawu abingu idza nuwone. 2 Ndipo ndidapenya, ndipo tawonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo adali nawo uta; ndipo adampatsa Korona; ndipo adapita kugonjetsa ndi kuti akagonjetse. 3 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachiwiri, ndidamva chamoyo chachiwiri nichinena, Idza, ndipo uwone. 4 Ndipo adatuluka kavalo wina, amene adali wofiyira: ndipo adampatsa iye womkwerayo mphamvu ya kuchotsa mtendere padziko lapansi, ndikuti aphane wina ndi mnzake: ndipo adampatsa iye lupanga lalikulu. 5 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira cha chitatu, ndidamva chamoyo chachitatu nichinena, Idza, nuwone. Ndipo ndidapenya, tawonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwerayo adali nawo muyeso m’dzanja lake. 6 Ndipo ndidamva mawu pakati pa zamoyo zinayi, nanena, Muyeso wa tirigu wogula lupiya; ndi miyeso itatu ya balele lupiya,tawona,iwe mafuta ndi vinyo usaziyipse. 7 Ndipo pamene adatsegura chosindikizira chachinayi, ndidamva mawu a chamoyo chachinayi nichinena, Idza nuwone. 8 Ndipo ndidapenya tawonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo Hade adatsatana naye; ndipo adawapatsa mphamvu padera lachinayi la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko. 9 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachisanu, ndidawona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene adali nawo: 10 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, ndi kunena, kufikira liti, o! inu Ambuye, woyera ndi wowona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko lapansi? 11 Ndipo adapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso atumiki anzawo, ndi abale awo amene adzaphedwa monganso iwo eni kuti kukwaniritsidwe. 12 Ndipo ndidawona pamene adatsegula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo,tawonani padali chibvomezi chachikulu; ndi dzuwa linada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi udakhala ngati mwazi; 13 Ndipo nyenyezi za m’mwamba zidagwa padziko lapansi, monga mkuyu utaya nkhuyu zake zosapsa, pogwedezeka ndi mphepo yolimba. 14 Ndipo Kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zidatunsidwa kuchoka m’malo mwawo. 15 Ndipo mafumu a dziko lapansi, ndi anthu akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi anthu amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi m’matanthwe a m’mapiri; 16 Ndipo adanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya Iye amene akhala pa mpando wa chifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa. 17 Chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wake wafika, ndipo akhoza kuyima ndani?

Chivumbulutso 7

1 Ndipo zitatha zinthu izi ndidawona angelo anayi alimkuyimilira pa ngodya zinayi za dziko lapansi, akugwira mphepo zinayi za dziko lapansi,kuti mphepo zisawombe padziko lapansi kapena panyanja, kapena pa mtengo uli wonse. 2 Ndipo ndidawona m’ngelo wina, adakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chosindikizira cha Mulungu wa moyo: ndipo adafuwula ndi mawu akulu kwa angelo anayi, kwa iyeyu kudapatsidwa mphamvu yakuyipsa dziko ndi nyanja, 3 Nanena, Musayipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titasindikiza chizindikiro atumiki a Mulungu wathu, pa mphumi pawo. 4 Ndipo ndidamva chiwerengero cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi a onse amafuko a ana a Israyeli. 5 Mwa fuko la yuda adasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri: mwa fuko la Rubeni adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri: mwa fuko la Gadi adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. 6 Mwa fuko la Aseri adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Nafitali adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Manase adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. 7 Mwa fuko la Simeon adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Levi adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. 8 Mwa fuko la Zebuloni adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Yosefe adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Benjamini adasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. 9 Zitatha izi, ndidapenya, tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu adakhoza kuliwerenga, wochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuyimilira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atabvala zobvala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo; 10 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, nanena, chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa. 11 Ndi kwa angelo onse akuyimilira pozinga mpando wa chifumu, ndi kwa akulu ndi zamoyo, zinayizo ndipo zidagwa nkhope zawo pansi ku mpando wachifumu nalambira Mulungu. 12 Ndi kunena, Ameni:Madalitso, ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi Ameni. 13 Ndipo m’modzi wa akulu adayankha, nanena ndi ine, Iwo wobvala zobvala zoyera ndiwo ayani? ndipo achokera kuti? 14 Ndipo ndidati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo adati kwa ine, Iwo ndiwo wochokera kutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo adatsuka zobvala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwana wankhosa. 15 Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku m’kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzakhala pakati pawo. 16 Sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena kutentha kulikonse. 17 Chifukwa Mwanawankhosa awkukhala pakati pa mpando wa chifumu adzawadyetsa, nadzawatsogolera ku akasupe amadzi amoyo: ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.

Chivumbulutso 8

1 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachisanu ndi chiwiri, mudakhala chete m’Mwamba monga kwa nthawi ya ola latheka. 2 Ndipo ndidawona angelo asanu ndi awiri amene adayimilira pamso pa Mulungu; ndipo adawapatsa malipenga asanu ndi awiri. 3 Ndipo adadza m’ngelo wina, nayima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolidi; ndipo adampatsa zofukiza zambiri, kuti aziyike pamodzi ndi mapemphero a woyera mtima onse pamwamba pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wachifumu. 4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a woyera mtima udakwera kutuluka m’dzanja la m’ngelo, pamaso pa Mulungu. 5 Ndipo m’ngeloyo adatenga mbale ya zofukiza, nayidzaza ndi moto wopala pa guwa la nsembe nauponya padziko lapansi; ndipo padakhala mabingu, ndi mawu, ndi mphezi, ndi zibvomerezi. 6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nawo malipenga asanu ndi awiri adadzikonzekeretsa kuti awombe. 7 Ndipo m’ngelo woyamba adawomba, ndipo padagwa matalala ndi moto, zosanganizikirana ndi mwazi, ndipo adaziponya pa dziko lapansi: ndipo limodzi la magawo atatu la mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera. 8 Ndipo m’ngelo wachiwiri adawomba, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto lidaponyedwa m’nyanja: ndipo limodzi la magawo atatu la nyanja lidasanduka mwazi; 9 Ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zidali m’nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu la zombo lidawonongeka. 10 Ndipo m’ngelo wachitatu adawomba, ndipo idagwa kuchokera Kumwamba nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muwuni, ndipo idagwa pa limodzi ndi magawo atatu la mitsinje, la pa akasupe a madzi; 11 Ndipo dzina lake la nyenyeziyo alitcha chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu la madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti adasanduka wowawa. 12 Ndipo m’ngelo wachinayi adawomba, ndipo limodzi la magawo atatu la dzuwa lidamenyedwa, ndi limodzi la magawo atatu la mwezi ndi limodzi lamagawo atatu la nyenyezi; kuti limodzi la magawo awo atatu linadetsedwa, ndi ndipo limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usikunso chimodzimodzi. 13 Ndipo ndidawona, ndipo ndidamva m’ngelo akuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mawu akulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mawu wotsala a lipenga la angelo atatu asadawombe amene ayeneranso kuti awombe.

Chivumbulutso 9

1 Ndipo m’ngelo wachisanu adawomba, ndipo ndidawona nyenyezi yochokera Kumwamba idagwa padziko; ndipo adampatsa iye chifunguliro cha dzenje la kupompho. 2 Ndipo adatsegula pa dzenje la pompho; ndipo udakwera utsi wotuluka m’dzenjemo, ngati utsi wa ng’anjo yayikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsiwo wa kudzenjewo. 3 Ndipo mu utsimo wa kudzenjewo mudatuluka dzombe padziko: ndipo adalipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko lapansi zirinayo mphamvu. 4 Ndipo adalilamulira ilo kuti lisayipse udzu wa padziko kapena chobiriwira chiri chonse, kapena mtengo uli wonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pawo ndiwo. 5 Ndipo kwa ilo adalipatsa mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe awo adali ngati mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu. 6 Ndipo m’masiku amenewo, anthu adzafunafuna imfa ndipo sadzayipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa. 7 Ndipo mawonekedwe adzombelo adafanana ndi akavalo wokonzekera kukachita nkhondo; ndi pamitu pawo ngati a Korona wonga a golidi, ndi pankhope pawo ngati nkhope za anthu. 8 Ndipo adali nalo tsitsi longa tsitsi la akazi, ndipo mano awo adali ngati mano a mikango. 9 Ndipo adali nazo zikopa zapachifuwa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko awo ngati mkokomo wa magareta, wa a kavalo ambiri akuthamangira kunkhondo. 10 Ndipo lidali ndi michira yofanana ndi ya chinkhanira, ndipo mudali mbola m’michira yawo: ndipo mphamvu yawo yidali yakuyipsa anthu miyezi isanu. 11 Ndipo lidali nayo Mfumu yakulilamulira, ndiye m’ngelo wa pompho; dzina lake m’chihebri Abadoni, ndi m’chihelene ali nalo dzina Apoliyoni. 12 Tsoka loyamba lapita, ndipo tawonani, akudzanso matsoka awiri m’tsogolomo. 13 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chimodzi adawomba, ndipo ndidamva mawu wochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu, 14 Nanena kwa m’ngelo wachisanu ndi chimmodzi wakukhala ndi lipenga, masula angelo anayi womangidwa pa mtsinje wa ukulu wa Firate. 15 Ndipo adamasulidwa angelo anayi, wokonzeka kufikira ola ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu la anthu. 16 Ndipo chiwerengero cha a nkhondo cha apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndipo ndidamva chiwerengero cha iwo, 17 Ndipo kotero ndidawona akavalo m’masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa zapachifuwa za moto, juwakinto ndi sulfure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo mkamwa mwawo mudatuluka moto ndi utsi ndi sulfure. 18 Ndi miliri imeneyi lidaphedwa limodzi la magawo atatu wa anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulfure, zotuluka m’kamwa mwawo. 19 Pakuti mphamvu yawo ili m’kamwa mwawo, ndi m’michira yawo; pakuti michira yawo ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo ndi iyo ndiyo yimene ayipsa nayo: 20 Ndipo anthu wotsala wosaphedwa nayo miliriyo sadalapa ntchito ya manja awo, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolidi, ndi siliva ndi amkuwa, ndi amwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya kapena kumva, kapena kuyenda: 21 Ndipo sadalapa umbanda wawo, kapena nyanga zawo, kapena chiwerewere chawo, kapena umbala wawo.

Chivumbulutso 10

1 Ndipo ndidawona m’ngelo wina wamphamvu alikutsika Kumwamba, wobvala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto: 2 Ndipo adali nako m’dzanja lake kabuku kofunyulula: ndipo adaponda nalo phazi lake lamanja panyanja ndi lamanzere lake pa mtunda. 3 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, monga ngati mkango wubangula: ndipo pamene adafuwula mabingu asanu ndi awiri adayankhula mawu awo. 4 Ndipo pamene adayankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndidati ndilembe; ndipo ndidamva mawu wochokera Kumwamba nanena kwa ine, sindikiza nacho chizindikiro zinthu zimene adayankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe. 5 Ndipo m’ngelo amene ndidamuwona alikuyimilira pa nyanja ndi pa mtunda, adakweza dzanja lake lamanja kuloza Kumwamba, 6 Nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene adalenga m’Mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi: 7 Komatu m’masiku amawu a m’ngelo wachisanu ndi chiwiri m’mene iye adzayamba kuwomba, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga adachinena kwa atumiki ake aneneri. 8 Ndipo mawu ndidawamva wochokera Kumwamba, adayankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku laling’ono lofunyululalo m’dzanja la m’ngelo wakuyimilira panyanja ndi padziko. 9 Ndipo ndidapita kwa m’ngelo, ndi kunena naye, ndipatse kabukuko. Ndipo adanena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m’mimba mwako, komatu m’kamwa mwako kadzazuna ngati uchi. 10 Ndipo ndidatenga kabuku m’dzanja la m’ngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kadali m’kamwa mwanga kozuna ngati uchi: ndipo pamene ndinakadya m’mimba mwanga mudawawa. 11 Ndipo adati kwa ine, uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.

Chivumbulutso 11

1 Ndipo adandipatsa ine bango ngati ndodo: ndipo m’ngelo adayimirira, wakunena kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo. 2 Ndipo bwalo lakunja kwa kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti lapatsidwa ilo kwa amitundu: ndipo mzinda wopatulika adzawupondereza miyezi makumi anayi mphambu iwiri. 3 Ndipo ndidzapatsa mphamvu mboni zanga ziwiri zonenera miyezi makumi anayi ndi iwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zitabvala chiguduli. 4 Izi ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoyikapo nyali ziwiri zakuyima pamaso pa Mulungu wa dziko lapansi. 5 Ndipo munthu wina akafuna kuyipsa izo, moto utuluka m’kamwa mwawo, nuwononga adani awo; ndipo wina akafuna kuyipsa izo, maphedwe ake ayenera kukhala wotero. 6 Izi ziri nawo ulamuliro wakutseka m’Mwamba, isagwe mvula masiku achinenero chawo: ndipo ulamuliro ziri nawo pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi ili yonse zifuna. 7 Ndipo pamene zidzatsiliza umboni wawo chirombo chokwera kutuluka m’pompho chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo. 8 Ndipo mitembo yawo idzagona pa msewu wa mzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, sodomu ndi Aigupto, umenenso Ambuye wathu adapachikidwa. 9 Ndipo mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe adzapenyera mitembo yawo masiku atatu ndi theka lake, ndipo sadzalola mitembo yawo iyikidwe m’manda. 10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwera pa iyo, nadzasekera, nadzatumizirana mphatso wina ndi mzake; chifukwa aneneri awa awiri adazunza iwo akukhala padziko lapansi. 11 Ndipo atapita masiku atatu ndi theka lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu udalowa mwa iwo, ndipo adayimirira chiliri; ndipo mantha akulu adawagwera iwo akuwapenya. 12 Ndipo adamva mawu akulu akuchokera Kumwamba akunena nawo, kwera kuno. Ndipo anakwera kumka Kumwamba; ndipo adani awo adawapenya. 13 Ndipo panthawi yomweyo padali chibvomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi la mzinda lidagwa; ndipo adaphedwa m’chibvomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri: ndipo wotsalawo adakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa Kumwamba. 14 Tsoka lachiwiri lachoka; ndipo tawonani, tsoka lachitatu lidza msanga. 15 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chiwiri adawomba, ndipo padakhala mawu akulu m’Mwamba, ndikunena, maufumu a dziko lapansi ayamba kukhala a Ambuye wathu, ndi a Khristu wake; ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi. 16 Ndipo akulu makumi awiri mphambu anayi akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yawo, adagwa nkhope zawo pansi nalambira Mulungu. 17 Nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvu yonse, amene muli ndi mudali ndi mudzali popeza mwadzitengera mphamvu yanu yayikulu, ndipo mwachita ufumu. 18 Ndipo amitundu adakwiya, ndipo udadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakuti Inu mupereke mphotho kwa atumiki anu ndi aneneri, ndi woyera mtima, ndi iwo akuwopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu; ndi kuwononga iwo amene adawononga dziko lapansi. 19 Ndipo adatsegulidwa kachisi wa Mulungu amene ali m’Mwamba; ndipo lidawoneka likasa la chipangano chake, m’kachisi mwake, ndipo padali mphezi, ndi mawu, ndi mabingu, ndi chibvomezi ndi matalala akulu.

Chivumbulutso 12

1 Ndipo chodabwitsa chachikulu chidawoneka m’mwamba; mkazi wobvekedwa dzuwa ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake Korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri: 2 Ndipo adali ndi pakati; ndipo adafuwula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala. 3 Ndipo chidawoneka chodabwitsa china m’mwamba, tawonani, chinjoka chofiyira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake akolona achifumu asanu ndi awiri. 4 Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu anyenyezi za kumwamba, nuziponya padziko lapansi. Ndipo chinjoka chidayimilira pamaso pa mkazi wakuti abale, kuti akabala, icho chikam’meze. 5 Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo adakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wachifumu wake. 6 Ndipo mkazi adathawira kuchipululu, kumene adali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi. 7 Ndipo mudali nkhondo m’mwamba: Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chidachita nkhondo, 8 Ndipo sichidalakika, ndipo sadapezekanso malo awo m’mwamba. 9 Ndipo chidaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana amene adanyenga dziko lonse lapansi: iye ada- ponyedwa pansi kudziko, ndi pamodzi ndi iye angelo ake. 10 Ndipo ndidamva mawu akulu m’Mwamba, nanena, Tsopano chafika chipulumutso ndi mphamvu, ndi ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake: pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku. 11 Ndipo iwo adamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwana wankhosa, ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo; ndipo sadakonda moyo wawo ngakhale kufikira imfa. 12 Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu ndi inu akukhala momwemo, tsoka wokhala pa mtunda ndi a mnyanja! Chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi kochepa. 13 Ndipo pamene chinjoka chidawona kuti chidaponyedwa pansi padziko, chidazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna. 14 Ndipo adampatsa mkazi mapiko awiri achiwombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, kumbuto yake, kumene adyetsedwako kanthawi ndi nthawi, ndi theka lanthawi, wochotsedwa pa nkhope ya njoka. 15 Ndipo njokayo idalabvura mkamwa mwake madzi ngati chigumula, potsata mkazi, kuti akakokoloredwe mkazi nawo. 16 Ndipo dziko lidathandiza mkaziyo, pamene lidatsegula pakamwa pake, ndi kumeza madzi achigumula amene chinjoka chidalabvula m’kamwa mwake. 17 Ndipo chinjoka chidakwiya ndi mkazi, nichinachoka kumka kuchita nkhondo ndi otsala ambewu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu Khristu.

Chivumbulutso 13

1 Ndipo ndidayimilira pa mchenga wa nyanja, ndipo ndidawona chirombo chakutuluka m’nyanja, chakukhala nayo mitu ndi iwiri, isanu ndi nyanga khumi ndi pamwamba pa nyanga zake akolona achifumu khumi, ndi pamitu yakeyo mayina a mwano. 2 Ndipo chirombo ndidachiwonacho chidafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi achimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chidampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu. 3 Ndipo ndidawona umodzi wa mitu yake udakhala ngati udalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la ku imfa lidapola: ndipo dziko lonse lapansi lidazizwa potsata chirombocho. 4 Ndipo adalambira chinjoka, chimene chidachipatsa mphamvu chirombocho: ndipo adalambira chirombo ndi kunena, Afanana ndi chirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kumenya nacho nkhondo? 5 Ndipo adachipatsa icho m’kamwa moyankhula zinthu zazikulu ndi zamwano; ndipo adachipatsa ulamuliro wakutero miyezi makumi anayi ndi iwiri 6 Ndipo chidatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala m’Mwamba. 7 Ndipo adachipatsa icho kuchita nkhondo ndi woyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo adachipatsa ulamuliro wa pafuko liri lonse, ndi malilime ndi manenedwe, ndi mitundu. 8 Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko lapansi, amene dzina lawo silidalembedwa m’buku la moyo la Mwana wankhosa wophedwa kuyambira kumaziko amakhazikitsidwe adziko lapansi. 9 Ngati munthu wina ali nalo khutu lakumva, amve. 10 Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka: munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiliro ndi chikhulupiriro cha woyera mtima. 11 Ndipo ndidawona chirombo china chirikutuluka pansi; ndipo chidali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wankhosa ndipo chidayankhula ngati chinjoka. 12 Ndipo chichita ulamuliro wonse wachirombo choyamba pamaso pake. Ndipo chichititsa dziko ndi iwo akukhala momwemo kuti alambire chirombo choyamba chimene bala lake lakuimfa lidapola. 13 Ndipo chichita zodabwitsa zazikulu, kutinso chitsitse moto uchokere m’mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu. 14 Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko mwa machitidwe a zozizwitsa amene icho chidapatsidwa mphamvu yakuchita pamaso pa chirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chirombo, chimene chidali nalo bala la lupanga nichinakhalanso ndi moyo. 15 Ndipo chidali ndi mphamvu yakupatsa moyo fano la chirombo, kuti fano la chilombo liyankhule, nichipangitse kuti onse osalambira fano lachirombo aphedwe. 16 Ndipo chipangitsa kuti onse, ang’ono ndi akulu, achuma ndi wosauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire chilembo pa dzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo. 17 Ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, kapena dzina la chirombo, kapena chiwerengero cha dzina lake. 18 Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chirombocho: pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.

Chivumbulutso 14

1 Ndipo ndidapenya, ndipo tawonani, Mwanawankhosayo alikuyimilira pa phiri la ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo. 2 Ndipo ndidamva mawu wochokera Kumwamba, ngati mau amkokomo wamadzi ambiri ndi ngati mawu a bingu lalikulu: ndipo mawu amene ndidawamva adakhala ngati a zeze akuyimba azeze awo: 3 Ndipo adayimba ngati nyimbo yatsopano ku mpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinayi, ndi akulu: ndipo palibe munthu adakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, wowomboledwa kuchokera kudziko lapansi. 4 Awa ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Awa ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kuli konse amukako. Iwowa adawomboledwa mwa anthu, amene ndiwo zipatso zowundukula za kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. 5 Ndipo m’kamwa mwawo simudapezeka chinyengo; popeza kuti ali wopanda chilema pamaso pampando wa Mulungu. 6 Ndipo ndidawona m’ngelo wina ali kuwuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko lapansi, kwa mtundu uli wonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu. 7 Ndi kunena ndi mawu akulu, Wopani Mulungu, mpatseni ulemerero Iye; pakuti yafika nthawi yachiweruziro chake: ndipo mlambireni Iye amene adalenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe a madzi. 8 Ndipo adatsala m’ngelo wina, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo mzinda waukulu wo umene udamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chiwerewere chake. 9 Ndipo adawatsata m’ngelo wina wachitatu, nanena ndi mawu akulu, Ngati wina alambira chirombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pa mphumi pake, kapena pa dzanja lake, 10 Iyenso adzamwako ku vinyo wa m’kwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m’chikho cha m’kwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi Sulfure, pamaso pa angelo woyera ndi pamaso pa Mwanawankhosa: 11 Ndipo utsi wa mazunzo awo ukwera ku nthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chirombocho ndi fano lake, ndi iye ali yense amene alandira chizindikiro cha dzina lake. 12 Pano pali chipiliro cha woyera mtima: cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu. 13 Ndipo ndidamva mawu wochokera Kumwamba, ndikunena, kwa ine, Lemba, Wodala akufa amene akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; Inde, ananena, Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; pakuti ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi. 14 Ndipo ndidapenya, tawonani, mtambo woyera, ndi pamtambopo padakhala wina monga Mwana wa munthu wakukhala naye Korona wa golidi pa mutu pake, ndi m’dzanja lake zenga lakuthwa. 15 Ndipo m’ngelo wina adatuluka m’kachisi, wofuwula ndi mawu akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza zokolola za dziko zankhwima. 16 Ndipo Iye wokhala pamtambo adaponya zenga lake padziko, ndipo zokolola za dziko zidamwetedwa. 17 Ndipo m’ngelo wina adatuluka m’kachisi wokhala m’Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso. 18 Ndipo m’ngelo wina adatuluka kuchokera paguwa la nsembe, ndiye wakukhala nayo mphamvu pamoto; nafuwula ndi mawu akulu kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m’dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu. 19 Ndipo m’ngelo adaponya zenga lake ku dziko nadula mphesa za m’munda wa ’dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu. 20 Ndipo moponderanso mphesa adamupondera kunja kwa mzinda, ndipo mwazi udatuluka moponderamo mphesa, nufikira mpaka kuzomangira pakamwa za pa akavalo mpata wa mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.

Chivumbulutso 15

1 Ndipo ndidawona chizindikiro china m’mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu. 2 Ndipo ndidawona ngati nyanja yamandala yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene adachilaka chirombocho, ndi fano lake ndi chizindikiro chake ndi chiwerengero cha dzina lake, adayimilira pa nyanja ya mandala, akukhala nawo azeze a Mulungu. 3 Ndipo ayimba nyimbo ya Mose mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, ndikuti, ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse; njira zanu nzolungama ndi zowongoka. Mfumu Inu ya woyera mtima. 4 Ndani amene adzakhala wosawopa inu ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera: chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza ziweruziro zanu zawonetsedwa. 5 Ndipo zitatha izi ndidawona, ndipo tawonani, padatseguka pa kachisi wa chihema cha umboni m’Mwamba: 6 Ndipo adatuluka m’kachisi angelo asanu ndi awiri, akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala chobvala choyera, ndi chonyezimira, namangira malamba agolidi pachifuwa pawo. 7 Ndipo chimodzi cha zamoyo zinayi chidapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu, wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi. 8 Ndipo kachisi adadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu adakhoza kulowa m’kachisi kufikira itakwaniritsidwa miliri isanu ndi awiri ya angelo asanu ndi iwiri.

Chivumbulutso 16

1 Ndipo ndidamva mawu akulu wochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu. 2 Ndipo adachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kudakhala chironda choyipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chirombo ndi pa iwo wolambira fano lake. 3 Ndipo m’ngelo wachiwiri adatsanulira mbale yake m’nyanja; ndipo kudakhala mwazi ngati wa munthu wakufa:ndipo zamoyo zonse za m’nyanja zidafa. 4 Ndipo m’ngelo wachitatu adatsanulira mbale yake ku mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo adasanduka mwazi. 5 Ndipo ndidamva m’ngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, Ambuye amene muli, mudali, ndipo mudzakhala, chifukwa mudaweruza chotero. 6 Popeza adakhetsa mwazi wa woyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; pakuti ayenera iwo. 7 Ndipo ndidamva wina wa pa guwa la nsembe, alimkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvu yonse, chiweruziro chanu chiri chowona ndi cholungama. 8 Ndipo m’ngelo wachinayi, adatsanulira mbale yake padzuwa; ndipo mphamvu idapatsidwa kwa iye kuti atenthe anthu ndi moto. 9 Ndipo adatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo adachitirabe mwano dzina la Mulungu wokhala nayo mphamvu pa miliri iyi: ndipo sadalapa kuti akapatse Mulungu ulemerero. 10 Ndipo m’ngelo wa chisanu adatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chirombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa;ndipo adatafuna malilime awo chifukwa cha kuwawa. 11 Ndipo adachitira mwano Mulungu wa m’Mwamba chifukwa cha zowawa zawo ndi zironda zawo; ndipo sadalapa ntchito zawo. 12 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chimodzi adatsanulira mbale yake pa mtsinje waukulu wa Firate; ndipo madzi ake adaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu wochokera kummawa kotulukira dzuwa. 13 Ndipo ndidawona mizimu itatu yonyansa yokhala ngati achule ikutuluka m’kamwa mwa chinjoka ndi mkamwa mwa chirombo ndi mwa m’neneri wonyenga. 14 Pakuti ali mizimu ya ziwanda yakuchita zozizwitsa; imene ituluka kumka kwa mafumu akudziko ndi adziko lonse lapansi, kuwasonkhanitsira iwo ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvu yonse. 15 Tawonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zobvala zake, kuti angayende wamaliseke, nangapenye anthu manyazi ake. 16 Ndipo adawasonkhanitsira ku malo wotchedwa mchinenedwe cha m’chihebri Harmagedo. 17 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chiwiri adatsanyulira mbale yake mumlenga lenga; ndipo m’menemo mudatuluka mawu akulu wochokera kukachisi wakumwamba ,kuchokera kumpando wachifumu ndi kunena, Chachitika. 18 Ndipo padakhala mphezi, ndi mawu, ndi mabingu; ndi kung’anima, ndi chibvomezi chachikulu chotero chonga sichidawonekepo chiyambire anthu padziko, chibvomezi champhamvu chotero, ndipo ndichachikulu ndithu. 19 Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndipo mizinda ya amitundu idagwa; ndipo Babulo waukulu udakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake 20 Ndipo zilumba zonse zidathawa, ndipo mapiri sadapezeke. 21 Ndipo pamenepo adagwa pa anthu matalala akulu wochokera Kumwamba, ndipo mwala wa talala, liri lonse wolemera ngati talenti: ndipo anthu adachitira Mulungu mwano chifukwa cha muliri wa matalala, pakuti muliri wake udali waukulu ndithu.

Chivumbulutso 17

1 Ndipo anadza m’modzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nayankhula ndi ine, nanena, idza kuno, ndidzakuwonetsa chiweruziro cha mkazi wa chigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri. 2 Amene mafumu adziko adachita chiwerewere naye, ndipo iwo akukhala padziko adaledzera ndi vinyo wa chiwerewere chake: 3 Ndipo adanditenga kunka nane kuchipululu, mu mzimu: ndipo ndidawona mkazi alinkukhala pa chirombo chamawangamawanga chofiritsa, chodzala ndi mayina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 4 Ndipo mkazi adabvala chobvala cha nsalu ya pepu ya mtundu wofiyiritsa, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale, nakhala nacho m’dzanja lake chikho chagolidi chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chiwerewere chake: 5 Ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina CHINSINSI, BABULO WAUKULU, AMAYI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO LAPANSI. 6 Ndipo ndidawona mkazi woledzera ndi mwazi wa woyera mtima, ndi mwazi wa wophedwa a Yesu: ndipo ndidazizwa pakuwona iye ndikuzizwa kwakukulu. 7 Ndipo m’ngelo adati kwa ine, uzizwa chifukwa chiyani? Ine ndidzakuwuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chirombo chakum’tenga iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 8 Ndipo chirombo chimene udachiwona chidaliko, koma kulibe; chidzatuluka m’pompho, ndi kumka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala pa dziko amene dzina lawo silidalembedwe m’buku la moyo chiyambire maziko a makhazikitsidwe adziko lapansi, pakuwona chirombo, kuti chidaliko, koma kulibe, ndipo chidzakhalako. 9 Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalako. 10 Ndipo ali mafumu asanu ndi awiri: asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siyinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi kochepa. 11 Ndipo chirombo chimene chidaliko, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chiri mwa zisanu ndi ziwirizo, nichimuka kuchitayiko. 12 Ndipo nyanga khumi uziwona ndiwo mafumu khumi, amene sadalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu kwa ola limodzi pamodzi ndi chirombo. 13 Iwo ali nawo mtima umodzi, ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chirombo. 14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka: chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu: ndi iwo akukhala naye, woyitanidwa, ndi wosankhidwa ndi wokhulupirika. 15 Ndipo adanena kwa ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe. 16 Ndipo nyanga khumi udaziwona, pachirombocho, izi zidzadana ndi mkazi wa chigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wamaliseke, nizidzadya nyama yake, nizidzamuwotcha iye ndi moto. 17 Pakuti Mulungu adayika kumtima kwawo kukakwaniritsa za chifuniro chake ndikuchita za mtima umodzi ndi kupereka ufumu wawo kwa chirombo kufikira akwaniritsidwa mawu a Mulungu. 18 Ndipo mkaziyo udamuwona ndiye mzinda waukuluwo umene uchita ufumu pa mafumu a dziko lapansi.

Chivumbulutso 18

1 Zitatha zinthu izi ndidawona m’ngelo wina wotsika pansi kuchokera Kumwamba wakukhala nawo ulamuliro waukulu; ndipo dziko lidaunikidwa ndi ulemerero wake. 2 Ndipo adafuwula ndi mawu wolimba, nanena, Wagwa, wagwa Babulo waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa. 3 Chifukwa ndi kuledzera kwa vinyo wa mkwiyo wa chiwerewere chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu adziko adachita naye chiwerewere; ndipo wochita malonda adziko adalemera ndi mphamvu yakudyerera kwake. 4 Ndipo ndidamva mawu ena wochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; 5 Pakuti machimo ake adaunjikizana kufikira, m’Mwamba, ndipo Mulungu adakumbukira zosalungama zake. 6 Kumbwezera iye mphotho, monganso iyeyu adakubwezerani inu, ndipo mumuwirikizire ndi kumuwirikizira mobwereza, monga mwa ntchito zake; m’chikhomo adathiramo, mumuthirire chowirikiza. 7 Monga momwe adadzichitira iye ulemu, nadyerera, momwemo mumchitire chomuzunza ndi chomuliritsa maliro: pakuti adanena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosawona maliro konse ine. 8 Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo adzapserera ndi moto: chifukwa Ambuye Mulungu wakumuweruza iye ndiye wolimba. 9 Ndipo mafumu a dziko wochita chiwerewere nadyerera naye, adzamlira iye nadzamlira maliro pamene adzawona utsi wakutentha kwake, 10 Poyima patali chifukwa chakuwopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babulo, mzinda wolimba! Pakuti mu ola limodzi chafika chiweruziro chako. 11 Ndipo wochita malonda am’dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ake: 12 Malonda a golidi, ndi siliva, ndi amwala wa mtengo wake, ndi a ngale ndi a nsalu ya bafuta, ndi ya pepu, ndi yonyezimira, ndi yofirira ya mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi zotengera ziri zonse za mtengo wake wapatali, ndi mkuwa ndi zachitsulo, ndi za nsangalabwi, 13 Ndi Kinamoni ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng’ombe, ndi nkhosa, ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a akapolo ndi miyoyo ya anthu. 14 Ndipo zipatso zimene moyo wako udazilakalaka zidakuchokera, ndipo zones zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzapezanso konse. 15 Wogulitsa zinthu izi, amene adalemera nazo, adzayima patali chifukwa cha mantha a chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo, 16 Nadzanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu wobvala bafuta ndi nsalu ya pepu ya mlangali wofiyiritsa wabwino, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale! 17 Pakuti mu ola limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere. Ndipo eni zombo, aliwonse, ndi wonse wopanga zombo, ndi onse akuchita malonda a panyanja, ndi amalinyero adayima patali, 18 Ndipo adalira ndi kufuwula powona utsi wa kutentha kwake, nanena, mzinda uti uwu ufanana ndi mzinda waukuluwo? 19 Ndipo adathira fumbi pamitu pawo, nafuwula ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka,mzinda waukuluwo, umene udalemera nawo onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa mwa kulemera kwake pa ola limodzi wasanduka bwinja. 20 Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi woyera mtima, ndi a tumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu wabwezerera inu pa iye. 21 Ndipo m’ngelo wolimba adanyamula mwala, ngati mphero yayikulu, nayiponya m’nyanja, nanena, chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse. 22 Ndipo mawu wa anthu woyimba zeze, ndi a woyimba, ndi a woliza zitoliro, ndi a woomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo munthu waluso ndi luso lina lirilonse lokhalamo silidzapezekanso mwa iwe; ndi kulira kwa mwala wa mphero, sikudzamvekanso konse mwa iwe. 23 Ndipo kuwunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mawu amkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti wotsatsa malonda anu adali anthu womveka am’dziko; pakuti ndi nyanga za ufiti wako, mitundu yonse idasocheretsedwa. 24 Ndipo mwa iye mudapezeka mwazi wa aneneri ndi woyera mtima, ndi onse amene adaphedwa padziko lapansi.

Chivumbulutso 19

1 Zitatha zinthu izi ndidamva ngati mawu akulu akhamu lalikulu m’Mwamba, liri kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi ulemu ndi mphamvu, zikhale kwa Ambuye Mulungu wathu: 2 Pakuti maweruzo ake ali wowona ndi wolungama: ndipo adaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene adayipsa dziko lapansi ndi chiwerewere chake, ndipo anambwezera chilango chifukwa cha mwazi wa atumiki ake pa dzanja la mkaziyo. 3 Ndipo adatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera ku nthawi za nthawi. 4 Ndipo adagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anayi ndi zamoyo zinayi, ndipo zidalambira Mulungu wakukhala pa mpando wa chifumu, nizinena, Ameni; Aleluya. 5 Ndipo mawu adachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, lemekezani Mulungu wathu atumiki ake, inu ndi inu nonse, akumuwopa Iye, ang’ono ndi akulu. 6 Ndipo ndidamva akukhala ngati mawu a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mawu a mabingu wolimba, nizinena, Aleluya: pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvu zonse. 7 Tiyeni tikondwere, tisekere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa: ndipo mkazi wake wadzikonzekeretsa. 8 Ndipo adampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu: pakuti bafuta ndiye zolungama za woyera mtima. 9 Ndipo adanena ndi ine, Lemba, wodala iwo amene ayitanidwa ku phwando lam’gonero la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo adanena ndi ine, awa ndiwo maneno owona a Mulungu. 10 Ndipo ndidagwa pamapazi ake kumlambira iye. Ndipo adanena ndi ine, tapenya, usatero; ine ndine mtumiki mzako, ndi mzawo wa abale ako akukhala nawo umboni wa Yesu: lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero. 11 Ndipo ndidawona mutatseguka m’Mwamba; ndipo tawonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo mchilungamo Iye aweruza, nachita nkhondo. 12 Maso ake ali ngati lawi la moto, ndipo pamutu pake padali akolona a chifumu ambiri; ndipo adali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina aliyense koma Iye yekha. 13 Ndipo adabvekedwa ndichobvala choviyikidwa m’mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mawu a Mulungu. 14 Ndipo magulu a nkhondo wokhala m’Mwamba adamtsata Iye, wokwera pa akavalo woyera, wobvala bafuta woyera woti mbuu. 15 Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu: ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo ya chitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo wa ukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvu yonse. 16 Ndipo ali nalo pa chobvala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE. 17 Ndipo ndidawona m’ngelo alikuyima m’dzuwa; ndipo adafuwula ndi mawu akulu akunena ndi mbalame zonse zakuwuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani ku phwando la m’gonero la Mulungu wamkulu; 18 Kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitawo, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi nyama ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang’ono ndi akulu. 19 Ndipo ndidawona chirombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo awo, wosonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake. 20 Ndipo chidagwidwa chirombocho, ndi pamodzi ndi m’neneri wonyenga amene adachita zozwizwitsa, pamaso pake, zimene adasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chirombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri adaponyedwa ali ndi moyo m’nyanja yamoto yakutentha ndi Sulfure. 21 Ndipo wotsalawa adaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lochokera kutuluka m’kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zidakhuta ndi nyama zawo.

Chivumbulutso 20

1 Ndipo ndidawona m’ngelo adatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha pompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. 2 Ndipo adagwira chinjoka, njoka yokalamba yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi. 3 Namponya kupompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso a mitundu kufikira kukwaniritsidwa kwa zaka chikwi; patatha izi adzayenera kumasulidwa iye kanthawi. 4 Ndipo ndidawona mipando ya chifumu, ndi iwo akukhala pamenepo; ndipo adawapatsa chiweruziro; ndipo ndidawona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi iwo amene sadalambira chirombo, kapena fano lake, nisadalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lawo; ndipo adakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi. 5 Koma wotsala wa akufa sadakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi.Uku ndiko kuwuka koyamba. 6 Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuwuka koyamba: pa iwowa imfa yachiwiri ilibe mphamvu; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo. 7 Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, Satana adzamasulidwa m’ndende yake; 8 Ndipo adzatuluka kukanyenga amitundu ali mu ngodya zinayi za dziko lapansi, gogi ndi magogi, kudzawasonkhanitsa kuti achite nkhondo: chiwerengero chawo cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja. 9 Ndipo adakwera nafalikira m’dziko, nazinga msasa wa woyera mtima ndi mzinda wa wokondedwawo; ndipo udatsika moto wochokera kumwamba nuwanyeketsa. 10 Ndipo mdierekezi wakusocheretsa iwo adaponyedwa m’nyanja ya moto ndi Sulfure, kumeneko kulinso chirombocho ndi m’neneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi. 11 Ndipo ndidawona mpando wa chifumu wa ukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m’Mwamba zidathawa pamaso pake, ndipo sadapezeka malo awo. 12 Ndipo ndidawona akufa, akulu ndi ang’ono alimkuyima pamaso pa Mulungu; ndipo mabuku adatsegulidwa; ndipo buku lina lidatsegulidwa, ndilo buku la moyo: ndipo akufa adaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zawo. 13 Ndipo nyanja idapereka akufawo adali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zidapereka akufawo adali m’menemo: ndipo adaweruzidwa munthu ali yense monga mwa ntchito zake. 14 Ndipo imfa ndi Hade zidaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. 15 Ndipo ngati munthu aliyense sadapezedwa wolembedwa m’buku la moyo, adaponyedwa m’nyanja ya moto.

Chivumbulutso 21

1 Ndipo ndidawona m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko lapansi loyamba zidachoka, ndipo kunalibenso nyanja. 2 Ndipo ine Yohane ndidawona mzinda woyerawo, Yerusaremu watsopano, wotsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu, wokonzedwa ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. 3 Ndipo ndidamva mawu akulu wochokera Kumwamba, ndi kunena, Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndipo Mulungu mwiniyekha adzakhala Mulungu wawo. 4 Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse kuyichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; kapena chisoni kapena maliro; ndipo sipadzakhalanso chowawitsa pamenepo; zoyambazo zapita. 5 Ndipo Iye wakukhala pa mpando wa chifumu adati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo adati kwa ine, Talemba; pakuti mawu awa ali wokhulupirika ndi wowona. 6 Ndipo adati kwa ine, zachitika. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe ku kasupe wa madzi a moyo kwa ulere. 7 Iye wakulakika adzalandira zinthu zonse; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. 8 Koma amantha, ndi wosakhulupirika, ndi wonyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi anyanga ndi wolambira mafano, ndi onse abodza, cholandira chawo chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi Sulfure; ndiyo imfa yachiwiri. 9 Ndipo anadza m’modzi kwa ine wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo adayankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuwonetsa iwe mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa. 10 Ndipo adanditenga mu mzimu kumka ku phiri lalikulu ndi lalitali, nandiwonetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu woyera, wotsika m’Mwamba kuchokera kwa Mulungu, 11 Wokhala nawo ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kudafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati Krustalo; 12 Ndipo udakhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pa zipata angelo khumi ndi awiri, ndi mayina wolembedwapo, ndiwo mayina a mafuko khumi ndi awiri wa ana a Israyeli. 13 Kum’mawa zipata zitatu; ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwera zipata zitatu ndi kumadzulo zipata zitatu. 14 Ndipo linga la mudziwo lidakhala nawo maziko khumi ndi awiri, ndi mmenemo mayina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa. 15 Ndipo iye wakuyankhula ndi ine adali nawo muyeso, bango lagolidi, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake ndi linga lake. 16 Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa ngodya zonse; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake; ndipo adayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri, utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana. 17 Ndipo adayesa linga lake, mikono zana mphambu makumi anayi kudza zinayi, muyeso wa munthu, ndiye m’ngelo. 18 Ndipo milimo ya linga lake ndiye yaspi: ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala woyera wowonekera bwino. 19 Ndipo maziko a linga la mzindawo adakometsedwa ndi miyala ya mtengo wapatali ya mitundu mitundu; maziko woyamba, ndi yaspi, achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinayi, ndi emaraldo; 20 Achisanu ndi sardoni; achisanu ndi chimodzi ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri ndi krusolito; achisanu ndi chitatu ndi berulo; achisanu ndi chinayi ndi topaziyo; akhumi ndi krusoprazo; khumi ndi chimodzi ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri ndi ametusto 21 Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chiri chonse pachokha cha ngale imodzi. Ndipo msewu wa mzinda ndi wagolidi woyengeka, ngati mandala wowonekera bwino. 22 Ndipo sindidawona kachisi mmenemo: pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo kachisi wake. 23 Ndipo pamzindapo panalibe dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uwunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa. 24 Ndipo mitundu ya iwo wopulumutsidwa adzayendayenda mwa kuwunika kwake: ndipo mafumu a dziko lapansi atenga ulemerero ndi ulemu wawo kulowa nawo momwemo. 25 Ndipo pazipata zake sipadzatsekedwa konse usana: pakuti sikudzakhala usiku komweko. 26 Ndipo adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nawo momwemo. 27 Ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kodetsedwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza: koma iwo wokhawo wolembedwa m’buku la moyo la Mwanawankhosa.

Chivumbulutso 22

1 Ndipo adandiwonetsa mtsinje wangwiro wa madzi a moyo, wonyezimira ngati Krustalo, wotuluka ku mpando wa chifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. 2 Pakati pa msewu wake, ndi tsidya lirilonse la mtsinje, ndi tsidya lija padali pamenepo mtengo wa moyo, wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi: ndipo masamba amtengo ndiwo akuchiritsa nawo mafuko. 3 Ndipo sipadzakhalanso temberero liri lonse; koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo atumiki ake adzamtumikira Iye. 4 Ndipo adzawona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo. 5 Ndipo sikudzakhalanso usiku kumeneko; ndipo sikufunika kuwunika kwa nyali, ngakhale kuwunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawunikira umenewu: ndipo adzachita ufumu ku nthawi zanthawi. 6 Ndipo adati kwa ine, Mawu awa ali wokhulupirika ndi woona: ndipo Ambuye Mulungu wa aneneri woyera adatuma m’ngelo wake kuwonetsera atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika msanga. 7 Tawona, Ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mawu achinenero cha buku ili. 8 Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya zinthu izi. Ndipo pamene ndidamva ndi kupenya ndinagwa pansi kulambira pa mapazi am’ngelo wakundiwonetsa zinthu izi. 9 Ndipo adanena iye ndi ine, Tapenya, usachite chotero: ine ndine mtumiki mzako, ndi mzawo wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga zonenera za buku ili: lambira Mulungu. 10 Ndipo adanena ndi ine, kuti, Usasindikiza chizindikiro mawu awa achinenero cha buku ili: pakuti nthawi yayandikira. 11 Iye wakukhala wosalungama, akhale wosalungama: ndi iye wonyansa akhale wonyansa: ndi iye wakukhala wolungama akhale wolungama; ndi iye amene ali woyera akhale woyera. 12 Ndipo, Tawonani, ndidza msanga: ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa munthu aliyense monga mwa ntchito yake. 13 Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza chiyambi ndi chitsiriziro. 14 Wodala iwo amene achita malamulo ake, kuti akakhale nawo ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe mu mzinda pa zipata. 15 Pakuti kunja kuli agalu, ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi wopembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita. 16 Ine Yesu ndatuma m’ngelo wanga kukakuchitirani inu umboni wa zinthu izi m’Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda ya m’bandakucha. 17 Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idza. Ndipo iye wakumva ludzu adze; ndipo aliyense wofuna, muloleni atenge madzi a moyo kwaulere. 18 Pakuti ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mawu achinenero cha buku ili, ngati munthu adzawonjezera pa zinthu izi, Mulungu adzamuwonjezera iye miliri yolembedwa m’bukumu: 19 Ndipo ngati munthu ali yense adzachotsako pa mawu a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi mu mzinda woyerawo, ndi pa zinthu izi zilembedwa m’bukumu. 20 Iye amene akuchitira umboni zinthu izi, anena, Indetu; ndidza msanga Ameni; inde,idzani, Ambuye Yesu. 21 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.